-
‘Mudzandiweramira Kuti Mundithandize’Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
-
-
KUDZICHEPETSA ndi khalidwe losiririka. Nthawi zonse timasangalala kukhala pa ubwenzi ndi anthu omwe ndi odzichepetsa. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti masiku ano n’zovuta kupeza anthu amene ndi odzichepetsadi, makamaka ngati anthuwo ali ndi udindo winawake. Nanga bwanji Yehova Mulungu, yemwe ndi wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse? Kodi iye ndi wodzichepetsa? Tiyeni tikambirane mawu a mneneri Yeremiya opezeka palemba la Maliro 3:20, 21.—Werengani.
-
-
‘Mudzandiweramira Kuti Mundithandize’Nsanja ya Olonda—2012 | June 1
-
-
Yeremiya ankakhulupirira kuti Yehova ‘adzawerama’ kuti athandize anthu amene alapadi kuchokera pansi pa mtima. Baibulo lina linamasulira vesi limeneli kuti: “Mundikumbukire ndipo munyonyomale kuti mundithandize.” Mawu amenewa akutithandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wokoma mtima komanso wachikondi. Pamenepa Yeremiya ankayembekezera kuti Yehova, yemwe ndi “Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi,” anyonyomala kuti athandize anthu ake kusiya njira zawo zoipa ndi kukhalanso naye pa ubwenzi. (Salimo 83:18) Chifukwa cha chiyembekezo chimenechi, Yeremiya anapeza chitonthozo pa ululu womwe ankamva mu mtima mwake. Mneneri wokhulupirikayu anatsimikiza mtima kuyembekezera mpaka nthawi ya Yehova yoti apulumutse anthu ake itakwana.—Vesi 21.
-