Kusenza Goli Ukali Wamng’ono
MU “Nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, achichepere amakumana ndi ziyeso zambiri. (2 Timoteo 3:1) Tsiku lililonse amamva manenanena olimbikitsa chiwerewere, kusuta, ndi makhalidwe ena oipa. Omwe amatsatira miyezo ya Baibulo angasekedwe chifukwa chokana kutsatira zomwe gulu likuchita, ndipo Akristu ena angaone kuti kugonja ndiko kwapafupi.
Chakumapeto kwa zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., Yeremiya analemba kuti: “Nkokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.” (Maliro 3:27) Kodi anatanthauzanji? Anatanthauza kuti kuphunzira kulimbana ndi mavuto ukali wamng’ono kumathandiza kuti udzathe kulimbana ndi mavuto aakulu utakula. Masoka, ngakhale ali osakondweretsa, ngosapeweka kwa Mkristu wachichepere kaya wachikulire. (2 Timoteo 3:12) Koma phindu la kukhulupirika limaposa mpumulo wosakhalitsa womwe kugonja kungabweretse.
Ngati ndinu wachichepere, limbanani ndi ziyeso zachikhulupiriro molimba mtima. Pamene muyesedwa kuti muyambe kuchita choipa, musagonje. Ngakhale kuti pa nthaŵiyo zingakhale zovuta kuchita zimenezi, mudzakhala ndi nkhaŵa zocheperapo. Yesu analonjeza kuti: “Senzani goli langa,. . . ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”—Mateyu 11:29, 30.
Lolerani mavuto obwera chifukwa chokhala mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Kutero kudzakupatsani njira yabwino ya moyo tsopano ndiponso chiyembekezo chodalirika cha mtsogolo. Monga momwe Baibulo limanenera, “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.