Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Maliro 1:1–5:22
Yehova Amapereka Chiyembekezo Pakati pa Chisoni
YEHOVA ali “Mulungu wa chiyembekezo,” ngakhale pakati pa chisoni. (Aroma 15:13) lyi ndi nsonga yomwe yamveketsedwa bwino m’bukhu la Maliro, lamalizidwa ndi Yeremiya mneneri ndi mboni ya Yehova mu 607 B.C.E. Koma tiyeni tiwunikire zina za ziphunzitso zomwe liri nazo.
Choyang’anizana Nacho cha Yerusalemu
Chimo silimabweretsa chisangalalo. Tawonani! Yerusalemu wochimwa, kwa ntahŵi imodzi wokhala likulu lodzala la Ayuda, akudzikhalira payekha. Yuda iyemwini ali ngati, mfumu yachikazi yamasiye yolira chifukwa wasakazidwa. “Okondedwa” oterowo onga Igupto sanampulumutse ku kugonjetsa kwa Chibabulo mu 607 B.C.E. Anthu sakupitanso ku Ziyoni kaamba ka mapwando. Ana ake ali a msinga, ndipo adani akuseka kugwa kwake. Alendo odetsedwa anyazitsa kachisi, ndipo anthu ake anayenera kupereka zinthu za mtengo kaamba ka chakudya. Zonsezi chifukwa cha uchimo!—1:1-11.
Yehova ali wolungama m’kulanga ochita zoipa. Ichi chikuvomerezedwa pamene Yerusalemu iyemwini akulankhula. Iye akufunsa ngati pali chisoni chirichonse chonga kupweteka komwe Mulungu anachititsa pa iye. Iye anatumiza moto womwe unapululutsa kachisi. Machimo a mzindawo anakhala goli, ndipo mwazi unatuluka ngati madzi a chipatso pamene Mulungu anaponda “choponderamo mpesa” chake. Ziyoni anatambasula manja m’chisoni ndi kuchonderera koma sanapeze womtonthoza, ndipo Yehova anali wolungama m’kulanga Yerusalemu wowukira. Achite mowopsya ndi adani ake osangalala.—1:12-22.
“Ukali wa Yehova”
Okhala ndi mathayo amakhala ndi liwongo ngati satsutsa chimo. Mulungu anagwetsa Yerusalemu “kuchokera kumwamba kufika pa dziko,” kulola chiwonongeko chake ndi chija cha “mpando wa mapazi” ake, kachisi. (Salmo 132:7) Iye motero “ananyazitsa ufumu” wa Yuda. Monga nyumba wamba ya pa kanthaŵi, kachisi anawonongedwa ndi adani omwe kufuula kwawo kwa chipambano kunali ngati kulira kwa phwando. Ana omafa anapempha chakudya kwa amayi awo. Koma ndani mokulira anali ndi liwongo? Aneneri onyenga omwe anapanga kulengeza kosokeretsa m’malo mwa kutsutsa chimo la Yerusalemu. (Yeremiya 14:13) Pemphero liri loyenera, popeza ambiri afa ‘m’tsiku la ukali wa Yehova’ limeneli!—2:1-22.
Chifundo cha Yehova Chimapirira
Tiyenera kuyembekezera mwa Yehova modekha. Yeremiya akupanga nsongayi pamene akulankhula moimira anthu ovutitsidwa. Mulungu akukaniza pemphero lake, ndipo wakhala mutu wa nkhani ya nyimbo yoseka ya adani ake. Chiyembekezo chake, kapena “chiyang’aniro kuchokera kwa Yehova,” chiwonekera kukhala chinatha. Koma adzakhala ndi “mkhalidwe wa kuyembekezera” chifukwa “Yehova ali wabwino kwa awo oyembekezera mwa iye.”—3:1-27.
Kulapa kowona kumabweretsa chifundo chaumulungu. Atatsimikiziridwa za ichi, Yeremiya akufulumiza kuti: “Lolani tibwerere kwa Yehova.” Monga ngati ndi mtambo waukali, Mulungu watsekereza kumufikira m’pemphero chifukwa ch machimo a anthu. Koma Yeremiya akupemphera kuti: “Ndaitanira dzina lanu, O Yehova. . . . Musabise khutu lanu ku mpumulo wanga.” Ndithudi, adani osalapa adzawonongedwa.—3:28-66.
“Mutitembenuzire kwa Inu”
Tingadzetse chiwonongeko pa ife eni mwa chimo ladala. Chifukwa cha chimo la Yuda, “ana amuna a mtengo wapatali a Ziyoni” anawonedwa ngati mbiya zosweka zopanda pake. M’kuzingidwa, awo ophedwa ndi lupanga anali bwinopo kuposa aja omafa mwapang’onopang’ono ndi njala. Mulungu, ndithudi, “anathiradi ukali wake woyaka.” Aneneri ndi ansembe oipitsidwa anali kupupulika mwa khungu, ndipo Mfumu Zedekiya—“wodzozedwa wa Yehova”—anagwidwa. Tsopano Mulungu akatembenuzira chisamaliro chake kwa Edomu wochimwa.—4:1-22.
Yehova yekha apatsa chiyembekezo chowona pakati pa chisoni. Yeremiya anazindikira ichi, popeza anachonderera kuti: “Kumbukirani, O Yehova, chimene chachitika kwa ife.” ‘Alendo akhala m’nyumba zathu. Tisenza zotulukapo za kulakwa kwa makolo athu, ndipo anyamata wamba asenza nkhuni m’chibalo cha chikakamizo.’ Komabe, Yeremiya akuyembekezera chifundo, akumapemphera kuti: “Tetembenuzireni kwa inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi.”—5:1-22.
Chotero, kenaka, wunikirani pa ziphunzitso zimenezi zophunzitsidwa mu Maliro: Chimo silimabweretsa chisangalalo, Mulungu ali wolungama m’kulanga ochimwa, ndipo athayo ali ndi liwongo ngati satsutsa mchitidwe wolakwa. Tiyenera modekha kuyembekezera mwa Yehova, tikumadalira kuti chifundo Chaumulungu chimabwera chifukwa cha kulapa kowona, pamene kuli kwakuti ife tingabweretse chiwonongeko pa ife eni mwa chimo ladala. Bukhu lowuziridwa limeneli limatitsimikiziranso kuti Yehova yekha amapereka chiyembekezo chowona pakati pa chisoni.
[Bokosi patsamba 27]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
◻ 1:15—‘Yehova anali atapondereza mopondera mpesa mwa namwaliyo mwana wamkazi wa Yuda’ chifukwa analamula ndi kuvomereza chomwe chianchitika. “Namwaliyo mwana wamkazi wa Yuda” anali Yerusalemu, wolingaliridwa kukhala mkazi wosadetsedwa. Pamene Ababulo anawononga likulu la mzinda wa Yuda limeneli mu 607 B.C.E., panali kukhetsedwa mwazi kokulira, koyerekezedwa ndi kupsyinya kwa madzi kuchokera ku mpesa m’zoponderamo mpesa. Yehova adzawona ku ichio kuti Chikristu cha Dziko, mnzake wa Yerusalemu, waphwanyidwa mofananamo.
◻ 2:6—“Dindiro” la Mulungu linali kachisi m’Yerusalemu. Pamene malo opatulika amenewo anawonongedwa ndi Ababulo, iye anali kulola iyo ‘kuichotsera mphamvu,’ mofanana ndi chisimba wamba m’munda. Mthunzi wosakhalitsa woterowo kuchokera ku dzuŵa lotentha umagwetesedwa.
◻ 3:16—Tsoka limodzi limene Yehova analilola kubwera pa Yerusalemu wosakhulupirira monga chotulukapo cha kugwa kwa mzindawo kwa Ababulo likulongosoledwa m’mawu awa, “Wathyolanso mano anga ndi tinsangalabwi.” Mwachidziŵikire, pamene Aisrayeli anali pa ulendo wawo wotuluka, iwo anayenera kuphika mkate wawo m’mayenje okumbidwa pansi. Chotero, mkatewu unakhala ndi timiyala, ndipo munthu wakudya mkate woterowo akakhoza kutyola mbali ya mano ake.
◻ 4:3—Nkhalwe ya amayi kulinga kwa ana awo pano ikusiyanitsidwa ndi chisamaliro cha umayi choperekedwa ndi nkhandwe. Ngakhale kuti nkhandwe zingalingaliridwe kukhala zirombo zolusa, ngakhaledi izo ‘zimapereka bele kuyamwitsa ana awo.’ Chifukwa cha kupereŵera kwa chakudya kokulira m’Yerusalemu wolaliridwayo, akazi Achiyuda a njala anakhala ankhalwe m’chakuti analibe mkaka wopereka kwa mbadwa zawo ndipo m’chenicheni anadya ana awo kuti akhale ndi moyo. (Maliro 2:20) Chotero, akaziwo anakhalanso ngati nthiwatiwa zomwe zimaikira mazira awo ndi kuwaleka iwo.
◻ 5:7—Ayuda a m’tsiku la Yeremiya anayenera kuchita ndi zolakwa za makolo awo, koma ichi sichitanthauza kuti Yehova mwachindunji amalanga ana chifukwa cha machimo a makolo awo. M’chenicheni, zotulukapo zoipa za kuchita cholakwa zimamvedwa ndi mibadwo ya pambuyo pake. (Yeremiya 31:29, 30) Ife chotero tidzachita bwino kukumbukira kuti ife mwaumwini timaŵerengera kwa Mulungu.—Aroma 14:12.