Amithenga a Mtendere Waumulungu Atchedwa Achimwemwe
“Oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yawo.” —YESAYA 35:10.
1. Kodi nchiyani chimene dzikoli likufunitsitsa?
MOSIYANA ndi kale lonse, lerolino mtundu wa munthu ukufunitsitsa mthenga wa uthenga wabwino. Wina woti anene choonadi ponena za Mulungu ndi zifuno zake akufunika mwamsanga, mboni yopanda mantha imene idzachenjeza oipa za chiwonongeko chilinkudzacho ndi kuthandiza anthu oona mtima kupeza mtendere waumulungu.
2, 3. Kwa Israyeli, kodi Yehova anakwaniritsa motani lonjezo lake lolembedwa pa Amosi 3:7?
2 M’nthaŵi ya Israyeli, Yehova analonjeza kuti adzapereka amithenga otero. Kumapeto kwa zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., mneneri Amosi anati: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” (Amosi 3:7) Zaka mazana zotsatira chilengezochi, Yehova anachita zinthu zamphamvu zambiri. Mwachitsanzo, mu 607 B.C.E., analanga koŵaŵa anthu ake osankhidwa chifukwa chakuti anampandukira ndipo anali ndi liwongo la mwazi. Analanganso mitundu yozungulira imene inakondwera ndi kuvutika kwa Israyeli. (Yeremiya, machaputala 46-49) Kenako, mu 539 B.C.E., Yehova anachititsa kugwa kwa ulamuliro wamphamvu wachibabulo wa dziko lonse, ndipo chifukwa cha zimenezo, mu 537 B.C.E., otsalira a Israyeli anabwerera kudziko lawo kukamanganso kachisi.—2 Mbiri 36:22, 23.
3 Zimenezi zinali zochitika zazikulu kwambiri, ndipo monga mwa mawu a Amosi, Yehova anaziulula pasadakhale kwa aneneri amene anatumikira monga amithenga, ochenjeza Israyeli za zimene zinali kudza. Chapakati pa zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., iye anautsa Yesaya. Chapakati pa zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E., anautsa Yeremiya. Ndiyeno, chakumapeto kwa zaka za zana limenelo, anautsa Ezekieli. Ameneŵa ndi aneneri ena okhulupirika anapereka umboni wosamalitsa ponena za zifuno za Yehova.
Kudziŵa Amithenga a Mulungu Lerolino
4. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti mtundu wa munthu ukufuna amithenga a mtendere?
4 Bwanji nanga lerolino? Ambiri m’dziko lerolino amachita mantha pamene aona kunyonyotsoka kwa chikhalidwe cha anthu. Awo amene amakonda chilungamo amapwetekedwa mtima pamene aona chinyengo ndi kuipa kwadzaoneni kwa Dziko Lachikristu. Monga momwe Yehova ananeneratu kudzera mwa Ezekieli, iwo “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.” (Ezekieli 9:4) Komabe, ambiri sakudziŵa kuti zifuno za Yehova ndi zotani. Ayenera kuuzidwa.
5. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti m’tsiku lathu kudzakhala amithenga?
5 Kodi lero pali aliyense amene amalankhula ndi mzimu wopanda mantha wa Yesaya, Yeremiya, ndi Ezekieli? Yesu anasonyeza kuti wina wake adzatero. Poneneratu za zochitika za m’tsiku lathu, iye anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Kodi ndani lerolino amene akukwaniritsa ulosiwo, amene akutumikira monga mthenga, mlaliki wa uthenga wabwino? Kufanana pakati pa tsiku lathu ndi nthaŵi ya Israyeli wakale kumatithandiza kuyankha funsolo.
6. (a) Fotokozani zokumana nazo za “Israyeli wa Mulungu” m’nkhondo yoyamba ya dziko. (b) Kodi Ezekieli 11:17 anakwaniritsidwa motani pa Israyeli wakale?
6 M’masiku amdima a Nkhondo Yadziko I, anthu amakono a Yehova, otsalira a “Israyeli wa Mulungu” wodzozedwayo, analoŵa mu undende wonga uja wa Israyeli ku Babulo. (Agalatiya 6:16) Anavutika mu undende wauzimu m’Babulo Wamkulu, mgwirizano wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, umene mbali yake yaikulu ndi yaliwongo koposa ndiyo Dziko Lachikristu. Komabe, mawu a Yehova kwa Ezekieli anasonyeza kuti sanasiyidwe kumeneko. Iye anati: “Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m’maiko mmene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.” (Ezekieli 11:17) Kuti akwaniritse lonjezo limenelo kwa Israyeli wakale, Yehova anautsa Koresi Mperisi, amene analanda Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Babulo ndi kutsegulira njira otsalira a Israyeli kuti abwerere ku dziko lakwawo. Koma bwanji lerolino?
7. Kodi ndi chochitika chotani cha mu 1919 chimene chinasonyeza kuti Yesu anachita motsutsana ndi Babulo Wamkulu? Fotokozani.
7 Kuchiyambi cha zaka za zana lino, kunali umboni wamphamvu wakuti Koresi Wamkulu akugwira ntchito. Kodi anali yani? Palibe wina koma Yesu Kristu, amene analongedwa ufumu chiyambire 1914 mu Ufumu wakumwamba. Mfumu yaikuluyo inasonyeza kukoma mtima kwa abale ake odzozedwa padziko lapansi pamene, m’chaka cha 1919, Akristu odzozedwa anamasulidwa mu undende wauzimu ndi kubwerera ‘kudziko’ lawo, munda wawo wauzimu. (Yesaya 66:8; Chivumbulutso 18:4) Choncho Ezekieli 11:17 anali ndi kukwaniritsidwa kwamakono. M’nthaŵi zakale kunafunika kuti Babulo agwe kuti njira itseguke yoti Aisrayeli abwerere ku dziko lawo. M’nthaŵi zamakono kubwezeretsedwa kwa Israyeli wa Mulungu kunali umboni wakuti Babulo Wamkulu anagwetsedwa ndi Koresi Wamkulu. Kugwa kumeneku kunalengezedwa ndi mngelo wachiŵiri wa pa Chivumbulutso chaputala 14, pamene anafuula kuti: “Wagwa, Babulo waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.” (Chivumbulutso 14:8) Kunali kubwerera m’mbuyo kotani nanga kwa Babulo Wamkulu, makamaka Dziko Lachikristu! Ndipo linalitu dalitso lalikulu chotani nanga kwa Akristu oona!
8. Kodi buku la Ezekieli limafotokoza motani chimwemwe cha anthu a Mulungu atamasulidwa mu 1919?
8 Pa Ezekieli 11:18-20, timaŵerenga mafotokozedwe a mneneriyo a chimwemwe cha anthu a Mulungu atabwezeretsedwa. Kukwaniritsidwa koyamba kwa mawu ake kunatanthauza kuyeretsedwa kwa Israyeli m’masiku a Ezara ndi Nehemiya. Kukwaniritsidwa kwamakono kunatanthauza chinachake chofanana nacho. Tiyeni tione kuti ndi motani. Yehova akuti: “Adzafikako [kudziko lawo], nadzachotsako zonyansa zake zonse, ndi zake zonse zakuipitsamo.” Monga mwa ulosiwo, kuyambira mu 1919, Yehova anayeretsa anthu ake ndi kuwapatsanso nyonga kuti amtumikire. M’malo awo auzimu anayamba kuchotsa machitachita onse achibabulo ndi ziphunzitso zake zimene zinawaipitsa m’maso mwake.
9. Kodi ndi madalitso aakulu otani amene Yehova anapatsa anthu ake, chiyambire 1919?
9 Kenako, malinga ndi vesi 19, Yehova akupitiriza kuti: “Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano mkati mwawo; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m’thupi mwawo, ndi kuwapatsa mtima wamnofu.” Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, mu 1919, Yehova anagwirizanitsa atumiki ake odzozedwa, kuwapatsa “mtima umodzi,” titero kunena kwake, kuti amtumikire “pheŵa ndi pheŵa.” (Zefaniya 3:9, NW) Ndiponso, Yehova anapatsa anthu ake mzimu woyera kuti akhale ndi nyonga pantchito yochitira umboni ndi kuti abale zipatso zabwino zolongosoledwa pa Agalatiya 5:22, 23. Ndipo m’malo mwa mtima wouma, wonga mwala, Yehova anawapatsa mtima wofeŵa, wolabadira, ndi womvera, mtima umene udzatsatira chifuniro chake.
10. Kodi nchifukwa ninji Yehova wadalitsa anthu ake obwezeretsedwa chiyambire 1919 kumka mtsogolo?
10 Kodi anachitiranji zimenezi? Yehova iye mwini akufotokoza. Timaŵerenga pa Ezekieli 11:20 kuti: “Kuti ayende m’malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo adzakhala anthu anga, ndi Ine ndidzakhala Mulungu wawo.” Israyeli wa Mulungu ameneyo anaphunzira kulabadira malamulo a Yehova m’malo motsatira zolingalira zawo. Anaphunzira kuchita chifuniro cha Mulungu mosaopa munthu. Chifukwa chake, iwo anaonekeratu kuti ali osiyana ndi Akristu oyerekezera a m’Dziko Lachikristu. Iwo anali anthu a Yehova. Ndiye chifukwa chake, Yehova anali wofunitsitsa kuwagwiritsira ntchito monga mthenga wake, “kapolo [wake] wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
Chimwemwe cha Amithenga a Mulungu
11. Kodi buku la Yesaya limachifotokoza motani chimwemwe cha anthu a Yehova?
11 Kodi mungathe kuyerekezera chimwemwe chawo atazindikira kuti anali pamalo apamwamba? Onse pamodzi, anabwereza mawu a Yesaya 61:10 akuti: “Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga.” Lonjezo la Yesaya 35:10 linakwaniritsidwa pa iwo: “Oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yawo; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.” Chimenechi ndicho chinali chimwemwe cha amithenga a Yehova a mtendere waumulungu kalelo mu 1919 pamene anayamba kulalikira uthenga wabwino kwa mtundu wonse wa munthu. Chiyambire pamenepo kudzafika lero, iwo sanaleke kuchita ntchitoyi, ndipo chimwemwe chawo chawonjezeka. Pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: “Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.” (Mateyu 5:9) Kuona kwa chilengezo chimenecho kwatsimikizidwa ndi otsalira a “ana a Mulungu” odzozedwawo chiyambire 1919 mpaka lero.
12, 13. (a) Kodi ndani anagwirizana ndi Israyeli wa Mulungu pa kutumikira Yehova, ndipo anadzipereka pa kuchitanji? (b) Kodi ndi chimwemwe chachikulu chotani chimene atumiki odzozedwa a Yehova akhala nacho?
12 Pamene zaka zinali kupita, chiŵerengero cha Israyeli wa Mulungu chinakula mpaka cha m’ma 1930 pamene kusonkhanitsa kwa otsala a odzozedwa kunali pafupi kutha. Kodi kuwonjezeka kwa alaliki a uthenga wabwino kunalekera pamenepo? Kutalitali. Khamu lalikulu la Akristu a chiyembekezo cha padziko lapansi anali atayamba kale kuonekera, ndipo ameneŵa anali kugwirizana ndi abale awo odzozedwa m’ntchito yolalikira. Mtumwi Yohane anaona khamu lalikulu limeneli m’masomphenya, ndipo akuwafotokoza mochititsa chidwi kuti: “Ali ku mpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 7:15) Inde, khamu lalikulu linatanganitsidwa ndi kutumikira Mulungu. Chotero, pamene chiŵerengero cha odzozedwa chinayamba kutsika, pambuyo pa 1935, ntchito yolalikira inapitabe patsogolo mwamphamvu yowonjezereka ndi atsamwali okhulupirika ameneŵa.
13 Mwa njira imeneyo Yesaya 60:3, 4 anakwaniritsidwa: “Amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kutuluka kwako. Tukula maso ako uunguzeunguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako aamuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.” Chimwemwe chimene zochitikazi zinadzetsa kwa Israyeli wa Mulungu chafotokozedwa bwino kwambiri pa Yesaya 60:5, pamene timaŵerenga kuti: “Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukudziwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.”
Gulu la Yehova Likupita Patsogolo
14. (a) Kodi ndi masomphenya otani a zinthu zakumwamba amene Ezekieli anaona, ndipo analandira lamulo lotani? (b) Kodi anthu a Yehova m’nthaŵi zamakono anazindikiranji, ndipo anaona kuti ali ndi ntchito yotani?
14 Mu 613 B.C.E., Ezekieli anaona m’masomphenya gulu la Yehova lakumwamba longa gareta likuyenda mopita patsogolo. (Ezekieli 1:4-28) Pambuyo pake, Yehova anati kwa iye: “Wobadwa ndi munthu iwe, Muka, nufike kwa nyumba ya Israyeli, nunene nawo mawu anga.” (Ezekieli 3:4) M’chaka chino cha 1997, tikuzindikira kuti gulu lakumwamba la Yehova likupitabe patsogolo mosalekeza kuti likwaniritse zifuno za Mulungu. Ndiye chifukwa chake timasonkhezerekabe kuuza ena za zifuno zimenezo. M’tsiku lake, Ezekieli ananena mawu amene anali ouziridwa mwachindunji ndi Yehova. Lerolino, timanena mawu a m’Mawu ouziridwa a Yehova, Baibulo. Ndipotu bukulo lili ndi uthenga wabwino chotani nanga kwa mtundu wa munthu! Pamene kuli kwakuti ambiri akuda nkhaŵa ndi mtsogolo, Baibulo limasonyeza kuti zinthu nzoipa kwambiri—ndipo panthaŵi imodzimodziyo, zili bwino kwambiri—kuposa mmene amaganizira.
15. Kodi nchifukwa ninji zinthu nzoipa kwambiri kuposa mmene ambiri amaganizira?
15 Zinthu nzoipa kwambiri chifukwa, monga tinaphunzirira m’nkhani zathazo, Dziko Lachikristu ndi zipembedzo zina zonse zonyenga zidzawonongedwa posachedwapa, kuwonongedweratu monga Yerusalemu mu 607 B.C.E. Ndiponso, gulu lonse landale la padziko lonse, losonyezedwa m’buku la Chivumbulutso monga chilombo cha mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi, lili pafupi kufafanizidwa, monga zinachitikira kwa mitundu yachikunja yoyandikana ndi Yerusalemu. (Chivumbulutso 13:1, 2; 19:19-21) M’tsiku la Ezekieli Yehova anafotokoza mwatsatanetsatane mantha ochititsidwa ndi chiwonongeko cha Yerusalemu chomwe chinali pafupi. Koma mawu akewo adzakhala atanthauzo kwambiri pamene anthu adzazindikira za chiwonongeko cha dzikoli chomwe chili pafupi kwambiri. Yehova anati kwa Ezekieli: “Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuŵaŵa mtima, uuse moyo pamaso pawo. Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo chifukwa ninji? Uzikati, Chifukwa cha mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uliwonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uliwonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona ilinkudza, inde idzachitika, ati Ambuye Yehova.” (Ezekieli 21:6, 7; Mateyu 24:30) Zochitika zochititsa mantha zili pafupi kwenikweni. Kudera nkhaŵa kwambiri anthu anzathu kumatisonkhezera kupereka chenjezolo, kuwauza “mbiri” ya mkwiyo wa Yehova ulinkudzawo.
16. Kwa ofatsa, kodi nchifukwa ninji zinthu zili bwino kwambiri kuposa mmene ambiri amaganizira?
16 Nthaŵi imodzimodziyo, kwa ofatsa zinthu zili bwino kwambiri kuposa mmene anthu ambiri amaganizira. M’njira yotani? M’njira yakuti Yesu Kristu anafera machimo athu ndipo tsopano akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. (1 Timoteo 1:15; Chivumbulutso 11:15) Mavuto a mtundu wa munthu amene amaoneka monga sangathetsedwe adzathetsedwa posachedwapa ndi Ufumu wakumwambawo. Imfa, matenda, ukatangale, njala, ndi chiwawa zidzakhala zinthu zakale, ndipo Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lapansi la paradaiso popanda wina wotsutsana nawo. (Chivumbulutso 21:3, 4) Mtundu wa munthu udzasangalala ndi mtendere waumulungu—unansi wamtendere ndi Yehova Mulungu ndiponso ndi wina ndi mnzake.—Salmo 72:7.
17. Kodi ndi ziwonjezeko zotani zimene zikudzetsa chimwemwe mumtima wa amithenga a mtendere waumulungu?
17 M’mbali zina za dziko, makamu aakulu kwambiri a ofatsa akulabadira uthengawu wa mtendere waumulungu. Kungotchula zitsanzo zingapo zokha, chaka chatha Ukraine anachitira lipoti chiwonjezeko cha 17 peresenti cha ofalitsa. Mozambique anachitira lipoti chiwonjezeko cha 17 peresenti, Lithuania chiwonjezeko cha 29 peresenti. Russia anali ndi chiwonjezeko cha 31 peresenti, pamene kuli kwakuti Albania anali ndi chiwonjezeko cha 52 peresenti cha ofalitsa. Ziwonjezeko zimenezi zikuimira anthu oona mtima zikwizikwi amene akufuna kukhala ndi mtendere waumulungu ndi amene aima kumbali ya chilungamo. Kukula mwamsanga kumeneku kumadzetsa chimwemwe pa gulu lonse la abale lachikristu.
18. Kaya anthu amvetsera kapena samvetsera, kodi tidzakhala ndi mzimu wotani?
18 Kodi kumene mumakhala anthu amalabadira mosavuta? Ngati zili tero, tikondwa nanu. Komabe, m’magawo ena, mumafunika kugwira ntchito molimbika maola ambirimbiri musanapeze munthu wochita chidwi ndi mmodzi yemwe. Kodi awo amene akutumikira m’magawo otero amagwetsa manja awo kapena kutaya mtima? Ayi. Mboni za Yehova zimakumbukira mawu a Mulungu kwa Ezekieli nthaŵi yoyamba pamene Iye anatuma mneneri wachichepereyo kukalalikira kwa Ayuda anzake kuti: “Ndipo iwowa, ngakhale akamva kapena akaleka kumva, (pakuti ndiwo nyumba yopanduka,) koma adzadziŵa kuti panali mneneri pakati pawo.” (Ezekieli 2:5) Monga Ezekieli, timapitirizabe kuuza anthu za mantha aumulungu kaya adzamva kapena sadzamva. Akamvetsera, timakondwa kwambiri. Ngati atikana, kutitonyola, ngakhale kutizunza, timapirira. Timamkonda Yehova, ndipo Baibulo limati: “Chikondi . . . chipirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:4, 7) Chifukwa chakuti timalalikira ndi chipiriro, anthu amadziŵa kuti Mboni za Yehova ndani. Akudziŵa uthenga wathu. Pamene mapeto adzabwera, adzadziŵa kuti Mboni za Yehova zinayesa kuwathandizira kupeza mtendere waumulungu.
19. Monga atumiki a Mulungu woona, kodi ndi mwaŵi waukulu uti umene tikuuona kukhala wofunika?
19 Kodi pali mwaŵi wina waukulu woposa kutumikira Yehova? Iyayi! Chimwemwe chathu chachikulu chimachokera paunansi wathu ndi Mulungu ndi kudziŵa kuti tikuchita chifuniro chake. “Odala anthu odziŵa liwu la lipenga; Ayenda m’kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.” (Salmo 89:15) Nthaŵi zonse tione kufunika kwa chisangalalo chakuti ndife amithenga a mtendere a Mulungu kwa mtundu wa munthu. Mwakhama tichitetu mbali yathu m’ntchitoyi mpaka pamene Yehova adzati yatha.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi amithenga a mtendere a Mulungu lerolino ndani?
◻ Timadziŵa motani kuti Babulo Wamkulu anagwa mu 1919?
◻ Kodi nkhaŵa yaikulu ya “khamu lalikulu” nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji mtsogolo ndi moipa kwambiri kuposa mmene anthu ambiri amaganizira lerolino?
◻ Kwa oongoka mtima, kodi nchifukwa ninji mtsogolo mudzakhala bwino kwambiri kuposa mmene amaganizira?
[Zithunzi patsamba 21]
Pamene aona kunyonyotsoka kwa chikhalidwe cha anthu, ambiri amachita mantha
[Zithunzi patsamba 23]
Amithenga a mtendere waumulungu ndiwo anthu achimwemwe koposa padziko lapansi lerolino