Yehova Asolola Lupanga Lake!
“Anthu onse adzadziŵa kuti ine, Yehova, ndasolola lupanga langa m’chimake.”—EZEKIELI 21:5.
1. Ndi molimbana ndi ndani amene Yehova anaponyera lupanga lake mu Yuda ndi Israyeli?
LUPANGA la Yehova moyenerera limapereka mantha mwa adani ake. Koma pamene iye analiponya ilo motsutsana ndi ochita zolakwa mu mafumu a Yuda ndi Israeyli, kodi iwo ndithudi anadziŵa chomwe chinali kuchitika? Inde, iwo anapangidwa kudziŵa kuti Yehova anatulutsa lupanga lake lophiphiritsira kuchokera m’chimake.—Ezara 9:6-9; Nehemiya 1:8; 9:26-30.
2. Nchiyani chimene Yehova ananena ponena za “lupanga” lake, kudzutsa mafunso otani?
2 Kupyolera mwa mneneri wake ndi mlonda Ezekieli, Mulungu ananena kuti: “Anthu onse adzadziŵa kuti ine, Yehova, ndasolola lupanga langa m’chimake.” (Ezekieli 21:5) Kodi mawu amenewo anagwira ntchito kokha m’nthaŵi zakale? Kapena kodi iwo ali ndi tanthauzo kaamba ka ife?
Kuneneratu kwa Chiŵeruzo cha Yerusalemu
3. Nchiyani chimene Ezekieli anauza andende mu Babulo, ndipo ichi chiri ndi kufanana nako kotani kwamakono?
3 Gareta wa Yehova anayendanso, ndipo malo a Ezekieli anasinthanso. Chinali ngati kuti gulu lakumwamba la Mulungu longa gareta linapita ku malo owonera pamwamba pa Phiri la Azitona. Kuchokera pamenepo Yesu ananeneratu kuwonongedwa komwe kunadza pa Yerusalemu mu 70 C.E., kusakaza kolosera kwa kutha kwa Chikirstu cha Dziko. (Marko 13:1-20) M’masomphenya, Ezekieli iyemwini anatengedwa kuchokera ku mtsinje wa Kebara, koma ndi mzimu wa Mulungu iye tsopano anabwezeretsedwa ku nyumba yake ya ndende mu Babulo. Kemeneko iye anauza andende ena ‘zonse zimene Yehova adamuwonetsa.’ Mofananamo, “mlonda” wodzozedwa wa Mulungu ndi mboni zoyanjana nazo lerolino zimalengeza zonse zomwe zavumbulutsidwa kwa iwo ndi Wokwera pa gareta ya kumwambayo.—Ezekieli 11:22-25.
4. Ndimotani mmene andende Achiyuda anavomerezera ku zochita zophiphiritsira za Ezekieli?
4 Kupyolera mwa machitidwe ophiphiritsira, Ezekieli anasonyeza Ayuda andende kuti stoka la mtunduwo linali kuyandikira. (Ŵerengani Ezekieli 12:1-7.) Mneneriyo ananyamula “katundu wa pa ulendo wa kundende” kuchitira chithunzi zinthu zochepera zimene ogwidwa akakhoza kunyamula pa mapewa awo. Mantha mwamsanga akafalikira m’Yerusalemu wozingidwayo. Ngakhale kuti ambiri sanatenge machenjezo oterowo mosamalitsa, Ezekieli anayenera kuuza anthuwo kuti: “Palibe amodzi a mawu anga adzazengerezekanso.” Leronso pali kusoweka kwa ulemu kaamba ka machenjezo ndi maulosi aumulungu, koma tingachite zochuluka kuthandiza ofuna chowonadi kuika chidaliro chawo m’kukwaniritsidwa kwawo.—Ezekieli 12:8-28.
5. Popeza “tsiku la Yehova” linali kuyandikira, ndi ziweruzo zotani zimene zinali zoyenera?
5 Awo amene sanali kumvetsera kwa mlonda wa Yehova anafunikira kudziŵa kuti iwo akamva “lupanga” la Mulungu. Chotero, awo amene ali ndi thayo la malingaliro oipa ponena za chisungiko cha Yerusalemu ndi Yuda anatsutsidwa. Aneneri onyenga anayerekezedwa ndi ankhadwe osakaza, ndipo chinasonyezedwa kuti onama anali kupaka njereza malinga omagwa, kapena zinthu zopanda pake, za anthuwo. Aneneri achikazi onyenga anatsutsidwanso. “Tsiku la Yehova” linayandikira, ndipo nkhope yake inalunjikitsidwa motsutsana ndi awo ‘ochoka kwa iye,’ kunena kuti, ‘odzipereka iwo eni kuchoka ku kutsatira Mulungu.’ Ngati tiri odzipereka kwa Yehova, ndithudi sitikafuna kuchoka ku utumiki wake wopatulika.—Ezekieli 13:1-14:11.
6. Kodi munthu aliyense akanapulumutsa anthu opanduka a Yuda, ndipo nchiyani chimene ichi chikutiphunzitsa?
6 Ndani yemwe akanapulumutsa anthu opatuka a Yuda? Osati ngakhale Nowa wolungama, Danieli, ndi Yobu akanakhoza kuwapulumutsa iwo pamene Mulungu anabweretsa ziŵeruzo zake pa dzikolo. Ngati tikayenera kukumanizana ndi chipulumutso, chotero, tiyenera kutenga thayo lathu laumwini pamaso pa Mulungu ndi kuchita chifuniro chake.—Ezekieli 14:12-23; Aroma 14:12.
7. Kodi Yuda anayerekezedwa ndi chiyani, komabe nchiyani chimene Mulungu akakhazikitsa ndi okhulupirika?
7 Chifukwa cha nzika zake zosakhulupirika, Yuda anayerekezedwa ndi mtengo wa mpesa wopanda chipatso chabwino ndipo woyenerera kokha kaamba ka moto. (Ezekieli 15:1-8) Iye anayerekezedwanso ndi khanda lotaidwa lopulumutsidwa ndi Mulungu kuchokera ku Igupto ndi kuleredwa kufikira ku ukazi. Yehova anamtenga iye monga mkazi wake, koma iye anatembenukira ku milungu yonyenga ndipo akavutika ndi chiwonongeko kaamba ka chigololo chake chauzimu. Komabe, ndi okhulupirika Mulungu ‘akakhazikitsa pangono losatha’—pangano latsopano ndi Israyeli wauzimu.—Ezekieli 16:1-63; Yeremiya 31:31-34; Agalatiya 6:16.
8. (a) Kodi Babulo ndi Igupto anayerekezedwa ndi chiyani? (b) Ndimotani mmene kuswa lumbiro lake kwa Zedekiya kuyenera kutiyambukirira ife?
8 Chotsatira, olamulira a Babulo ndi Igupto anayerekezedwa ndi ziwombankhanga zazikulu. Chimodzi chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza mwa kuchotsa Mfumu Yehoyakini ndi kumulowa m’malo iye ndi Zedekiya. Ngakhale kuti Zedekiya anatenga lumbiro lokhulupirika kwa Nebukadinezara, iye analiswa ilo, kufunafuna thandizo lankhondo la wolamulira wa Igupto, chiwombankhanga china chachikulu. Ngati Zedekiya anaphatikizapo dzina la Mulungu m’kupanga lumbiro lake, kuswa ilo kunabweretsa chitonzo pa Yehova. Lingaliro lenileni la kubweretsa chitonzo pa Mulungu liyenera kutiletsa ife kuchoka ku kutsimikizira kukhala onama ku mawu athu. Ife tiridi ndi mwaŵi wa kutenga dzina laumulungu monga Mboni za Yehova! —Ezekieli 17:1-21.
9, 10. (a) Ndi ulosi wotani umene walembedwa pa Ezekieli 17:22-24, koma nchiyani chomwe chiyenera kuchitidwa ngati tikayenera kupindula kuchokera ku kukwaniritsidwa kwake? (b) Ndani amene ali ndi thayo kaamba ka zotulukapo za mkhalidwe wathu?
9 Ulosi wa Umesiya wotenthetsa maganizo ukubwera potsatira. (Ŵerengani Ezekieli 17:22-24.) Pano, “ya nthete” iri Mfumu ya Umesiya, Yesu Krstu. Wodzalidwa ndi Yehova pa Phiri la Ziyoni la kumwamba, iye akakhala “nkungudza wokoma,” magwero a chitetezero ndi dalitso pamene adzalamulira dziko lapansi. (Chivumbulutso 14:1) Mu ichi ndithudi tingachirimike.
10 Ngati tikayenera kupindula kuchokera ku kukwaniritsdiwa kwa ulosi wa Umesiya, ngakhale kuli tero, tiyenera kusungirira unansi wabwino ndi Yehova. Andende anzake a Ezekieli mwachidziŵikire analingalira kuti iwo anali ndi kaimidwe kabwino ndi Mulungu ndipo anapatsa mlandu atsogoleri awo kaamba ka kuvutika kwawo. Koma mneneriyo analunjikitsa kuti munthu aliyense ali ndi thayo kaamba ka zotulukapo za mkhalidwe wa iyemwini. (Ezekieli 18:1-29; yerekezani Yeremiya 31:28-30.) Kenaka kunabwera kuchonderera. (Ŵerengani Ezekieli 18:30-32.) Inde, Yehova ali ndi chifundo kwa olapa ndipo satenga chikondwerero mu imfa ya aliyense. Chotero, Mulungu akunena kuti: ‘Bwererani ndi kukhala ndi moyo, anthu inu.’—Yerekezani ndi 2 Petro 3:9.
11. Kodi olamulira a Yuda anayerekezedwa ndi chiyani, ndipo nchiyani chimene chikachitika kwa iye pamene anakanthidwa ndi “lupanga” la Yehova?
11 Mu nyimbo ya maliro a kugwa kwa Yuda, olamulira ake anayerekezedwa ndi mikango yaing’ono. Mfumu Yehoyahazi anafa m’ndende ya Chiigupto, Yehoyakimu anagwidwa ndi Nebukadinezara, ndipo Yehoyakini anaikidwa m’ndende ku Babulo. Nebukadinezara potsatira anaika Zedekiya pa mpando wachifumu wa Yuda, koma iye anaukira. Kotheratu, monga mkango woikidwa m’chisa, Zedekiya ananyamulidwa wandende kupita ku Babulo. M’kusunga ndi nyimbo ya maliro ya ulosi, mu 607 B.C.E., Yuda anakhala mtengo wa mpesa wowonongedwa, “momwemo ulibe ndodo yolimba, ikhale ndodo yachifumu ya kuchita ufumu.” Iye anakanthidwa ndi “lupanga” la Yehova!—Ezekieli 19:1-14; Yeremiya 39:1-7.
12. (a) Mofanana ndi otsogolera awo, ndi m’cholakwa chotani chimene anzake a Ezekieli anadzilowetsamo? (b) Nchifukwa ninji anthu anafunsa ngati Ezekieli sanali kupanga mafanizo, ndipo ndi chenjezo lotani limene ichi chikupereka kaamba ka ife?
12 Atafikiridwa ndi “akulu ena a Israyeli,” Ezekieli analankhula uthenga wa Mulungu. Iye analoza kuti ngakhale kuti Yehova anapulumutsa Aisrayeli kuchoka ku Igupto ndi kuwapatsa iwo Lamulo Lake, iwo analikana ilo ndi kuchita kulambira mafano. Popeza anzake a Ezekieli anali ndi liwongo la kachitidwe kolakwa kofananako, Mulungu akadziika iyemwini pa chiŵeruzo motsutsana ndi iwo. Mwachidziŵikire ndi kukaikira ndipo osati chifukwa chakuti iwo sanamvetsetse zimene Ezekieli anatanthauza, anthu anafunsa kuti: “Kodi iye sakunena mafanizo?” Iwo posachedwa akadziŵa kuti panalibe chinachake cha mafanizo popena za uthenga wa mneneriyo. Ichi chiyenera kutichenjeza ife kusatengera mkhalidwe wokaikira kulinga ku kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Malemba.—Ezekieli 20:1-49.
Yehova Wankhondo
13. “Lupanga” la Mulungu limasonyeza chiyani, ndipo nchiyani chimene “anthu onse” akapangidwa kudziŵa pamene lupanga limenelo likagwiritsiridwa ntchito?
13 M’chaka cha chisanu ndi chiŵiri cha kukhala m’ndende (kufika Ab 10, 611 B.C.E.), zochepera pa zaka ziŵiri ndi theka zinatsala “nkhondo m’tstiku la Yehova” isanayambe motsutsana ndi Yuda ndi Yerusalemu. (Ezekieli 13:5; 20:1) Dziŵani chimene Yehova Wankhondo kenaka ananena kupyolera mwa Ezekieli. (Ŵerengani Ezekieli 21:1-5.) “Lupanga” la Mulungu limaimira nthumŵi za pa dziko lapansi zimene iye akazigwiritsira ntchito, koma zingaphatikizepo gulu lake la kumwamba, longa gareta. Nzika “zolungama” ndi “zoipa” za Yuda ndi Israyeli, limodzinso ndi mitundu yokhala ndi chifuno choipa kulinga kwa anthu a Mulungu, zikagwa ndi nsonga ya “lupanga” la Mulungu. Ndithudi, “anthu onse” akapangidwa kudziŵa kuti Yehova anali kumenyana nawo.
14. (a) Mofanana ndi Ezekieli, nkuchiyani kumene mboni zodzozedwa za Yehova zikuitanira chisamaliro? (b) Nchiyani chomwe chikusonyeza kuti atsogoleri a Chikristu cha Dziko sadzapulumuka “lupanga” la Mulungu”?
14 Mofanana ndi Ezekieli, mboni zodzozedwa za Yehova lerolino zimaitanira chisamaliro ku “lupanga” limene Mulungu akaligwiritsira ntchito molimbana ndi atsatiri a Chikirstu cha Dziko, mabwalo ake amene ali “nthaka ya Israyeli” yophiphiritsira. Mwamsanga “lupanga” limenelo likamvedwa ndi “anthu onse kuchokera kum’mwera kufika kumpoto,” ndi onse amene apanga chipembedzo chonyenga. Odzitsimikizira iwo eni a m’tsiku la Ezekieli analibe chifukwa cha kudzitukumulira, akumamaliza kuti “lupanga” la Yehova silikawapha” iwo. “Lupanga” limenelo linakana ndodo yachifumu yaufumu wa Yuda, mongadi mmene linakanira “mtengo” wina uliwonse, kapena ndodo yachifumu. Ndithudi, chotero, atsogoleri a Chikristu cha Dziko sadzasiidwa ndi nthumwi zakupha za Mulungu.—Ezekieli 21:6-17.
15. Ndi chochitika chotani chokhudza Nebukadinezara chimene chikusonyeza kuti palibe wina aliyense amene angatembenuzire kumbali “lupanga” la Yehova?
15 Ulosi wa Ezekieli ukupitiriza kusonyeza kuti palibe aliyense, kuphatikizapo ziwanda, amene angatembenuzire kumbali “lupanga” la Yehova. (Ŵerengani Ezekieli 21:18-22.) Ngakhale kuti Mfumu Nebukadinezara akagwiritsira ntchito kuwombeza maula kwa uchiwanda, Yehova akawona ku icho kuti wolamulira Wachibabulo akayenda molimbana ndi Yerusalemu, osati molimbana ndi likulu lofooka la Amoni la Raba. Kuchokera mu chotengera Nebukadinezara akasankha muvi woikidwa chizindikiro kaamba ka Yerusalemu. Iye akagwiritsira ntchito terafi (wachidziŵikire, mafano ang’ono mu mtundu wa munthu) ndipo akafunafuna kaamba ka zinzindikiro mu chiwindi cha nyama yophedwa. Mosasamala kanthu za kuwombeza maula, ngakhale kuli tero, iye akatenga msewu wopita ku likulu la Yuda ndi kulizinga ilo. Zowona, Nebukadinezara anapanga pangano ndi Mfumu Zedekiya. Koma chifukwa cha kuswa kwawo lumbiro, Zedekiya ndi Ayuda ena “akagwidwa pa dzanja” ndi kutsogozedwa andende ku Babulo.—Ezekieli 21:23, 24.
16. (a) Nchiyani chomwe chinachitika m’kukwaniritsa Ezekieli 21:25-27? (b) Ndi liti pamene Nthaŵi za Akunja zinayamba, ndipo kodi izo zinatha ndi chochitika chotani?
16 Mwa kupanduka, Zedekiya anadzivulaza iyemwini m’njira yakupha. (Ŵerengani Ezekiel 21:25-27.) Pamene mfumu ya Yuda inagwetsedwa, nduwira yachifumu ndi chisote chachifumu zinachotsedwa. (2 Mafumu 25:1-7) Ufumu “wokwezeka” wa Yuda ‘unatsitsidwa’ mwa kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Mwakutero mafumu Achikunja “otsika” “anakwezedwa,” kuwasiya iwo akulamulira dziko lapansi popanda kusokonezedwa ndi ufumu weniweni wa Mulungu. (Deuteronomo 28:13, 15, 36, 43, 44) Mwakutero inayambika “nthaŵi yoikidwiratu ya mitundu”—Nthaŵi za Akunja—zomwe zinatha mu 1914 pamene Mulungu anaika ufumu wake pa Yesu Kristu, ‘iye wokhala nako kuyenera kwa lamulo’ ku iwo. (Luka 21:20-24; Salmo 110:1, 2; Danieli 4:15-28; 7:13, 14) Ndi Yesu ali pa mpando wachifumu wa kumwamba, mitundu ya Kunja singapondereze pa chimene Yerusalemu wakale anaphiphiritsira, Ufumu wa wolowa m’malo wa lamulo wa Davide.—Ahebri 12:22.
17. Ndi “bodza” lotani limene linali kulengezedwa ndi aneneri a chiAmoni?
17 Aneneri a chiAmoni ankanena kuti likulu la Amoni, Raba, likapulumuka chowonongeko ndi lupanga la Nebukadinezara. Koma iri linali “bodza,” popeza dziko lonse la Amoni likasakazidwa. M’tsiku lathu, Mulungu walamula kuti chiwonongeko cha mitundu chikatsatira chija cha Chikristu cha Dziko, mongadi mmene Raba anawonongedwera pambuyo pa Yerusalemu.—Ezekieli 21:28-32; Chivumbulutso 16:14-16.
Yerusalemu Apatsidwa Mlandu
18. Ndi kaamba ka machimo otani amene Ezekieli anatsutsira Yerusalemu, ndipo ndimotani mmene tiyenera kuvomerezera ku ichi?
18 Kachiŵirinso akumalankhula mawu a Yehova, Ezekieli anatsutsa Yerusalemu kaamba ka machimo oterowo onga ngati kukhetsa mwazi, kulambira mafano, mkhalidwe wa chiwerewere, chinyengo, ndi kuiwala Mulungu. Mafumu ake a liwongo la mwazi anagwiritsira ntchito molakwika mphamvu ku nsonga ya kupha mwalamulo, ndipo onyenga anachotsa adani awo mwa kuwapatsa iwo mlandu wabodza. Kaamba ka zochita zolakwa zoterozo, nzika za Yerusalemu zikamwazidwa. Chidziŵitso cha ichi chiyenera kulimbikitsa chigamulo chathu cha kupewa kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu, chiwerewere, chinyengo, ndi machimo ena akulu.—Ezekieli 22:1-16.
19. Ndi mwanjira yotani imene anthu a Yuda akasungunulidwira, ndipo nchifukwa ninji kuphedwa kwawo kunaperekedwa?
19 Yehova akasungunulanso anthu a Yuda mu ng’anjo. Uku sikunali kuwayeretsa iwo m’dongosolo la kuyenga koma kunali kuwasungunula iwo mu mkwiyo wake wamoto. (Ezekieli 22:17-22) Chiweruzo chimenechi chinali choyenera bwino kwa aneneri opanga chiwembu, ansembe opanda lamulo, akalonga a umbombo, ndi anthu opanda chilungamo. Onse anatsutsidwa. Popeza palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo amene anali wolumgama, Mulungu akawatha iwo ndi moto wa mkwiyo wake.—Ezekieli 22:23-31.
Chilango Chiri Choyenerera
20. Ndi pa akazi ophiphiritsira ati pamene mkwiyo wa Mulungu ukatsanulidwira, ndipo ndi tsatanetsatane wotani amene mungapereke ponena za chizindikiritso chawo?
20 Kutsanuliridwa kwa mkwiyo wa Mulungu potsatira kunaimiridwa monga chiweruzo chomwe chinaperekedwa pa akazi aŵiri ophiphiritsira okhala ndi liwongo la chigololo chauzimu. Mmodzi anali Ohola, ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli wokhala ndi Samariya monga likulu lake. Iye anali “wamkulu” chifukwa cha kukhala wopangidwa ndi ambiri a mafuko a Israyeli, kuphatikizapo awo amene anachokera kwa ana akulu kwambiri a Yakobo, Rubeni ndi Simeoni. M’ng’ono wake anali Oholiba, Yuda wa mafuko aŵiri wokhala ndi Yerusalemu monga likulu lake. Ohola amatanthauza “Hema Wake.” Oholiba amatanthauza “Hema Wanga Ali mwa Iye,” amene ali woyenerera popeza hema wa Mulungu, kapena kachisi, anali mu Yuda.—Ezekieli 23:1-4.
21. Ndi m’chiyani mmene Ohola anafuna chisungiko, kupereka chenjezo lotani kaamba ka ife?
21 Ohola (Israyeli) anasiya kukhalapo pamene anagwetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E. Nchiyani chimene iye anachita? (Ŵerengani Ezekieli 23:5-7.) Ohola mopanda chikhulupiriro anafuna chisungiko m’chigwirizano cha ndale zadziko, koma ichi chinatsogoza m’kutengera kwake kulambira konyenga kwa ogwirizana nawo ake, kotero kuti ‘anadzidetsa iyemwini ndi mafano onyansa.’ Tikumatenga chenjezo kuchokera ku chigololo chauzimu cha Ohola, tiyenera kudzichinjiriza motsutsana ndi zigwirizano za kudziko zomwe zingawononge chikhulupiriro chathu.—Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:15-17.
22. Mofanana ndi Ohola ndi Oholiba, nchiyani chimene Chikirstu cha Dziko chikuchita, koma nchiyani chomwe chidzachitika kwa icho?
22 Chifukwa cha kulondola njira yolakwa kwambiri kuposa mkulu wake, Oholiba (Yuda) anavutika ndi tsoka la mtundu pa manja a Chibabulo mu 607 B.C.E. Ana ake anagwa ndi lupanga kapena antengedwa andende, ndipo iye ananyazitsidwa pakati pa amitundu. Mofanana ndi Ohola ndi Oholiba, Chikristu cha Dziko chikuchita chigololo chauzimu, chimo pamaso pa Mulungu amene chimadzinenera kumlambira. Chiprotestanti, limodzi ndi magulu ake ambirimbiri, chadzidetsa icho chokha ndi malonda ndi mphamvu za ndale zadziko moipirako kuposa mkulu wake, Chiroma Katolika. Chotero, Yehova adzawona ku icho kuti Chikristu cha Dziko chonse chawonongedwa. Kenaka anthu adzadziŵa kuti ali Wolamulira Ambuye Yehova. Chidzalimbikitsa chigamulo chathu kudana ndi zigwirizano zosayenerera za kudziko ngati tikumbukura kuti oyanjana nawo a Chikristu cha Dziko posachedwapa adzamuukira ndi kupereka chilango cha Mulungu pa iye monga mbali yokulira ya Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga.—Ezekieli 23:8-49; Chivumbulutso 17:1-6, 15-18.
Onyenga Adabwitsidwa
23. Ndimotani mmene Yerusalemu anaimidwira mu uthenga wa Mulungu kwa Ezekieli kumapeto kwa December ya 609 B.C.E., ndipo nchiyani chomwe chikachitika kwa iye?
23 Pa tsiku limodzimodzilo kumapeto kwa December pamene Nebukadinezara anayamba kuzinga kwake Yerusalemu kwa miyezi 18 (Tebeth 10, 609 B.C.E.), Mulungu anampatsa Ezekieli uthenga wina wa chithunzi. Mu iwo, Yerusalemu wozingidwayo anaimiridwa ndi mphika wophikira mu umene nzika za mzindawo ‘zikaphikidwa.’ Kuipa kwa makhalidwe kunapangitsa “dzimbiri” mu mphika wophikira wophiphiritsirawo. “Nthuli ndi nthuli,” cohita zolakwawo akatulutsidwa mu Yerusalemu, ndipo tsoka lake silikatha kufikira atavutika ndi chiwonongeko. Yehova anali ataweruza Yerusalemu mogwirizana ndi zochita zake zoipa, ndipo iye anayenera kuwonongedwa, mongadi mmene Chikristu cha Dziko chiyenera.—Ezekieli 24:1-14.
24. (a) Nchifukwa ninji Ezekieli sanasonyeze chisoni pamene mkazi wake anafa? (b) Pamene “lupanga” la Yehova litsikira pa icho, ndimotani mmene Chikristu cha Dziko chikachitira, ndipo nchiyani chimene icho chidzafikira kudziŵa?
24 Chotsatira, Ezekieli anayenera kuchita chitsanzo m’njira yachilendo. (Ŵerengani Ezekieli 24:15-18.) Nchifukwa ninji mneneriyo sanayenera kusonyeza chisoni pamene mkazi wake anafa? Kusonyeza kudabwitsidwa kumene Ayuda akakhalira pa chiwonongeko cha Yerusalemu, nzika zake, ndi kachisi. Ezekieli anali atanena kale zokwanira ponena za nkhani zoterozo ndipo sakalankhulanso uthenga wa Mulungu kachiŵirinso kufikira kugwa kwa Yerusalemu kunasimbidwa kwa iye. Mofananamo, Chikirstu cha Dziko ndi anthu ake a chipembedzo onyenga akadabwitsidwa pa nthaŵi ya chiwonongeko chawo. Ndipo pambuyo pa kuyambika kwa “chisautso chachikulu,” zimene gulu la mlonda lodzozedwa lakhala litanena kale ponena za mapeto ake zikakhala zokwanira. (Mateyu 24:21) Koma pamene “lupanga” la Mulungu litsikira pa Chikristu cha Dziko, anthu a chipempedzo odabwitsidwa amenewa ndi ena ‘adzayenera kudziŵa kuti iye ali Yehova.’—Ezekieli 24:19-27.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Nchiyani chimene chinachitika pamene Yehova anagwiritsira ntchito “lupanga” lake motsutsana ndi Yuda ndi Israyeli?
◻ Ndimotani mmene tiyenera kuyambukiridwira ndi kuswa lumbiro la kwa Nebukadinezara kochitidwa ndi Zedekiya?
◻ Nchiyani chimene “lupanga” la Mulungu limaimira?
◻ Ndi chochitika chotani chokhudza Nebukadinezara chimene chimasonyeza kuti palibe wina aliyense amene angatembenuzire kumbali “lupanga” la Yehova?
◻ Nchiyani chomwe chinachitika m’kukwaniritsa Ezekieli 21:25-27?
◻ Nchiyani chomwe chinaphiphiritsidwa ndi kusasonyeza chisoni kwa Ezekieli pamene mkazi wake anafa?
[Chithunzi patsamba 18]
Pamene Mfumu Zedekiya anaswa lumbiro lake kwa Nebukadinezara ndipo anatengedwa wandede, ndi ulosi uti womwe unayamba kukwaniritsidwa?