Yandikirani Mulungu
Kodi Mulungu Akakhululuka Machimo, Samawakumbukiranso?
YANKHO lachidule ndi loti inde. Ponena za anthu amene amawakonda, Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yeremiya 31:34) Choncho Yehova akutitsimikizira kuti akakhululukira anthu amene alapa, sakumbukiranso machimo awo. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova, yemwe ndi Mlengi wa chilengedwe chonse, sangathe kukumbukira machimo amene wakhululukira munthu? Mawu amene Ezekieli analemba akutithandiza kumvetsa tanthauzo la mawu akuti Mulungu akakhululuka, amaiwala.—Werengani Ezekieli 18:19-22.
Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Ezekieli, kulengeza za chiweruzo chake kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu. Mtunduwo unali utasiya kulambira Yehova ndipo dziko lonse linali litadzaza ndi chiwawa. Yehova analosera kuti Yerusalemu adzawonongedwa ndi Ababulo. Koma atafotokoza za chiweruzochi, Yehova anafotokozanso uthenga wopatsa chiyembekezo. Munthu aliyense anali ndi mwayi wosankha ngati akufuna kupulumuka chifukwa aliyense akanaimbidwa mlandu malinga ndi zochita zake.—Vesi 19, 20.
Kodi chikanachitika n’chiyani ngati munthu wina atasiya zoipa n’kuyamba kuchita zabwino? Yehova anati: “Munthu woipa akabwerera, kusiya machimo ake onse amene anali kuchita ndipo akasunga malamulo anga onse n’kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, adzakhalabe ndi moyo. Sadzafa ayi.” (Vesi 21) Apa n’zoonekeratu kuti Yehova anali ‘wokonzeka kukhululukira’ munthu wochimwa amene walapa n’kusiya zochita zake zoipa.—Salimo 86:5.
Nanga bwanji za machimo amene anachitawo? Yehova anafotokoza kuti: “Zolakwa zonse zimene anachita sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo.” (Vesi 22) Onani kuti vesili likuti zolakwa za munthu amene walapa “sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo.” Kodi n’chifukwa chiyani kudziwa zimenezi kuli kothandiza?
M’Baibulo, mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “kukumbukira” samangotanthauza kukumbukira zinthu zimene zinachitika kale. Buku lina linanena kuti: “Nthawi zambiri mawu akuti kukumbukira amasonyeza kuchita chinachake.” Motero, pamene Yehova ananena kuti munthu wochimwa akalapa zolakwa zake “sizidzakumbukiridwa ndipo sadzalangidwa nazo” ankatanthauza kuti sadzalanga kapena kuimba mlandu munthuyo chifukwa cha zolakwa zakezo.a
Mawu a palemba la Ezekieli 18:21, 22 ndi okhudza mtima chifukwa akusonyeza mmene Mulungu amakhululukira. Yehova akakhululukira munthu, ndiye kuti m’tsogolo sadzamuimbanso mlandu kapena kumulanga chifukwa cha machimo akewo. M’malomwake, iye amaponya kumbuyo kwake machimo onse a anthu amene alapa. (Yesaya 38:17) Zimakhala ngati kuti wafafaniza zoipa zonse zimene munthuyo anachita.—Machitidwe 3:19.
Chifukwa choti anthufe ndife opanda ungwiro, timachimwa kawirikawiri ndipo timafuna kuti Mulungu atichitire chifundo. (Aroma 3:23) Koma Yehova amafuna kuti tidziwe kuti tikalapa kuchokera pansi pa mtima, iye ndi wokonzeka kutikhululukira. Ndipo iye akatikhululukira amaiwala, kutanthauza kuti, sangatiimbenso mlandu kapena kutilanga chifukwa cha machimo amene anatikhululukira kale. Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri ndipo tikukhulupirira kuti mungakonde kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu chifukwa ndi wachifundo.
Mavesi amene mungawerenge mu July:
[Mawu a M’munsi]
a Mofanana ndi zimenezi, “kukumbukira zolakwa” kungatanthauze “kulanga munthu chifukwa cha machimo ake.”—Yeremiya 14:10.