-
Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda ChilungamoNsanja ya Olonda—2012 | August 1
-
-
MUNTHU wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Mawu amenewa, omwe analembedwa zaka 3,000 zapitazo, akufotokoza bwino mmene zinthu zilili m’dzikoli masiku ano. Anthu ambiri amakonda kugwiritsa ntchito molakwa mphamvu ndipo zimenezi zimachitika kulikonse. Nthawi zambiri anthu audindo amapondereza aumphawi, osauka ndi ovutika. Kodi Yehova amamva bwanji akamaona kupanda chilungamo kotereku? Yankho la funso limeneli likupezeka palemba la Ezekieli 22:6, 7, 31.—Werengani.
-
-
Yehova Amadana ndi Zinthu Zopanda ChilungamoNsanja ya Olonda—2012 | August 1
-
-
Chifukwa cha zimenezi Ezekieli anadzudzula atsogoleriwo komanso anthu amene ankawatsanzira posamvera Chilamulo cha Yehova. Ezekieli ananena kuti: “Anthu anyoza abambo ndi amayi awo.” (Vesi 7) Anthuwa sankalemekeza makolo awo ngati mmene Yehova ankafunira. Choncho iwo anachititsa kuti mtundu wawo usakhale wamphamvu chifukwa mabanja olimba ndi amene akanachititsa kuti mtunduwo ukhale wamphamvu.—Ekisodo 20:12.
Anthu oipawa ankadyera masuku pamutu anthu osauka. Iwo akamaphwanya Chilamulo cha Mulungu ankasonyeza kuti sakuzindikira kuti Yehova anawapatsa Chilamulocho chifukwa chowakonda. Mwachitsanzo, Chilamulo cha Mulungu chinawauza Aisiraeli kuti aziganizira anthu amene sanali Aisiraeli omwe ankakhala pakati pawo. (Ekisodo 22:21; 23:9; Levitiko 19:33, 34) Koma Aisiraeliwo ankachitira mlendo “zinthu mwachinyengo.”—Vesi 7.
Aisiraeli ankazunzanso “mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye,” ndipo anthu amenewa analibe wowathandiza. (Vesi 7) Yehova amadera nkhawa kwambiri ana ndiponso akazi amasiye. Iye analonjeza kuti adzapereka chilango kwa amene amazunza anthu amenewa.—Ekisodo 22:22-24.
-