Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezekieli—Gawo 1
CHINALI chaka cha 613 B.C.E. Mneneri Yeremiya anali ku Yuda, kulalikira mopanda mantha za chiwonongeko cha Yerusalemu ndi Yuda chomwe chinali chitayandikira. Apa n’kuti Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo itatengera kale Ayuda ambiri kuukapolo. Ena mwa iwo anali Danieli ndi anyamata anzake atatu, amene tsopano anali kugwira ntchito m’khoti la Akasidi. Ambiri mwa Ayuda ogwidwawo anakakhala cha ku mtsinje wa Kebara, “m’dziko la Akasidi.” (Ezekieli 1:1-3) Yehova anaonetsetsa kuti Ayuda ogwidwawo akhale ndi mneneri wawo. Anatero poika Ezekieli kuti akhale mneneri wawo. Iyeyu anali ndi zaka 30.
Buku la Ezekieli analimaliza mu 591 B.C.E., ndipo munalembedwa zinthu zimene zinachitika pa zaka 22. Ezekieli analemba bukuli mosamala ndiponso molondola zedi. Iye anachita kutchula tsiku, mwezi, ndiponso chaka cha maulosi ake. Gawo loyamba la uthenga wa Ezekieli limafotokoza kwambiri za kugwa ndi kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Ndipo gawo lachiwiri limafotokoza za mawu onena za chiweruzo cha Yehova kwa mitundu yoyandikana ndi Yuda. Gawo lotsiriza limafotokoza za kubwezeretsedwa kwa kulambira Yehova. Nkhani ino ifotokoza mfundo zazikulu zochokera pa Ezekieli 1:1–24:27. M’gawo limeneli muli masomphenya, maulosi, ndi zitsanzo zosonyeza zoopsa zimene zinadzagwera Yerusalemu.
“NDAKUIKA UKHALE MLONDA”
Pambuyo poona masomphenya ochititsa nthumanzi a mpando wachifumu wa Yehova, Ezekieli anapatsidwa ntchito. Yehova anamuuza kuti: “Ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, m’mwemo mvera mawu otuluka m’kamwa mwanga, nundichenjezere iwo.” (Ezekieli 3:17) Yehova analamula Ezekieli kuti achite mongoyerekezera zinthu ziwiri zosonyeza kuzingidwa kwam’tsogolo kwa Yerusalemu ndi zotsatirapo zake. Ponena za Yuda, Yehova ananena mawu otsatirawa, kudzera mwa Ezekieli: “Taonani, Ine ndikufikitsirani lupanga, ndipo ndidzawononga misanje yanu.” (Ezekieli 6:3) Kwa anthu okhala m’Yuda, Yehova anati: “Tsoka lako lakufikira.”—Ezekieli 7:7.
M’chaka cha 612 B.C.E., Ezekieli anafika ku Yerusalemu m’masomphenya. Zimene anaona m’kachisi wa Mulungu n’zonyansa zedi! Yehova anatumiza opereka chilango ochoka kumwamba (“amuna asanu ndi mmodzi” akuimira opereka chilangowa) posonyeza mkwiyo wake kwa Ayuda ampatukowo. Anthu amene anapulumuka chilangocho ndi okhawo okhala ndi “chizindikiro pa mphumi.” (Ezekieli 9:2-6) Koma choyamba, “makala a moto,” kutanthauza kuti uthenga wa Mulungu wonena za chiwonongeko, womwe uli woopsa ngati moto, anayenera kumwazidwa mumzindawo. (Ezekieli 10:2) Ngakhale kuti ‘Yehova anadzawabwezera njira ya oipa pamutu pawo,’ iye analonjeza kusonkhanitsanso Aisiraeli omwazikana.—Ezekieli 11:17-21.
Mzimu wa Mulungu unam’tenga Ezekieli n’kubwerera nayenso m’dziko la Akasidi. Iye anachita chitsanzo chosonyeza kuthawa kwa Zedekiya ndi anthu ena kuchoka mumzinda wa Yerusalemu. Anadzudzula aneneri onyenga. Anatsutsa anthu olambira mafano. Yuda anamufanizira ndi mpesa wachabechabe. Fanizo la ziwombankhanga ndi mpesa linasonyeza mavuto amene anadzabwera chifukwa choti Yerusalemu anadalira Iguputo. Ezekieli anamaliza fanizoli ponena lonjezo lakuti ‘Yehova adzabudula nsonga yosomphoka ya nthambi yanthete, ndi kuiwoka pa phiri lalitali.’ (Ezekieli 17:22) Komabe ku Yuda sinadzakhale “ndodo yachifumu ya kuchita ufumu.”—Ezekieli 19:14.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:4-28—Kodi galeta la kumwamba limaimira chiyani? Galetali limaimira mbali yakumwamba ya gulu la Yehova yomwe ili ndi zolengedwa zokhulupirika zauzimu. Galetali limayendera mzimu woyera wa Yehova. Wokwera galetali, amene akuimira Yehova, ali ndi ulemerero wosaneneka. Utawaleza wokongola ukuimira kudekha kwa Yehova.
1:5-11—Kodi zamoyo zinayi ndani? M’masomphenya ake achiwiri a galetali, Ezekieli ananena kuti zamoyo zinayizo anali akerubi. (Ezekieli 10:1-11; 11:22) Iye anatinso nkhope ya ng’ombe ija inali “nkhope ya kerubi.” (Ezekieli 10:14) Zili chonchotu chifukwa choti ng’ombe imaimira mphamvu, ndipo akerubi ndi zolengedwa zauzimu zamphamvu kwambiri.
2:6—N’chifukwa chiyani Yehova akutchula Ezekieli mawu akuti “wobadwa ndi munthu” mobwerezabwereza? Yehova akum’tchula choncho Ezekieli pofuna kum’kumbutsa kuti n’ngopangidwa ndi thupi ndi magazi, motero pali kusiyana kwakukulu kwambiri pakati iyeyu, yemwe anali wopereka uthenga, ndi Mulungu, Mwini uthengawo. Mabuku a uthenga wabwino amagwiritsa ntchito mawu omwewa ka 80 ponena za Yesu Khristu, ndipo zimenezi zimamveketsa bwino mfundo yakuti Mwana wa Mulunguyu anabwera padziko pano monga munthu weniweni, osati mngelo yemwe anangovala thupi la munthu.
2:9–3:3—N’chifukwa chiyani Ezekieli anamva kutsekemera podya mpukutu wa maliro ndi chisoni? Ezekieli anamva kutsekemera podya mpukutuwo chifukwa cha mmene ankaonera ntchito imene anapatsidwa. Iye ankaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala mneneri wa Yehova.
4:1-17—Kodi Ezekieli anachitadi zinthu zofanizira kuzingidwa kwa Yerusalemu komwe kunali kutayandikira? Zikuoneka kuti mneneriyu anachitadi zimenezi chifukwa choti anapempha kusintha mafuta ake ophikira ndiponso chifukwa choti Yehova anayankhadi pempholi. Kugonera kumanzere kwa masiku 390 kunaimira zaka 390 za zolakwa za mtundu wa mafuko khumi wa Isiraeli, kuchokera pamene unakhazikitsidwa mu 997 B.C.E., kufika pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. Ndipo kugonera kumanja kwa masiku 40 kukuimira zaka 40 za zolakwa za Ayuda, kuyambira m’chaka cha 647 B.C.E., nthawi yomwe Yeremiya anakhala mneneri, kufika mu 607 B.C.E. Kwa masiku 430 onsewo, Ezekieli ankangodalira chakudya chochepa ndiponso madzi pang’ono chabe, ndipo zimenezi zinkalosera kuti Yerusalemu akadzazingidwa kudzakhala njala.
5:1-3—Kodi zimene Ezekieli anachita potenga tsitsi lowerengeka pa gawo la tsitsi limene amayenera kuliwaza ku mphepo ndi kulimanga mu mkawo wa malaya ake zinali ndi tanthauzo lotani? Zimenezi zinkasonyeza kuti pambuyo pa zaka 70 zimene Yuda anakhala bwinja, anthu ochepa adzabwerera ku Yudako n’kuyambanso kulambira koona.—Ezekieli 11:17-20.
17:1-24—Kodi ziwombankhanga ziwirizi zikuimira ndani, nanga nthambi zanthete za mkungudza zikubudulidwa bwanji, ndipo kodi “nsonga yosomphoka ya nthambi zake zanthete” imene Yehova anawoka ikuimira ndani? Ziwombankhanga ziwirizo zikuimira olamulira a Babulo ndi olamulira a Iguputo. Chiwombankhanga choyamba chinapita ku nsonga ya mkungudza, kutanthauza kuti chinapita kwa wolamulira wa boma limene lili mumzera waufumu wa Davide. Chiwombankhanga chimenechi chinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zanthete pochotsa Mfumu Yoyakini wa Yuda n’kuikapo mfumu Zedekiya. Ngakhale kuti Zedekiya analumbira kuti adzakhala wokhulupirika, iye anakapempha thandizo kwa chiwombankhanga china chija, chomwe chikuimira wolamulira wa Iguputo, koma zimenezi sizinaphule kanthu. Iye anagwidwa ukapolo n’kukafera ku Babulo. Yehova anabudulanso ‘nsonga yosomphoka ya nthambi yanthete,’ yomwe ndi Mfumu Mesiya. Iyeyu anakawokedwa “pa phiri lalitali lothuvuka,” phiri la Ziyoni la kumwamba, ndipo kumeneko Mesiyayu akakhala “mkungudza wokoma,” wobweretsa madalitso osasimbika padziko lapansi.—Chivumbulutso 14:1
Zimene Tikuphunzirapo:
2:6-8; 3:8, 9, 18-21. Tisamaope anthu oipa kapena kuzengereza kuwauza uthenga wa Mulungu, womwenso uli wowachenjeza. Anthu akamapanda kutimvera ndiponso akamalimbana nafe, tizikhala olimba ngati mwala. Koma tizisamala kuti tisakhale okakala mtima, kapena opanda chifundo. Yesu ankamvera chisoni anthu amene ankawalalikira. Nafenso tizilalikira anthu ena chifukwa chowamvera chisoni.—Mateyo 9:36.
3:15. Atalandira ntchito imene Yehova anam’patsa, Ezekieli anakakhala ku Telabibu, ali ‘wodabwa kwa masiku asanu ndi awiri,’ chifukwa chosinkhasinkha za uthenga umene anayenera kulalikira. Kodi nafenso sitiyenera kupeza nthawi yophunzira ndi kusinkhasinkha bwinobwino pofuna kumvetsa zinthu zozama zauzimu?
4:1–5:4. Ezekieli anafunika kudzichepetsa ndiponso kulimba mtima kuti achite mongoyerekezera zinthu ziwiri zija zimene zinadzachitika patsogolo. Nafenso timafunika kudzichepetsa ndi kulimba mtima kuti tichite ntchito iliyonse imene Mulungu watipatsa.
7:4, 9; 8:18; 9:5, 10. Palibe chifukwa chomvera chisoni kapena kuchitira chifundo anthu olangidwa ndi Mulungu.
7:19. Yehova akamadzaweruza dongosolo loipa lino, ndalama sizidzathandiza m’njira ina iliyonse.
8:5-18. Mpatuko umawononga munthu mwauzimu. “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.” (Miyambo 11:9) Tingachite mwanzeru kupewa ngakhale kumvetsera chabe zonena za anthu ampatuko.
9:3-6. Kukhala ndi chizindikiro, kapena kuti umboni wakuti ndife atumiki a Mulungu obatizidwa ndiponso kuti tili ndi umunthu wachikhristu, n’kofunika kuti tipulumuke “chisautso chachikulu.” (Mateyo 24:21) Akhristu odzozedwa, omwe akuimiridwa ndi munthu wokhala ndi zolembera, akutsogolera pa ntchito yolemba zizindikiroyi, yomwe ndi ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Ngati tikufuna kuti tikhalebe ndi chizindikirochi, tiyenera kuthandiza mwakhama Akhristu odzozedwawa pantchitoyi.
12:26-28. Ezekieli anauzidwa kuti akanene ngakhale kwa anthu amene amanyoza uthenga wake, kuti: “Palibe amodzi a mawu [a Yehova] adzazengerezekanso.” Yehova asanawononge dongosolo lino la zinthu, ifenso tiziyesetsa mmene tingathere kuthandiza anthu kuyamba kudalira Yehovayo.
14:12-23. Kupeza chipulumutso ndi udindo wathu patokha. Palibe amene angatisenzere udindo umenewu.—Aroma 14:12.
18:1-29. Timatuta zimene tafesa.
“NDIDZAGUBUDUZA GUBUDUZA GUBUDUZA”
Mu 611 B.C.E., Aisiraeli atakhala ku ukapolo kwa zaka seveni, akuluakulu a mtunduwo anam’fikira Ezekieli pofuna “kufunsira kwa Yehova.” Iye anawauza za nthawi yaitali imene Aisiraeli anapandukira Mulungu ndipo anawachenjeza kuti Yehova ‘adzasolola lupanga lake m’chimake’ kuti awalange. (Ezekieli 20:1; 21:3) Yehova anauza kalonga wa Isiraeli (Zedekiya), kuti: “Chotsa chilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, chepsa chokwezeka. Ndidzagubuduza gubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo [Yesu Khristu]; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.”—Ezekieli 21:26, 27.
Mzinda wa Yerusalemu ukuimbidwa mlandu. Milandu imene anapalamula Ohola (Isiraeli) ndi Oholiba (Yuda) ikuvumbulidwa. Ohola anali ataperekedwa kale “m’dzanja la mabwenzi ake, m’dzanja la Aasuri.” (Ezekieli 23:9) Naye Oholiba anali atatsala pang’ono kuwonongedwa. Kuyambira m’chaka cha 609 B.C.E., mzinda wa Yerusalemu unazingidwa kwa chaka chimodzi ndi theka. Mapeto ake mzindawo unagwa ndipo zimenezi zinafoola kwambiri Ayuda moti analibe ngakhale mphamvu zolilira mzindawu. Ezekieli analamulidwa kuti asauze Ayuda a ku Babulowo za uthenga wa Mulungu mpaka atayamba kaye wamva za kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu kwa “wopulumukayo.”—Ezekieli 24:26, 27.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
21:3—Kodi “lupanga” limene Yehova anasolola m’chimake ndi chiyani makamaka? “Lupanga” limene Yehova anagwiritsa ntchito polanga Yerusalemu ndiponso Yuda linali Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo, pamodzi ndi ankhondo ake. N’kuthekanso kuti lupangali likuphatikizapo mbali ya kumwamba la gulu la Yehova, lomwe lili ndi zolengedwa zamphamvu zauzimu.
24:6-14—Kodi dzimbiri la mphika likuimira chiyani? Mzinda wa Yerusalemu utazingidwa anauyerekezera ndi mphika. Dzimbiri lake likuimira makhalidwe onyansa mumzindawu, monga chidetso ndi dama, ndiponso kukhetsa magazi. Chidetso chake chinafika poipa zedi moti ngakhale pamene mphikawo anauika pa moto wa makala, m’kati mwake mulibe kanthu, n’kuwonjezera kwambiri motowo, dzimbirilo linakanika kuchoka.
Zimene Tikuphunzirapo:
20:1, 49. Zimene akulu ena a Isiraeli ananena zikusonyeza kuti ankakayikira zimene Ezekieli anawauza. Tiziyesetsa kwambiri kuti tisakhale ndi mtima wokayikira machenjezo a Mulungu.
21:18-22. Nebukadinezara anawombeza maula kuti adziwe mtundu umene ayenera kuyamba kuukira. Koma Yehova anaonetsetsa kuti Nebukadinezarayo aukire Yerusalemu. Zimenezi zikusonyeza kuti ngakhale ziwanda sizingathe kusokoneza atumiki a Yehova opereka chilango chake.
22:6-16. Yehova amadana ndi miseche yoipa, chidetso, kupondereza ena, ndi kulandira ziphuphu. Tiyenera kuyesetsa kwambiri kupewa makhalidwe oipa amenewa.
23:5-49. Kugwirizana ndi mayiko ena pa zandale kunachititsa Isiraeli ndi Yuda kuyamba kulambira konyenga kwa anthu a m’mayikowo. Motero tizipewa kugwirizana kwambiri ndi anthu a kudziko chifukwa angathe kuwononga chikhulupiriro chathu.—Yakobe 4:4.
Uthenga Wamoyo Ndiponso Wamphamvu
M’machaputala 24 oyambirira a buku la Ezekieli timaphunziramo mfundo zofunika zedi. Muli mfundo zosonyeza zinthu zimene zimachititsa Mulungu kuti asatiyanje, zimene tingachite kuti Mulungu atichitire chifundo, ndiponso chifukwa chimene tiyenera kuchenjeza anthu oipa. Ulosi wonena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu umasonyeza moonekeratu kuti Yehova ndi Mulungu amene ‘amauza anthu ake zatsopano zisanabuke.’—Yesaya 42:9.
Maulosi ngati amene ali pa Ezekieli 17:22-24 ndi Ezekieli 21:26, 27 ankanena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya kumwamba. Posachedwapa, ulamuliro umenewo udzapangitsa kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi. (Mateyo 6:9, 10) Tizikhala ndi chikhulupiriro cha mphamvu kuti tidzapeze madalitso mu Ufumuwu. Ndithudi, “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—Aheberi 4:12.
[Chithunzi patsamba 12]
Kodi galeta la kumwamba limaimira chiyani?
[Chithunzi patsamba 14]
Kuthandiza mwakhama pantchito yolalikira kumatithandiza kuti tikhalebe ndi “chizindikiro”