Kuŵeta Limodzi ndi Mlengi Wathu Wamkulu
‘Yehova ndiye Mbusa wanga; sindidzasoŵa. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande achilungamo, chifukwa cha dzina lake.’—SALMO 23:1, 3.
1. Kodi ndimpumulo wachikondi wotani umene Yehova amapereka?
SALMO la 23, “salmo la Davide,” ladzetsa chitsitsimulo kumiyoyo yambiri yotopa. Lawalimbikitsa kukhala ndi chidaliro chonenedwa m’vesi 6: ‘Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse amoyo wanga: ndipo ndidzakhala m’nyumba ya Yehova masiku onse.’ Kodi chimenecho ndicho chikhumbo chanu, kukhala m’nyumba ya Yehova yolambirira masiku onse, muli wogwirizana ndi anthu ake amene tsopano akusonkhanitsidwa kuchokera m’mitundu yonse ya dziko lapansi? “Mbusa ndi woyang’anira wa moyo wanu,” Mlengi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu, adzakuthandizani kufikira chonulirapo chimenecho.—1 Petro 2:25.
2, 3. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova amaŵetera anthu ake mwachikondi? (b) Kodi ndimotani mmene “gulu lankhosa” la Yehova lawonjezerekera mofulumira?
2 Mlengi wa “miyamba yatsopano ndi dziko latsopano” ndiyenso Wolinganiza ndi Woyang’anira Wamkulu wa mpingo Wachikristu, “banja la Mulungu.” (2 Petro 3:13; 1 Timoteo 3:15) Iye ngwokondwerera kwambiri kuŵeta anthu ake, monga momwe Yesaya 40:10, 11 amasonyezera momvekera bwino kuti: ‘Tawonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; tawonani, mphotho yake iri ndi iye, ndipo chobwezera chake chiri patsogolo pa iye. Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana ankhosa pachapa pake, nadzawatengera pachifuŵa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.’
3 M’lingaliro lowonjezereka, ‘gulu la nkhosa limeneli’ likuphatikizapo awo amene ayenda m’chowonadi Chachikristu kwa nthaŵi yaitali ndi ‘ana a nkhosa’ amene asonkhanitsidwa nthaŵi yaposachedwapa—monga ziŵerengero zazikulu zimene tsopano zikubatizidwa mu Afirika ndi Kummaŵa kwa Yuropu. Mkono wa Yehova wamphamvu ndi wotetezera ukuwasonkhanitsira pachifuŵa chake. Ngakhale kuti iwo anali ofanana ndi nkhosa zosochera, tsopano aloŵa muunansi wapafupi ndi Mulungu wawo wokondedwa ndi Mbusa.
Mbusa Mnzake wa Yehova
4, 5. (a) Kodi “mbusa wabwino” ndani, ndipo kodi ndimotani mmene ulosi unasonyera kwa iye? (b) Kodi ndintchito yolekanitsa yotani imene Yesu akuyang’anira, ndi zotulukapo zapadera zotani?
4 Potumikira kudzanja lamanja la Atate wake kumwamba, ‘mbusa wabwino,’ Yesu Kristu, akuperekanso chisamaliro chachifundo kwa “nkhosa.” Iye anapereka moyo wake kupindulitsa choyamba ‘kagulu ka nkhosa’ ka odzozedwa ndiyeno, lerolino, khamu lalikulu la “nkhosa zina” zakezo. (Luka 12:32; Yohane 10:14, 16) Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu, amalankhula kwa nkhosa zonsezo akumati: ‘Tawonani, Ine, inedi ndidzaweruza pakati pazoŵeta ndi zoŵeta. Ndipo ndidzaziutsira mbusa mmodzi; iye adzazidyetsa, ndiye mtumiki wanga Davide, iye adzazidyetsa, adzakhala mbusa wawo. Ndipo ine Yehova ndidzakhala Mulungu wawo, ndi mtumiki wanga Davide kalonga pakati pawo: Ine Yehova ndanena.’ Ezekieli 34:20-24.
5 Mawuwo akuti ‘mtumiki wanga Davide’ amasonya molosera kwa Kristu Yesu, ‘mbewuyo’ amene ali woloŵa nyumba pampando wachifumu wa Davide. (Salmo 89:35, 36) M’tsiku lakuweruzidwa kwa amitundu lino, Mbusa ndi Mfumu mnzake wa Yehova, Kristu Yesu, Mwana wa Davide, akupitirizabe kulekanitsa “nkhosa” mwa anthu amene angadzinenere kukhala “nkhosa” koma m’chenicheni ali “mbuzi.” (Mateyu 25:31-33) “Mbusa mmodzi” ameneyu akudzutsidwiranso kudyetsa nkhosa. Nkukwaniritsidwa kokondweretsa chotani nanga kwa ulosi umenewu kumene tikuwona lerolino! Pamene andale zadziko akulankhula za kugwirizanitsa anthu kupyolera mwa dongosolo ladziko latsopano, kwenikweni Mbusa mmodziyo akugwirizanitsa nkhosa zochokera ku mitundu yonse kupyolera mwa mkupiti wakuchitira umboni m’zilankhulidwe zonse, umene gulu la Mulungu lokha padziko lapansi ndilo likhoza kuuchita.
6, 7. Kodi ndimotani mmene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wachititsira kuti “chakudya panthaŵi yoyenera” chikupezeka kwa nkhosa?
6 Pamene uthenga wa Ufumu ukufalikira mosalekeza m’magawo atsopano, gulu la “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” la Akristu odzozedwa, lotumidwa ndi Mbusa mmodzi likutsimikizira kuti makonzedwe onse akuchitidwa akutumiza “chakudya panthaŵi yoyenera.” (Mateyu 24:45) Zambiri za nthambi zosindikiza 33 za Watch Tower Society padziko lonse lopansi zikuwonjezera liŵiro lakusindikiza kuti zikhutiritse kufunika kowonjezereka kwa mabukhu ndi magazini ambiri ndi abwinopo ofotokoza Baibulo.
7 Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova likuchita zothekera zonse kuwongolera mkhalidwe wakutembenuzira m’zinenero pafupifupi 200 ndi kuyambitsa kutembenuzira m’zinenero zowonjezereka monga momwe zikufunikira kufola munda wa dziko lonse. Zimenezi zikuchirikiza lamulo limene Yesu anapereka kwa ophunzira ake pa Machitidwe 1:8 lakuti: ‘Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga . . kufikira malekezero ake adziko.’ Ndiponso, New World Translation of the Holy Scriptures, losindikizidwa kale lonse kapena mbali yake m’zinenero 14, tsopano likutembenuzidwira m’zinenero zina 16 za ku Yuropu, Afirika, ndi maiko Akummaŵa.
Kusangalala ndi “Mtendere wa Mulungu”
8. Kodi ndimotani mmene nkhosazo zadalitsidwira molemerera mwa pangano la mtendere limene Yehova wachita nawo?
8 Kupyolera mwa Mbusa wake mmodzi, Kristu Yesu, Yehova akuchita ‘pangano la mtendere’ ndi nkhosa Zake zodyetsedwa bwino. (Yesaya 54:10) Posonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu, nkhosazo zikutheketsedwa kuyenda m’kuunika. (1 Yohane 1:7) Iwo akusangalala ndi ‘mtendere wa Mulungu wakuposa lingaliro lonse ndi umene ukutetezera mitima yawo ndi mphamvu zolingalira kupyolera mwa Kristu Yesu.’ (Afilipi 4:7) Monga momwe Ezekieli 34:25-28 akupitirizira kufotokoza, Yehova akuŵeta nkhosa zake kuloŵa m’paradaiso wauzimu, mkhalidwe wokondweretsa wakutetezereka, kulemerera kotsitsimula, ndi kopindulitsa. Mbusa wachikondi ameneyu amati ponena za nkhosa zake: ‘Ndipo adzadziŵa kuti ine ndine Yehova, nditadula zomangira goli lawo, ndi kuwalanditsa m’manja mwa iwo akuwatumikiritsa. Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, . . . koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwawopsa.’
9. Kodi ndimwaŵi wotani umene watsegukira anthu a Mulungu mwa ‘kudulidwa kwa zomangira goli’?
9 Zaka zaposachedwapa, Mboni za Yehova m’maiko ambiri zawona kale kudulidwa kwa “zomangira goli lawo.” Iwo ngaufulu kulalikira kuposa ndi kale lonse. Ndipo tonsefe, m’dziko lirilonse, tigwiritsiretu ntchito bwino chisungiko chimene Yehova amapereka pamene tikupitirizabe kutsiriza ntchitoyo. Nchitsimikiziro chotani nanga chimene Yehova amapereka pamene tikuyandikira nthaŵi ya chisautso chachikulu koposa zonse zimene anthu adzawona!—Danieli 12:1; Mateyu 24:21, 22.
10. Kodi ndani amene Yehova wapereka kuti athandize Mbusa Wabwino, Kristu Yesu, ndipo kodi nchiyani chimene ena a amenewa anauzidwa ndi mtumwi Paulo?
10 Kukonzekerera tsiku limenelo lakulipsira kwake oipa, Yehova wagaŵira ansembe aang’ono kuthandiza Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, kusamalira gulu lankhosa. Amenewa afotokozedwa pa Chivumbulutso 1:16 monga chiŵerengero chokwanira cha “nyenyezi zisanu ndi ziwiri” m’dzanja lamanja la Yesu. M’zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo analankhula kwa bungwe loimira abusa aang’ono amenewa, akumati ‘Dzipenyerereni inu nokha ndi gulu lonse, palimene mzimu woyera wakuikani oyang’anira, kuti muŵete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Mwana wa Iye yekha.’ (Machitidwe 20:28) Lerolino, pali abusa aang’ono okwanira mazana makumi ambiri otumikira m’mipingo 69,558 padziko lonse lapansi.
Patsogolo Abusa Aang’ono Inu!
11. Kodi ndimotani mmene abusa ena atsogozera mwachipambano m’magawo amene afoledwa mwakaŵirikaŵiri?
11 Mmalo ambiri abusa amenewa ayenera kutsogoza m’magawo amene afoledwa mobwerezabwereza mkati mwa masiku otsiriza ano. Kodi angasungitse motani kutenthedwa maganizo kwakukulu kwa gulu lankhosa? Abusawo akhala akuchita moyamikirika koposa, ndipo imodzi ya njira zimene apeza chipambano ndiyo mwakusonkhezera ntchito yaupainiya wothandiza ndi upainiya wokhazikika. Abusa ambiri iwo eni akhala ndi phande muutumiki umenewu, ndipo ngakhale ofalitsa amene ali osakhoza kutero asonyeza mzimu waupainiya, kutumikira ndi chikondwerero chimene chimathandiza kugonjetsa mphwayi m’gawo. (Salmo 100:2; 104:33, 34; Afilipi 4:4, 5) Chotero, pamene kuipa ndi chipwirikiti zikukuta dzikoli, anthu ambiri onga nkhosa akugalamutsidwira kuchiyembekezo cha Ufumu.—Mateyu 12:18, 21; Aroma 15:12.
12. Kodi ndivuto lalikulu lotani limene liripo m’magawo owonjezereka mofulumira, ndipo kodi nthaŵi zina zimasamaliridwa motani zimenezi?
12 Vuto lina nlakuti kaŵirikaŵiri sipamapezeka abusa oyeneretsedwa okwanira kusamalira gulu lankhosa. Kumene chiwonjezeko chiri chofulumira, monga Kummaŵa kwa Yuropu, kuli mipingo yambiri yatsopano yopanda akulu alionse oikidwa. Nkhosa zofunitsitsa zikusenza thayolo, koma iwo ali opanda chidziŵitso kwambiri, ndipo chithandizo chikufunika kuphunzitsa nkhosa zimene zikuloŵa mu unyinji wawo m’mipingo. M’maiko onga Brazil, Mexico, ndi Zaire, kumene chiwonjezeko chiri chofulumira kwambiri, Mboni zachichepere pang’ono zimafunikira kugwiritsidwa ntchito kulinganiza utumiki ndi kuphunzitsa atsopano ena. Apainiya akupereka chithandizo chachikulu, ndipo kunoko alongo amaphunzitsa alongo atsopano. Yehova mwa mzimu wake akudalitsa zotulukapo. Chiwonjezeko chikupitirizabe kudza.—Yesaya 54:2, 3.
13. (a) Popeza kuti kututa nkwakukulu motero, kodi Mboni zonse ziyenera kupempherera chiyani? (b) Kodi mapemphero a anthu a Mulungu anayankhidwa motani nkhondo yadziko yachiŵiri isanaulike ndi mkati mwake?
13 M’maiko kumene ntchito yolalikira iri yokhazikika bwino lomwe, m’maiko kumene ziletso zachotsedwa posachedwapa, ndi m’magawo otsegulidwa chatsopano, mawu a Yesu a pa Mateyu 9:37, 38 akugwirabe ntchito akuti: ‘Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifuka chake pempherani mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.’ Ifenso, tifunikira kupemphera, kuti Yehova adzutse abusa owonjezereka. Iye wasonyeza kuti angathe kuchita zimenezi. Nkhondo Yadziko II isanaulike ndi mkati mwake, otsendereza ufulu onga ngati Asuri anayesa kuwononga psiti Mboni za Yehova. Koma moyankha mapemphero awo, Yehova anayenga gulu lawo, akumalipangitsa kukhaladi lateokratiki, ndipo anagaŵira “abusa” ofunikawo.a Izi zinali zogwirizana ndi ulosi wakuti: ‘Pamene a ku Asuri adzaloŵa m’dziko lathu, ndi pamene adzaponda mzinyumba zathu, tidzawaukitsira abusa asanu ndi aŵiri, ndi akalonga asanu ndi atatu’—ngakhale oposa akulu odzipatulira okwanira kutsogolera.—Mika 5:5.
14. Kodi ndichosoŵa chapadera chiti chimene chiri m’gulu, ndipo ndichilimbikitso chotani chimene chikuperekedwa kwa abale?
14 Pali kufunika kwapadera kwakuti Mboni zachimuna zonse zobatizidwa zikalimire mwaŵi wowonjezereka. (1 Timoteo 3:1) Mkhalidwewo ngwofulumira. Mapeto adongosolo lino akufika mofulumira. Habakuku 2:3 akuti: ‘Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.’ Abale, kodi mungathe kukalimira kuti muyeneretsedwe kulandira mwaŵi wowonjezereka m’ntchitoyi yakuŵeta—mapeto asanadze?—Tito 1:6-9.
Kuŵeta Kwateokratiki
15. Kodi ndim’njira yotani mu imene anthu a Yehova aliri teokrase?
15 Kuti akhale ndi phande lokwanira m’chiwonjezeko cha gulu la Yehova, anthu ake afunikira kukhala ateokratiki m’lingaliro lawo. Kodi angachite zimenezi motani? Eya, kodi liwu lakutilo “teokratiki” limatanthauzanji? Webster’s New Twentieth Century Dictionary imafotokoza “teokrase” kukhala “ulamuliro wa boma wochitidwa ndi Mulungu.” Muli m’lingaliro limeneli kuti “mtundu wopatulika” wa anthu a Yehova uli teokrase. (1 Petro 2:9; Yesaya 33:22) Monga ziŵalo kapena atsamwali a mtundu wateokratiki umenewo, Akristu owona ayenera kukhala ndi moyo ndi kutumikira momvera Mawu a Mulungu ndi malamulo ake amakhalidwe abwino.
16. Kwakukulukulu, kodi ndimotani, mmene tingadzisonyezere kukhala ateokratiki?
16 Mtumwi Paulo akufotokoza momvekera bwino mmene Akristu ayenera kukhalira ateokratiki. Choyamba, iye akuti ayenera “kuvala umunthu watsopano, umene unelengedwa m’chifanizo cha Mulungu, m’chowonadi ndi m’chilungamo.” Umunthu wa Mkristu uyenera kuumbidwa mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Mulungu olembedwa m’Mawu ake. Ayenera kukhala wokhulupirika kwa Yehova ndi malamulo Ake. Atasonyeza mwafanizo mmene zimenezi zingachitidwire, Paulo akulimbikitsa kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 4:24–5:1) Monga ana omvera, tiyenera kumvera Mulungu. Umu ndimo mmene teokrase yowona imachitira, kusonyeza kuti tikulamulidwadi ndi Mulungu!—Wonaninso Akolose 3:10, 12-14.
17, 18. (a) Kodi ndimkhalidwe wapadera wotani wa Mulungu umene Akristu ateokratiki amatsanzira? (b) M’mawu ake kwa Mose, kodi ndimotani mmene Yehova anagogomezera mkhalidwe Wake waukulu, koma kodi ndichenjezo lotani limene Iye anawonjezera?
17 Kodi ndiuti umene uli mkhalidwe waukulu wa Mulungu umene tiyenera kutsanzira? Mtumwi Yohane akuyankha pa 1 Yohane 4:8 pamene akuti: ‘Mulungu ndiye chikondi.’ Mavesi asanu ndi atatu pambuyo pake, m’vesi 16, iye akubwereza lamulo lamakhalidwe abwino lofunika limeneli kuti: ‘Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.’ Mbusa Wamkulu, Yehova, ali chitsanzo chenicheni cha chikondi. Abusa ateokratiki amamtsanzira mwakusonyezera chikondi chachikulu nkhosa za Yehova.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 3:16, 18; 4:7-11.
18 Teokrati Wamkulu anadzisonyeza kwa Mose monga ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulangira ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate awo, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinayi.’ (Eksodo 34:6, 7) Chotero Yehova amagogomezera mbali zosiyanasiyana za mkhalidwe wake wapadera wateokratiki, chikondi, pamene akuchenjeza mwamphamvu kuti adzalanga ochita mphulupulu ngati kuli koyenerera.
19. Mosiyana ndi Afarisi, kodi abusa Achikristu ayenera kuchita motani mwa njira Yateokratiki?
19 Kwa awo amene ali ndi malo a ntchito athayo m’gulu, kodi kukhala wateokratiki kumatanthauzanji? Yesu anati ponena za alembi ndi Afarisi a m’tsiku lake: ‘Amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.’ (Mateyu 23:4) Ndikutsendereza ndi kupanda chikondi kotani nanga! Teokrase yowona, kapena ulamuliro wochitidwa ndi Mulungu, umafunikiritsa kuŵeta gulu la nkhosa mwakugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino achikondi a mu Baibulo, osati kuthodwetsa nkhosa ndi timalamulo topangidwa ndi anthu tosatha. (Yerekezerani ndi Mateyu 15:1-9.) Panthaŵi imodzimodziyo, abusa ateokratiki ayenera kutsanzira Mulungu mwa kuwonjezera pachikondi chawo kuima nji pakusunga chiyero cha mpingo.—Yerekezerani ndi Aroma 2:11; 1 Petro 1:17.
20. Kodi ndimakonzedwe agulu otani amene abusa ateokratiki amazindikira?
20 Abusa owona amazindikira kuti mkati mwa masiku otsiriza ano, Yesu waika kapolo wake wokhulupirika ndi wanzeru kuyang’anira zinthu zake zonse ndikuti mzimu woyera watsogolera kapolo ameneyu m’kuika akulu akuweta nkhosa. (Mateyu 24:3, 47; Machitidwe 20:28) Chotero, kukhala wateokratiki kumaphatikizapo kuchitira ulemu waukulu kapoloyu, chifukwa cha makonzedwe agulu amene kapolo walinganiza, ndi chifukwa cha kakonzedwe ka akulu mkati mwa mpingo.—Ahebri 13:7, 17.
21. Kodi nchitsanzo chabwino kwambiri chotani chimene Yesu anapereka kwa abusa aang’ono?
21 Yesu mwiniyo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri, kuyang’ana mosalekeza kwa Yehova ndi Mawu Ake kupeza chitsogozo. Iye anati: ‘Sindikhoza kuchita kanthu mwa ine ndekha; monga momwe ndimva ndiweruza; ndipo maweruzidwe anga ali olungama; chifukwa kuti sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.’ (Yohane 5:30) Abusa aang’ono a Ambuye Yesu Kristu ayenera kukulitsa kaimidwe ka maganizo kodzichepetsa kofananako. Ngati mkulu nthaŵi zonse agwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kupeza chitsogozo, monga momwe anachitira Yesu, pamenepo iye alidi wateokratiki.—Mateyu 4:1-11; Yohane 6:38.
22. (a) Kodi ndim’njira yotani imene onse ayenera kuyesayesa kukhala ateokratiki? (b) Kodi ndichiitano chachifundo chotani chimene Yesu akupereka kwa nkhosa?
22 Amuna obatizidwa inu, kalimirani kuti muyeneretsedwe kulandira mathayo mumpingo! Inu nonse nkhosa zokondedwa, khalani ndi cholinga chakukhala ateokratiki, mukumatsanzira Mulungu ndi Kristu m’kusonyeza chikondi! Abusa ndi nkhosa zomwe akondweretu chifukwa chakuti alabadira chiitano cha Yesu chakuti: ‘Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; Chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima; ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.’—Mateyu 11:28-30.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani nkhani za Nsanja ya Olonda pa mutu wakuti “Gulu,” makope a June 1 ndi 15, 1938, (Chingelezi).
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi “gulu lankhosa” la Yehova nchiyani? ndipo kodi limaphatikizapo ayani?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu anachitira monga “mbusa wabwino” m’zaka za zana loyamba, ndi lerolino?
◻ Kodi ndimbali yaikulu yotani imene abusa aang’ono ali nayo m’kusamalira gulu lankhosa?
◻ Kodi tanthauzo lalikulu la liwulo “teokrase” nchiyani?
◻ Kodi ndimotani mmene Mkristu—makamaka mbusa wamng’ono—ayenera kuchitira kuti akhale wateokratiki?
[Chithunzi patsamba 20]
Mofanana ndi mbusa wodzipereka, Yehova amasamalira gulu lake lankhosa
[Chithunzi patsamba 23]
Kutsanzira mkhalidwe wa Yehova Mulugu wa chikondi ndiko mchitidwe wateokrase