“Adzadziŵa Kuti Ine Ndine Yehova”
“Sindidzalola dzina langa loyerali aliipsyenso; ndipo amitundu adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—EZEKIEL 39:7.
1, 2. Ndimotani mmene timadziŵira kuti Yehova sadzalekerera kosatha kuipsya kwa dzina lake loyera?
DZINA loyera la Yehova linaipsyidwa ndi Aisrayeli akale. Bukhu iri la Ezekieli likumveketsa bwino icho. Koma anthu a Chikristu cha Dziko aipsyanso dzina la Mulungu amane amadzinenera kumulambira.
2 Kodi Wolamulira wa Chilengedwe Chonseyu mopanda mapeto akalekerera kuipsyidwa kwa dzina lake? Ayi, popeza iye akulengeza kuti: “Sindidzalola dzina langa loyera aliipsyenso; ndipo amitundu adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.” (Ezekieli 39:7; onaninso Ezekieli 38:23.) Nchiyani chimene ichi chidzatanthauza? Ndipo ndi maphunziro otani amene angaphunziridwe kuchokera ku mitu yomalizira m’bukhu la Ezekieli?
Maulosi Otsutsana Ndi Ena
3. (a) Ndimotani mmene mitundu ina inachitira ku kuvutika kwa Yuda? (b) Kodi “mfumu” ya Turo inachotsedwa chifukwa cha mzimu wotani, ndipo ndimotani mmene chimenechi chiyenera kutiyambukirira ife?
3 Pamapeto pa kuwonongedwa kwa Yerusalemu, Amoni anaweruzidwa chifukwa cha kusonyeza chimwemwe pa kuvutika kwa Yuda, ndi Moabu chifukwa cha kutsanzira mkhalidwe wotonza kulinga kwa Yuda. Edomu anali ndi liwongo la nkhalwe, ndipo mzimu wobwezera wa Afilisti unayenera kubweretsa “zidzudzulo za ukali” za Mulungu. (Ezekieli 25:1-17; Miyambo 24:17, 18) Chifukwa cha kusangalala pa tsoka la Yerusalemu, mzinda wa Turo ukagwera kwa Nebukadinezara, kapena Nebukadirezara (katchulidwe kolinganako ndi ka Chibabulo). (Ezekieli 26:1-21) Iye anali monga chombo chotsimikizirika kumira. (Ezekieli 27:1-36) “Mfumu” ya Turo (mwachidziŵikire mzera wa kulamulira kwake) inachotsedwa chifukwa cha kukhala ndi mzimu wodzitukumula wonga uja wa Satana. (Ezekieli 28:1-26) Ndithudi, chotero, tiyenera kupewa mzimu wochimwa wa kudzikweza womwe ungatipangitse ife kuipsya dzina la Yehova.—Salmo 138:6; Miyambo 21:4.
4. Nchiyani chomwe chinasungidwira kaamba ka Farao ndi Igupto?
4 Ezekieli ananeneratu kupasulidwa kwa zaka 40 kwa Igupto. Chuma chake chikakhala malipiro a Nebukadirezara kaamba ka utumiki wa nkhondo woperekedwa kupereka chiweruzo cha Yehova pa Turo. (Ezekieli 29:1-21) Pamene Mulungu anawona ku icho kuti Aigupto anamwazidwa, ‘iwo akadziŵa kuti iye ali Yehova.’ (Ezekieli 30:1-26) Akumaimira Igupto, Farao wodzikweza anayerekezedwa ndi mtengo wa mkungudza wokwezedwa womwe ukadulidwa. (Ezekieli 31:1-18) Pomalizira, Ezekieli anaimbira nyimbo za maliro ponena za Farao ndi kufikira ku Igupto mu Sheol.—Ezekieli 32:1-32.
Ntchito ya Mlonda
5. (a) Ndi kokha pansi pa mikhalidwe yotani imene Mulungu amavomereza mlonda wauzimu? (b) Nchiyani chomwe chimatanthauza ‘kuyenda m’malamulo a moyo’?
5 Ezekieli anakumbutsidwa za ntchito yake monga mlonda. (Ezekieli 33:1-7) Ndithudi, Mulungu amavomereza mlonda wauzimu kokha ngati iye achita ntchito yake ndi kuchenjeza oipa. (Ŵerengani Ezekieli 33:8, 9.) Kenaka, mofanana ndi Ezekieli, gulu lodzozedwa la “mlonda” molimba mtima likulengeza machenjezo aumulungu. Popeza Mulungu satenga chikondwerero mu imfa ya oipa, iye sadzasungirira zolembera zawo zakale motsutsana ndi iwo ngati iwo alabadira machenjezo ndi ‘kuyenda m’malamulo a moyo.’ M’tsiku la Ezekieli, kuyenda m’malamulo amenewo kunatanthauza kusunga Chilamulo, koma tsopano chimatanthauza kulandira dipo la Krsitu ndi kukhala wotsatira wake. (1 Petro 2:21) Palibe chirichonse chowongoleredwa molakwika ponena za njira mu imene Mulungu amalangira kapena kufupira anthu, ndipo kusungidwa kupyola “chisautso chachikulu” kumadalira pa kugwirizana kotheratu ndi malamulo ake.—Ezekieli 33:10-20; Mateyu 24:21.
6. Lerolino, ndimotani mmene ambiri aliri ofanana ndi Ayuda andende a nthaŵi ya Ezekieli?
6 Pafupi ndi mapeto a 607 B.C.E., othaŵa kwawo anasimba chiwonongeko cha Yerusalemu, ndipo Ezekieli kachiŵirinso analankhula uthenga wa Yehova. (Ezekieli 33:21-29) Ndimotani mmene andendewa anavomerezera? (Ŵerengani Ezekieli 33:30-33.) Lerolino, ambiri ali ofanana ndi Ayuda andende kwa amene Ezekieli anali woimba wa ‘nyimbo ya chikondi ya woimba bwino.’ Pamene odzozedwa ndi oyanjana nawo aitanira kunyumba ndi nyumba, anthu amenewa amasangalala ndi kumvekera kwa uthenga wa Ufumu koma samaukupatira iwo. Kwa iwo, iwo uli ngati nyimbo yachikondi yosangalatsa, koma sapanga kudzipereka kwa Yehova, ndipo iwo sadzapulumuka “chisautso chachikulu.”
“Mbusa Mmodzi” wa Yehova
7. Ndi machitidwe otani a yehova m’nthaŵi yathu amene ali olingana ndi zochita zake ndi nkhosa zake m’tsiku la Ezekieli?
7 Mu uthenga wa kwa Ezekieli pambuyo pa kugwa kwa Yeruslemu, Yehova anatsutsa oipsya dzina Lake loyera, “abusa a Israyeli” a boma. Ndi moyenerera chotani nanga mmene mawu amenewo amayenerera olamulira a Chikristu cha Dziko! (Ŵerengani Ezekieli 34:1-6.) Mosiyana ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, atsogoleri a ndale zadziko a Chikrsitu cha Dziko amadzinenepetsa iwo eni mwakuthupi pa “nkhosa.” (Yohane 10:9-15) Koma monga mmene Mulungu anapulumutsira nkhosa zake mwa kulanda abusa adyera ulamuliro pamene Yuda anapasulidwa, chotero iye adzapulumutsanso nkhosa zake mwakulanda olamulira a Chikristu cha Dziko ulamuliro wawo mkati mwa “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 16:14-16; 19:11-21) Yehova anasonyeza chikondi kaamba ka anthu ake onga nkhosa pamene anawapulumutsa iwo kuchoka m’Babulo mu 537 B.C.E., mongadi mmene iye anasonyezera mkhalidwe umenewo pamene anagwiritsira ntchito Koresi Wamkulu, Yesu Kristu, kuwombola otsalira a Israyeli wauzimu kuchoka ku ukapolo wa Babulo Wamkulu mu 1919 C.E.—Ezekieli 34:7-14.
8. Nchiyani chimene Yehova akachita ngati ‘nkhosa yonenepa’ ikayenera kutsendereza gulu la nkhosa, ndipo ndimotani mmene abusa ang’ono Achikristu ayenera kuchitira ndi nkhosa?
8 Mulungu amapatsa nkhosa zake chisamaliro chachikondi. (Ŵerengani Ezekieli 34:15, 16.) Ngati ‘nkhosa yonenepa’ inayenera kutsendereza gulu la nkhosa za Mulungu lerolino, Yehova “akamudyetsa” iye mwa kumchotsa mu mpingo tsopano ndi kumuwononga iye “m’chisautso chachikulu.” Mu 1914 Yehova anaika pa otsalira odzozedwa “mbusa mmodzi,” Yesu Kristu. Chiyambire 1935 iye wakhala akutsogoza kusonkhanitsidwa kwa “khamu lalikulu” la nkhosa zina,” lomwe tsopano likutumikira ndi ‘nkhosa zodzozedwa za pa busa pa Yehova.’ Mofanana ndi Mulungu ndi Krsitu, abusa ang’ono Achikirstu ayenera kuchita ndi nkhosa zimenezi mofewa.—Ezekieli 34:17-31; Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; Salmo 23:1-4; Machitidwe 20:28-30.
“Munda wa Edeni”!
9. Popeza kuti Yehova anagamulapo kuti dziko la Yuda ndi Israyeli liyenera kusunga sabata, nchiyani chimene iye anachita?
9 Lingaliraninso dziko lokhalitsidwa bwinja la Yuda ndi Israyeli. Popeza Mulungu anagamulapo kuti likayenera kusunga sabata mwa kukhala osagwira ntchito kwa zaka 70, iye anachitapo kanthu kuletsa Edomu ndi mitundu ina kutenga gawo limenelo. (2 Mbiri 36:19-21; Danieli 9:2) M’chenicheni, Edomu ndi gawo lake la mapiri a Seira anakhalitsidwanso bwinja, monga mmene kunanenedweratu, akumalandidwa ndi Babulo mu 602-601 B.C.E.—Ezekieli 35:1–36:5; Yeremiya 25:15-26.
10. Kubwezeretsedwa kwa otsalira ku Yuda mu 537 B.C.E. kunaloza ku zochitika zotani m’tsiku lathu?
10 Kubwezeretsedwa kwa otsalira ku Yuda mu 537 B.C.E. kunalozera ku zochitika zosangalatsa m’tsiku lathu. Mu 1919 “mapiri a Israyeli,” kapena mkhalidwe wauzimu wa mboni zodzozedwa za Yehova, anayamba kukhalidwa ndi otsalira obwezeredwanso mwauzimu. (Ezekieli 36:6-15) Mulungu anawayeretsa iwo ku kudetsedwa kwa chipembedzo ndi kuika mwa iwo “mzimu watsopano” kuwatheketsa iwo kutulutsa chipatso cha mzimu wake woyera. (Agalatiya 5:22, 23) Ndiponso kuti dzina la Yehova lisaipsyidwe ndi anthu a kudziko chifukwa iye walanga anthu ake, iye wadalitsa otsalira mokulira.—Ezekieli 36:16-32.
11. M’chigwirizano ndi Ezekieli 36:33-36, nchiyani chimene Mulungu wachita ndi mkhalidwe wauzimu wa otsalira odzozedwa?
11 Pambuyo pa kubwerera ku Yuda kwa otsalirawo, dziko lokhalitsidwa bwinjalo linasinthidwa kukhala “munda wa Edeni” wobala zipatso. (Ŵerengani Ezekiel 36:33-36.) Mofananamo, chiyambire 1919 Yehova wasintha mkhalidwe womwe pa nthaŵi imodzi unali wabwinja wa otsalira odzozedwa kukhala paradaiso wauzimu wobala zipatso, tsopano wogawanidwa ndi “khamu lalikulu.” Popeza paradaiso wauzimu ameneyu wadzazidwa ndi anthu oyera, lolani Mkrsitu aliyense wodzipereka agwirire ntchito pa kumsunga iye kukhala woyera.—Ezekieli 36:37, 38.
Umodzi Ubwezeretsedwa
12. Kodi ndimotani mmene kupatsidwanso mphamvu kwa mtundu wakale Wachiyuda kunachitidwira chitsanzo pa Ezekiel 37:1-14, ndipo ndi kufananako kwamakono kotani kumene ichi chiri nako?
12 M’dende ya Chibabulo, Ayuda anali chifupifupi mtundu wakufa, wofanana ndi kokha mafupa a m’munda. (Ezekieli 37:1-4) Koma nchiyani chimene Ezekieli kenaka anawona? (Ŵerengani Ezekieli 37:5-10.) Mafupa amenewo anavekedwa ndi mitsempha, minofu, ndi khungu, ndipo anakhalitsidwanso amoyo ndi mpweya wa moyo. (Ezekieli 37:11-14) Mulungu anawukitsa mtundu wa Chiyuda pamene anthu 42,360 a mafuko onse a Israyeli ndi ena 7,500 osakhala Aisrayeli anawuka ku mwaŵi wawo wa kudzazanso Yuda, kumanganso Yerusalemu ndi kachisi wake, ndi kubwezeretsa kulambira kowona kumeneko. (Ezara 1:1-4; 2:64, 65) Mofananamo, mu 1918 otsalira ozunzidwa a Israyeli wauzimu anakhala ngati mafupa owuma amenewo—ophedwa m’chigwirizano ndi ntchito yawo yochitira umboni poyera. Koma mu 1919 Yehova anawadzutsanso iwo monga olengeza Ufumu. (Chivumbulutso 11:7-12) Kufanana kumeneko kuyenera kulimbikitsa chidaliro chathu kuti odzozedwa ndi oyanjana nawo amapanga gulu la padziko lapansi limene Yehova akuligwiritsira ntchito lerolino.— See the 1975 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 87-125.
13. Ndimotani mmene kubwezeretsedwa kwa umodzi wa gulu pakati pa anthu akale a Yehova kunachitiridwa chitsanzo pa Ezekieli 37:15-20, ndipo ndi kufananako kotani kumene kunalipo kaamba ka ichi?
13 Ndimotani mmene kubwezeretsedwa kwa umodzi wa gulu pakati pa anthu akale a Yehova kunachitidwira chitsanzo? (Ŵerengani Ezekieli 37:15-20.) Pali kufanana nako kwamakono kaamba ka kugwirizana kwa ndodo ziŵiri (imodzi yoikidwa chizindikiro kaamba ka ufumu wa mafuko aŵiri a Yuda, inayo kaamba ka mafuko khumi a Israyeli). Mkati mwa Nkhondo ya Dziko I, amuna odzikweza anayesera kuswa umodzi wa atumiki a Mulungu, koma mu 1919 odzozedwa okhulupirika anagwirizanitsidwa pansi pa Kristu, “mfumu yawo imodzi” ndipo “mbusa mmodzi.” M’kuwonjezerapo, mofanana ndi osakhala Aisrayeli 7,500 omwe anabwerera ku Yuda, awo a “khamu lalikulu” tsopano ali ogwirizana ndi otsalira odzozedwa. Chiri chisangalalo chotani nanaga kukhala mu paradaiso wauzimu, kutumikira Yehova m’chigwirizano pansi pa” mfumu yathu imodzi”!—Ezekieli 37:21-28.
Gogi Awukira!
14. Ndani amene ali Gogi wa Magogi, ndipo ndi kachitidwe kotani kamene iye adzatenga? (Ezekiel 38:1-17)
14 Chotsatira, chochitika cha dzawoneni chinanenedweratu. Akumayembekezera kuipsya dzina la Mulungu ndi kuwona anthu Ake, Gogi wa Magogi akaukira otsalira a Israyeli wauzimu, omwe amaimira “mkazi” wa Yehova, kepena gulu la kumwamba. (Chivumbulutso 12:1-17) Gogi ali “wolamulira wa dziko lino,” Satana Mdyerekezi. Iye analandira dzina lakuti Gogi pambuyo pa kutulutsidwa kwake kumwamba kutsatira kubadwa kwa Ufumu mu 1914. (Yohane 12:31) “Dziko la Magogi” ali malo kumene Gogi ndi ziwanda zake anatsekerezedwa kunsi kwa dziko. Pambuyo pa kusakaza kwa Chikristu cha Dziko ndi mbali yonse ya Babulo Wamkulu kochitidwa ndi mphamvu zotsutsa chipembedzo, Yehova adzabweretsa Gogi motsutsana ndi otsalira a Israyeli wauzimu ndi oyanjana nawo ake odzipereka owonekera kukhala osadzichinjiriza.—Ezekieli 38:1-17; Chivumbulutso 17:12-14.
15. Nchiyani chimene chidzachitika pamene Gogi adzawukira Mboni za Yehova?
15 Nchiyani chomwe chidzachitika pamene makamu a Gogi aukira Mboni za Yehova? (Ŵerengani Ezekieli 38:18-23.) Yehova adzapulumutsa anthu ake! Zida zake zidzakhala mvumbi waukulu, matalala akulu, moto wosakaza, mliri. M’kusokonezeka, magulu a Gogi adzatembenuzira malupanga awo molimbana wina ndi mnzake. Koma Mulungu asanawachotse iwo kotheratu, ‘adzapangidwa kudziŵa kuti iye ali Yehova.’
16. (a) Nchiyani chomwe chidzachitika a ku “dziko la Magogi”? (b) Ndimotani mmene tiyenera kuyambukiridwira ndi chidziŵitso cha zochitika zonenedweratu zokhudza Gogi?
16 Pamene Satana ndi ziwanda zake atsekeredwa ku phompho, “dziko la Magogi,” malo awo otsutsidwa okhala pa dziko lapansi, akapita kotheratu. (Chivumbulutso 20:1-3) Zida za nkhondo za Gogi zikakhala zochuluka kotero kuti chikatenga nthaŵi yokulira kuzitaya izo. Mbalame ndi zirombo zidzadzisangalatsa izo zokha pa mitembo yosaikidwa ya khamu la Gog. Ndimotani mmene chidziŵitso cha zonsezi chiyenera kutiyambukirira ife? Nkulekeranji, popeza kuphunzira kuti kuukira kwa Gogi kukuyandikira koma kuti Yehova adzapulumutsa anthu Ake kuyenera kuwonjezera chikhulupiriro chathu ndi kutipanga ife kusangalala kuti zochitika zoterozo zikatulukapo m’kuyeretsedwa kwa dzina la Mulungu loipsyidwa kwa nthaŵi yaitali! —Ezekieli 39:1-29.
Onani Malo Opatulika a Yehova!
17. (a) Kodi ndi masomphenya otani amene Ezekieli anapatsidwa mu 593 B.C.E.? (b) Kukhalapo kwa kachisi wa m’masomphenya kuli umboni wa chiyani?
17 Mu 593 B.C.E., chaka cha 14 pambuyo pa kuwonongedwa kwa kachisi mu Yerusalemu, Ezekieli anapatsidwa masomphenya a malo opatulika atsopano a kulambira kwa Yehova. Oyesedwa ndi chitsogozo cha ungelo cha mneneriyo, anali a msinkhu waukulu koposa. (Ezekieli 40:1–48:35) Kachisi ameneyu anachitira chithunzi “hema wowona, amene Yehova anamuika,” ndipo anali ndi “zoimira za zinthu za kumwamba.” Yesu Kristu analowa m’Malo ake Opatulikitsa, “kumwamba kwenikweni,” mu 33 C.E. kukapereka kwa Mulungu mtengo wa nsembe yake ya dipo. (Ahebri 8:2; 9:23, 24) Kachisi wa masomphenya amatsimikizira kuti kulambira koyera kudzapulumuka kuukira kwa Gogi. Ndi chitonthozo chotani nanga kaamba ka okonda dzina la Yehova!
18. Ndi ziti zomwe ziri mbali zina zolembedwa za kachisi wa m’masomphenya?
18 Kachisi anali ndi mbali zambiri. Mwachitsanzo, panali njira za chipata zisanu ndi chimodzi mu zipupa zake zakunja ndi zamkati. (Ezekieli 40:6-35) Zipinda zodyera makumi atatu (mwachidziŵikire kaamba ka anthu kudyeramo nsembe za mtendere) zinali m’bwalo lakunja. (40:17) Guwa la nsembe la nsembe zopsyereza linali m’bwalo la mkati. (43:13-17) Guwa la nsembe la mtengo, mwachidziŵikire kaamba ka kutenthako chonunkhira, linali m’chipinda choyamba cha kachisiyo. (41:21, 22) Malo Opatulikitsa anali a ukulu wa mikono 20 mbali zonse zinayi, ndipo khoma lozungulira kachisiyo linali mabango oyesera 500 (mamita 1,600) m’mbali zonse. Inali nyumba yaikulu chotani nanga yodzazidwa ndi ulemelero wa Mulungu!—Ezekieli 41:4; 42:16-20; 43:1-7.
19. Ndimotani mmene tiyenera kuyambukiridwira ndi tsatanetsatane wa kachisi ndi chenicheni chakuti awo otumikira pamenepo anayenera kukwaniritsa miyezo ya Mulungu?
19 Tsatanetsatane wokulira wa kachisi, nsembe, zopereka, ndi mapwando ziyenera kusindikiza pa ife chifuno cha kutsatira malangizo ochokera ku gulu la Mulungu mosamalitsa, kuzindikira kuti kuyesayesa kulikonse kuyenera kupangidwa kukwezeka Yehova ndi kulambira kwake. (Ezekieli 45:13-25; 46:12-20) Awo otumikira pa kachisi anayenera kukwaniritsa miyezo yapamwamba ya Mulungu, ndipo anayenera kuphunzitsa anthu ‘kusiyana pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba.’ (Ezekieli 44:15, 16, 23) Ichi chiyenera kutisonkhezera ife kusungirira chiyero monga anthu a Yehova.—Aefeso 1:3, 4.
20. (a) Nchiyani chomwe chikuphiphiritsiridwa ndi madzi omwe akuyenda kuchoka ku kachisi wa masomphenya? (b) Madzi ophiphiritsira amanewa adzakhala ndi chotulukapo chotani?
20 Kuchokera ku kachisiko kunayenda mtsinje womwe unachiritsa, kapena wokometseredwa, ndi madzi a mchere a Nyanja Yakufa, kotero kuti iwo anadzazidwa ndi nsomba. (Ezekieli 47:1-11) Madzi amenewa akuphiphiritsira makonzedwe a Mulungu kaamba ka moyo wosatha, kuphatikizapo nsembe ya Yesu, yomwe iri yokwanira kaamba ka opulumuka a kuukira kwa Gogi ndi ena, kuphatikizapo awo owukitsidwa. (Yohane 5:28, 29; 1 Yohane 2:2; Chivumbulutso 22:1, 2) Nyanja Yakufa inaimira mbali mu imene mtundu wa anthu wakhalamo—kutsutsidwa ku chimo la cholowa ndi imfa limodzinso ndi ulamuliro wa Satana. Mofanana ndi nsomba zambiri m’madzi okometseredwa a Nyanja Yakufa, mtundu wa anthu wowomboledwa udzapita patsogolo pansi pa mikhalidwe yochiritsidwa ya ulamuliro wa Umesiya.
21. Ezekieli 47:12 amasonyeza kuti mtundu wa anthu omvera udzasangalala ndi chiyani m’dziko latsopano?
21 Kuchiritsa kukugwirizananso ndi mitengo yomera m’mphepete mwa mtsinje wa masomphenya. (Ŵerengani Ezekieli 47:12.) M’dziko latsopano, mtundu wa anthu omvera udzasangalala ndi umoyo wangwiro wakuthupi ndi wauzimu. Ndipo nchifukwa ninji ayi? Masamba a mitengo yobala zipatso yowonedwa m’masomphenyawo ali ndi mikhalidwe yopita patsogolo ya kuchiritsa. Ndi madalitso otani nanga kaamba ka awo amene amadziŵa ndi kutumikira Yehova!
Kenaka Adzadziŵa!
22. Nchiyani chomwe chimasonyeza kuti Mulungu adzaika anthu kumene iye adzasankha m’Paradaiso?
22 Mwa kugwirizana ndi gulu la Yehova tsopano, tingakulitse mikhalidwe yomwe idzatipanga ife kukhala ogwirizanika pamene Mulungu adzaika anthu pamene iye asankha m’dziko lapansi la Paradaiso. Kunena kuti kudzakhala kuikidwa koteroko kwa anthu kwalingaliridwa ndi chenicheni chakuti ntchito ya mafuko inapangidwa kumpoto ndi kum’mwera kwa gawo lolamulira lowonedwa ndi Ezekieli m’masomphenya. “Chopereka” cha magawo atatu chimenecho cha dziko chinaphatikizapo gawo kaamba ka Alevi osakhala ansembe ndi gawo la ansembe lokhala ndi kachisi wa m’masomphenya. Pakati pa gawo la kum’mwera panali mzinda wokhala ndi gulu la ntchito la mafuko osakanizana pansi pa “kalonga” wosonkhanitsidwa, akalonga oimira a Mesiya mu “dziko latsopano.”—Ezekieli 47:13–48:34; 2 Petro 3:13; Salmo 45:16.
23. Kuti tikhale mbali ya mtundu wa anthu owomboledwa okhala m’Paradaiso, nchiyani chimene tiyenera kuchita tsopano?
23 Woikidwa ufumu m’malo ake opatulika a kumwamba, Mulungu adzadalitsa mzinda wophiphiritsira wowonedwa ndi Ezekieli. (Ŵerengani Ezekieli 48:35.) Mpando wa pa dziko lapansi umenewo wolamulira udzatchedwa Yehova-Shammah, kapena “Yehova Iyemwini Ali Pomwepo.” Pitirizani kusonyeza chikondi chanu chosalephera kaamba ka Mulungu, ndipo mungakhale mbali ya mtundu wa anthu wowomboledwa wokhala m’Paradaiso, pamane palibe aliyense pa dziko lapansi yemwe adzakhala mu mdima wauzimu koma onse akadziŵa kuti Yehova ali Mulungu yekha wa moyo ndi wowona. (Habakuku 2:14) Pewani kukhala okakamizidwa kudziŵa dzina la Mulungu motsutsana ndi chifuno chanu pamene oipa adzawonongedwa. Sonyezani chikhulupiriro, mukumasonyeza kuti mukuyembekezera kukhala pakati pa opulumuka pamene iye akwaniritsa mawu akuti: “Amitundu adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekieli 36:23.
Nchiyani Chomwe Munganene?
◻ Ndi kokha pansi pa mikhalidwe yotani pamene Yehova amavomereza mlonda wauzimu?
◻ Ndimotani mmene Yehova amachitira ndi nkhosa zake, ndipo ndimotani mmene abusa Achikristu ayenera kuchitira ndi izo?
◻ Ndimotani mmene kupatsidwanso mphamvu kwa mtundu Wachiyunda kunachitira chitsanzo? (Ezekieli 37:1-14) Nchiyani chomwe chiri kufanana nako kwamakono kwa ichi?
◻ Ndani yemwe ali Gogi wa Magogi, ndipo nchiyani chomwe chidachitika pamene iye aukira Mboni za Yehova?
◻ Nchiyani chomwe chikuphiphiritsiridwa ndi madzi omwe akuyenda kuchokera ku kachisi wowonedwa m’masomphenya?
[Mapu/Chithunzi patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Chopereka chopatulika ndi ntchito ya mafuko
THE GREAT SEA
ENTERING IN TO HAMATH
DAN
ASHER
NAPHTALI
MANASSEH
EPHRAIM
REUBEN
JUDAH
THE CHIEFTAIN
Holy Contribution
En-Eglaim
BENJAMIN
SIMEON
En-gedi
ISSACHAR
ZEBULUN
Tamar
GAD
Meribath-Kadesh
Salt Sea
Jordan River
Sea of Galilee
[Chithunzi patsamba 23]
Yehova amapatsa nkhosa zake chisamaliro chachikondi, monga mmene anchitira abusa akale. Chotero abusa Achikristu ayenera kuchita ndi gulu la Mulungu ndi chifundo