Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi zimene Ezekieli anauzidwa kuti aphatikize ndodo ziwiri n’kukhala imodzi zikuimira chiyani?
Kudzera mwa Ezekieli, Yehova ananeneratu kuti Aisiraeli adzakhalanso ogwirizana m’Dziko Lolonjezedwa. Ulosiwu unkanenanso za atumiki a Mulungu a m’masiku otsiriza ano kuti adzakhala ogwirizana.
Yehova anauza Ezekieli kuti alembe mawu pandodo ziwiri. Pandodo yoyamba anafunika kulembapo kuti: “Ndodo ya Yuda ndi anzake, ana a Isiraeli.” Ndipo pandodo inayo anafunika kulembapo kuti: “Ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu komanso anzawo onse a nyumba ya Isiraeli.” Ndipo ndodo ziwirizi anafunika kuziphatikiza kuti zikhale “ndodo imodzi.”—Ezek. 37:15-17.
Kodi mawu akuti “Efuraimu” akuimira chiyani? Yerobowamu mfumu yoyamba ya mafuko 10 akumpoto, anali wochokera mu fuko la Efuraimu lomwe linali lamphamvu. (Deut. 33:13, 17; 1 Maf. 11:26) Fukoli linachokera mwa mwana wa Yosefe dzina lake Efuraimu. (Num. 1:32, 33) Yosefe anapatsidwa madalitso apadera ndi bambo ake a Yakobo. Choncho mpake kuti ndodo yoimira ufumu wamafuko 10 inkatchedwa “ndodo ya Efuraimu.” Pa nthawi imene Ezekieli ankalemba ulosi wonena za ndodo ziwiriwu, anthu a mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli anali atatengedwa kalekale mu 740 B.C.E. ndi Asuri kupita ku ukapolo. (2 Maf. 17:6) Patapita zaka, Asuri anagonjetsedwa ndi Ababulo ndipo izi zinachititsa kuti Aisiraeli azipezeka mu ufumu wonse wa Babulo.
M’chaka cha 607 B.C.E., anthu a mu ufumu wamafuko awiri wakum’mwera komanso ena omwe anatsala a mu ufumu wakumpoto anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Mafumu ochokera m’fuko la Yuda ndi amene ankalamulira mu ufumu wamafuko awiriwu. Komanso ansembe ankakhala ku Yuda chifukwa ankatumikira kukachisi wa ku Yerusalemu. (2 Mbiri 11:13, 14; 34:30) Choncho m’pomveka kuti ndodo “ya Yuda” inkaimira ufumu wamafuko awiri wakum’mwera.
Kodi ulosi wophatikiza ndodo ziwirizi unakwaniritsidwa liti? Unakwaniritsidwa pamene Aisiraeli anabwerera ku Yerusalemu kukamanganso kachisi m’chaka cha 537 B.C.E. Pa nthawiyi anthu ochokera mu ufumu wamafuko awiri ndi ochokera mu ufumu wamafuko 10 anachokera limodzi ku ukapolo kubwerera ku Yerusalemu. Choncho mtundu wa Isiraeli sunalinso wogawikana. (Ezek. 37:21, 22) Aisiraeli anayambiranso kulambira Yehova mogwirizana. Mneneri Yesaya komanso Yeremiya ananeneratunso za mgwirizano umenewu.—Yes. 11:12, 13; Yer. 31:1, 6, 31.
Kodi ulosi wa Ezekieli unaneneratu chiyani chokhudza kulambira koyera? Ulosiwu unanena kuti Yehova adzachititsa kuti atumiki ake akhale ‘amodzi.’ (Ezek. 37:18, 19) Kodi zimenezi zikuchitika masiku ano? Inde, ulosiwu unayamba kukwaniritsidwa mu 1919 pamene gulu la Mulungu pang’ono ndi pang’ono linkakonzedwa komanso kuthandizidwa kuti likhale logwirizana. Apa ndiye kuti Satana analephera kugawanitsa anthu a Mulungu.
Pa nthawi imeneyo Akhristu ambiri anali ndi chiyembekezo chodzakhala mafumu ndi ansembe kumwamba limodzi ndi Yesu. (Chiv. 20:6) Mophiphiritsa anali ngati ndodo ya Yuda. Komabe kenako Akhristu ambiri amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi anayamba kugwirizana nawo. (Zek. 8:23) Akhristu amenewa ali ngati ndodo ya Yosefe ndipo alibe chiyembekezo chodzalamulira ndi Khristu.
Masiku ano Akhristu onsewa akutumikira Yehova motsogoleredwa ndi Mfumu Yesu Khristu ndipo ulosi wa Ezekieli unatchula Yesu kuti “mtumiki wanga Davide.” (Ezek. 37:24, 25) Yesu anapemphera kuti otsatira ake onse ‘akhale amodzi, mmene iye alili wogwirizana ndi Atate ake.’a (Yoh. 17:20, 21) Iye ananeneratunso kuti otsatira ake odzozedwa adzakhala “gulu limodzi” ndi a “nkhosa zina” ndipo iye adzakhala “m’busa” wawo. (Yoh. 10:16) Mogwirizana ndi mawu a Yesuwa, masiku ano anthu onse a Mulungu ndi ogwirizana, kaya akuyembekezera kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli.
a Pamene Yesu ankanena za chizindikiro cha masiku otsiriza anatchula mafanizo angapo. N’zochititsa chidwi kuti poyamba anatchula za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” yemwe ndi kagulu ka abale odzozedwa amene akutsogolera anthu a Mulungu. (Mat. 24:45-47) Kenako anafotokoza mafanizo onena za Akhristu odzozedwa onse. (Mat. 25:1-30) Pomaliza ananena za Akhristu odzakhala padziko lapansi amene akuthandiza abale a Khristu. (Mat. 25:31-46) Mofanana ndi zimenezi, m’masiku athu ano, ulosi wa Ezekieli unayamba kukwaniritsidwa pa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzapita kumwamba. Ngakhale kuti ufumu wa mafuko 10 sukuimira anthu odzakhala padziko lapansi, mgwirizano umene wafotokozedwa mu ulosiwu, umatikumbutsa mgwirizano umene uli pakati pa Akhristu odzakhala padziko lapansi ndi odzapita kumwamba.