Mvetserani—Mlonda wa Yehova Akulankhula!
“Ndakuika ukhale mlonda wa nyumba ya Israyeli, . . . nundichenjezere iwo.”—EZEKIELI 3:17.
1. Nchifukwa ninji tiyenera kumvetsera kwa “mlonda” wa Yehova pamene akulankhula?
“MLONDA” wa Yehova akulankhula uthenga wa Mulungu tsopano lino. Kodi mukumvetsera? Moyo wanu weniweniwo umadalira pa kuvomereza kwanu ku uthenga umenewo ndi chiyamikiro ndi kachitidwe. Posachedwapa, ‘mitundu idzadziŵa Yehova’ pamene iye adzayeretsa dzina lake loyera mwa kuwononga dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa ndi kusunga anthu ake. Kodi mukuyembekezera kukhala pakati pawo? (Ezekieli 36:23; 39:7; 2 Petro 3:8-13) Mungakhale tero, koma kokha ngati mumvetsera pamene “mlonda” wa Yehova akulankhula.
2. Kulephera kumvetsera kwa aneneri a Mulungu kunatulukapo m’chiyani kaamba ka ufumu wa Yuda?
2 Kulephera kumvetsera kwa aneneri a Mulungu kunabweretsa tsoka pa ufumu wa Yuda mu 607 B.C.E. Mitundu ya adani inayang’ana mwa chipambano pa kukhalitsidwa bwinja kumeneko pa manja a Chibabulo. Koma ndimotani nanga mmene dzina la Yehova linalemekezedwera pamene iye anapangitsa kubwerera kwa Ayuda okhulupirika ku dziko lakwawo mu 537 B.C.E.!
3. Nchiyani chimene bukhu la Ezekieli liri nacho?
3 Ponse paŵiri kukhalitsidwa bwinja ndi kubwezeretsedwa kumeneko zinanenedweratu ndi mlonda wa Yehova, Ezekieli. Bukhu la Baibulo lokhala ndi dzina lake ndipo lomalizidwa ndi iye mu Babulo chifupifupi mu 591 B.C.E. liri ndi (1) ntchito ya Ezekieli; (2) kuchitiridwa fanizo kwa ulosi; (3) mauthenga motsutsana ndi Israyeli; (4) kuneneratu za chiŵeruzo cha Yerusalemu; (5) maulosi otsutsana ndi mitundu ina; (6) malonjezo a kubwezeretsa; (7) ulosi wotsutsana ndi Gogi wa Magogi; ndi (8) masomphenya a malo opatulika a Mulungu. Tikukuitanani inu kuŵerenga bukhulo pamene tikuliphunzira ilo. Inu mwakutero mudzawona mmene likutiyambukirira ife lerolino ndipo mudzimvetsera pamene “mlonda” wa Yehova akulankhula.a
Mlonda wa Mulungu Apatsidwa Ntchito
4. (a) Nchiyani chimene Ezekieli anawona m’masomphenya? (b) Ndani omwe anali “zolengedwa zamoyo,” ndipo ndi mikhalidwe yotani imene zinali nayo?
4 Pa Tamuzi 5, 613 B.C.E. (m’chaka chachisanu cha kukhala m’ndende m’Babulo kwa mfumu ya Chiyuda Yehoyakini), wansembe wa zaka 30 zakubadwa Ezekieli anali pakati pa Ayuda andende pa “mtsinje wa Kebara,” ngalande yodziŵika ya Mtsinje wa Firate. M’masomphenya, iye anawona gareta ya kumwamba ya Yehova, yokhala ndi “zamoyo zinyai.” (Ŵerengani Ezekieli 1:4-10.) ‘Cholengedwa chamoyo’ chirichonse, kapena kerubi wa mapiko, anali ndi nkhope zinayi. (Ezekieli 10:1-20; 11:22) Izi zikusonyeza kuti akerubiwo anali ndi chikondi chopatsidwa ndi Mulungu (munthu), chilungamo (mkango), mphamvu (ng’ombe), ndi nzeru (chiwombankhanga). Kerubi aliyense anaima pambali pa ‘njinga mkati mwa njinga,’ ndipo mzimu wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito, inali yokhoza kuyendetsa iwo kupita kulikonse.—Ezekieli 1:1-21.
5. Nchiyani chimene gareta wakumwamba akuimira, ndipo ndimotani mmene kawonedwe kameneka ka iyo kayenera kuyambukirira anthu a Yehova?
5 Wokwera pa garetayo anali woimira wa ulemerero wa Yehova. (Ŵerengani Ezekieli 1:22-28.) Garetayo ikuimira bwino motani nanga gulu lauzimu la ungelo la Mulungu! (Salmo 18:10; 103:20, 21; Danieli 7:9, 10) Yehova akukwera pa iwo m’lingaliro la kulamulira zamoyo zimenezi ndi kuzigwiritsira ntchito izo mogwirizana ndi chifuno chake. Wokwerapoyo anali wodekha, mofanana ndi uta waleza wotsagana nawowo, koma Ezekieli anadabwitsidwa kowopsya. Ndithudi, kawonedwe kozizwitsa kameneka ka ulemerero wa Yehova ndi mphamvu monga Wolinganiza Wamkulu wa makamu ake akumwamba kayenera kutipanga ife kyamikira modzichepetsa kaamba ka mwaŵi wa kumtumikira iye monga mbali ya gulu lake la pa dziko lapansi.
6. (a) Ndi kuikidwa kotani kumene Ezekieli analandira, ndipo ndimotani mmene iye anawonera utumiki wa kwa Mulungu? (b) Ndi pakati pa anthu a mtundu wanji pamene Ezekieli anayenera kulosera, ndipo kodi chimenecho chiri cha phindu lotani kudziŵa mmene Mulungu anachitira ndi iye?
6 Ngakhale kuti akukumbutsidwa za chiyambi chake cha umunthu ndi mkhalidwe wake wotsika mwa kutchedwa “mwana wa munthu,” Ezekieli anaikidwa monga mneneri wa Yehova. (Ŵerengani Ezekieli 2:1-5.) Ezekieli akayenera kupita kwa “mitundu yopanduka,” maufumu a Israyeli ndi Yuda. Choyamba, mwa lamulo laumulungu iye anadya mpukutu wokhala ndi nyimbo za maliro, koma unkoma ngati uchi chifukwa iye anali woyamikira kukhala mneneri wa Mulungu. Mofananamo, Akristu odzozedwa ndi atumiki anzawo amachipeza icho chokoma kukhala moboni za Yehova. Ezekieli anayenera kulosera pakati pa anthu owuma mtima ndi woma mutu, koma Mulungu akapanga nkhope yake kukhala yogamulapo monga nkhope zawo chipumi chake cholimba monga diamond. Iye akalosera molimba mtima kaya iwo akamvetsera kapena ayi. Chiri chotenthetsa mtima kudziŵa kuti monga mmene Mulungu anachirikizira Ezekieli m’mikhalidwe yovuta, Iye adzatithandiza ife kuchitira umboni molimba mtima m’gawo lirilonse.—Ezekiel 2:6-3:11.
7. Ntchito ya Ezekieli inapereka thayo lotani?
7 Kudya mpukutu kunatulutsa mwa Ezekieli ‘mtima womyuka’ woyenerera ku uthenga wake. Pa Telabibu iye anakhala ‘wodabwa masiku asanu ndi aŵiri’ kusinkhasinkha pa uthengawo. (Ezekieli 3:12-15) Ife nafenso tifunikira kusinkhasinkha ndi kuphunzira mwakhama kuti timvetsetse zinthu zozama zauzimu. Pokhala anali ndi uthenga woulalikira, Ezekieli anapatsidwa ntchito monga mlonda wa Mulungu. (Ŵerengani Ezekieli 3:16-21.) Mlonda woikidwa chatsopanoyo anayenera kuchenjeza Aisrayeli okuswa lamulo kuti iwo anayang’anizana ndi chiŵeruzo chaumulungu.
8. Ndani amene akutumikira monga “mlonda” wa Yehova lerolino, ndipo ndani amene akuyanjana ndi iwo?
8 Ngati Ezekieli analephera monga mlonda, Yehova akanamsunga iye wathayo kaamba ka imfa ya minkholeyo. Ngakhale kuti awo amene sanamfune iye kupereka chidzudzulo akaika zingwe zophiphiritsira pa iye, iye molimba mtima akalengeza uthenga wa Mulungu. (Ezekieli 3:22-27) M’tsiku lathu, Chikristu cha Dziko chimakana kumvetsera ndipo chimayesera kuika zoletsa pa Akristu odzozedwa. Koma chiyambire 1919 odzozedwa amnewa atumikira monga “mlonda” wa Yehova, molimba mtima kulengeza uthenga wake kaamba ka “nthaŵi ya mapeto” ya dongosolo iri. (Danieli 12:4) Oyanjana nawo mu ntchito imeneyi liri “khamu lalikulu” lomawonjezereka la “nkhosa zina” za Yesu. (Chivumbulutso 7:9, 10; Yohane 10:16) Popeza gulu la “mlonda” likupitiriza kulankhula uthenga wa Mulungu, ndithudi aliyense wa odzozedwa ndi “khamu lalikulu” akafuna kulengeza iwo monga wofalitsa wokhazikika.
Maulosi Ochitiridwa Fanizo
9. (a) Ndimotani mmene Ezekieli anakhazikira chitsanzo kaamba ka ife? (b) Nchiyani chimene Ezekieli anachita kuti achitire chithunzi kugwira kwa Chibabulo kwa Yerusalemu, ndipo nchiyani chomwe chinasonyezedwa ndi masiku 390 ndi masiku 40?
9 Ezekieli kenaka anachitira fanizo maulosi osonyezedwa ndi ziwalo za thupi modzichepetsa ndi molimba mtima, kukhazikitsa chitsanzo chomwe chiyenera kutisonkhezera ife kuchita ntchito yathu yopatsidwa ndi Mulungu modzichepetsa ndipo molimba mtima. Kuti achitire chithunzi kuzinga kwa Chibabulo, iye anayenera kugona pansi akumayang’ana njerwa pa imene anazokotapo chithunzi cha Yerusalemu. Ezekieli anayenera kugonera kumbali yake ya kumanzere kwa masiku 390 kuti asenze mphulupulu ya ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli, kenaka kumbali yake ya kumanja kwa masiku 40 kuti asenze chimo la mafuko aŵiri a Yuda. Tsiku limodzi linaimira chaka. Chotero zaka 390 zinayambira kuchokera pa kukhazikitsidwa kwa Israyli mu 997 B.C.E. kufikira ku chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. Zaka 40 za Yuda zinachokera pa kuikidwa kwa Yeremiya monga mneneri wa Mulungu mu 647 B.C.E. kufikira ku kupasulidwa kwa Yuda mu 607 B.C.E.—Ezekieli 4:1-8; Yeremiya 1:1-3.
10. Ndimotani mmene Ezekieli anafanizira zotulukapo za kuzingako, ndipo ndi phunziro lotani limene tingaphunzire kuchokera ku chenicheni chakuti Mulungu anamdyetsa iye?
10 Ezekieli kenaka anachitira fanizo zotulukapo za kugwidwako. Kuti achitire chitsanzo njala, iye anadya kokha magramu mazana aŵiri a chakudya ndi chifupifupi mamililita mazana asanu a madzi pa tsiku. Mkate wake (kusakaniza kopanda lamulo kwa tirigu, balere, nyemba mphodza, mapira, ndi mawere zophikidwa pa ndowe) unali wodetsedwa. (Levitiko 19:19) Kachitidwe kameneka kanasonyeza kuti nzika za Yerusalemu zidzavutika ndi kusoweka kokulira. Koma chiri chotenthetsa mtima chotani nanga kudziwa kuti monga mmene Yehova anadyetsera Ezekieli pansi pa mikhalidwe yovuta, Mulungu adzatithandiza ife kukhalabe okhulupirika ndi kukwaniritsa ntchito yathu yolalikira m’chiyang’aniro cha zovuta zonse!—Ezekieli 4:9-17.
11. (a) Ndi machitidwe otani amene akutchulidwa pa Ezekieli 5:1-4, ndipo nchiyani chomwe chinali chizindikiritso chawo? (b) Chenicheni chakuti Mulungu anakwaniritsa mafanizo ochitiridwa chitsanzo a Ezekieli chiyenera kukhala ndi chotulukapo chotani pa ife?
11 Akumagwiritsira ntchito lupanga, Ezekieli kenaka anametsa tsitsi lake ndi ndevu. (Ŵerengani Ezekieli 5:1-4.) Awo akufa ndi njala ndi mliri adzakhala monga mbali yachitatu ya tsitsi la mneneriyo lomwe iye analitentha mkati mwa Yerusalemu. Akufa ndi nkhondo adzakhala monga gawo lachitatu lokanthidwa ndi lupanga. Opulumuka adzakhala omwazikana pakati pa mitundu monga gawo lachitatu la tsitsi lake lomwazidwa mu mphepo. Koma andende ena adzakhala mofanana ndi tsitsi lochepa lotengedwa ku gawo lomwazidwalo ndi kumangidwa m’malaya a Ezekieli kusonyeza kuti iwo adzatenga kulmabira kowona m’Yuda pamapeto pa zaka 70 za kupasulidwa. (Ezekieli 5:5-17) Chenicheni chakuti Yehova anakwaniritsa ichi ndi mafanizo ena a ulosi chiyenera kutifulumiza ife kukhulupirira iye monga Wokwaniritsa wa ulosi.—Yesaya 42:9; 55:11.
Chiwonongeko Kutsogolo!
12. (a) Ezekieli 6:1-7 amasonyeza kuti olowelera akachita chiyani? (b) Mogwirizana ndi ulosi wa Ezekieli, nchiyani chomwe chiri Yerusalemu wophiphiritsira, ndipo nchiyani chomwe chidzachitika kwa iye?
12 Mu 613 B.C.E., Ezekieli analankhula ku dzikolo kusonyeza chomwe chidzagwera nzika zolambira mafano za Yuda. (Ŵerengani Ezekieli 6:1- 7.) Oloŵerera akagwetsa malo okwezeka, zoimitsira za dzuŵa, ndi maguwa a nsembe ogwiritsidwa ntchito m’kulambira konama. Lingaliro lenilenilo la kusakaza ndi njala, mliri, ndi nkhondo kukampangitsa munthu kulira kuti “Kalanga ine!” ndi kugogomezera ichi mwa kuwomba m’manja ndi kuponda ndi phazi. Matupi akufa a adama auzimu akadzaza malo okwezeka. Pamene Chikristu cha Dziko, choimira chenicheni cha Yerusalemu, chidzavutika ndi chowonongeko chofananacho, chidzadziŵa kuti tsoka lake liri lochokera kwa Yehova.—Ezekieli 6:8-14.
13. Nchiyani chomwe chinali “ndodo” m’dzanja la Yehova, ndipo nchiyani chomwe chinayenera kutulukapo kuchokera ku kugwiritsira ntchito iye?
13 ‘Kutha kunali kufika pa ngodya zinayi za dziko,’ dongosolo la kachitidwe ka zinthu ka chipembedzo cha Yuda wosakhulupirika. “Tsoka” la zinthu zoipa likazinga mutu wa wolambira mafanoyo pamene “ndodo” m’dzanja la Mulungu—Nebukadinezara ndi makamu ake a Chibabulo—anachita motsutsana ndi anthu a Yehova ndi kachisi wake. Awo omwe anali ku “unyinji” wa Yuda wa ogula ndi ogulitsa akaphedwa kapena kutengedwa m’ndende, ndipo manja a aliwonse omwe anakhoza kukhala ndi moyo akagwa chifukwa cha mantha. Pa kugwetsedwa kwa dongosolo lawo la chipmenbedzo chonyenga, iwo akakhoza, monga mmene kuliri, kumeta mitu yawo kukhala ya mpala m’kulira maliro.—Ezekieli 7:1-18.
14. Nchiyani chomwe kupereka chiphuphu kukanalephera kuchita kaamba ka Yerusalemu, ndipo nchiyani chimene icho chimasonyeza ponena za Chikristu cha Dziko?
14 Yehova ndi makamu ake akupha sangapatsidwe chiphuphu. (Ŵerengani Ezekieli 7:19.) Kupereka chiphuphu sikukanapulumutsa “malo obisika,” Malo Opatulikitsa, ku kukhala odetsedwa pamene “achifwamba” a Akasidi anatenga zotengera zopatulika ndi kusiya kachisi wopasuka. Yehova ‘analeketsa kudzikuza kwa amphamvu’ pamene Mfumu Zedekiya anagwidwa ndipo akulu a ansembe Achilevi anaphedwa. (2 Mafumu 25:4-7, 18-21) Ayi, ochimwa m’Yerusalemu wogwidwayo akanapulumuka tsoka mwa kupereka chiphuphu pamene Mulungu ‘anawaŵeruza iwo’ monga akuswa pangano. Mofananamo, mkati mwa kusapatulika kowonekera kwa zinthu zolingaliridwa kukhala zopatulika mu Chikristu cha Dziko, iye sadzakhala wokhoza kupereka chiphuphu kuti athawe ku chiŵeruzo chake chaumulungu chomwe chikudza pa iye. Pa nthaŵiyo kudzakhala kuchedwa kwambiri kumvetsera kwa “mlonda” wa Yehova.—Ezekieli 7:20-27.
Kuusa Moyo pa Zinthu Zonyansa
15. Nchiyani chomwe Ezekieli anawona m’Yerusalemu, ndipo ndi chotulukapo chotani chimene ichi chiyenera kukhala nacho pa ife?
15 Pamene Ezekieli anawona masomphenya a Mulungu mu ulmerero pa Elul 5, 612 B.C.E., ‘chonga dzanja chinagwira tsitsi la pamutu pake’ ndi kumtenga iye kupita ku Yerusalemu mwa mzimu wa kuuzira. Gareta wa kumwamba anali atapitanso kumeneko. Chimene Ezekieli kenaka anawona chiyenera kutipangitsa ife kubwerera m’mbuyo pa lingaliro lenileni la kumvetsera kwa ampatuko. (Miyambo 11:9) Pa kachisi, ampatuko a Chiisrayeli anali kulambira chiphiphiritsiro cholambira mafano (mwinamwake mzati wopatulika) chomwe chinapangitsa Mulungu kuchita nsanje. (Eksodo 20:2-6) Akumalowa mkati mwa bwalo la mkati, ndi zinthu zonyansa zotani nanga zimene Ezekieli anawona! (Ŵerengani Ezekieli 8:10, 11.) Chinali chochititsa manyazi chotani nanga kuti akulu a Chiisrayeli 70 anali kupereka chonunkhiza kwa milungu yonyenga yoimiridwa ndi zosema zonyansa m’chipupa!—Ezekieli 8:1-12.
16. Masomphenya a Ezekieli amasonyeza chiyani ponena za zotulukapo za mpatuko?
16 Masomphenya a Ezekieli anasonyeza mmene mpatuko wauzimu uliri wakupha. Nkulekelanji, popeza akazi a Chiisrayeli anadzilowetsa m’kulirira pa Tamuzi, mulungu wa Chibabulo ndi wokonda wa mulungu wachikazi wa kubala Ishtar! Ndipo chinali chonyansa chotani nanga kuwona amuna 25 a Chiisrayeli m’bwalo la mkati la kachisi akulambira dzuŵa! (Deuteronomo 4:15-19) Ku mphuno ya Mulungu iwo ananyamula nthambi yonyansa, mwinamwake kuimira chiwalo cha mwamuna. Nchosadabwitsa kuti Yehova sanamvetsere ku mapemphero awo, mongadi mmene Chikristu cha Dziko chikafuna thandizo lake mosaphulapo kanthu mkati mwa “chisautso chachikulu”!—Ezekiel 8:13-18; Matthew 24:21.
Kuikidwa Chizindikiro Kaamba ka Chipulumuko
17. Ndi amuna asanu ndi aŵiri ati amene anawonedwa m’masomphenya, ndipo nchiyani chimene iwo anachita?
17 Potsatira, tikuwona amuna asanu ndi aŵiri—mmodzi mlembi wovala bafuta ndi asanu ndi mmodzi ena okhala ndi zida zophera. (Ŵerengani Ezekieli 9:1-7.) “Amuna sanu ndi mmodziwo” anaimira magulu akupha a kumwamba a Yehova, ngakhale kuti iye angagwiritsire ntchito nthumwi za pa dziko lapansi. Awo amene mphumi zawo zinaikidwa chizindikiro ndi ‘mwamuna wovala bafutayo’ akakumana ndi chifundo cha Mulungu chifukwa iwo sanamvere chifundo zinthu zonyansa zochitidwa m’kachisi. Kupha kochitidwa ndi “amuna sanu ndi mmodziwo” kunayamba pamenepo ndi akulu olambira mafano 70, akazi olirira Tamuzi, ndi olambira dzuŵa 25. Awa ndi ena osakhulupirika kwa Mulungu anaphedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E.
18. (a) Ndani amene ali ‘munthu wovala bafuta’ wamakono? (b) Nchiyani chomwe chiri “chizindikiro,” ndani amene tsopano ali nacho, ndipo kodi kukhala nacho kukatuluka m’chiyani?
18 ‘Munthu wovala bafuta’ wophiphiritsirayo ali gulu la Akristu odzozedwa. Iwo amapita kunyumba ndi nyumba kuika chizindikiro chophiphiritsira pa awo amene amakhala mbali ya “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Kristu. “Chizindikirocho” chiri umboni wakuti nkhosa zoterozo ziri anthu odzipereka, obatizidwa okhala ndi umunthu wonga wa Kristu. Iwo ‘amausa moyo ndi kulira pa zonyansa zonse’ zochitika mu Chikristu cha Dziko, ndipo atuluka m’Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:4, 5) “Chizindikiro” chawo chikachipangitsa icho kukhala chowonekeratu kwa magulu akupha a Mulungu kuti iwo ayenera kusiidwa mkati mwa “chisautso chachikulu.” Iwo angapeze “chizindikiro” chimenechi mwa kugawana ndi odzozedwa mkuikabe chizindikire pa ena. Chotero, ngati mwaikidwa kale ‘chizindikiro,’ gawanani mwachangu mu ntchito ‘yoika chizindikiro.’—Ezekieli 9:8-11.
Chiwonongeko Chamoto Kutsogolo!
19. Nchiyani chimene ‘munthu wovala bafuta’ wamakono akumwaza pa Chikristu cha Dziko?
19 Munthu wovala bafutayo anapita pakati pa magudumu a gareta wa kumwamba kukapeza makala a moto. Awa anaponyedwa pa Yerusalemu, kupereka chidziŵitso cha pasadakhale kuti chiwonongeko chake chikakhala chisonyezero cha mkwiyo wamoto wa Mulungu. (Ezekieli 10:1-8; Maliro 2:2-4; 4:11) M’tsiku la Ezekieli, mkwiyo wa Yehova unatsanuliridwa kupyolera mwa Ababulo. (2 Mbiri 36:15-21; Yeremiya 25:9-11) Koma bwanji ponena za tsiku lathu? Munthu wovala bafuta’ wophiphiritsirayo akumwaza uthenga wamoto wa Mulungu m’Chikristu cha Dziko chonse monga chidziŵitso chakuti mkwiyo waumulungu posachedwapa udzatulutsidwa pa iye ndi mbali yonse ya Babulo Wamkulu. Ndithudi, awo okana kumvetsera kwa “mlonda” wa Yehova alibe chiyembekezo cha chipulumuko.—Yesaya 61:1, 2; Chivumbulutso 18:8-10, 20.
20. (a) Ndimotani mmene chigwirizano pakati pa magudumu a magareta a kumwamba ndi akerubi chiyenera kutiyambukirira ife? (b) Nchiyani chimene akalonga ena anali kuchita, ndipo kodi iwo molakwika anayerekeza Yerusalemu ndi chiyani?
20 Chisamaliro chikukokedweranso ku gareta wa kumwamba, gulu lakumwamba la Mulungu. Tikumawona kugwirizana pakati pa magudumu a garetawo ndi akerubi, tiyenera kufulumizidwa kugwirizana kotheratu ndi gulu la pa dziko lapansi la Mulungu. Chifukwa cha chimvero, tiyeneranso kulichinjiriza ilo kuchokera kwa amuna onyenga. (Ezekieli 10:9-22) Panali amuna oterowo m’tsiku la Ezekieli, popeza iye anawona kalonga a boma 25 akumapangana upo kuwukira magulu akupha a Mulungu ndi thandizo la Aigupto. Iwo anayerekeza Yerusalemu kukhala mphika waukulu, ndipo iwo eni kukhala nyama yosungika mkati. Koma iwo anali olakwa motani nanga! “Lupanga” la “alendo” Achibabulo likapha ena a owukirawo, pamene kuli kwakuti ena akakhala andende. Ichi chinayenera kuchitika popeza Mulungu anawapatsa thayo Ayudawo kaamba ka kuswa pangano lake. (Ezekieli 11:1-13; Eksodo 19:1-8; 24:1-7; Yeremiya 52:24-27) Chifukwa chakuti Chikristu cha Dziko chimadzinenera kukhala m’pangano ndi Mulungu koma chimaika chidaliro mu zigwirizano za kudziko, icho chidzatha pansi pa chiwukiro cha mphamvu zakupha za Yehova.
21. Nchiyani chimene chinachitika pamapeto a kukhalitsidwa bwinja kwa zaka 70 kwa Yuda, ndipo ndi chichitika chofanana nacho chotani chimene chinayambukira otsalira odzozedwa?
21 Ngakhale kuti Aisrayeli ‘anamwazidwa pakati pa maiko,’ monga mu 617 B.C.E., Mulungu anali “malo opatulika,” kapena populumukirapo, kwa andende olapa. (Ezekieli 11:14-16) Koma nchiyani chinanso chimene chingayembekezeredwe? (Ŵerengani Ezekieli 11:17-21.) Pambuyo pa kusakazidwa kwa zaka 70 kwa Yuda, otsalira anabwezeretsedwa ku “nthaka ya Israyli” yoyeretsedwa. Molinganako, pambuyo pa kuikidwa m’ndende kwa Chibabulo, otsalira odzozedwa anawomboledwa mu 1919, ndipo pansi pa chitsongozo cha mzimu wa Mulungu, “nthaka” yomwe pa nthaŵi imodzi inali yokhalitsidwa bwinja ya Israyeli wauzimu yayeretsedwa. Chotero, awo ‘oikidwa chizindikiro’ kaamba ka kusungidwa tsopano akusangalala ndi chiyanjo chaumulungu limodzi ndi otsalira a Israyeli wauzimu obwezeretsedwa. Ndipo ngati mupitirizabe kumvetsera kwa “mlonda” wa Mulungu, inu mungakhale pakati pa opulumuka pamene Yehova asolola lupanga lake.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati nthaŵi ilola, wotsogoza ayenera kupangitsa malemba olembedwa m’zilembo zing’ono kuŵerengedwa mkati mwa phunziro la mpingo la nkhaniyi ndi ziŵiri zomwe zitsatira iyo. Mfundo zazikulu za Baibulo mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki zingatengedwenso kuchokera ku nkhani zimenezi m’maphunziro a posachedwapa a bukhu la Ezekieli.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kumvetsera pamene “mlonda” wa Yehova akulankhula?
◻ Nchiyani chomwe chinaimiridwa ndi gareta wa kumwamba wa Mulungu?
◻ Ndani amene akutumikira monga “mlonda” wa Yehova lerolino?
◻ Ndi machitidwe ampatuko otani amene Ezekieli anawona m’Yerusalemu, ndipo ndimotani mmene masomphenya amenewa ayenera kutiyambukirira ife?
◻ Ndani amene ali ‘munthu wovala bafuta’ wamakono, ndipo nchiyani chimene chiri “chizindikiro” chimene akuika pa mphumi?