Gareta Lakumwamba la Yehova Likuyenda
‘Kunena za [magudumu, “NW”] wina anazifuulira, ndiri chimvere ine, Kunkhulirani.’—EZEKIELI 10:13.
1. Kodi Yehova ali ndi choyendera chamtundu wanji?
MASIKU ano andege zajeti zonyezimira, atsogoleri adziko angalingalire kuti akusangalala ndi chipambano chabwino koposa choyendera. Komabe, Yehova Mulungu anavumbula zaka 2,600 zapitapo kuti iye ali ndi choyendera chamtundu wapamwamba kwenikweni, chimene palibe injiniya aliyense anachiwonapo. Choyenderachi ndi gareta lalikulu, lowopsa! Kodi kukumveka kwachilendo kuti Mlengi wachilengedwe chonse amakwera m’galimoto longa gareta? Ayi, pakuti galimoto lakumwamba la Yehova nlosiyana kwabasi ndi lowonedwapo ndi munthu lirilonse.
2. Kodi Ezekieli mutu 1 amalisonyeza motani gareta lakumwamba la Yehova, ndipo kodi mneneriyo akukokera chisamaliro chathu kwandani choyamba?
2 M’mutu 1 wa ulosi wa Ezekieli, Yehova akuchitiridwa chithunzi kukhala akukwera m’gareta lakumwamba lalikulu kwambiri. Galimoto lowopsa la magudumu anayi limeneli limayenda lokha ndipo lingachite zinthu zozizwitsa. Ezekieli analiwona gareta lakumwambali m’masomphenya mu 613 B.C.E., pamene anali paumodzi wa mifuleni yokumba ya Babulo wakalekale. Mneneriyo choyamba akukokera chisamaliro chathu kwa omwe akutumikira gareta la Yehova lakumwambali. Pamene tikuŵerenga, tiyeni tiyese kuwona m’masomphenya chimene Ezekieli anachiwona.
Zamoyo Zinayi
3. Kodi nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi nkhope zinayi za akerubi anayiwo?
3 Ezekieli akusimba motere: ‘Ndinapenya, ndipo tawonani, mkuntho wa mphepo wochokera kumpoto, mtambo waukulu ndi moto wofukusika m’mwemo, ndi pozungulira pake padachita cheza, . . . ndi mkati mwake mudawoneka mafaniziro a zamoyo zinayi.’ (Ezekieli 1:4, 5) Chirichonse cha zamoyo zinayizi, kapena akerubi, chinali ndi mapiko anayi ndi nkhope zinayi. Izo zinali ndi nkhope ya mkango, kutanthauza chilungamo cha Yehova; nkhope ya ng’ombe ya mphongo, kuimira mphamvu za Mulungu; ndi nkhope ya chiwombankhanga, kutanthauza nzeru Zake. Izo zinalinso ndi nkhope ya munthu, kutanthauza chikondi cha Yehova.—Deuteronomo 32:4; Yobu 12:13; Yesaya 40:26; Ezekieli 1:10; 1 Yohane 4:8.
4. Kodi nchifukwa ninji akerubiwo anali ndi nkhope zinayi, ndipo kodi liŵiro la akerubi linafanana ndi chiyani?
4 Kerubi aliyense anali ndi nkhope yoyang’ana kumbali imodzi ya mbali zinayizo. Chotero, akerubiwo akatembenuka mofulumira ndi kutsatira nkhope yomwe inalunjika kutsogolo kofunidwa. Koma kodi liŵiro la akerubiwo linafanana ndi chiyani? Eya, iwo akakhoza kuyenda paliŵiro la mphezi! (Ezekieli 1:14) Palibe galimoto lopangidwa ndi munthu lomwe lafikira liŵiro limenelo.
5. Kodi Ezekieli anawafotokoza motani magudumu a garetalo ndi mikombero yawo?
5 Mwadzidzidzi, magudumu a garetali awonekera. Iwo ngachilendo chotani nanga! Mavesi 16 ndi 18 akuti: ‘Mawonekedwe awo ndi mapangidwe awo anali ngati [magudumu aŵiri, NW] opingasitsana. Ndi mikombero yake inali yokuzika ndi yowopsa; ndi izi zinayi zinali ndi mikombero yawo yodzala ndi maso pozungulira pawo.’ Gudumu limodzi pambali pa kerubi aliyense likatulukapo magudumu anayi m’malo ogwirizana anayi. Magudumuwa ananyezimira mofanana ndi krustalo, mwala wochenima mopenyeka, wochezima moyezuka kapena wobiriŵira. Ichi chimawonjezera kuwalima kwina ndi kukongola ku masomphenya a ulemererowa. Popeza kuti mikombero ya magudumuwa inali ‘yodzala ndi maso moizungulira,’ iwo sankayenda kulikonse mwadzandidzandi. Ndipo magudumuwa anali aatali kwambiri, kwakuti akafika pamtunda wautali mwa kungozungulira kamodzi kuchoka pamaziko awo. Iwo, mofananana ndi akerubi anayiwo, akayenda paliŵiro lofanana ndi mphezi.
Magudumu Mkati mwa Magudumu
6. (a) Kodi ziri bwanji kuti garetalo linali ndi magudumu mkati mwa magudumu? (b) Kodi magudumuwo anagwirizana ndi chiyani m’kuyenda kwawoko?
6 Chinthu chinachake chinalinso chachilendo. Gudumu lirilonse linali ndi gudumu mkati mwake—gudumu lobulungira mofanana nalo limene linapingasa mkati mwa gudumu lakunjalo. Ndimwanjira yokhayi kunganenedwere kuti magudumuwa ‘poyenda anayenda kumbali zawo zinayi.’ (Vesi 17) Magudumuwo akatembenukira chapamodzi poyenda chifukwa chakuti panali mbali ya gudumu yoloza kotembenukira kulikonse. Magudumuwo anatsatira chitsogozo cha kuyenda kwa akerubi anayiwo. Pamagudumu anayiwo, thupi la gareta lonse la Mulungu likakhoza kuyenda mwa kuchilikizidwa kosawoneka ndi maso kofanana ndi chipangizo champhamvu chochilikizidwa molenjekeka m’mlengalenga pamene chikuzungulira pamwamba pamadzi.
7. Kodi nchiyani chomwe chinali magwero amphamvu za magudumuwo?
7 Kodi magudumuwo anaipeza kuti mphamvu imeneyi ya kutsatira mayendedwe onse a akerubi anayiwo? Kuchokera kwa mzimu woyera wa Mulungu Wamphamvuyonse. Vesi 20 likuti: ‘Kulikonse mzimu ukuti umuke, zinamuka . . . pakuti mzimu wa zamoyozo unali m’magudumuwo.’ Mphamvu yogwira ntchito yosawoneka yofananayo ya Mulungu imene inali mwa akerubi inalinso m’magudumuwo.
8. Kodi magudumuwo anapatsidwa dzina lotani, ndipo nchifukwa ninji?
8 Magudumuwo akutchedwa ndi liwu lakuti “kunkhulirani.” (Ezekieli 10:13) Ili mwachiwonekere linatchulidwa mogwirizana ndi chimene gudumu lirilonse limachita. Ilo limayenda mozungulira kapena kukunkhulika. Kutchula mbali imeneyi ya gareta lakumwamba ndi dzina loterolo kumatikumbutsa za liŵiro limene gareta lakumwambalo likuyenderapo. Ngakhale kuti magudumu ake anakunkhulika mofulumira kwenikweni, iwo anawonabe njira zawo chifukwa cha kudzala ndi maso kwawo.
9. Kodi Ezekieli anachifotokoza motani chomwe chinali pamwamba pa magudumu anayi a gareta oyenda mwaliŵirowo?
9 Koma tsopano tiyeni tiyang’ane pamwamba pa magudumu aatali owopsawa, oyenda mwaliŵiro kwenikweni ndikuwona chomwe chiri pamwambapo. Vesi 22 la Ezekieli mutu 1 likuti: ‘Pa mitu ya zamoyozi panali chifaniziro cha thambo, monga mawalidwe a krustalo wowopsa, loyalika pamwamba pamitu pawo.’ Thamboli, ngakhale kuti nlolimba gwa, linali lowalima mopenyekera, ‘monga mawalidwe a krustalo wowopsa.’ Linkang’anima mofanana ndi madiamond zikwizikwi atawalidwa ndi dzuŵa. Nzowopsadi!
Wokwera Gareta Waulemereroyo
10. (a) Kodi mpando wachifumu ndi Wokhalapoyo zafotokozedwa motani? (b) Kodi nchiyani chomwe chikutanthauzidwa ndi mfundo yakuti Wokwera pa garetalo wakutidwa ndi ulemerero?
10 Mwachiwonekere, garetalo likuima kuti Wokwerayo alankhule ndi Ezekieli. Pamwamba pa thambo, pali chifaniziro cha mpando wachifumu, mawonekedwe ake ngati mwala wa safiro, kapena wabiriŵiri. Pampando wachifumupo, pali Winawake wofanana ndi munthu wa padziko lapansi. Mpangidwe wa munthuyu unali mawonekedwe abwino kwabasi othandiza Ezekieli kuzindikira kuvumbulidwa kwaumulunguku. Koma mpangidwe wa munthuwu wakutidwa ndi ulemerero, kotero kuti ukuwala ngati chitsulo chakupsa, chipangizo chonyezimira cha siliva ndi golide. Ha, ndi kukongola kochititsa kakasi chotani nanga! Kuyambira mawonekedwe a m’chiuno a munthuyu, kunyezimira kwaulemereroku kwamzinga ponse paŵiri pamwamba ndi kunsi kwake. Chotero mpangidwe wonsewo wakometseredwa ndi ulemerero. Ichi chikusonyeza kuti Yehova ngwonyezimira mosaneneka. Ndiponso, Wokwera garetayo atsagana ndi utawaleza wokongola. Kutagwa mvula yamkuntho, kumakhala kodzetsa mtendere ndi kwabata chotani nanga titawona utawaleza! Pokhala ndi mkhalidwe wabata umenewu, Yehova amasungabe mikhalidwe yake ya nzeru, chilungamo, mphamvu, ndi chikondi kukhala zolinganizika mwangwiro.
11. Kodi Ezekieli anayambukiridwa motani ndi masomphenya a gareta ndi mpando wachifumu wa Yehova?
11 Gareta la Yehova ndi mpando wake wachifumu zazunguliridwa ndi kuwala ndi mitundumitundu yokongola. Ngwosiyana chotani nanga ndi Satana, kalonga wa mdima ndi wakupenduza! Ndipo kodi Ezekieli anayambukiridwa motani ndi zonsezi? Iye akuti: ‘Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mawu a wina wakunena.’—Ezekieli 1:28.
Chimene Garetalo Linasonyeza
12. Kodi gareta lakumwamba la Yehova limachitira chithunzi chiyani?
12 Kodi gareta lozizwitsali likuchitira chithunzi chiyani? Gulu lakumwamba la Yehova Mulungu. Nlopangidwa ndi zolengedwa zake zonse zauzimu zoyera muufumu wosawoneka—aserafi, akerubi, ndi angelo. Popeza kuti Yehova ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, zolengedwa zake zonse zauzimu zimagonjera kwa iye, ndipo amazikwera m’lingaliro la kuzilamulira kotheratu ndi kuzigwiritsira ntchito mogwirizana ndi chifuno chake.—Salmo 103:20.
13. (a) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti Yehova akukwera pa gulu lake? (b) Kodi ndimotani mmene masomphenya a gareta la magudumu anayi la Yehova lomwe likuyenda akukuyambukirani?
13 Yehova amayendetsa gulu limeneli monga ngati kuti ali pa gareta, kulipangitsa kupita kulikonse kumene mzimu ulisonyeza kumukako. Ilo silikuyenda mwadzandidzandi, popanda kulamuliridwa kapena kuyang’aniridwa kwaluntha. Mulungu sakulilola gululi kunka kulikonse kumene lingafune kumukako. Mmalomwake, ilo limatsatira chitsogozo chake. Chapamodzi, onse akunka patsogolo mogwirizana kukwaniritsa kotheratu zolinga za Mulungu. Ndigulu lakukwamba lozizwitsa chotani nanga lomwe likuvumbulidwa ndi masomphenyawa a gareta la Yehova lakumwamba la magudumu anayi limeneli lomwe likuyenda! Mogwirizana ndi ichi, gulu la Yehova laimiridwa kukhala liri ndi mbali zinayi, lolinganizika mwangwiro.
Kuikidwa Monga Mlonda
14. Kodi ndani yemwe akuchitiridwa chithunzi ndi mneneri Ezekieli?
14 Koma kodi ndani yemwe akuchitiridwa chithunzi ndi mneneri Ezekieli? Kuchokera m’zenizeni za m’mbiri, nkwachiwonekere kuti bungwe lodzozedwa ndi mzimu la Mboni za Yehova lagwirizanitsidwa ndi gareta lakumwambalo. Motero, Ezekieli amachitira chithunzi bwino lomwe otsalira odzozedwa a Mboni za Yehova chiyambire 1919. Gulu lakumwamba la Mulungu linadzagwirizana mwauzimu ndi otsalira odzozedwa m’chaka chimenecho, kuŵapatsanso mphamvu monga Mboni za Yehova padziko lonse. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 11:1-12.) Gulu longa garetalo linkayenda panthaŵiyo, monga momwe lidakayendabe lerolino. Kwenikweni, magudumu ake opita patsogolowo akuzungulira mofulumira kuposa kalelonse. Yehova akuzithamangitsira patsogolo mwaliŵiro!
15. Kodi liwu la Wokwera pa gareta wakumwamba likunenanji, ndipo kodi Ezekieli akulandira ntchito yotani?
15 Ezekieli anafuna kudziŵa chifukwa chimene gareta lakumwambali linayenda pamaso pake ndi kuima. Iye anadzazindikira pamene liwu linamvekera kwa iye kuchokera kwa Yemwe anakhala pa garetalo. Atachititsidwa nthumanzi ndi chochitika chowopsachi, Ezekieli anagwetsa nkhope pansi. Mvetserani pamene mawu a Wokwera gareta lakumwambalo akulankhula motere: ‘Wobadwa ndi munthu iwe, khala chiriri, ndipo ndidzanena nawe.’ (Ezekieli 2:1) Pamenepo Yehova anamuika Ezekieli kukhala mlonda ndi kuchenjeza nyumba yopanduka ya Israyeli. Iye wapatsidwadi ntchito ya kulankhula m’dzina laumulungu. Dzina la Ezekieli limatanthauza “Mulungu Amalimbitsa.” Chotero kuli tero kuti Mulungu walimbitsa gulu la Ezekieli ndi kulitumiza, kuwaika kukhala mlonda ku Chikristu Chadziko.
16, 17. (a) Kodi masomphenya a gareta lakumwamba anampindulitsa motani Ezekieli? (b) M’tsiku lathu, kodi ndimotani mmene kumvetsetsa masomphenya a gareta lakumwamba kunayambukira gulu la Ezekieli ndi khamu lalikulu?
16 Masomphenya a gareta lakumwamba anatsimikizira kukhala abwino ndi ozizwitsa kwa mneneri Ezekieli, koma anamkonzekeretsanso kaamba ka ntchito imene iye anapatsidwa monga mlonda kuchenjeza za chiwonongeko chomadzacho pa Yerusalemu. Zofananazi zakhaladi tero ndi gulu la mlonda lerolino. Kuzindikira kwawo masomphenya a kuyenda kwa gareta lakumwamba la Yehova kwakhala kolimbikitsa kwenikweni kwa otsalira odzozedwa. Mu 1931, anaphunzira zambiri ponena za masomphenya a Ezekieli, monga momwe kunavumbulidwira mu Bukhu Loyamba lakuti Vindication. Iwo anadzazidwa ndi kuzindikira kolama koteroko kwakuti kuyambira ndi kope la October 15, 1931, mpaka la August 1, 1950, chithunzi cha chikuto cha magazini a Nsanja ya Olonda chinakhala ndi chithunzi cholembedwa cha masomphenya a Ezekieli a gareta lakumwamba pa ngondya yake ya kulamanja. Motero, gulu la Ezekieli lachitapo kanthu pantchito yogaŵiridwa kwa iwo, ndipo lakhala likutumikira monga mlonda, likumapereka chenjezo laumulungu. Nthaŵi ya chiwonongeko chamoto cha Chikristu Chadziko chochokera kwa Yehova wokhala pampando wake wachifumu pa gareta lake lakumwamba sikudakhalepo pafupi motere!
17 Lerolino, ‘khamu lalikulu’ la anthu onga nkhosa lagwirizana ndi otsalira odzozedwa. (Chibvumbulutso 7:9) Chapamodzi, akupereka chenjezo la chiwonongeko chikudzacho pa Chikristu Chadziko ndi dongosolo lopanduka lonse la zinthu iri. Ntchito yochenjeza imeneyo idakakulirakulirabe, ndipo monga momwe zasonyezedwera pa Chibvumbulutso 14:6, 7, angelo akuichilikiza.
Kuyendera Limodzi ndi Gareta Lakumwamba
18. Kodi chiyenera kuchitidwa nchiyani kuti tipitirizebe kuchilikizidwa ndi angelo, ndipo kodi nchiyani chomwe tiyenera kulabadira?
18 Angelo ogonjerawo amayenda mogwirizana kwenikweni monga mbali ya gulu lakumwamba la Mulungu pamene akuthandiza atumiki a Yehova a padziko lapansi kukwaniritsa ntchito yawo ya kulengeza machenjezo a ziweruzo zaumulungu. Ngati tikufuna chitetezo chopitirizabe ndi chitsogozo cha atumiki amphamvu a Mulungu aungelowa, nafenso tiyenera kumayendabe mogwirizana ndi kumvana ndi kukunkhulira kophiphiritsirako. Kuwonjezerapo, monga mbali ya gulu lowoneka ndi maso la Yehova loyendera limodzi ndi gareta lake lakumwamba, tiyenera kumva msanga zitsogozo za mzimu wa Mulungu. (Yerekezerani ndi Afilipi 2:13.) Ngati ndife Mboni za Yehova, tiyenera kutembenukira kumene gareta lakumwambali likunkako. Sitiyeneradi kupikisana nalo. Titapatsidwa zitsogozo zonena za njira yomwe tiyenera kunkako, tiyenera kuitsatira. Chotero, mpingo sumapatukana.—1 Akorinto 1:10.
19. (a) Mongadi mmene magudumu a gareta lakumwamba ali ndi maso mowazungulira, kodi anthu a Yehova ayenera kukhala ogalamuka kuchiyani? (b) Kodi ndiiti imene iyenera kukhala njira ya kachitidwe kathu m’nthaŵi zovuta zino?
19 Maso ozungulira magudumu a gareta la Mulungu amatanthauza kugalamuka. Monga mmene gulu lakumwamba lirili logalamuka, nafenso tiyenera kukhala ogalamuka kuchilikiza gulu la Yehova la padziko lapansi. Mumpingo, kuchilikizaku tingakusonyeze mwakugwirizana ndi akulu akumaloko. (Ahebri 13:17) Ndipo mnthaŵi zoipa zino, Akristu ayenera kumamatira mwathithithi kugulu la Yehova. Sitifunikira kupereka mamasulidwe athuathu a zochitika, pakuti tikatero sitidzakhala tikuyendera limodzi ndi gareta lakumwamba la Yehova. Nthaŵi zonse tiyeni tidzifunse kuti, ‘Kodi gareta lakumwambali likuloza kuti?’ Ngati tiyendera limodzi ndi gulu lowoneka ndi maso la Mulungu, tidzakhala tikuyendera limodzi ndi mbali yosawoneka ya gululo.
20. Kodi mtumwi Paulo akupereka uphungu wabwino wotani pa Afilipi 3:13-16?
20 Pankhaniyi, Paulo analemba kuti: ‘Abale, ine sindiŵerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam’mbuyo, ndi kutambalitsira zam’tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ichi mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzavumbulutsira inu; chokhachi, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.’—Afilipi 3:13-16.
21. Kodi kupanga kupita patsogolo kwauzimu m’gulu la Mulungu kumakhala kothekera mwa kutsatira mayendedwe otani?
21 Liwu lakuti “mayendedwe” panopa silimatanthauza kanjira kopapatiza mmene sitingadzifutukule. Atumiki a Yehova ali ndi mayendedwe abwino kwambiri omwe amapanga nawo kupita patsogolo kwauzimu. Iwo ndi mayendedwe a kukhala ndi phunziro laumwini Labaibulo, kupezeka pamisonkhano yampingo, kukhala okhazikika m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu, ndi kusonyeza mikhalidwe ya gulu lakumwamba la Mulungu. Mayendedwe oterowo amawatheketsa kutsatira zitsogozo za gulu lakumwamba la Yehova longa gareta. Mwa kulimbikira mwanjirayi, tidzafikira chonulirapo chathu, kaya ikhale mphotho ya moyo wosafa kumwamba kapena moyo wosatha m’paradaiso wa padziko lapansi.
22. (a) Kuti otsalira odzozedwa ndi khamu lalikulu la nkhosa zina akhale olinganizidwa mogwirizana, kodi nchiyani chomwe chiyenera kuchitidwa? (b) Kodi nchiyani chomwe sichimabisika kwa Yehova?
22 Monga momwe Yohane 10:16 akusonyezera, “nkhosa zina” ndi gulu la Ezekieli akakhala ogwirizana. Chotero, nkofunika kuti onse okhala m’gulu la Yehova azindikire tanthauzo lokwanira ndi kupatulika kwa masomphenya olembedwa mu Ezekieli mutu 1 ngati ati ayende mogwirizana ndi gareta lakumwamba la Mulungu. Masomphenya ake amatithandiza kuzindikira kuti tiyenera kuyenda mogwirizana ndi gulu la Mulungu, lowoneka ndi losawoneka. Kumbukiraninso, kuti maso a Yehova “ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye.” (2 Mbiri 16:9) Palibe kanthu kamene Yehova samakawona, makamaka chirichonse chokhudzana ndi chifuniro chake cha kudziyeretsa yekha monga Mfumu Yachilengedwe chonse.
23. Ndi gareta lakumwamba la Yehova lomwe likuyenda, kodi nchiyani chomwe tiyenera kuchita?
23 Lerolino gareta lakumwamba la Yehova likuyendadi. Posachedwapa chirichonse chidzabweretsedwa ku ulemerero mogwirizana ndi Wolemekezeka yemwe akukwera garetalo—zonsezo kumuyeretsa monga Mfumu Ambuye wachilengedwe chonse. Aserafi ake, akerubi, ndi angelo akutichilikiza m’ntchito yathu yaikulu ya kulalikira kwa padziko lonse. Chotero, tiyeni tipite patsogolo ndi gulu lakumwamba la Yehova. Koma kodi ndimotani mmene tingayendere limodzi ndi gareta lakumwamba loyenda mwaliŵiro choterolo?
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimikhalidwe yotani imene ikuimiridwa ndi zolengedwa zinayi zowonedwa ndi Ezekieli?
◻ Kodi gareta lakumwamba la Yehova limachitira chithunzi chiyani?
◻ Kodi ndani yemwe akuchitiridwa chithunzi ndi mneneri wa Mulungu Ezekieli?
◻ Kodi kumvetsetsa gareta lakumwamba la Yehova kwayambukira motani gulu la Ezekieli ndi khamu lalikulu?