Mutu 8
Alanditsidwa ku Mano a Mikango!
1, 2. (a) Kodi Dariyo Mmedi analinganiza motani ufumu wake wofutukukawo? (b) Fotokozani ntchito ndi ulamuliro wa akalonga.
BABULO anagwa! Ulemerero wake wa zaka zana limodzi unafafanizidwa m’maola oŵerengeka chabe. Kenako nyengo yatsopano inalikuyamba. Nyengo ya Amedi ndi Aperisiya. Dariyo Mmedi, woloŵa m’malo mwa Belisazara monga mfumu, anali ndi chintchito cholinganiza ufumu wake wofutukukawo.
2 Imodzi mwa ntchito zimene Dariyo anayamba inali kusankha akalonga okwanira 120. Akuti aja amene anatumikira paudindo umenewo nthaŵi zina anali kuwasankha kuchokera m’banja la mfumu. Mulimonse mmene zinalili, kalonga aliyense anayang’anira chigawo chachikulu kapena dera locheperapo la ufumuwo. (Danieli 6:1) Ntchito zake zinaphatikizapo kukhometsa misonkho ndi kuitumiza kwa mfumu. Ngakhale kuti nthaŵi ndi nthaŵi nduna ina ya mfumu inkamuyendera kuona mmene akuyendetsera zinthu, kalonga anali ndi ulamuliro waukulu. Dzina lake la ntchito linatanthauza “woteteza Ufumu.” M’dera lake, kalonga amaonedwa ngati mfumu yaing’ono, yokhala ndi ulamuliro wofananako ndi wa mfumu.
3, 4. Kodi Dariyo anam’konderanji Danieli, ndipo mfumuyo inamuika paudindo wotani?
3 Kodi Danieli akakhala pamalo otani m’boma latsopano limeneli? Kodi Dariyo Mmedi, akam’pumitsa pantchito mneneri wachiyudayu wokalamba amene tsopano anali m’zaka za ma 90? Kutalitali! Mosakayikira, Dariyo anazindikira kuti Danieli anali atanenera molondola za kugwa kwa Babulo ndi kuti kulosera koteroko kunatheka ndi luntha laumulungu. Ndiponso, kwa zaka zambiri Danieli anakhala ndi andende osiyanasiyana obwera ku Babulo, choncho anali kudziŵa mokhalira nawo. Dariyo anafunitsitsa kusunga mtendere pakati pa iwo ndi nzika zatsopano zimene anazigonjetsa. Choncho, iye anafunitsitsa kuti munthu wanzeru ndi wa chidziŵitso ngati Danieli, akhale pafupi ndi mpando wake wachifumu. Paudindo wotani?
4 Ngati Dariyo anaika Myuda wandendeyu, Danieli, kukhala kalonga, anthu ake akanadabwa kwambiri. Koma tangolingalirani mmene iwo anazunguzikira maganizo pamene Dariyo analengeza kuti Danieli waikidwa kukhala mmodzi wa akuluakulu oyang’anira akalonga! Sizinali zokhazo, komanso Danieli “anaposa” akuluakulu anzakewo. Ndithudi, mwa iye munapezeka “mzimu wopambana.” Dariyo anafuna kum’patsa ngakhale udindo wa nduna yaikulu.—Danieli 6:2, 3.
5. Kodi akuluakulu enawo ndi akalonga anamva bwanji atamva za kusankhidwa kwa Danieli, ndipo n’chifukwa chiyani anamva choncho?
5 Mwachionekere, zimenezo zinakwiyitsa kwambiri akuluakulu enawo ndi akalonga. Iwo sanathe kupirira kuti Danieli, wosakhala Mmedi, wosakhalanso Mperisiya, komanso wosachokera ku banja la mfumu akhale paudindo wowayang’anira! Koma n’chifukwa chiyani Dariyo anakweza mlendoyo, ndi kusiya anthu a kwawo, ngakhalenso a banja lake enieniwo? Kachitidwe kameneko kanaonekadi kukhala kukondera koipa. Ndiponso, n’kwachidziŵikire kuti akalongawo anaona kukhulupirika kwa Danieli monga chopinga pamachitachita awo autambwali ndi achinyengo. Komabe, akuluakulu ndi akalongawo sakanatha kum’fikira Dariyo pankhaniyo. Ndi iko komwe, Dariyo amam’lemekeza kwambiri Danieli.
6. Kodi akuluakulu ndi akalongawo anayesa motani kum’gwetsa Danieli, ndipo analephera bwanji?
6 Choncho andale a nsanje ameneŵa anamvana kuti am’chitire chiwembu. Iwo “anayesa kum’tola chifukwa Danieli, kunena za ufumuwo.” Kodi panali cholakwika chilichonse mmene iye anayendetsera ntchito yake? Kodi anali wosakhulupirika? Akuluakulu ndi akalongawo analephera kupeza mlandu wosasamala zinthu kapena cholakwa chilichonse panjira imene Danieli anayendetsera ntchito yake. Kenako iwo anati: “Sitidzam’tola chifukwa chilichonse Danieli amene, tikapanda kum’tola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.” Choncho atambwali ameneŵa anakonza chiwembu. Iwo anaona kuti tsopano akam’khaulitsa ndi kum’maliziratu Danieli.—Danieli 6:4, 5.
CHIWEMBU CHAUMBANDA
7. Kodi akuluakulu ndi akalongawo anapempha chiyani kwa mfumu, ndipo anachita zimenezo m’njira yotani?
7 Dariyo anafikiridwa ndi akuluakulu ndi akalonga amene ‘anasonkhana kwa mfumuyo mofulumira.’ Mawu achialamu pano amatanthauza chipwirikiti cha anthu. Mwachionekere, amuna ameneŵa anaonetsa ngati kuti anafika kwa Dariyo ndi nkhani yofunika msangamsanga. Ayenera anaganiza kuti iye sadzakayikira pempho lawo ngati alipereka motsimikiza kwambiri monga lofuna kuchitapo kanthu nthaŵi yomweyo. Choncho mosazengereza, iwo anati: “Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango.”a—Danieli 6:6, 7.
8. (a) N’chifukwa chiyani Dariyo anaona kuti lamulo limene anapemphalo linali labwino? (b) Kodi cholinga chenicheni cha akuluakulu ndi akalongawo chinali chiyani?
8 Zolemba za mbiri yakale zimatsimikizira kuti kunali kofala kulambira mafumu a ku Mesopotamiya monga milungu. Choncho Dariyo ananyengerereka ndi pempho limenelo. Mwina iyenso anaonapo ubwino wina. Kumbukirani, Dariyo anali mlendo ndi watsopano kwa anthu okhala m’Babulo. Lamulo latsopano limeneli likathandiza kum’khazikitsa bwino monga mfumu, ndipo likalimbikitsa makamu okhala m’Babulo kusonyeza kukhulupirika kwawo ndi kuchirikiza ufumu watsopanowo. Koma popempha lamulo limenelo, akuluakulu ndi akalongawo sanaganize konse za ubwino wa mfumu. Cholinga chawo chenicheni chinali chakuti am’kole Danieli, popeza anadziŵa kuti iye anali ndi chizoloŵezi chopemphera kwa Mulungu katatu patsiku pamazenera otseguka a chipinda chake chapatsindwi.
9. N’chifukwa chiyani lamulo latsopanolo silinapereke vuto kwa ambiri amene sanali Ayuda?
9 Kodi lamulo loletsa kupemphera limeneli linapereka vuto kwa olambira onse a m’Babulo? Osati kwenikweni, makamaka chifukwa chiletsocho chinali cha mwezi umodzi wokha. Komanso, ndi ochepa amene sanali Ayuda, amene akanaona kuti n’kulakwa kulambira munthu kwakanthaŵi chabe. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Kulambira mfumu sikunali nkhani yaikulu kwa mitundu yambiri yolambira mafano; choncho pamene Ababulowo analamulidwa kulemekeza Dariyo Mmedi mwa kum’pembedza monga mulungu, anamvera lamulolo mosawiringula. Ayuda okha ndiwo ananyansidwa nalo lamulolo.”
10. Kodi Amedi ndi Aperisi ankaliona motani lamulo limene mfumu inapereka?
10 Mulimonse mmene zinalili, alendo a Dariyo anam’limbikitsa kuti ‘akhazikitse choletsacho, ndi kutsimikiza cholembedwacho, kuti chisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.’ (Danieli 6:8) Kumayiko a Kum’maŵa akale, chifuniro cha mfumu nthaŵi zambiri chinkaonedwa kukhala chosakanika. Zimenezi zinalimbikitsa maganizo akuti mfumu inali yosakhoza kulakwa. Ngakhale lamulo limene likanaphetsa anthu osalakwa linayenera kutsatiridwabe!
11. Kodi lamulo limeneli linam’khudza motani Danieli?
11 Mosaganizira za Danieli, Dariyo anasaina lamulolo. (Danieli 6:9) Mwakutero, iye mosadziŵa anasainira chilolezo cha kupha nduna imene anaiŵerengera koposa. Mulimonsemo, Danieli anakhudzidwa ndi lamulo limeneli.
DARIYO AKAKAMIZIKA KUPEREKA CHIWERUZO CHOIPA
12. (a) Kodi Danieli anatani atamva za lamulo latsopanolo? (b) Kodi ndani anali kum’yang’anira Danieli, ndipo chifukwa chiyani?
12 Posakhalitsa Danieli anadziŵa za lamulo loletsa kupemphera. Nthaŵi yomweyo, analoŵa m’nyumba mwake napita m’chipinda chake chapatsindwi, mmene mazenera anali otsegula openya ku Yerusalemu.b Mmenemo Danieli anayamba kupemphera kwa Mulungu “monga umo amachitira kale lonse.” Mwina Danieli anaganiza kuti anali yekha, koma achiwembuwo anali kum’yang’anira. Mwadzidzidzi, anafika ‘nam’sonkhanira.’ Mwachionekere anafika kwa iye mwaphuma muja anachitira kwa Dariyo. Tsopano anali kudzionera ndi maso awo—Danieli anali “kupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake.” (Danieli 6:10, 11) Akuluakulu ndi akalongawo anapeza umboni wonse umene ankafuna wokam’nenezera Danieli kwa mfumu.
13. Kodi adani a Danieli anakanena chiyani kwa mfumu?
13 Adani a Danieli anafunsa Dariyo mochenjera nati: “Kodi simunatsimikiza choletsacho, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense, masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango?” Dariyo anayankha nati: “Choona chinthuchi, monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi amene sasinthika.” Atatero iye, achiwembuwo msangamsanga anafika pamfundo imene amaifunayo. “Danieli uja wa ana a ndende a Yuda sasamalira inu, mfumu, kapena choletsa munachitsimikizacho; koma apempha pemphero lake katatu tsiku limodzi.”—Danieli 6:12, 13.
14. Mwachionekere, n’chifukwa chiyani akuluakulu ndi akalongawo anatcha Danieli kuti “wa ana andende a Yuda”?
14 Akuluakulu ndi akalongawo anatchulira dala kuti Danieli anali “wa ana andende a Yuda.” Mwachionekere, iwo anafuna kugogomeza mfundo yakuti Danieli, amene Dariyo anam’kweza chotero, anali kapolo wamba wachiyuda. Choncho, anaona kuti iye sakanakhala pamwamba pa lamulo—zinalibe kanthu mfumuyo inamuona motani!
15. (a) Kodi Dariyo anamva bwanji atamva nkhani imene akuluakulu ndi akalongawo anadza nayo kwa iye? (b) Kodi akuluakulu ndi akalongawo anasonyeza motani chidani chawo pa Danieli?
15 Mwinamwake akuluakulu ndi akalongawo anayembekezera kuti mfumuyo idzawafupa kaamba ka luso lawo la ushaidi. Ngati anaganizadi zimenezo, analemba m’madzi. Dariyo anavutika mtima kwabasi ndi uthenga umene anadza nawo kwa iye. M’malo mom’kwiyira Danieli kapena kum’tumiza kudzenje la mikango nthaŵi yomweyo, Dariyo anatha tsiku lonse akuganizira za mmene akanam’pulumutsira. Koma zidam’kanika. Posapita nthaŵi, achiwembuwo anafikanso, ndipo mopanda chisoni anaumirira kuti Danieli aphedwe.—Danieli 6:14, 15.
16. (a) N’chifukwa chiyani Dariyo analemekeza Mulungu wa Danieli? (b) Kodi Dariyo anali ndi chiyembekezo chotani ponena za Danieli?
16 Dariyo anaona kuti sakanatha kuchitira mwina pankhaniyo. Lamulolo silikanasinthidwa, ndipo sakanakhululukiranso “cholakwacho” cha Danieli. Dariyo anangouza Danieli kuti, “Mulungu wako amene um’tumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.” Zikuoneka kuti Dariyo anali kulemekeza Mulungu wa Danieli. Yehova ndiye anapatsa Danieli luntha loloserera kugwa kwa Babulo. Mulungu anapatsanso Danieli “mzimu wopambana,” umene unam’pangitsa kuwaposa akuluakulu enawo. Mwinamwake Dariyo anali kudziŵa kuti zaka zambiri m’mbuyomo Mulungu mmodzimodziyu anapulumutsa anyamata atatu achihebri m’ng’anjo yamoto. Mwachionekere, mfumuyo inali ndi chiyembekezo chakuti Yehova adzapulumutsa Danieli, pakuti Dariyo sakanatha kusintha lamulo limene anasainalo. Choncho, Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango.c Kenako, “anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi chosindikizira chake, ndi chosindikizira cha akulu ake, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.”—Danieli 6:16, 17.
ZINTHU ZITEMBENUKA MODABWITSA
17, 18. (a) N’chiyani chimasonyeza kuti Dariyo anapsinjika mtima kwambiri ndi zimene zinaonekera Danieli? (b) Chinachitika n’chiyani pamene mfumuyo inabwerera kudzenje la mikango m’mawa mwake?
17 Dariyo wachisoniyo anabwerera kunyumba yake yachifumu. Oimba nyimbo sanaloŵetsedwe kwa iye, chifukwa sinali nthaŵi yoti iye n’kusangalala. Choncho Dariyo sanagone usiku wonse, anali kusala kudya. “M’maso mwake munamuumira.” Mbandakucha, Dariyo anathamangira ku dzenje la mikango kuja. Anafuula ndi mawu achisoni: “Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene um’tumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwa mikango?” (Danieli 6:18-20) Modabwa, komanso motonthozedwa mtima kwambiri, anamva kuyankha!
18 “Mfumu, mukhale ndi moyo chikhalire.” Mwa kupereka moni waulemu umenewu, Danieli anaonetsa kuti analibe maganizo achidani kwa mfumuyo. Iye anadziŵa kuti gwero lenileni la kuzunzika kwake sanali Dariyo, koma akuluakulu ndi akalonga ansanjewo. (Yerekezani ndi Mateyu 5:44; Machitidwe 7:60.) Danieli anapitiriza kuti: “Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa.”—Danieli 6:21, 22.
19. Kodi akuluakulu ndi akalongawo anam’gwira m’maso motani Dariyo, ndipo anam’nyengerera motani?
19 Mawu amenewo analasa chikumbumtima cha Dariyo! Nthaŵi yonseyo iye amadziŵa kuti Danieli sanalakwe kuti aponyedwe m’dzenje la mikango. Dariyo amadziŵanso kuti akuluakulu ndi akalongawo anapanga chiwembu kuti aphe Danieli, ndi kutinso ananyengerera mfumu kuchita chinthu chokhutiritsa cholinga chawo chadyera. Mwa kunena kuti ‘akulu onse a ufumuwo’ anali atavomereza kuti lamulolo liperekedwe, iwo anapereka chithunzi chakuti anafunsira ngakhale kwa Danieli za nkhaniyo. Dariyo anaona kuti athana nawo atambwali ameneŵa. Koma choyamba, analamula kuti Danieli atulutsidwe m’dzenje la mikango. Modabwitsa, Danieli anatuluka ali bwinobwino, ngakhale kukandidwa kokha ayi!—Danieli 6:23.
20. Kodi n’chiyani chinachitikira adani a Danieli adumbowo?
20 Danieli tsopano anali pabwino, koma Dariyo anali ndi ntchito ina yoti achite. “Italamulira mfumu, anabwera nawo amuna aja adam’neneza Danieli, nawaponya m’dzenje la mikango, iwowa, ana awo, ndi akazi awo; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa awo onse.”d—Danieli 6:24.
21. Pochita ndi apabanja la anthu olakwa, kodi panali kusiyana kotani pakati pa Chilamulo cha Mose ndi malamulo a mitundu ina ya m’nthaŵi zakale?
21 Zikuoneka kuti inali nkhanza yoipitsitsa kuphera limodzi akazi awo ndi ana awo a anthu achiwembuwo. Mosiyana ndi zimene zinachitikazo, Chilamulo chimene Mulungu anapereka kudzera mwa mneneri wake Mose chinati: “Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.” (Deuteronomo 24:16) Komabe, m’mitundu ina ya m’nthaŵi zakale, sikunali kwachilendo kunyonga wochimwayo limodzi ndi apabanja lake, ngati cholakwacho chinali chachikulu kwambiri. Mwina anachita zimenezo poopera kuti apabanjawo angadzafune kubwezera panthaŵi ina. Komabe, chenicheni n’chakuti si Danieli anachititsa kuphedwa kwa mabanja a akuluakulu ndi akalongawo. Mwachidziŵikire, iye anamva chisoni kaamba ka tsoka limene amuna oipa amenewo anadzetsa pamabanja awo.
22. Kodi Dariyo anapereka chilengezo chatsopano chotani?
22 Akuluakulu ndi akalonga achiwembu aja panalibenso. Dariyo anapereka chilengezo chimene chinati: “Ndilamulira ine kuti m’mayiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala chikhalire, ndi ufumu wake n’ngwosawonongeka, ndi kulamulira kwake kudzakhala mpaka chimaliziro. Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m’mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Danieli ku mphamvu ya mikango.”—Danieli 6:25-27.
TUMIKIRANI MULUNGU MOSALEKEZA
23. Kodi Danieli anapereka chitsanzo chotani pantchito yake yakuthupi, ndipo tingafanane naye motani?
23 Danieli anapereka chitsanzo chabwino kwa atumiki a Yehova onse amakono. Khalidwe lake nthaŵi zonse linali lopanda chifukwa. Pantchito yake yakuthupi, Danieli anali “wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.” (Danieli 6:4) Mofananamo, Mkristu ayenera kukhala wakhama pantchito yake yolembedwa. Sitikutanthauza kukhala munthu wonyanyira pofuna kulongosola ntchito, amene maganizo ake onse amangokhala pa kupindula basi, kapena munthu amene amapondereza ena kuti iye apambane. (1 Timoteo 6:10) Malemba amafuna kuti Mkristu achite ntchito yake yakuthupi moona mtima komanso ndi moyo wonse, “monga kwa Ambuye.”—Akolose 3:22, 23; Tito 2:7, 8; Ahebri 13:18.
24. Kodi Danieli anaonetsa motani kukhala wosagonja pankhani ya kulambira?
24 Pakulambira kwake, Danieli anali wosagonja. Chizoloŵezi chake cha kupemphera chinali chodziŵika kwa onse. Ndiponso, akuluakulu ndi akalonga amadziŵa kuti kulambira inali nkhani yaikulu kwa Danieli. Choncho, anali otsimikiza kuti iye akapitirizabe ndi chizoloŵezi chakecho ngakhale chitaletsedwa ndi lamulo. Chitsanzo chabwino kwabasi kwa Akristu lerolino! Iwonso amadziŵika chifukwa choika patsogolo kulambira kwawo Mulungu. (Mateyu 6:33) Zimenezi ziyenera kumaonekera kwa anthu ena, chifukwa Yesu analamula otsatira ake kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.”—Mateyu 5:16.
25, 26. (a) Kodi ena angaganize motani poona mmene Danieli anachitira? (b) N’chifukwa chiyani Danieli anaona kuti kusintha chizoloŵezi chake kukanatanthauza kugonja?
25 Ena anganene kuti Danieli akanapeŵa chizunzo chimenecho mwa kupemphera kwa Yehova mseri kwa masiku 30 amenewo. Ndi iko komwe, palibe kakhalidwe kapena malo enieni ofunikira popemphera kuti Mulungu amve. Iye amatha kuzindikira ngakhale zosinkhasinkha za mumtima. (Salmo 19:14) Komabe, Danieli anaona kuti kusintha chizoloŵezi chake kulikonse kukakhala kugonja. Chifukwa chiyani?
26 Popeza chizoloŵezi cha Danieli cha kupemphera chinali chodziŵika kwambiri, kodi zikanatanthauzanji kwa anthu iye akanasiya mwadzidzidzi? Anthu oona akanaganiza kuti Danieli anaopa munthu ndi kuti lamulo la mfumu linapambana lamulo la Yehova. (Salmo 118:6) Koma kachitidwe ka Danieli kanasonyeza kuti kulambira kwake konse kunapita kwa Yehova yekha basi. (Deuteronomo 6:14, 15; Yesaya 42:8) Koma pochita zimenezi, sikuti Danieli ananyoza lamulo la mfumu mwachipongwe ayi. Komanso, iye sanachite mantha ndi kugonja. Danieli anangopitiriza ndi chizoloŵezi chake chokapemphera m’chipinda chapatsindwi, “monga umo amachitira kale lonse,” ngakhale lamulo la mfumu lisanaperekedwe.
27. Kodi atumiki a Mulungu lerolino angafanane motani ndi Danieli (a) pomvera maulamuliro aakulu? (b) pomvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu? (c) poyesa kukhala pamtendere ndi anthu onse?
27 Atumiki a Mulungu lerolino akhoza kutengera chitsanzo cha Danieli. ‘Amamvera maulamuliro aakulu,’ ndi kusunga malamulo a dziko limene amakhala. (Aroma 13:1) Komabe, pamene malamulo a munthu awombana ndi a Mulungu, anthu a Yehova amachita mofanana ndi atumwi a Yesu, amene ananena molimba mtima kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Mwa kutero, sikuti Akristu amakhala akulimbikitsa kupanduka kapena kugalukira boma ayi. M’malo mwake, cholinga chawo chimakhala kukhala pamtendere ndi anthu onse ‘m’moyo mwawo akhale odikha mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu.’—1 Timoteo 2:1, 2; Aroma 12:18.
28. Kodi Danieli anatumikira motani Yehova “kosalekeza”?
28 Kaŵiri konse Dariyo anatchula kuti Danieli anali kutumikira Mulungu “kosalekeza.” (Danieli 6:16, 20) Liwu lachialamu limene linatembenuzidwa kuti “kosalekeza” limatanthauza “kumazungulira.” Limapereka ganizo la mzera wozungulira wosalekeza, kapena chinthu chongopitirira. Mwachionekere, ndi mmene kukhulupirika kwa Danieli kunalili. Anachita chinthu chachidziŵikire. Sizinali zokayikitsa kuti kodi Danieli angatani atati akumane ndi ziyeso, kaya zazikulu kapena zazing’ono. Iye akanapitiriza m’njira imene anali ataikhazikitsa kale zaka zambirimbiri m’mbuyomo—njira yokhala wokhulupirika kwa Yehova.
29. Kodi atumiki a Yehova lerolino angapindule motani mwa kutsatira njira yokhulupirika ya Danieli?
29 Atumiki a Mulungu a lerolino ayenera kutsatira njira ya Danieli. Ndithudi, mtumwi Paulo analangiza Akristu onse kuganizira chitsanzo cha amuna akale oopa Mulungu. Mwa chikhulupiriro, iwo “anachita chilungamo, analandira malonjezano,” ndipo ponena za Danieli, “anatseka pakamwa mikango.” Monga Atumiki a Yehova lerolino, tiyeni tisonyeze chikhulupiriro mosalekeza mofanana ndi Danieli, komanso “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.—Ahebri 11:32, 33; 12:1.
[Mawu a M’munsi]
a Zolemba zamakedzana zimapereka umboni wosonyeza kuti “dzenje la mikango” linalipodi m’Babulo, ponena kuti olamulira a Kum’maŵa nthaŵi zambiri ankakhala ndi malo osungiramo nyama zakuthengo.
b Chipinda chapatsindwi chinali chapadera mmene munthu anatha kukapuma ngati sanafune wina kum’sokoneza.
c Kukhala ngati dzenje la mikangolo linali phanga lapansi pa nthaka lokhala ndi pakamwa pamwamba pake. Mwachionekere linalinso ndi zitseko zimene zimanyamulidwa poloŵetsa nyama.
d Liwu lakuti “adam’neneza” linatembenuzidwa kuchokera ku mawu achialamu amene angatembenuzidwenso kuti “anam’dyera miseche.” Izi zikusonyeza cholinga chadumbo cha adani a Danieli.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi n’chifukwa chiyani Dariyo Mmedi anaika Danieli paudindo wapamwamba?
• Kodi akuluakulu ndi akalonga anakonza chiwembu choipitsitsa chotani? Kodi Yehova anam’pulumutsa motani Danieli?
• Kodi mwaphunziranji mwa kumvetsera chitsanzo cha kukhulupirika kwa Danieli?
[Chithunzi chachikulu patsamba 114]
[Chithunzi chachikulu patsamba 121]
[Chithunzi patsamba 127]
Danieli anatumikira Yehova “kosalekeza.” Kodi mumatero?