Mutu 10
Ufumu “Woti Sudzawonongeka ku Nthaŵi Zonse”
ZIMENE zikuchitika m’dzikoli lerolino zikutsindika mfundo yakuti anthu sanapeze chimwemwe mwa kukana ulamuliro wa Yehova ndi kuyesa kudzilamulira. Palibe boma la anthu la mtundu uliwonse limene anthu onse popanda kukondera apindula nalo. Ngakhale kuti anthu adziŵa sayansi kwambiri kuposa kale lonse, iwo alephera kugonjetsa matenda kapena kuthetsa imfa, ngakhale pa munthu mmodzi. Ulamuliro wa anthu sunathetse nkhondo, chiwawa, upandu, chinyengo, kaya umphaŵi. Maboma opondereza akulamulirabe anthu m’mayiko ambiri. (Mlaliki 8:9) Umisiri wamakono, umbombo, ndi umbuli zonse zikuipitsa malo, madzi, ndi mphweya. Akuluakulu ena amasokoneza chuma, zomwe zimachititsa anthu ambiri kuvutika kupeza zofunika pamoyo. Zaka masauzande ambiri zimene anthu alamulirana zaonetsa mosavuta mfundo iyi: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
2 Kodi yankho lake n’chiyani? Ndi Ufumu wa Mulungu, womwe Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti aziupempherera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wakumwamba wa Mulungu walongosoledwa pa 2 Petro 3:13 monga “miyamba yatsopano,” yomwe idzalamulira “dziko latsopano,” ndiko kuti anthu olungama. Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndi wofunika kwambiri moti ndiwo unali nkhani yaikulu m’maulaliki a Yesu. (Mateyu 4:17) Iye anasonyeza malo amene Ufumuwu uyenera kukhala nawo pa moyo wathu, anati: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.”—Mateyu 6:33.
3 N’kofunika kwambiri kuphunzira za Ufumu wa Mulungu lerolino, chifukwa posachedwapa Ufumu umenewu udzachitapo kanthu kuti usinthe olamulira a dzikoli mpaka kalekale. Danieli 2:44 amaneneratu kuti: “Masiku a mafumu aja [maboma amene akulamulira pakalipano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [anthu sadzalamuliranso dziko lapansi], koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipo tsopanoli]. Nudzakhala chikhalire.” Motero Ufumuwo udzathetsa masiku otsiriza ano mwa kuwononga dziko lonse loipali. Ndiyeno Ufumu wakumwambawo udzakhala wokhawo womwe udzalamulire dziko lapansi. Tiyeneratu kuthokoza kwambiri kuti mpumulo umene udzabwera ndi zimenezi uli pafupi kwambiri tsopano!
4 M’chaka cha 1914, Kristu Yesu anaikidwa pa mpando monga Mfumu ndipo analamulidwa kuti ‘achite ufumu pakati pa adani ake.’ (Salmo 110:1, 2) Ndiponso m’chaka chimenecho, “masiku otsiriza” a dziko loipa lilipoli anayamba. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Panthaŵi imodzimodziyo, zochitika zimene Danieli anaona m’masomphenya aulosi zinachitikadi kumwamba. “Nkhalamba ya kale lomwe,” Yehova Mulungu, inapatsa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” Ponena za masomphenya amenewo, Danieli anati: “Ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.” (Danieli 7:13, 14) Mwa kugwiritsa ntchito Ufumu wakumwamba umenewu wolamuliridwa ndi Kristu Yesu, Mulungu adzachititsa anthu okonda chilungamo kukhala ndi zinthu zabwino zambirimbiri zimene iye anafuna kuti anthu akhale nazo pamene anaika makolo athu oyambirira m’Paradaiso.
5 Kodi mukufuna kukhala nzika yokhulupirika pamene Ufumuwo ukulamulira? Ngati n’choncho, mungakonde kudziŵa olamulira a boma lakumwamba limeneli ndiponso mmene likugwirira ntchito. Mungakonde kudziŵa zimene likuchita pakalipano, zimene lidzachita m’tsogolo, ndiponso zimene limafuna kuti inuyo muchite. Pamene muphunzira za Ufumuwu mosamalitsa, mudzauyamikira kwambiri. Ngati mulabadira ulamuliro wake, mudzakhala wokonzeka bwino kuuza ena zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzachitira anthu omvera.—Salmo 48:12, 13.
Olamulira a Ufumu wa Mulungu
6 Chimodzi mwa zinthu zoyambirira zimene mudzaona pamene mukuphunzira za Ufumuwu ndi chakuti mwa Ufumu Waumesiya, Yehova mwiniyo amaonetsa ulamuliro wake. Yehova ndiye anapatsa Mwana wake “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu.” Mwana wa Mulungu atapatsidwa mphamvu kuti ayambe kulamulira monga Mfumu, mawu omveka kumwamba analengeza moyenerera kuti: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova Mulungu], ndi wa Kristu wake: ndipo [iye Yehova] adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” (Chivumbulutso 11:15) Motero chilichonse chimene timaona chokhudza Ufumuwu ndiponso zimene umachita zingatipangitse kuyandikira kwambiri Yehova mwiniyo. Zimene timaphunzira ziyenera kutichititsa kukhala ndi chikhumbo chogonjera ulamuliro wake mpaka kalekale.
7 Lingaliraninso mfundo yakuti Yehova waika Yesu Kristu pa mpando wachifumu kuti akhale Wolamulira Wachiŵiri kwa iye. Popeza Yesu anali Mmisiri amene Mulungu anamugwiritsa ntchito popanga dziko lapansi ndi anthu, iye amadziŵa bwino kwambiri zinthu zimene timafunika kuposa mmene amadziŵira wina aliyense wa ife. Ndiponso, kuchokera poyambira penipeni pa mbiri ya anthu, iye anasonyeza kuti ‘amakondwera ndi ana a anthu.’ (Miyambo 8:30, 31; Akolose 1:15-17) Anthu amawakonda kwambiri moti anabwera yekha padziko lapansi ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo lotiwombolera. (Yohane 3:16) Motero iye anatikonzera njira yoti tithe kumasuka ku uchimo ndi imfa ndiponso kuti tikhale ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha.—Mateyu 20:28.
8 Ufumu wa Mulungu ndi boma lokhazikika bwino ndi lokhalitsa. Kukhalitsa kwa bomali n’kotsimikizika chifukwa Yehova mwiniyo safa. (Salmo 146:3-5, 10) Mosiyana ndi anthu amene amakhala mafumu, Yesu Kristu, yemwe Mulungu wamupatsa ufumu, nayenso sangafe. (Aroma 6:9; 1 Timoteo 6:15, 16) Kristu adzakhala pa mpando wachifumu kumwamba limodzi ndi atumiki enanso okhulupirika a Mulungu okwana 144,000 ochokera mu “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” Iwoŵanso akupatsidwa moyo wosakhoza kufa. (Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4; 1 Akorinto 15:42-44, 53) Ambiri mwa iwo ali kale kumwamba, ndipo otsala amene adakali padziko lapansi ndiwo amene ali “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wa masiku ano, kapolo amene akuyendetsa mokhulupirika zinthu zokhudza Ufumuwo padziko lapansi pano.—Mateyu 24:45-47.
9 Posachedwa pompa, panthaŵi yake ya Yehova, adzatumiza magulu ake akupha kuti agwire ntchito yoyeretsa dziko lapansi. Adzawonongeratu anthu amene mwa kusankha kwawo safuna kuvomereza ulamuliro wake ndipo amanyoza zimene iye mwachikondi amakonza kudzera mwa Yesu Kristu. (2 Atesalonika 1:6-9) Limenelo lidzakhala tsiku la Yehova, nthaŵi yomwe yayembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali kuti atsimikizidwe kuti iye ndiye Wolamulira Wamkulu wa Chilengedwe Chonse. “Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali . . . kudzawonongamo akuchimwa psiti.” (Yesaya 13:9) “Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la masauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii.”—Zefaniya 1:15.
10 Zipembedzo zonse zonyenga ndi maboma onse a anthu limodzi ndi magulu awo ankhondo, omwe asonkhezeredwa ndi wolamulira woipa wosaoneka wa dzikoli, adzawonongekeratu. Onse amene amagwirizana ndi dzikoli mwa kukhala ndi moyo wodzikonda, wachinyengo, komanso wotayirira adzawonongedwa. Satana ndi ziwanda zake adzachotsedwa kuti asakumanenso ndi anthu okhala padziko lapansi, adzatsekeredwa kwaokhaokha kwa zaka 1,000. Panthaŵiyo Ufumu wa Mulungu udzakhala wokhawo wolamulira chilichonse padziko lapansi. Umenewu udzakhalatu mpumulo waukulu zedi kwa onse amene amakonda chilungamo!—Chivumbulutso 18:21, 24; 19:11-16, 19-21; 20:1, 2.
Zolinga za Ufumuwo ndi Mmene Zikukwaniritsidwira
11 Ufumu Waumesiya udzakwaniritsa cholinga chonse choyambirira cha Mulungu chokhudza dziko lapansi. (Genesis 1:28; 2:8, 9, 15) Kufikira lerolino, anthu alephera kuthandiza kuti cholinga chimenecho chikwaniritsidwe. Komabe, “dziko lilinkudza” lidzagonjetsedwa kwa Mwana wa munthu, Yesu Kristu. Onse amene adzapulumuka pamene Yehova aweruza dziko lakale lino adzagwira ntchito limodzi mogwirizana motsogoleredwa ndi Kristu Mfumuyo. Iwo mosangalala adzachita zonse zimene iye adzawalamula, kotero kuti dziko lapansi lonse lidzakhala paradaiso. (Ahebri 2:5-9) Anthu onse adzasangalala ndi ntchito ya manja awo ndipo adzapindula kwambiri ndi zinthu zochuluka zimene dziko lapansi lidzapereka.—Salmo 72:1, 7, 8, 16-19; Yesaya 65:21, 22.
12 Adamu ndi Hava anali angwiro pamene analengedwa, ndipo cholinga cha Mulungu chinali chakuti ana awo adzaze m’dziko lapansi; ana onsewo anali oti akhale angwiro m’maganizo ndi m’thupi momwe. Cholinga chimenecho chidzakwaniritsidwa bwino pamene Ufumu ukulamulira. Kuti zitheke, zonse zimene uchimo unabweretsa zifunika kuchotsedwa, ndipo pachifukwa chimenechi Kristu sali kokha Mfumu, komanso ndi Mkulu wa Ansembe. Moleza mtima, adzathandiza anthu ake omvera kuti apindule ndi nsembe ya moyo wake waumunthu yomwe ili ndi mphamvu yotetezera machimo.
13 Pamene Ufumu ukulamulira, anthu okhala padziko lapansi adzapinduladi kwambiri. “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.” (Yesaya 35:5, 6) Khungu lokwinyika ndi ukalamba kapena matenda lidzakhala losalala kuposa la mwana, ndipo kukhala wofooka nthaŵi zonse kudzaloŵedwa m’malo ndi kukhala n’thanzi labwino zedi. “Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.” (Yobu 33:25) Lidzafika tsiku pamene palibe munthu adzakhala ndi chifukwa chonenera kuti, “Ine ndidwala.” Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti uchimo limodzi ndi zotsatira zake zomvetsa chisoni zidzachotsedwa pa anthu oopa Mulungu. (Yesaya 33:24; Luka 13:11-13) Inde, Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
14 Komabe, kukhala anthu angwiro kumaphatikizapo zambiri kuposa kukhala ndi matupi abwino ndi maganizo abwino. Kumaphatikizapo kuti anthuwo azionetsa makhalidwe a Yehova moyenerera, popeza kuti tinapangidwa ‘m’chifanizo cha Mulungu, monga mwa chikhalidwe chake.’ (Genesis 1:26) Kuti zimenezi zitheke padzafunika kuphunzira zambiri. M’dziko latsopano, ‘mudzakhalitsa chilungamo.’ Choncho monga ananeneratu Yesaya, “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (2 Petro 3:13; Yesaya 26:9) Kukhala achilungamo kumabweretsa mtendere, mtendere pakati pa anthu a mafuko onse, pakati pa anthu okondana, m’banja, ndipo chofunika kwambiri, mtendere ndi Mulungu mwiniyo. (Salmo 85:10-13; Yesaya 32:17) Amene adzadziŵa chilungamo adzaphunzitsidwa pang’onopang’ono chifuniro cha Mulungu pa iwo. Akadzayamba kukonda kwambiri Yehova m’mitima yawo, adzatsatira njira zake m’mbali iliyonse ya moyo wawo. Iwo adzatha kunena monga ananenera Yesu kuti, ‘ndichita Ine zimene zimakondweretsa Atate wanga nthaŵi zonse.’ (Yohane 8:29) Moyo udzakhalatu wosangalatsa kwambiri pamene zinthu zidzakhala choncho kwa anthu onse!
Zimene Wakwaniritsa Kale
15 Zinthu zochititsa kaso zimene Ufumu wa Mulungu ndi anthu olamuliridwa ndi Ufumuwo akwaniritsa kale zikuoneka. Mafunso ndi malemba otsatiraŵa akukumbutsani zina mwa zinthu zimenezi, limodzinso ndi zinthu zimene onse olamuliridwa ndi Ufumuwo angathe kuchita ndipo akuyenera kumazichita kumene tsopano lino.
Kodi Ufumu unalimbana ndi ndani choyamba, nanga zotsatira zake zinali zotani? (Chivumbulutso 12:7-10, 12)
Kodi ndi kusonkhanitsidwa kwa anthu otsala a gulu liti kumene kwakhala kukuchitika kuchokera pamene Kristu anaikidwa pa mpando wachifumu? (Chivumbulutso 14:1-3)
Kodi ndi ntchito yotani imene Yesu ananeneratu kuti adzagwira chisautso chachikulu chitayamba, monga kwalembedwa pa Mateyu 25:31-33?
Kodi ndi ntchito yoyambirira iti imene ikuchitika lerolino? Kodi ndani akugwira ntchitoyi? (Salmo 110:3; Mateyu 24:14; Chivumbulutso 14:6, 7)
N’chifukwa chiyani anthu andale ndi achipembedzo amene amatsutsa ntchito yolalikira alephera kuletsa ntchitoyi? (Zekariya 4:6; Machitidwe 5:38, 39)
Kodi miyoyo ya amene amagonjera ku ulamuliro wa Ufumu yasintha motani? (Yesaya 2:4; 1 Akorinto 6:9-11)
Ufumu wa Zaka 1,000
16 Satana ndi ziwanda zake atakaponyedwa ku phompho, Yesu Kristu ndi olowa ufumu anzake 144,000 adzalamulira monga mafumu ndi ansembe kwa zaka 1,000. (Chivumbulutso 20:6) Panthaŵi imeneyo, anthu adzakhala angwiro, chifukwa chakuti uchimo ndi imfa yobwera ndi Adamu zidzakhala zitachotsedweratu. Pakutha kwa Ulamuliro wa Zaka 1,000, pomwe Yesu adzakhala atagwira ntchito yake bwino monga Mfumu ndiponso Wansembe Waumesiya, iye “adzapereka ufumu” kwa Atate wake, “kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:24-28) Panthaŵi imeneyo, Satana adzamasulidwa kwa kanthaŵi kochepa kuti anthu owomboledwa akawayese ngati akuchirikizadi ulamuliro wa Yehova pa chilengedwe chonse. Mayeso omaliza amenewo akadzatha, Yehova adzawononga Satana pamodzi ndi onse amene anapanduka naye limodzi. (Chivumbulutso 20:7-10) Amene adzachirikiza ulamuliro wa Yehova, kapena kuti ufulu wake wolamulira, adzakhala atasonyeza bwino lomwe kuti ndi okhulupirika kwambiri. Ndiyeno adzawalola kukhala ndi ubale wawo woyenerera ndi Yehova. Yehova adzawalandira monga ana ake aamuna ndi aakazi, ndipo adzawavomereza kuti akhale ndi moyo wosatha.—Aroma 8:21.
17 Motero, ntchito ya Yesu ndiponso ya a 144,000 yokhudzana ndi dziko lapansi idzasintha. Kodi iwo adzagwira ntchito yanji m’tsogolo? Baibulo silinena. Koma ngati mokhulupirika tiima kumbali ya ulamuliro wa Yehova, tidzakhala tili ndi moyo pamapeto a Ulamuliro wa Zaka 1,000 ndipo tidzaona zimene Yehova wawakonzera limodzi ndi chilengedwe chake chodabwitsa chonsechi. Komabe, ulamuliro wa Kristu wa zaka 1,000 udzakhala “ulamuliro wosatha” ndipo Ufumu wake “sudzawonongeka.” (Danieli 7:14) M’lingaliro lotani? Mwa zina, ulamuliro sudzatengedwa ndi anthu ena amene adzakhala ndi maganizo osiyana, chifukwa Yehova ndiye adzakhala Wolamulira. Ndiponso, Ufumuwo “sudzawonongeka ku nthaŵi zonse” chifukwa zinthu zimene udzachita sizidzatha. (Danieli 2:44) Ndipo Mfumu komanso Wansembe Waumesiya limodzi ndi mafumu ndi ansembe anzake adzalemekezedwa mpaka kalekale chifukwa chotumikira Yehova mokhulupirika.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu ndiwo njira yokhayo yothetsera mavuto a anthu? Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu inayamba liti kulamulira?
• Kodi n’chiyani chokhudza Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzachita chomwe inuyo chimakusangalatsani kwambiri?
• Kodi ndi zinthu ziti zimene Ufumu wachita zomwe tikuziona pakalipano, nanga ifeyo tili ndi mbali yotani pa zimenezi?
[Mafunso]
1. Kodi m’mbiri yonse ya anthu zochitika za m’dzikoli zatsindika mfundo yotani?
2. Kodi njira yokha imene mavuto a anthu angathere ndi iti?
3. N’chifukwa chiyani kuphunzira za Ufumu wa Mulungu n’kofunika kwambiri tsopanoli?
4. Pa nkhani ya Ufumu, kodi n’chiyani chinachitika kumwamba mu 1914, nanga n’chifukwa chiyani zimenezo n’zofunika kwa ife?
5. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza Ufumu zimene tili nazo n’chidwi, ndipo n’chifukwa chiyani?
6. (a) Kodi Malemba amasonyeza motani kuti ndi ulamuliro wa yani umene umasonyezedwa mwa Ufumu Waumesiya? (b) Kodi zimene timaphunzira za Ufumu ziyenera kutikhudza motani?
7. N’chifukwa chiyani timachita chidwi mwapadera kuti Yesu Kristu ndi Wolamulira Wachiŵiri kwa Yehova?
8. (a) Mosiyana ndi maulamuliro a anthu, n’chifukwa chiyani boma la Mulungu lidzakhalitsa? (b) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi boma la kumwamba?
9, 10. (a) Kodi Ufumu udzachotsa zinthu zogaŵanitsa ndi zosokoneza anthu ziti? (b) Ngati sitifuna kukhala adani a Ufumu wa Mulungu, kodi tiyenera kupewa kulowerera m’zochitika zotani?
11. (a) Kodi Ufumu Waumesiya udzakwaniritsa motani cholinga cha Yehova cha dziko lapansi? (b) Chifukwa chakuti Ufumuwo ukulamulira, kodi n’chiyani chidzachitika kwa anthu okhala padziko lapansi panthaŵiyo?
12. Kodi anthu olamuliridwa ndi Ufumuwo adzakhala motani angwiro m’maganizo ndi m’thupi?
13. Kodi anthu adzapindula motani pamene Ufumu ukulamulira?
14. Kodi kukhala anthu angwiro kumaphatikizapo chiyani?
15. Pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’ndime ino, tchulani zimene Ufumu wakwaniritsa ndipo sonyezani zimene tiyenera kumachita pakali pano.
16. (a) Kodi Kristu adzalamulira kwa zaka zingati? (b) Kodi ndi zinthu zochititsa kaso zotani zimene zidzachitika m’kati mwa nthaŵi imeneyo ndiponso pambuyo pake?
17. (a) Kodi n’chiyani chidzachitikira Ufumu pamapeto a zaka 1,000? (b) Kodi ndi zoona m’lingaliro lotani kuti Ufumuwo “sudzawonongeka ku nthaŵi zonse”?
[Chithunzi pamasamba 92, 93]
Pamene Ufumu wa Mulungu ulamulira, anthu onse adzaphunzira chilungamo