Madalitso Aakulu Kudzera m’Pangano Latsopano
“Iye [“Yesu,” NW] . . . umonso ali Nkhoswe ya pangano labwino loposa.”—AHEBRI 8:6.
1. Kodi ndani anakhala ‘mbewu ya mkazi’ yolonjezedwa mu Edene, ndipo kodi ndi motani mmene ‘analalidwira chitende chake’?
ADAMU ndi Hava atachimwa, Yehova anapereka chiweruzo kwa Satana, amene ananyenga Hava, nati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Mbewu imene inalonjezedwa mu Edene inaonekera pomalizira pake pamene Yesu anabatizidwa mu Mtsinje wa Yordano mu 29 C.E. Paimfa yake pamtengo wozunzirapo mu 33 C.E., mbali ina ya ulosi umenewo inakwaniritsidwa. Satana ‘analalira chitende’ cha Mbewuyo.
2. Malinga ndi mawu a Yesu iyemwini, kodi imfa yake ikupindulitsa motani mtundu wa anthu?
2 Chosangalatsa nchakuti bala limenelo, ngakhale kuti linali lopweteka zedi, silinali lokhalitsa. Yesu anaukitsidwa kwa akufa kukhala mzimu wosakhoza kufa ndipo anakwera kwa Atate wake kumwamba, kumene anapereka mtengo wa mwazi wake wokhetsedwa monga “dipo la anthu ambiri.” Chotero, mawu ake awa anakwaniritsidwa: “Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa; kuti yense wakukhulupira akhale nawo moyo wosatha mwa Iye. Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Mateyu 20:28; Yohane 3:14-16; Ahebri 9:12-14) Pangano latsopano lili lofunika kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu.
Pangano Latsopano
3. Kodi pangano latsopano linaoneka liti kwa nthaŵi yoyamba kuti layamba kugwira ntchito?
3 Imfa yake itayandikira, Yesu anauza otsatira ake kuti mwazi wake wokhetsedwa ndiwo unali “mwazi . . . wa pangano [latsopano].” (Mateyu 26:28; Luka 22:20) Patapita masiku khumi iye atakwera kumwamba, pangano latsopano linaoneka kuti layamba kugwira ntchito pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa ophunzira ngati 120 amene anasonkhana m’chipinda china chapamwamba ku Yerusalemu. (Machitidwe 1:15; 2:1-4) Kuloŵetsa ophunzira 120 ameneŵa m’pangano latsopano kunasonyeza kuti tsopano pangano “loyambali,” pangano la Chilamulo, latha ntchito.—Ahebri 8:13.
4. Kodi pangano lakale linalephereka? Fotokozani.
4 Kodi pangano lakale linalephereka? Kutalitali. Nzoona kuti popeza tsopano linaloŵedwa m’malo ndi pangano lina, Aisrayeli akuthupi sanalinso anthu apadera a Mulungu. (Mateyu 23:38) Koma zimenezo zinachitika chifukwa chakuti Aisrayeli anali osamvera ndipo anakana Wodzozedwa wa Yehova. (Eksodo 19:5; Machitidwe 2:22, 23) Komabe, Chilamulo chinachita zambiri chisanachotsedwe. Kwa zaka mazana ambiri, chinali njira yolambirira Mulungu ndiponso chinawatetezera ku chipembedzo chonyenga. Chinali ndi zinthu zina zimene zinachitira chithunzi pangano latsopano ndipo, mwa nsembe zake zobwerezabwereza, chinasonyeza kuti munthu akufunadi kuomboledwa mwamsanga kuchokera ku uchimo ndi imfa. Ndithudi, Chilamulo chinali ‘namkungwi wakuwafikitsa kwa Kristu.’ (Agalatiya 3:19, 24; Aroma 3:20; 4:15; 5:12; Ahebri 10:1, 2) Komabe, dalitso lonse lolonjezedwa kwa Abrahamu linali kudzakwaniritsidwa m’pangano latsopanoli.
Mitundu Idalitsidwa Kudzera m’Mbewu ya Abrahamu
5, 6. Pakukwaniritsidwa koyamba kwauzimu kwa pangano la Abrahamu, kodi Mbewu ya Abrahamu ndani, ndipo ndi mtundu uti umene unali woyamba kulandira dalitso kudzera mwa iyeyo?
5 Yehova analonjeza Abrahamu kuti: “M’mbewu yako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadzidalitsa.” (Genesis 22:18, NW) M’pangano lakale, alendo ambiri ofatsa anadalitsidwa mwa kuyanjana kwawo ndi Israyeli, mtundu umene unali mbewu ya Abrahamu. Komabe, m’kukwaniritsidwa kwake kwenikweni kwauzimu, Mbewu ya Abrahamu inali munthu mmodzi wangwiro. Paulo anafotokoza zimenezi pamene anati: “Malonjezano ananenedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Sanena, Ndipo kwa zimbewu, ngati kunena zambiri; komatu ngati kunena imodzi, Ndipo kwa mbewu yako, ndiye Kristu.”—Agalatiya 3:16.
6 Inde, Yesu ndiye Mbewu ya Abrahamu, ndipo kudzera mwa Iye mitundu ikulandira dalitso lalikulu kwambiri kuposa lililonse limene Israyeli wakuthupi akanapereka. Inde, mtundu woyamba kulandira dalitso limeneli unali mtundu wa Israyeli womwewo. Pentekoste wa 33 C.E. atangopita, mtumwi Petro anati kwa gulu lina la Ayuda: “Inu ndinu ana a aneneri, ndi a panganolo Mulungu anapangana ndi makolo anu ndi kunena kwa Abrahamu, Ndipo mu mbewu yako mafuko onse a dziko adzadalitsidwa. Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.”—Machitidwe 3:25, 26.
7. Kodi ndi mitundu iti imene inadalitsidwa kudzera mwa Yesu, Mbewu ya Abrahamu?
7 Posapita nthaŵi dalitsolo linafikanso kwa Asamariya kenako kwa Akunja. (Machitidwe 8:14-17; 10:34-48) Chapakati pa 50 ndi 52 C.E., Paulo analembera Akristu a ku Galatiya ku Asia Minor kuti: “Malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse. Kotero kuti iwo a chikhulupiriro adalitsidwa pamodzi ndi Abrahamu wokhulupirikayo.” (Agalatiya 3:8, 9; Genesis 12:3) Ngakhale kuti Akristu ambiri ku Galatiya anali “amitundu,” iwo anadalitsidwa mwa Yesu chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Motani?
8. Kwa Akristu a m’tsiku la Paulo, kudalitsidwa kudzera m’Mbewu ya Abrahamu kunaphatikizapo chiyani, ndipo pomalizira pake ndi angati amene akulandira nawo dalitso limeneli?
8 Paulo anauza Akristu a ku Galatiya, amtundu uliwonse kuti: “Ngati muli a Kristu, muli mbewu ya Abrahamu, nyumba monga mwa lonjezano.” (Agalatiya 3:29) Kwa Agalatiya amenewo, dalitso lodzera m’Mbewu ya Abrahamu linaphatikizapo kutengamo mbali kwawo m’pangano latsopano ndiponso kukhala oloŵa nyumba anzake a Yesu, anzake a Yesu m’mbewu ya Abrahamu. Sitikudziŵa kuti Aisrayeli akale anali angati. Timangodziŵa kuti anadzakhala “ngati mchenga wa kunyanja.” (1 Mafumu 4:20) Komabe, tikudziŵa chiŵerengero chonse cha anzake a Yesu m’mbewu yauzimu—144,000. (Chivumbulutso 7:4; 14:1) Anthu 144,000 amenewo amachokera mu “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse” ya anthu ndipo nawonso akupereka kwa enanso madalitso a pangano la Abrahamu.—Chivumbulutso 5:9.
Ulosi Ukwaniritsidwa
9. Kodi amene ali m’pangano latsopano ali motani ndi malamulo a Yehova mkati mwawo?
9 Poneneratu za pangano latsopano, Yeremiya analemba kuti: “Ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba.” (Yeremiya 31:33) A m’pangano latsopano amatumikira Yehova chifukwa chakuti amamkonda. (Yohane 13:35; Ahebri 1:9) Chilamulo cha Yehova chinalembedwa m’mitima yawo, ndipo iwo amafunitsitsa kuchita chifuniro chake. Zoona, anthu ena okhulupirika m’Israyeli wakale anakondadi chilamulo cha Yehova. (Salmo 119:97) Koma ambiri sanachikonde. Ngakhale zili choncho, iwo anakhalabe mbali ya mtunduwo. Kulibe amene angakhalebe m’pangano latsopano ngati chilamulo cha Mulungu sicholembedwa mumtima mwake.
10, 11. Kwa amene ali m’pangano latsopano, kodi Yehova ‘akukhala Mulungu wawo’ motani, ndipo kodi onsewo adzamdziŵa motani?
10 Yehova anapitiriza kunena za awo a m’pangano latsopano kuti: “Ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga.” (Yeremiya 31:33) M’Israyeli wakale ambiri anali kulambira milungu ya mitundu ina, koma iwo anakhalabe Aisrayeli. Pamaziko a pangano latsopano, Yehova anapanga mtundu wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” kuti uloŵe m’malo mwa Israyeli wakuthupi. (Agalatiya 6:16; Mateyu 21:43; Aroma 9:6-8) Komabe, kulibe amene amakhalabe mumtundu watsopano umenewu wauzimu ngati asiya kulambira Yehova yekha.
11 Yehova ananenanso kuti: “Iwo onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo.” (Yeremiya 31:34) Ku Israyeli, ambiri anangomnyalanyaza Yehova, namati: “Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.” (Zefaniya 1:12) Kulibe amene angakhalebe m’Israyeli wa Mulungu ngati anyalanyaza Yehova kapena ngati aipsa kulambira koyera. (Mateyu 6:24; Akolose 3:5) Aisrayeli auzimu ndiwo “anthu akudziŵa Mulungu wawo.” (Danieli 11:32) Iwo amasangalala ‘kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu yekha woona, ndi cha Yesu Kristu.’ (Yohane 17:3, NW) Kudziŵa Yesu kumakulitsa chidziŵitso chawo chonena za Mulungu popeza kuti, m’njira yapadera kwambiri, Yesu “ndiye wamfotokoza [Mulungu].”—Yohane 1:18, NW; 14:9-11.
12, 13. (a) Kodi Yehova amakhululukira machimo a amene ali m’pangano latsopano pamaziko otani? (b) Ponena za kukhululukira machimo, kodi pangano latsopano liposa motani pangano lakale?
12 Pomalizira pake, Yehova analonjeza kuti: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.” (Yeremiya 31:34c) Chilamulo cha Mose chinali ndi malamulo mazana ambiri olembedwa amene Aisrayeli anauzidwa kuti aziwamvera. (Deuteronomo 28:1, 2, 15) Onse amene anaswa Chilamulo anali kupereka nsembe yophimba machimo awo. (Levitiko 4:1-7; 16:1-31) Ayuda ambiri anayamba kukhulupirira kuti atha kukhala olungama mwa ntchito zawo za m’Chilamulo. Komabe, Akristu amadziŵa kuti iwo sangapate chilungamo mwa ntchito zawo. Angathe kuchimwa. (Aroma 5:12) M’pangano latsopano, kukhala wolungama pamaso pa Mulungu nkotheka pamaziko a nsembe ya Yesu basi. Komabe, kukhala wotero ndi mphatso, chisomo cha Mulungu. (Aroma 3:20, 23, 24) Yehova amafunabe kuti atumiki ake azimumvera. Paulo akunena kuti awo amene ali m’pangano latsopano ali “omvera lamulo kwa Kristu.”—1 Akorinto 9:21.
13 Choncho, Akristu nawonso ali ndi nsembe ya uchimo, koma yamtengo waukulu kwambiri kuposa nsembe za m’pangano la Chilamulo. Paulo analemba kuti: “Wansembe aliyense [wotsatira pangano la Chilamulo] amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kaŵirikaŵiri, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo; koma Iye [Yesu], mmene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire.” (Ahebri 10:11, 12) Popeza kuti Akristu a m’pangano latsopano amakhulupirira nsembe ya Yesu, Yehova amawaona kukhala olungama, opanda tchimo, chotero oyenerera kudzozedwa monga ana ake auzimu. (Aroma 5:1; 8:33, 34; Ahebri 10:14-18) Akachimwa chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu, iwo angapemphe chikhululukiro kwa Yehova, ndipo pamaziko a nsembe ya Yesu, Yehova amawakhululukira. (1 Yohane 2:1, 2) Komabe, ngati angochimwa dala, iwo samakhalanso olungama ndipo samakhalanso ndi mbali m’pangano latsopano.—Ahebri 2:2, 3; 6:4-8; 10:26-31.
Pangano Lakale Ndiponso Latsopano
14. Kodi ndi mdulidwe wotani umene unali kufunika m’pangano la Chilamulo? m’pangano latsopano?
14 M’pangano lakale, amuna anali kudulidwa monga chizindikiro chakuti akutsatira Chilamulo. (Levitiko 12:2, 3; Agalatiya 5:3) Mpingo wachikristu utayambika, ena ankalingalira kuti Akristu osakhala Ayuda nawonso ayenera kuchita mdulidwe. Koma atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, motsogozedwa ndi Mawu a Mulungu ndi mzimu woyera, anazindikira kuti zimenezo zinali zosafunikira. (Machitidwe 15:1, 5, 28, 29) Patapita zaka zingapo, Paulo anati: “Siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m’malembo ayi.” (Aroma 2:28, 29) Mdulidwe weniweni, ngakhale kwa Ayuda akuthupi, sunalinso wofunika mwauzimu pamaso pa Yehova. Kwa awo amene ali m’pangano latsopano, mtima ndiwo uyenera kuchitidwa mdulidwe, osati thupi. Maganizo awo alionse, zikhumbo, ndi zisonkhezero zosakondweretsa Yehova kapena zodetsedwa pamaso pake ayenera kuzidula ndi kuzitaya.a Anthu ambiri lerolino ali umboni weniweni wa mphamvu ya mzimu woyera yosanduliza maganizo m’njira imeneyi.—1 Akorinto 6:9-11; Agalatiya 5:22-24; Aefeso 4:22-24.
15. Kodi Israyeli wakuthupi akufanana motani ndi Israyeli wa Mulungu pa ulamuliro wachifumu?
15 M’makonzedwe a pangano la Chilamulo, Yehova ndiye anali Mfumu ya Israyeli, ndipo m’kupita kwa nthaŵi anachita uchifumu wake kudzera mwa mafumu aumunthu ku Yerusalemu. (Yesaya 33:22) Yehova alinso Mfumu ya Israyeli wa Mulungu, Israyeli wauzimu, ndipo chiyambire 33 C.E., iye wakhala akulamulira kudzera mwa Yesu Kristu, amene analandira “mphamvu zonse . . . Kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18; Aefeso 1:19-23; Akolose 1:13, 14) Lerolino, Israyeli wa Mulungu amaona Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, umene unakhazikitsidwa mu 1914. Yesu ali Mfumu yabwino kwambiri kuposa mmene Hezekiya, Yosiya, ndi mafumu ena okhulupirika a m’Israyeli wakale analili.—Ahebri 1:8, 9; Chivumbulutso 11:15.
16. Kodi Israyeli wa Mulungu ndi wansembe wotani?
16 Israyeli sanali chabe ufumu komanso anali ndi ansembe odzozedwa. Mu 33 C.E., Israyeli wa Mulungu analoŵa m’malo mwa Israyeli wakuthupi nakhala “mtumiki” wa Yehova, “mboni” zake. (Yesaya 43:10) Kuyambira pamenepo, mawu a Yehova kwa Israyeli olembedwa pa Yesaya 43:21 ndi pa Eksodo 19:5, 6 anayamba kunena za Israyeli wauzimu wa Mulungu. Mtundu watsopano wauzimu wa Mulungu tsopano unakhala “mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake,” oyenera ‘kulalikira zoposazo za Yehova.’ (1 Petro 2:9) Onse pamodzi, amuna ndi akazi a Israyeli wa Mulungu, amapanga wansembe. (Agalatiya 3:28, 29) Monga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu, iwo tsopano amanena kuti: “Kondwerani, amitundu inu, ndi anthu ake.” (Deuteronomo 32:43) Awo a Israyeli wauzimu amene adakali padziko lapansi amapanga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Utumiki wopatulika wovomerezeka kwa Mulungu ungaperekedwe kokha mwa kuyanjana ndi ameneŵa.
Ufumu wa Mulungu—Kukwaniritsidwa Komaliza
17. Kodi ndi kubadwa kotani kumene a m’pangano latsopano amabadwa?
17 Aisrayeli amene anabadwa chaka cha 1513 B.C.E. chitapita analoŵa m’pangano la Chilamulo atangobadwa. Amene Yehova amaloŵetsa m’pangano latsopano nawonso amaloŵamo mwa kubadwa—koma iwo amabadwa mwauzimu. Yesu anatchula zimenezi kwa Mfarisi wotchedwa Nikodemo pamene anati: “Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona Ufumu wa Mulungu.” (Yohane 3:3) Ophunzira 120 amene analipo pa Pentekoste wa 33 C.E. ndiwo anali anthu opanda ungwiro oyamba kubadwa mwatsopano. Poyesedwa olungama m’pangano latsopano, analandira mzimu woyera monga “chikole” cha choloŵa chawo chaufumu. (Aefeso 1:14) Iwo ‘anabadwa mwa Mzimu,’ kukhala ana otengedwa a Mulungu, zimene zinawapangitsa kukhala abale a Yesu ndi kukhalanso “oloŵa anzake a Kristu.” (Yohane 3:6; Aroma 8:16, 17) “Kubadwa mwatsopano” kwawo kunatsegula njira ya ziyembekezo zosangalatsa kwambiri.
18. Kodi kubadwanso kumatsegulira a m’pangano latsopano mwaŵi wotani wa ziyembekezo zosangalatsa kwambiri?
18 Pochitira unkhoswe pangano latsopano, Yesu anapanganso pangano lina ndi otsatira ake, nati: “Ine ndipanga pangano ndi inu, monganso Atate anga anapanga pangano la ufumu ndi ine.” (Luka 22:29, NW) Pangano la Ufumu limeneli linalambula njira ya kukwaniritsidwa kwa masomphenya ochititsa chidwi, olembedwa pa Danieli 7:13, 14, 22, 27. Danieli anaona “wina ngati mwana wa munthu” akupatsidwa mphamvu za ufumu ndi “Nkhalamba yakale lomwe,” Yehova Mulungu. Kenako Danieli anaona kuti “ufumu unali wawo wa opatulikawo.” Yesu ndiye amene ali “ngati mwana wa munthu” amene, mu 1914, analandira Ufumu wakumwamba kuchokera kwa Yehova Mulungu. Ophunzira ake odzozedwa ndi mzimu ndiwo “opatulikawo” amene akugwirizana naye mu Ufumuwo. (1 Atesalonika 2:12) Motani?
19, 20. (a) Kodi lonjezo la Yehova kwa Abrahamu lidzakhala ndi kukwaniritsidwa komaliza ndiponso kwaulemerero kotani kwa a m’pangano latsopano? (b) Kodi ndi funso linanso liti limene tiyenera kukambitsirana?
19 Monga anachitira Yesu, odzozedwa ameneŵa atamwalira amaukitsidwa kwa akufa ali zolengedwa zauzimu zosakhoza kufa kuti akatumikire naye kumwamba monga mafumu ndi ansembe. (1 Akorinto 15:50-53; Chivumbulutso 20:4, 6) Chimenechitu ndi chiyembekezo chaulemerero waukulu! “Achita ufumu padziko,” osati padziko la Kanani lokha. (Chivumbulutso 5:10) Kodi ‘adzagonjetsa chipata cha adani awo’? (Genesis 22:17) Inde, ndiponso kotheratu, pamene adzaona kuwonongedwa kwa mkazi wachigololo wachipembedzo waudaniyo, Babulo Wamkulu, ndiponso pamene odzozedwa oukitsidwawo adzagwirizana ndi Yesu polamulira mitundu ndi “ndodo yachitsulo” ndiponso pamene adzaphwanya mutu wa Satana. Choncho iwo adzachita nawo ntchito yokwaniritsa mbali yomaliza ya ulosi wa pa Genesis 3:15.—Chivumbulutso 2:26, 27; 17:14; 18:20, 21; Aroma 16:20.
20 Koma tingafunsebe kuti, Kodi pangano la Abrahamu ndi pangano latsopano limangokhudza anthu 144,000 okhulupirikawo basi? Iyayi, enanso amene saali m’mapangano ameneŵa mwachindunji adzadalitsidwa mwa a 144,000 ameneŵa, monga momwe tidzaonera m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 470, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi liti pamene pangano latsopano linaoneka kwa nthaŵi yoyamba kuti layamba kugwira ntchito?
◻ Kodi pangano lakale linachita zotani?
◻ Kodi kwenikweni Mbewu ya Abrahamu ndani, ndipo kodi mitundu inatsatizana motani podalitsidwa kudzera m’Mbewu imeneyo?
◻ Kwa a 144,000, kodi kukwaniritsidwa komaliza kwa pangano la Abrahamu ndi pangano latsopano kudzakhala kotani?
[Chithunzi patsamba 15]
Kukhululukidwa machimo kuli ndi tanthauzo lalikulu kwa a m’pangano latsopano kuposa kwa a m’pangano lakale