Yehova Ndi “Woulula Zinsinsi”
“Ndithudi Mulungu wa anthu inu ndi Mulungu wa milungu yonse, Ambuye wa mafumu onse ndiponso Woulula zinsinsi.”—DAN. 2:47.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zam’tsogolo?
Kodi mitu 6 yoyamba ya chilombo ikuimira maufumu ati?
Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso ndi chifaniziro chimene Nebukadinezara anaona?
1, 2. Kodi Yehova watiululira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani wachita zimenezi?
KODI ndi maboma ati amene adzakhala amphamvu kwambiri padziko lapansi pa nthawi imene Ufumu wa Mulungu uzidzathetsa ulamuliro wa anthu? Tikudziwa yankho la funsoli chifukwa Yehova Mulungu, yemwe ndi “Woulula zinsinsi,” anatiululira. Iye amatithandiza kudziwa mabomawa kuchokera pa zimene mneneri Danieli ndiponso mtumwi Yohane analemba.
2 Yehova anasonyeza anthu amenewa masomphenya okhala ndi zilombo zosiyanasiyana. Komanso anauza Danieli tanthauzo la loto linalake la chifaniziro chachikulu kwambiri. Yehova anachititsa kuti zinthuzi zilembedwe m’Baibulo kuti zitithandize. (Aroma 15:4) Anachita zimenezi n’cholinga choti tikhale ndi chikhulupiriro champhamvu kuti posachedwapa Ufumu wake udzaphwanya maboma onse a anthu.—Dan. 2:44.
3. Kuti timvetse maulosi molondola, kodi choyamba tiyenera kudziwa chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?
3 Masomphenya a Danieli ndi Yohane amasonyeza mafumu 8, kapena kuti maulamuliro 8 a anthu. Amasonyezanso nthawi imene mafumuwa adzakhalapo. Koma kuti timvetse molondola za masomphenyawa, tiyenera kudziwa bwino tanthauzo la ulosi woyambirira wa m’Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti nkhani yaikulu m’Baibulo imakhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu. Choncho maulosi ena onse a m’Baibulo amakhudzana ndi ulosi woyambirirawu.
MBEWU YA NJOKA NDIPONSO CHILOMBO
4. Kodi mbewu ya mkazi ndi ndani, nanga mbewu imeneyi idzachita chiyani?
4 Anthu oyambirira atangopanduka m’munda wa Edeni, Yehova analonjeza kuti “mkazi” adzatulutsa “mbewu.”a (Werengani Genesis 3:15.) Analonjezanso kuti mbewu imeneyi idzaphwanya mutu wa njoka, kapena kuti Satana. Yehova anadzaulula kuti mbewuyi idzachokera mu mzera wa Abulahamu, mu mtundu wa Aisiraeli, m’fuko la Yuda ndiponso kuti idzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. (Gen. 22:15-18; 49:10; Sal. 89:3, 4; Luka 1:30-33) Mbali yaikulu ya mbewuyi inadzakhala Khristu Yesu. (Agal. 3:16) Mbali yachiwiri ya mbewuyi ndiyo anthu odzozedwa ndi mzimu mu mpingo wachikhristu. (Agal. 3:26-29) Yesu limodzi ndi odzozedwa amapanga Ufumu wa Mulungu. Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu kuti aphwanye Satana.—Luka 12:32; Aroma 16:20.
5, 6. (a) Kodi Danieli ndi Yohane analemba za maulamuliro amphamvu angati? (b) Kodi mitu ya chilombo chotchulidwa m’buku la Chivumbulutso imaimira chiyani?
5 Ulosi woyambirira umene Mulungu ananena mu Edeni uja unanenanso kuti Satana adzatulutsa “mbewu.” Unanena kuti mbewu yake idzadana ndi mbewu ya mkazi. Kodi mbewu ya njokayo ndi ndani? Ndi onse amene amatsanzira Satana podana ndi Mulungu ndiponso kudana ndi anthu a Mulungu. Kuyambira kalekale, Satana anakonza zoti mbewu yake izikhala ndi maufumu kapena maboma. (Luka 4:5, 6) Koma ndi maufumu ochepa okha padziko lapansi amene alowerera kwambiri m’zochita za anthu a Mulungu omwe ndi Aisiraeli ndiponso Akhristu odzozedwa. Kudziwa zimenezi kungatithandize kumvetsa chifukwa chake masomphenya a Danieli ndiponso Yohane amangonena za maulamuliro amphamvu 8 okha.
6 Cha m’ma 96 C.E., Yesu amene anali ataukitsidwa, anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya osiyanasiyana ochititsa chidwi. (Chiv. 1:1) M’masomphenya ena, Yohane anaona Mdyerekezi yemwe anaimiridwa ndi chinjoka chimene chinali chitaima m’mbali mwa nyanja yaikulu. (Werengani Chivumbulutso 13:1, 2.) Yohane anaonanso chilombo chachilendo chikutuluka m’nyanjayo ndipo Mdyerekezi anachipatsa ulamuliro waukulu. Kenako, mngelo anauzanso Yohane kuti mitu 7 ya chilombo chofiira, chomwe ndi chifaniziro cha chilombo cha pa Chivumbulutso 13:1, imaimira “mafumu 7,” kapena kuti maboma 7. (Chiv. 13:14, 15; 17:3, 9, 10) Pa nthawi imene Yohane analemba zimenezi, mafumu asanu anali atagwa, imodzi inalipo ndipo ‘inayo inali isanafikebe.’ Kodi mafumu kapena kuti maulamuliro amphamvu padziko lonse amenewa ndi ati? Tiyeni tikambirane za mutu uliwonse wa chilombo chotchulidwa m’buku la Chivumbulutso. Tionanso mmene ulosi wa Danieli ungatithandizire kudziwa za mafumuwa. Ulosiwu unalembedwa kudakali zaka zambiri ena mwa mafumuwa asanakhaleko.
MITU IWIRI YOYAMBA IKUIMIRA IGUPUTO NDI ASURI
7. Kodi mutu woyamba ukuimira ndani ndipo n’chifukwa chiyani tikutero?
7 Mutu woyamba wa chilombochi ukuimira Iguputo. Tikutero chifukwa chakuti Iguputo unali ufumu wamphamvu woyamba kudana ndi anthu a Mulungu, kapena kuti Aisiraeli. Mbewu ya mkazi yolonjezedwa inayenera kuchokera m’mbadwa za Abulahamu ndipo mbadwa zimenezi zinayamba kuchuluka kwambiri ku Iguputo. Ndiyeno ufumu wa Iguputo unayamba kupondereza Aisiraeliwo. Satana anayesa kuwononga anthu onse a Mulunguwo mbewuyo isanafike. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iye anachititsa Farao kuganiza zoti awononge ana aamuna onse a Aisiraeli. Yehova analepheretsa zimenezi ndipo anamasula anthu ake ku ukapolo ku Iguputo. (Eks. 1:15-20; 14:13) Kenako anathandiza Aisiraeliwo kukhazikika m’Dziko Lolonjezedwa.
8. Kodi mutu wachiwiri ukuimira ndani ndipo unayesa kuchita chiyani?
8 Mutu wachiwiri wa chilombo ukuimira Asuri. Ufumu wamphamvu umenewu unayesanso kuwononga anthu onse a Mulungu. N’zoona kuti Yehova anagwiritsa ntchito Asuri polanga ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli. Anachita zimenezi chifukwa iwo anali kulambira mafano komanso anapanduka. Koma kenako Asuri anaukiranso Yerusalemu. N’kutheka kuti Satana ankafuna kuwononga mzere wa mafumu umene Yesu anali kudzabadwira. Izi zinali zosemphana ndi cholinga cha Yehova. Choncho iye anapulumutsa anthu ake okhulupirika m’njira yozizwitsa powononga Asuriwo.—2 Maf. 19:32-35; Yes. 10:5, 6, 12-15.
MUTU WACHITATU UKUIMIRA BABULO
9, 10. (a) Kodi Yehova analola Ababulo kuchita chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinayenera kuchitika kuti ulosi ukwaniritsidwe?
9 Mutu wachitatu wa chilombo chimene Yohane anaona ukuimira ufumu umene likulu lake linali Babulo. Yehova analola Ababulo kuwononga Yerusalemu n’kutenga anthu ake kupita nawo ku ukapolo. Koma tsoka limeneli lisanafike, Yehova anachenjeza Aisiraeli opandukawo. (2 Maf. 20:16-18) Iye analosera kuti mzere wa mafumu amene anakhala “pampando wachifumu wa Yehova” ku Yerusalemu udzawonongedwa. (1 Mbiri 29:23) Koma Yehova analonjezanso kuti mbadwa ya Mfumu Davide, yomwe inali ‘yoyenerera mwalamulo,’ idzafika n’kutenga ufumuwo.—Ezek. 21:25-27.
10 Ulosi wina unasonyeza kuti Ayuda adzakhala akulambirabe pakachisi ku Yerusalemu pa nthawi imene Wodzozedwa, kapena kuti Mesiya amene Mulungu analonjeza, azidzafika. (Dan. 9:24-27) Ulosi wina, umene unalembedwa Aisiraeli asanapite ku ukapolo ku Babulo, unanena kuti Mesiyayo adzabadwira ku Betelehemu. (Mika 5:2) Kuti maulosi amenewa akwaniritsidwe, panafunika kuti Ayuda amasulidwe ku ukapolo, abwerere kwawo ndiponso amangenso kachisi. Koma Ababulo sankamasula akapolo awo. Ndiyeno kodi Ayudawo akanamasulidwa bwanji? Yehova anaulula zimenezi kwa aneneri ake.—Amosi 3:7.
11. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinaimira ufumu wa Babulo? (Onani mawu a m’munsi.)
11 Mneneri Danieli anali m’gulu la anthu amene anatengedwa n’kupita ku ukapolo ku Babulo. (Dan. 1:1-6) Yehova anamugwiritsa ntchito poulula maufumu amene anadzabwera pambuyo pa ufumu wa Babulo. Yehova anaulula zinsinsizi pogwiritsa ntchito zizindikiro zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, anachititsa Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo kulota za chifaniziro chachikulu chopangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana. (Werengani Danieli 2:1, 19, 31-38.) Kudzera mwa Danieli, Yehova anaulula kuti mutu wagolide wa chifanizirochi unkaimira ufumu wa Babulo.b Chifuwa ndi manja a chifanizirochi zinali zasiliva ndipo zinkaimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene unabwera pambuyo pa Babulo. Kodi ufumu umenewu unali uti ndipo unachita chiyani ndi anthu a Mulungu?
MUTU WACHINAYI UKUIMIRA MEDIYA NDI PERISIYA
12, 13. (a) Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zokhudza kugonjetsedwa kwa Babulo? (b) N’chifukwa chiyani zili zomveka kunena kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya ukuimiridwa ndi mutu wachinayi wa chilombo?
12 Kudakali zaka zoposa 100 kuti nthawi ya Danieli ifike, Yehova anaulula kudzera mwa mneneri Yesaya zinthu zina zokhudza ulamuliro wamphamvu padziko lonse umene udzagonjetse Babulo. Yehova anafotokoza mmene ufumuwo udzagonjetsere mzinda wa Babulo komanso dzina la munthu amene adzaugonjetse. Mfumu yodzagonjetsa Babulo inali Koresi wa ku Perisiya. (Yes. 44:28; 45:1-2) Danieli anaonanso masomphenya ena awiri okhudza ufumu wa Mediya ndi Perisiya. M’masomphenya oyamba, ufumuwu unaimiridwa ndi chimbalangondo chomwe chinali chotukuka mbali imodzi ndipo chinauzidwa kuti: “Idya nyama yambiri.” (Dan. 7:5) M’masomphenya achiwiri, Danieli anaona nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri yomwe inkaimiranso ufumu womwewu.—Dan. 8:3, 20.
13 Yehova anagwiritsa ntchito ufumu wa Mediya ndi Perisiya pofuna kukwaniritsa ulosi. Ufumuwu unagonjetsa Babulo n’kulola Aisiraeli kubwerera kwawo. (2 Mbiri 36:22, 23) Koma pa nthawi ina, ufumu womwewu unangotsala pang’ono kuwononga anthu onse a Mulungu. M’buku la Esitere muli nkhani ya chiwembu chimene nduna yaikulu ya ufumu wa Perisiya, dzina lake Hamani, anakonza. Iye anakonza zoti Ayuda onse amene anali m’zigawo zolamulidwa ndi ufumu wa Perisiya aphedwe. Ndipo iye anakonzeratu tsiku loti chiwembuchi chichitike. Koma Yehova analowererapo n’kupulumutsa anthu ake kuti asawonongedwe ndi mbewu ya Satana. (Esitere 1:1-3; 3:8, 9; 8:3, 9-14) Choncho, m’pomveka kunena kuti ufumu wa Mediya ndi Perisiya ukuimiridwa ndi mutu wachinayi wa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso.
MUTU WACHISANU UKUIMIRA GIRISI
14, 15. Kodi Yehova anaulula zinthu ziti zokhudza ufumu wakale wa Girisi?
14 Mutu wachisanu wa chilombo cha m’buku la Chivumbulutso ukuimira Girisi. Pomasulira loto la Nebukadinezara, Danieli anaulula kuti ufumuwu ukuimiridwanso ndi mimba ndi ntchafu zamkuwa za chifaniziro chija. Danieli anaonanso masomphenya awiri amene anafotokoza zinthu zochititsa chidwi zokhudza ufumuwu komanso mfumu yake yamphamvu.
15 M’masomphenya oyamba, ufumu wa Girisi unaimiridwa ndi kambuku wokhala ndi mapiko anayi. Izi zinasonyeza kuti ufumuwu uzidzagonjetsa mofulumira. (Dan. 7:6) M’masomphenya achiwiri, Danieli anaona mbuzi yokhala ndi nyanga imodzi yaikulu imene inapha mwamsanga nkhosa yamphongo yokhala ndi nyanga ziwiri, yomwe inkaimira ufumu wa Mediya ndi Perisiya. Yehova anauza Danieli kuti mbuziyi ikuimira Girisi ndipo nyanga yake yaikuluyo ikuimira mfumu yake ina. Kenako Danieli analemba kuti nyanga yaikuluyo idzathyoka ndipo m’malo mwake padzamera zina zinayi. Ngakhale kuti ulosiwu unalembedwa zaka mahandiredi angapo ufumu wa Girisi usanakhale wamphamvu, zonse zimene analemba zinakwaniritsidwa. Nyangayi ikuimira Alekizanda Wamkulu, yemwe anali mfumu yamphamvu ya ufumu wa Girisi. Iye anatsogolera pa nkhondo yomenyana ndi Mediya ndi Perisiya. Koma nyangayi inathyoka msanga. Tikutero chifukwa chakuti mfumuyi inamwalira ili ndi zaka 32 zokha ndipo pa nthawiyi inali yamphamvu kwambiri. Ndiyeno akuluakulu anayi a asilikali ake anagawana ufumuwu.—Werengani Danieli 8:20-22.
16. Kodi Antiyokasi Wachinayi anachita zotani?
16 Ufumu wa Girisi utagonjetsa Perisiya, unayamba kulamulira dziko limene anthu a Mulungu ankakhala. Pa nthawiyi, Ayuda anali atabwerera ku Dziko Lolonjezedwa ndipo anali atamanganso kachisi ku Yerusalemu. Ayudawo anali adakalibe anthu osankhidwa a Mulungu ndipo kachisi amene anamumanganso uja ndi amene anali malo awo olambirira. Koma m’zaka za m’ma 100 B.C.E., ufumu wa Girisi, womwe ndi mutu wachisanu wa chilombo chija, unaukira anthu a Mulungu. Antiyokasi Wachinayi anali mmodzi wa asilikali amene analowa m’malo mwa Alekizanda. Iye anaika guwa lansembe loperekera nsembe kwa milungu yonyenga m’bwalo la kachisi ku Yerusalemu. Analamula kuti munthu aliyense wotsatira chipembedzo chachiyuda aphedwe. Izi zikusonyeza kuti mbewu ya Satana inali kudana kwambiri ndi anthu a Mulungu. Koma posapita nthawi, ufumu wa Girisi unalowedwa m’malo ndi ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse. Kodi mutu wa 6 ukuimira ufumu uti?
MUTU WA 6 UKUIMIRA UFUMU WA ROMA UMENE UNALI ‘WOOPSA KWAMBIRI’
17. Kodi mutu wa 6 unachita chiyani chokhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Genesis 3:15?
17 Pa nthawi imene Yohane ankaona masomphenya a chilombo, ufumu wa Roma ndi umene unali wamphamvu. (Chiv. 17:10) Mutu wa 6 umenewu unachita chinthu chachikulu chokhudza kukwaniritsidwa kwa ulosi wa pa Genesis 3:15. Satana anagwiritsa ntchito asilikali achiroma kuti avulaze “chidendene” cha mbewu yolonjezedwa. Kodi anachita bwanji zimenezi? Iwo anaimba Yesu mlandu wabodza woukira boma ndipo anamupha. (Mat. 27:26) Koma bala limeneli linachira mwamsanga chifukwa Yehova anaukitsa Yesu.
18. (a) Kodi Yehova anasankha mtundu watsopano uti ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi mbewu ya njoka inasonyeza bwanji kuti inkalusirabe mbewu ya mkazi?
18 Atsogoleri achipembedzo a Isiraeli anagwirizana ndi Aroma pokonzera Yesu chiwembu ndipo Ayuda ambiri anakana Yesu. Choncho, Yehova anasiya kuona mtundu wa Isiraeli ngati anthu ake. (Mat. 23:38; Mac. 2:22, 23) M’malomwake, anasankha mtundu watsopano womwe ndi “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 3:26-29; 6:16) Mtundu watsopanowu ndi wa Akhristu odzozedwa ndipo wapangidwa ndi Ayuda komanso anthu amitundu ina. (Aef. 2:11-18) Yesu atafa n’kuukitsidwa, mbewu ya njoka inapitirizabe kulusira mbewu ya mkazi. Aroma anayesanso kuwononga mpingo wa Akhristu odzozedwa, womwe ndi mbali yachiwiri ya mbewu ya mkazi.c
19. (a) Kodi Danieli anafotokoza bwanji ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa nambala 6? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani imene ili patsamba 14?
19 M’loto la Nebukadinezara limene Danieli anamasulira, ufumu wa Roma ukuimiridwa ndi miyendo yachitsulo. (Dan. 2:33) Danieli anaonanso masomphenya ena osonyeza ufumu wa Roma komanso ulamuliro wina wamphamvu padziko lonse wochokera mu ufumu wa Roma womwewo. (Werengani Danieli 7:7, 8.) Kwa zaka zambiri, adani a ufumu wa Roma ankaona kuti ufumuwo uli ngati chilombo “choopsa kwambiri ndiponso chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri.” Koma ulosiwo unanena kuti “nyanga 10” zidzachokera mu ufumuwo ndipo nyanga ina yaing’ono idzamera yomwe idzakhala yamphamvu kwambiri. Kodi nyanga 10 zikuimira chiyani, nanga yaing’onoyo ikuimira chiyani? Kodi nyanga yaing’onoyo ikugwirizana bwanji ndi chifaniziro chachikulu chimene Nebukadinezara anaona? Nkhani imene ili patsamba 14 iyankha mafunso amenewa.
[Mawu a M’munsi]
a Mkazi ameneyu amaimira gulu la Yehova la zolengedwa zauzimu zakumwamba lomwe lili ngati mkazi wake.—Yes. 54:1; Agal. 4:26; Chiv. 12:1, 2.
b Ufumu wa Babulo unaimiridwa ndi mutu wa chifaniziro m’buku la Danieli komanso mutu wachitatu wa chilombo chofotokozedwa m’buku la Chivumbulutso. Onani tchati patsamba 12 ndi 13.
c Ngakhale kuti Aroma anawononga Yerusalemu mu 70 C.E., izi sizinakwaniritse ulosi wa pa Genesis 3:15. Pa nthawiyi, mtundu wa Isiraeli sunali anthu osankhidwa a Mulungu.