Mutu 10
Ndani Angalimbane ndi Kalonga wa Akalonga?
1, 2. N’chifukwa chiyani masomphenya amene Danieli anaona m’chaka chachitatu cha ulamuliro wa Belisazara ali ofunika kwa ife?
PAPITA zaka 57 chiwonongereni kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Belisazara ndi atate wake Nabonidasi, akulamulira limodzi Ufumu wa Babulo, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachitatu malinga ndi ulosi wa Baibulo.a Danieli mneneri wa Mulungu ali m’dziko landende ku Babulo. Ndipo mu “chaka chachitatu cha Belisazara mfumu,” Yehova atumizira Danieli masomphenya ovumbula mbali zina zobwezeretsa kulambira koona.—Danieli 8:1.
2 Masomphenya aulosi amene Danieli anaona anam’khudza kwambiri ndipo amatikhudzanso ife okhala mu “nthaŵi yachimaliziro.” Mngelo Gabrieli akuuza Danieli kuti: “Taona, ndidzakudziŵitsa chimene chidzachitika pa chitsiriziro cha mkwiyowo; pakuti pa nthaŵi yoikika m’pakutha pake.” (Danieli 8:16, 17, 19, 27) Ndi chidwi chenicheni, tiyeni tipende zimene Danieli anaona ndi tanthauzo lake kwa ife lero.
NKHOSA YAMPHONGO YA NYANGA ZIŴIRI
3, 4. Kodi Danieli anaona nyama yanji itaimirira kumtsinje, ndipo ikuimira chiyani?
3 “Ndinaona m’masomphenya,” akulemba motero Danieli, “tsono kunali, pakuona ine ndinali m’Susani, m’nyumba ya mfumu, ndiwo m’dziko la Elamu; ndinaona m’masomphenya kuti ndinali kumtsinje [wa] Ulai.” (Danieli 8:2) Kaya Danieli analidi ku Susani (Susa)—likulu la Elamu, lokhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 350 kum’maŵa kwa Babulo—kapena anali kumeneko m’masomphenya chabe sizikudziŵika.
4 Danieli akupitiriza kuti: “Ndinakweza maso anga ndi kupenya; taonani, panaima pamtsinje nkhosa yamphongo yokhala nazo nyanga ziŵiri.” (Danieli 8:3a) Kuti nkhosa yamphongoyo ikuimira chiyani sichikukhalabe chinsinsi kwa Danieli. Pambuyo pake mngelo Gabrieli akunena kuti: “Nkhosa yamphongo waiona ya nyanga ziŵiri ndizo mafumu a Mediya ndi Perisiya.” (Danieli 8:20) Amedi anachokera kumapiri a kum’maŵa kwa Asuri, ndipo Aperisi poyamba ankakhala moyo wosamukasamuka kumpoto kwa nyanja ya Perisiya. Komabe, pamene Ufumu wa Mediya ndi Perisiya unakula, anthu ake anakhala okonda zinthu zapamwamba.
5. Kodi nyanga imene “inaphuka m’mbuyo” inakhala yotalikirapo motani?
5 “Nyanga ziŵirizo zinali za msinkhu wautali,” akutero Danieli, “koma imodzi inaposa inzake; yoposayo inaphuka m’mbuyo.” (Danieli 8:3b) Nyanga yotalikirapoyo imene inatuluka pambuyo pake ikuimira Aperisi, pamene nyanga inayo ikuimira Amedi. Poyamba, Amedi ndiwo anali kulamulira. Koma mu 550 B.C.E., Koresi wolamulira wa Perisiya anagonjetsa mosavuta Mfumu Asitajesi ya Mediya. Ndiyeno Koresi anaphatikiza pamodzi miyambo ndi malamulo a mitundu iŵiriyo, nagwirizanitsanso maufumu awo, ndi kugonjetsanso madera ena. Kuyambira pamenepo, ufumuwo unakhala wophatikiza mbali ziŵirizo.
NKHOSA YAMPHONGO ICHITA MANGOLOMERA
6, 7. Kodi zinali motani kuti “panalibe zamoyo [“zilombo,”] zokhoza kuima pamaso” pa nkhosa yamphongo?
6 Popitiriza kufotokoza nkhosa yamphongoyo, Danieli akunena kuti: “Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m’dzanja lake, koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa.”—Danieli 8:4.
7 M’masomphenya apitawo amene anapatsidwa kwa Danieli, Babulo anaimiridwa ndi chilombo chimene chinatuluka panyanja chofanana ndi mkango cha mapiko ngati a chiwombankhanga. (Danieli 7:4, 17) Chilombo chophiphiritsa chimenecho sichinathe kulimbana ndi “nkhosa yamphongo” ya m’masomphenya atsopanoŵa. Babulo anagwa kwa Koresi Wamkulu mu 539 B.C.E. Pafupifupi zaka 50 pambuyo pake, “panalibe zamoyo [“zilombo,” NW],” kapena maboma andale, amene anakhoza kulimbana ndi Ufumu wa Mediya ndi Perisiya—ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachinayi wa mu ulosi wa Baibulo.
8, 9. (a) Kodi ‘nkhosa yamphongoyo inagunda [motani] kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera’? (b) Kodi buku la Estere limanenanji za mloŵa m’malo wa Dariyo 1, Mfumu ya Perisiya?
8 Pochokera “kum’maŵa”—kotulukira dzuŵa—Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Mediya ndi Perisiya unachita mulimonse mmene unafunira, ‘unagunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera.’ (Yesaya 46:11) Mfumu Kambisesi 2, amene analoŵa m’malo Koresi Wamkulu, anagonjetsa Igupto. Mloŵa m’malo wake anali Dariyo 1, mfumu ya Perisiya, amene analoŵera chakumadzulo nawoloka mfuleni wa Bosipola mu 513 B.C.E. ndi kulanda dera la Ulaya la Thiresi, limene likulu lake linali ku Bezantiya (tsopano Istanbul). M’chaka cha 508 B.C.E., anagonjetsa Thiresi, ndipo mu 496 B.C.E. anagonjetsa Makedoniya. Choncho, pofika nthaŵi ya Dariyo, “nkhosa yamphongo” ya Mediya ndi Perisiya inali italanda madera kumbali zitatu: kumpoto inalanda Babulo ndi Asuri, kumadzulo inalanda Asiyamina, ndipo kumwera inalanda Igupto.
9 Pochitira umboni ukulu wa Ufumu wa Mediya ndi Perisiya, Baibulo limanena za mloŵa m’malo wa Dariyo, Sasta 1, kuti anali “Ahasweroyo [amene] anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa mayiko zana limodzi mphambu makumi aŵiri kudza asanu ndi aŵiri.” (Estere 1:1) Koma ufumu waukulu umenewu unagonja kwa wina, ndipo pambali imeneyi, masomphenya a Danieli amavumbula mfundo zina zochititsa chidwi zimene ziyenera kulimbikitsa chikhulupiriro chathu pa mawu aulosi a Mulungu.
TONDE AGUNDA NDI KUGWETSA NKHOSA YAMPHONGO
10. M’masomphenya a Danieli, ndi nyama yanji imene inagunda ndi kugwetsa “nkhosa yamphongo”?
10 Taganizani mmene Danieli anadabwira ndi zimene akuona tsopano. Nkhaniyo ikuti: “Polingirapo ine, taonani, wadza tonde wochokera kumadzulo, pankhope ya dziko lonse lapansi, wosakhudza nthaka; ndi mbuziyo inali ndi nyanga yooneka bwino pakati pa maso ake. Ndipo anadzera nkhosa yamphongoyo yokhala ndi nyanga ziŵiri, imene ndidaiona ilikuima kumtsinje, naithamangira ndi mphamvu yake yaukali. Ndipo ndinamuona wayandikira pafupi pa nkhosa yamphongo, naŵaŵidwa mtima nayo, naigunda nkhosa yamphongo, nathyola nyanga zake ziŵiri; ndipo mphongoyo inalibe mphamvu yakuima pamaso pake, koma anaigwetsa pansi, naipondereza; ndipo panalibe wakupulumutsa mphongoyo m’dzanja lake.” (Danieli 8:5-7) Kodi zonsezi zikutanthauza chiyani?
11. (a) Kodi mngelo Gabrieli anam’fotokoza motani “tonde wamanyenje” ndi “nyanga yaikulu”? (b) Ndani anaimiridwa ndi nyanga yooneka bwinoyo?
11 Danieli limodzi ndi ife, sitikusiyidwa m’malere ponena za tanthauzo la masomphenyaŵa. Mngelo Gabrieli akuuza Danieli kuti: “Tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Helene [“Girisi,” NW], ndi nyanga yaikulu ili pakati pa maso ake ndiyo mfumu yoyamba.” (Danieli 8:21) Mu 336 B.C.E., mfumu yomalizira ya Ufumu wa Perisiya, Dariyo 3 (Kondomanasi), analongedwa ufumu. M’chaka chimenecho, Alesandro anakhala mfumu ya Makedoniya. Mbiri yakale imasonyeza kuti Alesandro Wamkulu ndiye anali “mfumu ya Helene [Girisi]” yonenedweratuyo. Kuyambira “kumadzulo,” m’chaka cha 334 B.C.E., Alesandro anayenda mofulumira kwambiri. Ngati kuti “osakhudza nthaka,” anagonjetsa maderawo ndi kugwetsa “nkhosa yamphongoyo.” Atathetsa ulamuliro wa Mediya ndi Perisiya wa zaka pafupifupi mazana aŵiri, Girisi anakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu wotchulidwa m’Baibulo. Kumeneku ndi kukwaniritsidwa kochititsa chidwi zedi kwa ulosi wa Mulungu!
12. Kodi “nyanga yaikulu” ya mbuzi yophiphiritsayo ‘inathyoka’ motani, ndipo ndani anali nyanga zinayi zimene zinaloŵa m’malo mwake?
12 Komabe ulamuliro wa Alesandro unali wosapita patali. Masomphenyawo akuvumbulanso kuti: “Ndipo tondeyo anadzikulitsa kwakukulu, koma atakhala wamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoka; ndi m’malo mwake munaphuka nyanga zinayi zooneka bwino, zoloza ku mphepo zinayi za mlengalenga.” (Danieli 8:8) Pofotokoza ulosiwo, Gabrieli akuti: “Kuti zinaphuka zinayi m’malo mwake mwa iyo itathyoka, adzauka maufumu anayi ochokera mu mtunduwu wa anthu, koma osakhala nayo mphamvu ya uja.” (Danieli 8:22) Malinga ndi ulosi, ali pachimake penipeni pa chipambano chake, Alesandro ‘anathyoka,’ kapena kuti anafa, pausinkhu wa zaka 32 zokha. Ndipo m’kupita kwa nthaŵi akazembe ake anayi anagaŵana pakati pawo ufumu wake waukuluwo.
NYANGA YAING’ONO YODABWITSA
13. N’chiyani chinaphuka mu imodzi ya nyanga zinayizo, ndipo chinachita motani?
13 Mbali yotsatira ya masomphenyawo ikutenga zaka zoposa 2,200, ndipo kukwaniritsidwa kwake kukufika m’nthaŵi yathu ino. Danieli akulemba kuti: “Mu imodzi ya izi [nyanga zinayizo] munaphuka nyanga yaing’ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum’maŵa, ndi ku dziko lokometsetsa. Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza. Inde inadzikulitsa kufikira kwa Kalonga wa khamulo, nim’chotsera nsembe yopsereza yachikhalire; ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa. Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika.”—Danieli 8:9-12.
14. Kodi mngelo Gabrieli ananenanji za zochita za nyanga yaing’ono yophiphiritsayo, ndipo n’chiyani chikachitikira nyangayo?
14 Tisanazindikire tanthauzo la mawu ogwidwawo, tiyenera timvetsere kaye kwa mngelo wa Mulungu. Atatchula za kuyamba kulamulira kwa maufumu anayi ochokera mu ufumu wa Alesandro, mngelo Gabrieli akuti: “Potsiriza pake pa ufumu wawo, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi. Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ayi, nidzawononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuwononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo. Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m’dzanja mwake, nadzadzikuza m’mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzawononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.”—Danieli 8:23-25.
15. Kodi mngeloyo anauza Danieli kuti achite chiyani ponena za masomphenyawo?
15 Mngeloyo akuuza Danieli kuti: “Koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.” (Danieli 8:26) Kukwaniritsidwa kwa mbali imeneyi ya masomphenyawo kunayenera kudzachitika patapita “masiku ambiri,” ndipo Danieli anayenera ‘kubisa masomphenyawo.’ Tanthauzo lake linakhalabe chinsinsi kwa Danieli. Koma panopo, “masiku ambiri” amenewo ayeneradi kuti anakwana kale. Choncho funso n’lakuti: ‘Kodi mbiri ya dziko ikuvumbula chiyani ponena za kukwaniritsidwa kwa masomphenya aulosi ameneŵa?’
NYANGA YAING’ONO IKHALA YAMPHAMVU KWAMBIRI
16. (a) Kodi nyanga yaing’ono inaphuka kuchokera m’nyanga yophiphiritsa iti? (b) Kodi Roma anakhala motani ulamuliro wachisanu ndi chimodzi wamphamvu padziko lonse wa mu ulosi wa Baibulo, koma n’chifukwa chiyani sunali nyanga yaing’ono?
16 Malinga ndi zochitika za m’mbiri, nyanga yaing’onoyo inali mphukira ya imodzi mwa nyanga zinayi zophiphiritsazo—yakumadzulo kwenikweni. Umenewu unali ufumu wa chihelene wa Kazembe Kasanda mfumu ya Makedoniya ndi Girisi. Pambuyo pake, ufumu umenewu unatengedwa ndi Kazembe Lasamekase, mfumu ya Thiresi ndi Asiyamina. M’zaka za zana lachiŵiri isanafike Nyengo Yathu Ino, madera akumadzulo ameneŵa a ufumu wa Chihelene analandidwa ndi Roma. Ndipo pofika m’chaka cha 30 B.C.E., Roma analanda maboma onse achihelene, nakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chimodzi wa mu ulosi wa Baibulo. Koma Ufumu wa Roma sindiwo unali nyanga yaing’ono ya m’masomphenya a Danieli, chifukwa ufumu ujawo sunapitirire mpaka ‘panthaŵi yoikika yachitsiriziro.’—Danieli 8:19.
17. (a) Kodi panali ubale wotani pakati pa Britain ndi Ufumu wa Roma? (b) Ndi ubale wotani umene uli pakati pa Ufumu wa Britain ndi ufumu wa Chihelene wa Makedoniya ndi Girisi?
17 Pamenepo, kodi mbiri yakale ikusonyeza kuti “mfumu ya nkhope yaukali” komanso yamtopola inali ndani? Britain ndiye anali mphukira yakumpoto chakumadzulo kwa Ufumu wa Roma. Kudzafika mpaka kumayambiriro kwa zaka za zana lachisanu la C.E., Britain wamakonoyu anali madera a Roma. M’kupita kwa nthaŵi, Ufumu wa Roma unatha, koma chitukuko cha Girisi ndi Roma chinapitirira m’Britain ndi m’madera ena a Ulaya amene ankalamulidwa ndi Roma. Octavio Paz, katswiri wa ndakatulo komanso mlembi wa ku Mexico amene anapata mphotho ya Nobel analemba kuti: “Pamene Ufumu wa Roma unagwa, Tchalitchi ndicho chinayamba kulamulira.” Anawonjezanso kuti: “Abambo a Tchalitchi, limodzi ndi akatswiri azamaphunziro anaphatikiza filosofi yachigiriki m’chiphunzitso chachikristu.” Ndipo Bertrand Russell, wafilosofi komanso katswiri wamasamu wa m’zaka za zana la 20 ananena kuti: “Kutukuka kwa mayiko a Azungu, kumene kunachokera kwa Agiriki, kunadalira maganizo afilosofi komanso asayansi amene anayambira ku Mileto [mzinda wa Agiriki wa ku Asiyamina] zaka zikwi ziŵiri ndi theka kalelo.” Choncho tingatero kuti gwero la chikhalidwe cha Ufumu wa Britain linali ufumu wa Chihelene wa Makedoniya ndi Girisi.
18. Ndani ali nyanga yaing’ono imene inakhala ‘mfumu ya nkhope yaukali panthaŵi yoikika yachitsiriziro’? Fotokozani.
18 Pofika mu 1763 Ufumu wa Britain unagonjetsa adani ake amphamvu, Spanya ndi France. Kuyambira nthaŵi imeneyo anakhala ngati dona wapanyanja komanso ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri wa mu ulosi wa Baibulo. Ngakhale pamene mayiko 13 achitsamunda a ku America anamasuka ku Britain mu 1776 ndi kukhazikitsa United States of America, Ufumu wa Britain unakulabe ndi kukuta gawo limodzi mwa anayi a dziko lonse lapansi komanso gawo limodzi mwa anayi a anthu ake onse. Ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri unaŵirikizanso mphamvu zake pamene United States of America anaphatikana ndi Britain ndi kupanga ulamuliro wogwirizana wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Kunena za chuma chake ndi mphamvu yake m’zankhondo, ulamuliro umenewu unali utakhaladi “mfumu ya nkhope yaukali.” Pamenepo, ndiye kuti nyanga yaing’onoyo imene inakhala ulamuliro wandale woopsa ‘panthaŵi yoikika yachitsiriziro,’ ndiyo Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America.
19. Kodi “dziko lokometsetsa” lotchulidwa m’masomphenyawo ndilo chiyani?
19 Danieli anaona kuti nyanga yaing’ono “inakula kwakukulu ndithu” kuloza “ku dziko lokometsetsa.” (Danieli 8:9) Dziko Lolonjezedwa limene Yehova anapereka kwa anthu ake osankhika, linali lokongola kwambiri moti linatchedwa “lokometsetsa mwa mayiko onse,” ndiko kuti mayiko onse padziko lapansi. (Ezekieli 20:6, 15) N’zoona kuti Britain analanda Yerusalemu pa December 9, 1917, ndipo m’chaka cha 1920, bungwe la League of Nations linapereka Palesitina m’manja mwa Great Britain, kuti alamulire dzikolo mpaka pa May 14, 1948. Koma masomphenyawo n’ngaulosi, ndipo ali ndi mbali zambiri zophiphiritsa. Ndipo “dziko lokometsetsa” lotchulidwa m’masomphenyawo silikuimira Yerusalemu ayi, koma mkhalidwe wa padziko lapansi wa anthu amene Mulungu akuwaona kukhala opatulika m’nthaŵi ya ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri. Tiyeni tione mmene Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America ukuyesera kuopseza opatulikawo.
“MALO AKE OPATULIKA” AGWETSEDWA
20. Kodi “khamu la kuthambo” ndani, nanga “nyenyezi” ndani zimene nyanga yaing’ono ikuyesa kuzigwetsera pansi?
20 Nyanga yaing’onoyo “ikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi.” Malingana ndi mafotokozedwe a mngelo, “khamu la kuthambo” komanso “nyenyezi” zimene nyanga yaing’onoyo ikuyesa kugwetsera pansi ndiwo “anthu opatulikawo.” (Danieli 8:10, 24) “Opatulika” ameneŵa ndiwo Akristu odzozedwa ndi mzimu. Chifukwa chokhala m’chiyanjo ndi Mulungu mwa pangano latsopano, logwira ntchito ndi magazi okhetsedwa a Yesu Kristu, iwo ali opatulika, oyeretsedwa, ndi opatulidwa kuti atumikire Mulungu ndi moyo wonse. (Ahebri 10:10; 13:20) Powapatsa mwayi wokhala oloŵa nyumba limodzi ndi Mwana wake m’cholandira chakumwamba, Yehova akuwaona kukhala opatulika. (Aefeso 1:3, 11, 18-20) Ndiye kuti m’masomphenya a Danieli, “khamu la kuthambo” limatanthauza otsalira padziko lapansi a 144,000 “opatulika,” amene adzalamulira kumwamba limodzi ndi Mwanawankhosa.—Chivumbulutso 14:1-5.
21. Kodi ndani akukhala mu “malo opatulika” amene ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri ukuyesa kuwapululutsa?
21 Lerolino, otsalira a 144,000 ndiwo oimira “Yerusalemu wakumwamba” padziko lapansi—Ufumu wa Mulungu wonga mzinda—ndi makonzedwe ake a kachisi. (Ahebri 12:22, 28; 13:14) M’ganizo limeneli iwo ali mu “malo opatulika” amene ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri ukuyesetsa kuti uwapondereze ndi kuwapululutsa. (Danieli 8:13) Ponena za malo opatulikawo monganso “pokhala malo ake [Yehova] opatulika,” Danieli akuti: “Nim’chotsera [Yehova] nsembe yopsereza yachikhalire; ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa. Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika.” (Danieli 8:11, 12) Kodi zimenezi zinakwaniritsidwa motani?
22. M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, kodi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri unachita ‘cholakwa’ choonekeratu chotani?
22 Kodi zinthu zinali motani kwa Mboni za Yehova pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse? Zinazunzidwa koopsa! Chizunzocho chinayambira m’mayiko a Nazi ndi a Fasizimu. Koma posakhalitsa ‘choonadi chinagwetsedwa pansi’ mu ufumu wonse wa ‘nyanga yaing’ono imene mphamvu yake inali itakula.’ “Khamu” la alengezi a Ufumu ndi ntchito yawo yolalikira “uthenga wabwino” zinaletsedwa pafupifupi m’mayiko onse amene anali mamembala a bungwe la British Commonwealth. (Marko 13:10) Mayiko ameneŵa polemba anthu usilikali, anakana kupatula Mboni za Yehova, pokana kuwalemekeza iwo monga atumiki a Mulungu oikidwa mwateokalase. Atumiki a Yehova okhulupirika ku United States anavutika ndi ziwawa za magulu ndi nkhanza zosiyanasiyana. Ndipo ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri unayesetsa kuti uchotse nsembe yachitamando—“chipatso cha milomo”—imene anthu a Yehova anaipereka kwa iye nthaŵi zonse monga “nsembe yopsereza yachikhalire” ya kulambira kwawo. (Ahebri 13:15) Motero, ulamuliro wamphamvu padziko lonse umenewo unachita ‘cholakwa’ choloŵerera m’malo a Mulungu Wam’mwambamwamba—“malo ake opatulika.”
23. (a) M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, kodi Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America ‘unaukira [motani] Kalonga wa akalonga’? (b) Kodi ‘Kalonga wa akalongayo’ ndani?
23 Mwa kuzunza “opatulikawo” m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, nyanga yaing’onoyo inachita mangolomera ‘kufikira kwa Kalonga wa khamulo.’ Kapena monga mmene mngelo Gabrieli ananenera, nyangayo ‘inaukira Kalonga wa akalonga.’ (Danieli 8:11, 25) Dzina laudindo lakuti ‘Kalonga wa akalonga’ limagwira ntchito kwa Yehova Mulungu yekhayo basi. Liwu lachihebri lakuti sar, lotembenuzidwa “kalonga,” n’logwirizana ndi verebu yotanthauza “kuchita ulamuliro.” Kupatulapo kunena za mwana wa mfumu kapena munthu waudindo wachifumu, liwulo limatanthauzanso mtsogoleri, kapena wamkulu. Buku la Danieli limatchulanso akalonga ena aungelo—mwachitsanzo, Mikaeli. Mulungu ndiye Kalonga Wamkulu wa akalonga oterowo. (Danieli 10:13, 21; yerekezani ndi Salmo 83:18.) Kodi tingaganize kuti alipo aliyense amene angalimbane ndi Yehova—Kalonga wa akalonga?
“MALO OPATULIKA” AKHALANSO OLUNGAMA
24. Kodi lemba la Danieli 8:14 likutitsimikizira za chiyani?
24 Palibe amene angalimbane ndi Kalonga wa akalonga—ngakhale “mfumu ya nkhope yaukali” monga Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America! Mfumu imeneyi yayesetsa kuti ipululutse malo opatulika a Mulungu, koma yalephera. Mngeloyo akuti: “Mpaka masiku zikwi ziŵiri mphambu mazana atatu [2,300] usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama,” kapena kuti “adzapambana.”—Danieli 8:13, 14; The New English Bible.
25. Kodi nyengo yaulosi ya masiku 2,300 ndi yaitali motani, ndipo iyenera kugwirizanitsidwa ndi chochitika chiti?
25 Masiku 2,300 amenewo ndi nyengo yaulosi. Ndiye kuti kuŵerengera kwake n’koyendera chaka chaulosi cha masiku 360. (Chivumbulutso 11:2, 3; 12:6, 14) Choncho masiku 2,300 ameneŵa ayenera kukhala zaka 6, miyezi 4, ndi masiku 20. Kodi nyengo imeneyi inali liti? Chabwino, m’ma 1930, anthu a Mulungu anayamba kukumana ndi chizunzo choŵirikiza m’mayiko osiyanasiyana. Ndipo m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinazunzidwa koopsa m’mayiko olamulidwa ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Chifukwa chiyani? Chifukwa cha kuumirira kwawo “kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Chifukwa chake, masiku 2,300 ayenera kugwirizanitsidwa ndi nkhondo imeneyo.b Koma tingati nyengo yaulosi imeneyo inayamba liti ndipo inatha liti?
26. (a) Kodi kuŵerengera masiku 2,300 kuyenera kuyambira liti makamaka? (b) Nanga masiku 2,300 amenewo anatha liti?
26 Kuti ‘malo opatulika ayesedwe,’ kapena kubwezeretsedwa, kukhala mmene ayenera kukhalira, ndiye kuti masiku 2,300 anayamba pamene anali “olungama” m’maso mwa Mulungu. Kwenikweni, nyengoyo iyenera kuti inayamba pa June 1, 1938, pamene Nsanja ya Olonda inatulutsa gawo 1 la nkhani yakuti “Gulu.” Gawo 2 linatuluka m’kope la June 15, 1938. Kuŵerenga masiku 2,300 (zaka 6, miyezi 4, ndi masiku 20 pa kalendala ya chihebri) kuchokera pa June 1 kapena 15, 1938, kumatifikitsa pa October 8 kapena 22, 1944. Patsiku loyamba la msonkhano wapadera umene unachitikira ku Pittsburgh, Pennsylvania, U.S.A., pa September 30 ndi October 1, 1944, pulezidenti wa Watch Tower Society anakamba nkhani ya mutu wakuti “Kulongosola Zinthu Kwateokalase Lerolino.” Pamsonkhano wapachaka wa bungwe loyendetsa ntchito pa October 2, chikalata cha Sosaite cha mfundo zoyendetsera gulu chinakonzedwanso pofuna kuchigwirizanitsa bwino kwambiri ndi kakonzedwe kateokalase mogwirizana ndi malamulo a boma. Pamene ziyeneretso za m’Baibulo zinamveketsedwa bwino, posakhalitsa dongosolo lotsatira teokalase kwambiri linakhazikitsidwa m’mipingo ya Mboni za Yehova.
27. Kodi panali umboni wotani wakuti “nsembe yopsereza yachikhalire” inali italetsedwa m’zaka zodzaza mazunzo za nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse?
27 Pamene masiku 2,300 anali m’kati panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, imene inayamba mu 1939, kupereka “nsembe yopsereza yachikhalire” pamalo opatulika a Mulungu kunaletsedwa koopsa chifukwa cha chizunzo. Mu 1938 Watch Tower Society inali ndi nthambi 39 zoyang’anira ntchito ya Mboni kuzungulira dziko lonse, koma pofika mu 1943 nthambizo zinatsala 21 zokha. Ziwonjezeko za olengeza Ufumu zinalinso zotsika kwambiri m’nthaŵiyo.
28, 29. (a) Pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inali kufika kumathero kwake, kodi chinachitika n’chiyani m’gulu la Yehova? (b) Kodi tinganene chiyani za kuyesetsa kwa mdani kuti apululutse ndi kuwononga “malo opatulika”?
28 Monga taonera kale, m’miyezi yakumathero kwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, Mboni za Yehova zinalimbanso mtima pofuna kulemekeza ulamuliro wa Mulungu mwa kum’tumikira monga gulu lateokalase. Ichi ndiye chinali cholinga polinganizanso ntchito ndi kukonzanso dongosolo la uyang’aniro mu 1944. Ndipo Nsanja ya Olonda ya October 15, 1944, inali ndi nkhani yakuti “Olinganizidwa Kaamba ka Ntchito Yomalizira.” Nkhani imeneyo limodzinso ndi nkhani zina zofotokoza utumiki zapanthaŵiyo zinasonyeza kuti masiku 2,300 anali atatha kale ndi kuti “malo opatulika” anakhalanso “olungama.”
29 Zoyesayesa zankhanza za mdaniyo zofuna kupululutsa ndi kuwononga “malo opatulika” zinalephereratu. Ndithudi, “opatulika” otsalawo padziko lapansi, limodzi ndi atsamwali awo a “khamu lalikulu,” anapambana. (Chivumbulutso 7:9) Ndipo malo opatulikawo, mumkhalidwe wake woyenera wateokalase, tsopano akupitiriza kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova.
30. Kodi n’chiyani chidzaonekera “mfumu ya nkhope yaukali” posachedwapa?
30 Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America udakali m’malo. Koma mngelo Gabrieli akuti, “adzathyoledwa popanda dzanja.” (Danieli 8:25) Posachedwa pompa, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wachisanu ndi chiŵiri umenewu wa mu ulosi wa Baibulo—“mfumu ya nkhope yaukali” imeneyi—udzathyoledwa, osati ndi manja a munthu, koma ndi mphamvu yoposa yaumunthu pa Armagedo. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 16:14, 16) N’kosangalatsa bwanji, kudziŵa kuti ufumu wa Yehova Mulungu, Kalonga wa akalonga, udzalemekezedwa panthaŵiyo!
[Mawu a M’munsi]
a Maulamuliro asanu ndi aŵiri amphamvu padziko lonse okhala ndi tanthauzo lapadera m’Baibulo ndiwo Igupto, Asiriya, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, Roma, ndi mgwirizano wa Britain ndi America. Onseŵa n’ngofunika mwapadera chifukwa achita zinthu zokhudza anthu a Yehova.
b Lemba la Danieli 7:25 limanenanso za nyengo ya nthaŵi pamene ‘opatulika a Wam’mwambamwamba adzalemetsedwa.’ Monga kwafotokozedwa m’mutu wapitawo, zimenezi zinagwirizanitsidwa ndi nkhondo yoyamba ya padziko lonse.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi n’chiyani chikuimiridwa ndi
“nkhosa yamphongo” ya “nyanga ziŵiri”?
“tonde wamanyenje” ndi “nyanga [yake] yaikulu”?
nyanga zinayi zophukira m’malo mwa “nyanga yaikulu”?
nyanga yaing’ono imene inaphuka pa imodzi mwa nyanga zinayi?
• M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, kodi Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America unayesa motani kupululutsa “malo opatulika,” ndipo kodi unapambana?
[Mapu/Chithunzi patsamba 166]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
Ufumu wa Mediya ndi Perisiya
MAKEDONIYA
IGUPTO
Mofi
AITIOPIYA
Yerusalemu
Babulo
Akimeta
Susa
Pesepoli
INDIYA
[Mapu/Chithunzi patsamba 169]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
Ufumu wa Girisi
MAKEDONIYA
IGUPTO
Babulo
Mtsinje wa Indase
[Mapu patsamba 172]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
Ufumu wa Roma
BRITANNIA
ITALIYA
Roma
Yerusalemu
IGUPTO
[Chithunzi chachikulu patsamba 164]
[Zithunzi patsamba 174]
Ena mwa anthu otchuka a Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America:
1. George Washington, pulezidenti woyamba wa America (1789-97)
2. Mfumukazi Victoria ya Britain (1837-1901)
3. Woodrow Wilson, pulezidenti wa America (1913-21)
4. David Lloyd George, nduna yaikulu ya Britain (1916-22)
5. Winston Churchill, nduna yaikulu ya Britain (1940-45, 1951-55)
6. Franklin D. Roosevelt, pulezidenti wa America (1933-45)