“Tapeza Ife Mesiya”!
“Anayamba [Andreya] kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Kristu).”—YOHANE 1:41.
1. Kodi Yohane Mbatizi anachitira umboni za chiyani ponena za Yesu wa ku Nazarete, ndipo kodi Andreya anagamula motani ponena za iye?
ANDREYA anapenda kwanthaŵi yaitali, mosamalitsa mwamuna Wachiyuda wotchedwa Yesu wa ku Nazarete. Iye analibe mawonekedwe a mfumu, kapena a munthu wanzeru, kapena a rabi. Analibe zovala zokongola zachifumu, kapena imvi, kapena manja osalala ndi khungu labwino. Yesu anali wachichepere—wazaka pafupifupi 30 zakubadwa—wokhala ndi manja okhuthala ndi khungu lochindikala la wogwira ntchito yamanja. Chotero Andreya mwina sanadabwe kumva kuti iye anali wopala matabwa. Mosasamala kanthu za zimenezo, Yohane Mbatizi anati ponena za mwamuna ameneyu: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!” Ladzulo lake, Yohane anali atanena kanthu kena kodabwitsa mowonjezereka kuti: “Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.” Kodi zimenezi zikanakhala zowona? Andreya anathera nthaŵi yowonjezereka kumvetsera Yesu tsiku lomwelo. Sitikudziŵa zimene Yesu ananena; tidziŵa kuti mawu ake anasintha moyo wa Andreya. Iye anafulumira kukafunafuna mbale wake, Simoni, ndi kufuula kuti, “Tapeza ife Mesiya”!—Yohane 1:34-41.
2. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulingalira umboni wakuti kaya Yesu anali Mesiya wolonjezedwayo?
2 Andreya ndi Simoni (amene Yesu anamutchanso Petro) pambuyo pake anadzakhala atumwi a Yesu. Pambuyo pazaka zoposa ziŵiri monga ophunzira ake, Petro anati kwa Yesu: “Inu ndinu Kristu [Mesiya], Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Atumwi okhulupirika ndi ophunzirawo potsirizira pake anatsimikizira mofunitsitsa kufera chikhulupiriro chimenecho. Lerolino, anthu owona mtima mamiliyoni ambiri ali odzipereka mofananamo. Koma pa umboni uti? Umboni, ndiiko komwe, umapanga kusiyana pakati pa chikhulupiriro ndi kuvomereza mwaumbuli chabe. (Wonani Ahebri 11:1.) Chotero tiyenitu tilingalire mbali zitatu za umboni zimene zimatsimikizira kuti Yesu analidi Mesiya.
Mzera Wobadwira wa Yesu
3. Kodi Uthenga Wabwino wa Mateyu ndi wa Luka umafotokozanji ponena za mzera wobadwira wa Yesu?
3 Mzera wobadwira wa Yesu ndiwo umboni woyamba umene Malemba Achikristu Achigiriki amapereka mochirikiza kukhala kwake Mesiya. Baibulo linaneneratu kuti Mesiya akadzera mumzera wa banja la Mfumu Davide. (Salmo 132:11, 12; Yesaya 11:1, 10) Uthenga Wabwino wa Mateyu umayamba motere: “Bukhu la kubadwa kwa Yesu Kristu, mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu.” Mateyu akuchirikiza mawu amphamvu ameneŵa mwa kulondola mzera wobadwira wa Yesu mwamzera wa atate wake wolera, Yosefe. (Mateyu 1:1-16) Uthenga Wabwino wa Luka ukulondola mzera wobadwira wa Yesu mwa amake wombala, Mariya, kupitirira Davide ndi Abrahamu mpaka kwa Adamu. (Luka 3:23-38)a Chotero olemba Mauthenga Abwino akulemba momvekera bwino kwambiri chigomeko chawo chakuti Yesu anali wolowa nyumba wa Davide, ponse paŵiri mwalamulo ndi m’lingaliro lachibadwidwe.
4, 5. (a) Kodi amene anakhala ndi moyo m’nthaŵi ya Yesu anatsutsa kukhala kwake mbadwa ya Davide, ndipo kodi nchifukwa ninji zimenezi ziri zofunika? (b) Kodi ndimotani mmene maumboni osakhala Abaibulo amachirikizira mzera wobadwira wa Yesu?
4 Ngakhale wotsutsa koposa wokaikira Yesu kukhala Mesiya sangakane kudzinenera kwa Yesu kukhala mwana wa Davide. Chifukwa ninji? Pali zifukwa ziŵiri. Choyamba, kudzinenera kumeneko kunabwerezedwa mofala kwambiri m’Yerusalemu kwazaka makumi ambiri mzindawo usanawonongedwe mu 70 C.E. (Yerekezerani ndi Mateyu 21:9; Machitidwe 4:27; 5:27, 28.) Ngati kudzinenerako kunali konama, alionse a otsutsa a Yesu—ndipo iye anali ndi ambiri—akanatsimikizira Yesu kukhala chinyengo kokha mwa kupenda mzera wake wobadwira m’malo osungira zinthu zakale a onse.b Koma mbiri yakale iribe cholembedwa cha aliyense wotsutsa Yesu kukhala mbadwa ya Mfumu Davide. Mwachiwonekere, kudzinenerako kunali kosatsutsika. Mosakaikira Mateyu ndi Luka analemba maina otsimikizirika m’zolemba zawo mwachindunji kuchokera m’mabukhu a anthu onsewo.
5 Wachiŵiri, magwero a kunja kwa Baibulo amatsimikizira kuvomerezedwa kwa onse kwa mzera wobadwira wa Yesu. Mwachitsanzo, Talmud ikusimba za rabi wa m’zaka za zana lachinayi kukhala akuukira motukwana Mariya, amayi wa Yesu, kaamba ka ‘kuchita chigololo ndi opala matabwa’; koma ndime imodzimodziyo ikuvomereza kuti “iye [Mariya] anali mbadwa ya mafumu ndi olamulira.” Chitsanzo choyambirira ndicho wolemba mbiri wa m’zaka za zana lachiŵiri Hegesippus. Iye anafotokoza kuti pamene Kaisala wa Roma Domitian anafuna kuwononga mbadwa zirizonse za Davide, adani ena a Akristu oyambirira anatsutsa adzukulu a Yuda, mbale wa Yesu mwa atate wina, “monga a banja la Davide.” Ngati Yuda anadziŵika kukhala mbadwa ya Davide, kodi Yesu nayenso sanali? Nzosakanika!—Agalatiya 1:19; Yuda 1.
Maulosi Aumesiya
6. Kodi maulosi Aumesiya ngochuluka motani m’Malemba Achihebri?
6 Mzera wina wa umboni wakuti Yesu anali Mesiya ndiwo ulosi wokwaniritsidwa. Maulosi amene amagwira ntchito kwa Mesiya ngochuluka m’Malemba Achihebri. M’bukhu lake lakuti The Life and Times of Jesus the Messiah, Alfred Edersheim anasonkhanitsa zigawo 456 za m’Malemba Achihebri zimene arabi a m’nthaŵi zakale anazilingalira kukhala zaumesiya. Komabe, arabiwo anali ndi malingaliro olakwa ambiri onena za Mesiya; zambiri za ndime zimene anasonyako siziri zaumesiya konse. Komano, pali pafupifupi makumi ambiri a maulosi amene amadziŵikitsa Yesu kukhala Mesiya.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 19:10.
7. Kodi ndimaulosi ena ati amene Yesu anakwaniritsa mkati mwa kukhala kwake kwanyengo yochepa padziko lapansi?
7 Pakati pawo pali: mudzi wobadwira (Mika 5:2; Luka 2:4-11); tsoka la kupululutsidwa kwa ana kumene kunachitika pambuyo pa kubadwa kwake (Yeremiya 31:15; Mateyu 2:16-18); iye akaitanidwa ku Igupto (Hoseya 11:1; Mateyu 2:15); olamulira adziko akagwirizana kuti amuwononge (Salmo 2:1, 2; Machitidwe 4:25-28); kuperekedwa kwake ndi ndalama 30 zasiliva (Zekariya 11:12; Mateyu 26:15); ngakhale mtundu wa imfa yake.—Salmo 22:16, NW, mawu amtsinde; Yohane 19:18, 23; 20:25, 27.c
Kufika Kwake Kunanenedweratu
8. (a) Kodi ndiulosi uti umene umasonyeza mwachindunji nthaŵi pamene Mesiya akafika? (b) Kodi ndimbali ziŵiri ziti zimene ziyenera kudziŵidwa kuti timvetsetse ulosi umenewu?
8 Tiyeni tisumike maganizo pa ulosi umodzi wokha. Pa Danieli 9:25, Ayuda anauzidwa nthaŵi pamene Mesiya akadza. Pamati: “Dziŵa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo la kukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masaba makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri.” Pakuwona koyamba ulosi umenewu ungawonekere kukhala wosamvekera bwino. Koma m’lingaliro lokulira, umatifunsira kupeza mbali ziŵiri za chidziŵitso: poyambira ndiponso utali wa nthaŵi. Mwafanizo, ngati munali ndi mapu imene inasonya ku chuma chokwiriridwa “mikwamba 50 kummaŵa kwa chitsime m’paki ya tauni,” mungapeze malowo kukhala osokoneza maganizo—makamaka ngati simunadziwe kumene kunali chitsime chimenechi, kapena kuti ‘mkwamba’ umodzi unali wautali motani. Kodi simukanafunafuna mfundo ziŵiri zimenezo kuti mukhoze kupeza chumacho? Eya, ulosi wa Danieli ngwofanana kwambiri, kusiyapo kuti tifuna kudziŵa nthaŵi yoyambira ndi kuŵerenga nyengo imene ikutsatira.
9, 10. (a) Kodi ndipati poyambira kuŵerenga masabata 69? (b) Kodi masabata 69 anali aatali motani, ndipo kodi ndimotani mmene timadziŵira zimenezi?
9 Choyamba, tifunikira poyambira pathu, deti pamene ‘mawu anatuluka a kukabwezeretsa ndi kumanganso Yerusalemu.’ Ndiyeno, tifunikira kudziŵa utali wa nthaŵi kuyambira panthaŵiyo, kuti masabata 69 (7 kuwonkhetsa 62) ameneŵa anali aatali motani. Alionse a mawuwo siovuta kuwapeza. Nehemiya akutiuza mwachimvekere kwambiri kuti mawu anatuluka a kukamanganso linga lozungulira Yerusalemu, potsirizira pake akumaupangitsa kukhala mzinda wobwezeretsedwa, mu “chaka cha makumi aŵiri cha Aritasasta mfumu.” (Nehemiya 2:1, 5, 7, 8) Zimenezo zimaika poyambira pathu kukhala 455 B.C.E.d
10 Tsopano ponena za masabata 69 ameneŵa, kodi angakhale masabata enieni a masiku asanu ndi aŵiri? Ayi, pakuti Mesiya sanawonekere patapita chaka chimodzi chokha pambuyo pa 455 B.C.E. Motero akatswiri Abaibulo ambiri ndi matembenuzidwe ochuluka (kuphatikizapo Tanakh Yachiyuda m’mawu amtsinde a vesi limeneli) akuvomereza kuti ameneŵa ndimasabata “a zaka.” Lingaliro la ‘masabata a zaka’ limeneli, kapena nyengo ya zaka zisanu ndi ziŵiri zirizonse, linali lozoloŵereka kwa Ayuda a m’nthaŵi zakale. Monga momwe anasungira tsiku lasabata patsiku lachisanu ndi chiŵiri lirilonse, iwo anasunga chaka chasabata pachaka chachisanu ndi chiŵiri chirichonse. (Eksodo 20:8-11; 23:10, 11) Chotero masabata 69 azaka akakhala 69 kuwirikiza zaka 7, kapena zaka 483. Chotsala chokha choti tichite ndicho kuŵerenga. Kuyambira mu 455 B.C.E., kuŵerenga zaka 483 kumatifikitsa m’chaka cha 29 C.E.—chaka chenichenicho chimene Yesu anabatizidwa ndi kukhala ma·shiʹach, Mesiya!—Wonani “Seventy Weeks,” mu Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, tsamba 899.
11. Kodi tingayankhe motani awo amene amanena kuti zimenezi ziri kokha njira yamakono yomasulilira ulosi wa Danieli?
11 Ena angatsutse akumati ameneŵa ali kokha malongosoledwe amakono a ulosiwo kuti uyenererane ndi mbiri yakale. Ngati ziri choncho, kodi nchifukwa ninji anthu m’tsiku la Yesu anali kuyembekezera Mesiya kuwonekera panthaŵi imeneyo? Wolemba mbiri Wachikristu Luka, olemba mbiri Achiroma Tacitus ndi Suetonius, wolemba mbiri Wachiyuda Josephus, ndi wanthanthi Wachiyuda Philo onsewo anakhala ndi moyo pafupifupi panthaŵiyi ndipo anachitira umboni mkhalidwe wa kuyembekezera umenewu. (Luka 3:15) Akatswiri ena lerolino akuumirira kuti chinali chitsenderezo cha Aroma chimene chinapangitsa Ayuda kulakalaka ndi kuyembekezera Mesiya m’masiku amenewo. Komabe, kodi nchifukwa ninji, Ayuda anayembekezera Mesiya panthaŵiyi koposa kutero mkati mwa chizunzo chankhalwe chochitidwa ndi Agiriki zaka mazana angapo pasadakhale? Kodi nchifukwa ninji Tacitus ananena kuti anali “maulosi achinsinsi” amene anapangitsa Ayuda kuyembekezera olamulira amphamvu kudza kuchokera ku Yudeya ndi “kupeza ulamuliro wa padziko lonse”? Abba Hillel Silver, m’bukhu lake lakuti A History of Messianic Speculation in Israel, akuvomereza kuti “Mesiya anayembekezeredwa pafupifupi m’mbali ya nusu yachiŵiri ya zaka za zana loyamba C.E.,” osati chifukwa cha chizunzo chochitidwa ndi Aroma, koma chifukwa cha “kuŵerenga nthaŵi kodziŵika kwa m’nthaŵiyo,” kopezedwa mwapang’ono m’bukhu la Danieli.
Anadziŵikitsidwa Kuchokera Kumwamba
12. Kodi ndimotani mmene Yehova anadziŵikitsira Yesu kukhala Mesiya?
12 Mtundu wachitatu wa umboni wa Yesu kukhala Mesiya ndiwo umboni wa Mulungu iyemwiniyo. Malinga ndi Luka 3:21, 22, Yesu atabatizidwa, iye anadzozedwa ndi nyonga yopatulika koposa ndi yamphamvu koposa m’chilengedwe chonse, mzimu woyera wa Yehova Mulungu iyemwiniyo. Ndipo mwamawu a iyemwini, Yehova anavomereza kuti anali atavomereza Mwana wake, Yesu. Pazochitika zina ziŵiri, Yehova analankhula ndi Yesu mwachindunji ali kumwamba, motero akumasonyeza chivomerezo Chake: kamodzi, pamaso pa atatu a atumwi a Yesu, ndipo panthaŵi ina, pamaso pa khamu la openyerera. (Mateyu 17:1-5; Yohane 12:28, 29) Ndiponso, angelo anatumidwa kuchokera kumwamba kudzatsimikiza malo antchito a Yesu monga Kristu, kapena Mesiya.—Luka 2:10, 11.
13, 14. Kodi Yehova anasonyeza motani chivomerezo chake cha Yesu kukhala Mesiya?
13 Yehova anasonyeza kuvomereza kwake wodzozedwa wake mwa kumpatsa mphamvu yochitira ntchito zazikulu. Mwachitsanzo, Yesu analankhula maulosi amene anafotokoza mwatsatanetsatane mbiri ya zochitika pasadakhale—zina zikumafikira kutsiku lathu.e Iye anachitanso zozizwitsa, zonga kudyetsa makamu anjala ndi kuchiritsa odwala. Iye anaukitsa ngakhale akufa. Kodi otsatira ake anangopeka chabe nkhani za ntchito zamphamvu zimenezi ndiiko komwe? Eya, Yesu anachita zambiri za zozizwitsa zake pamaso pa mboni zowona ndi maso, nthaŵi zina anthu zikwi zambiri panthaŵi imodzi. Ngakhale adani a Yesu sakatha kutsutsa kuti iye anachitadi zinthu zimenezi. (Marko 6:2; Yohane 11:47) Ndiponso, ngati otsatira a Yesu anali ndi chikhoterero cha kupeka zochitika zoterozo, pamenepo kodi nchifukwa ninji iwo akakhala osabisa mawu chotero ponena za zolephera za iwo eni? Kwenikweni, kodi iwo akanakhala ofunitsitsa kufera chikhulupiriro chozikidwa panthanthi wamba zimene iwo eni anali atapeka? Ayi. Zozizwitsa za Yesu ziri zenizeni za m’mbiri.
14 Umboni wa Mulungu wonena za Yesu kukhala Mesiya unaposa pamenepo. Kupyolera mwa mzimu woyera iye anatsimikizira kuti umboni wa Yesu wa kukhala Mesiya unalembedwa ndi kukhala mbali ya bukhu lotembenuzidwa ndi kufalitsidwa mofala koposa m’mbiri yonse.
Kodi Nchifukwa Ninji Ayuda Sanalandire Yesu?
15. (a) Kodi maumboni a Yesu omdziŵikitsa kukhala Mesiya ngambiri motani? (b) Kodi ndiziyembekezo zotani za Ayuda zimene zinachititsa ambiri a iwo kukana Yesu monga Mesiya?
15 Pamenepo, m’zonsezo, mbali zitatu zimenezi za umboni zimaphatikizapo mfundo mazana enieni ambiri zimene zimadziŵikitsa Yesu kukhala Mesiya. Kodi zimenezo sizokwanira? Tangoyerekezerani kuti mukufunsira laisensi yoyendetsera galimoto kapena khadi lotengera zinthu mwangongole ndi kuuzidwa kuti ziphaso zodziŵikitsira zitatu sizinali zokwanira—muyenera kubweretsa mazana ambiri. Nkusalingalira chotani nanga! Pamenepa, ndithudi, Yesu akudziŵikitsidwa mokwanira m’Baibulo. Pamenepa, kodi nchifukwa ninji, ambiri a anthu a mtundu wa Yesu mwiniyo anakana umboni wonsewu wakuti iye anali Mesiya? Chifukwa chakuti umboni, ngakhale kuti ngwofunika kwambiri kaamba ka chikhulupiriro chowona, sumatsimikizira chikhulupiriro. Mwachisoni, anthu ambiri amakhulupirira zimene afuna kukhulupirira, ngakhale ngati pali umboni wochuluka kwambiri. Ponena za Mesiya, Ayuda ambiri anali ndi malingaliro otsimikizirika onena za zimene anafuna. Iwo anafuna mesiya wandale zadziko, uyo amene akathetsa kutsendereza kwa Aroma ndi kubwezeretsa Israyeli kuulemerero wofanana m’njira yakuthupi ndi uja wa m’masiku a Solomo. Pamenepa, kodi ndimotani, mmene akavomerezera mwana wa wopala matabwa waumphaŵi, Mnazara ameneyu amene sanasonyeze chikondwerero chirichonse m’ndale zadziko kapena m’zachuma? Kodi ndimotani mmene, kwakukulukulu, iye akakhalira Mesiya pambuyo pa kuvutika ndi kufa imfa yochititsa manyazi pamtengo wozunzirapo?
16. Kodi nchifukwa ninji otsatira a Yesu anafunikira kusintha ziyembekezo za iwo eni ponena za Mesiya?
16 Ophunzira a Yesu enieniwo anavutika maganizo ndi imfa yake. Pambuyo pa kuuka kwake kwaulemerero, iwo mwachiwonekere anayembekezera kuti iye ‘akabwezeretsa ufumu kwa Israyeli’ panthaŵi yomweyo. (Machitidwe 1:6) Koma iwo sanakane Yesu kukhala Mesiya kokha chifukwa chakuti chiyembekezo chaumwini chimenechi sichinakwaniritsidwe. Iwo anaikabe chikhulupiriro mwa iye chozikidwa pa umboni wokwanira wopezeka, ndipo kuzindikira kwawo kunakula mwapang’onopang’ono; zinsinsi zinavumbuluka. Iwo anafikira powona kuti Mesiya sakatha kukwaniritsa maulosi onse onena za iye mkati mwa nthaŵi yake yaifupi monga munthu padziko lapansi lino. Eya, ulosi umodzi unalankhula za kudza kwake monga munthu wodzichepetsa, wokwera pamwana wa bulu, pamene wina unalankhula za kudza kwake muulemerero ali m’mitambo! Kodi onse aŵiri akakhala owona motani? Mwachiwonekere iye akafunikira kudza kwanthaŵi yachiŵiri.—Danieli 7:13; Zekariya 9:9.
Chifukwa Chake Mesiya Anafunikira Kufa
17. Kodi ndimotani mmene ulosi wa Danieli unamveketsera bwino kuti Mesiya akafunikira kufa, ndipo kodi nchifukwa ninji iye akafa?
17 Ndiponso, maulosi Aumesiya anamveketsa bwino lomwe kuti Mesiya anafunikira kufa. Mwachitsanzo, ulosi weniweniwo umene unaneneratu nthaŵi pamene Mesiya akadza unaneneratu m’vesi lotsatira kuti: “Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri, [amene anatsatira masabata asanu ndi aŵiri] wodzozedwayo adzalikhidwa.” (Danieli 9:26) Liwu Lachihebri lakuti ka·rathʹ logwiritsiridwa ntchito panopa kaamba ka “likhidwa” ndilo liwu limodzimodzi limene limagwiritsiridwa ntchito kaamba ka chilango cha imfa m’Chilamulo cha Mose. Mosakaikira Mesiyayo anafunikira kufa. Chifukwa ninji? Vesi 24 likutipatsa yankho kuti: “Kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza.” Ayuda anadziŵa bwino lomwe kuti nsembe yokha, imfa, ikakhoza kupanga chotetezera machimo.—Levitiko 17:11; yerekezerani ndi Ahebri 9:22.
18. (a) Kodi ndimotani mmene Yesaya chaputala 53 amasonyezera kuti Mesiya ayenera kuvutika ndi kufa? (b) Kodi nzowonekera kukhala kudzitsutsa zotani zimene ulosi umenewu umadzutsa?
18 Yesaya chaputala 53 amalankhula za Mesiya kukhala Mtumiki wapadera wa Yehova amene akafunikira kuvutika ndi kufa kukwirira machimo a ena. Vesi 5 limati: “Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu.” Ulosi umodzimodziwo, pambuyo pa kutiuza kuti Mesiya ameneyu anayenera kufa monga “nsembe yopalamula,” umavumbula kuti Munthu mmodzimodziyu “adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m’manja mwake.” (Vesi 10) Kodi zimenezo siziri kudzitsutsa? Kodi ndimotani mmene Mesiya akanafera, ndiyeno ‘nkutanimphitsa masiku ake’? Kodi ndimotani mmene akanaperekedwera monga nsembe ndiyeno pambuyo pake kupanga ‘chomkondweretsa Yehova kukhala chachipambano’? Ndithudi, kodi ndimotani mmene, iye akanafera ndi kukhalabe wakufa popanda kukwaniritsa maulosi ofunika kopambana onena za iye, ndiko kuti kuti akalamulira kosatha monga Mfumu ndi kubweretsa mtendere ndi chimwemwe kudziko lonse lathunthu?—Yesaya 9:6, 7.
19. Kodi chiukiriro cha Yesu chimagwirizanitsa motani maulosi owonekera kukhala odzitsutsa onena za Mesiya?
19 Kuwonekera kukhala kudzitsutsa kumeneku kunamveketsedwa bwino mwachozizwitsa chimodzi, chachilendo. Yesu anaukitsidwa. Ayuda owona mtima mazana ambiri anafikira kukhala mboni zowona ndi maso za chochitika chaulemerero chimenechi. (1 Akorinto 15:6) Mtumwi Paulo pambuyo pake analemba kuti: “[Yesu Kristu] adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando ku mapazi ake.” (Ahebri 10:10, 12, 13) Inde, kunali pambuyo poti Yesu waukitsidwira kumoyo wakumwamba, ndi pambuyo pa nyengo ya ‘kulindirira,’ kuti iye potsirizira pake akaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ndi kuchitapo kanthu motsutsana ndi adani a Atate wake, Yehova. M’mbali yake monga Mfumu yakumwamba, Yesu Mesiyayo amayambukira moyo wa munthu aliyense amene tsopano ali ndi moyo. M’njira yotani? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Pamene Luka 3:23 amati: “Yosefe, mwana wa Heli,” mwachiwonekere amatanthauza “mwana” m’lingaliro la kukhala “mpongozi,” popeza kuti Heli anali atate weniweni wa Mariya.—Insight on the Scriptures, Voliyamu 1, tsamba 913-17.
b Wolemba mbiri yakale Wachiyuda Josephus, popereka mzera wake wobadwira, akumveketsa bwino kuti zolembedwa zoterozo zinali zopezeka chaka cha 70 C.E. chisanafike. Zolembedwa zimenezi mwachiwonekere zinawonongedwera limodzi ndi mzinda wa Yerusalemu, zikumapangitsa zodzinenera kukhala Mesiya zonse zapambuyo pake kukhala zosakhoza kutsimikiziridwa.
c Wonani Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, tsamba 387.
Achibabulo, ndi Achiperisiya osonyeza kuti chaka chimene Aritasasta anayamba kulamulira chinali 474 B.C.E. Wonani Insight on the Scriptures, Voliyamu 2, tsamba 614-16, 900.
d Pali umboni wamphamvu wochokera m’mabukhu akale Achigiriki,
e Muulosi umodzi woterowo, iye ananeneratu kuti amesiya onama akabuka kuyambira m’tsiku lake kumkabe mtsogolo. (Mateyu 24:23-26) Wonani nkhani yapitayo.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nkupenderanji umboni wakuti kaya Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa?
◻ Kodi ndimotani mmene mzera wobadwira wa Yesu umachirikizira kukhala kwake Mesiya?
◻ Kodi ndimotani mmene maulosi Abaibulo amathandizira kutsimikizira kuti Yesu anali Mesiya?
◻ Kodi ndimnjira zotani zimene Yehova iyemwini anatsimikizirira kudziŵika kwa Yesu kwa kukhala Mesiya?
◻ Kodi nchifukwa ninji Ayuda ambiri anakana Yesu monga Mesiya, ndipo kodi nchifukwa ninji zifukwa zimenezi sizinali zomveka?
[Chithunzi patsamba 12]
Chirichonse cha zozizwitsa za Yesu chinapereka umboni wowonjezereka wa kukhala kwake Mesiya