Mutu 13
Mafumu Aŵiri Olimbana
1, 2. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi pa ulosi wolembedwa m’buku la Danieli chaputala 11?
MAFUMU aŵiri odana akukangana koopsa polimbanira ukulu. M’kupita kwa zaka, yoyambayo ipambana, kenako inayo ipambananso. Nthaŵi zina, mfumu imodzi ilamulira pamene inayo izilala, komanso pakukhala nyengo zimene mkanganowo ukuchita ngati watha. Kenako nkhondoyo ibukanso mwadzidzidzi, ndipo mkanganowo upitirira. Mwa amene atenga nawo mbali m’kulimbanaku pali Selukasi 1 Niketa Mfumu ya Suriya, Tolemi Lagasi Mfumu ya Igupto, Kileopatiya 1 mwana wa Mfumu ya Suriya amene anadzakhalanso Mfumukazi ya Igupto, Augusto ndi Tiberiyo Mafumu aakulu a Roma, komanso Zenobia Mfumukazi ya Palimelia. Pamene mkanganowo ukufika kumapeto ake, Germany wolamulidwa ndi chipani cha Nazi, mayiko a Komyunizimu, Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America, mabungwe a League of Nations ndi United Nations, onsewo atenga nawo mbali. Chochitika chomalizira n’chosadziŵika kwa lililonse la magulu andale ameneŵa. Mngelo wa Yehova analengeza ulosi wochititsa chidwi umenewu kwa mneneri Danieli zaka pafupifupi 2,500 zapitazo.—Danieli, chaputala 11.
2 Danieli ayenera kuti anasangalala kwabasi pakumva mngelo akumuululira tsatanetsatane wa mkangano wa pakati pa mafumu aŵiri alinkudza! Chochitikacho n’chochititsa chidwi kwa ifenso, pakuti kulimbanira ulamuliroko pakati pa mafumu aŵiriwo kumafika mpaka m’nthaŵi yathu ino. Kuona mmene mbiri yasonyezera kukwaniritsidwa kwa mbali yoyamba ya ulosiwo kudzalimbikitsa chikhulupiriro ndi chidaliro chathu pa kukwaniritsidwa kwa mbali yomaliza ya ulosiwo. Kupenda ulosi umenewu kudzatipatsa chithunzi chabwino cha nthaŵi imene tikukhala. Kudzatipangitsanso kukhala otsimikiza mtima kwambiri za kusatenga mbali pamkanganowo pamene tikuyembekezera moleza mtima kuti Mulungu adzatichitirepo kanthu. (Salmo 146:3, 5) Choncho, ndi chidwi chenicheni, tiyeni titchere khutu pamene mngelo wa Yehova alankhula kwa Danieli.
AUKIRA UFUMU WA GIRISI
3. Kodi mngelo anachirikiza ndani mu “chaka choyamba cha Dariyo Mmedi”?
3 “Ndipo ine,” anatero mngeloyo, “chaka choyamba cha Dariyo Mmedi [539 kapena 538 B.C.E.], ndinauka kum’limbikitsa ndi kum’khazikitsa.” (Danieli 11:1) Dariyo sanaliponso ndi moyo, koma mngeloyo anatchula ulamuliro wake monga poyambira uthenga waulosiwo. Dariyo ndiye mfumu imene inalamula kuti Danieli atulutsidwe m’dzenje la mikango. Analinso Dariyo amene analamula kuti anthu onse aope Mulungu wa Danieli. (Danieli 6:21-27) Komabe, amene mngeloyo anam’limbitsa, sanali Dariyo Mmedi, koma Mikaeli, mnzake wa mngeloyo—kalonga wa anthu a Danieli. (Yerekezani ndi Danieli 10:12-14.) Mngelo wa Mulungu anapereka chichirikizo chimenechi pamene Mikaeli anali kulimbana ndi kalonga wauchiŵanda wa Mediya ndi Perisiya.
4, 5. Kodi mafumu anayi a Perisiya onenedweratuwo anali ndani?
4 Mngelo wa Mulungu anapitiriza nati: “Taona, adzaukanso mafumu atatu m’Perisiya, ndi yachinayi idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nawo ufumu wa Helene [“Girisi,” NW].” (Danieli 11:2) Kodi mafumu a Perisiya ameneŵa anali ndani?
5 Mafumu atatu oyambirira anali Koresi Wamkulu, Kambisesi 2, ndi Dariyo 1. Popeza kuti Baradiya (kapena wonamizira wotchedwa Gomatala) analamulira miyezi isanu ndi iŵiri yokha, ulosiwo sunaphatikizepo ulamuliro wake waufupiwo. Mu 490 B.C.E., mfumu yachitatu, Dariyo 1, anayesa kulanda Girisi kachiŵiri. Komabe, Aperisiwo anagonjetsedwa ku Maratoni ndipo anabwerera ku Asiyamina. Ngakhale kuti Dariyo anakonzekera mwakhama nkhondo yam’tsogolo yodzalimbana ndi Girisi, sanaimenye chifukwa anamwalira patapita zaka zinayi. Nkhondoyo tsopano inatsala m’manja mwa mwana wake amene anam’loŵa m’malo, mfumu “yachinayi” Sasta 1. Iyeyo anali mfumu Ahaswero yemwe anadzakwatira Estere.—Estere 1:1; 2:15-17.
6, 7. (a) Kodi mfumu yachinayi ‘inautsa motani onse kuti alimbane ndi ufumu wa Girisi’? (b) Kodi zotsatira zake zinali zotani pamene Sasta anaukira Girisi?
6 Sasta 1 ‘anautsadi onse kuti alimbane nawo ufumu wa Girisi,’ ndiko kuti, gulu la maboma achigiriki odzilamulira. “Posonkhezeredwa ndi anyamata ake ofuna malo apamwamba,” limatero buku lakuti The Medes and Persians—Conquerors and Diplomats, “Sasta anayamba nkhondo kumtunda ndi panyanja.” Mgiriki wolemba mbiri yakale, Herodito, wa m’zaka za zana lachisanu B.C.E., analemba kuti “sipanakhalepo ndawala ya nkhondo yoposa imeneyi.” Zolemba zake zimasonyeza kuti asilikali apanyanja “anali amuna okwanira 517,610. Asilikali oyenda pansi anali 1,700,000; apamahachi anali 80,000; panalinso Aarabu oyendera pangamila, komanso Alibiya amene ankamenyera nkhondo pamagaleta, omwe anali ngati 20,000. Choncho, chiwonkhetso chonse cha asilikali akumtunda ndi apanyanja chinali amuna 2,317,610.”
7 Atakonzekera chigonjetso chowamaliziratu, Sasta 1 ananyamuka ndi chikhamu chake cha asilikali kuti akathane ndi Girisi mu 480 B.C.E. Ponyalanyaza machenjera a Girisi ofuna kuwachenjeneka ku Tempiliya, Aperisiwo anasakaziratu mzinda wa Atene. Koma atafika ku Salami, anagonjetsedwa koopsa. Agiriki anapambananso nkhondo ku Palatiya, mu 479 B.C.E. Palibe aliyense wa mafumu asanu ndi aŵiri oloŵa m’malo pampando wachifumu wa Sasta, mu Ufumu waukulu wa Perisiya, m’kati mwa zaka 143 zotsatirapo, amene analanda Girisi. Koma panauka mfumu ina yamphamvu m’Girisi.
UFUMU WAUKULU UGAŴIKA PANAYI
8. Kodi “mfumu yamphamvu” imene inauka ndani, ndipo ndi motani mmene ‘inachitira ufumu ndi ulamuliro waukulu’?
8 “Idzauka mfumu yamphamvu, nidzachita ufumu ndi ulamuliro waukulu, nidzachita monga mwa chifuniro chake,” anatero mngeloyo. (Danieli 11:3) Alesandro wa zaka 22 ‘anauka’ monga mfumu ya Makedoniya mu 336 B.C.E. Iye anakhaladi “mfumu yamphamvu”—Alesandro Wamkulu. Posonkhezereka ndi mapulani a bambo wake, Filipo 2, analanda madera a Perisiya a ku Middle East. Atawoloka mitsinje ya Firate ndi Tigirisi, asilikali ake okwanira 47,000 okha anabalalitsa asilikali a Dariyo 3 okwanira 250,000 ku Gogamela. Kenako, Dariyo anathaŵa koma anaphedwa, kumaliza mzera wa mafumu achiperisiya. Girisi tsopano anakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse, ndipo Alesandro ‘anachita ufumu ndi ulamuliro waukulu, nachita monga mwa chifuniro chake.’
9, 10. Kodi ulosi wakuti ufumu wa Alesandro sudzasiyidwira mbumba yake unakwaniritsidwa motani?
9 Ulamuliro wa Alesandro wa dziko lonse unali wakanthaŵi, pakuti mngelo wa Mulungu anawonjezera kuti: “Pakuuka iye ufumu wake udzathyoledwa, nudzagaŵikira ku mphepo zinayi za mlengalenga; koma sadzaulandira a mbumba yake akudza m’mbuyo, kapena monga mwa ulamuliro wake anachita ufumu nawo; pakuti ufumu wake udzazulidwa, ukhale wa ena, si wa aja ayi.” (Danieli 11:4) Alesandro sanafikire kwenikweni zaka 33 pamene anadwala mwadzidzidzi ndi kumwalira ali ku Babulo mu 323 B.C.E.
10 Ufumu wa Alesandro waukuluwo sunasiyidwire “mbumba yake.” Mbale wake Filipo 3 Arideyo analamulira zaka zosakwanira zisanu ndi ziŵiri kenako anaphedwa atam’konzera chiwembu Olimpiyasi, mayi wake wa Alesandro, mu 317 B.C.E. Alesandro 4, mwana wa Alesandro, analamulira mpaka 311 B.C.E pamene anaphedwa ndi Kasanda, mmodzi wa akazembe a bambo wake. Elakule, mwana wapathengo wa Alesandro, anayesa kulamulira m’dzina la atate wake koma anaphedwa mu 309 B.C.E. Ameneŵa ndiwo anali mapeto a mzera wa mafumu wa Alesandro, “ulamuliro wake” unachoka pabanja lake.
11. Ndi motani mmene ufumu wa Alesandro ‘unagaŵikira ku mphepo zinayi za mlengalenga’?
11 Alesandro atamwalira, ufumu wake ‘unagaŵikira ku mphepo zinayi za mlengalenga.’ Akazembe ake ambiri ankhondo anakangana pakati pawo polimbanira madera. Kazembe Antigonasi 1, wa diso limodzi, anayesa kuika ufumu wonse wa Alesandro pansi pa ulamuliro wake. Koma anaphedwa pankhondo ku Isasi ku Frugiya. Pofika chaka cha 301 B.C.E., anayi mwa akazembe a Alesandro anayamba kulamulira chigawo chachikulucho chimene mtsogoleri wawo anagonjetsa. Kasanda analamulira Makedoniya ndi Girisi. Lasamekase analamulira Asiyamina ndi Thiresi. Selukasi 1 Niketa anatenga Mesopotamiya ndi Suriya. Ndipo Tolemi Lagasi anatenga Igupto ndi Palesitina. Malinga n’kunena kwa ulosi, ufumu waukuluwo wa Alesandro unagaŵika kukhala maufumu anayi achihelene.
MAFUMU AŴIRI ODANA AONEKERA
12, 13. (a) Kodi maufumu anayi achihelene anachepa motani kuti atsale aŵiri? (b) Kodi Selukasi anakhazikitsa mzera wa mafumu wotani mu Suriya?
12 Atalamulira zaka zochepa, Kasanda anamwalira, ndipo mu 285 B.C.E., Lasamekase anatenga gawo la ku Ulaya la Ufumu waukulu wa Girisi. Mu 281 B.C.E., Lasamekase anaphedwa pankhondo yolimbana ndi Selukasi 1 Niketa, ndipo Selukasi anayamba kulamulira chigawo chachikulu cha madera a ku Asiya. Antigonasi 2 Gonatasi, mdzukulu wa mmodzi wa akazembe a Alesandro, anakhala mfumu ya Makedoniya mu 276 B.C.E. M’kupita kwa nthaŵi, Makedoniya anadalira Roma ndipo potsirizira pake anakhaliratu chigawo cha Roma mu 146 B.C.E.
13 Aŵiri okha pa maufumu anayi achihelene ndiwo anatsalapo—wina wolamulidwa ndi Selukasi 1 Niketa ndi winawo wolamulidwa ndi Tolemi Lagasi. Selukasi anakhazikitsa mzera wa mafumu achiselukasi ku Suriya. Pakati pa mizinda imene anaikhazikitsa panali Antiokeya—likulu latsopano la Suriya—ndi mzinda wakudoko wa Selukeya. Panthaŵi ina, mtumwi Paulo anadzaphunzitsa ku Antiokeya, kumene otsatira a Yesu anatchedwa Akristu kwa nthaŵi yoyamba. (Machitidwe 11:25, 26; 13:1-4) Selukasi anaphedwa mu 281 B.C.E., koma mzera wa mafumu a nyumba yake unalamulirabe mpaka 64 B.C.E. pamene Kazembe wachiroma Nayasi Pompeyi anatenga Suriya kukhala chigawo cha Roma.
14. Kodi mzera wa mafumu achitolemi unakhazikitsidwa liti mu Igupto?
14 Ufumu wachihelene umene unakhalitsa pa anayiwo unali wa Tolemi Lagasi, kapena Tolemi 1, amene analongedwa ufumu mu 305 B.C.E. Mzera wa mafumu achitolemi umene iye anaukhazikitsa unalamulira Igupto kufikira pamene Igupto anagonjetsedwa ndi Roma mu 30 B.C.E.
15. Ndi mafumu aŵiri ati amphamvu amene anatuluka m’maufumu anayi achihelene, ndipo anayambitsa mkangano wotani?
15 Choncho, mwa maufumu anayi achihelene, munatuluka mafumu amphamvu aŵiri—Selukasi 1 Niketa yemwe analamulira Suriya komanso Tolemi 1 yemwe analamulira Igupto. Pa mafumu aŵiri ameneŵa m’pamene panayambira mkangano wa nthaŵi yaitali pakati pa “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera,” wofotokozedwa m’Danieli chaputala 11. Mngelo wa Yehova sanatchule mayina a mafumuwo, chifukwa mayina ndi mitundu ya mafumu aŵiriwo inayenera kusintha m’zaka mazana ambiri. Atasiya mbali zosafunikira kwenikweni, mngeloyo anangotchula olamulira ndi zochitika zokhudzana ndi mkangano wawowo.
MKANGANOWO UYAMBIKA
16. (a) Kodi mafumu aŵiriwo anali kumpoto ndi kumwera kwa ndani? (b) Kodi ndi mafumu ati anali oyamba kutenga malo a “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera”?
16 Tamverani! Pofotokoza chiyambi cha mkangano woopsa umenewu, mngelo wa Yehova akuti: “Mfumu ya kumwera, ndiye wina wa akalonga ake [a Alesandro], idzam’posa mphamvu, nidzakhala nawo ulamuliro [mfumu ya kumpoto]; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu.” (Danieli 11:5) Mawu akuti “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera” amanena za mafumu okhala kumpoto ndi kumwera kwa anthu a Danieli, amene panthaŵiyo anamasuka ku ukapolo wa ku Babulo ndi kubwerera kudziko lakwawo la Yuda. “Mfumu ya kumwera” yoyambirira inali Tolemi 1 wa ku Igupto. Mmodzi wa akazembe a Alesandro amene anagonjetsa Tolemi 1 ndi kuchita “ulamuliro waukulu” anali Selukasi 1 Niketa, Mfumu ya Suriya. Iye anakhala “mfumu ya kumpoto.”
17. Kodi dziko la Yuda linali pansi pa ulamuliro wa ndani pamene unayambika mkangano wa pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera?
17 Pamene mkanganowo unayamba, dziko la Yuda linali pansi pa ulamuliro wa mfumu ya kumwera. Kuyambira pafupifupi 320 B.C.E., Tolemi 1 analimbikitsa Ayuda kupita ku Igupto monga olamulidwa ndi boma lachitsamunda. Ayuda obwerawo anachuluka mu Alesandriya, kumene Tolemi 1 anakhazikitsa laibulale yotchuka kwambiri. Ayuda a ku dziko la Yuda analamulidwabe ndi Igupto wa Tolemi, mfumu ya kumwera, mpaka 198 B.C.E.
18, 19. M’kupita kwa nthaŵi, kodi mafumu aŵiri odanawo analoŵa motani mu ‘pangano loyenera’?
18 Ponena za mafumu aŵiriwo, mngeloyo analosera kuti: “Pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anam’bala, ndi iye amene anam’limbitsa nthaŵi zija.” (Danieli 11:6) Kodi zimenezi zinachitika motani?
19 Ulosiwo sunaphatikizepo Antiyokasi 1, woloŵa m’malo mwa bambo wake Selukasi 1 Niketa, chifukwa sanamenyepo nkhondo yaikulu yolimbana ndi mfumu ya kumwera. Koma wom’loŵa m’malo, Antiyokasi 2, anamenya nkhondo ya nthaŵi yaitali yolimbana ndi Tolemi 2, mwana wa Tolemi 1. Antiyokasi 2 anali mfumu ya kumpoto pamene Tolemi 2 anali mfumu ya kumwera. Antiyokasi 2 anakwatira Lodise, ndipo anabereka mwana wamwamuna dzina lake Selukasi 2, pamene Tolemi 2 anabereka mwana wamkazi dzina lake Berinasi. Mu 250 B.C.E., mafumu aŵiriŵa ‘anapangana zoyenera.’ Pofuna kupereka malipiro a mgwirizanowu, Antiyokasi 2 anasudzula mkazi wake Lodise ndi kukwatira Berinasi, “mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera.” Mwa Berinasi, anabereka mwana wamwamuna amene anadzakhala pampando wachifumu wa Suriya m’malo mwa ana a Lodise.
20. (a) Kodi “dzanja” la Berinasi linalephera motani kuima? (b) Kodi Berinasi, “iwo adadza naye,” komanso ‘iye amene anam’limbitsa’ anaperekedwa motani? (c) Kodi ndani anakhala mfumu ya Suriya pamene Antiyokasi 2 anataya “dzanja lake,” kapena mphamvu yake?
20 “Dzanja” la Berinasi, kapena mphamvu yom’chirikiza, anali bambo wake, Tolemi 2. Bambo wakeyo atamwalira mu 246 B.C.E., iye ‘sanaisunge mphamvu ya dzanja lake’ kwa mwamuna wake. Antiyokasi 2 anam’kana mkaziyo, ndi kukwatiranso Lodise, nasankhiratu mwana wawo wodzam’loŵa m’malo. Malinga ndi chiwembu chimene Lodise anakonza, Berinasi anaphedwa limodzi ndi mwana wakeyo. Mwachionekere, akalinde amene anabweretsa Berinasi ku Suriya kuchokera ku Igupto—“iwo adadza naye”—anaphedwanso. Lodise anathiriranso mankhwala Antiyokasi 2, choncho ‘dzanja lakenso,’ kapena mphamvu yake, ‘silinaime.’ Motero, bambo wa Berinasi—“iye amene anam’bala”—ndi mwamuna wake Msuriya—amene ‘anam’limbitsa’ pakanthaŵi—anafa onse. Selukasi 2, mwana wa Lodise, ndiye anatsala monga mfumu ya Suriya. Kodi mfumu Tolemi yotsatira inachitapo chiyani poona zonsezi?
MFUMU IBWEZERA IMFA YA MLONGO WAKE
21. (a) Ndani anali ‘wophukira’ kuchokera ku “mizu” ya Berinasi, ndipo ‘anauka’ motani? (b) Kodi Tolemi 3 ‘anafika motani kulimbana ndi linga la mfumu ya kumpoto’ ndi kuigonjetsa?
21 “Pophukira mizu yake adzauka wina m’malo mwake,” anatero mngeloyo, “ndiye adzafika kulimbana nalo khamu lankhondo, nadzaloŵa m’linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nawo, nadzawalaka.” (Danieli 11:7) ‘Wophukirayo’ kuchokera kwa makolo a Berinasi, kapena “mizu,” anali mlongo wake. Pa imfa ya bambo wake, iye ‘anaima’ monga mfumu ya kumwera, Farao Tolemi 3 wa ku Igupto. Nthaŵi yomweyo ananyamuka kuti akabwezere imfa ya mlongo wake. Ali paulendo wokaonetsana ndi Mfumu ya Suriya Selukasi 2, imene Lodise anaigwiritsa ntchito pakupha Berinasi ndi mwana wake, anaukira “linga la mfumu ya kumpoto.” Tolemi 3 analanda linga la Antiokeya ndi kupha Lodise. Poloŵera chakum’maŵa kudzera m’dziko la mfumu ya kumpoto, anafunkha Babuloniya napitirira mpaka ku Indiya.
22. Kodi Tolemi 3 anabwezera chiyani ku Igupto, ndipo n’chifukwa chiyani ‘anasiya kulimbana ndi mfumu ya kumpoto pazaka zina’?
22 Kenako chinachitika n’chiyani? Mngelo wa Mulungu akutiuza kuti: “Ndi milungu yawo yomwe, pamodzi ndi akalonga awo [“mafano awo oyenga,” NW], ndi zipangizo zawo zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zake zidzaposa za mfumu ya kumpoto [“ndipo adzasiya kulimbana ndi mfumu ya kumpoto pazaka zina,” NW].” (Danieli 11:8) Zoposa zaka 200 m’mbuyomo, Mfumu ya Perisiya Kambisesi 2 inagonjetsa ndi kutengera kwawo milungu ya Aigupto, “mafano awo oyenga.” Pofunkha mzinda wa Susa, likulu lakale la Perisiya, Tolemi 3 anapezanso milungu yakwawo imeneyi naitenga ‘ndende’ ku Igupto. Anabwerakonso ndi zofunkha zambiri “zipangizo . . . zofunika za siliva ndi golidi.” Atabwerera kuti akathetse chipanduko chimene chinabuka kumudzi, Tolemi 3 ‘anasiya kulimbana ndi mfumu ya kumpoto,’ osaivulazanso.
MFUMU YA SURIYA IBWEZERA
23. N’chifukwa chiyani mfumu ya kumpoto ‘inabwerera kudziko lakelake’ itakaloŵa mu ufumu wa mfumu ya kumwera?
23 Kodi mfumu ya kumpoto inachita motani? Danieli anauzidwa kuti: “Adzaloŵa mu ufumu wa mfumu ya kumwera, koma adzabwera m’dziko lakelake.” (Danieli 11:9) Mfumu ya kumpoto—Mfumu ya Suriya Selukasi 2—inafuna kubwezera. Analoŵa mu ‘ufumuwo,’ kapena dziko, la mfumu ya kumwera ya Igupto koma anagonjetsedwa. Atangotsala ndi asilikali ochepa, Selukasi 2 ‘anabwerera ku dziko lakelake,’ ku Antiokeya, likulu la Suriya cha m’ma 242 B.C.E. Atamwalira, mwana wake Selukasi 3 analoŵa m’malo mwake.
24. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kwa Selukasi 3? (b) Ndi motani mmene Mfumu ya Suriya Antiyokasi 3 ‘inadzaloŵera, ndi kusefukira, ndi kupita’ m’dziko la mfumu ya kumwera?
24 Kodi ulosi unaneneratu chiyani za mphukira ya Mfumu ya Suriya Selukasi 2? Mngeloyo anauza Danieli kuti: “Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo aakulu ochuluka, amene adzaloŵa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake.” (Danieli 11:10) Ulamuliro wa Selukasi 3 unatha pamene iye anaphedwa asanalamulire zaka zitatu. Mbale wake, Antiyokasi 3, anam’loŵa m’malo pampando wachifumu wa Suriya. Mwana ameneyu wa Selukasi 2 anasonkhanitsa khamu lalikulu la asilikali kuti akalimbane ndi mfumu ya kumwera, imene panthaŵiyo inali Tolemi 4. Mfumu ya kumpoto yatsopanoyo ya Suriya inapambana polimbana ndi Igupto ndi kulandanso mzinda wa kudoko wa Selukeya, chigawo cha Kolesuriya, mizinda ya Turo ndi Tolemayi, ndi matauni ena apafupi. Anapitikitsa asilikali a Mfumu Tolemi 4 ndi kulanda mizinda yambiri ya Yuda. M’chilimwe cha 217 B.C.E., Antiyokasi 3 anachoka ku Tolemayi naloŵera kumpoto, ‘mpaka ku linga lake’ ku Suriya. Koma kusintha kunali pafupi.
ZINTHU ZITEMBENUKA
25. Kodi n’kuti kumene Tolemi 4 anakumana pankhondo ndi Antiyokasi 3, ndipo n’chiyani ‘chinaperekedwa m’dzanja’ la mfumu ya kumwera ya Igupto?
25 Mofanana ndi Danieli, tiyeni titchere khutu pamene mngelo wa Yehova aneneratu izi: ‘Mfumu ya kumwera idzaŵaŵidwa mtima, nidzatuluka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukulu; koma unyinjiwo udzaperekedwa m’dzanja lake.’ (Danieli 11:11) Atasonkhanitsa asilikali 75,000, Tolemi 4, monga mfumu ya kumwera, analoŵera kumpoto kukalimbana ndi mdani wake. Antiyokasi 3, mfumu ya kumpoto ya Suriya, anasonkhanitsanso “unyinji waukulu” wa asilikali 68,000 kuti akathane naye. Koma ‘unyinjiwo unaperekedwa m’dzanja’ la mfumu ya kumwera pankhondo ya kumzinda wa kudoko wa Rafia, pafupi ndi malire a Igupto.
26. (a) Kodi ndi “unyinji” wotani umene unachotsedwa ndi mfumu ya kumwera pankhondo ya ku Rafia, ndipo anamvana zotani m’pangano lawo la mtendere? (b) N’chifukwa chiyani Tolemi 4 ‘sanalakike’ mopitirira? (c) Ndani anakhala mfumu ya kumwera yotsatira?
26 Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzalakika.” (Danieli 11:12) Tolemi 4, mfumu ya kumwera, ‘inachotsa’ asilikali achisuriya oyenda pansi okwanira 10,000 ndi apamahachi 300 mwa kuwapha, ndipo anagwira andende 4,000. Pamenepo mafumuwo anapanga pangano la mtendere mmene anagwirizana kuti Antiyokasi 3 atenge doko lake la ku Suriya la Selukeya koma apereke mizinda ya Foinike ndi Kolesuriya. Chifukwa cha chipambano chimenechi, mtima wa mfumu ya kumwera ya Igupto ‘unakwezeka,’ makamaka motsutsana ndi Yehova. Yuda anakhalabe pansi pa ulamuliro wa Tolemi 4. Komabe, iye ‘sanalakike’ mopitirira pambuyo pogonjetsa mfumu yakumpoto ya Suriya. M’malo mwake, Tolemi 4 anatembenukira ku moyo wosadzisunga, ndipo mwana wake wa zaka zisanu, Tolemi 5, anakhaliratu mfumu ya kumwera zaka zambiri asanafe Antiyokasi 3.
NGWAZIYO IBWERANSO
27. Kodi mfumu ya kumpoto inabwerera motani “pa chimaliziro cha nthaŵi” kukalandanso madera kwa Igupto?
27 Chifukwa cha zipambano zake zonse, Antiyokasi 3 anatchedwa Antiyokasi Wamkulu. Ponena za iye, mngeloyo anati: “Mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pa chimaliziro cha nthaŵi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri.” (Danieli 11:13) “Nthaŵi” zimenezi zinali zaka 16 kapena kuposapo kuchokera pamene Aigupto anagonjetsa Asuriya ku Rafia. Pamene Tolemi 5 wamng’onoyo anakhala mfumu ya kumwera, Antiyokasi 3 ananyamuka ndi “unyinji wakuposa oyamba aja” kukalandanso madera amene mfumu ya kumwera ya Igupto inam’landa. Ndi cholinga chimenecho, anaphatikana ndi Mfumu Filipo 5 wa ku Makedoniya kuti amenyere limodzi nkhondoyo.
28. Kodi mfumu yaing’onoyo ya kumwera inali ndi mavuto otani?
28 Mfumu ya kumwera inalinso ndi mavuto ena mu ufumu wake. “Nthaŵi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwera,” anatero mngelo uja. (Danieli 11:14a) Ambiri ‘anaukiradi mfumu ya kumwera.’ Kuwonjezera pa kuyang’anizana ndi asilikali a Antiyokasi 3 limodzi ndi mnzakeyo wa ku Makedoniya, mfumu yaing’onoyo inalinso ndi mavuto ena kumudzi ku Igupto. Chifukwa chakuti namkungwi wake Agatokasi, amene ankalamulira m’malo mwake, analamulira Aigupto mwankhanza, ambiri anapanduka. Mngeloyo anawonjezera kuti: “Ndi achiwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.” (Danieli 11:14b) Ngakhale ena mwa anthu a Danieli anakhala ‘achiwawa,’ kapena olimbikitsa chipanduko. Koma “masomphenya” alionse amene Ayuda oterowo anali nawo othetsa ulamuliro wa Akunja pa dziko lawo anali achinyengo, ndipo analephera, kapena ‘kugwa.’
29, 30. (a) Kodi “ankhondo a kumwera” anagonja bwanji kwa ochokera kumpoto? (b) Kodi mfumu ya kumpoto ‘inadzaima motani m’dziko lokometsetsa’?
29 Mngelo wa Yehova anapitiriza kuti: “Mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika. Koma iye amene am’dzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m’dziko lokometsetsalo, ndi m’dzanja mwake mudzakhala chiwonongeko.”—Danieli 11:15, 16.
30 Magulu ankhondo a Tolemi 5, kapena “ankhondo a kumwera,” anagonja kwa ochokera kumpoto. Atafika ku Paneya (Kaisareya wa Filipo), Antiyokasi 3 anapitikitsa Kazembe Sikopasi wa ku Igupto limodzi ndi amuna osankhidwa 10,000, kapena “osankhika,” mpaka mu Sidoni, ‘mudzi wamalinga.’ Kumeneko Antiyokasi 3 ‘anaunda mtumbira,’ ndi kulanda doko la Foinike mu 198 B.C.E. Anachita malinga ndi “chifuniro chake” chifukwa asilikali a mfumu ya kumwera ya Igupto sanathe kulimbana naye. Ndiyeno Antiyokasi 3 anapita kukaukira Yerusalemu, likulu la “dziko lokometsetsa,” la Yuda. Mu 198 B.C.E., Yerusalemu ndi Yuda anachoka m’manja mwa mfumu ya kumwera ya Igupto ndi kukhala m’manja mwa mfumu ya kumpoto ya Suriya. Ndipo Antiyokasi 3, mfumu ya kumpoto, anayamba ‘kuima m’dziko lokometsetsa.’ Munali ‘chiwonongeko m’dzanja mwake’ kulinga kwa Ayuda ndi Aigupto onse otsutsa. Kodi mfumu ya kumpoto imeneyi inachita chifuniro chake cha iye mwini kufikira liti?
ROMA AIMITSA NGWAZIYO
31, 32. N’chifukwa chiyani mfumu ya kumpoto ‘inawongoka mtima pamodzi naye’ mwa kumvana za mtendere ndi mfumu ya kumwera?
31 Mngelo wa Yehova akutipatsa yankho ili: ‘Ndipo [mfumu ya kumpoto] idzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo idzachita chifuniro chake, nadzam’patsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye.’—Danieli 11:17.
32 Mfumu ya kumpoto, Antiyokasi 3, ‘inalimbitsa nkhope yake’ kuti ilamulire Igupto ndi “mphamvu ya ufumu wake wonse.” Koma m’malo mwake, ‘anawongoka mtima pamodzi naye’ mwa kumvana za mtendere ndi Tolemi 5, mfumu ya kumwera. Zimene Roma anafuna zinapangitsa Antiyokasi 3 kusintha mapulani ake. Pamene iye anaphatikana ndi Mfumu Filipo 5 ya Makedoniya kuti athane ndi mfumu ya Igupto yaing’onoyo ndi kulanda madera ake, anamkungwi a Tolemi 5 anakapempha chitetezo kwa Roma. Pofuna kutengera mwayi mpata umenewu kuti akulitse ulamuliro wake, Roma anaonetsa mangolomera ake.
33. (a) Kodi anamvana zotani zokhazikitsira mtendere pakati pa Antiyokasi 3 ndi Tolemi 5? (b) Kodi cholinga cha ukwatiwo pakati pa Kileopatiya 1 ndi Tolemi 5 chinali chiyani, ndipo nzeruyo inalephera chifukwa chiyani?
33 Poumirizidwa ndi Roma, Antiyokasi 3 anakamvana za mtendere ndi mfumu ya kumwera. Kusiyana ndi kupereka madera ogonjetsedwawo, malinga n’zimene Roma analamula, Antiyokasi 3 anafuna kupereka maderawo mwa dzina lokha, mwa kukwatitsa mwana wake wamkazi Kileopatiya 1—“mwana wamkazi wa akazi”—kwa Tolemi 5. Madera amene anaphatikizapo Yuda, “dziko lokometsetsa,” anayenera kuperekedwa monga chuma chake choloŵa nacho m’banja. Komabe, pachikwati chimenecho mu 193 B.C.E., mfumu ya Suriya sinalole kuti maderawo apite kwa Tolemi 5. Umenewu unali ukwati wandale, womangidwa ndi cholinga chakuti Igupto akhale pansi pa Suriya. Koma nzeruyo inalephera chifukwa Kileopatiya 1 sanapitirize “kuvomerezana naye,” pakuti pambuyo pake anakhala kumbali ya mwamuna wake. Pamene nkhondo inabuka pakati pa Antiyokasi 3 ndi Aroma, Igupto anakhala kumbali ya Roma.
34, 35. (a) Kodi ndi “zisumbu” ziti zimene mfumu ya kumpoto inatembenuzirako nkhope yake? (b) Kodi Roma anathetsa bwanji “kunyoza” kwa mfumu ya kumwera? (c) Kodi Antiyokasi 3 anafa motani, ndipo ndani anakhala mfumu ya kumpoto yotsatira?
34 Ponena za kulephera kwa mfumu ya kumpoto, mngeloyo anawonjezera kuti: “Pambuyo pake [Antiyokasi 3] adzatembenuzira nkhope yake kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina [Roma] adzaleketsa kunyoza kwake adanyoza nako [Roma]; inde adzam’bwezera yekha [Antiyokasi 3] kunyoza kwake. Pamenepo [Antiyokasi 3] adzatembenuzira nkhope yake ku malinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.”—Danieli 11:18, 19.
35 “Zisumbu” zimenezo zinali za Makedoniya, Girisi, ndi Asiyamina. Nkhondo inabuka m’Girisi mu 192 B.C.E., ndipo Antiyokasi 3 ananyengereredwa kupita ku Girisi. Posakondwa ndi zoyesayesa za mfumu ya Suriya zofuna kulanda madera enanso, Roma analengeza kuchita naye nkhondo. Atafika ku Tempiliya anagonjetsedwa ndi Roma. Patapita chaka ngati chimodzi chigonjereni pankhondo ya ku Maginesa mu 190 B.C.E., anatayikidwa zake zonse ku Girisi, Asiyamina, ndi madera akumadzulo kwa mapiri a Torasi. Roma anafuna malipiro aakulu kwambiri ndipo anaika mfumu ya kumpoto ya Suriya pansi pa ulamuliro wake. Pokhala anathamangitsidwa ku Girisi ndi ku Asiyamina komanso polandidwa ngalawa zake zonse za nkhondo, Antiyokasi 3 ‘anatembenuzira nkhope yake ku malinga a dziko lakelake,’ la Suriya. Aromawo ‘anam’bwezera yekha kunyoza kwake anawanyoza nako.’ Antiyokasi 3 anaphedwa pofuna kuba m’kachisi wa ku Elimasi, ku Perisiya, mu 187 B.C.E. Choncho iye ‘anagwa’ mu imfa ndipo analoŵedwa m’malo ndi mwana wake Selukasi 4, mfumu ya kumpoto yotsatira.
MKANGANOWO UPITIRIRA
36. (a) Kodi mfumu ya kumwera inayesa motani kupitiriza mkanganowo, koma kodi zinamuyendera motani? (b) Kodi Selukasi 4 anagwa motani, ndipo anam’loŵa m’malo ndani?
36 Monga mfumu ya kumwera, Tolemi 5 anayesa kulanda madera omwe anayenera kuwalandira monga chuma cha Kileopatiya choloŵa nacho m’banja, koma anam’dyetsa mankhwala ndipo zake zonse zinathera pompo. Anam’loŵa m’malo ndi Tolemi 6. Bwanji nanga za Selukasi 4? Pofuna ndalama zambiri zimene Roma anam’gamulira, anatumiza msungachuma wake Helidasi kuti akafunkhe chuma chimene anamva kuti chinali m’kachisi ku Yerusalemu. Pofunitsitsa mpando wachifumu, Helidasi anapha Selukasi 4. Komabe, Mfumu Yumenasi wa ku Pergamo ndi mbale wake Atalasi anatenga mbale wake wa mfumu yophedwayo ndi kum’longa ufumu monga Antiyokasi 4.
37. (a) Kodi Antiyokasi 4 anayesa motani kudzionetsa wamphamvu koposa Yehova Mulungu? (b) Kodi chitonzo chimene Antiyokasi 4 anayambitsa pakachisi mu Yerusalemu chinatsogolera ku chiyani?
37 Mfumu ya kumwera yatsopanoyo, Antiyokasi 4, inayesa kudzionetsa yamphamvu kuposa Mulungu mwa kuyesa kufafaniza makonzedwe a Yehova a kulambira. Ponyoza Yehova, anapatulira kachisi wa ku Yerusalemu kwa Zeu, kapena Jupita. Mu December 167 B.C.E., anamanga guwa la nsembe lachikunja pamwamba pa guwa la nsembe lalikulu m’bwalo la kachisi pamene ankaperekapo nsembe za tsiku ndi tsiku kwa Yehova. Patapita masiku khumi, anapereka nsembe kwa Zeu paguwa la nsembe lachikunjalo. Chitonzo chimenechi chinapangitsa kuti Ayuda apanduke motsogoleredwa ndi Amakabeo. Antiyokasi 4 analimbana nawo zaka zitatu. Mu 164 B.C.E., patsiku lokumbukira chitonzo chimenecho, Yuda Makabeo anapatuliranso kachisiyo kwa Yehova ndipo anakhazikitsanso phwando lopatulira lotchedwa Hanuka.—Yohane 10:22.
38. Kodi ulamuliro wa Amakabeo unatha motani?
38 Kukhala ngati Amakabeo analoŵa m’pangano ndi Roma mu 161 B.C.E. ndipo anakhazikitsa ufumu mu 104 B.C.E. Koma mkangano pakati pa iwo ndi mfumu ya kumpoto ya Suriya unapitirira. Potsirizira pake, Roma anapemphedwa kuti aloŵererepo. Kazembe wa Roma Nayasi Pompeyi analanda Yerusalemu mu 63 B.C.E. atam’zinga miyezi itatu. Mu 39 B.C.E., bungwe la aphungu a boma la Roma linasankha Herode—Mwedomu—kukhala mfumu ya Yudeya. Kumaliza ulamuliro wa Amakabeo, analanda Yerusalemu mu 37 B.C.E.
39. Kodi mwapindula motani mwa kupenda Danieli 11:1-19?
39 N’kosangalatsa bwanji! kuona mbali yoyamba ya ulosi wa mafumu aŵiri olimbana ikukwaniritsidwa m’mbali zake zonse. Ndithudi, n’kosangalatsa kwabasi kusuzumira m’mbiri yakale ya zaka 500 kuchokera pamene uthenga waulosiwo unaperekedwa kwa Danieli ndi kuzindikira olamulira otenga malo a mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera! Komabe, malo andale a mafumu aŵiri ameneŵa akhala akusintha pamene mkangano wawo ukupitirira m’nthaŵi yonse imene Yesu Kristu anayenda padziko lapansi mpaka m’nthaŵi yathu ino. Mwa kugwirizanitsa zochitika za m’mbiri ndi mbali zochititsa chidwi zovumbulidwa mu ulosi umenewu, tidzakhoza kuzindikira mafumu aŵiri olimbana ameneŵa.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi ndi mizera iŵiri iti ya mafumu amphamvu imene inachokera m’maufumu achihelene, ndipo mafumuwo anayamba mkangano wotani?
• Malinga ndi ulosi wa pa Danieli 11:6, kodi mafumu aŵiriwo ‘anapanga motani zoyenera’?
• Kodi mkanganowo unapitirira motani pakati pa
Selukasi 2 ndi Tolemi 3 (Danieli 11:7-9)?
Antiyokasi 3 ndi Tolemi 4 (Danieli 11:10-12)?
Antiyokasi 3 ndi Tolemi 5 (Danieli 11:13-16)?
• Kodi cholinga cha ukwati wa Kileopatiya 1 ndi Tolemi 5 chinali chiyani, ndipo nzeruyo inalephera chifukwa chiyani (Danieli 11:17-19)?
• Kodi kupenda Danieli 11:1-19 kwakupindulani motani?
[Tchati/Chithunzi patsamba 228]
MAFUMU A PA DANIELI 11:5-19
Mfumu ya Mfumu ya
Kumpoto Kumwera
Danieli 11:5 Selukasi 1 Niketa Tolemi 1
Danieli 11:6 Antiyokasi 2 Tolemi 2
(mkazi Lodise) (mwana Berinasi)
Danieli 11:7-9 Selukasi 2 Tolemi 3
Danieli 11:10-12 Antiyokasi 3 Tolemi 4
Danieli 11:13-19 Antiyokasi 3 Tolemi 5
(mwana Kileopatiya 1) Wom’loŵa m’malo:
Oloŵa m’malo: Tolemi 6
Selukasi 4 ndi
Antiyokasi 4
[Chithunzi]
Ndalama yosonyeza Tolemi 2 ndi mkazi wake
[Chithunzi]
Selukasi 1 Niketa
[Chithunzi]
Antiyokasi 3
[Chithunzi]
Tolemi 6
[Chithunzi]
Tolemi 3 ndi om’loŵa m’malo ake anamanga kachisiyu wa Horasi ku Idufu, kumtunda kwa Igupto
[Mapu/Zithunzi pamasamba 216, 217]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
Mawu akuti “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera” amanena za mafumu a kumpoto ndi kumwera kwa anthu a Danieli
MAKEDONIYA
GIRISI
ASIYAMINA
ISRAYELI
LIBIYA
IGUPTO
AITIOPIYA
SURIYA
Babulo
ARABIYA
[Chithunzi]
Tolemi 2
[Chithunzi]
Antiyokasi Wamkulu
[Chithunzi]
Gome lamwala lolembedwa malamulo a boma operekedwa ndi Antiyokasi Wamkulu
[Chithunzi]
Ndalama yosonyeza Tolemi 5
[Chithunzi]
Chipata cha Tolemi 3, ku Kanaki, mu Igupto
[Chithunzi chachikulu patsamba 210]
[Chithunzi patsamba 215]
Selukasi 1 Niketa
[Chithunzi patsamba 218]
Tolemi 1