Mutu 14
Mafumu Aŵiriwo Asintha
1, 2. (a) N’chiyani chinapangitsa Antiyokasi 4 kulabadira zofuna za Roma? (b) Kodi Suriya anakhala liti chigawo cha Roma?
MFUMU ya Suriya Antiyokasi 4 igonjetsa Igupto ndi kudziika yokha kukhala mfumu yake. Polabadira pempho la Mfumu ya Igupto Tolemi 6, Roma atumiza Kazembe Kayasi Popilasi Linasi ku Igupto. Iye ali ndi ngalawa zankhondo zambiri ndi lamulo lochokera ku Bungwe la Aphungu a Boma la Roma lokauza Antiyokasi 4 kuti atule pansi ufumu wake ku Igupto ndi kutuluka m’dzikomo. Atafika ku Elusasi, mlaga wa Alesandriya, mfumu ya Suriya ndi kazembe wa Roma akumana pamaso m’pamaso. Antiyokasi 4 akupempha mpata wakuti akafunsire kwa aphungu ake, koma Linasi alembera mfumuyo malire moizungulira naiuza kuti iyankhe isanadutse malirewo. Ponyazitsidwa, Antiyokasi 4 akuvomera zofuna za Aromawo nabwerera ku Suriya mu 168 B.C.E. Apa ndiye panathera mkangano wa pakati pa mfumu yakumpoto ya Suriya ndi mfumu ya kumwera ya Igupto.
2 Pokhala ndi mphamvu yaikulu m’zochitika za ku Middle East, Roma akumalamula Suriya zochita. Choncho, ngakhale kuti mafumu ena a mzera wachiselukasi akulamulira Suriya pambuyo pa imfa ya Antiyokasi 4 mu 163 B.C.E., iwo sakutenga malo a “mfumu ya kumpoto.” (Danieli 11:15) Potsirizira pake, Suriya akhala chigawo cha Roma mu 64 B.C.E.
3. Kodi Roma anakula mphamvu motani kuposa Igupto, ndipo zimenezo zinachitika liti?
3 Mzera wa mafumu achitolemi ukupitirizabe kukhala “mfumu ya kumwera” kupitirira pang’ono zaka 130 pambuyo pa imfa ya Antiyokasi 4. (Danieli 11:14) Pankhondo ya ku Akitumu, mu 31 B.C.E., wolamulira wa Roma Okutavia akugonjetsa magulu ankhondo ophatikiza a mfumukazi Kileopatiya 7 yomaliza ya mzera wachitolemi ndi chibwenzi chake cha ku Roma, Marko Antoni. Kileopatiya atadzipha chaka chotsatira, Igupto anakhalanso chigawo cha Roma ndipo sanalinso mfumu ya kumwera. Pofika chaka cha 30 B.C.E., Roma anali kulamulira Suriya ndi Igupto. Kodi tsopano tiyenera kuyembekezera kuti maulamuliro ena adzatenga malo a mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera?
MFUMU YATSOPANO ITUMIZA “WAMSONKHO”
4. Chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera ulamuliro wina kutenga malo a mfumu ya kumpoto?
4 M’nyengo ya masika ya 33 C.E., Yesu Kristu anauza ophunzira ake kuti: “Mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Danieli mneneri, chitaima m’malo oyera . . . iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri.” (Mateyu 24:15, 16) Pogwira mawu Danieli 11:31, Yesu anachenjeza otsatira ake za ‘chonyansa chopululutsa’ cham’tsogolo. Ulosi umenewo wonena za mfumu ya kumpoto unaperekedwa pafupifupi zaka 195 pambuyo pa imfa ya Antiyokasi 4, mfumu yomaliza ya Suriya kukhala pamalowo. Ndithudi, ulamuliro wina unafunikira kutenga malo a mfumu ya kumpoto. Kodi umenewo unali uti?
5. Kodi anauka ndani monga mfumu ya kumpoto, akumatenga malo a Antiyokasi 4?
5 Mngelo wa Yehova Mulungu ananeneratu kuti: “M’malo mwake [mwa Antiyokasi 4] adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku oŵerengeka adzathyoledwa iye, si mwa mkwiyo, kapena kunkhondo ayi.” (Danieli 11:20) Amene ‘anauka’ m’njira imeneyi anali mfumu yaikulu yoyamba ya Roma, Okutavia, amene ankadziŵika kuti Kaisara Augusto.—Onani mutu wakuti “Wina Alemekezedwa, Wina Anyozedwa,” patsamba 248.
6. (a) Kodi “wamsonkho” anatumidwa liti kukayendera “ulemerero wa ufumu,” ndipo zimenezo zinatanthauzanji? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Augusto anafa osati “mwa mkwiyo, kapena kunkhondo ayi”? (c) Kodi mfumu ya kumpoto inasintha motani?
6 “Ulemerero wa ufumuwo” wa Augusto unaphatikizapo “dziko lokometsetsa”—chigawo cha Roma cha Yudeya. (Danieli 11:16) Mu 2 B.C.E., Augusto anatumiza “wamsonkho” mwa kulamula kulembetsa mayina m’kaundula, kapena kuŵerenga anthu, mwina kuti adziŵe chiŵerengero chawo kaamba ka nkhani ya msonkho kapena kulemba anthu usilikali. Chifukwa cha lamulo limeneli, Yosefe ndi Mariya anayenda ulendo wopita ku Betelehemu kukalembetsa m’kaundula, ndipo kumeneko Yesu anabadwa kumalo onenedweratu. (Mika 5:2; Mateyu 2:1-12) Mu August, 14 C.E. “atatha masiku oŵerengeka,” kapena posakhalitsa chiperekereni lamulo lokalembetsa m’kaundula, Augusto anamwalira ali ndi zaka 76, osati “mwa mkwiyo,” mwa kuphedwa ndi chigaŵenga ayi, “kapena kunkhondo ayi,” koma chifukwa cha kudwala. Mfumu ya kumpoto inasinthadi! Mfumu imeneyi tsopano inakhala Ufumu Waukulu wa Roma mwa mafumu ake aakulu.
‘WONYOZEDWA AUKA’
7, 8. (a) Kodi ndani anauka m’malo mwa Augusto monga mfumu ya kumpoto? (b) N’chifukwa chiyani “ulemerero wa ufumuwo” unaperekedwa monyinyirikira kwa m’loŵa m’malo wa Augusto Kaisara?
7 Popitiriza ulosiwo, mngeloyo anati: “M’malo mwake [mwa Augusto] adzauka munthu woluluka [“wonyozedwa”, NW], amene anthu sanam’patsa ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mawu osyasyalika. Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga [“Mtsogoleri,” NW] yemwe wa chipangano.”—Danieli 11:21, 22.
8 ‘Wonyozedwayo’ anali Tiberiyo Kaisara, mwana wa Livia, mkazi wachitatu wa Augusto. (Onani mutu wakuti “Wina Alemekezedwa, Wina Anyozedwa,” patsamba 248.) Augusto ankadana ndi mwana wake wom’pezayo chifukwa cha makhalidwe ake oipa ndipo sanafune kuti adza khale Kaisara wotsatira. “Ulemerero wa ufumuwo” unaikidwa pa mwanayo monyinyirikira pakuti onse amene akanaloŵa m’malo anali atatha kumwalira. Augusto anayamba kulera mwanayo mu 4 C.E. ndipo anam’sankha kukhala wodzaloŵa ufumu. Augusto atamwalira, Tiberiyo wa zaka 54—wonyozedwayo—‘anauka,’ nakhala mfumu yaikulu ya Roma komanso mfumu ya kumpoto.
9. Kodi Tiberiyo ‘analanda motani ufumu ndi mawu osyasyalika’?
9 Buku lotchedwa The New Encyclopædia Britannica limanena kuti: “Tiberiyo anapinga ndale Bungwe la Aphungu a Boma ndipo anakanitsitsa pafupifupi mwezi wathunthu [Augusto atamwalira] kuti asamuike kukhala mfumu yaikulu.” Anauza Bungwe la Aphungulo kuti, kupatulapo Augusto, panalibenso wina amene akanatha kusenza mtolo wolamulira Ufumu Waukulu wa Roma, ndipo anapempha aphungu a bomawo kuti abwezeretse boma lakale la lipabuliki mwa kuika ulamuliro woterowo m’manja mwa gulu la anthu m’malo mwa munthu mmodzi. Will Durant analemba kuti: “Posafuna kuvomereza zimene iye anapempha, Bungwe la Aphungulo linam’pembedzera iye mpaka analandira ulamulirowo.” Durant anawonjezera kuti: “Mbali zonse ziŵiri zinapingana bwino ndale pamakambiranowo. Maganizo a Tiberiyo anali pa boma lotsata mfundo za lipabuliki, apo ayi akanawazemba maganizowo; Aphungu a bomawo amaopa [Tiberiyo] ndi kumuda, koma sanafune kukhazikitsanso boma la lipabuliki monga la m’mbuyomo, loyendetsedwa mwa kuchita misonkhano yosathandiza ya pakati pa aphungu a boma ndi anthu wamba.” Choncho Tiberiyo ‘analanda ufumu ndi mawu osyasyalika.’
10. Kodi ‘mayendedwe a chigumula anathyoledwa’ motani?
10 Ponena za “mayendedwe ake a chigumula”—magulu ankhondo a maufumu ozungulira, mngeloyo anati: “Adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa.” Tiberiyo atakhala mfumu ya kumpoto, mphwake Jemanikasi Kaisara anali mkulu wankhondo wa asilikali achiroma omwe anali kumtsinje wa Laini. Mu 15 C.E., Jemanikasi anatsogolera asilikali ake kunkhondo yokamenyana ndi Aminasi, ngwazi yachijeremani, ndipo anapambana. Komabe, zipambano zochepazo anazipeza motayikidwa kwambiri, ndipo pambuyo pake Tiberiyo anaimitsa nkhondoyo ku Germany. M’malo mwake, analimbikitsa nkhondo yapachiweniweni, pofuna kulepheretsa mitundu yachijeremani kugwirizana pamodzi. Kwenikweni Tiberiyo anatsata mfundo yodziteteza yolimbikitsa ubale ndi mayiko ena ndipo anachita khama pokhwimitsa chitetezo cha kumalire. Mfundo imeneyi inayesa kuthandiza. Mwa njira imeneyi ‘mayendedwe a chigumula’ analetsedwa ndi ‘kuthyoledwa.’
11. Kodi ‘Mtsogoleri wa chipangano anathyoledwa’ motani?
11 Winanso amene ‘anathyoledwa’ anali Mtsogoleri wa chipangano’ chimene Yehova Mulungu anapangana ndi Abrahamu chodalitsa mabanja onse padziko lapansi. Yesu Kristu ndiye anali Mbewu ya Abrahamu yolonjezedwa m’panganolo. (Genesis 22:18; Agalatiya 3:16) Pa Nisani 14, 33 C.E., Yesu anaimirira pamaso pa Pontiyo Pilato m’nyumba ya boma ya gavana wa Roma ku Yerusalemu. Ansembe achiyuda anaimba Yesu mlandu woukira mfumu yaikulu. Koma Yesu anauza Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi. . . . Ufumu wanga suli wochokera konkuno.” Posafuna kuti gavana wachiromayo amasule Yesu wosalakwayo, Ayudawo anafuula kuti: “Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.” Atafuula kuti Yesu aphedwe, iwo anati: “Tilibe Mfumu koma Kaisara.” Malinga ndi lamulo la “kuukira wolemekezeka,” limene Tiberiyo analiwonjezera ndi kuphatikizapo mawu wamba alionse onyoza Kaisara, Pilato anapereka Yesu kuti ‘athyoledwe,’ kapena kupachikidwa pamtengo wozunzikira.—Yohane 18:36; 19:12-16; Marko 15:14-20.
MFUMU YANKHANZA ‘ILINGIRIRA ZIWEMBU ZAKE’
12. (a) Ndani anapangana ndi Tiberiyo? (b) Kodi Tiberiyo ‘anakhala motani wamphamvu ndi anthu oŵerengeka’?
12 Poloserabe za Tiberiyo, mngeloyo anati: “Atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu oŵerengeka.” (Danieli 11:23) Mamembala a Bungwe la Aphungu a Boma la Roma mwalamulo ‘anapangana’ ndi Tiberiyo, ndipo iye anadalira iwo. Koma iye anali wachinyengo, ndipo anakhala “wamphamvu ndi anthu oŵerengeka.” Anthu oŵerengekawo anali Asilikali Olonda Nyumba ya Mfumu, okhala mumsasa pafupi ndi malinga a Roma. Kukhala moyandikana nawo kunadodometsa Bungwe la Aphungu a Boma ndipo kunathandiza Tiberiyo kulepheretsa aliyense amene akanafuna kuukira ulamuliro wake pakati pa anthu ake. Choncho, pokhala ndi alonda 10,000, Tiberiyo anakhalabe wamphamvu.
13. Kodi Tiberiyo anaposa makolo ake pachiyani?
13 Mngeloyo anapitiriza ulosiwo: “Adzafika kachetechete ku minda yokometsetsa ya derali, nadzachita chosachita atate ake, kapena makolo ake; adzawawazira zofunkha, ndi zankhondo, ndi chuma, nadzalingirira malinga ziwembu zake; adzatero nthaŵi.” (Danieli 11:24) Tiberiyo anali munthu wokayikira ena kwambiri, ndipo ulamuliro wake unadzaza mbiri yonyonga anthu. Makamaka chifukwa cholimbikitsidwa ndi Sajanesi, mkulu wa Asilikali Olonda Nyumba ya Mfumu, zaka zomalizira za ulamuliro wake zinali zoopsa kwambiri. Pomalizira pake, anakayikiranso ndi Sajanesi yemwe, mpaka anamunyonga. Kunena za kuzunza anthu, Tiberiyo anaposa ngakhale makolo ake.
14. (a) Kodi Tiberiyo anawazira motani ‘zofunkha ndi chuma’ m’zigawo zonse za Roma? (b) Kodi Tiberiyo anali atadziŵika kukhala wotani pamene amamwalira?
14 Komabe, Tiberiyo anawazira ‘zofunkha ndi chuma’ m’zigawo zonse za Roma. Pofika imfa yake, anthu ake onse anali ndi moyo wotukuka kwambiri. Misonkho inali yofeŵa, ndipo anathandiza kwambiri amene anali m’madera ovutika. Ngati asilikali kapena akuluakulu a boma anapondereza aliyense kapena kulimbikitsa kukondera posamalira nkhani, amalangidwa ndi mfumu. Ulamuliro wokhwima unapereka chitetezo kwa anthu, ndipo misewu yabwino inakweza malonda. Tiberiyo anaonetsetsa kuti zinthu zinali kuchitika mwachilungamo ndi mwakhama kunja komanso m’kati mwa Roma. Malamulo anakonzedwanso bwino, ndipo malangizo a moyo ndi chikhalidwe anawongoleredwa mwa kupititsa patsogolo njira zatsopano zokhazikitsidwa ndi Augusto Kaisara. Komabe, Tiberiyo ‘analingirira ziwembu zake,’ moti katswiri wolemba mbiri yakale wachiroma, Tasitasi anamutcha munthu wonyenga, wochenjera pogwira anthu m’maso. Pofika imfa yake m’March 37 C.E., Tiberiyo anali atadziŵika monga mfumu yankhanza.
15. Kodi zinthu zinali motani mu Roma kumathero kwa zaka za zana loyamba ndi kumayambiriro kwa zaka za zana lachiŵiri C.E.?
15 Otsatira Tiberiyo amene anatenga malo a mfumu ya kumpoto anaphatikizapo Gayo Kaisara (Kalegoli), Klaudiyo 1, Nero, Vasipashani, Tito, Domitani, Neva, Talajani, ndi Adiriya. Buku lakuti The New Encyclopædia Britannica limati: “Kwenikweni, amene anatsatira Augusto anapitiriza mfundo zake za uyang’aniro ndi ntchito yake yomanga, ngakhale kuti luso linatsikirapo koma kudzionetsera kunakula.” Buku limodzimodzilo limatchulanso kuti: “Chakumapeto kwa zaka za zana loyamba ndi kumayambiriro kwa zaka za zana lachiŵiri Roma anali pamwamba penipeni pa ulemerero wake ndi pa chiŵerengero cha anthu.” Ngakhale kuti Roma anali ndi vuto kumalire a ufumu wake panthaŵi imeneyi, kulimbana kwake koloseredwako ndi mfumu ya kumwera sikunachitike mpaka m’zaka za zana lachitatu C.E.
AUKA AYAMBANE NDI MFUMU YA KUMWERA
16, 17. (a) Ndani anatenga malo a mfumu ya kumpoto wotchulidwa pa Danieli 11:25? (b) Nanga anadzatenga malo a mfumu ya kumwera ndani, ndipo zinachitika motani?
16 Mngelo wa Mulungu anapitiriza ulosiwo, amvekere: ‘[Mfumu ya kumpoto] idzautsa mphamvu yake ndi mtima wake iyambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma [mfumu ya kumpoto] sidzaimika, popeza adzam’lingiririra ziwembu. Inde iwo akudyako chakudya chake adzamuwononga; ndi ankhondo ake adzasefukira, nadzagwa ambiri ophedwa.’—Danieli 11:25, 26.
17 Pafupifupi zaka 300 kuchokera pamene Okutavia anatenga Igupto kukhala chigawo cha Roma, Mfumu Yaikulu ya Roma Uleliya inatenga malo a mfumu ya kumpoto. Panthaŵiyo, Mfumukazi Setimaya Zenobia wa dziko lolamulidwa ndi Roma la Palimelia anatenga malo a mfumu ya kumwera.a (Onani mutu wakuti “Zenobia—Mfumukazi Yankhondo ya Palimelia,” patsamba 252.) Asilikali a ku Palimelia analoŵa mu Igupto mu 269 C.E. akumanamizira kuti akupereka chitetezo cha Roma. Zenobia anafuna kupanga Palimelia kukhala mzinda waukulu kum’maŵa ndipo anafunanso kulamulira zigawo za Roma za kum’maŵa. Pododoma ndi cholinga cha mayiyu, Uleliya ‘anautsa mphamvu yake ndi mtima wake’ kuti akalimbane ndi Zenobia.
18. Kodi zotsatira za nkhondo ya pakati pa Mfumu Yaikulu Uleliya, mfumu ya kumpoto, ndi Mfumukazi Zenobia, mfumu ya kumwera zinali zotani?
18 Monga ufumu wolamulidwa ndi Zenobia, mfumu ya kumwerayo ‘inachita nkhondo’ ndi mfumu ya kumpoto “ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu” lotsogoleredwa ndi akazembe aŵiri, Zabadasi ndi Zabayi. Koma Uleliya anagonjetsa Igupto ndi kuyamba ndawala yankhondo mu Asiyamina ndi Suriya. Zenobia anagonjetsedwa ku Emesa (tsopano Homs) ndipo anabwerera ku Palimelia. Pamene Uleliya anazinga mzindawo, Zenobia anayesetsa kuuteteza zolimba koma sanapambane. Iye ndi mwana wake anathaŵa kuloŵera ku Perisiya, koma anagwidwa ndi Aroma pa mtsinje wa Firate. Apalimeliawo anapereka mzinda wawo mu 272 C.E. Uleliya sanaphe Zenobia, anam’panga kukhala chionetsero chonyadira paligubo la chilakiko chake mu Roma mu 274 C.E. Mayiyu anakhala moyo wake wonse monga dona wolemekezeka wa Roma.
19. Kodi Uleliya anagwa motani ‘chifukwa cha ziwembu zimene’ anam’konzera?
19 Uleliya mwiniyo ‘sanaime chifukwa anam’lingirira ziwembu.’ Mu 275 C.E., ananyamuka ulendo wokamenyana ndi Aperisiya. Pamene anali ku Thiresi, poyembekeza mpata woti awoloke mifuleni ndi kuloŵa mu Asiyamina, aja amene ‘anadya chakudya chake’ anam’konzera ziwembu kuti ‘am’thyole.’ Anaitana mlembi wake Erosi kuti afotokoze chimene chinkachititsa zinthu kusayenda bwino. Koma Erosi anapeka mndandanda wa mayina a nduna zina zimene zinayenera kuphedwa. Ndunazo zitaona mndandandawo zinakonza chiwembu chakuti Uleliya aphedwe, ndipo anaphedwadi.
20. Kodi “ankhondo” a mfumu ya kumpoto ‘anasefukira’ motani?
20 Udindo wa mfumu ya kumpoto sunathe ndi imfa ya Mfumu Yaikuluyo Uleliya. Olamulira ena achiroma anatsatirapo. Panthaŵi inayake, panali mfumu yaikulu ya kumadzulo ndi mfumu yaikulu ya kum’maŵa. Motsogoleredwa ndi amuna ameneŵa “ankhondo ake” a mfumu ya kumpoto ‘anasefukira,’ kapena ‘kubalalika,’b ndipo ambiri ‘anagwa ophedwa’ ndi mitundu yachijeremani yowaloŵerera kuchokera kumpoto. Mtundu wa anthu otchedwa Agoti unawoloka malire ndi kuloŵerera Roma m’zaka za zana lachinayi C.E. Mitundu yosiyanasiyana inapitiriza kuloŵerera. Mu 476 C.E., mtsogoleri wachijeremani Odoasa anachotsa mfumu yaikulu yomalizira yolamulira Roma. Pofika kumayambiriro kwa zaka za zana lachisanu ndi chimodzi, Ufumu Waukulu wa Roma unaphwasulidwa kumadzulo, ndipo mafumu achijeremani anayamba kulamulira Britannia, Gau, Italiya, Kumpoto kwa Afirika, ndi Spanya. Chigawo cha kum’maŵa cha ufumuwo chinapitirira mpaka m’zaka za zana la 15.
UFUMU WAUKULU UGAŴIKA
21, 22. Kodi Kositantini anayambitsa kusintha kotani m’zaka za zana lachinayi C.E.?
21 Mosataya nthaŵi ndi kufotokoza mbali zosafunikira kwenikweni ponena za kugwa kwa Ufumu Waukulu wa Roma, umene unakhala zaka mazanamazana, mngelo wa Yehova anapitiriza kunenera zochitika zam’tsogolo za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera. Komabe, kupenda zochitika zina mu Ufumu Waukulu wa Roma kudzatithandiza kuzindikira mafumu aŵiri odanawo m’nthaŵi ya pambuyo pake.
22 M’zaka za zana lachinayi, Kositantini, Mfumu Yaikulu ya Roma, anapereka lamulo la boma lovomereza Chikristu champatuko. Iye anaitanitsa msonkhano wa tchalitchi ndi kuutsogolera ku Nesiya, Asiyamina, mu 325 C.E. Pambuyo pake, Kositantini anasamutsa nyumba yake yachifumu ku Roma kupita ku Bezantiyamu, kapena Kositantinopo, napanga mzindawo kukhala likulu lake latsopano. Ufumu Waukulu wa Roma unapitirira pansi pa ulamuliro wa mfumu yaikulu kufikira imfa ya Mfumu Yaikulu Tedosiyasi 1, pa January 17, 395 C.E.
23. (a) Kodi ndi kugaŵana Ufumu Waukulu wa Roma kotani kumene kunachitika pambuyo pa imfa ya Tedosiyasi? (b) Kodi Ufumu Wakum’maŵa unatha liti? (c) Kodi ankalamulira Igupto ndani pofika 1517?
23 Pambuyo pa imfa ya Tedosiyasi, Ufumu Waukulu wa Roma unagaŵidwa pakati pa ana ake. Onariasi anatenga chigawo chakumadzulo, ndipo Akadiasi anatenga chigawo cha kum’maŵa, ndi Kositantinopo monga likulu lake. Britannia, Gau, Italiya, Spanya, ndi Kumpoto kwa Afirika anali ena mwa madera a chigawo cha kumadzulo. Makedoniya, Thiresi, Asiyamina, Suriya, ndi Igupto anali madera a chigawo cha kum’maŵa. Mu 642 C.E., likulu la Igupto, Alesandriya, linatengedwa ndi Asaraseni (Aarabu), ndipo Igupto anakhala chigawo cha akalifa [atsogoleri achisilamu]. Mu January 1449, Kositantini 11 anakhala mfumu yaikulu yomalizira ya kum’maŵa. Ateki achiotomani motsogoleredwa ndi Sulutani Muhamedi 2 analanda Kositantinopo pa May 29, 1453, kuthetsa Ufumu Waukulu wa Roma Wakum’maŵa. M’chaka cha 1517 Igupto anakhala chigawo cha Turkey. Koma m’kupita kwa nthaŵi, dziko limeneli la mfumu yakale ya kumwera linadzalamulidwa ndi ufumu wina wochokera kuchigawo cha kumadzulo.
24, 25. (a) Malinga n’kunena kwa akatswiri a mbiri yakale ena, kodi Ufumu Wopatulika wa Roma unayambira pati? (b) Kodi potsirizira pake n’chiyani chinachitikira udindo wa “mfumu yaikulu” mu Ufumu Wopatulika wa Roma?
24 Kuchigawo chakumadzulo kwa Ufumu Waukulu wa Roma kunauka bishopu wachikatolika wa Roma, wotchedwa Papa Leo 1, amene anadziŵika ndi kulimbikitsa ulamuliro wa apapa m’zaka za zana lachisanu C.E. M’kupita kwa nthaŵi, papayo mwa iye yekha anakhazikitsa mfumu yaikulu ya chigawo cha kumadzulo. Zimenezi zinachitika m’Roma patsiku la Khirisimasi m’chaka cha 800 C.E., pamene Papa Leo 3 anakhazikitsa Mfumu Chalesi wachifulanki (Shalameni) monga mfumu yaikulu ya Ufumu wa Roma Wakumadzulo watsopano. Kulonga ufumu kumeneku kunayambitsanso ulamuliro wa mafumu aakulu mu Roma, ndipo malinga ndi kunena kwa akatswiri a mbiri yakale ena, akuti ichi ndicho chinali chiyambi cha Ufumu Wopatulika wa Roma. Kuyambira pamenepo panakhala Ufumu Wakum’maŵa ndi Ufumu Wopatulika wa Roma kumadzulo, onse anadzitcha Akristu.
25 M’kupita kwa nthaŵi, amene anatsatira Shalameni anakhala olamulira osathandiza. Ndipo nthaŵi ina udindo weniweniwo wa mfumu yaikulu unakhala wopanda munthu. Panthaŵiyo, Mfumu Otto 1 wachijeremani ndiye anali kulamulira chigawo chachikulu cha kumpoto ndi kumwera cha Italiya. Iye anadzilengeza yekha kukhala mfumu ya Italiya. Pa February 2, 962 C.E., Papa Yohane 12 anakhazikitsa Otto 1 kukhala mfumu yaikulu ya Ufumu Wopatulika wa Roma. Likulu lake linali ku Germany, ndipo mafumu aakuluwo anali Ajeremani, komanso anthu awo ambiri. Patapita zaka mazana asanu banja lachiositiria la Asibeki linatenga udindo wa “mfumu yaikulu” ndipo unakhalabe nawo kwa zaka zonse zotsala za Ufumu Wopatulika wa Roma.
MAFUMU AŴIRIWO AONEKERANSO BWINO
26. (a) Kodi tinganenenji za kutha kwa Ufumu Wopatulika wa Roma? (b) Ndani anadzaonekera monga mfumu ya kumpoto?
26 Napolioni 1 anakantha Ufumu Wopatulika wa Roma ndi nkhonya yopheratu pamene anakana kuuzindikira pambuyo pa zilakiko zake m’Germany m’chaka cha 1805. Polephera kuteteza ufumuwo, Mfumu Yaikulu Francis 2 anatula pansi ufumu wa Roma pa August 6, 1806, ndipo anabwerera ku boma lakwawo monga mfumu ya Austria. Patapita zaka 1,006, Ufumu Wopatulika wa Roma wokhazikitsidwa ndi Leo 3, papa wachikatolika wa Roma, ndi Shalameni, mfumu yachifulanki, unatha. Mu 1870, Roma anakhala likulu la ufumu wa Italiya, womasuka ku ulamuliro wa Vatican. Chaka chotsatira, ufumu wachijeremani unayamba ndi Wilhelm 1 amene anatchedwa kaisara, kapena kaiza. Choncho, mfumu ya kumpoto yamakono—Germany—inaonekera padziko.
27. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Igupto ayambe kulamudwa ndi Britain? (b) Kodi ndani anatenga malo a mfumu ya kumwera?
27 Nangano ndani anali mfumu ya kumwera yamakono? Mbiri yakale imasonyeza kuti Britain anakhala ufumu m’zaka za zana la 17. Pofuna kusokoneza njira za malonda za Britain, Napolioni 1 anagonjetsa Igupto mu 1798. Nkhondo inabuka, ndipo mgwirizano wa Britain ndi Ottoman unakakamiza Afalansa kuchoka mu Igupto, amene anali mfumu ya kumwera kumayambiriro kwa mkanganowu. M’zaka 100 zotsatira, mphamvu ya Britain pa Igupto inakula. Pambuyo pa 1882, Igupto anadalira Britain kotheratu. Pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inabuka mu 1914, Igupto anali m’manja mwa Turkey ndipo analamulidwa ndi kazembe woimira boma la Turkey. Turkey atakhala kumbali ya Germany m’nkhondo imeneyo, Britain anachotsa pampando kazembeyo ndi kulengeza Igupto kukhala dziko lolamulidwa ndi Britain. M’kupita kwa nthaŵi, Britain ndi America anagwirizana nakhala Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse. Pamodzi, anatenga malo a mfumu ya kumwera.
[Mawu a M’munsi]
a Popeza kuti mawu akuti “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwera” ndi mayina audindo, akhoza kutanthauza bungwe lililonse lolamulira, kuphatikizapo mfumu, mfumukazi, kapena chiungwe cha mayiko.
b Onani mawu a m’munsi pa Danieli 11:26 m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures—With References, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi ndi mfumu yaikulu iti ya Roma imene inayamba kuimirira monga mfumu ya kumpoto, ndipo inatumiza liti “wamsonkho”?
• Ndani anatenga malo a mfumu ya kumpoto pambuyo pa Augusto, ndipo ‘Mtsogoleri wa chipangano anathyoka’ motani?
• Kodi zotsatirapo zinali zotani pa nkhondo ya pakati pa Uleliya monga mfumu ya kumpoto ndi Zenobia monga mfumu ya kumwera?
• Kodi n’chiyani chinachitikira Ufumu wa Roma, ndipo ndi maulamuliro ati amene anatenga malo a mafumu aŵiriwo pofika kumapeto kwa zaka za zana la 19?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 248-251]
WINA ALEMEKEZEDWA, WINAYO ANYOZEDWA
WINA anasandutsa boma la lipabuliki lodzaza chiwawa kukhala ufumu wa dziko lonse. Winayo anawonjezera chuma cha dzikolo kuchulukitsa nthaŵi 20 m’zaka 23. Wina analemekezedwa atamwalira, koma winayo ananyozedwa. Ulamuliro wa mafumu a Roma aŵiriŵa unakuta zaka za moyo wa Yesu ndi utumiki wake. Kodi iwo anali ndani? Ndipo n’chifukwa chiyani wina analemekezedwa, pamene winayo ayi?
“ANAPEZA ROMA WA NJERWA NDIPO ANAM’SIYA WA MIYALA YONYEZIMIRA”
Mu 44 B.C.E pamene Juliasi Kaisara anaphedwa, mdzukulu wa mlongo wake Gayo Okutavia anali ndi zaka 18 zokha. Pokhala mwana wolera wa Juliasi Kaisara komanso woloŵa m’malo wake wamkulu, Okutavia wachinyamatayo ananyamuka mwachangu kupita ku Roma kuti akalandire choloŵa chake. Kumeneko anakumana ndi mdani wamphamvu—kazembe wamkulu wa Kaisara, Marko Antoni, yemwe anayembekezera kukhala woloŵa ufumu wamkulu. Kupingana ndale komwe kunatsatirapo ndi kulimbanira ulamuliro kunatenga zaka 13.
Ndi kokha pambuyo pogonjetsa magulu ankhondo ophatikizana pamodzi a Mfumukazi Kileopatiya ya Igupto ndi chibwenzi chake Marko Antoni (mu 31 B.C.E.) pamene Okutavia anaonekera kukhala wolamulira weniweni wa Ufumu wa Roma. Chaka chotsatira Antoni ndi Kileopatiya anadzipha okha, ndipo Okutavia analanda Igupto. Choncho, mbali yotsalira ya Ufumu wa Girisi inachotsedwa, ndipo Roma anakhala ulamuliro wamphamvu padziko lonse.
Pokumbukira kuti ulamuliro wankhanza wa Juliasi Kaisara unam’phetsa, Okutavia anachita mosamala kuti asabwerezenso kupusa kumeneko. Choncho, posafuna kukhumudwitsa Aroma okonda boma la lipabuliki, iye anabisa ulamuliro wake m’dzina la lipabuliki. Anakana mayina ngati “mfumu” kapena “wolamulira wamphamvu.” Kuwonjezerapo, analengezanso cholinga chake chopereka ulamuliro wa zigawo zonse m’manja mwa Bungwe la Aphungu a Boma la Roma ndi kupemphanso kutula pansi maudindo amene anali nawo. Nzeru imeneyi inagwira ntchito. Bungwe la Aphungulo poyamikira linalimbikitsa Okutavia kuti asachoke pamaudindo akewo ndi kuti alamulirebe zigawo zina.
Komanso, pa January 16, 27 B.C.E., Bungwe la Aphungulo linatcha Okutavia dzina laulemu lakuti “Augusto,” kutanthauza “Wokwezeka, Wopatulika.” Okutavia sanangolandira dzina laulemulo komanso anapatula mwezi umodzi ndi kuutcha dzina lake, nabwerekanso tsiku limodzi ku mwezi wa February kuti August akhale ndi masiku ambiri ngati July, mwezi wotengera dzina la Juliasi Kaisara. Choncho Okutavia anakhala mfumu yaikulu yoyamba ya Roma ndipo pambuyo pake anadziŵika monga Kaisara Augusto kapena “Wa August.” Pambuyo pake anapatsidwanso udindo wokhala “pontifex maximus” (mkulu wa ansembe), ndipo mu 2 B.C.E., chaka chimene Yesu anabadwa, Bungwe la Aphungu linam’tchanso Pater Patriae, “Tate wa Dziko Lake.”
M’chaka chimenecho, “lamulo linatuluka kwa Kaisara Augusto kuti dziko lonse lokhalamo anthu lilembedwe . . . Ndipo onse anamuka kulembedwa, munthu aliyense kumudzi wake.” (Luka 2:1-3) Chifukwa cha lamulo limeneli, Yesu anakabadwira ku Betelehemu kukwaniritsa ulosi wa Baibulo.—Danieli 11:20; Mika 5:2.
Boma la Augusto linadziŵika ndi kuona mtima pamlingo wabwinopo, linalinso ndi ndalama yokhazikika. Augusto anakhazikitsanso dongosolo labwino lotumizira makalata ndi mtokoma ndipo anamanga misewu ndi milatho. Anakonzanso gulu lankhondo, nakhazikitsa asilikali apanyanja achikhalire, ndi kusankhanso kagulu ka asilikali aluso lapamwamba kotchedwa Asilikali Olonda Nyumba ya Mfumu. (Afilipi 1:13, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Mu ulamuliro wake, alembi ngati Viji ndi Horasi anapita patsogolo kwambiri ndipo akatswiri a zosemasema anachita ntchito zokongola kwabasi zimene tsopano zili m’gulu la luso lapamwamba koposa. Augusto anamalizitsa kumanga nyumba zimene Juliasi Kaisara anasiyira panjira ndipo anakonzanso akachisi ambiri. Pax Romana (“Mtendere wa Roma”) imene iye anayambitsa inakhala zaka zoposa 200. Pa August 19, 14 C.E., ali ndi zaka 76, anamwalira ndipo pambuyo pake anayamba kum’lambira ngati mulungu wawo.
Augusto anadzitama kuti “anapeza Roma wa njerwa ndipo anam’siya wa miyala yonyezimira.” Posafuna kuti Roma abwerere ku masiku achiwawa a boma lakale la lipabuliki, iye anafuna kukonzekeretsa mfumu yaikulu yotsatira. Koma kunali kovuta kuti apeze woyenerera kum’loŵa m’malo. Mphwake, adzukulu ake aŵiri, mpongozi wake, ndi mwana wake wopeza onse anali atamwalira. Mwana wake wopeza Tiberiyo ndi yekhayo analipo kuti am’loŵe m’malo.
“WONYOZEDWA”
Mwezi usanathe chimwalirireni Augutso, Bungwe la Aphungu a Boma la Roma linakhazikitsa Tiberiyo wa zaka 54 monga mfumu yaikulu. Tiberiyo anakhala ndi moyo ndi kulamulira mpaka March 37 C.E. Choncho, ndiye anali mfumu yaikulu ya Roma m’nthaŵi ya utumiki wa Yesu.
Monga mfumu yaikulu, Tiberiyo anali ndi zabwino komanso zoipa zake. Mwa mikhalidwe yake yabwino, iye sanafune kuwononga ndalama pazinthu zokongola koma zosafunikira kwenikweni. Chifukwa cha zimenezo, ufumuwo unatukuka ndipo iye anali ndi chuma chothandiza pa ngozi ndi pazovuta zina. Ubwino wake winanso, Tiberiyo anadziona ngati munthu wamba, anakana mayina aulemu ambiri, ndipo analangiza kuti anthu anayenera kulambira Augusto osati iye. Sanatche mwezi uliwonse dzina lake muja anachitira Augusto ndi Juliasi Kaisara, ndipo sanalole ena kum’lemekeza mwa njira imeneyo.
Komabe, zoipa za Tiberiyo zinapambana zabwino zake. Anali wokayikira ena mopambanitsa komanso wonyenga m’zochita zake ndi ena. Komanso ulamuliro wake unadzaza mbiri yonyonga anthu—ambiri anali mabwenzi ake akale. Lamulo la “kusaukira wolemekezeka” mwa machitidwe ogalukira, analiwonjezera ndi kuphatikizapo mawu wamba onyoza iye. Kukhala ngati Ayuda anagwiritsa ntchito lamulo limeneli poumiriza Gavana wa Roma Pontiyo Pilato kuti aphe Yesu.—Yohane 19:12-16.
Tiberiyo anakhazikitsa Asilikali Olonda Nyumba ya Mfumu pafupi ndi Roma mwa kumanga msasa wawo kumpoto kwa linga la mzindawo. Kukhalapo kwa Alondawo kunaopseza Bungwe la Aphungu a Boma la Roma, limenenso limaopseza ulamuliro wake. Alonda ameneŵa analepheretsa upandu uliwonse. Tiberiyo analimbikitsanso dongosolo la ukazitape, ndipo zaka zomalizira za ulamuliro wake zinali zoopsa kwambiri.
Nthaŵi imene amamwalira, Tiberiyo anali kudziŵika kukhala wolamulira wankhanza. Atamwalira, Aroma anasangalala ndipo Bungwe la Aphungulo linakana kumuyesa mulungu. Pa zifukwa zimenezi ndi zinanso, tikuona mwa Tiberiyo kukwaniritsidwa kwa ulosi wonena kuti “wonyozedwa” adzauka monga “mfumu ya kumpoto.”—Danieli 11:15, 21.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi Okutavia anakhala motani mfumu yaikulu yoyamba ya Roma?
• Kodi tinganene chiyani za kutukuka kwa boma la Augusto?
• Kodi zabwino ndi zoipa za Tiberiyo zinali zotani?
• Kodi ulosi wokhudza “wonyozedwa” unakwaniritsidwa motani mwa Tiberiyo?
[Chithunzi]
Tiberiyo
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 252-255]
ZENOBIA—MFUMUKAZI YANKHONDO YA KU PALIMELIA
“ANALI wa maonekedwe oderapo . . . Mano ake oyera ngati mkaka, ndipo maso ake aakulu oderapo ankanyezimira mokopa mtima komanso anali wosiririka kwabasi. Mawu ake anali amphamvu koma okoma. Chifukwa chophunzira, amamvetsa maganizo a amuna. Amathanso kulankhula bwino Chilatini, komanso Chigiriki, Chisuriya, ndi zinenero za ku Igupto.” Izi ndi zinthu zimene katswiri wa mbiri yakale Edward Gibbon anatamanda nazo Zenobia—mfumukazi yankhondo ya mzinda wa Palimelia ku Suriya.
Mwamuna wa Zenobia anali munthu wolemekezeka wa ku Palimelia dzina lake Odenatasi, amene anafupidwa ndi udindo wa ukazembe wa Roma mu 258 C.E. chifukwa anapambana kumbali ya Ufumu Waukulu wa Roma polimbana ndi Perisiya. Patapita zaka ziŵiri, Odenatasi analandira kuchokera kwa Galenasi, Mfumu Yaikulu ya Roma, udindo wa corrector totius Orientis (gavana wa chigawo chonse cha Kum’maŵa). Imeneyi inali mphotho yoyamikira chipambano chake pogonjetsa Mfumu Shapari 1 ya Perisiya. M’kupita kwa nthaŵi, Odenatasi anadzitcha yekha “mfumu ya mafumu.” Zipambano za Odenatasi zingakhale makamaka chifukwa cha kulimba mtima kwa Zenobia ndi kuchenjera kwake.
ZENOBIA AYESETSA KUKHAZIKITSA UFUMU WAUKULU
Mu 267 C.E., pamene anakwera kwambiri paudindo, Odenatasi anaphedwa limodzi ndi mwana wake amene akanam’loŵa m’malo. Zenobia anatenga udindo wa mwamuna wake, chifukwa mwana wake anali wamng’ono kwambiri. Pokhala wokongola, wofunitsitsa kutsogola, wodziŵa kuyendetsa zinthu, wozoloŵera kumenya nkhondo limodzi ndi mwamuna wake, ndi wodziŵa bwino zinenero zambiri, mayiyu analemekezedwa ndi kuchirikizidwa ndi anthu ake. Zenobia amakonda kwambiri kuphunzira ndipo anali ndi anzake ambiri ophunzira. Mmodzi wa alangizi ake anali wafilosofi ndi katswiri pakulankhula dzina lake Kasiasi Longinasi yemwe ankatchedwa “laibulale yamoyo ndi miziyamu yoyenda.” M’buku lakuti Palmyra and Its Empire—Zenobia’s Revolt Against Rome, mlembi wake Richard Stoneman anati: “M’kati mwa zaka zisanu chimwalirireni Odenatasi . . . , Zenobia anali atadzikhazikitsa iyemwini m’maganizo mwa anthu ake monga mfumukazi ya Kum’maŵa.”
Kumbali ina ya ufumu wa Zenobia kunali dziko la Perisiya, limene iye ndi mwamuna wake analifooketsa, ndipo kumbali inayi kunali Roma yemwe anali m’kati mwa kupasuka. Ponena za mikhalidwe ya mu Ufumu Waukulu wa Roma panthaŵiyo, katswiri wa mbiri yakale J. M. Roberts anati: “Zaka za zana lachitatu . . . zinali nthaŵi yoipitsitsa mu Roma kumalire ake akum’maŵa ndi kumadzulo chimodzimodzi. Kumudzinso kunayambikanso nyengo ya nkhondo ndi mikangano yapachiweniweni. Mafumu aakulu 22 (kupatulapo onamizira) anabwera ndi kupita.” Kwinaku, dona wolemekezekayo wa ku Suriya anakhazikika zolimba monga mfumukazi m’dziko lake. Stoneman anati: “Mayiyu pogwiriziza maufumu aŵiriwo [Perisiya ndi Roma], anali wokhoza kukhazikitsa mbali yachitatu imene ikanawalamulira aŵiriwo.”
Mwayi wakuti Zenobia afutukule ulamuliro wake unafika mu 269 C.E. pamene wonamizira wokanganira ulamuliro wa Roma anaonekera mu Igupto. Asilikali a Zenobia mwachangu anakaloŵa mu Igupto, naswa wopandukayo, ndi kulanda dzikolo. Podzilengeza kukhala mfumukazi ya Igupto, iye anasulitsa ndalama m’dzina lake. Ufumu wake tsopano unakula kuchokera ku mtsinje wa Nile mpaka kumtsinje wa Firate. Apa m’pamene Zenobia anatengera malo a “mfumu ya kumwera.”—Danieli 11:25, 26.
LIKULU LA ZENOBIA
Zenobia analimbitsa ndi kukongoletsa likulu lake, Palimelia, moti mzindawo unafanana ndi mizinda yaikulu ya dziko la Roma. Chiŵerengero cha anthu ake chinapitirira 150,000. Palimelia anadzaza nyumba zachisangalalo zokongola, akachisi, minda yamaluŵa, zipilala, ndi zoumba zachikumbukiro. Mzindawo unazingidwa ndi linga limene amati linazungulira pamtunda wa makilomita 21. Zipilala za mamangidwe a ku Korinto zamsinkhu woposa mamita 15 zokwanira pafupifupi 1,500, zinandanda m’mbali mwa msewu waukulu. Zifaniziro zosema za ngwazi ndi za anthu achuma othandiza zinalipo zambiri mumzindamo. Mu 271 C.E., Zenobia anaimika chifanizo cha iyemwini ndi malemu mwamuna wake.
Kachisi wa mulungu Dzuŵa anali imodzi ya nyumba zokongola koposa mu Palimelia ndipo mosakayikira anali malo aakulu olambirira mumzindawo. Zenobia ayenera kuti analambira mulungu wogwirizana ndi mulungu dzuŵa. Komabe, Suriya wa m’zaka za zana lachitatu anali dziko la zipembedzo zambiri. Mu ufumu wa Zenobia munali odzitcha Akristu, Ayuda, ndi alambiri a dzuŵa ndiponso a mwezi. Kodi maganizo ake anali otani ponena za mitundumitundu ya kulambira imeneyi? Mlembi Stoneman anati: “Wolamulira wanzeru sanyalanyaza miyambo iliyonse imene anthu ake amaiona yoyenera kwa iwo. . . . Milunguyo, . . . iyenera kuti inali kumbali ya Palimelia.” Mwachionekere, Zenobia anali wololera zipembedzo za ena.
Chifukwa cha umunthu wake wokopawo, Zenobia anakondedwa ndi ambiri. Chofunika koposa ndicho mbali imene anachita poimira ufumu woloseredwa mu ulosi wa Danieli. Komabe, ulamuliro wake sunapyole zaka zisanu. Mfumu Yaikulu ya Roma Uleliya anagonjetsa Zenobia mu 272 C.E. ndipo anaphwasuliratu Palimeliya moti sakanakonzedwanso. Zenobia anachitidwa chifundo. Akuti anadzakwatiwa ndi phungu wa boma ndipo kukhala ngati anatha moyo wake wonse atapumitsidwa pantchito.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi umunthu wa Zenobia wafotokozedwa motani?
• Kodi zina mwa zipambano za Zenobia zinali zotani?
• Kodi maganizo a Zenobia anali otani pankhani ya chipembedzo?
[Chithunzi]
Mfumukazi Zenobia akulankhula kwa asilikali ake
[Tchati/Zithunzi patsamba 246]
MAFUMU A PA DANIELI 11:20-26
Mfumu ya Mfumu ya
Kumpoto Kumwera
Danieli 11:20 Augusto
Danieli 11:21-24 Tiberiyo
Danieli 11:25, 26 Uleliya Mfumukazi Zenobia
Kusweka Ufumu wa Britain, atsatiridwa
konenedweratu Ajeremani ndi Ulamuliro
kwa Ufumu wa Wamphamvu
Roma kuchititsa Padziko Lonse wa
kupangika kwa Britain ndi America
[Chithunzi]
Tiberiyo
[Chithunzi]
Uleliya
[Chithunzi]
Chifanizo cha Shalameni
[Chithunzi]
Augusto
[Chithunzi]
Ngalawa yankhondo ya Britain ya m’zaka za zana la 17
[Chithunzi chachikulu patsamba 230]
[Chithunzi patsamba 233]
Augusto
[Chithunzi patsamba 234]
Tiberiyo
[Chithunzi patsamba 235]
Chifukwa cha lamulo la Augusto, Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu
[Chithunzi patsamba 237]
Malinga n’kunena kwa ulosi, Yesu ‘anathyoledwa’ mu imfa
[Chithunzi patsamba 245]
1. Shalameni 2. Napolioni 1 3. Wilhelm 1 4. Asilikali achijeremani, nkhondo yoyamba ya padziko lonse