-
Kodi “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2020 | May
-
-
13. Kodi mfumu ya kumpoto inachita chiyani m’ma 1930 komanso pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse?
13 M’ma 1930, makamaka pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, mfumu ya kumpoto inazunza kwambiri anthu a Mulungu. Chipani cha Nazi chitayamba kulamulira dziko la Germany, Hitler ndi otsatira ake analetsa ntchito ya anthu a Mulungu. Mfumu ya kumpotoyi inapha anthu a Yehova pafupifupi 1,500 ndipo enanso ambiri inawatumiza kundende zozunzirako anthu. Danieli anali ataneneratu kuti zimenezi zidzachitika. Anati mfumu ya kumpoto ‘idzaipitsa malo opatulika’ ndiponso ‘idzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.’ Mfumuyi inachita izi poletsa ntchito yolalikira yomwe atumiki a Mulungu ankagwira. (Dan. 11:30b, 31a) Ngakhale Hitler yemwe anali mtsogoleri wadzikolo, anafika polumbira kuti adzapha anthu onse a Mulungu m’dziko la Germany.
-
-
Kodi “Mfumu ya Kumpoto” M’nthawi ya Mapeto Ndi Ndani?Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2020 | May
-
-
MAFUMU ODANA ANACHITIRA ZINTHU LIMODZI
17. Kodi “chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko” n’chiyani?
17 Mfumu ya kumpoto inathandiza mfumu ya kum’mwera poika “chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko.” (Dan. 11:31) “Chinthu chonyansa” chimenechi ndi bungwe la United Nations.
18. N’chifukwa chiyani bungwe la United Nations limatchedwa “chinthu chonyansa”?
18 Bungwe la United Nations limatchedwa “chinthu chonyansa” chifukwa limanena kuti likhoza kubweretsa mtendere padzikoli, zomwe ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungakwanitse. Ndiponso ulosi unanena kuti chinthu chonyansachi ndi “chobweretsa chiwonongeko” chifukwa bungweli lidzaukira ndi kuononga zipembedzo zonse zonyenga.—Onani tchati chakuti “Mafumu Awiri Olimbana M’nthawi ya Mapeto.”
-