Chilakiko Chotsiriza cha Mikaeli, Kalonga Wamkulu
“Nthaŵi yomweyi [adzaima, NW] Mikaeli kalonga wamkulu [amene akuimirira m’malo mwa, NW] ana a anthu a mtundu wako.”—DANIELI 12:1.
1. Kodi ndimkhalidwe wa maganizo wotani umene wasonyezedwa ndi olamulira adziko kulinga ku uchifumu wa Yehova, ndipo kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto yakhalira yofanana nawo?
“YEHOVA ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite?” (Eksodo 5:2) Ameneŵa anali mawu onyoza a Farao kwa Mose. Pokana kuvomereza Umulungu woposa wa Yehova, Farao anatsimikiza mtima kuikabe Israyeli muukapolo. Olamulira ena anyoza Yehova mofananamo, ndipo mafumu a muulosi wa Danieli amaphatikizidwapo. (Yesaya 36:13-20) Ndithudi, mfumu ya kumpoto yachita mopitirira pamenepo. Mngeloyo akuti: “Nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, . . . Ndipo sidzasamalira [Mulungu wa atate wake, NW], kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.”—Danieli 11:36, 37.
2, 3. Kodi ndim’njira yotani imene mfumu ya kumpoto inakanira “Mulungu wa atate wake” poyanja kulambira “mulungu” wina?
2 Kukwaniritsa mawu aulosi ameneŵa, mfumu ya kumpoto inakana “Mulungu wa atate wake” (kapena, “milungu ya makolo ake”), kaya ikhale milungu yachikunja ya Roma kapena mulungu wa Utatu wa Dziko Lachikristu. Hitler anagwiritsira ntchito Dziko Lachikristu kukwaniritsa zifuno zake koma maumboni akusonyeza kuti iye anali atalinganiza kuliloŵa mmalo ndi gulu latsopano, tchalitchi cha Germany. Womloŵa m’malo wake anachilikiza kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu. Motero mfumu ya kumpoto yadzipanga kukhala mulungu, ‘ikumadzikuza koposa onse.’
3 Ulosiwo ukupitiriza kuti: “Kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanaudziŵa, adzaulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.” (Danieli 11:38) Kwenikweni, mfumu ya kumpoto inaika chidaliro chake pasayansi yamakono ya zida zankhondo, “mulungu wa malinga.” Munthaŵi yonse ya mapeto, iye wafunafuna chipulumutso mwa “mulungu” ameneyu, akumawononga chuma chochuluka paguwa lake la nsembe.
4. Kodi ndichipambano chotani chimene mfumu ya kumpoto yakhala nacho?
4 “Adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wachilendo; aliyense womvomereza adzamchulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagaŵa dziko mwa mtengo wake.” (Danieli 11:39) Podalira mwa ‘mulungu [wake] wachilendo’ wankhondo, mfumu ya kumpoto yachita ‘mwamphamvu,’ ikumatsimikiza kukhala ulamuliro wa magulu ankhondo wolimba ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1) Awo amene anachilikiza ziphunzitso zake anafupidwa ndi chichilikizo cha ndale, ndalama, ndipo nthaŵi zina m’zankhondo.
“Munthaŵi ya Mapeto”
5, 6. Kodi ndimotani mmene mfumu ya kummwera ‘yalimbanirana’ ndi inzake, ndipo kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto yachitira?
5 Pa Danieli 11:40a timaŵerenga kuti: “[Munthaŵi ya mapeto, NW] mfumu ya kummwera idzalimbana naye.” Vesi limeneli ndi ena otsatira analingaliridwa kuti adzakwaniritsidwa mtsogolo mwathu. Komabe, ngati panopa “nthaŵi ya mapeto” ili yofanana ndi imene imatchulidwa pa Danieli 12:4, 9, tiyenera kuyembekezera kukwaniritsidwa kwa mawu ameneŵa m’masiku otsiriza onse. Kodi mfumu ya kummwera ‘yalimbana’ ndi mfumu ya kumpoto m’nthaŵi ino? Inde, yaterodi. Pambuyo pa nkhondo yadziko yoyamba, pangano lolanga mwamtendere linalidi ‘kulimbana,’ lochititsa kubwezera. Itapambana munkhondo yadziko yachiŵiri, mfumu ya kummwera inalunjikitsa zida zankhondo zowopsa za nyukliya pamdani wakeyo nilinganiza mgwirizano wamphamvu wa magulu ankhondo motsutsana naye, gulu lotchedwa NATO. Pamene zaka zinali kupita, ‘kulimbana’ kwake kunaphatikizapo kuzonda dziko la eni ndi zipangizo za luso lapamwamba ndiponso kuputa maiko ndi pakamwa ndi magulu ankhondo.
6 Kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto inachitira? “Mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kavumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzaloŵa m’maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.” (Danieli 11:40b) Mbiri ya masiku otsiriza yakhala ndi kufalikira kwa ulamuliro wa mfumu ya kumpoto. M’nkhondo yadziko yachiŵiri, “mfumu” ya Nazi inasefukira kunja kwa malire ake kuloŵa m’maiko apafupi. Pamapeto a nkhondoyo, “mfumu” yoiloŵa m’malo inamanga ufumu wamphamvu kunja kwa malire ake. Mu Nkhondo Yapakamwa, mfumu ya kumpoto inamenyana ndi wopikisana naye wake mwa kuchilikiza nkhondo za pakati pamitundu ina ndi ziukiro za mu Afirika, Asia, ndi Latin America. Iyo inazunza Akristu owona, ikumachepetsa (komatu osati kuimitsa) ntchito yawo. Ndipo kuukira kwake ndi magulu ankhondo ndi ndale kunaika maiko angapo muulamuliro wake. Zimenezi nzolingana kwambiri ndi momwe mngeloyo analoserera kuti: “Adzaloŵanso m’dziko lokometsetsalo [mkhalidwe wauzimu wa anthu a Mulungu] ndi maiko ambiri adzapasuka.”—Danieli 11:41a.
7. Kodi nkulephera kotani kumene kunalipo pakufutukuka kwa ulamuliro wa mfumu ya kumpoto?
7 Komabe, ngakhale kuti—m’lingaliro la wopikisana naye wake—mfumu ya kumpoto yalalira mochititsa mantha, iyo sinapeze chipambano chadziko. “Opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Moabu, ndi oyamba a ana a Amoni.” (Danieli 11:41b) M’nthaŵi zakale, Edomu, Moabu, ndi Amoni anali pakati pa Igupto ndi Suriya. Lerolino iwo angaonedwe kukhala akuimira maiko ndi magulu amene mfumu ya kumpoto inalalira koma inali yosakhoza kuwagonjetsa.
‘Igupto Sadzapulumuka’
8, 9. Kodi ndimotani mmene chiyambukiro cha mfumu ya kumpoto chamvedwera, ngakhale ndi wopikisana naye wake wamkulu?
8 Mngeloyo akupitiriza kunena kuti: “Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Aigupto lomwe silidzapulumuka. Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma [chobisika, NW] cha golidi, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Aigupto; Alubi ndi Akusi adzatsata mapazi ake.” (Danieli 11:42, 43) Ngakhale mfumu ya kummwera, “Igupto,” sinapulumuke ziyambukiro za ulamuliro wofutukuka wa mfumu ya kumpoto. Mwachitsanzo, iyo inagonjetsedwa mu Vietnam. Nangano bwanji za “Alubi ndi Akusi”? Maiko oyandikana ndi Igupto wakale ameneŵa angaphiphiritsirenso bwino lomwe mitundu imene ili yoyandikana ndi “Igupto” wamakono ndi kuti panthaŵi zina yakhala ‘yotsata mapazi,’ a mfumu ya kumpoto.
9 Kodi mfumu ya kumpoto yalamulira ‘chuma chobisika cha Igupto’? Eya, iyo sinagonjetsedi mfumu ya kummwera, ndipo kufikira mu 1993 mkhalidwe wadziko unakupanga kukhala kowonekera kuti sidzatero. Koma iyo inali ndi chiyambukiro champhamvu panjira imene mfumu ya kummwera inagwiritsirira ntchito chuma chake. Chifukwa cha kuwopa wopikisana nayeyo, mfumu ya kummwera yapereka chuma chambiri chaka chilichonse kuchilikizira magulu ankhondo apamtunda, apanyanja, ndi a mlengalenga kukhala amphamvu. Kaamba ka chifukwa chimenechi mfumu ya kumpoto inganenedwe kukhala ‘itachita mwamphamvu,’ kulamulira kayendetsedwe ka chuma cha mfumu ya kummwera.
Mkupiti Wotsiriza wa Mfumu ya Kumpoto
10. Kodi ndim’njira yotani imene mngelo akufotokozera mapeto a mpikisano wapakati pa mafumu aŵiriwo?
10 Kodi mpikisano umenewu wa mafumu aŵiriwo udzapitirizabe kosatha? Ayi. Mngeloyo anauza Danieli kuti: “Mbiri yochokera kummaŵa ndi kumpoto idzamvuta [mfumu ya kumpoto]; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuwononga konse ambiri. Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira [mapeto ake, NW] wopanda wina wakumthandiza.”—Danieli 11:44, 45.
11, 12. Kodi nzochitika zandale zaposachedwapa zotani zimene zachitika zokhudza mpikisano wa pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera, ndipo nchiyani chimene titi tidziŵe?
11 Zochitika zimenezi zidakali mtsogolo, chotero sitinganene mwatsatanetsatane mmene ulosiwo udzakwaniritsidwira. Posachedwapa, mkhalidwe wa ndale wa mafumu aŵiriwo wasintha. Mpikisano waukulu pakati pa United States ndi maiko a Kummaŵa kwa Ulaya wazilala. Ndiponso, Soviet Union anapasuka mu 1991 ndipo kulibenso.—Onani kope la Nsanja ya Olonda la March 1, 1992, pamasamba 4, 5.
12 Chotero kodi ndani amene ali mfumu ya kumpoto tsopano? Kodi iye ayenera kukhala limodzi la maiko amene kale anali mbali ya Soviet Union? Kapena kodi iye akusintha kudziŵika kwake kotheratu, monga momwe wachitira poyambapo nthaŵi zingapo? Sitinganene. Kodi ndani amene adzakhala mfumu ya kumpoto pamene lemba la Danieli 11:44, 45 likwaniritsidwa? Kodi mpikisano wa mafumu aŵiriwo udzabukanso? Nanga bwanji za zida zambiri zanyukliya zokundikidwazo zimene zidakalipobe m’maiko angapo? Nthaŵi yokha ndiyo imene idzapereka mayankho a mafunso ameneŵa.
13, 14. Kodi timadziŵanji ponena za mtsogolo mwa mafumu aŵiriwo?
13 Pali chinthu chimodzi chimene tikudziŵa. Posachedwapa, mfumu ya kumpoto idzachititsa mkupiti wankhondo umene udzayambitsidwa ndi ‘mbiri yochokera kummaŵa ndi kumpoto imene idzamvuta.’ Mkupiti umenewu udzachitika “mapeto” ake atangotsala pang’ono kudza. Tikhoza kudziŵa zochuluka ponena za “mbiri” imeneyi ngati tilingalira maulosi ena a Baibulo.
14 Komabe, choyamba, onani kuti zochita za mfumu ya kumpoto zimenezi sizikunenedwa kuti nzotsutsana ndi mfumu ya kummwera. Iyo sikugonjetsedwa ndi mdani wake wamkuluyo. Mofananamo, mfumu ya kummwera sikuwonongedwa ndi mfumu ya kumpoto. Mfumu ya kummwera (m’maulosi ena yosonyezedwa monga nyanga yotsiriza kutuluka pachilombo) ikuwonongedwa “popanda dzanja [laumunthu]” ndi Ufumu wa Mulungu. (Danieli 7:26; 8:25) Kwenikweni, mafumu onse apadziko lapansi potsirizira pake akuwonongedwa ndi Ufumu wa Mulungu pankhondo ya Armagedo, ndipo zimenezi mwachionekere ndizo zimene zikuchitikira mfumu ya kumpoto. (Danieli 2:44; 12:1; Chivumbulutso 16:14, 16) Pa Danieli 11:44, 45 pamafotokoza zochitika zimene zikutsogolera kunkhondo yotsiriza imeneyo. Mposadabwitsa kuti ‘sipadzakhala wothandiza’ pamene mfumu ya kumpoto iwonongedwa!
15. Kodi ndimafunso ofunika ati amene akutsalira oti ayankhidwe?
15 Pamenepo, kodi ndimaulosi ena ati amene amafotokoza za “mbiri” imene idzasonkhezera mfumu ya kumpoto kuyamba “kupha ndi kuwononga konse ambiri”? Ndipo kodi ndani amene ali “ambiri” amene iye adzawononga?
Mbiri Yochokera Kummaŵa
16. (a) Kodi nchochitika chapadera chotani chimene chiyenera kuchitika Armagedo isanadze? (b) Kodi ndani amene ali “mafumu ochokera potuluka dzuŵa”?
16 Nkhondo yotsiriza ya Armagedo isanachitike, mdani wamkulu wa kulambira kowona ayenera kuwonongedwa—Babulo Wamkulu wonga mkazi wachigololoyo, ulamuliro wa padziko lonse wa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 18:3-8) Chiwonongeko chake chikuonedweratu mwa kutsanulidwa kwa mbale yachisanu ndi chimodzi ya mkwiyo wa Mulungu pamtsinje wa Firate wophiphiritsira. Mtsinjewo ukuuma “kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuŵa.” (Chivumbulutso 16:12) Kodi mafumu ameneŵa ndayani? Sianthu enanso koma Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu!a
17. (a) Kodi Baibulo limatiuzanji ponena za chiwonongeko cha Babulo Wamkulu? (b) Kodi nchiyani chimene mbiri “yochokera kummaŵa” ingakhale?
17 Chiwonongeko cha Babulo Wamkulu chafotokozedwa bwino lomwe m’buku la Chivumbulutso kuti: “Nyanga khumi udaziona [‘mafumu’ olamulira m’nthaŵi ya mapeto], ndi chilombo [chilombo chofiiritsa, choimira gulu la Mitundu Yogwirizana], izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto.” (Chivumbulutso 17:16) Zowonadi, mitunduyo ‘ikulusira nyama zambiri’! (Danieli 7:5) Koma kodi nchifukwa ninji olamulira, kuphatikizapo mfumu ya kumpoto, adzawononga Babulo Wamkulu? Chifukwa chakuti ‘Mulungu wapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake.’ (Chivumbulutso 17:17) Mbiri “yochokera kummaŵa” ingatanthauzenso mchitidwe umenewu wa Yehova, pamene, mwanjira imene asankha, aika m’mitima mwa atsogoleri aumunthu lingaliro la kuwononga mkazi wachigololo wamkulu wachipembedzoyo.—Danieli 11:44.
Mbiri Yochokera Kumpoto
18. Kodi ndimbali ina iti imene mfumu ya kumpoto ikuukira, ndipo kodi imeneyo ikuika mfumuyo m’malo ati pamene mapeto ake afika?
18 Komanso pali mbali ina imene mfumu ya kumpotoyo ikuukira mwamkwiyo. Mngeloyo akuti “adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika.” (Danieli 11:45) M’nthaŵi ya Danieli, nyanja yamchere inali Mediterranean, ndipo phiri lopatulika linali Ziyoni, malo a kachisi wa Mulungu panthaŵi ina. Nchifukwa chake, m’kukwaniritsidwa kwa ulosiwo, mfumu yokwiya ya kumpotoyo ikuchititsa mkupiti wankhondo molimbana ndi anthu a Mulungu! Lerolino, m’lingaliro lauzimu, mawu akuti “pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika” amaika mfumuyo kukhala ili m’malo auzimu a atumiki odzozedwa a Mulungu, amene atuluka ‘m’nyanja’ ya mtundu wa anthu otalikirana ndi Mulungu ndipo ali ndi chiyembekezo cha kukalamulira m’phiri la Ziyoni la kumwamba ndi Yesu Kristu.—Yesaya 57:20; Ahebri 12:22; Chivumbulutso 14:1.
19. Monga momwe kwasonyezedwera muulosi wa Ezekieli, kodi tingadziŵe motani mbiri imene ikusonkhezera kuukira kwa Gogi? (Onani mawu amtsinde.)
19 Ezekieli, amene anakhalako m’tsiku la Danieli, nayenso analosera za kuukiridwa kwa anthu a Mulungu ‘m’masiku otsiriza.’ Iye anati udaniwo ukuyambitsidwa ndi Gogi wa Magogi, kutanthauza Satana Mdyerekezi. (Ezekieli 38:16) Mophiphiritsira, kodi nkumbali iti kumene Gogi akutulukira? Yehova, kupyolera mwa Ezekieli, akunena kuti: “Udzatuluka m’malo mwako m’malekezero a kumpoto.” (Ezekieli 38:15) Chifukwa chake, mbiri ‘yochokera kumpoto’ ingatanthauzedi manenanena onyenga a Satana osonkhezera mfumu ya kumpoto ndi mafumu ena onse kuukira anthu a Yehova.b—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 16:13, 14; 17:14.
20, 21. (a) Kodi nchifukwa ninji Gogi adzasonkhezera mitundu, kuphatikizapo mfumu ya kumpoto, kuukira anthu a Mulungu? (b) Kodi adzapambana m’kuukirako?
20 Gogi akulinganiza chiukiro chotheratu chimenechi chifukwa cha kulemerera kwa “Israyeli wa Mulungu,” amene, limodzi ndi khamu lalikulu la nkhosa zina, salinso mbali ya dziko lake. (Agalatiya 6:16; Yohane 10:16; 17:15, 16; 1 Yohane 5:19) Gogi akuyang’ana mwaukali pa “mtundu wa anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoŵeta [zauzimu] ndi chuma.” (Ezekieli 38:12; Chivumbulutso 5:9; 7:9) M’kukwaniritsa mawu ameneŵa, lerolino anthu a Yehova akulemerera koposa ndi kale lonse. M’maiko ambiri a ku Ulaya, Afirika, ndi Asia kumene panthaŵi ina analetsedwa, tsopano akulambira momasuka. Pakati pa 1987 ndi 1992, “zofunika” zoposa miliyoni imodzi zinachokera m’mitundu ya anthu ndi kuloŵa m’nyumba ya Yehova ya kulambira kowona. Kunena mwauzimu, iwo ngolemera ndi amtendere.—Hagai 2:7; Yesaya 2:2-4; 2 Akorinto 8:9.
21 Powona mkhalidwe Wachikristu wauzimu kukhala “midzi yopanda malinga” yosavuta kugonjetsa, Gogi akupanga kuyesayesa kwakukulu kuwononga chopinga chimenechi pakulamulira kwake anthu onse. (Ezekieli 38:11) Koma iye akulephera. Pamene mafumu apadziko lapansi aukira anthu a Yehova, iwo ‘adzafikira chimaliziro chawo.’ Motani?
Mfumu Yachitatu
22, 23. Pamene Gogi aukira, kodi ndani amene adzaima kuchilikiza anthu a Mulungu, ndipo ndi zotulukapo zotani?
22 Ezekieli akunena kuti kuukira kwa Gogi ndiko chizindikiro chakuti Yehova Mulungu auke mmalo mwa anthu ake ndi kuwononga magulu ankhondo a Gogi “pamapiri a Israyeli.” (Ezekieli 38:18; 39:4) Zimenezi zikutikumbutsa zimene mngelo anauza Danieli kuti: “Nthaŵi yomweyi adzaima Mikaeli kalonga wamkulu amene akuimirira m’malo mwa ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthaŵi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthaŵi yomwe ija; ndipo nthaŵi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m’buku.”—Danieli 12:1.
23 Mu 1914, Yesu—Mikaeli wankhondo wakumwambayo—anakhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 11:15; 12:7-9) Chiyambire pamenepo, waimirira ‘mmalo mwa ana a mtundu wa Danieli.’ Komabe, posachedwapa iye “adzaima” m’dzina la Yehova monga Mfumu Yankhondo yosagonjetseka, akumapereka “chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera [mbiri yabwino ya, NW] Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:8) Mitundu yonse ya padziko lapansi, kuphatikizapo mafumu a muulosi wa Danieli, “idzadziguguda pachifuwa.” (Mateyu 24:30) Pokhala ali ndi malingaliro oipa m’mitima mwawo kulinga kwa ‘anthu a mtundu wa Danieli,’ iwo adzawonongedwa kosatha ndi “Mikaeli, kalonga wamkulu.”—Chivumbulutso 19:11-21.
24. Kodi phunziro lino la ulosi wa Danieli liyenera kukhala nchiyambukiro chotani pa ife?
24 Kodi sitimalakalaka kudzaona chipambano chachikulu chimenecho cha Mikaeli ndi Mulungu wake, Yehova? Pakuti chilakiko chimenecho chidzatanthauza ‘chipulumutso,’ kwa Akristu owona. (Yerekezerani ndi Malaki 4:1-3.) Chifukwa chake, poyembekezera mtsogolo mwaphamphu, timakumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Lalikira mawu; chita nawo panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Tiyeni tigwire zolimba pa Mawu a moyo ndi kufunafuna mwakhama nkhosa za Yehova pamene nyengo yabwino ikupitirizabe. Tayandikira mapeto a makani a moyo. Mfupo yake ikuonekera. Tonsefe titsimikizetu kupirira kufikira mapeto ndipo motero tikakhale pakati pa awo amene adzapulumutsidwa.—Mateyu 24:13; Ahebri 12:1.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., pamasamba 229-30.
b Mwanjira ina, mbiri ‘yochokera kumpoto’ ingakhale ikuchokera kwa Yehova, polingalira za mawu ake kwa Gogi: “Ndidzakutembenuza . . . kukowa m’chibwano mwako ndi zokowera ndi kukutulutsa.” “Ndidzakutembenuza, . . . kukweza iwe uchoke kumalekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe kumapiri a Israyeli.”—Ezekieli 38:4; 39:2; yerekezerani ndi Salmo 48:2.
Kodi Mukuzindikira?
◻ Kodi ndimotani mmene mfumu ya kummwera yalimbanirana ndi mfumu ya kumpoto m’nthaŵi ya mapeto?
◻ Kodi nchiyani chimene tidzafunikira kudziŵabe ponena za chotulukapo cha mpikisano wa mafumu aŵiriwo?
◻ Kodi nzochitika ziŵiri ziti zimene motsimikizirika zidzaphatikizapo mfumu ya kumpoto Armagedo isanadze?
◻ Kodi ndimotani mmene “Mikaeli, kalonga wamkulu,” adzatetezerera anthu a Mulungu?
◻ Kodi tiyenera kuchita motani ndiphunziro lathu la ulosi wa Danieli?
[Zithunzi patsamba 19]
Mfumu ya kumpoto yalambira mulungu wosiyana ndi milungu ya makolo ake
[Mawu a Chithunzi]
Pamwamba kumanzere ndi pakati: UPI/Bettmann; pansi kumanzere: Reuters/Bettmann; pansi kumanja: Jasmin/Gamma Liaison