Mutu 16
Mafumu Olimbanawo Akuyandikira Chimaliziro Chawo
1, 2. Kodi ulamuliro wa mfumu ya kumpoto unasintha motani itatha nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse?
PONENA za mkhalidwe wa zandale wa United States ndi Russia, wafilosofi wachifalansa ndi katswiri wa mbiri yakale, Alexis de Tocqueville, mu 1835 analemba kuti: “Wina amagwiritsa ntchito ufulu pochita zinthu; winayo amagwiritsa ntchito ukapolo. Njira zawo . . . [zili] zosiyana kotheratu; komabe, aliyense amaoneka kukhala ataitanidwa mwa chinsinsi cha Mulungu kuti tsiku lina adzalamule tsogolo la theka la dziko.” Kodi mawu ameneŵa anakwaniritsidwa motani pambuyo pa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse? Katswiri wa mbiri yakale J. M. Roberts analemba kuti: “Kumapeto kwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, tsogolo la dziko linaonekadi kukhala m’manja mwa maboma aŵiri amphamvu koma osiyana kwambiri, wina unali ku Russia wakale, ndipo wina ku United States of America.”
2 M’kati mwa nkhondo ziŵirizo za padziko lonse, Germany anali mdani wamkulu wa mfumu ya kumwera—Ulamuliro Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain ndi America—ndipo unali utatenga malo a mfumu ya kumpoto. Komabe, itapita nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, dzikolo linagaŵika. West Germany anagwirizana ndi mfumu ya kumwera, ndipo East Germany anagwirizana ndi ulamuliro wina wamphamvu—chitaganya cha mayiko a Komyunizimu chotsogoleredwa ndi Soviet Union. Chitaganya chimenechi, kapena chiungwe chandale, chinaima monga mfumu ya kumpoto, motsutsana ndi mgwirizano wa Britain ndi America. Ndipo mkangano wa pakati pa mafumu aŵiriŵa unatchedwa Nkhondo ya Mawu imene inakhala kuchokera 1948 mpaka 1989. M’mbuyomo, mfumu ya kumpoto ya Germany inachita ‘motsutsana ndi chipangano chopatulika.’ (Danieli 11:28, 30) Kodi chitaganya cha Komyunizimu chikachita motani ndi chipanganocho?
AKRISTU OONA AKUGWA KOMA APAMBANA
3, 4. Kodi ndani “akuchitira choipa chipangano,” ndipo akhala paubale wotani ndi mfumu ya kumpoto?
3 “Akuchitira choipa chipanganocho,” anatero mngelo wa Mulungu, ‘[mfumu ya kumpoto] idzawaipsa, ndi kuwasyasyalika.’ Mngeloyo anawonjezera kuti: “Koma anthu akudziŵa Mulungu wawo adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu. Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi laŵi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.”—Danieli 11:32, 33.
4 Amene “akuchitira choipa chipanganocho” sangakhale ena koma atsogoleri a Matchalitchi Achikristu, amene amadzinenera kukhala Akristu koma machitidwe awo amanyoza dzina lenilenilo la Chikristu. M’buku lake lakuti Religion in the Soviet Union, Walter Kolarz anati: “[M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse] Boma la Soviet Union linapemphetsa chithandizo cha chuma ndi chichirikizo kwa Matchalitchi chotetezera dziko lawo.” Nkhondoyo itapita, atsogoleri a matchalitchi anayesa kusunga ubale wawowo, mosasamala kanthu za kusakhulupirira Mulungu kwa ulamuliro umene tsopano unali mfumu ya kumpoto. Choncho, kuposa kale lonse, panthaŵiyi Matchalitchi a Chikristu anakhala kwambiri mbali ya dzikoli—mpatuko wonyansa m’maso mwa Yehova.—Yohane 17:16; Yakobo 4:4.
5, 6. Kodi “anthu akudziŵa Mulungu wawo” ndani, ndipo zinthu zinawayendera motani mu ulamuliro wa mfumu ya kumpoto?
5 Nanga bwanji za Akristu oona—“anthu akudziŵa Mulungu wawo” ndi “aphunzitsi”? Ngakhale kuti anali ‘omvera maulamuliro aakulu,’ Akristu okhala mu ulamuliro wa mfumu ya kumpoto sanali mbali ya dziko. (Aroma 13:1; Yohane 18:36) Mmene anasamalira kupereka kwa “Kaisara zake za Kaisara,” anaperekanso kwa “Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Chifukwa chake, chikhulupiriro chawo chinaikidwa pachiyeso.—2 Timoteo 3:12.
6 Zotsatira zake zinali zakuti Akristu oona ‘anagwa’ komanso ‘anapambana.’ Anagwa m’ganizo lakuti anakumana ndi mazunzo aakulu, mpaka ena kuphedwa. Koma anapambana m’ganizo lakuti ambiri anakhalabe okhulupirika. Analaka dziko, monga anachitira Yesu. (Yohane 16:33) Komanso, sanaleke kulalikira, ngakhale ataponyedwa m’ndende. Mwakutero, ‘analangiza ambiri.’ Ngakhale kuti m’mayiko ambiri olamulidwa ndi mfumu ya kumpoto munali mazunzo, chiŵerengero cha Mboni za Yehova chinaŵirikiza. Chifukwa cha kukhulupirika kwa “aphunzitsi” amenewo, “khamu lalikulu” lomakulakulabe laonekera m’mayiko amenewo.—Chivumbulutso 7:9-14.
ANTHU A YEHOVA AYENGEDWA
7. Kodi ndi “thandizo laling’ono” lotani limene Akristu odzozedwa okhala mu ulamuliro wa mfumu ya kumpoto analandira?
7 “Pakugwa iwo [anthu a Mulungu] adzathandizidwa ndi thandizo laling’ono,” anatero mngeloyo. (Danieli 11:34a) Chipambano cha mfumu ya kumwera pankhondo yachiŵiri ya padziko lonse chinapereka mpumulo kwa Akristu ena okhala mu ulamuliro wa mfumu inzakeyo yodana nayo. (Yerekezani ndi Chivumbulutso 12:15, 16.) Mofananamo, aja amene anazunzidwa ndi mfumu yotsatirapo anapeza mpumulo nthaŵi ndi nthaŵi. Pamene Nkhondo ya Mawu inali kutha, atsogoleri ambiri anazindikira kuti Akristu okhulupirika sanali chiopsezo m’pang’ono pomwe moti anawapatsa chilolezo cha boma. Chithandizo chinafikanso kuchokera kwa khamu lalikulu limene linali kukula mofulumira, amene analabadira ulaliki wokhulupirika wa odzozedwawo ndi kuwathandiza.—Mateyu 25:34-40.
8. Kodi ena anadziphatika motani kwa anthu a Mulungu “ndi mawu osyasyalika”?
8 Sikuti onse amene amaonetsa kuti akutumikira Mulungu m’nthaŵi ya Nkhondo ya Mawu anali ndi zolinga zabwino. Mngeloyo anali atachenjeza kuti: “Ambiri adzaphatikizana nawo ndi mawu osyasyalika.” (Danieli 11:34b) Ambiri anaonetsa chidwi m’choonadi koma sanafune kudzipatulira kwa Mulungu. Komanso ena amene ankaoneka ngati alandira choonadi kwenikweni anali akazitape a boma. Lipoti lochokera ku dziko lina linati: “Ena mwa akapirikoni ameneŵa anali Akomyunizimu olumbiritsidwa amene anazembera m’gulu la Ambuye, ndipo anasonyeza changu chachikulu, mpaka anasankhidwa pamaudindo aakulu autumiki.”
9. N’chifukwa chiyani Yehova analola Akristu okhulupirika ena ‘kugwa’ chifukwa cha ozemberawo?
9 Mngeloyo anapitiriza kuti: ‘Adzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa [kuti awayenge, ndi kuwatsuka, NW], ndi kuwayeretsa, mpaka nthaŵi ya chitsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthaŵi yoikika.’ (Danieli 11:35) Ozemberawo anachititsa okhulupirika ena kugwa m’manja mwa akuluakulu a boma. Yehova analola zimenezo kuchitika pofuna kuyenga ndi kuyeretsa anthu ake. Monga mmene Yesu ‘anaphunzirira kumvera ndi [zinthu] adamva kuŵaŵa nazo,’ okhulupirika ameneŵanso anaphunzira kupirira mwa kuyesedwa kwa chikhulupiriro chawo. (Ahebri 5:8; Yakobo 1:2, 3; yerekezani ndi Malaki 3:3.) Choncho, iwo ali ‘oyengedwa, otsukidwa, ndi oyeretsedwa.’
10. Kodi mawu akuti “mpaka nthaŵi ya chitsiriziro” amatanthauzanji?
10 Anthu a Yehova anayenera kugwa ndi kuyengedwa “mpaka nthaŵi ya chitsiriziro.” N’zoona kuti iwo amayembekezera kuzunzidwa kufikira mapeto a dongosolo la zinthu loipali. Komabe, kuyeretsedwa kwa anthu a Mulungu chifukwa cha kuloweredwa ndi mfumu ya kampoto kunali pa “nthaŵi yoikika.” Choncho, pa Danieli 11:35, “nthaŵi ya chitsiriziro” iyenera kunena za chitsiriziro cha nyengo ya nthaŵi yofunikira kuti anthu a Mulungu ayengedwe pamene akupirira nkhanza za mfumu ya kumpoto. Mwachionekere, kugwako kunatha pa nthaŵi yoikika ndi Yehova.
MFUMUYO IDZIKUZA
11. Kodi mngelo ananenanji za maganizo a mfumu ya kumpoto kulinga ku ufumu wa Yehova?
11 Ponena za mfumu ya kumpoto, mngeloyo anawonjezera kuti: “Mfumu idzachita monga mwa chifuniro chake, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iliyonse [pokana kulemekeza ufumu wa Yehova] nidzanena zodabwitsa pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzachitidwa ukaliwo; pakuti chotsimikizika m’mtimacho chidzachitika. Ndipo sidzasamalira milungu ya [“Mulungu wa,” NW] makolo ake, kapena choikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.”—Danieli 11:36, 37.
12, 13. (a) Kodi mfumu ya kumpoto inakana motani “Mulungu wa makolo ake”? (b) Kodi “akazi” amene “chokhumba” chawo mfumu ya kumpoto sinachiganizire anali ndani? (c) Kodi mfumu ya kumpoto inalemekeza “mulungu” wotani?
12 Pokwaniritsa mawu aulosi ameneŵa, mfumu ya kumpoto inakana “Mulungu wa makolo ake,” monga Utatu wa Mulungu wa m’Matchalitchi Achikristu. Mayiko a Komyunizimu analimbikitsa chiphunzitso chokana Mulungu. Choncho mfumu ya kumpoto inadzipanga mulungu, ‘ikumadzikuza koposa onse.’ Posaganizira ‘chokhumba akazi’—akaziwo ndi mayiko ogonjera kwa iye, monga North Vietnam, amene anatumikira boma lake—mfumuyo inachita “monga mwa chifuniro chake.”
13 Popitiriza ulosiwo, mngeloyo anati: “Kumalo kwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ake sanamudziŵa, adzam’lemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.” (Danieli 11:38) Kwenikweni, mfumu ya kumpoto inaika chidaliro chake pa zida zankhondo zasayansi yamakono, “mulungu wa malinga.” Iye anafuna chipulumutso kwa “mulungu” ameneyu, napereka chuma chochuluka paguwa lake la nsembe.
14. Kodi mfumu ya kumpoto ‘inachita molimba’ m’njira yotani?
14 “Adzachita molimbana ndi malinga olimba koposa, pom’thandiza mulungu wachilendo; aliyense wom’vomereza adzam’chulukitsira ulemu, nadzawachititsa ufumu pa ambiri, nadzagaŵa dziko mwa mtengo wake.” (Danieli 11:39) Podalira “mulungu wachilendo” wa zida za nkhondo, mfumu ya kumpoto inachita ‘molimba,’ nikhala ulamuliro wamphamvu m’zankhondo mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1) Aja amene analimbikitsa mfundo zakezo anapatsidwa chithandizo m’zandale, zachuma, ndipo nthaŵi zina m’zankhondo.
‘KUKANKHANA’ M’NTHAŴI YOTSIRIZA
15. Kodi mfumu ya kumwera ‘inakankhana’ motani ndi mfumu ya kumpoto?
15 Mngeloyo anauza Danieli kuti: “Nthaŵi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana [“idzakankhana,” NW] naye.” (Danieli 11:40a) Kodi mfumu ya kumwera ‘yakankha’ mfumu ya kumpoto m’kati mwa “nthaŵi ya chimaliziro”? (Danieli 12:4, 9) Inde, yaterodi. Itatha nkhondo yoyamba ya padziko lonse, pangano la mtendere lokhaulitsira mfumu ya kumpoto ya panthaŵiyo—Germany—linalidi ‘kukankha,’ koiputa kuti ibwezere. Mfumu ya kumwera itapambana nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, inatetekera zida zake zoopsa za nyukiliya kwa mdani wakeyo ndipo inam’konzera mgwirizano wankhondo wamphamvu, wotchedwa North Atlantic Treaty Organization (NATO). Ponena za ntchito ya NATO, katswiri wa mbiri yakale wachibritishi anati: “Chinali chida chopambana ‘chokhaulitsira’ USSR, amene anaoneka kukhala wosokoneza kwambiri mtendere wa Ulaya. Ntchito yake inakhala zaka 40, ndipo inagwirika mwachipambano chosakanika.” M’kupita kwa zaka za Nkhondo ya Mawu, ‘kukankha’ kwa mfumu ya kumwera kunaphatikizapo ukapirikoni wa luso lapamwamba kwambiri limodzinso ndi zokambirana zokhudza ubale wawo komanso kuopseza ndi zida zankhondo.
16. Kodi mfumu ya kumpoto inachita motani pokankhidwa ndi mfumu ya kumwera?
16 Kodi mfumu ya kumpoto inachitapo motani? “Mfumu ya kumpoto idzam’dzera ngati kavumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzaloŵa m’mayiko, nadzasefukira ndi kupitirira.” (Danieli 11:40b) Mbiri ya masiku otsiriza yaonetsa kuti mfumu ya kumpoto yatsata mfundo zofutukula ulamuliro wake padziko lonse. M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, “mfumu” ya Nazi inasefukira malire ake mpaka m’mayiko ozungulira. Itatha nkhondo imeneyo, “mfumu” yotsatira inamanga ufumu waukulu wamphamvu. M’kati mwa Nkhondo ya Mawu, mfumu ya kumpoto inamenyana ndi mdani wake kudzera m’nkhondo zothandiza mayiko ena omenyana komanso magulu ogalukira boma mu Afirika, Asiya, ndi Latin America. Mfumu imeneyi inazunza Akristu oona, kuwatsekereza ntchito yawo—koma sanathe kuwalepheretsa. Ndipo ziopsezo zake m’zandale ndi m’zankhondo zinachititsa mayiko ambiri kukhala pansi pa ulamuliro wake. Mngeloyo anali atanenera ndendende kuti: “Adzaloŵanso m’dziko lokometsetsalo [malo auzimu a anthu a Yehova] ndi mayiko ambiri adzapasuka.”—Danieli 11:41a.
17. Kodi n’chifukwa chiyani mfumu ya kumpoto inalephera kufutukula ulamuliro wake padziko lonse?
17 Komabe, mfumu ya kumpoto sinathe kugonjetsa dziko lonse. Mngeloyo anati: “Opulumuka dzanja lake ndi aŵa: Edomu, ndi Moabu, ndi oyamba a ana a Amoni.” (Danieli 11:41b) M’nthaŵi zakale, Edomu, Moabu, ndi Amoni anali pakati pa chigawo cha mfumu ya kumwera ya Igupto ndi chigawo cha mfumu ya kumpoto ya Suriya. M’nthaŵi zamakono amaimira mayiko ndi mabungwe amene mfumu ya kumpoto inafuna kuwalamulira koma inalephera.
IGUPTO SAKUPULUMUKA
18, 19. Kodi mfumu ya kumwera inapanikizidwa motani ndi mphamvu ya mdani wake?
18 Mngelo wa Yehova anapitiriza kuti: ‘[Mfumu ya kumpoto] idzatambalitsiranso dzanja lake kumayiko; dziko la Aigupto lomwe silidzapulumuka. Ndipo idzachita mwamphamvu ndi chuma cha golidi, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Aigupto; Alubi [“Alibiya,” NW] ndi Akusi adzatsata mapazi ake.’ (Danieli 11:42, 43) Ngakhale mfumu ya kumwera, “Igupto,” sinapulumuke njira za mfumu ya kumpoto zofutukula ulamuliro wake. Mwachitsanzo, mfumu ya kumwera inagonjetsedwa koopsa ku Vietnam. Nanga bwanji za “Alibiya ndi Akusi”? Mayiko oyandikana ndi Igupto wakale ameneŵa angaimire mayiko oyandikana ndi “Igupto” wamakono (mfumu ya kumwera). Nthaŵi zina, ‘atsata mapazi’ a mfumu ya kumpoto.
19 Kodi mfumu ya kumpoto yachitadi mphamvu pa ‘chuma cha Igupto’? Iyo yakhaladi ndi ulamuliro pa njira imene mfumu ya kumwerayo yagwiritsira ntchito chuma chake. Poopa mdani wakeyo, mfumu ya kumwera yawononga chuma chochuluka kwambiri pofuna kukhala ndi gulu lankhondo lamphamvu, lakumtunda, lapanyanja, ndi lam’mwamba. M’ganizo limeneli, mfumu ya kumpoto ‘inachita mphamvu,’ kapena inalamulira kayendetsedwe ka chuma cha mfumu ya kumwera.
KUUKIRA KOMALIZA
20. Kodi mngelo akufotokoza motani kuukira komaliza kwa mfumu ya kumpoto?
20 Mkangano wa pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera—kaya m’zankhondo, zachuma, kapena m’njira zina—ukufika kumapeto ake. Pounika mbali zina za kulimbana kwam’tsogolo, mngelo wa Yehova anati: “Mbiri yochokera kum’maŵa ndi kumpoto idzam’vuta [mfumu ya kumpoto]; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuwononga konse ambiri. Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakum’thandiza.”—Danieli 11:44, 45.
21. Kodi n’chiyani chimene tisakudziŵabe ponena za mfumu ya kumpoto?
21 Pamene Soviet Union inapasuka mu December 1991, mfumu ya kumpoto inagwa koopsa. Kodi adzakhala mfumu imeneyi ndani pokwaniritsidwa Danieli 11:44, 45? Kodi lidzakhala limodzi la mayiko omwe anali mu Soviet Union? Kapena udzakhala ulamuliro wina wachilendo kotheratu, monga mmene zakhalira nthaŵi zingapo m’mbuyomu? Kodi mayiko owonjezereka tsopano amene akupanga zida za nyukiliya adzayambitsa mpikisano watsopano wa zida zankhondo ndi kutenga malo a mfumu imeneyo? Mayankho a mafunso ameneŵa adzadziŵika m’kupita kwa nthaŵi. Tingachite bwino kusaganizira za m’mutu mwathu. Pamene mfumu ya kumpoto iyamba kuukira kwake komaliza, kukwaniritsidwa kwa ulosiwo kudzaonekera bwino lomwe kwa onse okhala ndi chidziŵitso cha m’Baibulo.—Onani mutu wakuti “Mafumu a pa Danieli Chaputala 11,” tsamba 284.
22. Ndi mafunso otani amene angakhalepo ponena za kuukira komaliza kwa mfumu ya kumpoto?
22 Ngakhale zili choncho, tikudziŵa zimene mfumu ya kumpoto idzachita posachedwa. Pokwera mtima ndi mbiri “yochokera kum’maŵa ndi kumpoto,” adzatuluka iye ndi ukali waukulu ‘ndi kuwononga ambiri.’ Kodi ukali umenewu idzausonyeza kwa ndani? Ndipo ndi “mbiri” yotani imene idzabutsa chiwawa chimenecho?
AKWIYA NDI MBIRI YOVUTITSA MAGANIZO
23. (a) Kodi ndi chochitika chapadera chotani chimene chiyenera kuchitika isanakanthe Armagedo? (b) Kodi “mafumu ochokera potuluka dzuŵa” ndani?
23 Taganizirani zimene buku la Chivumbulutso limanena za kutha kwa Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Isanachitike “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” Armagedo, mdani wamkulu wa kulambira koona ameneyu ‘adzapserera ndi moto.’ (Chivumbulutso 16:14, 16; 18:2-8) Chiwonongeko chake chikusonyezedwa mwa kutsanuliridwa kwa mbale zisanu ndi imodzi za mkwiyo wa Mulungu pa mtsinje wophiphiritsa wa Firate. Mtsinjewo ukuphwa kotero “kuti ikonzeke njira ya mafumu ochokera potuluka dzuŵa.” (Chivumbulutso 16:12) Kodi mafumu ameneŵa ndani? Si ena alionse koma Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu!—Yerekezani ndi Yesaya 41:2; 46:10, 11.
24. Kodi “mbiri yochokera kum’maŵa” iyenera kukhala chiyani?
24 Chiwonongeko cha Babulo Wamkulu chafotokozedwa momvekera bwino m’buku la Chivumbulutso, limene limati: “Nyanga khumi udaziona [mafumu olamulira m’nthaŵi ya mapeto], ndi chilombo [United Nations], izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzam’khalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzam’psereza ndi moto.” (Chivumbulutso 17:16) Kodi olamulirawo adzamuwononga Babulo Wamkulu chifukwa chiyani? Chifukwa ‘Mulungu adzapatsa kumtima kwawo kuchita za m’mtima mwake.’ (Chivumbulutso 17:17) Mwa olamulira ameneŵa mulinso mfumu ya kumpoto. Zimene ikumva “kochokera kum’maŵa” zingatanthauzenso kachitidwe ka Yehova kameneka, pamene adzaika m’mitima ya atsogoleri aumunthu maganizo akuti awononge mkazi wachigololo wachipembedzo wamkuluyo.
25. (a) Kodi mkwiyo wa mfumu ya kumpoto ukulunjikitsidwa kwa ndani makamaka? (b) Kodi mfumu ya kumpoto ‘ikumanga kuti mahema a nyumba yake yachifumu’?
25 Koma mkwiyo wa mfumu ya kumpoto ukulunjikitsidwa kwa wina wapadera. Iye “adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika,” akutero mngeloyo. M’nthaŵi ya Danieli, nyanja yamchere inali nyanja ya Mediterranean ndipo phiri lopatulika linali phiri la Ziyoni, pamene panali kachisi wa Mulungu. Choncho, pakukwaniritsidwa kwa ulosiwo, mfumu ya kumpoto yokwiyayo ikuukira anthu a Mulungu. M’ganizo lauzimu, malo a “pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika” amaimira malo auzimu a atumiki odzozedwa a Yehova. Iwo atuluka mu “nyanja” ya mtundu wa anthu opatuka kwa Mulungu ndipo ali ndi chiyembekezo chodzalamulira m’Phiri la Ziyoni lakumwamba limodzi ndi Yesu Kristu.—Yesaya 57:20; Ahebri 12:22; Chivumbulutso 14:1.
26. Monga taonera mu ulosi wa Ezekieli, kodi woyambitsa uthenga “wochokera . . . kumpoto” ayenera kukhala ndani?
26 Ezekielinso, amene anakhalapo m’nthaŵi ya Danieli, ananenera za kuukiridwa kwa anthu a Mulungu mu “masiku otsiriza.” Iye anati adzayambitse nkhanzazo ndi Gogi wa Magogi, ndiye Satana Mdyerekezi. (Ezekieli 38:14, 16) Mophiphiritsa, kodi Gogiyo akubwera kuchokera kuti? Ku “malekezero a kumpoto,” akutero Yehova, kudzera mwa Ezekieli. (Ezekieli 38:15) Kaya kuukirako kukakhala koopsa chotani, sikudzawononga anthu a Yehova. Kuukira kumeneku kudzachititsidwa ndi Yehova pofuna kuwononga magulu a Gogi. Chotero, Yehova akuti kwa Satana: ‘Ndidzakukoŵa m’chibwano mwako ndi zokoŵera.’ ‘Ndidzakukweza iwe uchoke ku malekezero a kumpoto; ndipo ndidzadza nawe ku mapiri a Israyeli.’ (Ezekieli 38:4; 39:2) Choncho, uthenga “wochokera . . . kumpoto” umene ukunyanyula mtima wa mfumu ya kumpoto uyenera kuchokera kwa Yehova. Koma kunena za uthenga wake wa mbiri “yochokera kum’maŵa ndi kumpoto,” Mulungu yekha ndiye adziŵa, ndipo zidzadziŵika panthaŵi yake.
27. (a) N’chifukwa chiyani Gogi adzalimbikitsa mitundu, kuphatikizapo mfumu ya kumpoto, kuti aukire anthu a Yehova? (b) Kodi kuukira kwa Gogi kudzatha motani?
27 Ponena za Gogi, iye akukonzekera nkhondo yadzaoneni poona ulemerero wa “Israyeli wa Mulungu,” amene, limodzi ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” salinso mbali ya dzikoli. (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 7:9; Yohane 10:16; 17:15, 16; 1 Yohane 5:19) Gogiyo akuyang’anira ndi diso la nkhwezule “anthu osonkhanidwa mwa amitundu, odzionera zoŵeta ndi chuma [chauzimu].” (Ezekieli 38:12) Poona malo auzimu a Akristu monga “dziko la midzi yopanda malinga” limene akhoza kulifunkha mosavuta, Gogi akukunga nyonga zake zonse kuti afafanize anthu ameneŵa amene akuwaona kukhala chopinga kuti atenge mphamvu zonse zolamulira mtundu wa anthu. Koma zim’kanika. (Ezekieli 38:11, 18; 39:4) Pamene mafumu a dziko lapansi, kuphatikizapo mfumu ya kumpoto, aukira anthu a Yehova, ‘adzafikira chimaliziro chawo.’
‘MFUMUYO IDZAFIKA KUCHIMALIZIRO CHAKE’
28. Kodi tikudziŵanji za tsogolo la mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera?
28 Pakulimbana komaliza, mfumu ya kumpoto sidzalimbana ndi mfumu ya kumwera. Choncho, mfumu ya kumpoto sidzamalizidwa ndi mdani wake wamkulu. Mofananamo, mfumu ya kumwera sidzawonongedwa ndi mfumu ya kumpoto. Mfumu ya kumwera idzawonongedwa, “popanda dzanja” la munthu, koma ndi Ufumu wa Mulungu.a (Danieli 8:25) Ndipo pa Armagedo, mafumu onse a dziko lapansi adzachotsedwa ndi Ufumu wa Mulungu, ndipo n’zimene zidzaonekeranso mfumu ya kumpoto. (Danieli 2:44) Danieli 11:44, 45 amafotokoza zochitika zotsogolera ku nkhondo yomaliza imeneyo. N’chifukwa chake sipadzakhala “wakum’thandiza” pamene mfumu ya kumpoto ifika kuchimaliziro chake!
[Mawu a M’munsi]
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi mfumu ya kumpoto inasintha motani itatha nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse?
• Kodi pomalizira pake n’chiyani chidzaonekera mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera?
• Kodi mwapindula motani ndi kupenda ulosi wa Danieli wonena za mkangano wa pakati pa mafumu aŵiriwo?
[Chithunzi patsamba 284]
MAFUMU A PA DANIELI CHAPUTALA 11
Mfumu ya Mfumu ya
Kumpoto Kumwera
Danieli 11:5 Selukasi 1 Niketa Tolemi 1
Danieli 11:6 Antiyokasi 2 Tolemi 2
(mkazi wake Lodise) (mwana wamkazi Berinasi)
Danieli 11:7-9 Selukasi 2 Tolemi 3
Danieli 11:10-12 Antiyokasi 3 Tolemi 4
Danieli 11:13-19 Antiyokasi 3 Tolemi 5
(mwana wamkazi Woloŵa m’malo: Tolemi 6
Kileopatiya 1)
Oloŵa m’malo:
Selukasi 4 ndi
Antiyokasi 4
Danieli 11:20 Augusto
Danieli 11:21-24 Tiberiyo
Danieli 11:27-30a Ufumu Waukulu Britain, kenako
wa Germany Ulamuliro Wamphamvu
(Nkhondo yoyamba Padziko Lonse
ya padziko lonse) wa Britain ndi America
Danieli 11:30b, 31 Ufumu Wachitatu wa Hitler Ulamuliro Wamphamvu
(Nkhondo yachiŵiri Padziko Lonse
ya padziko lonse) wa Britain ndi America
Danieli 11:32-43 Chitaganya cha Ulamuliro Wamphamvu
mayiko a Komyunizimu Padziko Lonse
(Nkhondo ya Mawu) wa Britain ndi America
[Mawu a M’munsi]
b Ulosi wa pa Danieli chaputala 11 suneneratu mayina a maulamuliro andale amene amatenga malo a mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kumwera pa nthaŵi zosiyanasiyana. Mayinawo amadziŵika kokha pamene zochitikazo ziyamba kuoneka. Ndiponso, popeza kuti mkanganowo umachitika m’zigawozigawo, zimakhalapo nyengo zina zimene kulimbanako kumalekeka—mfumu ina imalamulira pamene inayo imangokhala.
[Chithunzi chachikulu patsamba 271]
[Zithunzi patsamba 279]
“Kukankha” kwa mfumu ya kumwera kwaphatikizapo ukapirikoni wa luso lapamwamba ndi kuopseza ndi zida zankhondo