Apereka Chiweruzo m’Chigwa Chotsirizira Mlandu
‘Amitundu akwerere ku chigwa cha Yosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse.’—YOWELI 3:12.
1. Kodi nchifukwa ninji Yoweli akuona aunyinji atasonkhana “m’chigwa chotsirizira mlandu”?
“AUNYINJI, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu!” Mawu amphamvu amenewo timawaŵerenga pa Yoweli 3:14. Kodi aunyinji ameneŵa asonkhaniranji? Yoweli akuyankha kuti: “Layandikira tsiku la Yehova.” Ndilo tsiku lalikulu lakuti Yehova adzichotsere chitonzo—tsiku lopereka chiweruzo pa makamu amene akana Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa mwa Kristu Yesu. Tsopano, “angelo anayi” a m’Chivumbulutso chaputala 7 adzataya “mphepo zinayi za dziko,” kudzetsa “masauko aakulu [“chisautso chachikulu,” NW], monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.”—Chivumbulutso 7:1; Mateyu 24:21.
2. (a) Kodi nchifukwa ninji malo operekerako chiweruzo cha Yehova akutchedwa moyenerera kuti “chigwa cha Yosafati”? (b) Kodi Yehosafati moyenerera anatani ataukiridwa?
2 Pa Yoweli 3:12, malo amene akuperekerako chiweruzo chimenechi akutchedwa “chigwa cha Yosafati.” Moyenerera, panthaŵi yovuta kwambiri m’mbiri ya Yuda, Yehova anapereka chiweruzo kumeneko m’malo mwa Mfumu yabwinoyo, Yehosafati, imene dzina lake limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Woweruza.” Kupenda zimene zinachitika nthaŵiyo kudzatithandiza kumvetsa bwino zimene zili pafupi kuchitika m’nthaŵi yathu. Nkhaniyo ikupezeka mu 2 Mbiri chaputala 20. M’vesi 1 ya chaputala chomwecho, timaŵerenga kuti “ana a Moabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.” Kodi Yehosafati anatani? Anachita zomwe atumiki okhulupirika a Yehova amachita nthaŵi zonse atakhala m’vuto. Anatembenukira kwa Yehova kuti amtsogoze, napemphera ndi mtima wonse nati: “Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nawo aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziŵa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.”—2 Mbiri 20:12.
Yehova Ayankha Pemphero
3. Kodi Yehova anapereka malangizo otani kwa Yuda pamene mitundu yapafupi inawaukira?
3 Pamene “Ayuda onse anakhala chiriri pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda awo, akazi awo, ndi ana awo,” Yehova anapereka yankho. (2 Mbiri 20:13) Monga momwe amagwiritsira ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” lerolino, momwemonso Wakumva pemphero wamkuluyo anapatsa mphamvu mneneri Yahazieli Mlevi kuti apereke yankho Lake kwa osonkhanawo. (Mateyu 24:45) Timaŵerenga kuti: “Atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhaŵa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. . . . Si kwanu kuchita nkhondo kuno ayi; chirimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova. . . . Musaope, kapena kutenga nkhaŵa; maŵa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.”—2 Mbiri 20:15-17.
4. Kodi ndi motani mmene Yehova anafunira kuti anthu ake akhale okangalika, osati ongokhala phee, pamene anayang’anizana ndi chitokoso cha adani awo?
4 Zimene Yehova anafuna kwa Mfumu Yehosafati ndi anthu ake zinali zambiri osati kungokhala chabe osachita kanthu, kuyembekeza kuti awalanditse mozizwitsa. Anafunikira kulimba mtima kuti apirire chitokoso cha mdani wawo. Mfumuyo ndi ‘Ayuda onse, ndi makanda awo omwe, akazi awo ndi ana,’ anasonyeza chikhulupiriro cholimba pamene, momvera, analaŵira m’mamaŵa ndi kutuluka kukakumana ndi makamu oukirawo. Paulendowo, mfumuyo inapitiriza kupereka malangizo ateokrase ndi chilimbikitso, niiti: “Limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.” (2 Mbiri 20:20) Kukhulupirira Yehova! Kukhulupirira aneneri ake! Imeneyo ndiyo inali njira yake ya chipambano. Momwemonso lero, pamene tipitiriza ndi kukangalika kwathu mu utumiki wa Yehova, tisakayiketu kuti mwina iye sadzalimbitsa chikhulupiriro chathu kuti tipambane!
5. Kodi Mboni za Yehova lerolino zili zokangalika motani pamene zikutamanda Yehova?
5 Monga Ayuda a m’tsiku la Yehosafati, tiyenera ‘kuyamika Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.’ Ndipo tingamyamike motani? Mwa kulalikira Ufumu mwachangu! Monga Ayudawo ‘anayamba kuimba, ndi kulemekeza,’ ifenso tiwonjezere ntchito pa chikhulupiriro chathu. (2 Mbiri 20:21, 22) Inde, tisonyezetu chikhulupiriro cholimba chofananacho pamene Yehova akukonzekera kuukira adani ake! Ngakhale kuti ulendowu ungaoneke wautali, titsimikizetu mtima kupirira, kukhala ndi chikhulupiriro chokangalika, monganso akuchitira anthu ake olakika kumadera okhala ndi mavuto aakulu padziko lero. M’maiko ena amene muli zizunzo zoopsa, chiwawa, njala, ndi mavuto aakulu a chuma, atumiki okhulupirika a Mulungu akuona chiwonjezeko chodabwitsa, malinga ndi 1998 Yearbook of Jehovah’s Witnesses.
Yehova Apulumutsa Anthu Ake
6. Kodi chikhulupiriro cholimba chimatithandiza motani kukhala okhulupirika lerolino?
6 Mitundu yosapembedza yozinga Yuda inayesa kuwameza anthu a Mulungu amenewo, koma ndi chikhulupiriro cholimba atumiki a Mulunguwo anachitapo kanthu mwa kuimbira Yehova zitamando. Ifenso tingasonyeze chikhulupiriro chofanana lero. Mwa kudzitangwanitsa ndi ntchito zotamanda Yehova, tidzalimbitsa zovala zathu zankhondo zauzimu, kusasiya mpata woti Satana aloŵetserepo machenjera ake. (Aefeso 6:11) Chikhulupiriro cholimba chidzatiletsa kuchenjeneka ndi zosangulutsa zoluluzika, kukonda chuma, ndi kuchita mphwayi imene ili mzimu wa dziko lomafa limene latizingali. Chikhulupiriro cholakika chimenechi chidzatithandiza kutumikirabe mokhulupirika limodzi ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” pamene atidyetsa mosaleka chakudya chauzimu choperekedwa “panthaŵi yake.”—Mateyu 24:45.
7. Kodi Mboni za Yehova zatani poukiridwa mosiyanasiyana?
7 Chikhulupiriro chathu chozikidwa pa Baibulo chidzatithandiza kulimbika polimbana ndi udani umene amabutsa aja okhala ndi mzimu wa “kapolo woipa” wotchulidwa pa Mateyu 24:48-51. Ampatuko ali yakaliyakali kufesa mabodza ndi manenanena m’maiko ambiri lerolino, ngakhale kuchita upo ndi olamulira ena pakati pa amitundu, kukwaniritsa ulosi umenewo ndendende. Pamene kwakhala koyenera, Mboni za Yehova zachitapo kanthu, malinga ndi Afilipi 1:7, ‘kudzikanira, ndi kutsimikiza Uthenga Wabwino.’ Mwachitsanzo, pa September 26, 1996, pamlandu wina ku Greece, oweruza asanu ndi anayi a European Court of Human Rights, ku Strasbourg, anagwirizana kugamula kuti “Mboni za Yehova zilinso pakati pa ‘zipembedzo zodziŵika,’” ndipo ziyenera kukhala ndi ufulu wotsata ziphunzitso zawo, chikumbumtima, ndi chikhulupiriro, ngakhalenso ufulu wolalikira chikhulupiriro chawo. Koma za ampatuko, chiweruzo cha Mulungu chimati: “Chidawayenera iwo cha nthanthi yoona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.”—2 Petro 2:22.
8. M’tsiku la Yehosafati, kodi Yehova anapereka motani chiweruzo pa adani a anthu Ake?
8 M’tsiku la Yehosafati, Yehova anapereka chiweruzo pa amene anafuna kuwononga anthu Ake. Timaŵerenga kuti: “Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m’phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha. Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m’phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwawononga psiti; ndipo atatha okhala m’Seiri, anasandulikirana kuwonongana.” (2 Mbiri 20:22, 23) Ayuda anatcha malowo Chigwa cha Beraka, Beraka kutanthauza “Dalitso.” Ngakhale nthaŵi yathu ino, chiweruzo chimene Yehova adzapereka pa adani ake chidzadzetsa madalitso aakulu kwa anthu ake.
9, 10. Kodi ndani amene asonyeza kuti ali oyenera chiweruzo choopsa cha Yehova?
9 Tingafunse kuti, Kodi ndani lero amene adzalandira chiweruzo choopsa cha Yehova? Kuti tipeze yankho lake, tipitenso ku ulosi wa Yoweli. Yoweli 3:3 akutchula adani a anthu ake omwe “apereka mwana wamwamuna kusinthana ndi mkazi wadama, nagula vinyo ndi mwana wamkazi kuti amwe.” Inde, iwo amaona atumiki a Mulungu kukhala apansi kwambiri kwa iwo, ana awo osasiyana konse ndi mtengo wa mkazi wadama kapena mtengo wa chikho cha vinyo. Adzayankha mlandu umenewo.
10 Oyeneranso chiweruzo ndi aja ochita chigololo chauzimu. (Chivumbulutso 17:3-6) Ndipo amene ali ndi mlandu makamaka ndi aja amene amasonkhezera olamulira andale kuzunza Mboni za Yehova ndi kuletsa ntchito yawo, monga momwe akhala akuchitira atsogoleri achipembedzo amsokonezo ku Eastern Europe posachedwapa. Yehova watsimikiza kuti adzatsutsa anthu ngati amenewo ochita zauchimo.—Yoweli 3:4-8.
“Mukonzeretu Nkhondo”!
11. Kodi Yehova akuwatokosa motani adani ake kuchita nkhondo?
11 Kenako, Yehova akupempha anthu ake kulengeza chitokoso chotsatirachi kwa amitundu: “Mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.” (Yoweli 3:9) Chimenechi ndi chilengezo cha nkhondo yachilendo—nkhondo yolungama. Mboni zokhulupirika za Yehova zimadalira zida zauzimu pamene zikuyankha manenanena onama, kutsutsa mabodza ndi choonadi. (2 Akorinto 10:4; Aefeso 6:17) Posachedwapa, Mulungu adzakonzeratu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Idzachotsa padziko lapansi onse otsutsa uchifumu wa Mulungu. Anthu ake padziko lapansi sadzamenyako nkhondoyo ayi. M’lingaliro lenileni ndiponso mophiphiritsa, iwo ‘asula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape.’ (Yesaya 2:4) Kusiyana ndi zimenezo, Yehova akutokosa amitundu kuti achitire mwina akumati: “Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo.” (Yoweli 3:10) Akuwapempha kuti agwiritsire ntchito zida zawo zonse zamakono. Koma amitunduwo sangapambane, pakuti nkhondoyo ndi chilakiko chomwe nza Yehova!
12, 13. (a) Ngakhale kuti Nkhondo ya Mawu inatha, nchiyani chikusonyeza kuti mitundu yambiri idakali yankhondo? (b) Kodi amitundu sanakonzekere chiyani?
12 Kumayambiriro a ma 1990, amitundu analengeza kuti Nkhondo ya Mawu yatha. Polingalira zimenezo, kodi cholinga chachikulu cha United Nations chokhazikitsa mtendere ndi chisungiko chakwaniritsidwa? Kutalitali! Kodi zimene zachitika ku Burundi, Democratic Republic of Congo, Iraq, Liberia, Rwanda, Somalia, ndi dziko lomwe kale linali Yugoslavia zikutiuza chiyani? Malinga ndi mawu a Yeremiya 6:14, iwo akunena kuti: “Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.”
13 Ngakhale kuti nkhondo yeniyeni yatha m’madera ena, maiko omwe ali mamembala a UN akali pampikisano wopanga zida zankhondo zamphamvu kwambiri. Ena akali nazo nkhokwe zawo za zida za nyukiliya. Enanso akupanga zida za makhemikolo kapena za tizilombo toyambitsa matenda zopululutsa nazo anthu. Pamene maiko amenewo asonkhana ku malo ophiphiritsira otchedwa Armagedo, akuwatokosa kuti: “Wofooka anene, Ndine wamphamvu. Fulumirani, idzani, amitundu inu nonse pozungulirapo; sonkhanani pamodzi.” Ndiyeno Yoweli akuwonjezapo pempho lake kuti: ‘Mutsitsire komweko amphamvu anu, Yehova.’—Yoweli 3:10, 11.
Yehova Ateteza Ake
14. Kodi amphamvu a Yehova ndani?
14 Kodi amphamvu a Yehova ndani? Pafupifupi nthaŵi 280 m’Baibulo, Mulungu woona akutchedwa “Yehova wa makamu.” (2 Mafumu 3:14) Makamu ameneŵa ndiwo magulu a angelo kumwamba okonzeka kuchita zimene Yehova awauza. Pamene Asuri anayesa kugwira Elisa, Yehova anachita kutsegula maso mnyamata wa Elisa kuti aone chifukwa chake iwo sakanapambana: “Taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.” (2 Mafumu 6:17) Yesu anati akanapempha Atate wake kutumiza “mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri.” (Mateyu 26:53) Pofotokoza Yesu pamene akubwera kudzapereka chiweruzo pa Armagedo, Chivumbulutso chimati: “Magulu ankhondo okhala m’Mwamba anamtsata Iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbu. Ndipo m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda Iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 19:14, 15) Moponderamo mphesa mophiphiritsamo mwalongosoledwa bwino kuti “moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.”—Chivumbulutso 14:17-20.
15. Kodi Yoweli akuifotokoza motani nkhondo ya Yehova pa amitundu?
15 Nangano kodi Yehova akuliyankha motani pempho la Yoweli lakuti atsitse amphamvu ake a Mulungu? Ndi mwa mawu otsatirawa olongosola bwino akuti: “Agalamuke amitundu, nakwerere ku chigwa cha Yosafati; pakuti ndidzakhala komweko kuweruza amitundu onse ozungulira. Longani zenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mphesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zawo nzazikulu. Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu. Dzuŵa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuŵala kwawo. Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mawu ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka.”—Yoweli 3:12-16.
16. Kodi ndani adzaphatikizidwa pa amene Yehova adzaweruza?
16 Monga momwedi dzinalo Yehosafati limatanthauzira kuti “Yehova Ndiye Woweruza,” momwemonso Mulungu, Yehova, adzatsimikiza kotheratu uchifumu wake pamene apereka chiweruzo. Ulosiwo ukuti omwe adzalandira chiweruzo choopsa ndi “aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu.” Otsalira pa ochirikiza chipembedzo chonyenga adzakhala pakati pa aunyinji amenewo. Adzaphatikizaponso aja otchulidwa m’Salmo lachiŵiri—amitundu, anthu, mafumu a dziko lapansi, ndi akulu—amene akonda dongosolo ili loipa la dziko m’malo ‘motumikira Yehova ndi mantha.’ Ameneŵa safuna ‘kupsompsona Mwanayo.’ (Salmo 2:1, 2, 11, 12) Savomereza kuti Yesu ndiye Mfumu yachiŵiri kwa Yehova. Ndiponso, aunyinji opita ku chiwonongeko adzaphatikizapo anthu onse amene Mfumu yaulemereroyo idzawaweruza kuti ndi “mbuzi.” (Mateyu 25:33, 41) Nthaŵi ikadzafika yakuti Yehova adzume ali ku Yerusalemu wakumwamba, Mfumu yake ya mafumuyo yoikika idzakwera kavalo kudzapereka chiweruzo. Inde, thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka! Komabe, tikudziŵa kuti: “Yehova adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israyeli.”—Yoweli 3:16.
17, 18. Kodi opulumuka chisautso chachikulu ndani, ndipo adzasangalala ndi mikhalidwe yotani?
17 Chivumbulutso 7:9-17 chimanena kuti amene adzapulumuka chisautso chachikulu ndiwo “khamu lalikulu” la anthu osonyeza chikhulupiriro m’mphamvu yowombola anthu ya mwazi wa Yesu. Ameneŵa adzatetezereka tsiku la Yehova, pamene aunyinji osonkhanawo a mu ulosi wa Yoweli akumana ndi chiweruzo choopsa. Kwa opulumuka, Yoweli akuti: “Mudzadziŵa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala m’Ziyoni, phiri langa lopatulika,”—malo okhalamo Yehova kumwamba.—Yoweli 3:17a.
18 Ndiyeno ulosiwo ukutiuza kuti malo a Ufumu wa Mulungu wakumwamba ‘adzakhala opatulika, osapitanso alendo pakati pake.’ (Yoweli 3:17b) Kumwamba ndi padziko lapansi mu Ufumu umenewo wakumwamba, simudzakhala alendo, pakuti onse adzagwirizana pakulambira koyera.
19. Kodi Yoweli akuchifotokoza motani chimwemwe chonga cha m’paradaiso cha anthu a Mulungu lerolino?
19 Ngakhale tsopano, anthu a Yehova padziko lapansi pano ali ndi mtendere wochuluka. Mogwirizana, akulengeza ziweruzo zake m’maiko oposa 230 ndiponso m’zinenero zoposa 300 zosiyanasiyana. Yoweli akulosera bwino lomwe za kulemera kwawo motere: “Kudzachitika tsiku ilo mapiri adzakhetsa vinyo wozuna, ndi pazitunda padzayenda mkaka, ndi m’mitsinje yonse ya Yuda mudzayenda madzi.” (Yoweli 3:18) Inde, Yehova adzapitiriza kutsanulira atamandi ake padziko lapansi madalitso osefukira ndi osangalatsa, kulemera, ndi madzi ambirimbiri a choonadi chamtengo wapatali. Uchifumu wa Yehova udzakhala utatsimikizidwa kotheratu m’chigwa chotsirizira mlandu, ndipo kudzakhala chimwemwe chokhachokha pamene iye adzakhala nawo kosatha anthu ake owomboledwa.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Yehova anawapulumutsa motani anthu ake masiku a Yehosafati?
◻ Kodi ndani amene Yehova aweruza kuti ayenera kuwonongedwa “m’chigwa chotsirizira mlandu”?
◻ Kodi amphamvu a Mulungu ndani ndipo adzachita chiyani pankhondo yomaliza?
◻ Kodi alambiri okhulupirika ali ndi chimwemwe chotani?
[Chithunzi patsamba 21]
Yuda anauzidwa kuti: ‘Musaope pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu’
[Chithunzi patsamba 23]
Yehova akutokosa adani ake kuti ‘asule makasu awo akhale malupanga’
[Chithunzi patsamba 24]
Baibulo limatchula za khamu lalikulu limene lidzapulumuka chisautso chachikulu