Tsiku la Yehova Layandikira
“Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m’dziko.”—YOWELI 1:2.
1, 2. Kodi ndi mkhalidwe wotani m’Yuda umene unasonkhezera Yehova kuuzira Yoweli kunena ulosi wake wamphamvu?
“KALANGA ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.” Chilengezo chimenechi kuopsa kwake! Unali uthenga wa Mulungu kwa anthu ake womwe mneneri wake Yoweli anaupereka.
2 Mawu amenewo a Yoweli 1:15 anawalembera ku Yuda, mwina cha m’chaka cha 820 B.C.E. Panthaŵiyo dzikolo linali ndi mapiri obiriŵira bwino ndi msipu. Linali ndi zipatso ndi dzinthu dzochuluka. Mabusa ake anali aakulu ndithu ndi obiriŵira. Koma zinthu sizinali bwino ayi. Kulambira Baala kunali ponseponse m’Yerusalemu ndi m’dziko lonse la Yuda. Anthu anali kuledzera ndipo amavina monyanyula pamaso pa mulungu wonyenga ameneyo. (Yerekezerani ndi 2 Mbiri 21:4-6, 11.) Kodi Yehova akanalola zonsezi kupitiriza?
3. Kodi Yehova anachenjeza za chiyani, ndipo mitundu iyenera kukonzekera chiyani?
3 Buku la Baibulo la Yoweli limafotokoza bwino za yankho lake. Yehova Mulungu anali kudzatsimikiza uchifumu wake ndi kuyeretsa dzina lake loyera. Tsiku lalikulu la Yehova linayandikira. Ndiyeno Mulungu anali kudzapereka chiweruzo pa mitundu yonse ku “chigwa cha Yosafati.” (Yoweli 3:12) Akonzekeretu nkhondo kumenyana ndi Wamphamvuyonse, Yehova. Ifenso tikuyang’anizana ndi tsiku lalikulu la Yehova. Chotero tiyeni tiwapende mosamalitsa mawu a ulosi wa Yoweli onena za nthaŵi yathu ndi nthaŵi yakale.
Tizilombo Tikwerera Dziko
4. Kodi chochitika chotchulidwa m’chenjezo la Yoweli chinali kudzakhala chachikulu motani?
4 Mwa mneneri wake, Yehova anati: “Imvani ichi, akuluakulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m’dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu? Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana awo, ndi ana awo afotokozere mbadwo wina.” (Yoweli 1:2, 3) Akulu ndi anthu onse anayenera kuyembekeza chinthu chimene sichinachitikepo m’moyo wawo kapena masiku a makolo awo. Chimenecho chinali kudzakhala chachilendo kwambiri koti adzachifotokozera mbadwo wachitatu! Kodi chochitika chodabwitsa chimenechi chinali chiyani? Kuti tipeze yankho, tiyeni tiyerekezere kuti tili m’tsiku la Yoweli kalelo.
5, 6. (a) Ufotokozeni mliri umene Yoweli akulosera. (b) Kodi Magwero a mliri umenewo anali ndani?
5 Tamverani! Yoweli akumva mawu obangula kutali. Thambo lichita mdima, ndipo kulira koopsa ndi kwachilendo kumeneko kukukula pamene mdimawo ufika pamwamba pa mutu. Ndiyeno mtambo wonga utsiwo ukutsika. Limenelo ndi khamu la tizilombo tambirimbiri. Ndiye tikuwononga zinthu kwadzaoneni! Tsopano, taonani Yoweli 1:4. Tizilombo timene tabwerati si dzombe chabe louluka losamukasamuka. Ayi! Zimene zikubweranso ndi makamu anjala a dzombe loyenda pansi, losauluka. Pofika ndi chimphepo, dzombelo likufika mwadzidzidzi, ndi phokoso lake ngati magaleta. (Yoweli 2:5) Chifukwa cha njala yake yaikulu, dzombe lambirimbiri lingasandutse paradaiso weniweni kukhala chipululu panthaŵi yochepa.
6 Ndiponso zimbalanga zikuyendayenda—mbozi. Makamu ambirimbiri a zimbalanga zanjala amadya masamba a zomera pang’onopang’ono, tsamba ndi tsamba, kufikira masamba a zomerazo atatheratu. Ndipo zilizonse zimene zisiya, dzombe lidya. Ndipo zimene dzombe lisiya, mphemvu zothamanga kwambiri zizitheratu. Koma tazindikirani izi: Pa Yoweli chaputala 2, vesi 11, Mulungu akutcha khamu la dzombelo “khamu lake lankhondo.” Inde, iye anali Magwero a mliri wa dzombelo umene unasakaza dzikolo ndi kudzetsa njala yaikulu. Liti? “Tsiku la Yehova” litayandikira kwambiri.
“Galamukani, Oledzera Inu”!
7. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo a Yuda anali otani? (b) Kodi atsogoleri a Dziko Lachikristu lerolino ali ofanana motani ndi atsogoleri achipembedzo a Yuda?
7 Pokhala atsogoleri achipembedzo a Yuda ndiwo khamu la anthu a mbiri yoipa, lamulo lotsatira likunenedwa kwa iwo kuti: “Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano; pakuti waletsedwa pakamwa panu.” (Yoweli 1:5) Inde, zidakwa zauzimu za Yuda anaziuza ‘kugalamuka,’ kusaledzeranso. Komatu musaganize kuti zimenezi zangokhala mbiri yakale basi. Tsopano lino, lisanafike tsiku lalikulu la Yehova, akuluakulu a Dziko Lachikristu mophiphiritsa aledzeratu naye vinyo watsopano koti sakumva lamulo limeneli la Wam’mwambamwamba. Mmene adzadabwira nanga pamene tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova lidzawagalamutsa kuwachotsa vinyo m’mutu!
8, 9. (a) Kodi Yoweli akulifotokoza motani dzombe ndi mliri wake? (b) Kodi dzombe likuimira yani lerolino?
8 Tayang’anani khamu lalikululo la dzombe! “Mtundu wadza, wakwerera dziko langa, wamphamvu wosaŵerengeka, mano ake akunga mano a mkango, nukhala nawo mano achibwano a mkango waukulu. Unawonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nuukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka. Lirani ngati namwali wodzimangira m’chuuno chiguduli, chifukwa cha mwamuna wa unamwali wake.”—Yoweli 1:6-8.
9 Kodi umenewu wangokhala chabe ulosi wonena za “mtundu” wa dzombe lokwerera Yuda? Ayi, umakhudzanso zina zambiri. Pa Yoweli 1:6 ndi Chivumbulutso 9:7, anthu a Mulungu akuimiridwa ndi dzombe. Khamu lamakono la dzombelo si china ayi kusiyapo khamu lankhondo la dzombe lodzozedwa la Yehova, limene tsopano latsagana ndi anzawo okwanira ngati 5,600,000 a “nkhosa zina” za Yesu. (Yohane 10:16) Kodi sizikukukondweretsani kukhala pakati pa namtindi ameneyu wa alambiri a Yehova?
10. Kodi mliri wa dzombe ukuchita zotani m’Yuda?
10 Pa Yoweli 1:9-12, tikuŵerenga za zotsatira zake za mliri wa dzombe. Makamu ake otsatizana akuwonongeratu dzikolo. Posoŵa dzinthu, vinyo, ndi mafuta, ansembe osakhulupirikawo akulephera kupitiriza ntchito yawo. Ndi nthaka yomwe ikulira, pakuti dzombelo lawononga mbewu zake, ndipo mitengo ya zipatso yatsala yopanda zipatso. Pokhala mitengo ya mpesa yawonongeka, palibenso vinyo wa ambiyang’ambewo olambira Baala amenenso ndi zidakwa zauzimu.
“Dzigugudeni Pachifuŵa, Ansembe Inu”
11, 12. (a) Kodi ndani amadzitcha ansembe a Mulungu lerolino? (b) Kodi mliri wamakono wa dzombe ukuwakhudza motani atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu?
11 Tamverani uthenga wa Mulungu kwa ansembe amenewo opulupudza: “Mudzimangire chiguduli m’chuuno mwanu, nimulire [“dzigugudeni pachifuŵa,” NW], ansembe inu; bumani, otumikira kuguwa la nsembe inu.” (Yoweli 1:13) Pakukwaniritsidwa kwake koyamba kwa ulosi wa Yoweli, ansembe achilevi anatumikira kuguwa la nsembe. Nanga bwanji za kukwaniritsidwa kwake komaliza? Lero, akuluakulu a Dziko Lachikristu atenga udindo wotumikira kuguwa la nsembe la Mulungu, akumati ali atumiki ake, “ansembe” ake. Koma kodi chikuchitika nchiyani tsopano pokhala kuti dzombe lamakono la Mulungu lili yakaliyakali?
12 Pamene “ansembe” a Dziko Lachikristu aona anthu a Yehova ali pantchito ndi kuwamva akuchenjeza za chiweruzo cha Mulungu, mtima wawo sukhala m’malo ayi. Amadziguguda pachifuŵa chifukwa chokwiya ndi kusakaza kwake kwa uthenga wa Ufumu. Ndipotu amabuma pamene nkhosa zawo ziwathaŵa. Popeza mabusa awo akhala apululu, afunde chiguduli usiku, kulirira malipiro awo otayika. Posakhalitsa, ntchito yawo idzawatheranso! Makamaka, Mulungu akuwauza kuti alire usiku wonse chifukwa chimaliziro chawo chayandikira.
13. Kodi Dziko Lachikristu lonse lidzalabadira chenjezo la Yehova?
13 Malinga ndi Yoweli 1:14, kuti zinthu ziwakhalire bwino, afunika kulapa ndi ‘kufuulira kwa Yehova’ kuti awathandize. Kodi tingayembekeze akuluakulu onse a Dziko Lachikristu kutembenukira kwa Yehova? Kutalitali! Ena mwa iwo angalabadire chenjezo la Yehova. Koma njala yawo yauzimu ya atsogoleri achipembedzo ameneŵa ndi anthu awo idzapitiriza. Mneneri Amosi analosera kuti: “Taonani, akudza masiku, ati Ambuye Yehova, akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Koma ife tikuyamikira chotani nanga phwando lauzimu la zinthu zonona limene Mulungu mwachikondi akutikonzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”!—Mateyu 24:45-47.
14. Kodi mliri wa dzombe uli chizindikiro cha chiyani?
14 Mliri wa dzombe unali ndipo ukali chizindikiro cha kanthu kena. Kanthu kanji? Yoweli akutiuza mosabisa, kuti: “Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.” (Yoweli 1:15) Khamu la dzombe la Mulungu limene likuloŵerera dziko lonse lero likusonyeza bwino kuti tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova layandikira. Inde, anthu onse a mtima wowongoka akulilakalaka tsiku lapaderalo la kuŵerengera mlandu pamene Yehova adzapereka chiweruzo chake pa oipa ndi kuwagonjetsa monga Mfumu ya Chilengedwe Chonse.
15. Poona mkhalidwe wapululu wa dziko, kodi amene alabadira machenjezo a Mulungu akutani?
15 Malinga ndi zimene Yoweli 1:16-20 akusonyeza, chakudya chinasoŵeratu m’Yuda wakale. Ngakhalenso chimwemwe. Zosungiramo zinawonongeka, ndipo nkhokwe zinapasuka. Posoŵa msipu chifukwa chakuti dzombe linapululutsa zomera, ng’ombe zinapupulikapupulika zitasokonezeka ndipo nkhosa zinafa. Limenelo linali tsoka lalikulu kwambiri. Nanga zinthu zinali bwanji kwa Yoweli mavutowo adakali choncho? Malinga ndi vesi 19, iye anati: “Ndifuulira kwa Inu Yehova.” Leronso, ambiri akulabadira machenjezo a Mulungu ndi kufuulira kwa Yehova Mulungu mwachikhulupiriro.
“Tsiku la Yehova Lilinkudza”
16. Kodi nchifukwa ninji “okhala m’dziko” ayenera kunjenjemera?
16 Tamverani lamulo ili lochokera kwa Mulungu: “Muombe lipenga m’Ziyoni, nimufuulitse m’phiri langa lopatulika; onse okhala m’dziko anjenjemere.” (Yoweli 2:1) Nchifukwa ninji ayenera kutero? Ulosiwo ukuyankha: “Pakuti tsiku la Yehova lilinkudza, pakuti liyandikira; tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m’mbandakucha moyalika pamapiri.” (Yoweli 2:1, 2) Tsiku lalikulu la Yehova nlofulumizadi.
17. Kodi dziko ndi anthu m’Yuda anakhudzidwa motani ndi mliri wa dzombe?
17 Taganizani za zotsatira zake za masomphenya a ulosiwo pamene dzombe losatopalo linasandutsa mundawo wonga Edene kukhala chipululu. Tamverani mmene akufotokozera khamu la dzombelo: “Maonekedwe awo aoneka ngati akavalo, nathamanga ngati akavalo ankhondo. Atumphako ngati mkokomo wa magaleta pamwamba pa mapiri, ngati kulilima kwa malaŵi a moto akupsereza ziputu, ngati mtundu wamphamvu wa anthu ondandalikira nkhondo. Pamaso pawo mitundu ya anthu ikumva zoŵaŵa, nkhope zonse zitumbuluka.” (Yoweli 2:4-6) Pamene mliri wa dzombe unakantha m’tsiku la Yoweli, nsautso ya olambira Baala inakula, ndipo nkhope zawo zinasonyeza nkhaŵa yawo.
18, 19. Kodi ntchito ya anthu a Mulungu lerolino yakhala motani ngati mliri wa dzombe?
18 Kulibe chimene chinaletsa dzombe ladongosolo ndi losatopa limenelo. Linathamanga “ngati amphamvu” nilikwera ndi malinga omwe. Pamene ‘lina linagwa m’zida, lina siinathyoke nkhondo yawo.’ (Yoweli 2:7, 8) Chimenechitu ndi chithunzi cha ulosi chooneka bwino kwambiri cha khamu lamakono la Mulungu la dzombe lophiphiritsa! Leronso, khamu la dzombe la Yehova likulunjikabe kutsogolo. Palibe “linga” limene likulilephera kukwera. Silimataya kukhulupirika kwake kwa Mulungu koma nlokonzeka kufa, monga zinachitira Mboni zikwizikwi zimene ‘zinagwa m’zida’ chifukwa chokana kutamanda Hitler mu ulamuliro wa Germany wa Nazi.
19 Khamu la dzombe lamakono la Mulungu lachitira umboni mosamalitsa ‘m’mudzi’ wa Dziko Lachikristu. (Yoweli 2:9) Lachita zimenezo padziko lonse lapansi. Lidakakwerabe zopinga zonse ndi kuloŵa m’nyumba zambirimbiri, kufikira anthu m’makwalala, ndi kulankhula nawo pafoni, ndi kuonana nawo mwanjira iliyonse yotheka pamene likulengeza uthenga wa Yehova. Inde, lagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo mamiliyoni zikwi zambiri ndipo lidzagaŵirabe ambirimbiri pautumiki wawo wosatha—poyera ndi kunyumba ndi nyumba.—Machitidwe 20:20, 21.
20. Kodi ndani akuchirikiza dzombe lamakono, ndipo patsatira zotani?
20 Yoweli 2:10 akusonyeza kuti khamu lalikulu la dzombelo lili ngati mtambo umene ungadetse dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi. (Yerekezerani ndi Yesaya 60:8.) Kodi mukukayika za amene akuchirikiza khamu lankhondo limeneli? Mawu amphamvu oposa kubangula kwa dzombelo akumveka pa Yoweli 2:11: “Yehova amveketsa mawu ake pamaso pa khamu lake lankhondo; pakuti a m’chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti iye wakuchita mawu ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?” Inde, Yehova Mulungu akutumiza khamu lake lankhondo la dzombe tsopano—lisanafike tsiku lake lalikulu.
‘Yehova Sazengereza’
21. Kodi chidzachitika nchiyani pamene ‘tsiku la Yehova lidza ngati mbala’?
21 Monga Yoweli, mtumwi Petro analankhula za tsiku lalikulu la Yehova. Analemba kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; mmene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.” (2 Petro 3:10) Mwa mphamvu ya Satana Mdyerekezi, “miyamba” yoipa ya maboma ikulamulira “dziko,” kutanthauza, anthu otalikirana ndi Mulungu. (Aefeso 6:12; 1 Yohane 5:19) Miyamba yophiphiritsa imeneyi ndi dziko siidzapulumuka kutentha kwa mkwiyo wa Mulungu patsiku lalikulu la Yehova. M’malo mwake, padzakhala ‘miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmene mudzakhalitsa chilungamo, monga mwa lonjezano lake.’—2 Petro 3:13.
22, 23. (a) Kodi tiyenera kuchitanji poona kuleza mtima kwachifundo kwa Yehova? (b) Kodi tiyenera kuchitanji poona kuti tsiku la Yehova layandikira?
22 Pokhala ndi zochenjenetsa zonse zamakono ndi ziyeso pa chikhulupiriro chathu, tingaiŵale kuti nthaŵi zathu zino zikufuna changu. Koma pamene dzombe lophiphiritsa likumkabe patsogolo, anthu ambiri akulabadira uthenga wa Ufumu. Ngakhale kuti Mulungu walola nthaŵi ya zimenezi, tisaganize kuti kuleza mtima kwake ndi kuchedwa ayi. “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”—2 Petro 3:9.
23 Pamene tikuyembekeza tsiku lalikulu la Yehova, tilabadiretu mawu a Petro olembedwa pa 2 Petro 3:11, 12 akuti: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, mmenemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam’mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.” Mayendedwe ameneŵa amaphatikizapo kuyendera kwathu limodzi ndi khamu la Yehova la dzombe mwa kutengamo mbali nthaŵi zonse ndipo mwatanthauzo m’kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mapeto asanafike.—Marko 13:10.
24, 25. (a) Kodi mukumva bwanji pokhala ndi mwayi wogwira nawo ntchito ya khamu la dzombe la Yehova? (b) Kodi Yoweli akudzutsa funso lotani latanthauzo?
24 Khamu la dzombe la Mulungu silidzasiya ntchito yake mpaka litafika tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Kukhalapo kwake kwa khamu la dzombe losaletseka limeneli ndiko umboni wosakanika wakuti tsiku la Yehova layandikira. Kodi simuli wokondwa kutumikira limodzi ndi dzombe la Mulungu lodzozedwa ndi anzake pakuukira komaliza lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova?
25 Ndipotu tsiku la Yehova lidzakhala lalikulu zedi! Ndiye chifukwa chake akufunsa kuti: “Akhoza kupirira nalo ndani?” (Yoweli 2:11) Funso limeneli ndi enanso ambiri adzayankhidwa m’nkhani ziŵiri zotsatira.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova anachenjeza kuti kudzakhala mliri wa tizilombo m’Yuda?
◻ Pakukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi wa Yoweli, kodi dzombe la Yehova ndani?
◻ Kodi atsogoleri a Dziko Lachikristu amaumva motani mliri wa dzombe, ndipo kodi ena mwa iwo angazipeŵe motani zotsatira zake?
◻ Kodi mliri wa dzombe wakula motani m’zaka za zana la 20, ndipo upitirizabe mpaka liti?
[Chithunzi patsamba 9]
Mliri wa tizilombo unali chizindikiro cha kanthu kena koopsa koposa
[Mawu a Chithunzi]
Mtengo wosabala: Chithunzi cha FAO/G. Singh
[Chithunzi patsamba 10]
Yehova Mulungu ndiye akuchirikiza mliri wamakono wa dzombe
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Dzombe: Chithunzi cha FAO/G. Tortoli; nthenje ya dzombe: Chithunzi cha FAO/Desert Locust Survey