CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOWELI 1-3
“Ana Anu Aamuna ndi Ana Anu Aakazi Adzanenera”
Akhristu odzozedwa amagwira ntchito yonenera. Iwo amauza ena za “zinthu zazikulu za Mulungu” ndipo amalengeza “uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mac. 2:11, 17-21; Mat. 24:14) Ankhosa zina amathandiza odzodzedwawa pogwira nawo ntchito yolalikira.
Kodi ‘kuitana pa dzina la Yehova’ kumatanthauza chiyani?
Kudziwa dzinalo
Kulemekeza dzinalo
Kudalira komanso kukhulupirira mwiniwake wa dzinalo
Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndingathandize bwanji Akhristu odzozedwa omwe amagwira ntchito yonenera?’