Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Yoweli 1:1–3:21
Itanirani pa Dzina la Yehova ndi Kupulumuka!
“NGATI mliriwo sulamulirika, iwo ukafalikira Kum’mawa kwa Africa ndi ku Near East. Likakhala tsoka.” Inanena tero nduna ya UN Food and Agriculture Organization ponena za tizirombo tanjala tomwe pa nthaŵi ino tikuloŵerera kumpoto cha kumadzulo kwa Africa mwa mabiliyoni—dzombe.
Mu chifupifupi chaka cha 820 B.C.E., mneneri wa Mulungu Yoweli analankhula ponena za mliri wofananawo. M’mawu owonekera osapambanika kaamba ka kulongosoka ndi kutsimikizirika, analongosola mmene mtundu wa Yuda ukasakazidwira ndi kupha kwa tizirombo. Ngakhale kuli tero, mliri umenewo unali wochitira chithunzi chinachake chowonekera koposa chiwopsyezo cha kulinganizika kwa unansi pakati pa zinthu zamoyo ndi malo ozizinga. Kunali kulengezedwa kwa “tsiku la Yehova”! Mbadwo wathu ukuyang’anizana ndi “tsiku lowopsya limenelo” ndi mkwiyo wake wonse wa chiwonongeko. Ndi chiyembekezo chotani cha chipulumutso chomwe chiripo? Ndipo kodi ndi maphunziro otani amene tingaphunzire kuchokera ku bukhu la ulosi la Yoweli?
Kulowerera kwa Tizirombo Kochititsa Mantha
Kulapa kuli kofunikira kaamba ka chipulumutso mkati mwa tsiku lowopsya la Yehova. Kupyolera m’maso a Yoweli, tikuwona tsoka pamene dziko likuchotseredwa zomera ndi unyinji wa zimbalanga, dzombe, zirimanine, ndi mphemvu. Ansembe, amuna akulu, ndi nzika za Yuda zikufulumizidwa kulapa “nafuulira Yehova kaamba ka thandizo.” Zosungiramo zawonongeka, ndipo nkhokwe zapasuka popeza zakhala zopanda zotulutsa. Nyama zoweta ziyendayenda mosokonezeka, kufunafuna podyera popanda phindu. Ndi tsiku lopasula chotani nanga kuchokera kwa Wamphamvuyonseyo!—1:1-20.
Kuyandikira kwa tsiku la Yehova kuyenera kutifulumiza ife kudziloŵetsa mu machitidwe oyera ndi zochita zaumulungu. (2 Petro 3:10-12) Yoweli akutitheketsa ife kuwona ilo monga tsiku la mdima, mitambo, ndi mitambo yochindikala. Dzombelo liri kalambulabwalo wochititsa mantha wa tsiku limenelo. M’kugalamuka kwawo, dziko la Yuda longa Edeni likhala chipululu chosakazidwa. Kowopsya, kachiŵirinso, kuli kumvekera kwenikweni kwa dzombelo, popeza kuli ngati kuja kwa gareta ndi kwa moto wowopsya wopsyereza ziputu. Pamene dzombelo likuyandikira “ngati mtundu wamphamvu wa anthu, ondandalikira nkhondo,” liphimba malinga, kuthamangira m’mizinda, ndi kuloŵa m’nyumba. Ngakhale dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi zadetsedwa mkati mwa ‘tsiku lowopsya la Yehova.’—2:1-11.
Njira ya Chipulumutso
Kaamba ka chipulumutso, tiyenera kuzindikira kuti ‘Yehova ali Mulungu ndipo palibe wina.’ “Munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse,” akuchenjeza tero Yehova. Achikulire ndi achichepere akufulumizidwa kusonkhana mu msonkhano wowona mtima kupempha chiyanjo chaumulungu. Mulungu adzasonyeza kumvera chifundo, kubwezera kaamba ka kusakaza kwa tiziromboto, ndi kudalitsa anthu ake ndi zochuluka. Awo ozindikira malo a Yehova monga Mulungu yekha wowona ndi Magwero a chipulumutso sadzachititsidwa manyazi.—2:12-27.
Chipulumutso chathu chimadaliranso pa kuitanira pa dzina la Yehova m’chikhulupiriro. Lisanadze “tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsya,” Mulungu ‘adzatsanulira mzimu wake pa anthu onse.’ Achichepere ndi achikulire, amuna ndi akazi, adzachita ntchito yolosera. Chotero, ambiri adzadziŵa kuti ‘aliyense wodzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.’—2:28-32.
Chiweruzo Pa Mitundu
Yehova adzapulumutsa anthu ake okhulupirika pamene apereka chiweruzo pa a mitundu. (Yerekezani ndi Ezekieli 38:18-23; Chibvumbulutso 16:14-16.) Turo, Sidoni, ndi Filistiya ayenera kulipira kaamba ka kuvutitsa anthu a Mulungu ndi kuwagulitsa iwo mu ukapolo. Yehova adzabweretsa andende a Yuda ndi Yerusalemu, ndipo akutokosa adani ake, akumanena kuti: “Mudonzeretu nkhondo!” Koma iwo sali olingana ndi Mulungu, yemwe akupereka chiweruzo pa iwo mu “chigwa cha Yosafati” chophiphiritsira. Ngakhale kuti miyamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka, Yehova adzakhala populumukirapo kaamba ka anthu ake. Okhulupirika adzapulumuka chiweruzo pa amitundu ndipo adzasangalala ndi moyo pansi pa mikhalidwe ya paradaiso.—3:1-21.
Maphunziro ofunika kukumbukira: Kulapa kuli kofunikira pasadakhale ngati munthu akayenera kupulumutsidwa mkati mwa tsiku lowopsya la Yehova. Kuyandikira kwa tsikulo kuyenera kutifulumidzitsa ife kudziloŵetsa m’machitachita oyera ndi zochita zaumulungu. Ndithudi, chipulumutso chathu chimadalira pa kuzindikira kuti Yehova yekha ali Mulungu. Ndipo ngati tiitanira pa dzina lake m’chikhulupiriro, iye adzatipulumutsa ife pamene apereka chiweruzo pa mitundu.
Ulosi wa Yoweli umatipatsa ife ngakhale chakudya chowonjezereka choyenera kulingalira. Nkulekeranji, popeza kuti “tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsya” liri lotsimikizirika kudza! Mtundu wa anthu uyenera kuchenjezedwa. Mofanana ndi dzombe mu ulosi wa Yoweli, Mboni za Yehova zikusakaza Chikristu cha Dziko mwa kuchivumbula mosalekeza ponena za mkhalidwe wake wosabala wauzimu. Ichi chikudzutsa ukali ndi chitsutso cha atsogoleri ake, koma zopinga zirizonse zonga linga zomwe angayesere kukhazikitsa m’njira ya dzombe lophiphiritsiralo zimatsimikizira kukhala zosagwira ntchito. Yehova watsanulira mzimu wake pa anthu ake, kuwakonzekeretsa iwo kulengeza ziweruzo zake. Chotero, mu kanthaŵi kochepa komwe katsala tsiku lowopsya la Mulungu lisanafike, lolani kuti tikhale ndi kugawanamo kokwanira m’kuthandiza ena ‘kuitanira pa dzina la Yehova ndi kupulumutsidwa.’
[Bokosi patsamba 30]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:2—Yoweli akulankhula ndi “akulu” omwe anasokeretsa mtundu. Chifukwa chakuti “nzika za dzikolo” zinatsatira chitsogozo chonyenga chimenecho, iwo analinso oŵerengera mlandu m’maso mwa Yehova. Lerolino, atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko mofananamo asokeretsa nkhosa zawo. Mofanana ndi Yoweli, Mboni za Yehova zalunjikitsa uthenga wawo ku gulu la atsogoleri a chipembedzo limenelo. Komabe, anthu mwachisawawa ayenera kukhala ndi Mawu a Mulungu atalalikidwa kwa iwo chifukwa chakuti iwo nawonso adzapereka kuŵerengera kwa Yehova.—Yesaya 9:15-17; Aroma 14:12.
○ 2:1-10, 28—Aisrayeli anachenjezedwa kuti ngati samvera Mulungu, dzombe ndi zolengedwa zina zikasakaza mbewu zawo. (Deuteronomo 28:38-45) Popeza Malemba samalemba kuwukira kulikonse kwa tizirombo pa Kanani pa magawo otchulidwa ndi Yoweli, mliri umene iye analongosola unali mwachidziŵikire wochitira chithunzi. Mwachiwonekere, ulosiwo unayamba kukwaniritsidwa pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene Yehova anayamba ‘kutsanulira mzimu wake’ pa atsatiri a Yesu, omwe anazunza anthu a chipembedzo chonyenga ndi uthenga wawo wopatsidwa ndi Mulungu. (Machitidwe 2:1, 14-21; 5:27-29) Mboni za Yehova tsopano zikuchita ntchito yosakaza yofananayo.
○ 2:12, 13—M’nthaŵi zakale, kung’amba zovala za wina kunali chiwonetsero chakunja cha chisoni. (Genesis 37:29, 30; 44:13) Koma ichi chikanachitidwa mosawona mtima, mwachinyengo. Yoweli anamveketsa icho kuti malongosoledwe akunja a chisoni sanali okwanira. Anthuwo anafunikira ‘kung’amba mitima yawo’ mwa kusonyeza kulapa kwa mtima wonse.
○ 2:31, 32—Yehova anapereka populumukirapo kuchokera ku chiwonongeko kaamba ka okhulupirika m’nthaŵi ya Yoweli. Tsopano, mu “masiku otsiriza” ano, Mulungu akupanga chipulumutso kukhala chothekera kupyolera mwa Yesu Kristu. (2 Timoteo 3:1; Aroma 5:8, 12; 6:23) Ngakhale kuli tero, pali pa dzina la Yehova pamene anthu ochimwa ayenera kuitanira kaamba ka chipulumutso. Ichi chimatanthauza kudziŵa dzina laumulungulo, kulilemekeza ilo kotheratu, ndi kudalira kotheratu pa Yemwe ali nalo. Chotero awo oitanira pa dzina la Yehova m’chikhulupiriro “adzapulumutsidwa” pamene Mulungu adzapereka chiweruzo chake pa mitundu mkati mwa “tsiku [lake] lalikulu ndi lowopsya.” —Zefaniya 2:2, 3; 3:12; Aroma 10:11-13.
○ 3:2, 14—Malo ophiphiritsira kaamba ka kupereka chiweruzo chaumulungu mu “tsiku la Yehova” akutchedwa “chigwa chotsiriza mlandu.” Chikutchedwanso “chigwa cha Yosafati.” Ichi chiri choyenerera, popeza kuti dzina lakuti Yosafati limatanthauza kuti “Yehova Ndi Woweruza.” Mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Yosafati, Mulungu anapulumutsa Yuda ndi Yerusalemu kuchoka ku magulu ankhondo a Moabu, Amoni, ndi gawo la mapiri la Sieri, kuwapangitsa iwo kukhala osokonezeka ndi kuphana wina ndi mnzake. (2 Mbiri 20:1-30) M’tsiku lathu, “chigwa cha Yosafati” chimatumikira monga choponderamo mpesa chophiphiritsira mu chimene mitundu ikuphwanyidwa monga mpesa kaamba ka ovutitsa anthu a Yehova.
○ 3:6—Turo, Sidoni, ndi Filistiya anali ndi liwongo la kugulitsa anthu a Yuda ndi Yerusalemu mu ukapolo kwa Agriki. Mothekera, Ayuda ena ogwidwa ndi mitundu ina anabwera m’manja mwa ogulitsa akapolo a ku Turo, Sidoni, ndi Filistiya. Choipirapobe, mwinamwake mitundu imeneyi inapanga Ayuda kukhala akapolo omwe anafuna populumukirapo kuchokera kwa adani awo. Mosasamala kanthu za chimene chinali nkhaniyo, Mulungu anaitana ogulitsa moyo wa anthu amenewo kuŵerengera kaamba ka kuvutitsa anthu ake. Ichi chimasonyeza chomwe chikuyembekezera mitundu yomwe ikuzunza atumiki a Yehova lerolino.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.