Kumbukirani Tsiku la Yehova
‘Layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu.’—YOWELI 3:14.
1. Kodi nchifukwa ninji nkhondo yopatulika ikudzayo yolengezedwa ndi Yehova idzakhala yosiyana ndi nkhondo “zopatulika” za anthu?
‘MULALIKIRE ichi mwa amitundu, [‘Patulikitsani nkhondo!’, NW].’ (Yoweli 3:9) Kodi imeneyi ndinkhondo yopatulika? Titayang’ana kumbuyo kupenda Nkhondo Zamtanda, nkhondo zachipembedzo, ndi nkhondo zadziko ziŵiri—m’mene Chikristu Chadziko chinachita mbali yaikulu—mwina tingachite mantha kulingalira za nkhondo “yopatulika.” Komabe, nkhondo yopatulika ya muulosi wa Yoweli siiri nkhondo pakati pa mitundu. Siiri kumenyana kwaudani kolimbanira nthaka kapena chuma, kobisalira m’dzina la chipembedzo. Iyo ndinkhondo yolungama. Ndinkhondo ya Mulungu imene idzachotsa umbombo, nkhwidzi, kuipa, ndi chitsenderezo padziko lapansi. Idzalemekeza uchifumu woyenerera wa Yehova pachilengedwe chake chonse. Nkhondoyo idzatsegulira Ufumu wa Kristu njira yoloŵetsera mtundu wa anthu m’Zaka Chikwi za mtendere, kukhupuka, ndi chimwemwe zonenedweratu ndi aneneri a Mulungu.—Salmo 37:9-11; Yesaya 65:17, 18; Chivumbulutso 20:6.
2, 3. (a) Kodi “tsiku la Yehova” loloseredwa pa Yoweli 3:14 nchiyani? (b) Kodi chifukwa ninji amitundu amayenerera zimene adzayang’anizana nazo patsikulo?
2 Pamenepa, kodi “tsiku la Yehova” lonenedweratu pa Yoweli 3:14 nchiyani? Yehova mwiniyo akudzuma nati: ‘Kalanga ine, tsikuli! Pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.’ Kodi lidzakhala chiwonongeko motani? Pambuyo pake mneneriyo akulongosola nati: ‘Aunyinji, aunyinji m’chigwa chotsirizira mlandu! Pakuti layandikira tsiku la Yehova m’chigwa chotsirizira mlandu.’ (Yoweli 1:15; 3:14) Patsiku limeneli Yehova adzapereka chiweruzo chake paunyinji wa anthu osapembedza amene amakana uchifumu wake woyenerera kumwamba ndi padziko lapansi. Chiri chosankha cha Yehova chakuwononga dongosolo la zinthu lausatanali limene lagwira mtundu wa anthu mumsampha wake kwa nthaŵi yaitali.—Yeremiya 17:5-7; 25:31-33.
3 Dongosolo loipa la zinthu padziko lapansi likuyang’anizana ndi chiweruzo chimenecho. Koma kodi dongosolo la dziko nloipadi kwambiri chotero? Eya, kupenda mbiri yake kumasonyeza zimenezo! Yesu anatchula njira yodziŵira zimenezo pa Mateyu 7:16 kuti: ‘Mudzaŵazindikira ndi zipatso zawo.’ Kodi mizinda yaikulu yadziko sinafikire pakukhala midzi ya anamgoneka, upandu, mantha, chisembwere, ndi kuipitsa? M’maiko ambiri ufulu wopezedwa chatsopano ukudodometsedwa ndi chisokonezo cha ndale zadziko, kupereŵera kwa chakudya, ndi umphaŵi. Anthu oposa biliyoni imodzi amadya mosakwanira. Ndiponso, mliri wa AIDS, wosonkhezeredwa ndi anamgoneka ndi njira za moyo wachisembwere, ukuwopseza mbali yaikulu ya dziko lapansi. Makamaka kuyambira pakuulika kwa Nkhondo Yadziko ya I mu 1914, pakhala kunyonyotsoka kwa padziko lonse m’mbali iriyonse ya moyo.—Yerekezerani ndi 2 Timoteo 3:1-5.
4. Kodi Yehova akupereka chitokoso chotani kwa amitundu?
4 Komabe, Yehova wakhala akusonkhanitsa anthu m’mitundu yonse omwe mwachimwemwe amalandira malangizo onena za njira zake ndi kuyenda m’mabande ake. Mtundu umenewu wapadziko lonse wasula malupanga kukhala zolimira mwakusiya njira zachiwawa zadziko. (Yesaya 2:2-4) Inde, malupanga kukhala zolimira! Koma kodi zimenezi sizikuwombana ndi mfuu imene Yehova akuchititsa kulengezedwa pa Yoweli 3:9, 10? Pamenepo timaŵerenga kuti: ‘Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere. Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo.’ Eya, Yehova panopa akutokosa olamulira adziko kubweretsa magulu awo ankhondo amphamvu ophatikizidwa pamodzi kudzalimbana naye pa Armagedo. Koma iwo sadzapambana! Adzagonjetsedwa kotheratu!—Chivumbulutso 16:16.
5. Kodi nchiyani chidzachitika pamene “munda wampesa wa m’dziko”umwetedwa?
5 Mopandukira Mfumu Ambuye Yehova, olamulira amphamvu amanga nkhokwe za zida zowopsa—koma zopanda pake! Yehova alamula motere pa Yoweli 3:13: ‘Longani zenga, pakuti dzinthu dzacha; idzani, pondani, pakuti chadzala choponderamo mpesa; zosungiramo zisefuka; pakuti zoipa zawo nzazikulu.’ Mawu amenewo amagwirizana ndi Chivumbulutso 14:18-20, kumene mngelo wonyamula zenga lakuthwa akulamulidwa kuti ‘tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko; pakuti mpesa wake wapsa ndithu.’ Mngeloyo akuponya zenga lake ndi kukokera mitundu yopandukayo ‘moponderamo mpesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.’ Mophiphiritsira, mwazi utuluka moponderamo mpesa nufikira zapakamwa za akavalo, kufikira mastadiya 1,600—pafupifupi makilomita 300! Kalanga ine, mitundu yonyoza Yehova imeneyo ili ndi chiyembekezo chowopsa chotani nanga!
Nzika Zomvera Lamulo
6. Kodi Mboni za Yehova zimawawona motani amitundu ndi olamulira awo?
6 Kodi zimenezi zimatanthauza kuti Mboni za Yehova sizimachitira ulemu amitundu ndi olamulira awo? Kutalitali! Zimachita chisoni ndi chisalungamo chimene onse angathe kuwona bwino lomwe, ndipo zimachenjeza za tsiku la Yehova lomafika mofulumira la kupereka chiweruzo chake. Panthaŵi imodzimodzi, zimamvera modzichepetsa uphungu wa mtumwi Paulo pa Aroma 13:1 wakuti: ‘Anthu onse amvere maulamuliro aakulu.’ Zimapereka ulemu woyenera kwa olamulira ameneŵa aumunthu, koma osati kuwalambira. Monga nzika zomvera lamulo, zimatsatira miyezo ya Baibulo ya kuwona mtima, kukhulupirika, ndi ukhondo ndi kukulitsa makhalidwe abwino m’mabanja awo. Zimathandiza ena kuphunzira mmene iwonso angachitire zimenezo. Zimakhala mwamtendere ndi anthu onse, sizimaphatikizidwa m’zisonyezero zotsutsa kapena zipanduko zandale. Mboni za Yehova zimafuna kupereka chitsanzo chabwino m’kumvera malamulo a maulamuliro aakulu, pamene zikuyembekezera Wolamulira Wamkulukulu, Mfumu Ambuye Yehova, kubwezeretsa mtendere weniweni ndi boma lolungama padziko lino lapansi.
Kupereka Chiweruzo Chake
7, 8. (a) Kodi amitundu adzagwedezedwa mwanjira yanji, ndipo mdima udzawagwera motani? (b) Kodi Yoweli amaimira yani lerolino, ndipo mosiyana ndi dziko, kodi ameneŵa ngodalitsika motani?
7 M’mawu ophiphiritsira omvekera bwino, Yehova apereka malongosoledwe owonjezereka onena za kuperekedwa kwa chiweruzo chake: ‘Dzuŵa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuŵala kwawo. Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mawu ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israyeli.’ (Yoweli 3:15, 16) Mkhalidwe wa anthu wowonekera kukhala wokhupuka, ndi woŵala udzasandulika mdima wandiweyani, wowopsa, ndipo dongosolo ladziko lomanyonyotsokali lidzagwedezeka kuchotsedwapo, kuwonongedwa ndi chivomezi, titero kunena kwake!—Hagai 2:20-22.
8 Tawonani chilimbikitso chosangalatsa chakuti Yehova adzakhala populumukira ndi linga la anthu ake! Chifukwa ninji zili choncho? Chifukwa chakuti iwo ali mtundu wogwirizana—mtundu wapadziko lonse—umene walabadira mawu a Yehova akuti: ‘Momwemo mudzadziŵa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ (Yoweli 3:17) Popeza kuti dzina la Yoweli limatanthauza “Yehova Ndiye Mulungu,” iye moyenerera amaimira Mboni zodzozedwa zamakono za Yehova, zimene zimatumikira molimba mtima kulengeza uchifumu wa Yehova. (Yerekezerani ndi Malaki 1:11.) Titatembenukira kumawu otsegulira ulosi wa Yoweli, timapeza mmene akuneneratu momvekera bwino za ntchito ya anthu a Mulungu lerolino.
Khamu la Dzombe
9, 10. (a) Kodi ndimliri wotani umene Yoweli akulosera? (b) Kodi ndimotani mmene Chivumbulutso chikubwerezera ulosi wa Yoweli wonena za mliri, ndipo kodi mliri umenewu ukuyambukira motani Chikristu Chadziko?
9 Tsopano tamverani ‘mawu a Yehova a kwa Yoweli’: ‘Imvani ichi, akulu akulu inu, nimutchere khutu, inu nonse okhala m’dziko. Chachitika ichi masiku anu kodi, kapena masiku a makolo anu? Mufotokozere ana anu ichi, ndi ana anu afotokozere ana awo, ndi ana awo afotokozere mbadwo wina. Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.’—Yoweli 1:1-4.
10 Umenewu ndimkupiti wachilendo kwambiri, umene sudzaiŵalika konse. Magulumagulu a tizilombo, kwakukulukulu dzombe, awononga dzikolo. Kodi zimenezi zimatanthauzanji? Chivumbulutso 9:1-12 chimalankhulanso za mliri wa dzombe, wotumizidwa ndi Yehova motsogozedwa ndi “mfumu yakulilamulira, mngelo wa phompho,” yomwe mosakaikira ndi Kristu Yesu. Maina akewo Abadoni (m’Chihebri) ndi Apoliyoni (m’Chihelene) amatanthauza “Chiwonongeko” ndi “Wowononga.” Dzombe limeneli limaimira Akristu odzozedwa otsalira amene, tsopano m’tsiku la Ambuye, amatuluka kukasakaza msipu wa Chikristu Chadziko mwakuvumbula kotheratu chipembedzo chake chonyenga ndi kulengeza chiweruzo cha Yehova.
11. Kodi ndimotani mmene dzombe lamakono likuchirikizidwira, ndipo ndayani kwenikweni amene ali chandamali cha kuukira kwake?
11 Monga kwasonyezedwera ndi Chivumbulutso 9:13-21, mliri wa dzombe utsatiridwa ndi mliri waukulu wa ankhondo apakavalo. Zimenezi zilidi zowona chotani nanga lerolino, pamene Akristu odzozedwa otsalira zikwi zoŵerengeka akuchirikizidwa ndi “nkhosa zina” zoposa mamiliyoni anayi onse pamodzi kupanga ankhondo apakavalo osatsutsika! (Yohane 10:16) Amagwirizana kulengeza ziweruzo zoluma za Yehova pa opembedza mafano a Chikristu Chadziko ndi amene ‘sanalapa mbanda zawo, kapena nyanga zawo, kapena chigololo chawo, kapena umbala wawo.’ Atsogoleri achipembedzo—ponse paŵiri Achikatolika ndi Achiprotesitanti—amene akangalika m’kuchirikiza nkhondo zambanda m’zaka za zana lino, limodzinso ndi ansembe okonda kugona ana ndi alaliki oluluzika a pa TV, ali pakati pa amene akulandira mauthenga achiweruzo ameneŵa.
12. Kodi nchifukwa ninji atsogoleri a Chikristu Chadziko ayenera kulandira mauthenga achiweruzo, ndipo kodi nchiyani chidzawachitikira posachedwa, pamodzi ndi ziŵalo zonse za Babulo Wamkulu?
12 Kwa atsogoleri achipembedzo “aufulu” oluluzika amenewo, chiitano cha Yehova chikumveka chakuti: ‘Galamukani, oledzera inu, nimulire; bumani, nonse akumwa vinyo, chifukwa cha vinyo watsopano, pakuti waletsedwa pakamwa panu.’ (Yoweli 1:5) M’zaka za zana lino la 20, chipembedzo cha Chikristu Chadziko chalola mkhalidwe woluluzika wa dziko mmalo mwa malamulo amakhalidwe abwino a Mawu a Mulungu. Kumwerekera m’njira zadziko kwa chipembedzo chonyenga ndi ziŵalo zake kwawonekera kukhala kozuna, koma ha, iwo atuta nthenda yauzimu ndi yakuthupi yowopsa chotani nanga! Posachedwa, monga kwalongosoledwera pa Chivumbulutso 17:16, 17, kuukiridwa kwa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko lonse wachipembedzo chonyenga, ndi kuwonongedwa kwake ndi maulamuliro andale zadziko, zidzakhala za “m’mtima” wa Mulungu. Ndikokha panthaŵiyo, pamene adzawona kuti chiweruzo cha Yehova chikuperekedwa pa iye, mpamene ‘adzagalamuka’ m’kuledzera kwake.
‘Mtundu Waukulu ndi Wamphamvu’
13. Kodi khamu la dzombe limawonekera kukhala ‘mtundu waukulu ndi wamphamvu’ ku Chikristu Chadziko mwanjira yotani?
13 Mneneri wa Yehova apitiriza kulongosola khamu la dzombe monga ‘mtundu waukulu ndi wamphamvu,’ ndipo umawonekadi motero kwa Babulo Wamkulu. (Yoweli 2:2) Mwachitsanzo, atsogoleri ake achipembedzo amadandaula kuti zipembedzo za Chikristu Chadziko zalephera kupanga ophunzira m’Japani Wachibuda. Komabe, lerolino, Mboni za Yehova Zachijapani zoposa 160,000 zakuta dziko limenelo muunyinji wawo ndipo zikuchititsa maphunziro awo Abaibulo m’nyumba za anthu zoposa 200,000. Mu Italiya, Mboni za Yehova zokwanira 180,000 tsopano zazindikiridwa kukhala zachiŵiri kwa Akatolika m’chiŵerengero. Wansembe wamkulu wa Roma Katolika ku Italiya anadandaula mosaphula kanthu kuti Mboni za Yehova zikutenga ‘Akatolika okhulupirika okwanira pafupifupi 10,000’ m’tchalitchicho chaka chirichonse.a Mbonizo nzachimwemwe kulandira anthu otero.—Yesaya 60:8, 22.
14, 15. Kodi ndimotani mmene Yoweli akulongosolera khamu la dzombe, ndipo kodi zimenezi zakwaniritsidwa motani lerolino?
14 Polongosola khamu la dzombe la Mboni zodzozedwa, Yoweli 2:7-9 amati: ‘Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lirilonse njira yake, osasokonezeka m’mabande awo. Sakankhana, ayenda lirilonse mopita mwake; akagwa m’zida, siithyoka nkhondo yawo. Alumphira mudzi, athamanga palinga, akwerera nyumba, aloŵera pamazenera ngati mkhungu.’
15 Eya, alidi malongosoledwe opereka chithunzi chabwino cha khamu lankhondo la “dzombe” lodzozedwa, tsopano lophatikana ndi atsamwali oposa mamiliyoni anayi a nkhosa zina! Palibe “linga” laudani wachipembedzo limene lingaliletse. Molimba mtima, ‘lapitirizabe kuyenda molongosoka m’njira imodzimodziyi’ ya kuchitira umboni ndi ntchito zina Zachikristu poyera. (Yerekezerani ndi Afilipi 3:16, NW.) Mmalo mololera molakwa, lakhala lofunitsitsa kuyang’anizana ndi imfa, monga momwe Mboni zikwi zambiri zinachitira zomwe ‘zinagwa m’zida’ chifukwa chokana kuchitira saluti Hitler Wachikatolika wa Jeremani wa Nazi. Khamu la dzombelo lachitira umboni mokwanira mu “mudzi” wa Chikristu Chadziko, kukwera pazopinga zonse, kuloŵa m’nyumba mofanana ndi mkhungu, titero kunena kwake, pakuti lagaŵira zofalitsidwa zofotokoza Baibulo zokwanira mabiliyoni ambiri m’ntchito yake yakunyumba ndi nyumba. Chiri chifuniro cha Yehova kuti umboni umenewu uperekedwe, ndipo palibe mphamvu m’mwamba kapena padziko lapansi yomwe ingauletse.—Yesaya 55:11.
“Anadzazidwa ndi Mzimu Woyera”
16, 17. (a) Kodi nliti pamene mawu a Yoweli 2:28, 29 anakhala ndi kukwaniritsidwa kwapadera? (b) Kodi ndimawu aulosi ati a Yoweli amene sanakwaniritsidwe kotheratu m’zaka za zana loyamba?
16 Yehova akuuza Mboni zake kuti: ‘Mudzadziŵa kuti ine ndiri pakati pa Israyeli [wauzimu], ndi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina.’ (Yoweli 2:27) Anthu ake analoŵa mumkhalidwe umenewu wamtengo wapatali pamene Yehova anayamba kukwaniritsa mawu ake a pa Yoweli 2:28, 29 akuti: ‘Kudzachitika mtsogolo mwake, ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera.’ Zimenezi zinachitika pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene ophunzira a Yesu osonkhana anadzozedwa ‘ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera.’ Ndi mphamvu ya mzimu woyerayo, analalikira, ndipo patsiku lomwelo, ‘anawonjezedwa anthu ngati zikwi zitatu.’—Machitidwe 2:4, 16, 17, 41.
17 Pachochitika chosangalatsa chimenecho, Petro nayenso anagwira mawu a Yoweli 2:30-32 akuti: ‘Ndipo ndidzawonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa. Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.’ Mawu amenewo anakwaniritsidwa pamlingo wochepa pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E.
18. Kodi nliti pamene kukwaniritsidwa kwakukulu kwa Yoweli 2:28, 29 kunayamba kuchitika?
18 Komabe, pakakhala kugwira ntchito kwina kwa Yoweli 2:28-32. Ndithudi, ulosi umenewu wakhala ndi kukwaniritsidwa kodabwitsa kuyambira September 1919. Panthaŵiyo msonkhano wosaiŵalika wa anthu a Yehova unachitika ku Cedar Point, Ohio, U.S.A. Mzimu wa Mulungu unawonekera bwino, ndipo atumiki ake odzozedwa anasonkhezeredwa kuyamba mkupiti wapadziko lonse wochitira umboni umene wafika mpaka lerolino. Ha, pakhala kufutukuka kwakukulu kotani nanga! Opezekapo pamsonkhanowo ku Cedar Point oposa 7,000 afikira chiwonkhetso chokwanira 10,650,158 cha opezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu pa March 30, 1991. Mwa ameneŵa, kokha 8,850 anadziwonetsera kukhala Akristu odzozedwa. Chimwemwe chawo chakula motani nanga powona zipatso zapadziko lonse zodzetsedwa ndi mzimu wamphamvu wa Yehova!—Yesaya 40:29, 31.
19. Polingalira za kuyandikira kwa tsiku la Yehova, kodi aliyense wa ife ayenera kukhala ndi kaimidwe kotani kamaganizo?
19 Patsogolo pathupa pali ‘tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa’ limene lidzasakaza dongosolo la zinthu la Satana. (Yoweli 2:31) Mwachimwemwe, “yense amene akaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumutsidwa.” (Machitidwe 2:21) Motani? Mtumwi Petro akutiuza kuti “tsiku la [Yehova, NW] lidzadza ngati mbala” nawonjezera kuti: ‘Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi [kukumbukira, NW] kudza kwake kwa tsiku la [Yehova].’ Pomakumbukira kuti tsiku la Yehova layandikira, tidzasangalalanso kuwona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova la “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano” lolungama.—2 Petro 3:10-13.
[Mawu a M’munsi]
a La Repubblica, Roma, Italiya, November 12, 1985, ndi La rivista del clero italiano, May 1985.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi “tsiku la Yehova” nchiyani?
◻ Kodi ‘munda wampesa wa m’dziko’ udzamwetedwa motani, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi ndimwanjira yotani imene mliri wa dzombe wakanthira Chikristu Chadziko chiyambire 1919?
◻ Kodi mzimu wa Yehova unatsanulidwa motani pa anthu ake mu 33 C.E., ndiponso mu 1919?