Kodi ‘Adzapulumuka Ndani’?
“Yense amene akaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumutsidwa.”—MACHITIDWE 2:21.
1. Kodi nchifukwa ninji tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. linali posinthira mbiri ya dziko lonse?
TSIKU la Pentekoste wa 33 C.E. linali posinthira mbiri ya dziko lonse. Chifukwa ninji? Chifukwa tsiku limenelo mtundu watsopano unabadwa. Poyamba, sunali mtundu waukulu kwambiri—unali chabe ophunzira a Yesu 120 osonkhana m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu. Koma lero, pamene mitundu yochuluka yomwe inaliko panthaŵiyo yaiŵalika, mtundu umene unabadwa m’chipinda chapamwambacho udakali nafe. Mfundo imeneyi njofunika kwambiri kwa ife tonse, pakuti ndi mtundu umenewu umene Mulungu anasankha kuti ukhale mboni yake kwa anthu.
2. Kodi pobadwa mtundu watsopano panachitika zozizwitsa zotani?
2 Pamene mtundu watsopanowo unayamba kukhalako, panachitika zinthu zazikulu zimene zinakwaniritsa mawu a ulosi wa Yoweli. Timaŵerenga za zochitikazo pa Machitidwe 2:2-4: “Mwadzidzidzi anamveka mawu ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo. Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogaŵanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha. Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga mzimu anawalankhulitsa.” Mwanjira imeneyi amuna ndi akazi 120 okhulupirika amenewo anakhala mtundu wauzimu, oyamba mwa amene mtumwi Paulo pambuyo pake anatcha “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16.
3. Kodi ndi ulosi uti wa Yoweli womwe unakwaniritsidwa pa Pentekoste wa 33 C.E.?
3 Makamu anasonkhana kuti afufuze za “mphepo yolimba” ija, ndipo mtumwi Petro anawafotokozera kuti zimenezo zinali kukwaniritsa mbali ina ya ulosi wa Yoweli. Ulosi uti? Eya, tamverani zimene ananena: “M’masiku otsiriza, anena Mulungu, Ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto; ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera. Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m’thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi; dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera; ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.” (Machitidwe 2:17-21) Mawuwo omwe Petro anagwira amapezeka pa Yoweli 2:28-32, ndipo kukwaniritsidwa kwake kunatanthauza kuti nthaŵi inali kuwathera Ayuda. “Tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera,” nthaŵi yoŵerengera mlandu Aisrayeli osakhulupirika, linayandikira. Koma kodi akanapulumuka ndani? Ndipo zimenezo zinaimira chiyani?
Kukwaniritsidwa Kuŵiri kwa Ulosi
4, 5. Polingalira zomwe zikachitika mtsogolo mwake, kodi Petro anapereka uphungu wotani, ndipo nchifukwa ninji uphunguwo unali kudzagwira ntchito masiku a mtsogolo kupyola nthaŵi yake?
4 Pazaka zotsatira 33 C.E., Israyeli wauzimu wa Mulungu anatukuka, koma mtundu wakuthupi wa Israyeli sunatero ayi. Mu 66 C.E., Israyeli wakuthupi anathirana nkhondo ndi Roma. Mu 70 C.E., Israyeli anatsala pang’ono kutheratu ndipo Yerusalemu ndi kachisi wake anamtentha yense mpaka pansi. Pa Pentekoste wa 33 C.E., Petro anapereka uphungu wabwino chifukwa cha tsoka linalikudzalo. Pogwiranso mawu Yoweli, iye anati: “Yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.” Myuda aliyense payekha anafunika kudzisankhira kuitanira pa dzina la Yehova. Zimenezo zinaphatikizapo kulabadira malangizo ena a Petro akuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu.” (Machitidwe 2:38) Omvetsera Petrowo anafunikira kuvomereza kuti Yesu ndiye Mesiya, amene mtundu wa Israyeli unamkana.
5 Mawu a ulosi wa Yoweli amenewo anawakhudza mtima kwambiri ofatsa m’zaka za zana loyamba. Komabe, lero ali ndi mphamvu yaikulu koposa chifukwa, malinga ndi zochitika m’zaka za zana la 20 zino, ulosi wa Yoweli ukukwaniritsidwa kachiŵirinso. Tiyeni tione mmene zikuchitikira.
6. Kodi ndi motani mmene Israyeli wa Mulungu anayamba kudziŵikira bwino pamene 1914 inayandikira?
6 Atumwi atatha kufa, Israyeli wa Mulungu anabisika ndi namsongole wa Chikristu chonyenga. Koma panthaŵi ya mapeto omwe anayamba mu 1914, mtundu umenewu wauzimu unadziŵikanso bwino kwambiri. Zonsezi zinakwaniritsa fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole. (Mateyu 13:24-30, 36-43) Pamene chaka cha 1914 chinayandikira, Akristu odzozedwa anayamba kudzilekanitsa ndi Dziko Lachikristu losakhulupirikalo, kukana molimba ziphunzitso zake zonyenga nalalikira molimbika za mapeto analinkudza a “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) Koma nkhondo yadziko yoyamba, imene inaulika mu 1914, inabutsa nkhani zimene iwo sanazikonzekere. Popanikizika kwambiri ambiri analefuka, ndipo ena anagonja. Pamene 1918 inafika, ntchito yawo yolalikira inali itaimiratu.
7. (a) Kodi nchiyani chinachitika mu 1919 chofanana ndi Pentekoste wa 33 C.E.? (b) Kuyambira 1919, kodi kutsanulidwa kwa mzimu wa Mulungu kunawakhudza motani atumiki a Yehova?
7 Komatu zimenezo sizinakhalitse ayi. Kuyambira 1919, Yehova anayamba kutsanulira mzimu wake pa anthu ake mwanjira imene inakumbutsa za Pentekoste wa 33 C.E. Inde, mu 1919 panalibe zolankhula malilime ndi zamphepo yolimba. Tidziŵa malinga ndi mawu a Paulo pa 1 Akorinto 13:8 kuti nthaŵi ya zozizwitsa inatha kalekale. Koma umboni wakuti analandira mzimu wa Mulungu unaonekeratu mu 1919 pamene Akristu okhulupirika anapezanso nyonga pamsonkhano ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., nayambanso ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mu 1922 anapitanso ku Cedar Point ndipo chilimbikitso chakuti “Lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake,” chinawasonkhezera kwambiri. Monga momwe zinachitikira m’zaka za zana loyamba, dziko linakakamizika kudziŵa kuti mzimu wa Mulungu watsanulidwa. Mkristu aliyense wodzipatulira—mwamuna ndi mkazi, mkulu ndi wamng’ono—anayamba ‘kunenera,’ kutanthauza, kulengeza “zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:11) Monga Petro, iwo analimbikitsa ofatsa kuti: “Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.” (Machitidwe 2:40) Kodi ofuna akanachita motani zimenezo? Mwa kulabadira mawu a Yoweli opezeka pa Yoweli 2:32 akuti: “Yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.”
8. Kodi zinthu zamuyendera motani Israyeli wa Mulungu kuyambira 1919?
8 Chiyambire zakazo, ntchito yokhudza Israyeli wa Mulungu yapitabe patsogolo. Kuika chizindikiro pa odzozedwa kukuoneka kuti kwafika patali, ndipo kuyambira m’ma 1930 khamu lalikulu la ofatsa oyembekezera kudzakhala padziko lapansi laonekera. (Chivumbulutso 7:3, 9) Onsewo akudziŵa kuti afunika kuchita changu, pakuti kukwaniritsidwa kwachiŵiri kwa Yoweli 2:28, 29 kukusonyeza kuti tayandikira kwambiri tsiku lokulirapo la Yehova, loopsadi, pamene dongosolo la zinthu la dziko la zipembedzo, ndale, ndi malonda lidzawonongedwa. Tili ndi chifukwa chabwino ‘choitanira pa dzina la Yehova’ ndi chikhulupiriro chonse chakuti adzatilanditsa!
Kodi Timaitana Motani pa Dzina la Yehova?
9. Kodi zinthu zina zophatikizidwa pa kuitana pa dzina la Yehova nzotani?
9 Kodi kuitana pa dzina la Yehova kumaphatikizapo chiyani? Nkhani yake ya Yoweli 2:28, 29 ikutithandiza kuyankha funsolo. Mwachitsanzo, sikuti Yehova amamva munthu aliyense woitana pa dzina lake. Mwa mneneri wina, Yesaya, Yehova anauza Aisrayeli kuti: “Pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva.” Kodi Yehova anakaniranji kumva anthu ake? Iye yekha akufotokoza kuti: “Manja anu adzala mwazi.” (Yesaya 1:15) Yehova samvetsera aliyense amene ali ndi mlandu wa mwazi kapena wozoloŵera kuchimwa. Ndiye chifukwa chake Petro anauza Ayuda pa Pentekoste kuti alape. M’nkhani ya Yoweli 2:28, 29, tikupeza kuti Yowelinso akugogomezera kulapa. Mwachitsanzo, pa Yoweli 2:12, 13, timaŵerenga kuti: “Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro; ndipo ng’ambani mitima yanu, si zovala zanu ayi; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima.” Kuyambira 1919, Akristu odzozedwa anatsatira mawu ameneŵa. Analapa zolakwa zawo natsimikiza mtima kusagonjanso kapena kulefuka. Zimenezo zinatsegulira njira mzimu wa Mulungu kuti autsanulire pa iwo. Aliyense wofuna kuitana pa dzina la Yehova ndi kumvedwa ayenera kutsatira njira imodzimodziyo.
10. (a) Kodi kulapa kwenikweni nkutani? (b) Kodi Yehova amatani ndi kulapa kwenikweni?
10 Kumbukirani kuti kulapa kwenikweni kumafuna zambiri osati chabe kungonena kuti “Ndalapa.” Aisrayeli ankang’amba zovala zawo kusonyeza chisoni chawo chachikulu. Koma Yehova akuti: “Ng’ambani mitima yanu, si zovala zanu ayi.” Kulapa kwenikweni kumachokera mumtima, pansi penipeni pa mtima wathu. Kumaphatikizapo kufulatira zoipa, mongadi timaŵerengera pa Yesaya 55:7: “Woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova.” Kumaphatikizapo kuda uchimo, monga momwedi Yesu anachitira. (Ahebri 1:9) Ndiyeno, tiyenera kuyang’ana kwa Yehova kuti atikhululukire mwa kugwiritsira ntchito nsembe ya dipo chifukwa Yehova ndiye “wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima.” Adzatilola kumlambira, ndipo adzalandira nsembe yathu yaufa yauzimu ndi nsembe yothira. Adzamva tikaitana pa dzina lake.—Yoweli 2:13.
11. Kodi kulambira koona kuyenera kukhala ndi malo otani m’moyo wathu?
11 Pa Ulaliki wa pa Phiri, Yesu anatiuza kanthu kena kofuna kukakumbukira pamene anati: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33) Tisaone kulambira kwathu ngati nkhani wamba, imene tingachite mwachiphamaso poyesa kutonthoza chikumbumtima chathu. Kutumikira Mulungu kuyenera kukhala patsogolo m’moyo wathu. Ndiye chifukwa chake mwa Yoweli, Yehova akunenabe kuti: “Ombani lipenga m’Ziyoni . . . Sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa maŵere; mkwati atuluke m’chipinda mwake, ndi mkwatibwi m’mogona mwake.” (Yoweli 2:15, 16) Mwachibadwa amene angokwatirana kumene amatengeka maganizo, amangofuna kusamalirana iwo okha basi. Komanso ngakhale iwo, afunikira kuika patsogolo kutumikira Yehova. Pasakhale chotsogola pakusonkhanitsidwa kwathu kwa Mulungu, kuitana pa dzina lake.
12. Kodi lipoti la Chikumbutso la chaka chatha likusonyeza motani kuti pakhoza kukhala chiwonjezeko?
12 Tikumaganiza zimenezo, ndi bwino kuti tipende ziŵerengero zomwe Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1997 la Mboni za Yehova likusonyeza. Chaka chatha tinali ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa Ufumu 5,599,931—inde khamu lalikuludi la atamandi! Opezeka pa Chikumbutso anali 14,322,226—kuposa chiŵerengero cha ofalitsa ndi mamiliyoni pafupifupi asanu ndi atatu ndi theka. Chiŵerengero chimenecho chikusonyeza kuti pakhoza kukhala chiwonjezeko chachikulu. Ambiri mwa anthu mamiliyoni asanu ndi atatu ndi theka amenewo anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova monga anthu okondwerera kapena ana a makolo obatizidwa. Ochuluka anapezeka pamsonkhano nthaŵi yoyamba. Kupezekapo kwawo kunapatsa Mboni za Yehova mpata wabwino wowadziŵa ndi kuwapempha kuti awathandize kupita patsogolo. Ndiyenso, panali aja amene amapezeka pa Chikumbutso chaka chilichonse ndipo mwina amapezeka pamisonkhano ina ingapo, koma osapita patsogolo. Inde, onsewo ngaufulu kupezeka pamisonkhano. Koma tikuwalimbikitsa kuganizapo mosamalitsa pa mawu a ulosi wa Yoweli ndi kuona zinanso zimene angachite kuti atsimikize kuti Yehova adzawamva pamene aitana pa dzina lake.
13. Ngati tikuitana pa dzina la Yehova, kodi tiyenera kuchita chiyani kwa ena?
13 Mtumwi Paulo anagogomezera mbali ina ya kuitana pa dzina la Mulungu. M’kalata yake kwa Aroma, anagwira mawu a ulosi wa Yoweli akuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.” Ndiyeno anati: “Iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira?” (Aroma 10:13, 14) Inde, ena ambiri amene mpaka pano sanamdziŵe Yehova afunika kuitana pa dzina lake. Amene akumdziŵa Yehova ayenera kulalikira komanso kuwafunafuna ndi kuwathandiza.
Paradaiso Wauzimu
14, 15. Kodi ndi madalitso otani a paradaiso amene anthu a Yehova akusangalala nawo chifukwa choitana pa dzina lake mwanjira imene imamkondweretsa?
14 Ndi mmene odzozedwa ndi ankhosa zina omwe amaonera zinthu, ndipo motero, Yehova akuwadalitsa. “Yehova anachitira dziko lake nsanje, nachitira anthu ake chifundo.” (Yoweli 2:18) Mu 1919, Yehova anachitira anthu ake nsanje ndi chifundo pamene anawabwezeretsa ndi kuwaloŵetsa m’malo ake a ntchito yauzimu. Ameneyo ndiyedi paradaiso wauzimu, wofotokozedwa bwino ndi Yoweli motere: ‘Usaopa, dziko iwe; kondwera, nusekerere; pakuti Yehova wachita zazikulu. Musamaopa, nyama za kuthengo inu; pakuti m’chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zawo; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zawo. Mukondwere tsono, inu ana a Ziyoni, nimusekerere mwa Yehova Mulungu wanu; pakuti adzayamba kukupatsani mvula yamyundo, monga mwa chilungamo chake; nakuvumbitsirani mvula, mvula yamyundo ndi yamasika mwezi woyamba. Ndipo madwale adzakhala ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; zidzasefuka m’zosungiramo zawo.’—Yoweli 2:21-24.
15 Chithunzi chake nchosangalatsa kwambiri. Zinthu zitatu zazikulu zofunika pamoyo m’Israyeli—tirigu, mafuta a azitona, ndi vinyo—limodzinso ndi zifuyo zochuluka. Lero mawu a ulosi amenewo akukwaniritsidwa mwauzimu. Yehova akutipatsa chakudya chonse chauzimu chimene tikufuna. Kodi tonsefe sitikukondwera ndi chakudya cha mwanaalirenji chimenechi chimene Mulungu wapereka? Zoona, malinga ndi ulosi wa Malaki, Mulungu wathu ‘watitsegulira mazenera a kumwamba, ndi kutitsanulira mdalitso wakuti asoŵeka malo akuulandira.’—Malaki 3:10.
Mapeto a Dongosolo la Zinthu
16. (a) Kodi kutsanulidwa kwa mzimu wa Yehova kumatanthauzanji m’nthaŵi yathu ino? (b) Kodi mtsogolo muli zotani?
16 Yoweli akulosera za kutsanulidwa kwa mzimu wa Yehova atalosera za mikhalidwe ya paradaiso wa anthu a Mulungu. Pamene Petro anagwira mawu ulosiwo pa Pentekoste, anati unakwaniritsidwa “m’masiku otsiriza.” (Machitidwe 2:17) Kutsanulidwa kwa mzimu wa Mulungu kalelo kunatanthauza kuti masiku otsiriza a dongosolo la zinthu lachiyuda anali atayamba. Kutsanulidwa kwa mzimu wa Mulungu pa Israyeli wa Mulungu m’zaka za zana la 20 zino kukutanthauza kuti tili m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu la dziko lonse. Polingalira zimenezi, kodi mtsogolo muli zotani? Ulosi wa Yoweli ukupitiriza kutiuza kuti: “Ndidzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.”—Yoweli 2:30, 31.
17, 18. (a) Kodi ndi tsiku lotani la Yehova loopsa lomwe linafika pa Yerusalemu? (b) Kodi kutsimikizika kwa tsiku loopsa la Yehova lamtsogolo kukutisonkhezera kutani?
17 Mu 66 C.E., mawu ameneŵa a ulosi anayamba kuchitikadi m’Yudeya pamene zinthu mosapeŵeka zinafika pachimake patsiku la Yehova loopsa mu 70 C.E. Mmene zinalili zoopsa panthaŵiyo kupezeka pa aja amene sanali kuitana pa dzina la Yehova! Lerolino, zinthu zoopsa zonga zimenezo zili mtsogolomu, pamene Yehova adzawononga dongosolo lonseli la zinthu la dziko. Komabe, zitheka kupulumuka. Ulosiwo ukupitiriza kunena kuti: “Kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi m’Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.” (Yoweli 2:32) Mboni za Yehova zikuthokozadi kuti zikulidziŵa dzina la Yehova, ndipo zikhulupiriradi kuti adzazipulumutsa zikaitana pa iye.
18 Nanga nchiyani chidzachitika pamene tsiku la Yehova lalikulu ndi loonekera lifika padzikoli ndi ukali wake wonse? Zimenezo zidzafotokozedwa m’nkhani yophunzira yomaliza.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndi liti pamene Yehova kwanthaŵi yoyamba anatsanulira mzimu wake pa anthu ake?
◻ Kodi zinthu zina zophatikizidwa pa kuitana pa dzina la Yehova nzotani?
◻ Kodi ndi liti pamene tsiku la Yehova lalikulu ndi loonekera linafika pa Israyeli wakuthupi?
◻ Kodi Yehova amawadalitsa motani amene aitana pa dzina lake lerolino?
[Chithunzi patsamba 15]
Mtundu watsopano unabadwa pa Pentekoste wa 33 C.E.
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kuchiyambi kwa zaka za zana lino, Yehova anatsanuliranso mzimu wake pa anthu ake kukwaniritsa Yoweli 2:28, 29
[Chithunzi patsamba 18]
Anthu ayenera kuthandizidwa kuitana pa dzina la Yehova