Musawopa, Kagulu ka Nkhosa Inu”
“Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.”—LUKA 12:32.
1. Kodi maziko a mawu a Yesu akuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu” ndi otani?
“TAFUNAFUNANI Ufumu [wa Mulungu].” (Luka 12:31) Pamene Yesu ananena mawu ameneŵa kwa ophunzira ake, anatchula lamulo limene latsogolera kalingaliridwe ka Akristu kuyambira m’tsiku lake kufikira lerolino. Ufumu wa Mulungu uyenera kukhala pamalo oyamba m’moyo wathu. (Mateyu 6:33) Komabe, m’cholembedwa cha Luka, Yesu anapitiriza kunena mawu achikondi ndi opatsa chidaliro ku kagulu kapadera ka Akristu. Iye anati: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.” (Luka 12:32) Monga Mbusa Wabwino, Yesu anadziŵa kuti mtsogolo munali nthaŵi zovuta kwa ophunzira ake okondedwa. Koma panalibe chifukwa kwa iwo chokhalira amantha ngati anapitiriza kufunafuna Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chake, chisonkhezero cha Yesu sichinali lamulo laukali. M’malo mwake, linali lonjezo lachikondi limene linasonkhezera chidaliro ndi kulimbika mtima.
2. Kodi ndayani amene amapanga kagulu ka nkhosa, ndipo nchifukwa ninji ali ndi mwaŵi waukulu kwambiri?
2 Yesu anali kulankhula kwa ophunzira ake, ndipo anawatcha “kagulu ka nkhosa.” Anali kulankhulanso kwa awo amene Yehova ‘akapatsa ufumu.’ Powayerekezera ndi makamu aakulu amene akalandira Yesu pambuyo pake, chiŵerengero cha kagulu kameneka chinalidi chochepa. Anaonedwanso kukhala amtengo wapatali chifukwa chakuti anasankhidwa kaamba ka mtsogolo mwabwino koposa, kukagwiritsiridwa ntchito mu utumiki wachifumu. Atate wawo, Mbusa Wamkulu, Yehova, waitana kagulu ka nkhosa ndi cholinga chakuti iwo akalandire choloŵa chakumwamba mogwirizana ndi Ufumu Waumesiya wa Kristu.
Kagulu ka Nkhosa
3. Kodi ndi masomphenya aulemerero ati a kagulu ka nkhosa amene Yohane anaona?
3 Nangano, kodi ndani amene amapanga kagulu ka nkhosa kameneka kokhala ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimenecho? Ndi otsatira Yesu Kristu amene amadzozedwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 2:1-4) Powaona monga oimba akumwamba okhala ndi azeze m’manja mwawo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira pa phiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pawo. Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa. Ndipo m’kamwa mwawo simunapezedwa bodza; ali opanda chilema.”—Chivumbulutso 14:1, 4, 5.
4. Kodi ndi malo otani amene kagulu ka nkhosa kali nawo pa dziko lapansi?
4 Kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., odzozedwa ndi obadwa ndi mzimu ameneŵa atumikira monga akazembe a Kristu pa dziko lapansi. (2 Akorinto 5:20) Lerolino, pali otsalira okha amene akutumikira monga kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. (Mateyu 24:45; Chivumbulutso 12:17) Makamaka kuyambira mu 1935, iwo agwirizana ndi “nkhosa zina,” Akristu amene ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi, amene chiŵerengero chawo tsopano chili m’mamiliyoni. Ameneŵa akuthandiza kulalikira mbiri yabwino pa dziko lonse lapansi.—Yohane 10:16.
5. Kodi mkhalidwe wamaganizo wa otsalira a kagulu ka nkhosa uli wotani, ndipo nchifukwa ninji sayenera kuwopa?
5 Kodi mkhalidwe wamaganizo wa otsalira a kagulu ka nkhosa amene adakali pa dziko lapansi ngwotani? Podziŵa kuti adzalandira “ufumu wosagwedezeka,” amapereka utumiki wawo wopatulika ndi mantha aumulungu ndi chinthenthe. (Ahebri 12:28) Amazindikira modzichepetsa kuti wawowo uli mwaŵi wosayerekezereka umene umadzetsa chisangalalo chachikulu. Iwo apeza “ngale imodzi ya mtengo wapatali” imene Yesu anatchula pamene analankhula za Ufumu. (Mateyu 13:46) Pamene chisautso chachikulu chomaliza chikuyandikira, odzozedwa a Mulungu samawopa. Mosasamala kanthu za zimene zidzagwera dziko la mtundu wa anthu mu “tsiku la Ambuye, lalikulu ndi loonekera,” iwo alibe mantha oziziritsa m’nkhongono akuwopa za mtsogolo. (Machitidwe 2:19-21) Kodi angawoperenji?
Chiŵerengero Chichepa
6, 7. (a) Kodi nchifukwa ninji chiŵerengero cha a kagulu ka nkhosa amene akali pa dziko lapansi chili chochepa kwambiri? (b) Kodi aliyense ayenera kuona motani chiyembekezo chimene ali nacho?
6 M’zaka zaposachedwa chiŵerengero cha a kagulu ka nkhosa omwe akali pa dziko lapansi chachepa kwambiri. Zimenezi zinasonyezedwa ndi lipoti la Chikumbutso la 1994. M’mipingo pafupifupi 75,000 ya anthu a Yehova pa dziko lonse, 8,617 okha ndiwo anasonyeza kudzinenera kwawo kukhala ziŵalo za otsalira mwa kudya zizindikiro. (Mateyu 26:26-30) Mosiyana ndi zimenezo, opezekapo onse anali 12,288,917. Akristu odzozedwa akudziŵa kuti umu ndimmene ziyenera kukhalira. Yehova wasankha chiŵerengero chochepa, cha 144,000, kupanga kagulu ka nkhosa, ndipo wakhala akukasonkhanitsa kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E. Moyenerera, kuitanidwa kwa kagulu ka nkhosa kukafika pamapeto ake pamene chiŵerengero chake chinali pafupi kukwanira, ndipo umboni umasonyeza kuti kusonkhanitsa konse kwa odalitsidwa kwambiri ameneŵa kunatha mu 1935. Komabe, nkhosa zina zinaloseredwa kuti zikachuluka m’nthaŵi ya mapeto kukhala “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” Kuyambira mu 1935 Yehova wakhala akusonkhanitsa unyinji wa a khamu lalikulu limeneli amene ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso wa pa dziko lapansi.—Chivumbulutso 7:9; 14:15, 16; Salmo 37:29.
7 Ochuluka a kagulu ka nkhosa amene akali pa dziko lapansi tsopano ali ndi zaka za m’ma 70, 80, ndi 90. Angapo apyola chaka cha 100 cha moyo wawo. Onsewa, mosasamala kanthu za usinkhu wawo, amadziŵa kuti mwa chiukiriro chakumwamba, adzagwirizana ndi Yesu Kristu m’kupita kwa nthaŵi ndipo adzalamulira limodzi naye mu Ufumu wake waulemerero. A khamu lalikulu adzakhala nzika za pa dziko lapansi za Kristu Mfumu. Yense akondweretu ndi zimene Yehova wasungira awo amene amkonda. Sizili kwa ife kusankha chiyembekezo chimene tikufuna kukhala nacho. Zimenezo zili kwa Yehova kuti asankhe. Magulu onsewo angasangalale ndi chiyembekezo chawo cha mtsogolo mwachimwemwe, kaya mu Ufumu wakumwamba kapena pa dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu umenewo.—Yohane 6:44, 65; Aefeso 1:17, 18.
8. Kodi kusindikizidwa chizindikiro kwa a 144,000 kwafika pati, ndipo nchiyani chimene chidzachitika pamene kumalizidwa?
8 Kagulu ka nkhosa ka 144,000 ndiko “Israyeli wa Mulungu,” amene waloŵa m’malo Israyeli wakuthupi m’zifuno za Mulungu. (Agalatiya 6:16) Chifukwa chake, otsalira ali otsala a mtundu wauzimu umenewo umene udakali pa dziko lapansi. Otsala amenewo akusindikizidwa chizindikiro kaamba ka chivomerezo chotsiriza cha Yehova. Mtumwi Yohane anaona zimenezi zikuchitika m’masomphenya, ndipo anasimba kuti: “Ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuŵa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mawu aakulu kuitana angelo anayi, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja, nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pawo. Ndipo ndinamva chiŵerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israyeli [wauzimu].” (Chivumbulutso 7:2-4) Popeza ntchito imeneyi ya kusindikiza chizindikiro Israyeli wauzimu mwachionekere yatsala pang’ono kwambiri kutha, zochitika zokondweretsa zimene ziti zichitike posachedwapa zikusonyezedwa. Kunena zoona, “chisautso chachikulu,” pamene mphepo zinayi za chiwonongeko zidzamasulidwa kuwomba dziko lapansi, chiyenera kukhala pafupi kwambiri.—Chivumbulutso 7:14.
9. Kodi kagulu ka nkhosa kamaona motani chiŵerengero chomawonjezereka cha khamu lalikulu?
9 Awo a khamu lalikulu amene asonkhanitsidwa kale chiŵerengero chawo chili m’mamiliyoni. Ha, mmene zimenezi zimasangalatsira mitima ya otsalira nanga! Ngakhale kuti chiŵerengero cha a kagulu ka nkhosa amene akali pa dziko lapansi chikupitirizabe kutsika, iko kaphunzitsa ndi kukonzekeretsa amuna oyenerera a khamu lalikulu kusenza mathayo a m’gulu la Mulungu lomafutukuka la pa dziko lapansi. (Yesaya 61:5) Monga momwe Yesu anasonyezera, padzakhala opulumuka chisautso chachikulu.—Mateyu 24:22.
“Musawopa”
10. (a) Kodi ndi kuukira kotani kumene kudzadza pa anthu a Mulungu, ndipo kodi kudzachititsa chiyani? (b) Kodi ife aliyense payekha tikufunsidwa mafunso otani?
10 Satana ndi ziŵanda zake aponyedwa ku dziko lapansi. Iyeyo ndi makamu ake akusonkhezeredwa kuukira kotheratu anthu a Yehova. Kuukira kumeneku, konenedweratu m’Baibulo, kukufotokozedwa monga kuukira kwa Gogi wa ku Magogi. Kodi mpayani makamaka pamene Mdyerekezi akulunjikitsa chiukiro chake? Kodi si paziŵalo zotsirizira za kagulu ka nkhosa, Israyeli wauzimu wa Mulungu, amene akukhala mwamtendere “pakati pa dziko”? (Ezekieli 38:1-12) Inde, koma otsalira a kagulu kokhulupirika ka odzozedwa, limodzi ndi mabwenzi awo okhulupirika, a nkhosa zina, adzaona mmene chiukiro cha Satana chidzasonkhezera Yehova Mulungu kuchitapo kanthu mwamsanga. Iye adzaloŵererapo kutetezera anthu ake, ndipo zimenezi zidzasonkhezera kuulika kwa “tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa.” (Yoweli 2:31) Lerolino, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru akuchita ntchito yofunika, yopulumutsa moyo, akumachenjeza za kuloŵerera kwa Yehova kukudzako. (Malaki 4:5; 1 Timoteo 4:16) Kodi inu mukuchirikiza mokangalika utumiki umenewo, mukumalalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova? Kodi mudzapitiriza kuchita motero monga wolengeza Ufumu wopanda mantha?
11. Kodi nchifukwa ninji mkhalidwe wamaganizo wa kulimba mtima uli wofunika lerolino?
11 Polingalira za mkhalidwe wa dziko umene ulipowu, kuli kwapanthaŵi yake chotani nanga kwa kagulu ka nkhosa kulabadira mawu amene Yesu anawauza: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu”! Mkhalidwe wamaganizo wa kulimba mtima umenewo ngwofunika polingalira zonse zimene zikuchitidwa tsopano mogwirizana ndi chifuno cha Yehova. Munthu aliyense payekha wa a kagulu ka nkhosa amazindikira kufunika kwa kupirira kufikira mapeto. (Luka 21:19) Monga momwe Yesu Kristu, Mbuye wa kagulu ka nkhosako, anapiririra nakhala wokhulupirika kufikira mapeto a moyo wake wa pa dziko lapansi, choteronso aliyense wa otsalira ayenera kupirira ndi kukhala wokhulupirika.—Ahebri 12:1, 2.
12. Kodi ndimotani mmene Paulo, mofanana ndi Yesu, analangizira Akristu odzozedwa kusakhala ndi mantha?
12 Odzozedwa onse ayenera kukhala ndi lingaliro lofanana ndi lija la mtumwi Paulo. Onani mmene mawu ake, monga wodzozedwa ndi wolengeza wapoyera wa chiukiriro, alili ogwirizana ndi chilangizo cha Yesu cha kusawopa. Paulo analemba kuti: “Kumbukira Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wochokera m’mbewu ya Davide, monga mwa uthenga wabwino wanga; mmenemo ndimva zoŵaŵa kufikira zomangira, monga wochita zoipa; koma mawu a Mulungu samangika. Mwa ichi ndipirira zonse, chifukwa cha osankhika, kuti iwonso akapeze chipulumutsocho cha mwa Kristu Yesu, pamodzi ndi ulemerero wosatha. Okhulupirika mawuwa: Pakuti ngati tidamwalira ndi iye, tidzakhalanso moyo ndi iye: ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi iye: ngati timkana iye, iyeyunso adzatikana ife: ngati tikhala osakhulupirika, iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sakhoza kudzikana yekha.”—2 Timoteo 2:8-13.
13. Kodi ndi zikhulupiriro zozama ziti zimene ziŵalo za kagulu ka nkhosa zili nazo, ndipo zimenezi zimawasonkhezera kuchitanji?
13 Mofanana ndi mtumwi Paulo, ziŵalo zotsala za kagulu ka nkhosa kodzozedwa zili zofunitsitsa kupirira ndi mavuto pamene zikulengeza uthenga wamphamvu woperekedwa m’Mawu a Mulungu. Zikhulupiriro zawo zili zozama kwambiri popeza amadalira malonjezo a Mulungu a chipulumutso ndi a kupatsidwa kwawo “korona wa moyo” ngati akhala okhulupirika kufikira imfa. (Chivumbulutso 2:10) Mwa kulandira chiukiriro chapanthaŵi yomweyo ndi kusintha, adzagwirizanitsidwa ndi Kristu, kulamulira limodzi naye monga mafumu. Ha, ndi chipambano chotani nanga cha njira yawo ya kusunga umphumphu monga olaka dziko!—1 Yohane 5:3, 4.
Chiyembekezo Chapadera
14, 15. Kodi ndimotani mmene chiyembekezo cha chiukiriro cha kagulu ka nkhosa chilili chapadera?
14 Chiyembekezo cha chiukiriro chimene kagulu ka nkhosa kali nacho ndi chapadera. Motani? Choyamba, chikuchitika chiukiriro cha anthu onse “olungama ndi osalungama” chisanachitike. (Machitidwe 24:15) Kwenikweni, chiukiriro cha odzozedwa chimatsatira malo awo audindo, monga momwe asonyezera bwino mawu aŵa a pa 1 Akorinto 15:20, 23: “Kristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula cha iwo akugona. Koma yense m’dongosolo lake la iye yekha, chipatso choundukula Kristu; pomwepo iwo a Kristu, pa kubwera kwake.” Mwa kukhala ndi mtundu wa chipiriro ndi chikhulupiriro chimene Yesu anasonyeza, kagulu ka nkhosa kamadziŵa zimene zikuwayembekezera pamene amaliza moyo wawo wa pa dziko lapansi, makamaka chiyambire pamene Ambuye woona anadza ku kachisi wake mu 1918.—Malaki 3:1.
15 Paulo akutipatsa chifukwa chinanso choonera chiukiriro chimenechi kukhala chapadera. Monga momwe kwalembedwera pa 1 Akorinto 15:51-53, iye analemba kuti: “Taonani, ndikuuzani chinsinsi [chopatulika, NW]; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza. . . . Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi cha imfa ichi kuvala chosafa.” Mawu ameneŵa amagwira ntchito kwa awo a kagulu ka nkhosa amene akufa mkati mwa kukhalapo kwa Kristu. Popanda kugona mu imfa kwa nyengo yaitali ya nthaŵi, iwo amavekedwa kusafa, “m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso.”
16, 17. Ponena za chiyembekezo chawo cha chiukiriro, kodi Akristu odzozedwa ali odalitsidwa kwambiri motani lerolino?
16 Malinga ndi kuzindikira kumeneku, tingathe kumvetsetsa lingaliro la mawu a mtumwi Yohane opezeka pa Chivumbulutso 14:12, 13. Iye analemba kuti: “Pano pali chipiriro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu. Ndipo ndinamva mawu ochokera kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.”
17 Ndi mfupo yapadera chotani nanga imene ikuyembekezera otsalira a kagulu ka nkhosa! Chiukiriro chawo chimafika mofulumira, atangogona mu imfa. Ndi kusintha kwapadera kotani nanga kumene otsalira amakhala nako pamene akutenga magawo awo kumwamba m’malo a mizimu! Limodzi ndi kulemekezedwa kwa kagulu ka nkhosa kotero kumene kukuchitika ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi aakulu a Baibulo kumene kukuyandikira mapeto ake, ziŵalo zotsiriza zotsala za kagulu ka nkhosa ziyeneradi ‘kusawopa.’ Ndipo kupanda mantha kwawo kumalimbikitsa awo a khamu lalikulu, amene ayenera kukulitsa mkhalidwe wamaganizo wopanda mantha wofananawo pamene akuyembekezera chiwomboledwe mkati mwa nthaŵi ya mavuto aakulu koposa amene dziko lapansi silinaonepo.
18, 19. (a) Kodi nchifukwa ninji nthaŵi imene tikukhalamo ili yofulumiza? (b) Kodi nchifukwa ninji odzozedwa ndi a nkhosa zina omwe ayenera kukhala opanda mantha?
18 Kusimba zochita za kagulu ka nkhosa kumakhozetsa iwo ndi khamu lalikulu kupitirizabe kuwopa Mulungu woona. Ola la chiweruzo choperekedwa ndi iye lafika, ndipo nthaŵi yabwino yotsalayo njamtengo wapatali. Nthaŵiyo ilidi yofinimpha kwa ena kuchitapo kanthu. Komabe, ifeyo sitimawopa kuti chifuno cha Mulungu chidzalephera. Chidzapambanadi!
19 Mawu aakulu akumwamba amvedwa kale akumati: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” (Chivumbulutso 11:15) Ndithudi, Mbusa Wamkulu, Yehova, akutsogolera nkhosa zake zonse “m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.” (Salmo 23:3) Kagulu ka nkhosa mosalakwa kakutsogoleredwa ku mfupo yawo yakumwamba. Ndipo nkhosa zina zidzalanditsidwa motetezereka kupyola chisautso chachikulu kukalandira moyo wamuyaya m’gawo la pa dziko lapansi la Ufumu waulemerero wa Mulungu mu ulamuliro wa Kristu Yesu. Chifukwa chake, pamene kuli kwakuti mawu a Yesu ananenedwa kwa kagulu ka nkhosa, ndithudi atumiki a Mulungu onse pa dziko lapansi ali ndi chifukwa chomvetsera mawu ake akuti: “Musawopa.”
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kuyembekezera kutsika kwa chiŵerengero chotsala cha kagulu ka nkhosa?
◻ Kodi mkhalidwe wa otsalira odzozedwa uli wotani lerolino?
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu sayenera kuwopa, mosasamala kanthu za kuukira komayandikira kwa Gogi wa ku Magogi?
◻ Kodi nchifukwa ninji chiukiriro cha a 144,000 chili chapadera, makamaka lerolino?