Yehova Adzaweruza ndi Kulanga Oipa
‘Konzekera kukumana ndi Mulungu wako.’—AMOSI 4:12.
1, 2. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti Mulungu adzathetsa kuipa?
KODI Yehova adzathetsa kuipa ndi kuvutika kumene kuli padziko lapansiku? Kuchiyambiyambi kwa zaka za m’ma 2000 zino, funso limeneli likuoneka kuti n’lofunika kwambiri kusiyana ndi kale lonse. Zikuoneka kuti kulikonse komwe tingayang’ane padziko lapansili, anthu akuchitirana nkhanza. Tikulakalaka dziko limene lidzakhala lopanda chiwawa, uchigawenga, ndi katangale.
2 Chinthu chosangalatsa n’chakuti tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti Yehova adzathetsa kuipa konse. Makhalidwe a Mulungu amatitsimikizira kuti iye adzalanga oipa. Yehova ndi Mulungu wolungama. Pa Salmo 33:5, Mawu ake amatiuza kuti: “Iye ndiye wakukonda chilungamo ndi chiweruzo.” Salmo lina limati: “Moyo wake [wa Yehova] umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Zoonadi Yehova, Mulungu wamphamvu yonse ameneyu, amenenso amakonda chilungamo ndi chiweruzo, sangalekerere mpaka kalekale zinthu zomwe amazida.
3. Kodi tikapendanso ulosi wa Amosi tiphunzira chiyani?
3 Taganiziraninso chifukwa china chimene tingatsimikizire kuti Yehova adzathetsa kuipa. Mbiri ya zimene iye anachita kumbuyoku imatsimikizira zimenezi. Zitsanzo zogwira mtima kwambiri za zinthu zimene Yehova anachita kwa oipa zikupezeka m’buku la m’Baibulo la Amosi. Kupendanso ulosi wa Amosi kutiphunzitsa zinthu zitatu zokhudza chiweruzo cha Mulungu. Choyamba, chiweruzocho nthawi zonse chimakhala choyenerera. Chachiwiri, chiweruzo cha Mulungu sichithawika. Ndipo chachitatu, chimasankha, chifukwa Yehova amalanga anthu oipa koma amachitira chifundo anthu olapa amene ali ndi mtima wabwino.—Aroma 9:17-26.
Chiweruzo cha Mulungu Chimakhala Choyenerera Nthawi Zonse
4. Kodi Yehova anatuma Amosi kupita kuti, ndipo anamutuma kuti akatani?
4 M’nthawi ya Amosi, mtundu wa Israyeli unali utagawanika kale kukhala maufumu awiri. Mbali imodzi inali ufumu wa kum’mwera wa Yuda wa mafuko awiri. Mbali inayo inali ufumu wakumpoto wa Israyeli wa mafuko khumi. Yehova anapatsa Amosi ntchito yoti akhale mneneri, ndipo anam’tumiza ku Israyeli kuchoka kwawo ku Yuda. Mulungu anatuma Amosi kumeneko kuti akalengeze chiweruzo Chake.
5. Kodi Amosi analosera za mitundu iti choyamba, ndipo n’chifukwa chiyani inayenerera kuweruzidwa ndi kulangidwa ndi Mulungu?
5 Amosi sanayambe n’kulengeza chiweruzo cha Yehova pa ufumu wakumpoto wa Israyeli, umene unali utalowerera. M’malo mwake anayamba ndi kulengeza chiweruzo pa mitundu isanu ndi umodzi yapafupi. Mitundu yake inali Aaramu, Filistia, Turo, Edomu, Amoni, ndi Moabu. Koma kodi mitundu imeneyi inayenereradi kuweruzidwa ndi kulangidwa ndi Mulungu? Inde inayenereradi. Chifukwa chimodzi n’choti mitundu imeneyi inali paudani wosamwerana madzi ndi anthu a Yehova.
6. N’chifukwa chiyani Mulungu anati adzadzetsa masoka pa Aaramu, Filistia, ndi Turo?
6 Mwachitsanzo Yehova anadzudzula Aaramu “popeza anapuntha Gileadi.” (Amosi 1:3) Aaramu analanda malo a fuko la Gileadi, dera la Israyeli kum’mawa kwa mtsinje wa Yordano, ndipo anazunza kwambiri anthu a Mulungu kumeneko. Bwanji za Filistia ndi Turo? Afilisti anali ndi mlandu wotengera Aisrayeli ku ndende kapena kuti ku ukapolo, n’kuwagulitsa kwa Aedomu, ndipo Aisrayeli ena anagudwa ndi ochita malonda aukapolo a ku Turo. (Amosi 1:6, 9) Tangoganizani zimenezo. Kugulitsa anthu a Mulungu kukhala akapolo! N’zosadabwitsa kuti Yehova anati adzadzetsa masoka pa Aaramu, Filistia, ndi Turo.
7. Kodi mitundu ya Edomu, Amoni, ndi Moabu inali paubale wotani ndi Israyeli, koma kodi inawachitira zinthu motani Aisrayeliwo?
7 Mitundu ya Edomu, Amoni, ndi Moabu inali yapachibale ndiponso mitundu itatu yonseyi inali paubale ndi Aisrayeli. Aedomu anali mbadwa za Abrahamu kudzera kwa mbale wake wa Yakobo wamapasa, Esau. Choncho tingati anali aphwawo a Aisrayeli. Aamoni ndi Amoabu anali mbadwa za Loti, mwana wa mchimwene wake wa Abrahamu. Koma kodi Edomu, Amoni, ndi Moabu anachitira zinthu Aisrayeli monga abale awo enieni? Ayi, sanatero m’pang’onong’ono pomwe! Edomu mwankhanza anagwiritsa ntchito lupanga polimbana ndi “mphwake,” ndipo Aamoni anachita nkhanza zosaneneka kwa Aisrayeli ali akapolo. (Amosi 1:11, 13) Ngakhale kuti Amosi sanatchule nkhanza zimene Amoabu anachitira anthu a Mulungu, Amoabuwo anali ndi mbiri yoipa yotsutsa Israyeli. Chilango chimene chinali kubwera pa mitundu itatu ya paubale imeneyi chinali chachikulu. Yehova anati adzaiwononga ndi moto.
Chiweruzo cha Mulungu Sichithawika
8. N’chifukwa chiyani chiweruzo cha Mulungu pa mitundu isanu ndi umodzi yokhala pafupi ndi Israyeli chinali chosathawika?
8 N’zosachita kufunsa kuti mitundu yonse isanu ndi umodzi imeneyi yomwe inatchulidwa kumayambiriro kwa ulosi wa Amosi inayenerera kuweruzidwa ndi kulangidwa ndi Mulungu. Ndipo panalibe njira yoti mitunduyi ikanathawira chilango chawocho. Kuyambira Amosi chaputala 1, vesi 3, mpaka chaputala 2, vesi 1, Yehova analankhula nthawi zisanu ndi imodzi kuti: “Sindidzabweza kulanga kwake.” Ndipo n’zoona kuti mogwirizana ndi mawu ake, Yehova sanabwezedi dzanja lake polanga mitundu imeneyo. Mbiri imasonyeza kuti mitundu yonseyo inakumana ndi tsoka pambuyo pake. Ndipotu, mitundu inayi mwa imeneyo, Filistia, Moabu, Amoni, ndi Edomu, m’kupita kwa nthawi sinakhalekonso!
9. Kodi anthu a ku Yuda anayenerera kuchitidwa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anayenerera zimenezi?
9 Ulosi wa Amosi tsopano ukukhudza mtundu wachisanu ndi chiwiri, dera la kwawo kwa Amosi la Yuda. Anthu a ufumu wakumpoto wa Israyeli ayenera kuti anadabwa kumva Amosi akulengeza za chiweruzo cha ufumu wa Yuda. N’chifukwa chiyani anthu okhala m’Yuda anayenerera kuweruzidwa ndi kulangidwa? “Popeza akaniza chilamulo cha Yehova,” amatero Amosi 2:4. Yehova sanachepetse kuphwanya Chilamulo chake kwadala kumeneko. Malinga ndi Amosi 2:5, iye ananeneratu kuti: “Ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zachifumu za m’Yerusalemu.”
10. N’chifukwa chiyani Yuda sakanatha kuthawa tsoka lake?
10 Yuda wosakhulupirikayo sakanathawa tsoka limene linali kubweralo. Yehova ananena kachisanu ndi chiwiri kuti: “Sindidzabweza kulanga kwake.” (Amosi 2:4) Yuda analandira chilango chonenedweratucho pamene anasakazidwa ndi Ababulo m’chaka cha 607 Yesu Asanabwere. Kachiwirinso tikuona kuti anthu oipa sangathe kuthawa chiweruzo cha Mulungu.
11-13. Amosi analosera makamaka podzudzula mtundu uti, ndipo kodi ndi kuponderezana kotani kumene kunalipo kumeneko?
11 Mneneri Amosi anali atangolengeza kumene chiweruzo cha Yehova pa mitundu isanu ndi iwiri. Koma aliyense amene anaganiza kuti Amosi anali atamaliza analakwitsa kwambiri. Amosi anali asanamalize kulengeza uthenga wake. Ntchito ya Amosi makamaka inali yolengeza uthenga wopweteka wa chiweruzo pa ufumu wakumpoto wa Israyeli. Ndipo Aisrayeli anayenera kulandira chiweruzo ndi chilango cha Mulungu chimenechi chifukwa chakuti khalidwe lawo ndi chipembedzo chawo zinali zonyansa.
12 Ulosi wa Amosi umasonyeza poyera kuponderezana kumene kunali kutafala mu ufumu wa Israyeli. Pa nkhani imeneyi, Amosi 2:6, 7 amati: “Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israyeli, kapena zinayi, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato. Ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa.”
13 Anthu olungama anali kugulitsidwa ndi “ndalama,” mwina kutanthauza kuti oweruza akalandira ndalama za chiphuphu anali kulanga anthu opanda mlandu. Okongoza ndalama anali kugulitsa anthu osowa kuti akhale akapolo ndi mtengo wogulira “nsapato,” mwina pofuna kuti abweze ngongole yochepa zedi. Anthu opanda chifundowo ‘analiralira,’ kapena kuti anayesetsa, kutsitsa ‘osauka’ mpaka osaukawo ankatenga fumbi n’kuliponya pamutu pawo, kusonyeza kuvutika maganizo, chisoni, kapena manyazi awo. Katangale anali ponseponse moti ‘ofatsa’ sakanatha kupeza chilungamo.
14. Kodi ndani amene anali kuchitiridwa nkhanza mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi?
14 Taonani anthu amene anali kuchitiridwa nkhanza. Anali anthu olungama, osowa, osauka, ndi ofatsa a m’dzikolo. Pangano la Chilamulo cha Yehova ndi Israyeli linkanena kuti anthu ovutika ndi osowa aziwachitira chifundo. M’malo mwake zinthu zinali zoipa zedi kwa anthu oterewa mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi.
‘Konzekera Kukumana ndi Mulungu Wako’
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani Aisrayeli anachenjezedwa kuti: ‘Konzekera kukumana ndi Mulungu wako’? (b) Kodi lemba la Amosi 9:1, 2 likusonyeza bwanji kuti oipa sakanatha kuzemba chilango cha Mulungu? (c) Kodi n’chiyani chinachitikira ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi m’chaka cha 740 Yesu Asanabwere?
15 Popeza chiwerewere ndi machimo ena zinali ponseponse mu Israyeli, panali pomveka kuti mneneri Amosi anachenjeza mtundu wopandukawo kuti: ‘Konzekera kukumana ndi Mulungu wako.’ (Amosi 4:12) Israyeli wosakhulupirikayo sakanapulumuka chiweruzo cha Mulungu choyandikiracho chifukwa Yehova analengeza kachisanu ndi chitatu kuti: “Sindidzabweza kulanga kwake.” (Amosi 2:6) Ponena za anthu oipa amene anafuna kubisala, Mulungu anati: “Wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi. Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.”—Amosi 9:1, 2
16 Anthu oipa sakanazemba chilango cha Yehova mwa kukumba “mpaka kunsi kwa manda,” mawu ophiphiritsira kuyesera kubisala pansi pa nthaka. Ndipo sakanathawa chiweruzo cha Mulungu mwa ‘kukwera kumwamba,’ kutanthauza kuyesera kupeza malo obisala pamwamba pa mapiri aatali. Chenjezo la Yehova linali lomveka, ndipo mfundo yake inali yakuti: Malo alionse amene anthu angabisaleko iye sangalephere kufikako. Potsatira chilungamo cha Mulungu, ufumu wa Israyeli unafunika kuti ulangidwe chifukwa cha ntchito zake zoipa. Ndipo nthawi imeneyo inafikadi. M’chaka cha 740 Yesu Asanabwere, patapita zaka pafupifupi 60 kuchokera pamene Amosi analemba ulosi umenewu, ufumu wakumpoto wa Israyeli unagonjetsedwa ndi Asuri.
Chiweruzo cha Mulungu Chimasankha
17, 18. Kodi Amosi chaputala 9 chikutisonyeza chiyani za chifundo cha Mulungu?
17 Ulosi wa Amosi watithandiza kuona kuti chiweruzo cha Mulungu chimakhala choyenerera ndipo sichithawika. Koma buku la Amosi limasonyezanso kuti chiweruzo cha Yehova chimasankha. Mulungu angapeze anthu oipa kulikonse kumene abisala, ndipo angathe kuwalanga. Angapezenso anthu olapa ndi olungama, amene amawachitira chifundo. Chaputala chomaliza cha buku la Amosi chikufotokoza bwino kwambiri phunziro limeneli.
18 Malinga ndi Amosi chaputala 9, vesi 8, Yehova anati: “Sindidzawononga nyumba ya Yakobo kuitha konse.” Monga momwe mavesi 13 mpaka 15 akusonyezera, Yehova analonjeza kuti ‘adzabwezanso undende’ wa anthu ake. Anthu amenewo adzaonetsedwa chifundo, adzatetezedwa ndipo adzalemera. “Wolima adzapezana ndi wodula,” analonjeza choncho Yehova. Tangoganizani kukhala ndi zokolola zochuluka zoti zina zisanaikidwebe m’nkhokwe nyengo yotsatira yolima ndi yobzala kukhala itafika!
19. Kodi n’chiyani chinachitikira anthu otsalira a ku Israyeli ndi Yuda?
19 Tinganene kuti chiweruzo cha Yehova pa anthu oipa a ku Yuda ndi Israyeli chinali chosankha chifukwa anthu olapa ndi amtima wabwino anachitiridwa chifundo. Pokwaniritsa lonjezo la kubwezeretsedwa lolembedwa mu Amosi chaputala 9 limeneli, otsalira olapa a ku Israyeli ndi Yuda anabwerako ku ukapolo wa ku Babulo m’chaka cha 537 Yesu Asanabwere. Atafikanso kudziko lawo lokondedwa, anayambiranso kulambira koyera. Ali pamtendere, anamanganso nyumba zawo ndi kulima minda ya mphesa ndi minda ina.
Yehova Adzaweruza ndi Kulanga Oipa!
20. Kodi mauthenga achiweruzo amene tapendawa omwe Amosi ananena ayenera kutitsimikizira chiyani?
20 Mauthenga a chiweruzo cha Mulungu amene tapendawa, omwe Amosi ananena ayenera kutitsimikizira kuti Yehova adzachotsa kuipa konse komwe kulipo masiku ano. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire kuti zimenezi zidzachitikadi? Choyamba, zitsanzo zakale zimenezi zosonyeza zimene Mulungu anachita kwa oipa m’mbuyomu zikusonyeza kuti adzachitapo kanthu nthawi yathu ino. Chachiwiri, chilango chimene Mulungu anapereka pa ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi wampatuko uja chikusonyeza kuti Mulungu adzawononga Matchalitchi Achikristu, omwe ali mbali yoipa kwambiri ya ‘Babulo Wamkulu,’ ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga.—Chivumbulutso 18:2
21. N’chifukwa chiyani Matchalitchi Achikristu akuyenerera kulangidwa ndi Mulungu?
21 Palibe kukayikira kuti Matchalitchi Achikristu akuyenereradi kulangidwa ndi Mulungu. Kuipa kwa kapembedzedwe kake ndi khalidwe lake n’koonekeratu. Chiweruzo cha Yehova pa Matchalitchi Achikristu ndi dziko lonse la Satana n’choyenerera. N’chosathawikanso chifukwa nthawi yoti alangidwe ikadzakwana, mawu a Amosi pa chaputala 9, vesi 1 adzagwira ntchito. Mawuwo amati: “Wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.” Inde, kaya anthu oipa adzabisale chotani, Yehova adzawapezabe.
22. Kodi ndi mfundo ziti zokhudza chiweruzo cha Mulungu zimene zafotokozedwa bwino pa 2 Atesalonika 1:6-8?
22 Chiweruzo cha Mulungu nthawi zonse chimakhala choyenerera, chosathawika, ndiponso chosankha. Tingaone zimenezi pa mawu amene ananena mtumwi Paulo, akuti: “N’kolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu.” (2 Atesalonika 1:6-8) “N’kolungama kwa Mulungu” kubwezera anthu amene akuyenerera chilango chifukwa chozunza odzozedwa ake. Chiweruzo chimenecho chidzakhala chosathawika, chifukwa oipa sadzapulumuka ‘vumbulutso la Ambuye Yesu pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto.’ Chiweruzo cha Mulungu chidzakhalanso chosankha chifukwa Yesu adzabwezera chilango “iwo osam’dziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.” Ndipo chiweruzo cha Mulungu chidzabweretsera mpumulo anthu oopa Mulungu amene akuzunzika.
Chiyembekezo cha Olungama
23. Kodi m’buku la Amosi tingapezemo chiyembekezo ndi chitonthozo chotani?
23 Ulosi wa Amosi uli ndi uthenga wabwino kwambiri wa chiyembekezo ndi chitonthozo kwa anthu amene ali ndi mtima wabwino. Monga momwe ananeneratu m’buku la Amosi, Yehova sanawonongeretu anthu ake akale. Pomalizira pake anasonkhanitsa anthu ogwidwa ukapolo a ku Israyeli ndi Yuda, ndipo anawabwezeretsa kwawo ndi kuwadalitsa powateteza ndi kuwalemeretsa kwambiri. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani masiku ano? Zikutitsimikizira kuti pamene Yehova azidzapereka chiweruzo chake, adzapeza anthu oipa kulikonse komwe angabisale ndipo adzapezanso anthu amene akuwaona kuti ndi ofunika kuwachitira chifundo, kulikonse komwe angakhale padziko lapansi.
24. Kodi atumiki a Yehova adalitsidwa motani masiku ano?
24 Pamene tikuyembekezera nthawi yoti chiweruzo cha Yehova cholanga oipa chibwere, kodi ife monga atumiki ake okhulupirika chikutichitikira n’chiyani? Yehova watidalitsa moti talemera kwambiri mwauzimu. Kulambira kwathu n’kopanda mabodza ndi chinyengo zimene zimachokera ku ziphunzitso zabodza za Matchalitchi Achikristu. Yehova watidalitsanso potipatsa chakudya chauzimu chochuluka. Koma kumbukirani kuti madalitso ambiri ochokera kwa Yehova amenewa amabweretsanso udindo waukulu. Mulungu akuyembekezera kuti tichenjeze ena za chiweruzo chimene chikubwera. Timayesetsa kuchita zonse zomwe tingathe kuti tipeze anthu “ofuna moyo wosatha.” (Machitidwe 13:48, NW) Zoonadi, tikufuna kuthandiza anthu ambiri kuti nawonso asangalale ndi kulemera kwathu kwauzimu. Ndipo tikufuna kuti adzapulumuke Mulungu akamadzaweruza ndi kulanga oipa m’tsogolo muno. Koma kuti tipeze madalitso amenewa, tiyenera kukhala ndi mtima woyenera. Ulosi wa Amosi umafotokozanso zimenezi, monga momwe tionere mu nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi ulosi wa Amosi umasonyeza bwanji kuti chiweruzo cha Yehova chimakhala choyenerera nthawi zonse?
• Kodi Amosi anapereka umboni wotani wosonyeza kuti chiweruzo cha Mulungu sichithawika?
• Kodi buku la Amosi limasonyeza bwanji kuti Mulungu amasankha akamapereka chiweruzo chake?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Ufumu wa Israyeli sunapewe chiweruzo cha Mulungu
[Chithunzi patsamba 18]
M’chaka cha 537 Yesu Asanabwere, otsalira a Israyeli ndi Yuda anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ku Babulo