Maphunziro Kuchokera m’Malemba: Amosi 1:1-9:15
Kuzimiririka kwa Mtundu
“DZIKONZERETU kukomana ndi Mulungu wako,” akutero “Yehova Mulungu wamakamu” ku mtundu wa Israyeli. (Amosi 4:12, 13) Chifukwa chake? Atachititsidwa khungu ndi kupita patsogolo, Aisrayeli anaiwala Chilamulo chake ndipo anali ndi liwongo la kuipitsa dziko lake lopatulika ndi kulambira mafano, chisembwere, kukhetsa mwazi, ndi chiwawa.
Monga mneneri wa Yehova, Amosi akuimitsidwa kulengeza uthenga wa chenjezo osati kokha ku mtundu wake wa Yuda koma makamaka ku ufumu wa kumpoto wa Israyeli. Iye akutsutsa Israyeli chifukwa cha njira yake ya moyo ya kumwerekera kwaumwini ndi kuneneratu za kuzimiririka kwa pambuyo pake m’manja a mitundu ya adani. Bukhu la Amosi, lolembedwa nthaŵi ina yake pakati pa 829 B.C.E. ndi 804 B.C.E., limapereka chidziŵitso m’kuthekera kwa Mulungu kwa kuwoneratu matsoka omadza, ndipo limapereka machenjezo a pa nthaŵi yake.
Chiwonongeko cha Moto cha Adani a Mulungu
Palibe amene angathawe ziweruzo za Mulungu. Ndi mowona chotani nanga mmene ichi chinatsimikizira kukhala kaamba ka mitundu ya Damasiko (Aramu), Gaza (Filistiya), Turo, Edomu, Amoni, Moabu, ndi Yuda! Yehova ‘sadzabweza’ dzanja lake kuleka kulimbana nawo kaamba ka m’chitidwe wawo wolakwa. Mosasamala kanthu za chimenecho, tsoka lawo lonenedweratu linangotumikira kugogomezera chiweruzo chimene Israyeli anayang’anizana nacho kaamba ka kulephera kusungirira unansi wake wa pangano ndi Mulungu ndi kusunga malamulo ake.—Amosi 1:1–2:16.
Labadirani chenjezo la Mulungu. “Inu nokha ndinakudziŵani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi,” atero Yehova kwa Israyeli. (Amosi 3:2) Ngakhale kuli tero, njira yawo yochimwa inasonyeza chitonzo kaamba ka dzina la Mulungu ndi ufumu. Ambiri anali ogamulapo kukhala achuma, kukhala mu mkhalidwe wabwino wakudza mosachotsa thukuta ndi ‘nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuŵa,’ modyera masuku pamutu abale a iwo eni. (Amosi 3:15) Ndi miyeso yachinyengo, iwo mwadyera ananyenga osauka. Kukana kwawo kulambira kowona kunatanthauza kuti chilango cha Yehova chinali pafupi. Komabe, ‘Yehova sakachita chinthu chirichonse pokhapo atachivumbula icho kwa atumiki ake.’ Chotero, Amosi ananeneratu ziweruzo za Yehova ndi kuchenjeza iwo kuti: “Dzikonzeretu ndi kukomana ndi Mulungu wako.”—Amosi 3:1–4:13.
Yehova Ali Chipulumutso
Mulungu adzasonyeza chifundo kwa awo olapa. “Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo,” Iiri pempho la Yehova kwa Israyeli. (Amosi 5:4) “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.” (Amosi 5:15) Mawu oterowo, ngakhale kuli tero, anyalanyazidwa. Ampatuko anakonda kupita ku Beteli ndi Giligali, maziko a kulambira mafano, kumeneko kukapereka nsembe kwa milungu yonyenga. (Amosi 5:26; 1 Mafumu 12:28-30) Pa mipando yokometsedwa ya minyanga, ochita zoipa ovala bwino akumwa vinyo wotsekemera ndi kudzimwerekeretsa iwo eni ndi zakudya zabwino koposa ndi mafuta. (Amosi 5:11; 6:4-6) “Tsiku la Yehova” likubwera, ndipo “pali lye mwini” Mulungu walumbira chiwonongeko cha Israyeli. (Amosi 5:18; 6:8) Yehova adzadzutsa mtundu wodzapondereza Israyeli ndi kumtsogoza mu ukapolo.—Amosi 5:1–6:14.
Opani Yehova, osati otsutsa. Chiwonongeko cha Israyeli chikanabweretsedwa ndi gulu la dzombe kapena moto wosakaza. Amosi anapempha kwa Mulungu mokomera Israyeli, ndipo “Yehova anachita chisoni” pa chiweruzo chake, chotero sichinachitidwe mwa njira imeneyi. Ngakhale kuli tero, monga womanga wofufuza kuwongoka kwa khoma ndi chingwe, Yehova “sadzalekanso” Israyeli. (Amosi 7:1-8) Mtunduwo uyenera kuwonongedwa. Wokwiyitsidwa ndi uthenga wa mneneriyo, Amaziya, wansembe wa kulambira kwa mwana wa ng’ombe, mwachinyengo akupeza Amosi ndi mlandu wa kuwukira ufumu ndi kulamulira iye ‘kuthaŵira ku dziko la Yuda, ndi kusachitanso uneneri uliwonse’ pa Beteli. (Amosi 7:12, 13) Kodi Amosi akuchita mantha? Ayi! Iye mopanda mantha akuneneratu za imfa ya Amaziya ndi tsoka kaamba ka banja lake. Monga mmene chipatso chimakololedwa pa nthaŵi ya kututa, chotero iri nthaŵi kaamba ka Yehova kuchita kuŵerengera ndi Israyeli. Sipadzakhala kuthaŵa.—Amosi 7:1–8:14.
Pali chiyembekezo kaamba ka awo okhulupirira mwa Yehova. “Sindidzawononga nyumba ya Yakobo kuitha konse,” atero Yehova. Padakali chiyembekezo kaamba ka ena a ana a Yakobo koma osati kaamba ka ochimwa. Chiwonongeko chawo chiri chotsimikizirika. Mosasamala kanthu za chimenecho, Yehova “adzabwezanso undende wa anthu” a Israyeli.—Amosi 9:1-15.
Maphunziro kaamba ka lerolino: Aja odzipanga iwo eni kukhala adani a Mulungu adzaweruzidwa moyenerera imfa. Ngakhale kuli tero, aliyense wolabadira uthenga wa chenjezo laumulungu la kulapa adzalandira chifundo cha Yehova ndi kusungidwa wamoyo. Ngati tiwopa Mulungu, sitidzalola otsutsa kutiletsa kuchita chifuno chake.
[Bokosi patsamba 22]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:5—Mizinda yakale inali ndi malinga a atali ndi zipata zazikulu. Kuti atseke zipata zimenezi, mipiringidzo yaitali ya chitsulo kapena mkuwa inayedzeketsedwa kwa izo mkati. ‘Kuthyola mipiringidzo wa Damasiko’ kunatanthauza kuti mzinda waukulu wa Aramu ukagwa kwa Asuri. Chikakhala ngati kuti zipata zake za mzinda sizikanatsekedwa chifukwa mipiringidzo yake inathyoledwa.—2 Mafumu 16:8, 9.
○ 4:1—Akazi okonda zokondweretsa okhala m’Samariya anatchedwa “ng’ombe zazikazi za ku Basana.” Pabusa polemera pa Basana panathandizira kupereka malo abwino obalirako ziweto. (Deuteronomo 32:14; Ezekieli 39:18) “Ng’ombe zazikazi za ku Basana” zadyera zimenezi mwachiwonekere zinasonkhezera “azimbuye,” kapena amuna awo, kulanda ndalama kuchokera kwa osauka kotero kuti adzaze “nyumba za minyanga” zawo. (Amosi 3:15) Machitidwe oterowo, ngakhale ndi tero, anatulukapo m’chilango chaumulungu.
○ 4:6—Kalongosoledwe kakuti “mano oyera” kalongosoledwa ndi mawu ofanana akuti “kusowa mkate.” Chotero kamawonekera kulozera ku nthaŵi ya njala, pamene mano anali oyera chifukwa panalibe chirichonse chakudya. Mwachiwonekere, Yehova analongosola kusavomereza kwake kulambira mafano kwa ufumu wa mafuko khumi mwa kutumiza njala ku dzikolo, monga momwe analonjezera kale pasadakhale. (Deuteronomo 28:48) Ngakhale kuli tero, osatinso kameneka kapena malongosoledwe ena a chiweruzo chaumulungu anafikira mitima ya anthu akuswa pangano amenewa.—Amosi 4:6, 8-11.
○ 5:2—Pamene Amosi ananena ulosi wake, anthuwo limodzi ndi dziko la Israyeli anali asanagonjetsedwe ndi kuwonongedwa ndi ulamuliro wakunja. Chotero, iwo anali anachitiridwa chithunzi monga namwali. Mu kokha zaka zochepa, ngakhale ndi tero, namwali Israyeli akagwa kwa Asuri ndi “kutengedwa kumka naye kundende kutsogolo kwa Damasiko.” (Amosi 5:27) Amosi ali wotsimikiza chotero za chiwonongeko cha Israyeli chifukwa cha kusakhulupirika kwake kotero kuti akukulongosola iko monga ngati kunali kutachitika kale.
○ 7:1—“Ndicho chibwereza atawasengera mfumu” chimalozera mwachiwonekere kwenikweni ku msonkho kapena malipiro ochitidwa ndi mfumu kupereka zakudya kaamba ka nyama zake ndi ankhondo. Msonkho wa mfumuwo unafunikira kulipiridwa choyamba, pambuyo pa umene anthu akatenga “udzu,” kapena zomera, kaamba ka kugwiritsira ntchito kwawo. Koma asanachite tero, dzombe linabwera ndi kudya zobzalidwa pambuyo pake zimenezi.
○ 8:2—Zipatso za chirimwe zinatoledwa kumapeto kwa nyengo ya kututa. Mapeto a chaka cha malimidwe chotero anaimira kuti Israyeli anafika ku chitsiriziro chake. “Sindidzawalekanso,” analengeza tero Yehova. Mtunduwo unayandikira kuperekedwa kwa chiweruzo chake.
○ 9:7—Chifukwa cha makolo awo okhulupirika, Yehova anasankha Aisrayeli, napulumutsa makolo awo kuchokera ku ukapolo ku Igupto, ndi kuwabweretsa iwo mu Kanani. Koma panalibe maziko a kunyada pa ichi, kaamba kakuti kuipa kwawo kunawapatsa kaimidwe kamodzimodziko monga Akusi. (Yerekezani ndi Aroma 2:25.) Mofananamo, kupulumutsidwa kuchokera ku Igupto sikunalinso chitsimikizo cha chivomerezo chaumulungu chopitirizabe monga mmene chinaliri chenicheni chakuti Afilisti ndi a Aramu anali kukhala m’malo osakhala malo awo oyambirira. Kukhala mbadwa kuchokera kwa makolo okhulupirika sikunali kokhoza kupulumutsa Aisrayeli. Kaimidwe kovomerezedwa ndi Mulungu kamadalira pa kugwirizana ndi chifuno chake.—Amosi 9:8-10; Machitidwe 10:34, 35.