Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Yopa—Doko Lotchuka Lakale
ISRAYELI WAKALE anali ndi gombe lalitali, lamchenga. Komabe Aisrayeli sanali odziŵika mwapadera kukhala anthu aumoyo wa m’nyanja. Mtundu wa gombe lawo ungakhale unali chochititsa.
Ilo linali mzera wosalekeza wa madoko ndi zitunda, zopangidwa ndi mchenga wotengeredwa ku nyanja ndi Mtsinje wa Nile.a Ngati munawutsatira ndi bwato kuchokera ku malire a Igupto, simukanapeza doko lachibadwa lenileni kum’mwera kwa Phiri la Karimeli.
Koma chifupifupi theka la mtunda mokwezeka gombe la Israyeli mukanawona pagomo mzinda wa Yopa. Monga mmene chithunzithunzicho chikusonyezera, mdadada wa miyala ya mphepete mwa nyanja inapanga mtunda wotambalala waung’ono. Pamene kuli kwakuti doko lopangidwa linali lochepera ku lomwe linali chapatali cha kumpoto pa Acre (Ptolemaïs), ilo linapangitsabe Yopa kukhala yotchuka. (Machitidwe 21:7) Kufikira pamene Herode Wamkulu anamanga doko losakhala lachibadwa la Kaisareya, Yopa inali malo abwino koposa m’mphepete mwa gombelo okochezapo zombo. Ichi chimawunikira zilozero zina za Baibulo ku Yopa.
Pamene anadzipereka kuthandiza Solomo m’kumanga kachisi, Huramu mfumu ya Turo inanena kuti: “Ndipo tidzabwera [ndi mitengo kuchokera ku Lebano] kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.” (2 Mbiri 2:1, 11, 16) Mitengo yoyandamitsa imeneyi ingakhale inachokera ku madoko a Chifoinike a Turo kapena Sidoni. (Yesaya 23:1, 2; Ezekieli 27:8, 9) Kupitirira Karimeli, mitengo ya mkungudza yoyandamitsa inatsikira ku Yopa. Kuchokera kumeneko mitengo ya mkungudzayo inkatengeredwa ku Yerusalemu, makilomita 55 kum’mawa/kum’mawa koma chakum’mwera. Yopa inalinso doko lotsitsirapo mitengo ya mkungudza pamene Ayuda anamanganso kachisi pambuyo pa kutengedwa mu ukapolo.—Ezara 3:7.
Mwinamwake ogwira ntchito opita ndi matabwawo anakwera zombo za Chifoinike, zofanana ndi chitsanzo chowonetsedwacho. Pamene inu mukuphunzira iyo, kumbukirani kuti pambuyo pakuti Yehova anatuma Yona ku Nineve, mneneriyo anathaŵira njira yosiyanako. “[Yona] anatsikira ku Yopa, napezako chombo chomuka ku Tarisi, napereka ndalama zake, natsikira mmenemo, kuti apite nawo ku Tarisi kuzemba Yehova.”—Yona 1:1-3.
Mwachiwonekere, Yona anakwera chombo chonyamula katundu choyenda panyanja cha mtundu umenewo, chomwe chinali chokhoza kuyenda ulendo wautali kuchokera ku Yopa kupita ku Tarisi (mwachiwonekere Spain yakale). Icho mothekera chinali ndi mzati wosemedwa wautali kutsogolo, cha pamene panamangiriridwa nangula wa mwala. Apaulendo, oyendetsa, ndi katundu wina ankakwana padenga la chombocho, lomwe silinasonyezedwe pa chithunzithunzicho. Kunsi kwa dengalo kunali chipinda, kumene katundu wowonjezeka ankasungidwa ndi kumene Yona anapita kukagona. Chombocho chinapangidwa ndi matabwa olimba a tsanya ndipo chinali ndi mlongoti wa mkungudza kuchirikiza tanga lalikulu. Onani mbali zonse ziŵiri ndandanda ya nkhafi zazitali (mwinamwake za mtengo wa oak kuchokera ku Basani). Tsopano talingalirani chombocho pa nyanja ndipo chowopsyezedwa ndi namondwe wamphamvu. Mvetserani amalinyero akulirira kwa milungu yawo kaamba ka thandizo kufikira pomalizira akakamizidwa kuponyera Yona pa nyanja kotero kuti iwo asawonongeke.—Ezekieli 27:5-9; Yona 1:4-15.
Yopa ya m’zana loyamba inali mudzi wa mpingo wa Akristu, ena a iwo angakhale anali ogwira ntchito pa madoko kapena omwe kale anali amalinyero. Chiŵalo cha mpingo wa kudoko la kunyanja wotanganitsidwa umenewu anali Myuda wachikazi Dorika (Tabita). “Mkazi ameneyo anadzala ndi ntchito zabwino ndi zachifundo zimene anazichita.” M’chaka cha 36 C.E., Dorika anadwala namwalira, chomwe chinachititsa ambiri kulira, akumambukira ntchito zake zabwino zochuluka. Akristu anzake anabweretsa mtumwi Petro kuchokera ku Luda (Lod yamakono, pafupi ndi bwalo landege la Tel Aviv) ku Yopa. Petro anawukitsa mlongo wokondedwa ameneyu, chozizwitsa chimene “chinadziŵika ku Yopa konse, ndipo ambiri anakhulupirira.”—Machitidwe 9:36-42.
Petro anakhala mu Yopa kwa kanthaŵi ku nyumba ya Simoni, wofufuta zikopa. Kuno mtumwiyo anakhala ndi masomphenya omwe anamtsogolera kutenga ena a abale a mpingo wa Yopa kumpoto pa msewu wa m’mphepete mwa nyanja kupita ku doko latsopano la Kaisareya. Kumeneko Petro analalikira ndi kubatiza kazembe Wachiroma Korneliyo, Wakunja wosadulidwa woyambirira kukhala Mkristu wodzozedwa ndi mzimu. (Machitidwe 9:43–10:48) Ndi chisangalalo chotani ndi chimwemwe chomwe chinayenera kukhala chinaliko mu Yopa pamene abalewo anabwerera ndi uthenga wa chochitika chachikulu chimenechi m’mbiri Yachikristu!
Lerolino alendo ambiri amachezera Yopa, imene iri mbali ya Tel Aviv-Jaffa wamakono, ndipo iwo mosavuta angakumbukirenso zochitika za m’Baibulo zomwe zinachitika pa doko lotchuka limeneli.
[Mawu a M’munsi]
a Inu mungawone bwino gombe lamchenga limeneli m’chithunzithunzi cha satellite pa chikuto cha 1989 Kalenda ya Mboni za Yehova. Kalenda imeneyi imaperekanso chithunzithunzi chokulirapo cha kawonedwe komwe kali pamwambako ka Yopa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.