-
Anaphunzira pa Zolakwa ZakeNsanja ya Olonda—2009 | January 1
-
-
Koma mwadzidzidzi anangoona chinthu chinachake chachikulu, chabii chikubwera poteropo. Kenako chinam’thamangira kukamwa kwake kuli yasaa ndipo Yona anangozindikira kuti cham’meza.
Apa anaona kuti basi wajiwa. Komabe Yona anadabwa kuti adakali moyo. Sanalumidwe kapena kugayidwa m’mimbamo ndipo ankapuma bwinobwino ngakhale kuti amenewa anayenera kukhala manda ake. Kenaka Yona anayamba kuchita mantha kwambiri. Iye sanakayikirenso kuti Mulungu wake,Yehova, ndi amene ‘anaikiratu chinsomba chachikulu kuti chim’meze.’c—Yona 1:17.
Yona anakhala m’mimba mwa chinsombacho kwa maola ambiri. Muchimdima cha ndiweyani chimenechi, iye anayamba kusinkhasinkha ndiponso kupemphera kwa Yehova Mulungu. Pemphero lake, lomwe lili m’chaputala chachiwiri cha buku la Yona, limatithandiza kum’dziwa bwino Yonayu. Limasonyeza kuti Yona ankadziwa bwino Malemba chifukwa anatchula mfundo zambiri za m’buku la Masalmo. Limasonyeza kuti iye anali ndi mtima woyamikira kwambiri. Yona ananena kuti: “Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mawu akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso n’cha Yehova.”—Yona 2:9.
Yona anaphunzira kuti Yehova angathe kupulumutsa munthu aliyense, kulikonse ndiponso nthawi ina iliyonse. Ngakhale kuti mtumiki wakeyu anali ‘m’mimba mwa nsomba,’ Yehova anam’pulumutsa. (Yona 1:17) Ndi Yehova yekha amene akanatha kusunga munthu m’mimba mwa chinsomba n’kukhala bwinobwino kwa masiku atatu, usana ndi usiku. Masiku ano ndi bwino kuti tizikumbukira kuti Yehova ndi “Mulungu amene m’dzanja mwake muli mpweya wanu.” (Danieli 5:23) Popanda Yehova sibwenzi tikumapuma n’kukhala ndi moyo. Kodi timayamikira zimenezi? Ndiyetu tizimumvera Yehovayo nthawi zonse.
Nanga kodi Yona uja anatani? Kodi anayamba kumvera Yehova posonyeza kuyamikira kwake? Inde. Patatha masiku atatu, nsomba ija inam’pititsa m’mphepete mwa nyanja ndipo “inam’sanzira Yona kumtunda. (Yona 2:10) Tangoganizirani kuti Yona anayenda ulendo wonsewo popanda ngakhale kusambira. Komabe, atafika kumtundako anafunika kudziwa kolowera. Pasanapite nthawi, Yona anakumananso ndi chiyeso china chimene chinaonetsa kuti iyeyu analidi munthu woyamikira. Lemba la Yona 3:1, 2, limati: “Ndipo mawu a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti, Nyamuka, pita ku Nineve mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.” Kodi Yona anatani?
-
-
Anaphunzira pa Zolakwa ZakeNsanja ya Olonda—2009 | January 1
-
-
c Mawu a Chiheberi akuti “nsomba,” m’Chigiriki anawamasulira kuti “chilombo cha m’nyanja,” kapena “chinsomba chachikulu.” Sitingathe kudziwa kuti imeneyi inali nsomba yamtundu wanji kwenikweni, komabe tikudziwa kuti m’nyanja ya Mediterranean muli nsomba zikuluzikulu zotchedwa shaki zimene zingathe kumeza munthu wathunthu. M’nyanja zina nsomba zimenezi zimatha kukula kwambiri moti zina zimakhala zazitali mamita 15, kapenanso kuposa.
-
-
Anaphunzira pa Zolakwa ZakeNsanja ya Olonda—2009 | January 1
-
-
Ndipotu zinthu zina zodabwitsa zimachitika popanda mphamvu ya Mulungu. Mwachitsanzo, akuti mu 1758, munthu wina anagwa m’sitima yomwe inkayenda pa nyanja ya Mediterranean ndipo anamezedwa ndi chinsomba cha mtundu wa shaki. Anthu anachiwombera chinsombacho ndipo chinalavula munthuyo asanavulale paliponse ndipo anapulumuka. Ngati izi zinachitikadi ndiye kuti n’zodabwitsa kwambiri koma si zozizwitsa. Ndiyeno kodi Mulungu sangagwiritse ntchito mphamvu zake m’njira yoposa pamenepa?
Anthu otsutsawa amanenanso kuti munthu sangakhale moyo kwa masiku atatu m’mimba mwa chinsomba. Koma tikudziwa kuti anthu amatha kuika mpweya m’mathanki kuti azitha kupuma ali pansi pa nyanja. Ndiyeno kodi Mulungu akanalephera kugwiritsa ntchito mphamvu zake ndi nzeru zake zapamwamba kuti Yona akhalebe moyo kwa masiku atatu? Pajatu mngelo wa Yehova anauza mayi wa Yesu Mariya kuti, “pakuti zimene Mulungu wanena, sizilephereka.” (Luka 1:37)
-