Kuyenda ndi Mulungu—Tikumadikira Umuyaya
“Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.”—MIKA 4:5.
1. Kodi nchifukwa chiyani Yehova akutchedwa ‘Mfumu ya nthaŵi zosatha’?
YEHOVA MULUNGU analibe chiyambi. Moyenerera amatchedwa “Nkhalamba ya kale lomwe,” popeza wakhalako kwa muyaya wonse. (Danieli 7:9, 13) Yehova adzakhalanso kwamuyaya kutsogoloku. Iye yekha ndiye ‘Mfumu ya nthaŵi zosatha.’ (Chivumbulutso 10:6; 15:3) Ndipo kwa iye, zaka chikwi zili “ngati dzulo, litapita, ndi monga ulonda wa usiku.”—Salmo 90:4.
2. (a) Kodi cholinga cha Mulungu kwa anthu omvera nchiyani? (b) Kodi chiyembekezo chathu ndi zolinga zathu tiyenera kuzisumika pa chiyani?
2 Popeza Mpatsi wa moyo ali wamuyaya, anatha kupatsa anthu aŵiri oyamba, Adamu ndi Hava, chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso. Komano chifukwa cha kusamvera, Adamu anataya ufulu wokhala ndi moyo wosatha, napatsa uchimo ndi imfa kwa mbadwa zake. (Aroma 5:12) Koma kupanduka kwa Adamu sikunaletse cholinga choyambirira cha Mulungu. Chifuniro cha Yehova nchakuti anthu omvera akhale ndi moyo kosatha, ndipo adzakwaniritsa cholinga chake kosalephera. (Yesaya 55:11) Chotero tiyenera kusumika chiyembekezo chathu ndi zolinga zathu pa kutumikira Yehova tikumadikira umuyaya. Pamene kuli kwakuti tikufuna kukumbukira “tsiku la Mulungu,” mpofunika kukumbukira kuti cholinga chathu ndicho kuyenda ndi Mulungu kosatha.—2 Petro 3:12.
Yehova Achitapo Kanthu Panthaŵi Yake Yoikidwiratu
3. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yehova ali ndi “nthaŵi yoikidwiratu” yokwaniritsira zolinga zake?
3 Monga oyenda ndi Mulungu, tikufunitsitsa kuchita chifuniro chake. Tikudziŵa kuti Yehova ndiye Wosunganthaŵi Wamkulu, ndipo tili ndi chidaliro chakuti salephera kukwaniritsa zolinga zake panthaŵi yake yoikidwiratu. Mwachitsanzo, “pokwaniridwa nthaŵi, Mulungu anatuma Mwana wake.” (Agalatiya 4:4) Mtumwi Yohane anauzidwa kuti panali “nthaŵi [yoikidwiratu, NW]” yokwaniritsira zinthu zaulosi zimene anaona. (Chivumbulutso 1:1-3) Pali “nthaŵi [yoikidwiratu, NW] ya akufa yakuti aweruzidwe.” (Chivumbulutso 11:18) Zaka zoposa 1,900 zapitazo, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti Mulungu “anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.”—Machitidwe 17:31.
4. Tidziŵa bwanji kuti Yehova akufuna kuthetsa dongosolo loipa ili la zinthu?
4 Yehova adzathetsa dongosolo loipa ili la zinthu, pakuti dzina lake likuchitidwa mwano m’dziko lamakonoli. Oipa achuluka. (Salmo 92:7) Mwa mawu ndi ntchito zawo, amachita chipongwe kwa Mulungu, ndipo zimampweteka kuona atumiki ake akutukwanidwa ndi kuzunzidwa. (Zekariya 2:8) Ndiye chifukwa chake Yehova walamula kuti gulu lonse la Satana lithetsedwe posachedwapa! Mulungu wakhazikitsa nthaŵi yeniyeni pamene adzachita zimenezi, ndipo maulosi a Baibulo amene akukwaniritsidwa akusonyeza bwino lomwe kuti tsopano tili ‘m’nthaŵi ya chimaliziro.’ (Danieli 12:4) Adzachitapo kanthu posachedwa kudalitsa onse omkonda.
5. Kodi Loti ndi Habakuku anaiona motani mikhalidwe imene inawazinga?
5 Atumiki akale a Yehova analakalaka kuona mapeto a kuipa. Loti wolungamayo anali “wolema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa aja.” (2 Petro 2:7) Pochita chisoni ndi mmene mikhalidwe inalili pomzinga ponse, mneneri Habakuku anadandaula kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu? Ndifuulira kwa inu za chiwawa, koma simupulumutsa. Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndewu, nauka makani.”—Habakuku 1:2, 3.
6. Kodi Yehova anati chiyani poyankha pemphero la Habakuku, ndipo tikuphunzirapo chiyani?
6 Mbali ya yankho la Yehova kwa Habakuku inali m’mawu awa: “Masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Chotero Mulungu ananena kuti adzachitapo kanthu pa “nyengo yoikidwiratu.” Ngakhale kuti zingaoneke ngati kuchedwa, Yehova adzakwaniritsabe cholinga chake—kosalephera!—2 Petro 3:9.
Kutumikira ndi Changu Chosatha
7. Ngakhale kuti Yesu sanadziŵe nthaŵi yeniyeni pamene tsiku la Yehova likadza, kodi anaichita motani ntchito yake?
7 Kodi tifunikira kudziŵa nthaŵi yeniyeni ya Yehova yochitira zinthu kuti tiyende ndi Mulungu mwachangu? Ayi. Talingalirani zitsanzo zina. Yesu anali kufunitsitsa kudziŵa nthaŵi imene chifuniro cha Mulungu chidzachitika padziko lapansi monga kumwamba. Inde, Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ngakhale kuti Yesu anadziŵa kuti pempho limeneli lidzayankhidwa, sanadziŵe nthaŵi yake yeniyeni. Mu ulosi wake waukulu wonena za mapeto a dongosolo ili la zinthu, anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:36) Popeza kuti Yesu Kristu ali wofunika kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa zolinga za Mulungu, ndiye adzapha adani a Atate wake wakumwamba. Komabe, pamene Yesu anali padziko lapansi ngakhale iye sanadziŵe pamene Mulungu adzachitapo kanthu. Kodi zimenezo zinampangitsa kukhala ndi changu chochepa mu utumiki wa Yehova? Ayi! Ataona Yesu akuyeretsa kachisi mwachangu, “akuphunzira ake anakumbukira kuti kunalembedwa, Changu cha panyumba yanu chandidya ine.” (Yohane 2:17; Salmo 69:9) Yesu anadzitangwanitsa ndi ntchito imene anatumidwa kuchita, ndipo anaichita ndi changu chosalekeza. Anatumikiranso Mulungu akudikira umuyaya.
8, 9. Pamene ophunzira anafunsa za kubwezeretsedwa kwa Ufumu, anauzidwa chiyani, ndipo anatani?
8 Ndi mmenenso anachitira ophunzira a Kristu. Yesu anakumana nawo ali pafupi kukwera kumwamba. Nkhaniyo imati: “Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthaŵi ino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” Mofanana ndi Mbuye wawo, anafunitsitsa kuti Ufumuwo udze. Koma Yesu anayankha kuti: “Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa Iye yekha. Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.”—Machitidwe 1:6-8.
9 Palibe umboni wakuti ophunzirawo anagwa ulesi ndi yankho limeneli. M’malo mwake, iwo anatanganidwa mwachangu ndi ntchito yolalikira. M’milungu ingapo, anadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chawo. (Machitidwe 5:28) Ndipo mkati mwa zaka 30, anafutukula ntchito yawo kufika pamlingo woti Paulo anatha kunena kuti uthenga wabwino unalalikidwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23) Ngakhale kuti Ufumuwo ‘sunabwezeredwe kwa Israyeli’ monga momwe ophunzirawo anayembekezera molakwa ndipo sunakhazikitsidwe kumwamba panthaŵi yawo, anatumikirabe Yehova mwachangu akumadikira umuyaya.
Kupenda Zolinga Zathu
10. Kusadziŵa pamene Mulungu adzawononga dongosolo la Satana kumatipatsa mpata woonetsa chiyani?
10 Atumikinso amakono a Yehova amalakalaka kuona mapeto a dongosolo ili loipa la zinthu. Komabe, chachikulu kwa ife sikulanditsidwa kwathu kuloŵa m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu. Tikufuna kuona dzina la Yehova litayeretsedwa ndi uchifumu wake utatsimikizidwa. Chifukwa cha zimenezi, ndife okondwa kuti Mulungu sanatiuze ‘tsiku kapena nthaŵi’ yoikidwa yowononga dongosolo la Satana. Zimenezi zimatipatsa mpata woonetsa kuti tili otsimikiza mtima kuyenda ndi Mulungu kwamuyaya chifukwa chakuti timamkonda ndipo osati kuti tili ndi zolinga zadyera zakanthaŵi.
11, 12. Kodi kukhulupirika kwa Yobu kunayesedwa motani, ndipo kodi chiyeso chimenecho chimatikhudza bwanji ife?
11 Kukhala kwathu okhulupirika kwa Mulungu kumatithandizanso kuonetsa kuti Mdyerekezi ananama pamene ananena kuti Yobu wolungamayo—ndiko kutinso anthu onga iye—amatumikira Mulungu chifukwa cha dyera. Yehova atafotokoza kuti mtumiki wake Yobu anali munthu wangwiro, woongoka, woopa Mulungu, Satana mwanjiru anati: “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe? Kodi simunamchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoŵeta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.” (Yobu 1:8-11) Mwa kukhala kwake wokhulupirika poyesedwa, Yobu anasonyeza kuti zonena zanjiru zimenezi zinali zabodza.
12 Mwa kukhala okhulupirika mofananamo, tingatsutse chinenezo chilichonse chausatana chakuti tikutumikira Mulungu chabe chifukwa chodziŵa kuti mphotho ili pafupi. Kusadziŵa nthaŵi yeniyeni pamene chiweruzo cha Mulungu chidzaperekedwa pa oipa kumatipatsa mpata wosonyeza kuti timakondadi Yehova ndipo tikufuna kuyenda m’njira zake kosatha. Zimasonyeza kuti tili okhulupirika kwa Mulungu ndipo timakhulupirira njira imene iye amachitira zinthu. Ndiponso, kusadziŵa tsiku ndi nthaŵi kumatithandiza kukhala atcheru ndi ogalamuka mwauzimu chifukwa tidziŵa kuti mapeto afika nthaŵi iliyonse, monga mbala usiku. (Mateyu 24:42-44) Mwa kuyenda ndi Yehova tsiku ndi tsiku, timakondweretsa mtima wake ndi kupereka yankho kwa Mdyerekezi, amene amtonza.—Miyambo 27:11.
Konzekerani Umuyaya!
13. Kodi Baibulo limasonyezanji za kukonzekera za m’tsogolo?
13 Amene akuyenda ndi Mulungu tsopano akudziŵa kuti nkwanzeru kukonzekera za m’tsogolo pamlingo woyenera. Pozindikira mavuto ndi zofooka za ukalamba, anthu ambiri amayesa kugwiritsa ntchito bwino unyamata wawo ndi nyonga kuti pamoyo wawo waukalamba akakhale ndi ndalama zokwanira. Bwanji nanga za tsogolo lathu lauzimu lofunika koposalo? Miyambo 21:5 imati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphaŵi.” Kukonzekera tikumadikira umuyaya nkothandizadi. Popeza sitikudziŵa nthaŵi yeniyeni pamene mapeto a dongosolo ili adzadza, tiyenera kulingalirapo kwambiri pa zosoŵa zathu za m’tsogolo. Komatu tisapambanitse ndipo tiike zinthu zaumulungu patsogolo m’moyo. Anthu opanda chikhulupiriro angaganize kuti kuika mtima wako pa kuchita chifuniro cha Mulungu nkusaona patali. Kodi ndi mmene zililidi?
14, 15. (a) Kodi Yesu anasimba fanizo lotani lonena za kukonzekera za m’tsogolo? (b) Nchifukwa chiyani munthu wachuma wa m’fanizo la Yesu sanali kuona patali?
14 Yesu anasimba fanizo lopatsa nzeru pankhaniyi. Anati: “Munda wake wa munthu mwinichuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga? Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani? Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.”—Luka 12:16-21.
15 Kodi Yesu anali kunena kuti munthu wachumayo sakanagwira ntchito pofuna kukhala ndi chuma chokwanira m’tsogolo? Ayi, pakuti Malemba amalimbikitsa kugwira ntchito kwambiri. (2 Atesalonika 3:10) Chimene munthu wachumayo analakwa chinali chakuti sanachite zofunikira kuti akhale nacho “chuma cha kwa Mulungu.” Ngakhale ngati akanasangalala ndi chuma chake zaka zambiri, akanafabe pomaliza pake. Sanali kuona patali, sankaganiza za umuyaya.
16. Kodi nchifukwa chiyani tingadalire Yehova kaamba ka tsogolo lachisungiko?
16 Kuyenda ndi Yehova tikudikira umuyaya kumathandiza ndiponso nkuoneratu zapatali. Ndiyo njira yabwino kwambiri yokonzekera m’tsogolo. Pamene kuli kwanzeru kukonzekera zinthu zothandiza ngati sukulu, ntchito, ndi maudindo a m’banja, tizikumbukira nthaŵi zonse kuti Yehova sasiya atumiki ake okhulupirika. Mfumu Davide inaimba kuti: “Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.” (Salmo 37:25) Mofananamo Yesu analonjeza kuti Mulungu adzasamalira onse ofuna Ufumu ndi kuyenda m’njira zolungama za Yehova.—Mateyu 6:33.
17. Tidziŵa bwanji kuti mapeto ali pafupi?
17 Ngakhale kuti tikutumikira Mulungu tikumadikira umuyaya, timakumbukirabe tsiku la Yehova. Maulosi a Baibulo amene akukwaniritsidwa akupereka umboni wosatsutsika wakuti tsikulo layandikira. Zaka za zana lino zakhala za nkhondo, miliri, zivomezi, ndi njala, limodzi ndi kuzunzidwa kwa Akristu oona ndi kulalikidwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi. Zonsezi ndi zochitika za m’nthaŵi ya mapeto a dongosolo ili loipa la zinthu. (Mateyu 24:7-14; Luka 21:11) Dziko ladzala ndi aja “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-5) Masiku ano oŵaŵitsa otsiriza, moyo kwa ife atumiki a Yehova ngwovuta. Mmenetu timalakalakira tsiku pamene Ufumu wa Yehova udzachotsa kuipa konse! Pakali pano, titsimikizetu kuyenda ndi Mulungu tikumadikira umuyaya.
Kutumikira Tikumadikira Moyo Wosatha
18, 19. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti anthu okhulupirika akale anatumikira Mulungu akudikira umuyaya?
18 Pamene tikuyenda ndi Yehova, tikumbukire chikhulupiriro cha Abele, Enoke, Nowa, Abrahamu, ndi Sara. Atawatchula, Paulo analemba kuti: “Iwo onse adamwalira m’chikhulupiriro, osalandira malonjezano, komatu adawaona ndi kuwalankhula kutali, navomereza kuti ali alendo ndi ogonera padziko.” (Ahebri 11:13) Okhulupirika amenewo ‘anakhumba lina loposa [“malo oposa,” NW], ndilo la m’Mwamba.’ (Ahebri 11:16) M’chikhulupiriro, anayembekezera malo oposa mu ulamuliro wa Ufumu wa Mesiya wa Mulungu. Tili otsimikiza kuti Mulungu adzawafupa ndi moyo wamuyaya m’malo oposa amenewo—Paradaiso wapadziko lapansi wolamuliridwa ndi Ufumuwo.—Ahebri 11:39, 40.
19 Mneneri Mika anatchula chikhumbo chimene anthu a Yehova ali nacho cha kulambira Mulungu kwamuyaya. Analemba kuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mlungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” (Mika 4:5) Mika anatumikira Yehova mokhulupirika kufikira imfa. Ataukitsidwa m’dziko latsopano, mneneri ameneyo mosakayikira adzapitiriza kuyenda ndi Mulungu nthaŵi yomka muyaya. Ali chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife amene tikukhala mkati mwenimweni mwa nthaŵi ya mapeto!
20. Kodi tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?
20 Yehova amayamikira chikondi chimene timaonetsa pa dzina lake. (Ahebri 6:10) Amadziŵa kuti nkovuta kwa ife kukhala okhulupirika kwa iye m’dzikoli lolamulidwa ndi Mdyerekezi. Koma ngakhale kuti “dziko lapansi lipita, . . . iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:17; 5:19) Choncho pokhala Yehova akutithandiza, titsimikize kupirira mayesero amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Tisumiketu maganizo athu ndi moyo pa madalitso odabwitsa olonjezedwa ndi Atate wathu wachikondi wakumwamba. Amenewa tingawapeze tikapitiriza kuyenda ndi Mulungu tikumadikira umuyaya.—Yuda 20, 21.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi cholinga cha Mulungu kwa anthu omvera nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa chiyani Yehova sanachitepo kanthu kuthetsa dziko losapembedzali?
◻ Nchifukwa chiyani kusadziŵa nthaŵi yeniyeni pamene Mulungu adzachitapo kanthu sikuyenera kufooketsa changu chathu?
◻ Kodi mapindu ena a kuyenda ndi Mulungu tikumadikira umuyaya ndi otani?
[Chithunzi patsamba 17]
Kuyenda ndi Mulungu kumafuna kuti timtumikire mwachangu mmene anachitira ophunzira oyambirira a Kristu