Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Nahumu 1:1-3:19
Chipulumutso Nchothekera Pamene Mulungu Abwezera Chilango
“KATSALA kanthaŵi ndipo oipa adzatha psyiti.” (Salmo 37:10) Kunena kuti mawuwa adzakwaniritsidwa kwasonyezedwa mwamphamvu m’mabukhu a Baibulo olembedwa ndi Nahumu ndi Habakuku. Amuna olimba mtima amenewa anamaliza kulemba maulosi awo mu ufumu wa Yuda mkati mwa mbali yothera ya zana lachisanu ndi chiwiri B.C.E.
Choyamba, lingalirani ulosi wa Mulungu wolengezedwa ndi Nahumu. Kodi ndi maphunziro otani omwe iwo uli nawo?
Kubwezera Chilango kwa Mulungu Nkotsimikizirika
Yehova amafuna kudzipereka kotheratu. (Eksodo 20:5) M’kugamula kotsutsana ndi likulu la Asuri, Nineve, Nahumu akusonyeza kuti kubwezera chilango kwa Mulungu kudzaperekedwa pa adani amene samampatsa lye kudzipereka koteroko. Nkulekeranji, popeza pamaso pake mapiri agwedezeka, zitunda zisungunuka, ndi dziko lapansi likwezeka! Ndani angaime molimbana ndi kutentha kwa ukali wake?—1:1-6.
Tingadalire pa Yehova monga populumukirapo. Inde, Mulungu amachinjiriza awo ofunafuna populumukirapo mwa iye. Adani ake pokhala atawonongedwa, kutsendereza sikudzabukanso kwa nthaŵi yachiŵiri. Pali mbiri yabwino ya mtendere kaamba ka Yuda, popeza kuti kulambira kowona sikudzatsekerezedwa.—1:7–2:2.
Anthu osalungama sadzapambana. Ichi chiri chowonekera kuchokera ku chimene chinachitika ku Nineve. Kachitidwe kake ka nkhanza kwa akapolo kanapangitsa iye kukhala “mudzi wa mwazi.” Mofanana ndi phanga la mikango, mzinda wolimbitsidwa mwamphamvu umenewu unawoneka kukhala wachisungiko kumbuyo kwa malinga ake ochindikala. Koma mwa lamulo la Mulungu, Nineve akavutika ndi tsoka lofananalo limene anapereka kwa No-amoni wakale, kapena Tebetsi, pa Mtsinje wa Nile. Chifukwa cha machimo ake, likulu la Asuri likakhalitsidwa bwinja. Ulosi umenewu unakwaniritsidwa pamene magulu ankhondo osanganizana a mfumu Yachibabulo Nabopolassar ndi Cyaxares Mmedi analanda Nineve mu 632 B.C.E.—2:3–3:19.
Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Habakuku 1:1-3:19
HABAKUKU anaphunzira kuti Yehova m’nthaŵi Yake yoyenera akachitapo kanthu motsutsana ndi opondereza ankhanza. Koma ‘mwa chikhulupiriko chake wolungama adzakhalabe.’ (2:4) Komabe, ndi maphunziro owonjezereka otani omwe tingaphunzire kuchokera ku ulosi umenewu?
Chipulumutso kwa Awo Okhala ndi Chikhulupiriro
Yehova amamvetsera ku madandaulo a atumiki ake. Habakuku akufunsa kuti: “Yehova, ndidzafuula mpaka liti osamva inu?” Inde, palibe chilungamo, ndipo oipa azungulira olungama. Koma Mulungu amamva, ndipo monga gulu lake lopereka chilango, iye “awukitsa Akasidi.” Komabe, ndimotani mmene angagwiritsire ntchito mphamvu yonga nkhondo? Mneneriyo akuyembekezera yankho la Mulungu, akumadikira chidzudzulo.—1:1–2:1.
Kokha olungama ndi okhulupirika adzakhalabe ndi moyo. Yehova akutsimikizira Habakuku za ichi. Ngakhale kuti pangawoneke kukhala kuchedwa, pa nthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu masomphenya aulosi “afika ndithu, osazengereza.” Mdani wodzitukumulayo yemwe akulanda mitundu sadzachifikira chonulirapo chake. Ndithudi, Akasidiwo sadzapita osalangidwa.—2:2-5.
Tsoka kwa Oipa!
Pewani phindu losalungama, chiwawa, ndi kulambira mafano. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tsoka liri lotsimikizirika kaamba ka amene akuchulukitsa chimene sichiri chake, kupanga phindu loipa, kumanga mzinda mwa kukhetsa mwazi, kuchititsa ena mwachiwawa kumwa chikho cha kugonjetsedwa kochititsa manyazi, ndi kukhulupirira m’mafano opanda moyo. Mulungu adzabweretsa ntchito ya oterewa kumathedwe. Dziko lonse lapansi lidzadziŵitsidwa za ulemerero wa Yehova, kwa amene onse ayenera kuima pamaso pake m’mantha a ulemu odekha.—2:6-20.
Dikirani moleza mtima pa Yehova kaamba ka chipulumutso. M’pemphero, Habakuku akukumbukira zisonyezero zapapitapo za mphamvu ya Mulungu. Pakati pa zinthu zina, Yehova anapyola pa dziko lapansi, akuponda mitundu mu ukali. Iye anapitanso patsogolo kaamba ka chipulumutso cha anthu ake. Atazizwitsidwa, Habakuku akugamulapo “[kuyembekezera modekha, NW} tsiku la nsauko.” Mosasamala kanthu za nthaŵi zoipa zimene ziyenera kuyang’anizidwa, iye adzatumpha mwa Yehova ndi kukhala wosangalala mwa Mulungu wa chipulumutso chake.—3:1-19.
[Bokosi patsamba 24]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
o 1:4—Basana, Karimeli, ndi Lebano anali malo okongola, achonde, ndi obala zipatso. Kwa iwo kufota kukatanthauza tsoka kaamba ka awo odalira pa iwo. Ichi chimagogomezera kuwopsya kwa kutsanulidwa kwa mkwiyo wa Yehova..
o 1:10—Nineve anadzilingalira iyemwini kukhala wosaloŵerereka monga ngati minga yomangana, ndipo anali wodzala ndi chiyembekezo. Koma akalikwiridwa mosavuta monga mmene moto umadyera udzu wowuma. Mofananamo, adani a anthu amakono a Mulungu sadzaimirira molimbana ndi ziweruzo zamoto za Yehova.
o 2:6—Chifukwa cha mvula yamphamvu pa nthaŵi ya kusakazidwa kwa Nineve, Mtsinje wa Tigrisi unasefukira. Kumeneku kunadzaza chigawo cha mzinda ndi kugwetsa mbali ya linga. Chotero, chinali chopepuka kwa ogonjetsa kutenga likulu la Asuri.
o 2:11-13—Mofanana ndi zirombo zakuthengo, Asuri anawononga ndi kupha mitunduyo. Chikuwonekeranso kuti mkango unali chiphiphiritso cha mtundu. Zowumbidwa zambiri za mikango zinapezedwa m’mabwinja a Nineve.
o 3:3, 4—Mofanana ndi mkazi waganyu, Nineve ananyenga mitundu ndi zopereka zokometseredwa za ubwenzi ndi malonjezano a thandizo. Koma awo otcheredwa msampha mwamsanga anakumanizana ndi kuwawa pansi pa goli lake lopondereza, monga momwe chasonyezedwera m’nkhani ya mfumu ya Chiyuda Ahazi.—2 Mbiri 28:16, 20, 21.
[Bokosi patsamba 25]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:2-4—Chikhulupiriro cha Habakuku mwa Yehova monga Mulungu yemwe samalekerera kuipa chinamufulumiza iye kufunsa chifukwa chimene kuipa kunafalikira. Iye anali wofunitsitsa kuti malingaliro ake awongoleredwe. (2:1) Pamene timadabwa chifukwa chimene zinthu zina zimalekereredwa, chidaliro chathu m’chilungamo cha Yehova chiyenera mofananamo kutithandiza kusunga kulinganizika kwathu ndi kuyembekeza pa iye.—Salmo 42:5, 11.
○ 2:5—Ababulo anali mwamuna wokhalamo ambiri amene anagwiritsira ntchito makina ake a nkhondo kugonjetsa mitundu. Mofanana ndi Shelo ndi imfa zimene nthaŵi zonse ziri zokonzekera kaamba ka minkhole yowonjezereka, iye anakhumba kugonjetsa kwa nkhondo kowonjezereka. (Yerekezani ndi Miyambo 30:15, 16.) Monga osonkhezeredwa ndi kumwa kwamphamvu, iye anakhala wopambana ndi zilakiko. Koma nkhondo zake za kugonjetsa zinatha pamene Babulo anagwa mu 539 B.C.E.
○ 3:13—Mphamvu yopulumutsa ya Mulungu kaŵirikaŵiri inakumanizidwa ndi anthu ake osankhidwa ndi odzozedwa, mtundu wa Israyeli. (Salmo 28:8, 9) M’kupita kwa nthaŵi, unabala Mesiya, “mbewu” ya “mkazi” wakumwamba wa Mulungu. (Genesis 3:15) Yehova adzapulumutsanso ziŵalo zotsalira za “mbewuyo,” otsalira a ophunzira odzozedwa ndi mzimu a Yesu, kuchokera ku kuwukiridwa ndi Satana ndi mitundu.—Chibvumbulutso 12:17.
[Chithunzi patsamba 24]
Kupakidwa utoto kochitidwa ndi katswiri wofukula zapansi A. H. Layard kusonyeza nyumba yachifumu ya ku Asuri
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy of the Trustees of the British Museum, London