Muzikhulupirira Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo
“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu.”—MIY. 3:5.
1. N’chifukwa chiyani anthufe timafunika kulimbikitsidwa?
TONSEFE timafunika kulimbikitsidwa chifukwa timakhala ndi nkhawa, timakhumudwa komanso timazunzika. Mwina mtima umatiwawa chifukwa cha ukalamba, matenda kapena imfa ya anzathu. Ndipo ena panopa akutsutsidwa kwambiri. Kunena za chiwawa ndiye chili paliponse. Timadziwa kuti zonsezi zimangosonyezeratu kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ omwe ndi ovuta. Dzuwa likamakalowa tsiku lililonse timakhala kuti tikuyandikira kwambiri dziko latsopano. (2 Tim. 3:1) Koma vuto ndi lakuti ena takhala tikuyembekezera kwa nthawi yaitali kuti Yehova akwaniritse zimene analonjeza ndipo mwina mavuto athu akungowonjezereka. Ndiye kodi ndi ndani amene angatilimbikitse?
2, 3. (a) Kodi timadziwa zotani zokhudza Habakuku? (b) Kodi kukambirana buku la Habakuku kungatithandize bwanji?
2 Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambirane mfundo za m’buku la Habakuku. Baibulo silifotokoza kwambiri za moyo wa Habakuku koma mfundo za m’buku lake ndi zolimbikitsa kwambiri. Zikuoneka kuti dzina lake limatanthauza kuti “Kukumbatira.” Mwina dzinali limasonyeza kuti Yehova amatonthoza anthu ngati kuti akuwakumbatira, apo ayi limasonyeza kuti anthu a Mulungu amamudalira kwambiri ngati kuti amukumbatira. Polankhula ndi Yehova, Habakuku anafunsa mafunso osapita m’mbali. Yehova analola kuti mafunso a Habakuku alembedwe podziwa kuti ndi mafunso amene ifenso tingafunse.—Hab. 2:2.
3 Baibulo limangofotokoza zimene Habakuku anakambirana ndi Yehova. Buku la Habakuku ndi mbali ya zinthu zimene zinalembedwa kalekale n’kusungidwa m’Mawu a Mulungu omwe “amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.” (Aroma 15:4) Kodi mfundo za m’buku la Habakuku zingatithandize bwanji? Zingatithandize kudziwa mmene tingasonyezere kuti timakhulupirira Yehova. Bukuli limatithandizanso kudziwa kuti n’zotheka kuti mtima wathu uzikhala m’malo tikakumana ndi mavuto kapena tikamazunzidwa. Ndiye tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane mfundo za m’buku la Habakuku.
TIZIPEMPHERA KWA YEHOVA
4. N’chifukwa chiyani Habakuku ankavutika maganizo?
4 Werengani Habakuku 1:2, 3. Habakuku anakhala moyo pa nthawi yovuta kwambiri. Iye anakhumudwa chifukwa anthu ambiri anali oipa komanso ankhanza. Ndiye Habakuku ankati akaona kupanda chilungamo komanso kuzunzana kwa anthu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi zoipazi zidzatha liti? N’chifukwa chiyani Yehova watenga nthawi yaitali asanathetse zoipa?’ Habakuku atasowa mtengo wogwira anapemphera kwa Yehova kuti athandizepo. Mwina iye anafika poganiza kuti Yehova sankamvera chisoni anthu amene akuvutikawo chifukwa zinaoneka ngati akuchedwa kuwathandiza. Muyenera kuti mukumvetsa mmene Habakuku ankamvera mumtima mwake.
5. Tchulani mfundo yaikulu imene tikuiphunzira m’buku la Habakuku. (Onani chithunzi choyambirira.)
5 Koma kodi Habakuku anasiya kukhulupirira Mulungu? Kodi anayamba kuganiza kuti malonjezo a Mulungu sangakwaniritsidwe? Ayi. Umboni wake ndi wakuti anafotokozera Mulungu zimene zinkamudetsa nkhawa osati anthu. Zikuoneka kuti chimene chinkamudetsa nkhawa ndi nthawi imene inadutsa Mulungu asanathandize anthu kapena chifukwa chimene Mulunguyo analolera kuti iye avutike choncho. Popeza Yehova analola Habakuku kuti alembe maganizo akewa, kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti tisamaope kumufotokozera zimene zikutidetsa nkhawa kapena kutikayikitsa. Yehova amatilimbikitsa kuti tizipemphera kwa iye n’kumamukhuthulira zamumtima mwathu. (Sal. 50:15; 62:8) Lemba la Miyambo 3:5 limatilimbikitsa kuti tiyenera ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse ndipo tisamadalire luso lathu lomvetsa zinthu.’ Habakuku ayenera kuti ankawadziwa malangizo amenewa ndipo ankawatsatira.
6. Kodi kupemphera n’kofunika bwanji?
6 Habakuku ankayesetsa kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ankamuona kuti ndi Mnzake wapamtima komanso Atate wake. Iye sankaona kuti alibiretu mtengo wogwira ndipo anapewa kudalira luso lake lomvetsa zinthu. M’malomwake anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yopemphera n’kumafotokozera Yehova nkhawa zake. Ndipotu Yehova, yemwe ndi Wakumva pemphero, amatiuza kuti tizisonyeza kuti timamudalira popemphera kwa iye n’kumuuza zonse zimene zikutidetsa nkhawa. (Sal. 65:2) Tikamatero tidzaona Yehova akutithandiza ngati kuti watikumbatira n’kumatitsogolera mokoma mtima. (Sal. 73:23, 24) Iye adzatithandiza kuzindikira maganizo ake pa chilichonse chimene chikutisautsa mtima. Ndipotu munthu akamapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima m’pamene amasonyeza kuti amamudalira kwambiri.
TIZIMVETSERA MAWU A YEHOVA
7. Kodi Yehova anatani atamva madandaulo a Habakuku?
7 Werengani Habakuku 1:5-7. Habakuku atafotokozera Yehova nkhawa zake, ayenera kuti ankayembekezera kuti aone mmene Yehova angamuyankhire. Popeza Yehova ndi wachifundo komanso womvetsa zinthu, sanakalipire Habakuku chifukwa chomudandaulira. Iye ankadziwa kuti mneneri wakeyo wachita zimenezo chifukwa chopanikizika ndi mavuto. Choncho anamuuza mawu opita kwa Ayuda osamvera ofotokoza zimene zichitike pasanapite nthawi yaitali. N’kutheka kuti Habakuku anali woyamba kuuzidwa ndi Yehova kuti mapeto a zinthu zoipazo ali pafupi kwambiri.
8. N’chifukwa chiyani Habakuku anadabwa ndi yankho la Yehova?
8 Yehova anasonyeza Habakuku kuti anali wokonzeka kuthetsa zoipazo. Anali atangotsala pang’ono kulanga anthu oipa komanso ankhanzawo. Ponena kuti “m’masiku anu” Yehova ankatanthauza kuti apereka chiweruzocho Habakukuyo kapena Aisiraeli anzake a pa nthawiyo ali moyo. Zimene Yehova ananenazi si zimene Habakuku ankayembekezera. Kodi zimenezi zinayankha mafunso ake odandaula aja? Mawu amene Yehova anamuuza anasonyeza kuti Ayuda adzavutika kwambiri.a Akasidi (Ababulo) anali oipa mtima komanso ankhanza kuposa anthu amtundu wa Habakuku omwe ankadziwa mfundo za Yehova. Nanga n’chifukwa chiyani Yehova anasankha kugwiritsa ntchito mtundu wosalambira Mulungu komanso wankhanzawu kuti ulange anthu ake? Kodi mukanakhala kuti ndi inuyo amene mukuuzidwa zimenezi, mukanatani?
9. Kodi Habakuku ayenera kuti ankadzifunsa mafunso ati?
9 Werengani Habakuku 1:12-14, 17. Habakuku anamvetsa zoti Yehova adzagwiritsa ntchito Ababulo polanga anthu oipa m’dziko lake, koma ankadabwabe. Koma anauzabe Yehova modzichepetsa kuti iye ndi “Thanthwe” lake. (Deut. 32:4; Yes. 26:4.) Habakuku anapitiriza kukhulupirira kuti Yehova ndi wachikondi komanso wokoma mtima. Popeza mneneriyu ankakhulupirira kwambiri Yehova, anamasuka kumudandauliranso. N’chifukwa chiyani Mulungu adzalola kuti zinthu zipitirire kuipa mu Yuda? Bwanji osangothetseratu zoipazo mwamsanga? N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonse adzalola kuti anthu azunzike kwambiri? N’chifukwa chiyani akungokhala chete pamene zoipa zikuchulukirachulukira? Iye ankaona kuti Mulungu ndi ‘woyera kwambiri moti sangaonerere zinthu zoipa’ zikuchitika.
10. N’chiyani chingachititse kuti tikhale ndi maganizo ngati amene Habakuku anali nawo?
10 Nthawi zina nafenso mumtima mwathu tikhoza kumva ngati mmene anamvera Habakuku. Timakonda kumvetsera mawu a Yehova. Timawerenga komanso kuphunzira Mawu ake mwachikhulupiriro ndipo zimenezi zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo. Zimene gulu lake limatiphunzitsa zimatithandiza kudziwa zimene walonjeza. Koma mwina tingamadzifunse kuti, “Kodi mavuto athu adzatha liti?” Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Habakuku anachita?
TIZIYEMBEKEZERA YEHOVA
11. Kodi Habakuku ankafunitsitsa kutani atamva mawu a Yehova?
11 Werengani Habakuku 2:1. Zimene Habakuku anakambirana ndi Yehova zinamuthandiza kuti mtima wake ukhale m’malo. Choncho anaona kuti azingoyembekezera popanda kukayikira kuti Yehova adzathandizapo. Sikuti maganizo amenewa anangokhala nawo kwa kanthawi kochepa. Paja iye nthawi ina ananenanso kuti: “Ndidzayembekezera mofatsa tsiku la nsautso.” (Hab. 3:16) Pali atumiki a Yehova enanso amene anali oleza mtima ngati Habakuku ndipo chitsanzo chawo chimatithandiza kuti tisasiye kuyembekezera Yehova.—Mika 7:7; Yak. 5:7, 8.
12. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Habakuku?
12 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Habakuku anachita? Choyamba, kaya mavuto atipanikize chotani, sitiyenera kusiya kupemphera kwa Yehova. Chachiwiri, tiyenera kumamvetsera zimene Yehova amatiuza kudzera m’Mawu ake komanso gulu lake. Chachitatu, tiyenera kuyembekeza Yehova moleza mtima ndipo tisamakayikire kuti adzathetsa mavuto athu pa nthawi yake. Tikamatsanzira Habakuku pa nkhani yolankhula ndi Yehova kuchokera mumtima, kumvetsera mawu ake komanso kumuyembekezera moleza mtima, maganizo athu adzakhala m’malo ndipo tidzatha kupirira mavuto athu. Chiyembekezo chathu chidzatithandiza kukhala oleza mtima ndipo izi zingachititse kuti tizikhalabe osangalala ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Chiyembekezo chathu chimatithandiza kuti tisamakayikire zoti Atate wathu wakumwamba adzathetsa mavuto athu.—Aroma 12:12.
13. Kodi lemba la Habakuku 2:3 lingatilimbikitse bwanji?
13 Werengani Habakuku 2:3. Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri ataona kuti Habakuku watsimikiza mumtima mwake kuti azimuyembekezera. Wamphamvuyonse ankadziwa kuti Habakuku wapanikizika ndi mavuto. Choncho anamutonthoza pomutsimikizira kuti mayankho a mafunso ake adzapezeka. Anamuuzanso kuti mavutowo atha pasanapite nthawi yaitali. Apa tingati Yehova anauza Habakuku kuti: “Tangoleza mtima ndipo uzindikhulupirira. Ndiyankha mafunso akowo ngakhale kuti zikuoneka ngati ndikuchedwa.” Yehova anakumbutsa Habakuku kuti iye ali ndi nthawi yoyenera kukwaniritsa malonjezo ake. Anamuuza kuti ayenera kuyembekezera kuti aone mmene Yehovayo akwaniritsire zolinga zake. Pamapeto pake, mneneriyo sadzanong’oneza bondo ngakhale pang’ono.
14. Kodi tiyenera kuchita chiyani pa nthawi imene takumana ndi mavuto?
14 Kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso kumvetsera mawu ake kumatithandiza kuti tikhale olimba mtima komanso odekha pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto. Yesu anatsindikanso ubwino wokhulupirira Yehova podziwa kuti amachita zinthu pa nthawi yake, osati kumangoganizira za “nthawi kapena nyengo” zimene Yehovayo sanaulule panopa. (Mac. 1:7) Choncho tiyeni tisataye mtima koma tiziyembekezera Yehova modzichepetsa, mwachikhulupiriro komanso moleza mtima. Tizigwiritsa ntchito nthawi imene tili nayo potumikira Yehova ndi moyo wathu wonse.—Maliko 13:35-37; Agal. 6:9.
TIKAMAKHULUPIRIRA YEHOVA TIDZAKHALA NDI MOYO KOMANSO TSOGOLO LABWINO
15, 16. (a) Kodi m’buku la Habakuku muli malonjezo otani? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa malonjezo amenewa?
15 Yehova analonjeza anthu olungama amene amamukhulupirira kuti: “Wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake. Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” (Hab. 2:4, 14) Malinga ndi lembali, anthu amene amakhulupirira Yehova n’kumamuyembekezera moleza mtima adzalandira moyo wosatha.
16 Munthu akangoona koyamba mawu a pa Habakuku 2:4 akhoza kuganiza kuti ndi chiganizo chongonena mawu wamba. Koma mtumwi Paulo anaona kuti limeneli ndi lonjezo la Yehova lofunika kwambiri moti anagwira mawu amenewa katatu. (Aroma 1:17; Agal. 3:11; Aheb. 10:38) Kaya wolungama akumane ndi mavuto otani, chikhulupiriro chake chingamuthandize kuti adzapeze moyo wosatha n’kudzaona cholinga cha Yehova chikukwaniritsidwa. Yehova amafuna kuti tiziona patali.
17. Kodi Yehova watitsimikizira mfundo ziti m’buku la Habakuku?
17 M’buku la Habakuku muli phunziro lofunika kwambiri kwa anthu amene tikukhala m’masiku otsirizafe. Yehova akutitsimikizira kuti adzapereka moyo wosatha kwa wolungama aliyense amene amasonyeza kuti amamukhulupirira. Choncho kaya tikumane ndi mavuto otani, tiyeni tizilimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova. M’buku la Habakuku, Yehova watitsimikiziranso kuti adzatithandiza komanso kutipulumutsa. Iye amangotipempha kuti tizimukhulupirira komanso kuyembekezera moleza mtima Ufumu wake. Mu Ufumuwo, padziko lonse padzakhala atumiki ake ofatsa komanso osangalala okhaokha.—Mat. 5:5; Aheb. 10:36-39.
TIZIKHULUPIRIRA YEHOVA MOSANGALALA
18. Kodi Habakuku anatani atamva mawu a Yehova?
18 Werengani Habakuku 3:16-19. Mawu a Yehova anathandiza kwambiri Habakuku. Habakuku anaganizira kwambiri zinthu zochititsa mantha zimene Yehova anachita poteteza anthu ake m’mbuyomo. Zimenezi zinamuthandiza kuti apitirize kumukhulupirira kwambiri. Ankadziwa kuti Yehova sachedwa kuthandizapo. Zimenezi zinamukhazika mtima m’malo ngakhale kuti ankadziwa kuti mavuto ake apitirirabe kwakanthawi. Habakuku anasiya kukayikira n’kuyamba kusangalala komanso kukhulupirira kwambiri kuti Yehova apulumutsa anthu ake. Iye analankhula mawu ochititsa chidwi kwambiri osonyeza kuti ankakhulupirira ndi mtima wonse kuti zimene ankayembekezera zidzachitika. Akatswiri ena amaganiza kuti zimene Habakuku analankhula muvesi 18 zinkatanthauza kuti: “Ndidzadumphadumpha chifukwa chosangalala ndi Ambuye. Ndidzavina mozungulirazungulira chifukwa chosangalala ndi Mulungu.” Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri kwa tonsefe. Yehova watilonjeza zinthu zabwino komanso watitsimikizira kuti sachedwa kukwaniritsa cholinga chake.
19. Kodi Yehova angatilimbikitse bwanji ngati mmene analimbikitsira Habakuku?
19 Uthenga wofunika kwambiri wa Habakuku ndi woti tizidalira kwambiri Yehova. (Hab. 2:4) Kuti tizimudalira kwambiri, tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu pochita zinthu izi: (1) Kupemphera nthawi zonse n’kumauza Yehova chilichonse chimene chikutidetsa nkhawa; (2) kutsatira malangizo alionse ochokera m’Mawu a Mulungu kapena gulu lake komanso (3) kuyembekezera Yehova moleza mtima komanso mwachikhulupiriro. Habakuku anachita zinthu zitatu zonsezi. Ngakhale kuti anayamba kulemba buku lake ndi mawu odandaula, anamaliza ndi mawu osonyeza kuti walimba mtima komanso akusangalala. Ifenso tikamachita zimenezi tidzamva ngati Yehova watikumbatira. Zimenezi zingatilimbikitse kwambiri m’dziko lamavutoli.
a Lemba la Habakuku 1:5 limati “anthu inu” posonyeza kuti tsoka limene linkabweralo linadzakhudza dziko lonse la Yuda.