MUTU 7
Tumikirani Yehova Mogwirizana ndi Mfundo Zake Zabwino Kwambiri
1. Kodi anthu a ku Yerusalemu m’nthawi ya Zefaniya ankaona bwanji mfundo za Yehova?
M’NTHAWI ya Zefaniya, anthu a ku Yerusalemu ankaganiza kuti “Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.” Iwo ankaona ngati Yehova alibe nazo ntchito zoti kaya atsatira mfundo zake kapena ayi. Zefaniya ananena kuti iwo ‘ankakhala mosatekeseka ngati vinyo amene nsenga zake zakhazikika pansi.’ Apa Zefaniya ankatanthauza kuti anthuwo ankafuna kumakhala moyo wawofuwofu, popanda kusokonezedwa ndi uthenga uliwonse woti akufunika kumatsatira mfundo za Mulungu. Komabe, Mulungu anauza Ayudawo kuti iye ‘adzafufuza ndi nyale mu Yerusalemu mosamala kwambiri, ndipo adzalanga anthu’ amene akunyalanyaza mfundo zake. Zoonadi, Yehova ali ndi mfundo zimene amafuna kuti anthu azitsatira, ndipo amakhudzidwa ndi mmene anthu ake amaonera mfundozo.—Zefaniya 1:12.
2. Kodi kumene mukukhala, anthu amaona bwanji nkhani yokhala ndi mfundo zoyenera kuzitsatira?
2 Masiku anonso anthu ambiri amadana n’zoti azitsatira mfundo zinazake. Mwina munamva ena akunena kuti, “Munthu ali ndi ufulu wochita chilichonse chimene akufuna.” Ena amaganiza kuti, ‘Ngati ndilibe ndalama kapena ngati sindingakwanitse kupeza zimene ndikufuna, palibe vuto kuchita chilichonse chimene chingandithandize kupeza zimene ndikufunazo.’ Iwo saganizira n’komwe mmene zochita zawozo zingakhudzire Mulungu, ndipo saganiziranso kuti Mulungu angafune kuti iwo achite chiyani. Kodi inuyo mumaona bwanji nkhaniyi? Kodi mumaona kuti ndi bwino kutsatira mfundo za Mlengi wathu?
3, 4. N’chifukwa chiyani mumaona kuti n’zothandiza kuti anthu akhale ndi mfundo zoti azitsatira?
3 Anthu ambiri amene safuna kutsatira mfundo za Mulungu sadandaula kutsatira mfundo zosiyanasiyana za anthu pa moyo wawo. Mwachitsanzo, ganizirani mfundo yokhala ndi madzi abwino. Maboma ambiri amakhazikitsa mfundo zothandiza kuti anthu azipeza madzi abwino. Kodi chingachitike n’chiyani ngati boma lakhazikitsa mfundo zimene zikuchititsa kuti anthu azimwa madzi oipa? Zimenezi zingayambitse matenda otsegula m’mimba kapena matenda ena, ndipo ana ndi amene angakhudzidwe kwambiri. Koma n’kutheka kuti inu mukumwa madzi abwino chifukwa chakuti boma linakhazikitsa mfundo zabwino. Bungwe lina limene limaonetsetsa kuti mayiko akugwiritsa ntchito miyezo yofanana ya zinthu, linanena kuti: “Maboma akanakhala kuti sanakhazikitse mfundo zabwino zoti anthu aziyendera, mwamsanga tikanaona zotsatira zake. Kawirikawiri sitidziwa mmene mfundo zimenezi zimathandizira kuti zinthu zizikhala zabwino kwambiri, zotetezeka, zodalirika, zothandiza komanso zotheka kuzisinthanitsa ndi zinthu zina zimene zili ndi muyezo kapena mtengo wofanana. Zonsezi zimathandiza kuti opanga zinthuzo azipeza phindu lalikulu akagulitsa zinthu zawozo.”—International Organization for Standardization.
4 Ngati mukuvomereza kuti kutsatira mfundo zinazake za anthu pa moyo wathu n’kothandiza, kodi sizomveka kuyembekezera kuti Mulungu azipereka mfundo zabwino kwa anthu odziwika ndi dzina lake?—Machitidwe 15:14.
KODI MFUNDO ZA MULUNGU N’ZOVUTA KUZITSATIRA?
5. Kudzera mwa Amosi, kodi Yehova anasonyeza bwanji kufunika kotsatira mfundo zake?
5 Munthu amene akumanga nyumba, amafunika kutsatira mfundo zimene zingathandize kuti nyumbayo ikhale yolimba. Izi zili choncho chifukwa ngati khoma limodzi lapotoka, nyumba yonse ingapendame kapena ingakhale ndi ming’alu. Zimenezi zingapangitse kuti anthu aziopa kukhalamo. Amosi, yemwe anali mneneri m’zaka za m’ma 800 B.C.E., anaona masomphenya okhudza mtundu wa mafuko 10 wa Isiraeli. Pa nthawiyo, mtunduwo unali ngati khoma kapena nyumba imeneyi. Iye anaona Yehova ataima pamwamba pa khoma, ali ndi “chingwe chowongolera m’dzanja lake.” Mulungu anauza Amosi kuti: “Ine ndiika chingwe chowongolera pakati pa anthu anga Aisiraeli, ndipo sindidzawakhululukiranso.” (Amosi 7:7, 8) Chingwe chowongolera chimenechi ankachimangirira kuchitsulo. Ndipo akafuna kuona ngati khoma lili lowongoka, ankamangirira mbali ina ya chingwecho m’mwamba mwa khoma ndipo chitsulocho chinkalendewera m’munsi mwake. Khoma lophiphiritsa lomwe Amosi anaona Yehova ataimapo, “linamangidwa pogwiritsa ntchito chingwe chowongolera” ndipo linali lowongoka kwambiri. Komabe mu nthawi ya Amosi, Aisiraeli anali atasiya kutsatira mfundo za Mulungu moti anali ngati khoma limene lapendama, lomwe linkafunika kugwetsedwa kuti lisavulaze anthu.
6. (a) Kodi mfundo yomwe yatchulidwa mobwerezabwereza m’mabuku 12 a aneneri ndi iti? (b) N’chifukwa chiyani munganene kuti mfundo za Mulungu n’zosavuta kuzitsatira?
6 Pamene mukuphunzira mabuku 12 a aneneri, muona kuti mfundo yomwe ikunenedwa mobwerezabwereza ndi yakuti, tiyenera kutsatira mfundo za Mulungu. Sikuti uthenga wonse womwe uli m’mabuku amenewa unali wodzudzula anthu amene sankatsatira mfundo zabwino za Mulungu. Nthawi zina Yehova akayang’ana Aisiraeli, omwenso anali opanda ungwiro, ankaona kuti akutsatira mfundo zake. Zimenezi ndi umboni woti mfundo zake n’zosavuta kuzitsatira ndipo nafenso tingakwanitse kuzitsatira. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani yotsatirayi.
7. Kodi Zekariya akutithandiza bwanji kuona kuti anthu opanda ungwiro angakwanitse kutsatira mfundo za Yehova?
7 Ayuda amene anabwerera kwawo kuchoka ku ukapolo, anayamba ntchito yomanganso kachisi koma atangomanga maziko ake, anasiya kaye ntchitoyo. Choncho Mulungu anatumiza aneneri ake, Hagai ndi Zekariya, n’cholinga choti akawalimbikitse kuti ayambirenso ntchitoyo. M’masomphenya ena amene Zekariya anaona, Yehova ananena kuti Zerubabele, bwanamkubwa wa ku Yuda, anali ndi “chingwe cha mmisiri womanga nyumba m’dzanja [lake],” pamene ankaika mwala womaliza pomalizitsa kumanga kachisi. Kachisiyo anamangidwa potsatira mfundo zimene Mulungu anapereka. (Zekariya 4:10) Koma taonani mfundo yochititsa chidwi yomwe inanenedwa pambuyo poti kachisi wamalizidwa. Mfundo yake ndi yakuti: “Maso 7 amenewa ndiwo maso a Yehova, ndipo akuyang’ana uku ndi uku padziko lonse lapansi.” Mulungu anaona Zerubabele akuika mwala wotsiriza wapakona pamalo pake ndipo popeza amaona chilichonse, anaona kuti kachisiyo anali atamangidwa bwino, motsatira mfundo zimene iye anapereka. Pamenepa tikuphunzira kuti n’zotheka kuti anthu azitsatira mfundo za Yehova ngakhale kuti n’zapamwamba. Zerubabele ndi anthu ake anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa choti analimbikitsidwa ndi Hagai komanso Zekariya. Mofanana ndi Zerubabele, inunso mungathe kuchita zomwe Mulungu amafuna. Ndipotu kudziwa zimenezi n’kolimbikitsa kwambiri.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUTSATIRA MFUNDO ZA YEHOVA?
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amapatsa anthu mfundo zoti azitsatira? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu anali ndi ufulu wouza Aisiraeli kuti azitsatira malamulo ake?
8 Popeza Mulungu ndi Mlengi wathu, iye ali ndi ufulu wotiuza mfundo zoti tizitsatira. (Chivumbulutso 4:11) Yehova samafunika kutiuza chilichonse chomwe tikuyenera kuchita. Iye anatipatsa chikumbumtima chomwe chimatithandiza kusankha zochita. (Aroma 2:14, 15) Mulungu anauza anthu oyamba kuti asadye “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Zipatso zimenezi zinkasonyeza kuti Mulungu ali ndi ufulu wotiuza zimene zili zabwino kapena zoipa. Inuyo mukudziwa zomwe zinachitika. (Genesis 2:17; 3:1-19) Hoseya anayerekezera machimo amene Aisiraeli anachita ndi zimene Adamu anachita. Iye analemba kuti: “[Aisiraeli], mofanana ndi munthu wochokera kufumbi, aphwanya pangano.” (Hoseya 6:7) Apa Hoseya anasonyeza kuti Aisiraeliwo anachimwa mwadala mofanana ndi Adamu.
9 Kodi tchimo limene iwo anachita linali lotani? ‘Iwo anaphwanya pangano la Chilamulo.’ Mulungu anapulumutsa Aisiraeli ku ukapolo m’dziko la Iguputo, ndipo iye anali ndi ufulu wouza anthu akewo mfundo zoti azitsatira. Ndipotu Aisiraeli anavomereza pangano limene anachita ndi Yehova. Izi zikutanthauza kuti iwo anavomerezanso kutsatira mfundo zimene Mulungu angawapatse. (Ekisodo 24:3; Yesaya 54:5) Komabe, Aisiraeli ambiri analephera kutsatira Chilamulo, ndipo anali ndi milandu yosiyanasiyana monga kukhetsa magazi, kupha anthu, ndiponso kuchita dama.—Hoseya 6:8-10.
10. Kodi Mulungu anachita chiyani pothandiza anthu amene ankalephera kutsatira mfundo zake?
10 Yehova anatumiza aneneri monga Hoseya kuti akathandize anthu akewo. Kumapeto kwa buku lake laulosi, Hoseya ananena kuti: “Ndani ali ndi nzeru kuti amvetse zinthu zimenezi? Wochenjera ndani kuti adziwe zimenezi? Pakuti njira za Yehova ndi zowongoka ndipo anthu olungama ndi amene adzayendamo, koma olakwa adzapunthwa m’njira zimenezo.” (Hoseya 14:9) Chakumayambiriro kwa Hoseya chaputala 14, mneneriyu anatsindika mfundo yoti anthu ankafunika kubwerera kwa Yehova. Ndipo anthu anzeru akanatha kuona kuti Yehova wapereka njira zowongoka zoti anthu ake ayendemo. Popeza ndinu mtumiki wodzipereka wa Yehova Mulungu, mosakayikira mukufunitsitsa kukhalabe wolungama ndi kuyendabe m’njira zake.
11. N’chifukwa chiyani mukuona kuti ndi bwino kutsatira malamulo a Mulungu?
11 Lemba la Hoseya 14:9 likutithandizanso kuona ubwino woyenda m’njira zolungama za Mulungu. Lembali likusonyeza kuti munthu akamachita zimene Mulungu akufuna, amalandira madalitso ambiri. Mulungu amatidziwa bwino chifukwa ndi Mlengi wathu ndipo zimene amafuna kuti tizichita zimakhala zothandiza ife tomwe. Kuti timvetse mmene Mulungu amationera, tiyeni tiganizire za galimoto ndi amene anapanga galimotoyo. Wopanga galimoto amadziwa mmene analumikizira zitsulo zosiyanasiyana za galimotoyo. Amadziwanso kuti pamafunika kuchotsa mafuta akale muinjini n’kuthiramo atsopano, ndipo zimenezi ziyenera kumachitika pafupipafupi. Kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu atanyalanyaza mfundo imeneyi mwina poganiza kuti galimotoyo ikuyenda popanda vuto lililonse? Posakhalitsa, injiniyo ingawonongeke kwambiri. N’chimodzimodzinso anthufe. Mlengi wathu anatipatsa malamulo oti tizitsatira, ndipo tikamawatsatira, timapindula ndi ife tomwe. (Yesaya 48:17, 18) Tikamvetsa zoti malamulo komanso mfundo za Mulungu zimathandiza ifeyo, timafunitsitsa kuzitsatira.—Salimo 112:1.
12. Kodi kuyenda m’dzina la Mulungu kumathandiza bwanji kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhale wolimba?
12 Madalitso aakulu amene timapeza tikamatsatira malamulo a Mulungu ndi akuti timakhala mabwenzi ake apamtima. Tikamatsatira mfundo za Mulungu n’kumaona kuti n’zabwino komanso zothandiza, timayamba kum’konda kwambiri. Mneneri Mika anafotokoza zimenezi momveka bwino. Iye anati: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.” (Mika 4:5) Ndithudi, kuyenda m’dzina la Yehova ndi mwayi waukulu zedi. Ndipo tikamachita zimenezi timathandizira kuyeretsa dzina la Mulungu komanso timasonyeza kuti iye ndiye woyenera kutilamulira. Zimenezi zimachititsa kuti mwachibadwa, ifenso tizisonyeza makhalidwe amene iye ali nawo. Choncho aliyense payekha, ayenera kuyesetsa kuti ubwenzi wake ndi Mulungu ukhale wolimba.—Salimo 9:10.
13. N’chifukwa chiyani kuopa dzina la Mulungu n’kosiyana ndi kuopa chinthu choopsa?
13 Anthu amene amatsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo komanso kuyenda m’dzina lake, ndiye kuti amaopa dzina la Mulungu. Mantha amene munthu woopa dzina la Mulungu amakhala nawo ndi osiyana ndi amene amakhala nawo akamaopa chinthu chinachake choopsa. Yehova anauza anthu oopa dzina lake kuti: “Koma inu amene mukuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakuwalirani ndipo m’mapiko mwake mudzakhala mphamvu yochiritsa. Inu mudzanyamuka ndi kudumphadumpha ngati ana a ng’ombe amphongo onenepa.” (Malaki 4:2) Mogwirizana ndi ulosi umenewu, Yesu Khristu ndiye “dzuwa la chilungamo.” (Chivumbulutso 1:16) Panopa iye akuwala kwambiri ndipo akuchiritsa anthu mwauzimu, koma m’tsogolo muno adzawala ndi kuchiritsa anthu onse odwala. Anthu amene akuchiritsidwa mwauzimu akusangalala kwambiri chifukwa chakuti tsopano amasuka. Iwo akusangalala ngati mwana wa ng’ombe wonenepa amene akusangalala ‘n’kumadumphadumpha.’ Mwina inunso mungavomereze kuti choonadi chakumasulani m’zinthu zambiri.—Yohane 8:32.
14, 15. Kodi mumapeza madalitso otani mukamatsatira mfundo za Yehova?
14 Madalitso ena amene timapeza tikamatsatira mfundo za Mulungu ndi oti timakhala bwino ndi anthu anzathu. Habakuku anatchula masoka asanu amene anali oti adzagwere Ayuda ochita zinthu zoipa. Iye ananena kuti masokawo adzagwera anthu osirira mwansanje, opeza phindu mwachinyengo, okhetsa magazi, ochita chiwerewere, komanso olambira mafano. (Habakuku 2:6-19) Zimenezi zikusonyezeratu kuti Yehova ali ndi mfundo zimene akufuna kuti tiziyendera pa moyo wathu. Koma onani kuti pa zinthu zoipa zimene zatchulidwazo, zinayi zikukhudza mmene timachitira zinthu ndi anthu anzathu. Choncho tikamaona anthu ngati mmene Mulungu amawaonera, sitingawachitire zoipa. Izi zikutanthauza kuti tikamachita zofuna za Mulungu tidzakhala bwino ndi anzathu.
15 Madalitso enanso amene timapeza tikamatsatira mfundo za Mulungu ndi oti banja lathu limakhala losangalala. Masiku ano anthu ambiri amaona kuti m’banja mukakhala mavuto, njira yabwino yowapewera n’kungothetsa banjalo. Koma kudzera mwa mneneri Malaki, Yehova ananena kuti: “Ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Malaki 2:16) Kutsogoloku tikambirana mwatsatanetsatane lemba la Malaki 2:16. Koma panopa tingaone palembali kuti mwanzeru, Mulungu anapereka mfundo zoti anthu onse m’banja azitsatira. Ndipo akamatsatira mfundo zimenezo, m’banja mumakhala mtendere. (Aefeso 5:28, 33; 6:1-4) N’zoona kuti tonse ndife opanda ungwiro, choncho m’banja simungalephere kukhala mavuto. Komabe, m’buku la Hoseya, Mulungu “amene amapangitsa banja lililonse, kumwamba ndi padziko lapansi, kukhala ndi dzina,” anatithandiza kumvetsa kuti n’zotheka kuthetsa mavuto ena a m’banja, ngakhale aakulu kwambiri. Tikambirananso zimenezi m’mutu wina kutsogoloku. (Aefeso 3:15) Tsopano tiyeni tione zinthu zina zimene tikuyenera kuchita potsatira mfundo za Mulungu.
“DANANI NDI CHOIPA NDIPO MUZIKONDA CHABWINO”
16. Kodi lemba la Amosi 5:15 likutiuza chiyani chokhudza mfundo za Mulungu?
16 Munthu woyambirira, Adamu, anasankha mopanda nzeru pa nkhani yoti aziyendera mfundo za ndani zokhudza chabwino kapena choipa. Kodi ifeyo timasankha mwanzeru? Amosi akutilimbikitsa kuti tiganizire mozama pa nkhani imeneyi. Iye anati: “Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.” (Amosi 5:15) Poikira ndemanga pa vesili, William Rainey Harper, yemwe anali pulofesa wa kuyunivesite ya Chicago, wophunzitsa zinenero komanso mabuku a ku Middle East, analemba kuti: “Zimene Amosi ankaona kuti n’zabwino kapena zoipa n’zogwirizana ndi chifuniro cha Yahweh.” Imeneyi ndi mfundo yaikulu imene tikuphunzira m’mabuku onse a aneneri 12. Kodi ndife okonzeka kutsatira mfundo za Yehova pa nkhani yokhudza chabwino ndi choipa? Tingapeze mfundo zimenezi m’Baibulo ndipo zafotokozedwa momveka bwino ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” yemwe ndi gulu la Akhristu odzozedwa, odziwa bwino Malemba.—Mateyu 24:45-47.
17, 18. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kudana ndi zoipa? (b) Perekani chitsanzo cha mmene tingasonyezere kuti timadana kwambiri ndi zoipa.
17 Kudana ndi zoipa kumatithandiza kupewa zinthu zosasangalatsa Mulungu. Mwachitsanzo, munthu angadziwe kuti kuonera zolaula pa Intaneti n’koipa ndipo angayesetse kuzipewa. Komabe, kodi amamva bwanji mumtima mwake akadziwa kuti pamalo enaake a pa Intaneti pamapezeka zinthu zolaula? (Aefeso 3:16) Ngati atagwiritsa ntchito malangizo opezeka pa Amosi 5:15, sizingamuvute kudana ndi zoipa, choncho angathe kupewa zinthu zosasangalatsa Mulungu.
18 Ganizirani chitsanzo china. Kodi mungayese n’komwe kugwadira mafano olimbikitsa kugonana? N’zachidziwikire kuti simungachite zimenezi. Koma Hoseya ananena kuti makolo a Aisiraeli ankachita chiwerewere polambira Baala wa ku Peori. (Numeri 25:1-3; Hoseya 9:10) Zikuoneka kuti Hoseya ananena zimenezi chifukwa chakuti tchimo lalikulu limene anthu a mu ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 ankachita, linali kulambira Baala. (2 Mafumu 17:16-18; Hoseya 2:8, 13) Aisiraeli ankachita makhalidwe onyansa kwambiri. Iwo ankagwadira mafano pamiyambo yawo yomwe anthu ankagonana mwachisawawa. Mulungu anawadzudzula kwambiri chifukwa cha zimene ankachitazi, ndipo kudziwa zimenezi kungatithandize kupewa misampha imene Satana waika pa Intaneti. Masiku ano anthu ambiri amalambira amuna ndi akazi otchuka komanso okongola amene amachita zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa anthu. Koma ifeyo amene tikudziwa machenjezo a aneneri okhudza kulambira mafano, sitichita nawo zimenezi.
MUZIKUMBUKIRA MAWU A MULUNGU
19. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Yona anachita ali m’mimba mwa chinsomba?
19 Mwina mukuyesetsa kutsatira mfundo zabwino kwambiri za Mulungu, komabe mukukumana ndi mavuto kapena mayesero. Zimenezi zingachititse kuti nthawi zina muziona ngati simungakwanitse kupirira mwinanso mungathedwe nzeru. Ndiye kodi mungatani zoterezi zikachitika? (Miyambo 24:10) Kuganizira zimene zinachitikira Yona, yemwe analinso wopanda ungwiro, kungatithandize kudziwa zomwe tingachite. Kumbukirani zimene anachita ali m’mimba mwa chinsomba. Iye anapemphera kwa Yehova ndipo mawu amene anatchula m’pemphero lake ndi ochititsa chidwi.
20. Potengera chitsanzo cha Yona, kodi mungatani kuti muzikumbukira malemba mukakumana ndi mavuto?
20 Pamene Yona ankapemphera kwa Mulungu ali m’mimba mwa chinsomba, kapena kuti “m’Manda akuya,” anagwiritsa ntchito mawu a m’masalimo omwe ankawadziwa bwino. (Yona 2:2) Pa nthawiyo n’kuti akuvutika kwambiri maganizo koma iye anapemphera kwa Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo anagwiritsa ntchito mawu amene Davide analemba. Mwachitsanzo, yerekezerani mawu amene ali pa Yona 2:3 ndi omwe ali pa Salimo 69:1, 2.a Kodi sizoonekeratu kuti pa nthawiyo Yona ankadziwa bwino masalimo a Davide amene anali nawo?Iye anakumbukira masalimo ouziridwa amenewa chifukwa ‘mumtima mwake’ munali mawu a Mulungu. (Salimo 40:8) Inuyo mukakumana ndi mavuto, kodi mungathe kukumbukira malemba alionse amene mungawagwiritse ntchito pothana ndi mavutowo? Kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama panopa, kudzakuthandizani kwambiri m’tsogolo kuti muzigwiritsa ntchito mfundo za Mulungu posankha zochita kapena pothana ndi mavuto.
MUZIOPA MULUNGU M’NJIRA YOYENERA
21. Kodi mukufunikira kuchita chiyani kuti muzitha kutsatira mfundo za Mulungu nthawi zonse?
21 Komabe pali zinanso zimene munthu ayenera kuchita kuti azitsatira mfundo za Yehova nthawi zonse kuwonjezera pa kungokumbukira Mawu a Mulungu. Mneneri Mika akutiuza chinthu chinanso chimene tiyenera kuchita kuti tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Iye anati: “Munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu.” (Mika 6:9) Munthu yemwe ali ndi nzeru zopindulitsa amatha kugwiritsa ntchito mfundo zomwe akudziwa pa moyo wake. Choncho kuti munthu akhale ndi nzeru zimenezi, ayenera kuopa dzina la Mulungu.
22, 23. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anatumiza Hagai kwa Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo? (b) N’chifukwa chiyani simuyenera kukayikira kuti mungathe kutsatira mfundo za Mulungu nthawi zonse?
22 Kodi mungatani kuti muziopa dzina la Mulungu? Ganizirani za Hagai amene anali mneneri, Ayuda atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo. M’buku lake la mavesi 38 okha, Hagai anagwiritsa ntchito dzina la Yehova m’malo okwana 35. M’chaka cha 520 B.C.E., pamene Yehova anauza Hagai kuti akhale mneneri, n’kuti patadutsa zaka 16 kuchokera pamene Ayuda anayamba kugwira ntchito yomanganso kachisi ku Yerusalemu. Komabe pofika m’chakachi n’kuti ntchitoyo itaima. Anthu a Mulungu anali atafooka chifukwa chotsutsidwa ndi adani. (Ezara 4:4, 5) Anthuwo ankaganiza kuti nthawi yoti amangenso kachisi inali isanakwane. Koma Yehova anawauza kuti: “Ganizirani mofatsa zimene mukuchita. . . . Mumange nyumbayi kuti ndisangalale nayo komanso nditamandidwe.”—Hagai 1:2-8.
23 Choncho, Bwanamkubwa Zerubabele, Mkulu wa Ansembe Yoswa komanso “anthu ena onse anayamba kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wawo. . . . Pamenepo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova.” Ndiyeno Mulungu anawalimbikitsa powatsimikizira kuti: “Ine ndili ndi inu.” Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, anthuwo anayamba kupita “kukagwira ntchito panyumba ya Yehova.” (Hagai 1:12-14) Ayudawo, omwe poyamba anagwa mphwayi, anayambanso kugwira ntchitoyo ngakhale kuti adani awo ankawatsutsa. Iwo anayamba kugwira ntchitoyo chifukwa ankafuna kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu.
24, 25. Pogwiritsa ntchito zitsanzo, fotokozani mmene mungagwiritsire ntchito mfundo zimene takambirana m’mutu uno.
24 Kodi inuyo mutazindikira mfundo za Mulungu zimene mukufunika kutsatira pa nkhani inayake, mungalimbe mtima n’kusonyeza kuti mumaopa Yehova osati anthu? Mwina ndinu mlongo wosakwatiwa amene mukugwira ntchito ndipo kuntchito kwanu kuli mwamuna wina yemwe satsatira mfundo za Mulungu zimene inuyo mumatsatira. Komabe mwamunayo ndi wokoma mtima komanso amakuchitirani zinthu zabwino. Kodi mungakumbukire lemba limene lingakukumbutseni mfundo za Yehova komanso kuopsa konyalanyaza mfundozo? Mwachitsanzo, mwina mungakumbukire lemba la Hoseya 4:11, lomwe limati: “Dama, vinyo wakale ndi vinyo wotsekemera zimawononga nzeru za munthu.” Monga munthu woopa Mulungu, lemba limeneli lingakulimbikitseni kutsatira mfundo zake ndipo mungakane ngati mwamunayo atakupemphani kuti mupite kwinakwake kokasangalala. Komanso ngati atayamba kukukopani, mungathe ‘kuthawa’ chifukwa chakuti mukuopa kukhumudwitsa Mulungu wanu wachikondi.—Genesis 39:12; Yeremiya 17:9.
25 Tsopano, ganiziraninso chitsanzo chija cha munthu amene akuyesetsa kuti apewe kuonera zinthu zolaula pa Intaneti. Mwina angakumbukire mawu a pa Salimo 119:37 omwe ndi pemphero. Lembali limati: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” Kapenanso angaganizire mawu amene Yesu ananena pa ulaliki wa paphiri akuti, “aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:28) Kuopa Yehova komanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutsatira mfundo zake kungathandize Mkhristu kupewa chilichonse chimene chingawononge makhalidwe ake. Choncho nthawi zonse mukayamba kuganiza kapena kulakalaka kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za Mulungu, yesetsani kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muziopa kwambiri Mulungu. Ndiponso muzikumbukira zimene Yehova akukuuzani kudzera mwa Hagai kuti: “Ine ndili ndi inu.”
26. Kodi tikambirana chiyani m’gawo lotsatira?
26 N’zotheka kutumikira Yehova mogwirizana ndi mfundo zake zabwino kwambiri ndipo zinthu zingatiyendere bwino. Mukapitiriza kuphunzira mabuku 12 a aneneri, mudzamvetsa bwino mfundo za Mulungu, kapena kuti zimene amafuna kuti aliyense wa ife azichita. M’gawo lotsatira la buku lino tikambirana mbali zikuluzikulu zitatu zimene Yehova amafuna kuti tizigwiritsa ntchito mfundo zake zabwino. Mbali zimenezi zikukhudza makhalidwe athu, banja lathu komanso mmene timachitira zinthu ndi anthu ena.
a Yerekezeraninso Yona 2:4-9 ndi Salimo 31:22; 30:3; 142:2, 3; 18:6; 31:6; 3:8. Masalimowa asanjidwa mogwirizana ndi mmene mfundo za palemba la Yona 2:4-9 zasanjidwira.