Kodi Adzapulumuka Ndani “Nthaŵi ya Nsautso”?
“Ali yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa.”—YOWELI 2:32.
1. Malinga ndi kunena kwa Danieli ndi Malaki, kodi nchiyani chimene chimadziŵikitsa amene akuyembekezera chipulumutso pakudza kwa “nthaŵi ya nsautso”?
POWONERATU tsiku lathu, mneneri Danieli analemba kuti: ‘Padzakhala [nthaŵi ya nsautso, NW] siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthaŵi yomwe ija; ndipo nthaŵi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene ampeza wolembedwa m’bukhu.’ (Danieli 12:1) Ngotonthoza chotani nanga mawu amenewo! Yehova adzakumbukira anthu ake ovomerezedwa, monga momwenso Malaki 3:16 akulengezera kuti: ‘Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi bukhu la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.’
2. Kodi kukumbukira dzina la Yehova kumadzetsa chiyani?
2 Kukumbukira dzina la Yehova kumapatsa chidziŵitso cholongosoka cha iye, Kristu wake, ndi zifuno zake zonse zaulemerero za Ufumu. Chifukwa chake, anthu ake amaphunzira njira yomulemekezera, kuloŵa muunansi wodzipereka kotheratu ndi iye, ndi kumkonda ‘ndi mtima wawo wonse ndi nzeru zawo zonse ndi mphamvu zawo zonse.’ (Marko 12:33; Chivumbulutso 4:11) Yehova wapanga makonzedwe achisomo, kupyolera mwa nsembe ya Yesu Kristu, kotero kuti ofatsa a padziko lapansi apeze moyo wosatha. Chotero, aŵanso amafuula mwachidaliro ndi mawu a khamu lakumwamba lomwe linatamanda Mulungu panthaŵi yakubadwa kwa Yesu, kuti: ‘Ulemerero ukhale kwa Mulungu kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.’—Luka 2:14.
3. Mtendere usanadze padziko lino lapansi, kodi nchiyani chimene Yehova adzachita?
3 Mtendere umenewo uli pafupi kwambiri koposa mmene anthu aganizira. Koma choyamba chiweruzo cha Yehova chiyenera kuperekedwa padziko loipali. Mneneri wake Zefaniya akulengeza kuti: ‘Tsiku lalikulu la Yehova liri pafupi, liri pafupi lifulumira kudza.’ Kodi tsiku limenelo nlotani? Ulosiwo ukupitiriza kuti: ‘Mawu a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo moŵaŵa mtima. Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii; tsiku la lipenga ndi la kufuulira midzi yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungondya. Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova.’—Zefaniya 1:14-17; onaninso Habakuku 2:3; 3:1-6, 16-19.
4. Kodi ndayani lerolino amene akulabadira chiitano cha kudziŵa ndi kutumikira Mulungu?
4 Mwachimwemwe, mamiliyoni ambiri lerolino akulabadira chiitano cha kudziŵa ndi kutumikira Mulungu. Ponena za Akristu odzozedwa, oloŵetsedwa m’pangano latsopano, zinaloseredwa kuti: ‘Iwo onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova.’ (Yeremiya 31:34) Ameneŵa apititsa patsogolo ntchito yamakono yakuchitira umboni. Ndipo tsopano pamene ochuluka a otsalira odzozedwa amaliza njira yawo ya moyo wapadziko lapansi, ‘khamu lalikulu’ la “nkhosa zina” ladza ‘kudzatumikira Mulungu usana ndi usiku,’ m’kakonzedwe kake konga kachisi. (Chivumbulutso 7:9, 15; Yohane 10:16) Kodi inuyo ndinu mmodzi wa amene akusangalala ndi mwaŵi umenewu wosayerekezeka?
Mmene “Zofunika za Amitundu” Zimafikira
5, 6. Mitundu yonse isanagwedezeke m’chiwonongeko, kodi ndintchito yopulumutsa yotani imene ikuchitika?
5 Tiyeni tsopano titembenukire ku Hagai 2:7, kumene Yehova akulosera za nyumba yake yauzimu yolambirira. Iye akuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.” Maulosi a Baibulo amasonyeza kuti ‘kugwedeza amitundu’ kumatanthauza kuperekedwa kwa chiweruzo cha Yehova pa amitundu. (Nahumu 1:5, 6; Chivumbulutso 6:12-17) Chotero, kachitidwe ka Yehova koloseredwa pa Hagai 2:7 kadzakwaniritsidwa pamene mitundu idzagwedezedwa—kufafanizidwa. Nanga bwanji ponena za “zofunika za amitundu onse”? Kodi zidzafunikira kuyembekezera kugwedeza komaliza kowonongako kuti zifike? Kutalitali.
6 Yoweli 2:32 amanena kuti ‘ali yense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m’phiri la Ziyoni ndi m’Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.’ Yehova amawaitana, ndipo iwo amaitanira pa dzina lake ndi chikhulupiriro m’nsembe ya Yesu kusanachitike kugwedeza komalizira kwa chisautso chachikulu. (Yerekezerani ndi Yohane 6:44; Machitidwe 2:38, 39.) Mwachimwemwe, khamu lalikulu la mtengo wapatalilo, limene tsopano lafikira chiŵerengero cha oposa mamiliyoni anayi, ‘lifika’ m’nyumba ya Yehova yolambirira likuyembekezera ‘kugwedeza [kwake] amitundu onse’ pa Armagedo.—Chivumbulutso 7:9, 10, 14.
7. Kodi nchiyani chikuphatikizidwa ‘m’kuitanira pa dzina la Yehova’?
7 Kodi opulumuka ameneŵa amaitanira motani pa dzina la Yehova? Yakobo 4:8 akutipatsa yankho, akumati: ‘Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu. Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu.’ Monga momwe achitira otsalira odzozedwa amene analambula njira, awo okhala ndi chiyembekezo cha kukhala a khamu lalikulu lopulumuka Armagedo ayenera kuchitapo kanthu motsimikizirika. Ngati muyembekezera kupulumuka, muyenera kupapira Mawu oyeretsa a Yehova ndi kugwiritsira ntchito miyezo yake yolungama m’moyo wanu. Muyenera kukhala otsimikizira kupatulira moyo wanu kwa Yehova, mukuphiphiritsira zimenezi ndi ubatizo wa m’madzi. Kuitanira kwanu pa Yehova m’chikhulupiriro kumaphatikizaponso kumchitira umboni. Motero, pa Aroma mutu 10, 9 ndi 10, Paulo akulemba kuti: ‘Ngati udzavomereza m’kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka: pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo chilungamo; ndi m’kamwa avomereza kutengapo chipulumutso.’ Ndiyeno, mu vesi 13, mtumwiyo akugwira mawu ulosi wa Yoweli, akumagogomezera kuti “amene ali yense adzaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka.”
‘Funani, Funani, Funani’
8. (a) Malinga nkunena kwa mneneri Zefaniya, kodi Yehova amafunanji kuti apereke chipulumutso? (b) Kodi ndichenjezo lotani limene liwulo “kapena” pa Zefaniya 2:3 limatipatsa?
8 Titatembenukira kubukhu la Baibulo la Zefaniya, mutu 2, 2 ndi 3, timaŵerenga zimene Yehova amafuna kaamba ka chipulumutso: ‘Lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani cifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’ Samalani ndi liwulo “kapena.” Siiri nkhani yakuti mukapulumutsidwa kamodzi, mwapulumutsidwa nthaŵi zonse. Kubisika kwathu patsikulo kumadalira pakupitirizabe kwathu kuchita zinthu zitatuzo. Tiyenera kufuna Yehova, kufuna chilungamo, ndi kufuna chifatso.
9. Kodi amene amafuna chifatso amafupidwa motani?
9 Ndithudi, mfupo ya kufunafuna chifatso ili yabwino koposa! Pa Salmo 37, mavesi 9 mpaka 11, timaŵerenga kuti: ‘Iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ Ndipo bwanji ponena za kufunafuna chilungamo? Vesi 29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Ponena za kufunafuna Yehova, mavesi 39 ndi 40 amatiuza kuti: ‘Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, iye ndiye mphamvu yawo m’nyengo ya nsautso. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa: awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira iye.’
10. Kodi ndayani omwe awonekera poyera m’kukana kwawo kufuna Yehova ndi chifatso?
10 Timagulu tampatuko ta Chikristu Chadziko talephera kufuna Yehova. Atsogoleri awo achipembedzo amanyansidwadi ndi dzina lake la mtengo wapatalilo, modzigangira akumalichotsa m’Mabaibulo omwe amatembenuza. Amafuna kulambira Ambuye kapena Mulungu wopanda dzina ndi kulemekeza Utatu wachikunja. Ndiponso, Chikristu Chadziko sichimafuna chilungamo. Ambiri a okhulupirira ake amatengera kapena kuchirikiza njira zamoyo zolekereza. Mmalo mofuna chifatso monga momwe anachitira Yesu, amanyada, mwachitsanzo pawailesi yakanema, amasonyeza moyo wawo wamwana alirenji ndipo kaŵirikaŵiri wachisembwere. Ansembe amadzilemeretsa mwakudyera masuku pamutu nkhosa zawo. Kunena m’mawu a Yakobo 5:5, iwo ‘adyerera padziko, ndipo achita zowakondweretsa.’ Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, adzapezadi kuti mawu owuziridwa otsatirawa agwira ntchito kwa iwo: ‘Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo.’—Miyambo 11:4.
11. Kodi munthu wosayeruzika ndani, ndipo ndimotani mmene wakulitsira liŵongo lake lamwazi?
11 M’zaka za zana loyamba C.E., monga momwe mtumwi Paulo akusimbira m’kalata yake yachiŵiri kwa Atesalonika, Akristu ena anasangalala mopambanitsa, nalingalira kuti tsiku la Yehova linadza panthaŵiyo. Koma Paulo anachenjeza kuti choyamba mpatuko waukulu unayenera kudza, ndi “munthu wosayeruzika” kuvumbulidwa. (2 Atesalonika 2:1-3) Tsopano, m’zaka za zana lino la 20, timazindikira ukulu wa mpatukowo ndi mmene atsogoleri achipembedzo osayeruzikawo a Chikristu Chadziko aliri pamaso pa Mulungu. M’masiku ano otsiriza kuyambira 1914, atsogoleri achipembedzo akulitsa liŵongo lawo lamwazi mwakuchirikiza ‘kusula makasu kukhala malupanga.’ (Yoweli 3:10) Ndiponso apitirizabe kuphunzitsa mabodza, onga ngati kusakhoza kufa kwachibadwa kwa moyo wa munthu, purigatoriyo, chizunzo cha moto wa helo, ubatizo wa makanda, Utatu, ndi zina zotero. Kodi adzaima pati pamene Yehova apereka chiweruzo chake? Miyambo 19:5 imati: “Wolankhula mabodza adzaonongeka.”
12. (a) Kodi “miyamba” yaumunthu ndi “dziko” zimene zidzapululutsidwa posachedwa nchiyani? (b) Kodi tikutengapo phunziro lanji pachiwonongeko chirinkudza cha dziko lino loipa?
12 Pa 2 Petro 3:10, timaŵerenga kuti: ‘Tsiku la [Yehova, NW] lidzadza ngati mbala; m’mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam’mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito ziri momwemo zidzatenthedwa.’ Maulamuliro oipa omwe aphimba anthu monga miyamba, pamodzi ndi mbali zonse zomwe zimapanga chitaganya cha anthu cha makhalidwe onyonyotsoka, adzasesedwa kuchoka padziko lapansi la Mulungu. Opanga ndi ochita malonda a zida zopululutsa, aphyuta, ochirikiza zipembedzo onyenga ndi atsogoleri awo, ochirikiza makhalidwe onyansa, chiwawa, ndi upandu—onsewo adzachoka. Adzasungunuka ndi mkwiyo wa Yehova. Koma m’mavesi 11 ndi 12, Petro awonjezera chenjezo ili kwa Akristu: ‘Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la [Yehova, NW].’
Mikayeli Amenya Nkhondo!
13, 14. Kodi Wolemekeza wamkulu wa ulamuliro wa Yehova ndani, ndipo kodi wakhala wokangalika motani chiyambire 1914?
13 Kodi ndimotani mmene aliyense adzapulumukira mkati mwa “nthaŵi ya nsautso” ya Yehova? Mtumiki wa Mulungu wopereka populumukira ndiye mkulu wa angelo Mikayeli, amene dzina lake limatanthauza “Wonga Mulungu Ndani?” Moyenerera pamenepa, Ndiye amalemekeza ulamuliro wa Yehova, kukweza Yehova monga Mulungu wowona yekha ndi Mfumu Ambuye woyenera wa chilengedwe chonse.
14 Nzochitika zochititsa nthumanzi chotani nanga zimene Chivumbulutso mutu 12, 7 mpaka 17, chikufotokoza ponena za “tsiku la Ambuye” chiyambire 1914! (Chivumbulutso 1:10) Mikayeli, mkulu wa angelo, akuponyera Satana wopandukayo kudziko lapansi kuchokera kumwamba. Pambuyo pake, monga kwafotokozedwera pa Chivumbulutso mutu 19, 11 mpaka 16, wotchedwa “Wokhulupirika ndi Wowona” ‘aponda moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.’ Wankhondo wamphamvu wakumwamba ameneyu atchedwa dzina la ‘Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye.’ Pomalizira pake, Chivumbulutso mutu 20, 1 ndi 2, chimasimba za mngelo wamkulu akuponya Satana kuphompho nambindikiritsa m’menemo zaka chikwi. Mwachiwonekere, malemba onseŵa akusonya kwa Wolemekeza mmodzi wa uchifumu wa Yehova, Ambuye Yesu Kristu, amene Yehova anamuika pampando wake wachifumu wa ulemerero wakumwamba mu 1914.
15. Kodi ndimwanjira yapadera yotani imene Mikayeli ‘adzaimirira’ posachedwa?
15 Mikayeli wakhala ‘ali chiimire,’ monga momwe amanenera Danieli 12:1, (NW), mmalo mwa anthu a Yehova kuyambira pamene anaikidwa monga Mfumu mu 1914. Koma posachedwapa Mikayeli ‘adzaimirira’ m’lingaliro lapadera kwambiri—monga Mtumiki wa Yehova wochotsa kuipa konse padziko lapansi ndipo monga Wopulumutsa chitaganya chapadziko lonse cha anthu a Mulungu. Kuwopsa kwa “nthaŵi ya nsautso” imeneyo kwasonyezedwa ndi mawu a Yesu pa Mateyu 24:21, 22: ‘Pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.’
16. Kodi ndianthu ati amene adzapulumuka chisautso chachikulu?
16 Tili achimwemwe chotani nanga kuti anthu ena adzapulumuka panthaŵi imeneyo! Ayi, osati anthu onga Ayuda opanduka amene anakodwa m’Yerusalemu mu 70 C.E., amene ena anatengedwa monga akapolo ku Roma. Mmalomwake, opulumuka “nthaŵi ya mapeto” adzafanana ndi mpingo Wachikristu umene udathaŵa kale kuchoka m’Yerusalemu pamene kumangira satsa komalizira kunayamba. Iwo adzakhala anthu akeake a Mulungu, mamiliyoni a khamu lalikulu limodzi ndi otsalira odzozedwa alionse omwe adzakhala akadali amoyo padziko lapansi. (Danieli 12:4, NW) Khamu lalikulu ‘likutuluka m’chisautso chachikulu.’ Chifukwa ninji? Chifukwa ‘atsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.’ Amasonyeza chikhulupiriro m’mphamvu yowombola ya mwazi wokhetsedwa wa Yesu ndi kusonyeza chikhulupiriro chawo mwakutumikira Mulungu mokhulupirika. Ngakhale tsopano, Yehova, ‘Wakukhala pampando wachifumu,’ amatambasulira hema wake pa iwo kuwatetezera, pamene Mwanawankhosa, Kristu Yesu, akuwaŵeta ndi kuwatsogolera ku akasupe amadzi amoyo.—Chivumbulutso 7:14, 15.
17. Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu kwenikweni likulimbikitsidwira kuchitapo kanthu kotero kuti likabisike patsiku la nsautso lirinkudzalo?
17 Pofuna Yehova, chilungamo, ndi chifatso, mamiliyoni a khamu lalikulu sayenera kulola kuti chikondi chawo choyamba cha chowonadi chizirale! Ngati ndinu mmodzi wa anthu onga nkhosa ameneŵa, kodi muyenera kuchitanji? Monga momwe kwalongosoledwera pa Akolose mutu 3, mavesi 5 mpaka 14, (NW), muyenera ‘kuvula [kotheratu] umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.’ Pofuna chithandizo cha Mulungu, yesayesani ‘kudziveka umunthu watsopano, wozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka.’ Mwachifatso, kulitsani ndi kusunga changu chotamanda Yehova ndi kudziŵitsa zifuno zake zazikulu kwa ena. Motero, mungabisike mu “nthaŵi ya nsautso,” tsiku la “mkwiyo waukali wa Yehova.”
18, 19. Kodi chipiriro chakhala chofunika motani kaamba ka chipulumutso?
18 Tsikulo layandikira! Likubwera mofulumira pa ife. Kusonkhanitsidwa kwa anthu opanga khamu lalikulu kwakhala kukuchitika tsopano kwa zaka zokwanira pafupifupi 57. Ena a ameneŵa afa ndipo akuyembekezera chiukiriro chawo. Koma ulosi wa Chivumbulutso umatipatsa chitsimikizo chakuti monga kagulu khamu lalikulu lidzatuluka m’chisautso chachikulu monga maziko a chitaganya cha “dziko latsopano.” (Chivumbulutso 21:1) Kodi inuyo mudzakhalamo? Zimenezo nzotheka, popeza kuti Yesu anati pa Mateyu 24:13: ‘Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.’
19 Zipsinjo zimene anthu a Yehova akukumana nazo m’dongosolo lakale lino zingapitirizebe kuwonjezereka. Ndipo pamene chisautso chachikulu chosautsacho chikantha, inu mungakumane ndi mavuto. Koma mamatirani kwa Yehova ndi gulu lake. Khalani ogalamuka! ‘Mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.’—Zefaniya 3:8.
20. Pamene “nthaŵi ya nsautso” yakaindeinde ikuyandikira nthaŵi zonse, kodi tiyenera kuchitanji?
20 Kuti titetezeredwe ndi kulimbikitsidwa, Yehova mwachisomo wapereka kwa anthu ake “chinenero choyera,” chomwe chimaphatikizapo uthenga waukulu wa Ufumu wake ulinkudzawo, “kuti iwo onse aitanire padzina la Yehova, kuti amtumikire mogwirizana.” (Zefaniya 3:9, NW) Pamene “nthaŵi ya nsautso” yakaindeinde ikuyandikira mofulumira, tiyeni titumikire mwachangu, kuthandiza ofatsa ‘kuitanira pa dzina la Yehova’ kuti apeze chipulumutso.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi Yehova adzachitanji asanadzetse mtendere padziko lapansi?
◻ Malinga ndi kunena kwa Yoweli, kodi munthu ayenera kuchitanji kuti apulumutsidwe?
◻ Malinga ndi kunena kwa Zefaniya, kodi ndimotani mmene ofatsa angadzapezere chitetezo ku mkwiyo waukali wa Yehova?
◻ Kodi “munthu wosayeruzika” ndani, ndipo ndimotani mmene wakulitsira liŵongo lake lamwazi?
◻ Kodi chipiriro nchofunika motani m’nkhani yachipulumutso?