CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ZEPHANIYA 1–HAGAI 2
Funafunani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike
Kuwonjezera pa kudzipereka kwa Yehova, pali zambiri zimene tiyenera kuchita kuti tidzapulumuke patsiku la mkwiyo wake. Tiyenera kumvera malangizo amene Zefaniya anapereka kwa Aisiraeli.
Bwerani kwa Yehova: Tipitirize kukonda Yehova komanso kugwirizana ndi gulu lake
Yesetsani kukhala olungama: Tizitsatira mfundo zolungama za Yehova
Yesetsani kukhala ofatsa: Tiyenera kumvera Mulungu modzichepetsa n’kumalola kuti azitilangiza
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene ndingachite kuti ndizifunafuna Yehova, ndikhale wolungama komanso kuti ndikhale wofatsa