Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi mawu akuti “kapena,” pa Zefaniya 2:3, amatanthauza kuti atumiki a Mulungu sangakhale otsimikiza zodzalandira moyo wosatha?
Lemba limeneli limati: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Kodi n’chifukwa chiyani vesili limati “kapena”?
Kuti timvetse mmene Yehova adzachitire zinthu ndi anthu ake okhulupirika pa Armagedo, ndibwino kuti tikumbutsane zimene Baibulo limaphunzitsa pankhani ya zimene Mulungu adzachitire anthu amene akufa nthawi ya chiweruzoyi isanafike. Ena mwa okhulupirikawa amaukitsidwa kupita kumwamba n’kukakhala ngati angelo, pamene ena adzaukitsidwa kudzakhala padziko lapansi ndi chiyembekezo chokhala m’Paradaiso kwa moyo wosatha. (Yohane 5:28, 29; 1 Akorinto 15:53, 54) Ngati Yehova amakumbukira ndiponso amapereka mphoto kwa anthu okhulupirika amene amafa Armagedo isanafike, ndiye kuti mosakayikira adzachitanso chimodzimodzi ndi atumiki ake amene adzakhale ndi moyo pa tsiku la mkwiyo wake.
Komanso mawu ouziridwa a mtumwi Petro n’ngolimbikitsa. Iye analemba kuti: “[Mulungu] anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula; ndipo pakuisandutsa makala midzi ya Sodoma ndi Gomora anaitsutsa, . . . ndipo anapulumutsa Loti wolungamayo . . . Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” (2 Petro 2:5-9) Ngakhale kuti Yehova anawononga anthu oipa m’mbuyomo, Iye anapulumutsa Nowa ndi Loti, amene anam’tumikira mokhulupirika. Yehova adzapulumutsanso anthu odzipereka kwa Iyeyo akamadzawononga anthu oipa pa Armagedo. “Khamu lalikulu” la anthu olungama lidzapulumuka.—Chivumbulutso 7:9, 14.
Motero zikuoneka kuti mawu akuti “kapena” sakutchulidwa pa Zefaniya 2:3 pokayikira kuti mwinamwake Mulungu angalephere kupulumutsa anthu amene amasangalala nawo. Komano akutanthauza kuti, kuti munthu alowe pamzera wodzapulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Yehova ayenera kaye kuyamba kufuna chilungamo ndiponso chifatso. Munthuyo adzapulumuka patsikuli akapitirizabe kufuna chifatso ndiponso chilungamo.—Zefaniya 2:3.
[Chithunzi patsamba 31]
“Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo”