MUTU 16
Gulu la Abale Logwirizana
KWA zaka pafupifupi 1,500, Yehova Mulungu ankachita zinthu ndi mtundu wa Isiraeli omwe anali anthu ake. Kenako, “anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Anthu odziwika ndi dzina lake amenewa ndi Mboni zake, anthu amene amaganiza komanso kuchita zinthu mogwirizana padziko lonse. Kugwirizana kwa anthu a Mulungu kumatheka chifukwa cha ntchito yolalikira imene Yesu anapatsa otsatira ake. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”—Mat. 28:19, 20.
Muli m’gulu la abale logwirizana la padziko lonse, limene sililola kuti kusiyana kwa mayiko, mitundu, chuma kapena maphunziro ziwagawanitse
2 Popeza munadzipereka kwa Yehova ndi kubatizidwa, munakhala wotsatira wa Yesu Khristu. Ndiponso muli m’gulu la abale logwirizana la padziko lonse, limene sililola kuti kusiyana kwa mayiko, mitundu, chuma kapena maphunziro ziwagawanitse. (Sal. 133:1) Zimenezi zimachititsa kuti muzikonda ndi kulemekeza abale ndi alongo anu mu mpingo omwe mwina poyamba sizikanatheka kuti mugwirizane nawo. Monga abale, timakondana kwambiri ndipo chikondi chimenechi chimaposa mgwirizano uliwonse umene anthu angakhale nawo kaya chifukwa cha banja, chikhalidwe kapena chipembedzo.—Maliko 10:29, 30; Akol. 3:14; 1 Pet. 1:22.
TIYENERA KUSINTHA KAGANIZIDWE KATHU
3 Ngati ena zikuwavuta kuthetsa tsankho pa nkhani ya mmene amaonera anthu a mitundu ina, ndale, zikhalidwe, ndi zina, angachite bwino kuganizira za Akhristu Achiyuda oyambirira omwe anafunika kusiya kusala anthu a mitundu ina. Mwachitsanzo, pamene Petulo anatumidwa kuti apite ku nyumba kwa Koneliyo, Yehova anamuthandiza mwachikondi kuti akwanitse utumiki umene anamupatsawo.—Machitidwe chap. 10.
4 M’masomphenya, Petulo anauzidwa kuti aphe ndi kudya nyama zimene Ayuda ankaziona kuti n’zodetsedwa. Iye atakana, anamva mawu ochokera kumwamba akumuuza kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa usiyiretu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.” (Mac. 10:15) Panafunika kuti Mulungu achite zimenezi pomuthandiza Petulo kuti asinthe maganizo ake chifukwa cha ntchito imene ankafuna kumupatsa yoti apite kunyumba kwa munthu yemwe sanali Myuda. Pomvera malangizo a Yehova, Petulo anauza anthu amene anasonkhana kumeneko kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti n’kosaloleka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa fuko lina kapena kumuyandikira. Koma tsopano Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti woipitsidwa kapena wonyansa. N’chifukwa chake ndabwera mosanyinyirika mutanditumizira anthu aja. Choncho ndikufuna ndidziwe chimene mwandiitanira.” (Mac. 10:28, 29) Kenako, Petulo anaona yekha umboni wakuti Yehova anavomereza Koneliyo ndi anthu a m’banja lake.
5 Saulo wa ku Tariso, yemwe anali Mfarisi wophunzira kwambiri anafunika kudzichepetsa kuti ayambe kugwirizana ndi anthu omwe kale sankagwirizana nawo. Ndiponso ankalandira malangizo amene anthuwo ankamupatsa. (Mac. 4:13; Agal. 1:13-20; Afil. 3:4-11) Tingathe kuona kuti anthu monga Serigio Paulo, Diyonisiyo, Damarisi, Filimoni, Onesimo ndi ena atalandira uthenga wabwino, anafunika kusintha kaganizidwe kawo kuti akhale ophunzira a Yesu Khristu.—Mac. 13:6-12; 17:22, 33, 34; Filim. 8-20.
KUYESETSA KUTI MGWIRIZANO WATHU USATHE
6 Mosakayikira, chikondi cha abale ndi alongo a mu mpingo wanu ndi chimene chinakuthandizani kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso kuti mukhale m’gulu lake. Munaona chizindikiro chomwe chimadziwikitsa ophunzira oona a Yesu Khristu, monga mmene iye ananenera kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:34, 35) Ndipo mumayamikira kwambiri Yehova ndi gulu lake poona kuti chikondi chimene chili pakati pa abale ndi alongo a mu mpingo wanu ndi chomwenso chikupezeka pakati pa abale athu padziko lonse. Zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo womwe umanena zokhudza kusonkhanitsa anthu m’masiku otsiriza kuti azitumikira Yehova mogwirizana komanso mwamtendere.—Mika 4:1-5.
7 Poona kuchuluka kwa zinthu zogawanitsa anthu masiku ano, ena amaona kuti n’zosatheka kugwirizanitsa anthu ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.” (Chiv. 7:9) Taganizirani kusiyana kumene kulipo pakati pa anthu ophunzira kwambiri ndi anthu wamba. Kukangana pa nkhani zachipembedzo kwapangitsanso anthu a fuko limodzi kapena m’dziko limodzi kukhala osagwirizana. Kukonda kwambiri mayiko awo, kwapangitsa anthu kukhala ogawanika pa nkhani zandale. Mukaganiziranso kusiyana kumene kulipo pa nkhani zachuma ndi nkhani zina zomwe zimagawanitsa anthu, mukhoza kuona kuti kugwirizanitsa anthu ochokera m’mayiko, m’magulu ndiponso m’zinenero zosiyanasiyana kuti azikondana kuchokera pansi pa mtima komanso kuti azikhala mwamtendere ndi chozizwitsa chachikulu chomwe sichingatheke ndi wina aliyense koma Mulungu Wamphamvuyonse yekha basi.—Zek. 4:6.
8 Mgwirizano umenewo ndi wothekadi, ndipo munthu akadzipereka ndi kubatizidwa, amakhala mmodzi wa abale ogwirizanawo. Pamene mukusangalala ndi mgwirizano umenewu, muyenera kukumbukiranso kuti muli ndi udindo wothandiza kuti mgwirizanowu usathe. Mungachite zimenezi pomvera ndi kugwiritsa ntchito mawu a mtumwi Paulo opezeka pa Agalatiya 6:10 akuti: “Ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.” Tiyeneranso kutsatira malangizo akuti: “Musachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.” (Afil. 2:3, 4) Tikamayesetsa kuona abale ndi alongo athu mmene Yehova amawaonera, tidzapitiriza kusangalala ndi mtendere komanso tidzakhala nawo pa ubwenzi wabwino.—Aef. 4:23, 24.
TIYENERA KUMADERANA NKHAWA
9 Anthu onse mu mpingo amakhala mogwirizana ndipo amasamalirana mwachikondi monga mmene mtumwi Paulo anasonyezera bwino m’fanizo lake. (1 Akor. 12:14-26) Ngakhale kuti ena a abale athu mu ubale wathu wa padziko lonse umenewu ali kutali kwambiri, timadera nkhawa za miyoyo yawo. Mwachitsanzo, abale athu akamazunzidwa, tonsefe timakhudzidwa ndipo timawamvera chisoni. Komanso ngati abale athu akusowa zinthu zofunika kapena akuvutika chifukwa cha ngozi zachilengedwe ndiponso nkhondo, tonse timayesetsa kupeza njira zowathandizira mwauzimu komanso kuwapatsa zinthu zimene akufunikira.—2 Akor. 1:8-11.
10 Tonsefe tiyenera kumapempherera abale athu tsiku lililonse. Abale ena akukumana ndi mayesero okakamizidwa kuti achite zoipa. Mavuto amene abale athu ena akukumana nawo amakhala oonekeratu, pomwe mavuto ena monga kutsutsidwa ndi anthu ogwira nawo ntchito komanso achibale, angakhale osaonekera kwa anthu ena. (Mat. 10:35, 36; 1 Ates. 2:14) Mavuto amene abale athu akukumana nawo, amatidetsa nkhawa chifukwa tili m’banja limodzi la padziko lonse. (1 Pet. 5:9) M’gululi muli ena amene amagwira ntchito mwakhama potumikira Yehova, omwe amatsogolera pa ntchito yolalikira ndi kuyang’anira mipingo. Palinso ena omwe apatsidwa udindo woyang’anira mmene ntchito yolalikira ikuyendera padziko lonse. Anthu onsewa tiyenera kumawapempherera. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timakonda ndiponso kudera nkhawa abale athu, ngakhale kuti sitingathe kuchita zambiri kuti tiwathandize.—Aef. 1:16; 1 Ates. 1:2, 3; 5:25.
11 M’masiku otsiriza ano, dziko lapansili ladzaza ndi mavuto osiyanasiyana, choncho anthu a Yehova ayenera kukhala okonzeka kuthandizana. Nthawi zina pangafunike kutumiza zinthu zambiri kuti zikathandize anthu omwe akhudzidwa ndi mavuto monga zivomerezi, kusefukira kwa madzi ndi zina. Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Pokumbukira malangizo a Yesu, ophunzira a ku Antiokeya anatumiza mosangalala mphatso ndi zinthu zina zofunika kwa abale awo a ku Yudeya. (Mac. 11:27-30; 20:35) Patapita nthawi, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti azithandiza nawo pa ntchito yothandiza abale ovutika yomwe inkagwiridwa mwadongosolo. (2 Akor. 9:1-15) Masiku anonso, abale athu akakumana ndi mavuto ndipo pakafunika kuti athandizidwe, gulu la Mulungu komanso Mkhristu aliyense payekha, amayesetsa kuthandizapo mofulumira.
YEHOVA ANATISANKHA KUTI TICHITE CHIFUNIRO CHAKE
12 Gulu lathu la abale ogwirizana padziko lonse linakhazikitsidwa kuti lizichita chifuniro cha Mulungu. Pa nthawi ino, chifuniro cha Mulungu ndi choti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lonse kuti ukhale umboni ku mitundu yonse. (Mat. 24:14) Yehova amafuna kuti tikamagwira ntchito imeneyi, tizitsatira mfundo zake za makhalidwe abwino. (1 Pet. 1:14-16) Kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ipite patsogolo, tiyenera kukhala anthu ofunitsitsa kugonjerana. (Aef. 5:21) Panopo m’pofunika kwambiri kuti tizifunafuna Ufumu wa Mulungu choyamba, m’malo mwa zofuna zathu. (Mat. 6:33) Kukumbukira zimenezi nthawi zonse pamene tikugwira ntchito yolalikira uthenga wabwino, kungatithandize kuti tizisangalala ndipo m’tsogolo tidzapeza madalitso osatha.
13 Monga Mboni za Yehova, ndife anthu apadera kwambiri. Ndife osiyana kwambiri ndi anthu ena. Mulungu anatisankha kuti tikhale oyera ndipo tizimutumikira mwakhama komanso modzipereka. (Tito 2:14) Kulambira Yehova n’komwe kumachititsa kuti tikhale osiyana ndi ena. Kuwonjezera pa mfundo yoti timagwira ntchito mogwirizana ndi abale athu padziko lonse, timalankhulanso chinenero chimodzi cha choonadi ndipo timachita zinthu mogwirizana ndi choonadicho. Zimenezi zinanenedweratu pamene Yehova kudzera mwa mneneri wake Zefaniya, ananena kuti: “Ndidzapatsa mitundu ya anthu chilankhulo choyera kuti onse aziitanira pa dzina la Yehova ndi kumutumikira mogwirizana.”—Zef. 3:9.
14 Kenako Yehova anauzira Zefaniya kuti afotokoze zokhudza ubale wa padziko lonse umene tili nawo masiku ano. Iye anati: “Otsala mwa Isiraeli sadzachita zinthu zosalungama kapena kunena bodza. Sadzakhala ndi lilime lachinyengo koma iwo adzadya ndi kugona pansi momasuka ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Zef. 3:13) Timachita zinthu mogwirizana chifukwa choti timaphunzira Mawu a Yehova omwe ndi choonadi ndipo tinasintha moyo wathu kuti tizitsatira mfundo za Yehova. N’chifukwa chake timakwanitsa kuchita zinthu zimene anthu ena amaona ngati n’zosatheka. Ndifedi anthu apadera, anthu a Mulungu amene tikumulemekeza padziko lonse.—Mika 2:12.