-
Onse Alemekeze Yehova!Nsanja ya Olonda—1997 | January 1
-
-
19. Kodi tingakhale ndi phande motani pakukwaniritsidwa kwa Hagai 2:6, 7?
19 Mwaŵi wathu wa kukhala ndi phande pakukwaniritsidwa kwamakono kwa Hagai 2:6, 7 uli wosangalatsa: “Atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthaŵi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” Umbombo, ukatangale ndi chidani nzofala kwambiri m’dziko lino la m’zaka za zana la 20. Lilidi m’masiku ake otsiriza, ndipo Yehova wayamba kale ‘kuligwedeza’ mwa kuchititsa Mboni zake ‘kulalikira tsiku lake lakubwezera.’ (Yesaya 61:2) Kugwedeza koyamba kumeneku kudzafika pachimake pachiwonongeko cha dziko lapansi pa Armagedo, koma nthaŵiyo isanafike, Yehova akusonkhanitsa “zofunika za amitundu onse”—anthu ofatsa ndipo onga nkhosa a padziko lapansi—kaamba ka utumiki wake. (Yohane 6:44) “Khamu lalikulu” limeneli tsopano ‘likutumikira’ m’mabwalo apadziko lapansi a nyumba yake yolambiriramo.—Chivumbulutso 7:9, 15.
-
-
Ulemerero Waukulu Kwambiri wa nyumba ya YehovaNsanja ya Olonda—1997 | January 1
-
-
Ulemerero Waukulu Kwambiri wa nyumba ya Yehova
“Ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” —HAGAI 2:7.
1. Kodi mzimu woyera ukugwirizana motani ndi chikhulupiriro ndi ntchito?
POLALIKIRA kunyumba ndi nyumba, mmodzi wa Mboni za Yehova anakumana ndi mkazi wa tchalitchi cha Pentecostal amene anati, ‘Ifeyo tili ndi mzimu woyera, koma inu ndinu mukugwira ntchito.’ Mwanzeru, anamfotokozera kuti munthu amene ali ndi mzimu woyera, mwachibadwa adzasonkhezeredwa kuchita ntchito ya Mulungu. Yakobo 2:17 amati: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.” Mwa thandizo la mzimu wa Yehova, Mboni zake zakulitsa chikhulupiriro cholimba, ndipo iye ‘wadzaza nyumba yake ndi ulemerero’ mwa kuzipatsa ntchito zolungama—makamaka ‘kulalikira uthenga uwu wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.’ Atachita ntchitoyi moti Yehova nkukhutira nayo, “pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
-