Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Zefaniya 1:1–3:20
Funani Yehova ndi Kumtumikira Iye ndi Mtima Wonse
ZAKA zina 50 Ababulo asanasakaze Yuda wampatuko, Yehova analengeza kupyolera mwa mneneri wake Zefaniya kuti: “Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka.” (1:1, 2) Koma Mulungu anasonyezanso anthu ake njira yopitira ku chisungiko. (2:3; 3:9) Mwanjirayi, bukhu la Zefaniya liri ndi maphunziro a phindu kaamba ka onse amene tsopano akuyang’anizana ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.”—Chibvumbulutso 16:14.
Tsiku la Yehova Liri Pafupi
Pokhala ndi tsiku la Yehova liri pafupi chotero, aliyense amene anapatuka kwa Mulungu ayenera mwamsanga kubwerera kwa iye. Pakati pa amene Mulungu “adzatha” pali awo “akubwerera osamtsata Yehova.” Iwo atembenuka ndipo samadzidetsa nkhaŵa iwo eni ndi chifuno cha Mulungu. Ndi mkhalidwe wangozi chotani nanga! Iwo uyenera kuwongoleredwa mofulumira.—Zefaniya 1:3-11.
Chuma chakuthupi sichingapereke chisungiko m’tsiku la Yehova. Ena amene amadzinenera kutumikira Yehova amadzitanganitsa iwo eni m’zotsatira zakuthupi, akumaloŵerera m’malo a ntchito abwino. Koma ndi kudzinyenga kwaumwini kotani nanga! Zinthu zawo zakuthupi sizidzapereka chisungiko mu “tsikulo.”—Zefaniya 1:12-18.
Chipulumutso Nchothekera
Kuti mubisike m’tsiku la Yehova, choposa chidziŵitso cha chisawawa cha Malemba chiri chofunika. “Ofatsa” amene “anachita chiweruzo Chake” akulangizidwa ‘kufuna Yehova, kufuna chilungamo, kufuna chifatso.’ Kokha awo amene “akulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro” ndiwo amene adzapulumutsidwa.—Zefaniya 2:1-3; Mateyu 24:13.
Mitundu imene ikupondereza anthu a Yehova lerolino idzawonongedwa. Iwo adzakhala ndi chokumana nacho chofananacho monga Moabu, Amoni, Asuri, ndi mitundu ina yozungulira Yuda. Chiwonongeko chikuyembekezeranso Babulo Wamkulu. (Chibvumbulutso 18:4-8) Ichi chimatilimbikitsa ife kupitirizabe m’kulengeza chiweruzo cha Mulungu chotani nanga!—Zefaniya 2:4-15.
Anthu Obwezeretsedwa
Yehova tsopano akukonzekeretsa anthu ake kaamba ka chipulumuko. Kodi inu mwasiya malingaliro a Chibabulo ndi kuyamba kulankhula “chinenero choyera, (NW)” cha chowonadi cha mtengo wapatali cha Baibulo? Kodi inu ‘mumaitana pa dzina la Yehova’ mwa kudzipereka inu eni kwa iye? Kodi inu ‘mukubweretsa mphatso,’ uko ndiko kuti, “chipatso cha milomo yovomereza dzina lake”? Kaamba ka chipulumuko, muyenera kutumikira “ndi mtima umodzi” ndi anthu odzipereka a Yehova.—Zefaniya 3:1-10; Aroma 10:13-15; Ahebri 13:15.
Kaamba ka chipulumutso, tiyenera kufuna Yehova ndi kukweza dzina lake loyera. Kudzikuza, chisalungamo, ndi mabodza ziribe malo pakati pa anthu ake. (Aefeso 4:25-32) Kokha “ofatsa ndi odzichepetsa” ndiwo adzapulumutsidwa pamene ayeretsa dzina lake.—Zefaniya 3:11-20.
Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Hagai 1:1–2:23
BUKHU la Hagai limatipereka ife ku 520 B.C.E., zaka 17 pambuyo pa kubwerera kwa otsalira Achiyuda ku Yerusalemu kukamanganso kachisi wa Yehova. (Hagai 1:1) Imeneyo inali nthaŵi kaamba ka aliyense kuika mtima wake pa ntchito ya Mulungu. Komabe, Yehova anachipeza kukhala chofunika kutumiza mneneri Hagai kukakumbutsa anthu Ake za thayo lawo. Kodi muli maphunziro m’chimenechi kaamba ka ife?
Ikani Ntchito ya Yehova Choyamba
Musaike nkomwe zikondwerero zakuthupi patsogolo pa ntchito zauzimu. Ayuda amene anabwerera ku dziko lakwawo anali ndi chifukwa cha kudera nkhaŵa pa kusatsimikizirika kwa ndalama, anansi a nkhalwe, ndi zina zotero. Koma zimenezi sizinali zochititsa za kunyalanyaza kwawo, m’kayang’anidwe ka mikhalidwe yawo yosangalatsa ya moyo. Kokha pambuyo pa kudzutsidwa ndi Hagai ndi pamene iwo anayamba kugwira ntchito pa kachisi. Mofananamo lerolino, ife tifunikira ‘kuika mitima yathu pa njira zathu’ ndi kukhalabe otsimikizira kuti tikuchirikiza ntchito ya Mulungu ku mlingo wokwanira wothekera.—Hagai 1:2-15.
Yehova amadalitsa zoyesayesa za awo ochita ntchito yake mwa mtima wonse. Mulungu akadalitsa ntchito ya Zerubabele ndi Ayuda ena m’kumaliza kachisi, ndipo ulemerero wake ukapambana uja wa nyumba yoyambayo. Pokhala ndi “khamu lalikulu” likuvomereza ku uthenga wa Ufumu lerolino, “zofunika za amitundu onse” zikubwera ku kachisi wauzimu wa Yehova, ndipo iye ‘wadzaza nyumba yake ndi ulemerero.’—Hagai 2:1-9; Chibvumbulutso 7:9.
Utumiki wa Mtima Wonse Ngofunika
Utumiki wathu umakhala wa phindu kokha ngati tiri audongo, zolinga zathu ziri zoyera, ndipo tikutumikira Yehova ndi mtima wonse. Kunyalanyaza nyumba ya Mulungu kunapangitsa Ayuda kukhala odetsedwa, koma iye akadalitsa iwo mwamsanga pamene ntchito ya kachisi inayamba. Chotero, ngati titi tisangalale ndi dalitso la Yehova, tiyenera kuwongolera chirichonse chofunikira chisamaliro ndi kuika mtima wathu pa ntchito yake. (Yerekezani ndi Numeri 19:11-13.) Pamene tikuyembekeza kaamba ka Mulungu kugwedeza miyamba ndi dziko lapansi, kugwetsa maufumu, lolani kuti titsatire Zerubabele wophiphiritsira, Yesu Kristu, ndi kugawanamo ndi mtima wonse mu ntchito ya Yehova.—Hagai 2:10-23.
[Bokosi patsamba 30]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
o Zefaniya 1:5—Malikamu, mothekera mofanana ndi Milikomu, Moleki, kapena Moloki, anali mulungu wonyenga wamkulu wa Aamoni. (1 Mafumu 11:5, 7) Kulambira kwa Moleki kunaphatikizapo kupereka nsembe ana konyansa ndipo kunatsutsidwa ndi Chilamulo.—Levitiko 20:2-5; Machitidwe 7:42, 43.
o Zefaniya 2:14—Monga kunanenedweratu, mizati yokwezedwa ya Nineve ndi malikulu ake zomwe zinapasulidwa zinadzakhala malo a mbalame ndi zirombo. Mbalame mwachiwonekere ndi mphepo ‘zinaimba’ mumazenera osiidwa. Poloŵera ndipo ngakhale mkati mwa nyumba yachifumu zinasakazidwa.
o Zefaniya 3:9—Chinenero chofala cha munthu sichimatsimikizira chigwirizano, monga momwe zasonyezedwera ndi nkhondo zomenyedwa pakati pa anthu a chinenero chimodzi. “Chinenero choyera” chiri chowonadi cha Malemba, “chitsanzo cha mawu a moyo.” (2 Timoteo 1:13) Chimapambana kunyada, chimalemekeza Mulungu, ndipo chimagwirizanitsa onse ochilankhula.
o Hagai 1:6—Popeza kuti Ayuda anali kunyalanyaza kachisi wa Yehova, iwo sanakhale ndi dalitso lake. Chotero, anafesa zochuluka koma anatuta mbewu zochepera ndipo anasowa chakudya ndi chakumwa chokwanira kukhutiritsa zosowa zawo. Zovala zawo zinali mu mkhalidwe ndi mu unyinji wosakwanira kuwasunga iwo ofunda, ndipo olandira ndalama anawoneka ngati kuti anali kuika ndalama zawo m’thumba lodzala zibowo. Mosiyana ndi Ayuda amenewo, lolani kuti tisanyalanyaze konse zikondwerero zaumulungu.—Miyambo 10:22; Nehemiya 10:39.
o Hagai 2:9—Pamene kuli kwakuti kachisi “woyambayo,” womangidwa ndi Solomo, anaimirira kwa zaka 420, “nyumba yotsirizira” inagwiritsiridwa ntchito kwa zaka 584 (515 B.C.E.-70 C.E.). Chotero kachisi wachiŵiri anakhala kwa nthaŵi yotalikirako. Alambiri owonjezereka anapita ku iyo, monga pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene Ayuda ndi otembenuzidwira ku Chiyuda anasonkhana kumeneko ochokera kutsidya kwa Yudeya. M’kuwonjezerako, Mesiya, Yesu Kristu, anaphunzitsa mu “nyumba yotsirizira.” Nsonga zimenezi zinaipatsa iyo ulemerero wachipembedzo wokulira.