Ayuda
Tanthauzo: Monga momwe akugwiritsidwira ntchito mofala lerolino, mawuwa akusonya kwa anthu a mbadwa Zachihebri ndi ena amene atembenuzidwira ku Chiyuda. Baibulo limasonyanso chenicheni chakuti pali Akristu amene ali Ayuda mwauzimu ndi amene amapanga “Israyeli wa Mulungu.”
Kodi Ayuda achibadwidwe lerolino ali anthu osankhidwa a Mulungu?
Chimenecho ndicho chikhulupiriro cha Ayuda ambiri. Encyclopaedia Judaica (Jerusalem, 1971, Vol. 5, danga 498) imati: “ANTHU OSANKHIKA, malongosoledwe odziŵika anthu Achiisrayeli osonyeza unansi wapadera ndi wosayerekezereka kwa mulungu wachilengedwe chonse. Lingaliro limeneli lakhala lalikulukulu m’mbiri yonse ya ganizo Lachiyuda.”—Wonani Deuteronomo 7:6-8; Eskodo 19:5.
Ochuluka m’Dziko Lachikristu ali ndi malingaliro ofanana. Chigawo cha “Chipembedzo” cha Journal and Constitution (January 22, 1983, p. 5-B) ya Atlanta inasimba kuti: “Mosiyana ndi ziphunzitso za matchalitchi za zaka mazana ambiri zakuti Mulungu ‘anatemberera anthu ake Israyeli’ ndi kuloŵedwa mmalo ndi ‘Israyeli watsopano,’ iye [Paul M. Van Buren, wophunzitsa Zaumulungu pa Yunivesite ya Temple mu Philadelphia] akunena kuti tsopano matchalitchi akutsimikizira kuti ‘pangano pakati pa Mulungu ndi anthu Achiyuda nlamuyaya. Kusintha kwa ganizo kozizwitsa kumeneku kwapangidwa ndi Aprotesitanti ndi Akatolika, kumbali zonse ziŵiri za Atlantic.’” The New York Times (February 6, 1983, p. 42) inawonjezera kuti: “‘Pali chokondweretsa ponena za kuyenera kwa uthenga wabwino ndi Israyeli ndi chikhulupiriro chakuti chirichonse chimene Aisrayeli achita chiyenera kuchirikizidwa, chifukwa chakuti Mulungu ali kumbali ya Israyeli,’ anatero Timothy Smith, profesala wa zaumulungu pa Yunivesite ya Johns Hopkins ndi mlaliki Wachiwesley.” Ena m’Dziko Lachikristu amayembekezera kutembenuzidwa ndi chipulumutso chotheratu cha Israyeli yense wachibadwidwe. Ena ali ndi lingaliro lakuti nthaŵi zonse pakhalapo mgwirizano wosalekanitsika pakati pa Mulungu ndi Israyeli, chotero amalingalira kuti ali Akunja okha amene ayenera kuyanjanitsidwa kupyolera mwa Kristu.
Talingalirani: Pambuyo pa undende wa ku Babulo, pamene Israyeli anabwezeretsedwa kudziko lawo, anthuwo anafunikira kubwezeretsa kulambira kowona m’dziko lawo lopatsidwa ndi Mulungu. Imodzi yantchito zawo zolinganizidwa zoyamba inali kumangidwanso kwa kachisi wa Yehova m’Yerusalemu. Komabe, chiyambire chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma mu 70 C.E., kachisiyo sanamangidwenso konse. Mmalo mwake, malo amene kachisi analipo kale ali ndi kachisi Wachisilamu. Ngati Ayuda, amene amanena kuti ali pansi pa Chilamulo cha Mose, akanakhala mu Yerusalemu lerolino monga anthu osankhidwa a Mulungu, kodi kachisi wopatulidwira kukulambiridwa kwake sakanamangidwanso?
Mat. 21:42, 43, NW: “Yesu anati kwa iwo [ansembe aakulu ndi akulu a Ayuda m’Yerusalemu]: ‘Kodi simunaŵerenge konse m’Malemba kuti, “Mwala umene womanga anakana ndiwo umene wakhala mwala waukulu wapangondya. Izi zachokera kwa Yehova, ndipo nzodabwitsa m’maso mwathu”? Ichi ndicho chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu ndi kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.’”
Mat. 23:37, 38: “Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafunaai! Wonani, nyumba yanu yasiyidwa yabwinja.”
Kodi pangano la Mulungu ndi Abrahamu limapereka chitsimikiziro chakuti Ayuda adzapitirizabe kukhala anthu osankhidwa a Mulungu?
Agal. 3:27-29: “Nonse amene munabatizidwa kwa Kristu mudavala Kristu. Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse pamodzi mwa Kristu Yesu. Koma ngati muli a Kristu, muli mbewu ya Abrahamu, [oloŵa nyumba] monga mwa lonjezano.” (Chotero, m’lingaliro la Mulungu, sikulinso kukhala mbadwa ya Abrahamu kumene kumatsimikizira amene ali mbewu ya Abrahamu.)
Kodi Ayuda onse adzatembenuzidwira kukukhulupirira Kristu ndi kupeza chipulumutso chamuyaya?
Aroma 11:25, 26: “Sindifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang’ono pa Israyeli, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunaloŵa; ndipo chotero [“ndimo mmene,” TEV; “motero,” CC, By; Chigiriki, houʹtos] Israyeli yense adzapulumuka.” (Tawonani kuti kupulumutsidwa kwa “Israyeli yense” kukumalizidwa, osati mwa kutembenuzidwa kwa Ayuda onse, koma mwa ‘kuloŵetsedwamo’ kwa anthu ochokera pakati pa mitundu Yachikunja. Otembenuza ena amamasulira vesi 26 kuti: “Ndiyeno pambuyo pa zimenezi Israyeli yense adzapulumutsidwa.” Koma A Manual Greek Lexicon of the New Testament [Edinburgh, 1937, G. Abbott-Smith, p. 329] ikufotokoza houʹtos kukhala lotanthauza “mwanjira imeneyi, chotero.”)
Kuti tikhale ndi chidziŵitso cholondola cha zimene zalembedwa pa Aroma 11:25, 26, tiyeneranso kupenda mawu oyambirira a mu Aroma awa: “Siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suuli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m’thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mu mtima; ndipo mdulidwe uli wamtima, mu mzimu, sim’malembo ayi.” (2:28, 29) “Onse akuchokera kwa Israyeli saali Israyeli.”—9:6.
Kodi kuli kofunika kwa Ayuda kukhulupirira Yesu Kristu kuti apulumutsidwe?
Yes. 53:1-12 adaneneratu imfa ya Mesiya ‘kunyamula machimo a ambiri ndi kutetezera olakwa.’ Danieli 9:24-27 inagwirizanitsa kudza kwa Mesiya ndi imfa yake ndi ‘kumaliza cholakwacho ndi kukhululukidwa kwa machimo.’ (JP) Malemba onse aŵiriwo amasonyeza kuti Ayuda anali ofunikira kutetezeredwa ndi kukhululukidwa kotero. Kodi iwo akayembekezera kukana Mesiya ndi kulandira chiyanjo cha Iye amene anamtuma?
Mac. 4:11, 12: “[Ponena za Yesu Kristu, mtumwi Petro anasonkhezeredwa ndi mzimu woyera kulankhula kwa olamulira Achiyuda ndi akulu m’Yerusalemu kuti:] Iye ndiye mwala woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba umene unayesedwa mutu wapangondya. Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lakumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Ngakhale kuli kwakuti mtundu wa Israyeli wakuthupi suulinso ndi chiyanjo chapadera cha Mulungu , njira njotsegukira Ayuda alionse paokha, monga momwe iriri kwa anthu amitundu yonse, kupindula ndi chipulumutso chimene chinatheketsedwa kupyolera mwa Yesu Mesiyayo.)
Kodi zochitika zimene zikuchitika m’Israyeli lerolino zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo?
Ezek. 37:21, 22: “Atero Ambuye YEHOVA: Tawonani, ndidzatenga ana a Israyeli pakati pa amitundu kumene adamkako, ndi kuwasokolotsa kumbali zonse, ndi kuloŵa nawo m’dziko mwawo; ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m’dzikomo, pamapiri a Israyeli; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse.” (Israyeli lerolino saali mtundu wolamulidwa ndi mfumu ya mzera wachifumu wa Davide. Yawoyo ndiyo lipabliki.)
Yes. 2:2-4: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga yamapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzanka, nati: ‘Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa zanjira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.’ . . . Ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Lerolino m’Yerusalemu, pamalo amene kale panali kachisi palibe “nyumba ya Mulungu wa Yakobo,” koma mmalo mwake, msikiti Wachisilamu. Ndipo palibe zimene Israyeli kapena anansi ake akuchita “kusula malupanga awo kukhala zolimira.” Kuti apulumuke akudalira pa kukhala okonzekera zankhondo.)
Yes. 35:1, 2, JP: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti see lidzasangalala, ndi kuphuka ngati duŵa. Lidzaphuka mochuluka, ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuimba; lidzapatsidwa ulemerero wa Lebano, ndi ukulu wa Karimeli ndi Saroni; anthuwo adzawona ulemerero wa AMBUYE, ukulu wa Mulungu wathu.” (Ntchito zapadera za kuwokanso nkhalango ndi zakuthirira zachitidwa mwachipambano m’Israyeli. Koma atsogoleri ake sakupereka thamo kwa Ambuye Mulungu. Monga momwe amene kale anali nduna yaikulu, David Ben-Gurion, adanenera: “Israyeli ngwotsimikiza . . . kugonjetsa chipululu chamchenga ndi kuchipangitsa kukhala chobalitsa mwa mphamvu ya sayansi ndi mzimu wa ukalambule bwalo, ndi kusanduliza dzikoli kukhala phata la demokrase.”)
Zek. 8:23, JP: “Kudzali m’masiku awo, kuti amuna khumi adzagwira, ochokera m’zinenero zonse za amitundu, adzagwiradi mkawo wa iye amene ali Myuda, akumati: Tidzamka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Kodi ulosiwu ukusonya kwa Mulungu uti? M’chinenero Chachihebri dzina lake [יהוה, limene kaŵirikaŵiri latembenuzidwa kukhala Yehova] limawonekera zoposa nthaŵi 130 m’bukhu limodzi lokha iri la Malemba Opatulika. Lerolino pamene munthu wina agwiritsira ntchito dzina limenelo, kodi anthu amanena kuti munthuyo ayenera kukhala Myuda? Ayi; kwa zaka mazana ambiri, kukhulupirira malaulo kwachititsa anthu onse Achiyuda kupeŵa kutchula kulikonse dzina laumwini la Mulungu. Kukula kwa mwadzidzidzi kwa kukondweretsedwa ndi chipembedzo lerolino kophatikizapo Israyeli wakuthupi sikumayenerana ndi malongosoledwe a ulosiwu.)
Pamenepa, kodi ndimotani, mmene zochitika mu Israyeli wamakono ziyenera kuwonedwera? Monga mbali chabe ya zochitika zapadziko lonse zonenedweratu m’Baibulo. Zimenezi zikuphatikizapo nkhondo, kusayeruzika, kuzirala kwa kukonda Mulungu, ndi kukonda ndalama.—Mat. 24:7, 12; 2 Tim. 3:1-5.
Kodi maulosi onena za kubwezeretsedwa kwa Israyeli akwaniritsidwa pakati pa ayani lerolino?
Agal. 6:15, 16, NW: “Pakuti mdulidwe suuli kanthu kusadulidwanso sikuli kanthu, koma kulengedwa kwatsopano ndiko kuli kanthu. Ndipo awo onse amene atsatira chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israyeli wa Mulungu.” (Chotero “Israyeli wa Mulungu” samatsimikiziridwanso pamaziko a kuchita mogwirizana nchofunika chotchulidwa kwa Abrahamu kaamba ka amuna onse abanja lake cha kudulidwa. Mmalo mwake, monga momwe kwafotokozedwera pa Agalatiya 3:26-29, awo amene ali a Kristu ndi ana obadwa ndi mzimu a Mulungu “alidi mbewu ya Abrahamu.”)
Yer. 31:31-34: “Tawonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; . . . ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziŵe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova.” (Pangano latsopano limenelo linapangidwa, osati ndi mtundu wa Israyeli wakuthupi, koma ndi otsatira okhulupirika a Yesu Kristu amene anapatsidwa chiyembekezo cha moyo kumwamba. Poyambitsa Chikumbutso cha imfa yake, Yesu anawapatsa chikho cha vinyo ndipo anati: “Chikho ichi ndipangano latsopano m’mwazi wanga.” [1 Akor. 11:25])
Chiv. 7:4: “Ndinamva chiŵerengero cha iwo osindikizidwa chizindikiziro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israyeli.” (Koma m’mavesi otsatira, mwatchulidwa “fuko la Levi” ndi “fuko la Yosefe.” Amenewa sanaphatikizidwe m’ndandanda zamafuko 12 a Israyeli wakuthupi. Mokondweretsa, pamene kuli kwakuti kukunenedwa kuti anthu “akasindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israyeli,” fuko la Dani ndi fuko la Efraimu silikutchulidwa. [Yerekezerani ndi Numeri 1:4-16.] Panopa otchulidwawo ayenera kukhala Israyeli wauzimu wa Mulungu, kwa awo amene Chivumbulutso 14:1-3 chimasonyeza kuti adzakhala ndi phande limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba.)
Aheb. 12:22: “Mwayandikira ku Phiri la Ziyoni, ndi mudzi wa Mulungu wa moyo, Yerusalemu wakumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo.” (Chotero sikuli ku Yerusalemu wapadziko lapansi koma ku “Yerusalemu wakumwamba” kumene Akristu owona amayang’anako kaamba ka kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu.)