Chaputala 19
“Nkhondo ya Tsiku Lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” Yoyandikirayo
1. (a) Kodi nchiyani chimene mitundu idzakakamiza Mulungu Wamphamvuyonse kulemba “m’bukhu la Nkhondo za Yehova,” ndipo kodi bukhu limenelo linali chiyani? (b) Kodi bukhu limenelo lidzamalizidwa ndi nkhondo iti?
POTSIRIZIRA PAKE mitundu yafika panthaŵi imene ikukakamiza Mulungu Wamphamvuyonse kuti alembe mapeto otsimikizirika “m’bukhu la Nkhondo za Yehova.” (Numeri 21:14) Bukhu lenileni limenelo linali cholembedwa cha nkhondo zimene Yehova adamenyera anthu ake. Mwachiwonekere, Mose analiŵerenga. Bukhulo lingakhale litayamba ndi nkhondo ya Abrahamu yachipambano imene adamenyana ndi mafumu amene adagwira Loti, imene Yehova adamenyera Abrahamu. (Genesis 14:1-16, 20) Posachedwapa, “bukhu la Nkhondo za Yehova lidzamalizidwa mwa kuwonjezera chaputala chatsopano—chochitika cha chipambano chake chachikulu koposa. Imeneyo idzakhala “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Armagedo, mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Chivumbulutso 16:14, 16) “Bukhu” lathunthu lidzasonyeza kuti Mulungu Wamphamvuyonse sanagonjetsedwepo m’nkhondo.
2, 3. (a) Chiyambire kuyambika kwa Chikristu, kodi nchiyani chimene chakhala chochitika ponena za kumenya “nkhondo” kwa Yehova? (b) Kodi nchiyani chimene chidzasonkhezera Yehova kumenyera nkhondo atumiki ake m’nthaŵi yathu?
2 Ndithudi, kuyambira chiyambi cha Chikristu kufikira tsopano, Yehova watetezera anthu ake kupyolera mwa njira zina zosakhala za nkhondo. Yehova sanamenyere nkhondo Mboni zake Zachikristu monga momwe anachitira kwa Israyeli m’Chilamulo cha Mose. Koma nthaŵi idzafika posachedwa mtsogolo muno pamene adzamenyera nkhondo atumiki ake odzipereka amakono. Kodi nchiyani chimene chidzasonkhezera nkhondo imeneyo pa Armagedo?
3 Kuulika kwa nkhondo ya Mulungu kusanachitike, Babulo Wamkulu ulamuliro wa dziko wa chipembedzo chonyenga, adzakhala atawonongedwa. Satana Mdyerekezi ndi owononga Babulo Wamkulu a ndale zadziko osakonda chipembedzo adzakwiya ndi chenicheni chakuti Mboni za Yehova zidzakhala gulu lokha lachipembedzo limene lidzakhalako. Olamulira adziko adzakhala asanafikire chonulirapo chawo cha kukhala ndi dziko losapembedza Mulungu. Chotero, tsopano, iwo adzaukira kotheratu olambira Yehova, amene wolamulira wawo wachilengedwe chonse iwo akana ndi kunyozera! Motero kwenikweni iwo adzamenyana ndi Mulungu.—Chivumbulutso 17:14, 16; yerekezerani ndi Machitidwe 5:39.
“Yehova Wamakamu” Ayambiranso Kumenya Nkhondo
4. (a) Kodi Yehova amalabadira motani chiukiro cha Gogi? (b) Kodi nchiyani chimene kulabadira kumeneko kudzatsimikizira, mogwirizana ndi dzina lakuti “Yehova wamakamu”?
4 Satana Mdyerekezi, Gogi wa ku Magogi wophiphiritsira, adzatsogolera chiukiro chimenechi pa anthu a Yehova. Pamene Gogi agwiritsira ntchito magulu ake osakhulupirira mwa Mulungu kuukira anthu a Yehova, kuŵafunkha ndi kuwawononga, Yehova adzaloŵerera ndi kumenyera nkhondo anthu ake, monga momwe kudanenedweratu pa Ezekieli 38:2, 12, 18-20. Kulabadira kwa Yehova kwanenedweratunso pa Zekariya 14:3: “Pamenepo Yehova adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja, monga anachitira nkhondo tsiku la kudumana.” Mwanjira imeneyi Mulungu wa Baibulo adzapereka umboni kumitundu yonse yamakono kuti iye akali chikhalirebe Mulungu Wankhondo, monga momwedi analiri m’masiku a Israyeli wakale, pamene, monga momwe kwalembedwera m’Malemba Opatulika Achihebri, analongosoledwa kukhala “Yehova wamakamu” nthaŵi 260.—Salmo 24:10; 84:12.
5, 6. (a) Kodi ndinkhondo iti imene tsopano ikuulika, ndipo ndani amene akutsogolera magulu ankhondo akumwamba kuloŵa m’nkhondo? (b) Kodi ncholembedwa chotani chimene mtumwi Yohane akupereka cha magulu ankhondo akumwamba oloŵa m’nkhondo?
5 Pamene “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” lifika, idzakhala nthaŵi ya “nkhondo” imene idzachitika patsiku limenelo. Yehova adzapereka chizindikiro kwa Kazembe wake Wankhondo, Yesu Kristu. M’dzina la Yehova, iye ndi magulu ankhondo akumwamba miyandamiyanda ya angelo achita nkhondo, monga ngati kuti akukwera pa akavalo ankhondo. (Yuda 14, 15) Mofanana ndi mtola nkhani wankhondo, mtumwi Yohane akutipatsiratu pasadakhale chochitika cha chilakiko chowononga chimene Kazembe Wankhondo wa Yehova adzapeza mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse”:
6 “Ndipo ndinawona mutatseguka m’mwamba; ndipo tawonani kavalo woyera ndi iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali laŵi lamoto, ndi pamutu pake pali nduŵira zachifumu zambiri . . . Ndipo magulu ankhondo okhala m’mwamba anamtsata iye, okwera pa akavalo oyera, ovala bafuta woyera woti mbuu. Ndipo mkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo: ndipo aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wamkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse. Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye.”—Chivumbulutso 19:11-16.
7. Kodi kupondedwa kwa choponderamo mphesa chophiphiritsira cha mkwiyo wa Mulungu chimaphiphiritsira chiyani kwa amitundu?
7 Kazembe wa Nkhondo mfumuyo, Yesu Kristu, akutsogolera magulu ankhondo akumwamba m’kuukira kogonjetsa motsutsana ndi adani onse pa Armagedo. Iye akusanduliza bwalo lankhondo limenelo kukhala choponderamo mphesa chachikulu! Popeza kuti Mfumu ya mafumu “aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse,” zimenezi zikutanthauza kuti mitundu idzaphwanyidwa kotheratu. Iwo adzaponyedwa mofanana ndi mphesa zakupsa mu “choponderamo mphesa” chachikulu kumene “mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse” udzawagwera nchotulukapo chowononga. Magulu ankhondo akumwamba adzagwirizana m’kuponda ‘choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.’—Chivumbulutso 14:18-20.
8. Kodi Yehova amalongosola motani maluso ake a nkhondo?
8 Mboni za Yehova padziko lapansi sizimanyamulira “lupanga” magulu ankhondo a Gogi, koma Yehova amatero. Imeneyi iri nkhondo yake! Ndipo tsopano potsirizira pake mitundu m’dziko lopita patsogolo mwa sayansi imeneyi idzamuwona akuchita nkhondo! Tamverani pamene akulongosola maluso ake ankhondo: “Ndipo ndidzamuitanira [Gogi] lupanga kumapiri anga onse, ati Ambuye Yehova, munthu aliyense lupanga lake lidzawombana nalo la mbale wake. Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulfure. Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekieli 38:21-23.
Zida Zankhondo za Mulungu Zogwiritsiridwa Ntchito pa Mdani
9. Kodi ndiziti zimene ziri zina za zida zankhondo zimene Yehova adzagwiritsira ntchito kumenyera adani ake?
9 Monga zida zomenyera nkhondo, Yehova adzagwiritsira ntchito mphamvu za chilengedwe: mvula yaliyambwe, matalala akupha, kuvumba kwa moto ndi sulfure, madzi otumphuka kuchokera pansi panthaka, ndi mphezi zogundazo. Pakugwira ntchito kwa njira ya Mulungu yophera adani ake, kuunika kudzakhala kwakukulu mopambanitsa usiku ndi usana kotero kuti dzuŵa lenileni ndi mwezi zidzawonekera kukhala zosafunikanso kuunikira. Zidzakhala ngati kuti izo zinaimirira chiriri, zosagwira ntchito monga zounikira koma kulola misisi yoyaka moto ya Yehova kutulutsa mphamvu zounikira. (Habakuku 3:10, 11) Yehova ali ndi zinthu zambiri za chilengedwe zimene angagwiritsire ntchito kumenyera nkhondo.—Yoswa 10:11; Yobu 38:22, 23, 29.
10. Mogwirizana ndi kunena kwa Zekariya 14:12, kodi nchiyaninso chimene adzagwiritsira ntchito “m’tsiku lankhondo” lirinkudzalo?
10 ‘M’tsiku la nkhondo,’ lirinkudzalo Yehova adzagwiritsiranso ntchito chawola ndi “mliri.” Mneneri Zekariya analemba za zimenezi: “Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nawo mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: Nyama yawo idzawonda akali chiriri pamapazi awo, ndi maso awo adzapuŵala m’funkha mwawo, ndi lirime lawo lidzanyala mkamwa mwawo.”—Zekariya 14:12.
11. Kodi nchiyani chimene chidzachitika pamene “mliri” ukantha ankhondo amene akuukira anthu a Yehova?
11 Mosasamala kanthu kuti “mliri” udzakhala weniweni kapena ayi, udzatontholetsa pakamwa pamene pamayasamira kulankhula zithupso zochititsa mantha! Lirime lidzavunda! Maso adzachita khungu, kotero kuti oukira akanthe kokha mwa khungu. Maso adzavunda! Minofu ya ankhondo amphamvu idzatayikiridwa ndi nyonga iwo ali chiimire ndi mapazi awo—osati ali kwala monga mitembo. Minofu yokuta mafupa awo idzavunda!—Yerekezerani ndi Habakuku 3:5.
12. Kodi “mliri” udzayambukira motani misasa ya ankhondo a mdani ndi zida zawo?
12 “Mliri” udzakantha mwadzidzidzi m’misasa yawo ya ankhondo. Magaleta awo oukira adzasokonezeka mothedwa nzeru! (Zekariya 14:15; yerekezerani ndi Eksodo 14:24, 25.) Osonyeza mmene zida zawo zankhondo zidzakhalira zopanda pake ndiwo mawu a Zekariya 14:6: “Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, sikudzakhala kuunika, zoŵalazo zidzada.” Sikudzakhala kuunika kwa kumwamba kwa chiyanjo cha Mulungu. Kuunika kodzipangira kwa sayansi yamakono sikudzachotsa mdima wa kupanda chiyanjo cha Mulungu. Zinthu zogwira ntchito zidzasokonezeka, monga ngati kuti zagwidwa ndi chisanu—zaundana.
13. Kodi nchiyani chimene chidzawonjezera mantha amene Yehova akusonkhezera pakati pa oukirawo?
13 Zonsezi ziri zochititsa mantha mokwanira! Koma chowonjezera pamantha ameneŵa chidzakhala chisokonezo chimene Mulungu adzachititsa pakati pa oukirawo. Kugwirizana kwawo pa chochita chawo chotsutsana ndi Mboni za Yehova kudzatha. Mofanana ndi ankhondo ovala zisoti zobisa mitu yawo m’chisonyezero cha Roma, iwo adzamenyana wina ndi mnzake mosawonana. Chisokonezo chakupha chidzakhala chofalikira pamene iwo akuphana wina ndi mnzake.—Zekariya 14:13.
14. (a) Kodi kuchuluka kwa ophedwa panthaŵiyo kudzakhala kotani, ndipo ndimotani mmene mbalame ndi zirombo zidzakhalira ndi phande m’kupindula ndi chilakiko cha Yehova? (b) Kodi ndimkhalidwe wotani umene opulumuka adzakhala nawo kulinga kwa “ophedwa a Yehova”?
14 Kuphedwa kwa aunyinji patsiku limenelo loposa masiku onse kudzakhala kwakukulu, chifukwa chakuti magulu ankhondo okhala kumbali ya Gogi m’nkhondo imeneyo adzakhala ambiri. (Chivumbulutso 19:19-21) Imeneyo idzakhaladi nkhondo ya padziko lonse, chifukwa chakuti palibe chigawo cha dziko lapansi chimene chidzapulumuka chiwonongeko. Kwenikweni, ophedwa pa Armagedo sadzaikidwa m’manda okhala ndi zizindikiro zoŵakumbukira. Mbalame zamitundu yonse ndi zirimbo zakuthengo zidzakhala ndi phande m’kupindula ndi chipambano cha Mulungu ndipo, panthaŵi imodzimodziyo zidzathandiza kuyeretsa dziko lapansi mwa kuchotsa mitembo yambiriyo imene idzakhala mbwee panthaka mofanana ndi ndoŵe, yosaliridwa maliro, yosaikidwa m’manda, ndi yonyansa kwa opulumukawo. (Ezekieli 39:1-5, 17-20; Chivumbulutso 19:17, 18) “Akuphedwa a Yehova” adzakhala atadzipezera mtonzo wosatha.—Yeremiya 25:32, 33; Yesaya 66:23, 24.
Dzina la Yehova Lidzalemekezedwa
15. Kodi nchochitika chapadera chotani chimene pamenepo chidzakhala chitakwaniritsidwa, ndipo ndi chiyambukiro chotani padzina la Yehova?
15 Mwanjira imeneyo, “Yehova wamakamu” kupyolera mwa Kazembe wake Wankhondo, Yesu Kristu, adzazipezera ulemerero wosafwifwa. Pamenepo chochitika chachikulu koposa m’mbiri ya chilengedwe chonse chidzakhala chitakwaniritsidwa—kulemekezedwa kwa ufumu wachilengedwe chonse wa Yehova ndi kuyeretsedwa kwa dzina lake lopatulika. (Ezekieli 38:23; 39:6, 7) Yehova adzazipangira dzina loposa chinthu chirichonse chimene chinalongosoledwa “m’bukhu la Nkhondo za Yehova” ndi m’Malemba Opatulika Achihebri a Baibulo Lopatulika. (Yerekezerani ndi Yesaya 63:12-14.) Ha ndidzina lokongola chotani nanga limene Yehova adzadzipangira mwa chilakiko chochititsa mantha mu “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse”! Pamenepo onse okonda dzina limenelo adzalitamanda mokondwera kosatha, akumaimba zitamando zake!
16. Chifukwa cha “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” yoyandikira, kodi ndipemphero lotani limene likuperekedwera “khamu lalikulu”?
16 Pamenepa, pitani patsogolo kunkhondo, Oo Yehova wamakamu, limodzi ndi Mwana wanu wachifumu Yesu Kristu pambali panu! (Salmo 110:5, 6) Zikhaletu zokondwera mboni zanu zokhulupirika padziko lapansi chifukwa cha chilakiko chanu chosayerekezeka kudzera mwa Mfumu yanu Yesu Kristu “pankhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” “Khamu lalikulu” ‘lituluketu mwachisangalalo m’chisautso chachikulu’ kukhala mboni zanu za padziko lapansi kosatha. (Chivumbulutso 7:14) M’chisamaliro chanu chachikondi, apulumuketu kuloŵa m’Kulamulira kwa Zaka Chikwi kopanda nkhondo kwa ‘Kalonga wanu wa Mtendere.’ Akhaletu umboni wowoneka kwa akufa owukitsidwa m’kulemekezedwa kwa ulamuliro umene moyenerera uli wanu m’chilengedwe chonse. Tikukuyamikani chifukwa cha kulemba chimaliziro chachikulu “m’bukhu la Nkhondo za Yehova.” Nkhani imeneyi ya kulakika kwanu kosayerekezereka ikhaletu kosatha m’cholembedwa cha m’mbiri ya zochitika za zaka zonse za mbiri yachilengedwe chonse!
[Chithunzi pamasamba 156, 157]
Yehova wamakamu adzachita nkhondo ndi mitundu