Manja Anu Alimbike
“Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mawu awa pakamwa pa aneneri.”—ZEKARIYA 8:9.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kulabadira mabuku a Hagai ndi Zekariya?
MAULOSI a Hagai ndi Zekariya analembedwa zaka pafupifupi 2,500 zapitazo, komabe maulosiwa ndi ofunika kwambiri pa moyo wanu. Nkhani za m’Baibulo zopezeka m’mabuku awiriwa si mbiri wamba. Nkhanizi ndi mbali ya ‘zonse zimene zinalembedwa kale kuti zitilangize.’ (Aroma 15:4) Zambiri mwa zinthu zimene timawerenga m’mabukuwa zimatithandiza kuganizira za zinthu zenizeni zimene zakhala zikuchitika kuchokera pamene Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914.
2 Pofotoza za zochitika ndiponso moyo wa anthu a Mulungu akale kwambiri, mtumwi Paulo anati: “Koma izi zinachitika kwa iwowa monga zotichenjeza, ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife.” (1 Akorinto 10:11) Motero, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi mabuku a Hagai ndi Zekariya ali ndi phindu lotani m’masiku athu ano?’
3. Kodi Hagai ndi Zekariya analimbikitsa za chiyani?
3 Monga momwe nkhani yapitayi yasonyezera, maulosi a Hagai ndi Zekariya anali kukhudza nthawi imene Ayuda anabwerera ku dziko limene Mulungu anawapatsa pambuyo pomasulidwa ku ukapolo wa ku Babulo. Aneneri awiriwa analimbikitsa ntchito yomanganso kachisi. Ayuda anamanga maziko a kachisiyo m’chaka cha 536 B.C.E. Ngakhale kuti Ayuda ena achikulire anaganizira zakale, kwakukulukulu panthawiyo panali ‘kufuula mokondwera.’ Komatu, chinthu china chachikulu kwambiri chachitika m’masiku athu ano. Motani?—Ezara 3:3-13.
4. Kodi nkhondo yoyamba ya padziko lonse itangotha panachitika zotani?
4 Nkhondo yoyamba ya padziko lonse itangotha, anthu odzozedwa a Yehova anamasulidwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. Izi zinali chizindikiro chachikulu choti Yehova anali kuwathandiza. Poyamba, zinaoneka ngati kuti atsogoleri a zipembedzo pamodzi ndi anzawo andale, athetsa ntchito ya Ophunzira Baibulo yolalikira ndi kuphunzitsa. (Ezara 4:8, 13, 21-24) Koma Yehova Mulungu anachotsa zopinga zimene zinali kulepheretsa ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. M’zaka zapitazi kuchokera mu 1919, ntchito ya Ufumu yapita patsogolo ndipo palibe chilichonse chimene chakwanitsa kuiimitsa.
5, 6. Kodi lemba la Zekariya 4:7 likulosera za chochitika chachikulu chiti?
5 Sitingakayikire kuti ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa imene atumiki omvera a Yehova akuchita m’nthawi yathu ino, idzapitirizabe ndi thandizo la Yehovayo. Pa Zekariya 4:7, timawerenga kuti: “Adzatulutsa mwala wa chimbudzi [kapena kuti, mwala wapamwamba wotsiriza], ndi kufuula [nawo], Chisomo, chisomo.” Kodi zimenezi zimaimira chochitika chachikulu chiti cha m’nthawi yathu ino?
6 Lemba la Zekariya 4:7 likulosera za nthawi imene kulambira Ambuye Mfumu, kumene ndiko kulambira koona, kudzafike pa kukhala kwangwiro m’mabwalo a padziko lapansi a kachisi wake wauzimu. Kachisi ameneyu ndi dongosolo limene Yehova anakonza loyandikirira kwa iye mwa kum’lambira pamaziko a nsembe yophimba machimo ya Kristu Yesu. N’zoona kuti kachisi wamkulu wauzimu ameneyu wakhalapo kuyambira m’nthawi ya Akristu oyambirira. Ngakhale zili choncho, kulambira koona m’mabwalo a padziko lapansi kudzakhala kwangwiro m’tsogolo. Olambira ambirimbiri tsopano akutumikira m’mabwalo a padziko lapansi a kachisi wauzimu ameneyu. Anthu amenewa limodzi ndi ena ambiri amene adzauke kwa akufa adzafika pokhala angwiro mu Ulamuliro wa Yesu Kristu wa Zaka 1,000. Pamapeto pa zaka 1,000 zimenezi, olambira oona a Mulungu okha ndiwo adzatsale padziko loyeretsedwa.
7. Kodi Yesu ali ndi udindo wotani pankhani yofikitsa kulambira koona paungwiro m’masiku athu ano, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi ziyenera kutilimbikitsa?
7 Bwanamkubwa Zerubabele ndi Yoswa, Mkulu wa Ansembe, anaona kachisiyo akumalizidwa mu 515 B.C.E. Lemba la Zekariya 6:12, 13 linaneneratu za udindo wa Yesu wofanana ndi wa anthu awiriwa pofikitsa kulambira koona paungwiro. Limati: “Atero Yehova wa makamu, ndi kuti, Taonani, munthu dzina lake ndilo Mphukira, ndipo adzaphuka m’malo mwake, nadzamanga Kachisi wa Yehova; inde . . . nadzasenza ulemererowo, nadzakhala ndi kulamulira pa mpando wachifumu wake; nadzakhala wansembe pampando wachifumu wake.” Popeza kuti Yesu, yemwe ali kumwamba ndipo akuchititsa mzere wa Davide wa mafumu kuphukira, ndiye akuthandizira ntchito ya Ufumu pa kachisi wauzimu, kodi mukuganiza kuti pali aliyense amene angaiimitse ntchitoyo? Palibe amene angatero. Kodi zimenezi siziyenera kutilimbikitsa kupitabe patsogolo ndi utumiki wathu, mosadodometsedwa ndi nkhawa za tsiku ndi tsiku?
Zinthu Zofunika Kwambiri
8. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsogoza ntchito ya pakachisi wauzimu m’moyo wathu?
8 Kuti Yehova atithandize ndiponso kuti tilandire madalitso ake, tiyenera kutsogoza ntchito ya pakachisi wauzimu m’moyo wathu. Mosiyana ndi Ayuda amene anati, “Nthawi siinafike,” tiyenera kukumbukira kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (Hagai 1:2; 2 Timoteo 3:1) Yesu ananeneratu kuti otsatira ake okhulupirika adzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. Tisamale kuti tisanyalanyaze mwayi wathu wa utumiki umenewu. Ntchito yolalikira ndi kuphunzitsayi yomwe inaimitsidwa kwa kanthawi ndi otsutsa a m’dzikoli inayambanso mu 1919, koma siinamalizidwe. Komatu musakayikire kuti idzamalizidwa.
9, 10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atidalitse, ndipo kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa ife?
9 Malinga ngati tipitiriza kugwira ntchitoyi mwakhama, tidzadalitsidwa, monga gulu komanso aliyense payekhapayekha. Taonani lonjezo la Yehova lomwe lingatitsimikizire zimenezi ifeyo. Ayuda atayambanso ndi mtima wonse kulambira ndi kupitiriza kugwira ntchito yomanga maziko a kachisi, Yehova anati: “Kuyambira lerolino ndidzakudalitsani.” (Hagai 2:19) Adzayambanso kuwakonda monga kale. Tsopano onani madalitso amene ali mu lonjezo la Mulungu: “Padzakhala mbewu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame awo; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chawo.”—Zekariya 8:9-13.
10 Monga momwe Yehova anadalitsira Ayuda mwauzimu ndi mwakuthupi, iye angatidalitse nafenso ngati tikhala akhama, ndiponso amtima wosangalala pogwira ntchito imene watipatsa. Madalitso amenewa akuphatikizapo kukhala amtendere pakati pathu, chitetezo, chitukuko, ndi kupita patsogolo mwauzimu. Komano musakayikire kuti Mulungu angapitirize kutidalitsa ngati tikuchita ntchito pakachisi m’njira imene Yehova akufunira.
11. Kodi tingadzipende motani?
11 Ino ndiyo nthawi yoti ‘mtima wathu usamalire njira zathu.’ (Hagai 1:5, 7) Tiyenera kuyamba takhala pansi kaye n’kuona bwinobwino kuti tikutsogoza chiyani pamoyo wathu. Madalitso a Yehova pa ifeyo lerolino akudalira khama lathu podzetsa ulemerero pa dzina lake ndi kupitirizabe ntchito yathu pa kachisi wake wauzimu. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi zinthu zimene ndimaona kukhala zofunika kwambiri kwa ine zasintha? Kodi changu changa pa Yehova, pa choonadi chake, ndiponso pa ntchito yake chikufanana ndi chomwe ndinali nacho pamene ndinkabatizidwa? Kodi maganizo ofuna kukhala ndi moyo wapamwamba akundilepheretsa kuikira mtima pa Yehova ndi Ufumu wake? Kodi kuopa anthu, kuda nkhawa ndi zimene ena angaganize, kukundibwezera m’mbuyo?’—Chivumbulutso 2:2-4.
12. Kodi lemba la Hagai 1:6, 9 likusonyeza zinthu zotani zimene zinali kuchitika pakati pa Ayuda?
12 Sitikufuna kuti Mulungu atimane madalitso ake chifukwa chonyalanyaza ntchito yodzetsa ulemerero pa dzina lake. Kumbukirani kuti pambuyo poyamba bwino, Ayuda omwe anabwerera kwawo anayamba ‘kuthamangira yense kunyumba kwake,’ ndi zimene limatiuza lemba la Hagai 1:9. Iwo anatanganitsidwa ndi kufunafuna zosowa zawo za tsiku ndi tsiku ndiponso ndi moyo wawo. Mapeto ake, ‘anatuta pang’ono,’ kunali njala ya chakudya, chakumwa, ndi kusoweka kwa zovala zofunda bwino. (Hagai 1:6) Yehova anawachotsera madalitso ake. Kodi pali zimene ifeyo tingaphunzirepo?
13, 14. Kodi tingagwiritse ntchito motani phunziro la pa Hagai 1:6, 9, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?
13 Kodi simukuvomereza kuti tiyenera kupewa kufunafuna zinthu zaumwini moti n’kulephera kulambira Yehova, ngati tikufuna kuti tipitirize kudalitsidwa ndi iye? Tikuyenera kutero kaya zochita zomwe zikutilepheretsa kum’lambirazo ndi kufunafuna chuma, kuchita nawo malonda omwe amati amalemeretsa munthu mwachangu, kuyamba maphunziro apamwamba pofuna kuti tipeze ntchito yosiririka kwambiri m’dzikoli, kapena kuyamba zinthu zina zongofuna kukhutiritsa nazo zokhumba zathu.
14 Zinthu zimenezi sizingakhale zoipa mwa izo zokha ayi. Koma kodi simukuona kuti poganizira za moyo wosatha, sitingalakwitse kunena kuti zinthu zimenezi ndi “ntchito zakufa”? (Ahebri 9:14) Motani? Mwauzimu ndi zakufa, zopanda pake, zosapindulitsa. Munthu akalimbikira ntchito zimenezi amatha kufa mwauzimu. Zinachitikapo kwa Akristu ena odzozedwa a m’nthawi ya atumwi. (Afilipi 3:17-19) Zachitikapo kwa anthu ena m’nthawi yathu ino. Mwina mukudziwapo anthu ena amene anayamba kusokonezedwa pang’onopang’ono pa ntchito zachikristu ndiponso kulekana ndi mpingo; ndipo pano sakusonyeza maganizo alionse ofuna kuyambanso kutumikira Yehova. Tikukhulupirira kuti anthu amenewa adzabwerera kwa Yehova, koma mfundo n’njakuti kulimbikira “ntchito zakufa” kumatayitsa munthu ubwenzi womwe anali nawo ndi Yehova ndiponso madalitso ake. Mungathe kuona kuti zimenezi zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri. Zingapangitse kuti munthu asakhale ndi chimwemwe ndi mtendere, zomwe ndi zipatso za mzimu wa Mulungu. Ndipo ganiziraninso za kuipa kosakhalanso ndi mwayi wopindula ndi ubale wachikondi, wachikristu.—Agalatiya 1:6; 5:7, 13, 22-24.
15. Kodi lemba la Hagai 2:14 likusonyeza motani kukula kwa nkhani ya kulambira kwathu?
15 Iyitu ndi nkhani yaikulu. Onani pa Hagai 2:14 mmene Yehova anaonera Ayuda amene ananyalanyaza nyumba yake yolambiriramo n’kumathera nthawi pa kukongoletsa nyumba zawo, m’njira yeniyeni kapena mophiphiritsa. “Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja awo; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa.” Nsembe zilizonse zachiphamaso zimene Ayuda a mitima iwiriwa anali kupereka pa guwa la nsembe logwirizira ku Yerusalemu zinali zosavomerezeka malinga ngati iwo anali kunyalanyaza kulambira koona.—Ezara 3:3.
Mulungu Walonjeza Kuti Atithandiza
16. Mogwirizana ndi masomphenya amene Zekariya analandira, kodi Ayuda anatsimikizira za chiyani?
16 Ayuda omvera amene anagwira ntchito yomanganso kachisi wa Mulungu anatsimikiziridwa kuti Mulungu adzawathandiza, malinga ndi masomphenya asanu ndi atatu amene iye anaonetsa Zekariya. Masomphenya oyamba anatsimikizira anthuwo kuti kachisi adzamalizidwa ndipo Yerusalemu ndi Yuda adzatukuka malinga ngati Ayuda amvera ndi kupitiriza kuchita ntchito imene inalipo nthawiyo. (Zekariya 1:8-17) Masomphenya achiwiri anawalonjeza kuti maboma onse amene anali kutsutsana ndi kulambira koona adzachotsedwapo. (Zekariya 1:18-21) Masomphenya ena anawatsimikizira kuti Mulungu adzateteza ntchito yomangayo, anthu a mitundu yambiri adzakhamukira ku nyumba ya Yehova yolambiriramo nyumbayo ikadzatha, mtendere weniweni ndi chitetezo, kuchotsedwa kwa zopinga zooneka ngati zosatheka kuzisuntha zimene zinali kupinga ntchito imene Mulungu anapereka, kuthetsedwa kwa khalidwe loipa, ndiponso kuti angelo adzawayang’anira ndi kuwateteza. (Zekariya 2:5, 11; 3:10; 4:7; 5:6-11; 6:1-8) Mungathe kuona chifukwa chake pambuyo potsimikiziridwa kuti Mulungu adzawathandiza, anthu omvera anasintha moyo wawo, n’kuika mtima wawo pa kukwaniritsa ntchito imene Mulungu anawamasulira ku ukapolo.
17. Malingana ndi chitsimikizo chomwe tili nacho, kodi tiyenera kudzifunsa zotani?
17 Mofananamo, chitsimikizo chomwe tili nacho chakuti kulambira koona kudzapambana chiyenera kutilimbikitsa kuchita ntchito yathu mwakhama ndiponso chiyenera kutilimbikitsa kuganiza mozama za nyumba yolambiriramo ya Yehova. Dzifunseni kuti: ‘Ngati ndimakhulupirira kuti ino ndiyo nthawi yoti tichite ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira, kodi zolinga zanga ndi moyo wanga n’zogwirizana ndi zimene ndimakhulupirirazo? Kodi ndimathera nthawi yokwanira pa kuphunzira Mawu aulosi a Mulungu, kuikirapo mtima wanga, ndi kulankhula za mawuwo ndi Akristu anzanga komanso anthu amene ndimakumana nawo?’
18. Kodi m’tsogolomu muli zotani malinga ndi chaputala 14 cha buku la Zekariya?
18 Zekariya anatchula za kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu komwe kudzatsatiridwe ndi nkhondo ya Armagedo. Timawerenga kuti: “Lidzakhala tsiku la palokha lodziwika ndi Yehova; palibe usana, palibe usiku; koma kudzatero kuti madzulo kudzati mbe.” Inde, tsiku la Yehova lidzakhaladi la mdima ndi loopsa kwa adani ake padziko lapansi. Koma idzakhala nthawi ya kuwala kosatha kwa olambira okhulupirika a Yehova. Idzakhalanso nthawi yomwe Yehova adzawakomere mtima. Zekariya anafotokozanso mmene chilichonse m’dziko latsopanolo chidzalengezere chiyero cha Yehova. Kulambira koona pa kachisi wauzimu wamkulu wa Mulungu ndi kulambira kokhako komwe kudzakhale padziko lapansi. (Zekariya 14:7, 16-19) Chimenechi chinalitu chitsimikizo chachikulu kwambiri! Tidzaona zimene analosera zikukwaniritsidwa ndipo tidzaonanso umboni wotsimikiza kuti Yehova ndiyedi woyenera kulamulira. Lidzakhaladi tsiku lapadera, tsiku lake la Yehova.
Madalitso Amuyaya
19, 20. Kodi n’chifukwa chiyani mukuona kuti lemba la Zekariya 14:8, 9 ndi lolimbikitsa?
19 Pambuyo pa chochitika chachikulu zedi chimenechi, Satana ndi ziwanda zake adzatsekeredwa m’phompho, osatha kuchita chilichonse. (Chivumbulutso 20:1-3, 7) Ndiyeno kudzakhala madalitso mu Ulamuliro wa Kristu wa Zaka 1,000. Lemba la Zekariya 14:8, 9 likuti: “Kudzachitika tsiku lomwelo kuti madzi amoyo adzatuluka ku Yerusalemu; gawo lawo lina kumka ku nyanja ya kum’mawa, ndi gawo lina kumka ku nyanja ya kumadzulo; adzatero nyengo ya dzinja ndi ya mwamvu. Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.”
20 “Madzi a moyo,” kapena kuti “mtsinje wa madzi a moyo,” umene ukuimira makonzedwe a Yehova othandiza anthu kuti akhale ndi moyo, udzayenda mosalekeza kuchokera ku likulu la Ufumu wa Mesiya. (Chivumbulutso 22:1, 2) Khamu lalikulu la olambira Yehova, amene adzapulumuke Armagedo, lidzapindula mwa kumasulidwa ku chilango cha imfa chomwe chinaperekedwa kwa Adamu. Ngakhale anthu amene anamwalira kale adzapindula mwa kuukitsidwa. Motero, padzayamba chigawo chatsopano cha ulamuliro wa Yehova wa padziko lonse lapansi. Munthu aliyense padziko lapansi adzavomereza kuti Yehova ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndipo ndiye yekha amene ayenera kulambiridwa.
21. Kodi tiyenera kuchita chiyani?
21 Malinga ndi zonse zimene Hagai ndi Zekariya analosera ndiponso zonse zimene zakwaniritsidwa, tili ndi chifukwa champhamvu chopitirizira ntchito imene Mulungu watipatsa kuti tichite m’mabwalo a padziko lapansi a kachisi wake wauzimu. Kufikira nthawi imene kulambira koona kudzafike pa kukhala kwangwiro, tiyeni tonse tipitirize kuika Ufumu patsogolo m’moyo wathu. Zekariya 8:9 akutilimbikitsa kuti: “Alimbike manja anu, inu akumva masiku ano mawu awa pakamwa pa aneneri.”
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndi zochitika ziti zimene zikupangitsa mabuku a Hagai ndi Zekariya kukhala ofunika kwambiri masiku ano?
• Kodi Hagai ndi Zekariya akutipatsa phunziro lotani pankhani ya zinthu zofunika kwambiri?
• N’chifukwa chiyani kuphunzira mabuku a Hagai ndi Zekariya kukutipatsa chifukwa chokhalira otsimikizira zam’tsogolo?
[Chithunzi patsamba 26]
Hagai ndi Zekariya analimbikitsa Ayuda kugwira ntchito ndi mtima wonse kuti alandire madalitso
[Zithunzi patsamba 27]
Kodi ‘mukuthamangira kunyumba yanu’?
[Chithunzi patsamba 28]
Yehova analonjeza madalitso ndipo waperekadi