“Kondani Choonadi ndi Mtendere”!
“Mawu a Yehova wa makamu anadza kwa ine, ndi kuti, . . . Kondani choonadi ndi mtendere.”—ZEKARIYA 8:18, 19.
1, 2. (a) Kodi mbiri ya anthu ponena za mtendere njotani? (b) Kodi nchifukwa ninji dziko lamakonoli silidzaona mtendere weniweni?
“DZIKO silinakhalepo ndi mtendere. Kwina kwake—ndipo kaŵirikaŵiri m’malo ambiri panthaŵi imodzi—kwakhala nkhondo nthaŵi zonse.” Anatero Profesa Milton Mayer wa pa University of Massachusetts, U.S.A. Ndi ndemanga yomvetsa chisoni kwambiri ponena za anthu! Zoonadi, anthu akhala akufuna mtendere. Andale akhala akuyesayesa kuusungitsa mwa njira zosiyanasiyana, kuyambira ndi Pax Romana ya m’nthaŵi za Roma mpaka mkhalidwe wa “Mutually Assured Destruction” wa mkati mwa Nkhondo ya Pakamwa. Komabe, zoyesayesa zawo zonse zinalephera kotheratu. Monga momwe Yesaya ananenera zaka mazana ambiri zapitazo, ‘mithenga ya mtendere yalira koŵaŵa.’ (Yesaya 33:7) Nchifukwa ninji zakhala tero?
2 Chifukwa chake nchakuti kuti pakhale mtendere wokhalitsa sipayenera kukhala udani, ndi umbombo; mtendere uyenera kuzikidwa pa choonadi. Mtendere sungazikidwe pa mabodza. Nchifukwa chake polonjeza kwa Israyeli wakale za kubwezeretsedwa ndi mtendere wake Yehova anati: “Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira.” (Yesaya 66:12) Mulungu wa dongosolo lino la zinthu, Satana Mdyerekezi, ali “wambanda,” wakupha, ndi “wabodza, ndi atate wake wabodza.” (Yohane 8:44; 2 Akorinto 4:4) Kodi dziko lokhala ndi mulungu wotero lingakhale motani ndi mtendere?
3. Kodi ndi mphatso yabwino kwambiri yotani imene Yehova wapatsa anthu ake, mosasamala kanthu kuti akukhala m’dziko lodzala ndi mavuto?
3 Komabe, mosiyana kwambiri, Yehova amapatsa mtendere kwa anthu ake ngakhale pamene akukhala m’dziko la Satana losakazidwa ndi nkhondo. (Yohane 17:16) M’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., iye anakwaniritsa lonjezo lake kupyolera mwa Yeremiya ndi kupatsa mtundu wake wapadera “mtendere ndi choonadi” pamene anawabwezeretsa ku dziko lawo. (Yeremiya 33:6) Ndipo m’masiku ano otsiriza, wapereka “mtendere ndi choonadi” kwa anthu ake mu “dziko” lawo, kapena mkhalidwe wawo wauzimu wapadziko lapansi, ngakhale kuti iwo apyola nthaŵi zovuta kwambiri zimene dzikoli laziona kufikira lerolino. (Yesaya 66:8; Mateyu 24:7-13; Chivumbulutso 6:1-8) Pamene tipitiriza kukambitsirana kwathu chaputala 8 cha Zekariya, tidzakhala ndi chidziŵitso chakuya cha mtendere ndi choonadi zimene Mulungu watipatsa ndi kuona zimene tiyenera kuchita kuti tipitirizebe kukhala nawo.
“Alimbike Manja Anu”
4. Kodi Zekariya analimbikitsa Aisrayeli kuchita motani ngati anafuna kukhala ndi mtendere?
4 Kachisanu ndi chimodzi m’chaputala 8 cha Zekariya, tikumva chilengezo cholimbikitsa chochokera kwa Yehova chakuti: “Atero Yehova wa makamu: Alimbike manja anu, ndi akumva masiku ano mawu awa pakamwa pa aneneri amene anakhalako tsiku lakuikidwa maziko a nyumba ya Yehova wa makamu, ndiyo Kachisi, kuti amangidwe. Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakuloŵa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.”—Zekariya 8:9, 10.
5, 6. (a) Chifukwa cha kulefuka kwa Aisrayeli, kodi mkhalidwe unali wotani m’Israyeli? (b) Kodi ndi masinthidwe otani amene Yehova analonjeza Israyeli ngati adzaika kulambira kwake patsogolo?
5 Zekariya ananena mawu ameneŵa pamene kachisi anali kumangidwanso m’Yerusalemu. Poyamba, Aisrayeli amene anabwerako ku Babulo analefulidwa ndipo analeka ntchito ya kumanga kachisi. Chifukwa chakuti anasamalira ubwino wa iwo eni, iwo analibe dalitso ndipo analibe mtendere kuchokera kwa Yehova. Ngakhale kuti analima minda yawo ndi kusamalira minda yawo ya mpesa, iwo sanatukuke. (Hagai 1:3-6) Zinali ngati kuti analikugwira ntchito ‘mosalipidwa.’
6 Tsopano popeza kachisi anali kumangidwanso, Zekariya analimbikitsa Ayuda ‘kulimbika,’ molimba mtima kuika kulambira kwa Yehova patsogolo. Kodi nchiyani chikanachitika ngati iwowo akanachita zimenezo? “Tsopano sindidzakhala kwa otsala a anthu awa monga momwe ndinakhalira masiku oyamba, ati Yehova wa makamu. Pakuti padzakhala mbewu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame awo; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale choloŵa chawo. Ndipo kudzachitika kuti, monga munali chotembereretsa mwa amitundu, inu nyumba ya Yuda, ndi nyumba ya Israyeli, momwemo ndidzakusungani, ndipo mudzakhala chodalitsa nacho; musawope, alimbike manja anu.” (Zekariya 8:11-13) Ngati Israyeli akanachita zimenezi motsimikiza mtima, iye akanatukuka. Poyamba, pamene amitundu anafuna kutchula chitsanzo cha temberero, iwo anali kutchula Israyeli. Tsopano Israyeli akanakhala chitsanzo cha dalitso. Ndi chifukwa chabwino kwambiri cha ‘kulimbitsa manja awo’!
7. (a) Kodi ndi masinthidwe osangalatsa otani amene anthu a Yehova aona, amene chipambano chake chaonekera m’chaka chautumiki cha 1995? (b) Poyang’ana lipoti la chaka, kodi mukuona maiko ati amene ali ndi ziŵerengero zazikulu za ofalitsa, apainiya, maola?
7 Bwanji nanga lerolino? Eya, m’zaka za kumbuyo 1919 isanakwane, anthu a Yehova analibe changu kwambiri. Sanapeŵeretu kutenga mbali mu nkhondo yoyamba yadziko, ndipo anali ndi chizoloŵezi cholondola munthu m’malo mwa Mfumu yawo, Yesu Kristu. Choncho, ena analefulidwa ndi chitsutso chochokera mkati ndi kunja kwa gulu. Ndiyeno, mu 1919, iwo analimbitsa manja awo ndi thandizo la Yehova. (Zekariya 4:6) Yehova anawapatsa mtendere, ndipo anatukuka kwambiri. Zimenezi zikusonyezedwa ndi mbiri yawo ya zaka 75 zapitazi, yofika m’chaka chautumiki cha 1995. Monga anthu amodzi, Mboni za Yehova zimapeŵa utundu, ufuko, tsankho ndi zinthu zina zonse zochititsa udani wa mtundu wina uliwonse. (1 Yohane 3:14-18) Amatumikira Yehova m’kachisi wake wauzimu ndi changu chenicheni. (Ahebri 13:15; Chivumbulutso 7:15) Chaka chatha chokha, anathera maola oposa pa biliyoni imodzi kulankhula ndi ena za Atate wawo wakumwamba! Mwezi uliwonse anachititsa maphunziro a Baibulo 4,865,060. Pafupifupi 663,521 anachitako utumiki waupainiya. Pamene atumiki a m’Dziko Lachikristu afuna kupereka chitsanzo cha anthu amene alidi achangu pa kulambira kwawo, iwo nthaŵi zina amatchula Mboni za Yehova.
8. Kodi ndi motani mmene Mkristu aliyense payekha angapindulire ndi “mbewu ya mtendere”?
8 Chifukwa cha changu chawo, Yehova akupatsa anthu ake “mbewu ya mtendere.” Aliyense amene akulitsa mbewu imeneyo adzaona mtendere ulikukula mumtima mwake ndi m’moyo wake. Mkristu aliyense wachikhulupiriro amene amafuna mtendere ndi Yehova ndi Akristu anzake ali ndi choonadi ndi mtendere wa anthu a dzina la Yehova. (1 Petro 3:11; yerekezerani ndi Yakobo 3:18.) Kodi zimenezo si zodabwitsa?
“Musawopa”
9. Kodi ndi kusintha kotani kwa njira yochitira ndi anthu ake kumene Yehova analonjeza?
9 Tikuŵerenga chilengezo chachisanu ndi chiŵiri chochokera kwa Yehova tsopano. Kodi chikuti bwanji? “Atero Yehova wa makamu: Monga ndinalingirira kuchitira inu choipa, muja makolo anu anautsa mkwiyo wanga, ati Yehova wa makamu, ndipo sindinawaleka; momwemonso ndinalingirira masiku ano kuchitira chokoma Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda; musawopa.”—Zekariya 8:14, 15.
10. Kodi ndi mbiri yotani ya Mboni za Yehova imene imasonyeza kuti akhala osawopa?
10 Ngakhale kuti anthu a Yehova anali omwazikana mwauzimu mkati mwa nkhondo yoyamba yadziko, mitima yawo inafuna kuchita zimene zinali zoyenera. Chifukwa chake, pambuyo pa kupereka chilango, Yehova anasintha mochitira nawo. (Malaki 3:2-4) Lerolino, timayang’ana kumbuyo ndi kumuyamika kuchokera pansi pa mtima kaamba ka zimene wachita. Zoonadi, ‘tadedwa ndi anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 24:9) Ambiri amangidwa, ndipo ena afera chikhulupiriro chawo. Kaŵirikaŵiri timayang’anizana ndi mphwayi kapena udani. Koma sitiwopa. Tikudziŵa kuti Yehova ngwamphamvu kuposa chitsutso china chilichonse, chooneka kapena chosaoneka. (Yesaya 40:15; Aefeso 6:10-13) Sitidzaleka kulabadira mawuŵa akuti: “Yembekeza Yehova: Limbika, ndipo [limbitsa mtima wako, NW].”—Salmo 27:14.
“Nenani Choonadi Yense ndi Mnzake”
11, 12. Kodi nchiyani chimene tiyenera kukumbukira aliyense payekha ngati tikufuna kulandira madalitso ochuluka amene Yehova amapereka kwa anthu ake?
11 Kuti tilandire madalitso ochuluka ochokera kwa Yehova, pali zinthu zimene tiyenera kukumbukira. Zekariya akunena kuti: “Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m’zipata zanu; ndipo musalingirira choipa mumtima mwanu yense pa mnzake; nimusakonde lumbiro lonama; pakuti izi zonse ndidana nazo, ati Yehova.”—Zekariya 8:16, 17.
12 Yehova akutilimbikitsa kulankhula choonadi. (Aefeso 4:15, 25) Samamva mapemphero a awo amene amalingalira zinthu zoipa, kubisa choonadi kuti apindule iwo eni, kapena kulumbira monama. (Miyambo 28:9) Popeza amada mpatuko, amafuna kuti ife timamatire ku choonadi cha Baibulo. (Salmo 25:5; 2 Yohane 9-11) Ndiponso, monga amuna akulu okhala pa zipata za mudzi mu Israyeli, akulu osamalira nkhani zachiweruzo ayenera kuzika uphungu wawo ndi zigamulo zawo pa choonadi cha Baibulo, osati pa malingaliro awoawo. (Yohane 17:17) Yehova akufuna kuti iwo afunefune “chiweruzo cha mtendere,” akumayesayesa monga abusa achikristu kubwezeretsa mtendere pakati pa otsutsana ndi kuthandiza ochimwa olapa kupezanso mtendere ndi Mulungu. (Yakobo 5:14, 15; Yuda 23) Nthaŵi imodzimodziyo, amasungitsa mtendere wa mpingo, akumachotsa molimba mtima awo amene amasokoneza mtenderewo mwa kupitiriza kuchimwira dala.—1 Akorinto 6:9, 10.
“Chimwemwe ndi Chikondwerero”
13. (a) Kodi ndi kusintha kotani ponena za kusala kudya kumene Zekariya analosera? (b) Kodi ndi kusala kudya kotani kumene kunachitidwa m’Israyeli?
13 Tsopano, tikumva chilengezo chachisanu ndi chitatu chokhudza mtima chakuti: “Atero Yehova wa makamu: Kusala kwa mwezi wachinayi, ndi kusala kwa mwezi wachisanu, ndi kusala kwa mwezi wachisanu ndi chiŵiri, ndi kusala kwa mwezi wakhumi kukhale kwa nyumba ya Yuda chimwemwe ndi chikondwerero, ndi nyengo zoikika zosekerera; chifukwa chake kondani choonadi ndi mtendere.” (Zekariya 8:19) Pansi pa Chilamulo cha Mose, Aisrayeli anasala kudya pa Tsiku Lachitetezero kusonyeza chisoni chawo pa machimo awo. (Levitiko 16:29-31) Nthaŵi za kusala kudya zinayi zimene zatchulidwa ndi Zekariya mwachionekere zinali kusungidwa kuti asonyeze chisoni pa zimene zinachitika pamene Yerusalemu anagonjetsedwa ndi kuwonongedwa. (2 Mafumu 25:1-4, 8, 9, 22-26) Komabe tsopano, kachisi anali kumangidwanso ndi Yerusalemu namakhalanso ndi anthu. Chisoni chinali kusanduka chikondwerero, ndipo kusala kudya kunakhala nyengo zoikika zosekerera.
14, 15. (a) Kodi ndi motani mmene phwando la Chikumbutso linalili chinthu chachikulu chokondweretsa, ndipo zimenezi ziyenera kutikumbutsanji? (b) Malinga ndi zimene lipoti la chaka likusonyeza, kodi ndi maiko ati amene anali ndi ziŵerengero zazikulu kwambiri za pa Chikumbutso?
14 Lerolino, sitimasunga nthaŵi za kusala kudya zotchulidwa ndi Zekariya kapena kusala kudya konenedwa m’Chilamulo. Popeza Yesu anapereka moyo wake kaamba ka machimo athu, tikusangalala ndi madalitso a Tsiku lalikulu Lachitetezero. Machimo athu amakwiriridwa, osati pamlingo wochepa chabe, koma kotheratu. (Ahebri 9:6-14) Potsatira lamulo la Mkulu wa Ansembe wakumwamba, Yesu Kristu, timasunga Chikumbutso cha imfa yake monga phwando lokha lolemekezeka pakalenda yachikristu. (Luka 22:19, 20) Kodi sitimakhala ndi “chimwemwe ndi chikondwerero” pamene tisonkhana pamodzi paphwandolo chaka chilichonse?
15 Chaka chatha, anthu 13,147,201 anasonkhana kuti achite phwando la Chikumbutso, 858,284 kuposa 1994. Ndi khamu lalikuludi! Tangolingalirani za chimwemwe chimene chinali m’mipingo 78,620 ya Mboni za Yehova pamene anthu ochuluka kwambiri anafika pa Nyumba zawo za Ufumu kaamba ka phwandolo. Ndithudi, onse amene analipo anasonkhezeredwa ‘kukonda choonadi ndi mtendere’ pamene anali kukumbukira imfa ya Uyo amene ali “njira, ndi choonadi, ndi moyo” ndi amene tsopano akulamulira monga “Kalonga Wamtendere” wamkulu wa Yehova! (Yohane 14:6; Yesaya 9:6) Phwandolo linali ndi tanthauzo lapadera kwa awo amene analichita m’maiko osakazidwa ndi chipoloŵe ndi nkhondo. Abale athu ena anaona masoka owopsa kwambiri mu 1995. Komabe, ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, unasunga mitima yawo ndi maganizo awo mwa Kristu Yesu.’—Afilipi 4:7.
‘Tiyeni Tipepeze Yehova’
16, 17. Kodi anthu a amitundu ‘angapepeze Yehova’ motani?
16 Komabe, kodi mamiliyoni onsewo amene anafika pa Chikumbutso anachokera kuti? Mawu a Yehova achisanu ndi chinayi akufotokoza kuti: “Atero Yehova wa makamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m’midzi yambiri adzafika, ndi okhala m’mudzi umodzi adzamuka ku mudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso. Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amphamvu azadza kufunafuna Yehova wa makamu m’Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova.”—Zekariya 8:20-22.
17 Anthu amene anafika pa Chikumbutso anafuna “kufunafuna Yehova wa Makamu.” Ambiri a ameneŵa anali atumiki ake odzipatulira ndi obatizidwa. Mamiliyoni a enawo opezekapo anali asanapangebe chosankha chimenecho. M’maiko ena chiŵerengero cha pa Chikumbutso chinali chachikulu kuŵirikiza kanayi kapena kasanu kuposa chiŵerengero cha ofalitsa a Ufumu. Okondwerera ochuluka ameneŵa akufuna chithandizo kuti apitirize kupita patsogolo. Tiyeni tiwaphunzitse kusangalala ndi chidziŵitso chakuti Yesu anafera machimo athu ndipo tsopano akulamulira mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 5:7, 8; Chivumbulutso 11:15) Ndipo tiyeni tiwalimbikitse kuti adzipatulire kwa Yehova Mulungu ndi kugonjera Mfumu yake yoikidwa. M’njira imeneyi ‘adzapepeza Yehova.’—Salmo 116:18, 19; Afilipi 2:12, 13.
‘Amuna Khumi a Manenedwe Onse a Amitundu’
18, 19. (a) Pakukwaniritsidwa kwa Zekariya 8:23, ndani amene ali “Myuda” lerolino? (b) Kodi ndani lerolino amene ali “amuna khumi” amene ‘akugwira mkawo wa munthu ali Myuda’?
18 Kwa nthaŵi yomaliza mu chaputala chachisanu ndi chitatu cha Zekariya, tikuŵerenga kuti: “Atero Yehova wa makamu.” Kodi chilengezo cha Yehova nchotani? “Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) M’nthaŵi ya Zekariya, Israyeli wakuthupi anali mtundu wosankhidwa wa Mulungu. Komabe, m’zaka za zana loyamba, Israyeli anakana Mesiya wa Yehova. Chifukwa chake, Mulungu wathu anasankha “Myuda”—Israyeli watsopano—monga anthu ake apadera, “Israyeli wa Mulungu” wopangidwa ndi Ayuda auzimu. (Agalatiya 6:16; Yohane 1:11; Aroma 2:28, 29) Chiŵerengero chomaliza cha ameneŵa chinali kudzakhala 144,000, osankhidwa mwa anthu kukalamulira ndi Yesu mu Ufumu wake wakumwamba.—Chivumbulutso 14:1, 4.
19 Ambiri mwa a 144,000 ameneŵa amwalira kale okhulupirika ndipo apita kumwamba kukalandira mphotho yawo. (1 Akorinto 15:51, 52; Chivumbulutso 6:9-11) Ochepa akali padziko lapansi ndipo ameneŵa akusangalala kuona kuti “amuna khumi” amene asankha kupita ndi “Myuda” ndiwo “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.”—Chivumbulutso 7:9; Yesaya 2:2, 3; 60:4-10, 22.
20, 21. Pamene mapeto a dziko lino ayandikira, kodi ndi motani mmene tingakhalire pa mtendere ndi Yehova?
20 Pamene mapeto a dziko lino akuyandikira mosapeŵeka, Dziko Lachikristu lakhala ngati Yerusalemu m’nthaŵi ya Yeremiya: “Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthaŵi yakuchira, ndipo taonani mantha!” (Yeremiya 14:19) Mantha amenewo adzafika pachimake pamene amitundu adzaukira chipembedzo chonyenga ndi kuchithetsa mwachiwawa. Mwamsanga zitangochitika, amitundu nawonso adzawonongedwa m’nkhondo yomaliza ya Mulungu, Armagedo. (Mateyu 24:29, 30; Chivumbulutso 16:14, 16; 17:16-18; 19:11-21) Imeneyotu idzakhaladi nthaŵi yachipoloŵe!
21 M’nthaŵi yonseyo, Yehova adzatetezera awo amene amakonda choonadi ndi kukulitsa “mbewu ya mtendere.” (Zekariya 8:12; Zefaniya 2:3) Choncho, tiyeni tikhaletu osungika m’dziko la anthu ake, tikumamtamanda poyera mwachangu ndi kuthandiza anthu ambirimbiri ‘kupepeza Yehova.’ Ngati titero, tidzakhala ndi mtendere wa Yehova nthaŵi zonse. Inde, “Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu: Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.”—Salmo 29:11.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi ndi motani mmene anthu a Mulungu ‘analimbitsira manja awo’ m’nthaŵi ya Zekariya? Lerolino?
◻ Kodi timatani tikakumana ndi chizunzo, udani, ndi mphwayi?
◻ Kodi ‘kunena choonadi yense ndi m’nzake’ kumaphatikizapo chiyani?
◻ Kodi ndi motani mmene munthu ‘angapepezere Yehova’?
◻ Kodi chochititsa chimwemwe chachikulu chimene chikusonyezedwa pa kukwaniritsidwa kwa Zekariya 8:23 nchiyani?
[Chithunzi patsamba 18]
Chaka chatha, Mboni za Yehova zinathera maola 1,150,353,444 kulankhula ndi anthu za Ufumu wa Mulungu