Kuchita Zimene Mulungu Amafuna Kumalemekeza Yehova
“Ndidzam’bukitsa [“Ndim’lemekeza,” NW] ndi kum’yamika.”—SALMO 69:30.
1. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amayenera kupatsidwa ulemu? (b) Kodi timamulemekeza ndi kum’yamika bwanji?
YEHOVA ndiye Mulungu wamphamvuyonse, Wolamulira wa Chilengedwe chonse, ndiponso Mlengi. Motero, dzina lake ndi zolinga zake n’zoyenera ulemu. Kulemekeza Yehova kumatanthauza kum’patsa ulemu waukulu, kum’kweza, ndi kum’tamanda. Kuti tichite zimenezo “ndi kum’yamika” tifunika kum’thokoza nthaŵi zonse chifukwa cha zimene akutichitira pakalipano komanso zimene adzatichitira m’tsogolo. Maganizo amene tifunika kukhala nawo awasonyeza pa Chivumbulutso 4:11, pamene zolengedwa zauzimu zokhulupirika kumwamba zinalengeza kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” Kodi tingalemekeze bwanji Yehova? Tingatero mwa kuphunzira za iye ndiyeno n’kumachita zimene iye amafuna kwa ife. Tiyenera kuganiza monga mmene wamasalmo anachitira pamene ananena kuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga.”—Salmo 143:10.
2. Kodi Yehova adzatani nawo anthu amene amam’lemekeza, ndiponso amene sam’lemekeza?
2 Yehova amaona anthu amene amamulemekeza kukhala a mtengo wapatali. N’chifukwa chake iye ndiye “wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Kodi mphoto yake ndi yotani? Yesu ananena m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Inde, amene ‘amalemekeza Yehova ndi kum’yamika’ “adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Koma ‘woipa sadzalandira mphoto.’ (Miyambo 24:20) Ndipo kulemekeza Yehova kukufunika mwachangu m’masiku otsiriza ano, chifukwa posachedwapa adzawononga oipa ndi kupulumutsa olungama. “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17; Miyambo 2:21, 22.
3. N’chifukwa chiyani tifunika kulabadira zimene zili m’buku la Malaki?
3 Zimene Yehova amafuna zimapezeka m’Baibulo, popeza “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu.” (2 Timoteo 3:16) M’Mawu a Mulungu amenewo muli nkhani zosiyanasiyana zofotokoza mmene Yehova amadalitsira amene amamulemekeza ndiponso zimene zimachitikira anthu amene sam’lemekeza. Nkhani ina yofotokoza zimenezi ndi ya zimene zinachitika m’Israyeli pa nthaŵi ya mneneri Malaki. Iye analemba buku lodziŵika ndi dzina lake cha m’ma 443 B.C.E., nthaŵi imene Nehemiya anali kazembe wa Yuda. Buku lamphamvu ndiponso losangalatsa limeneli lili ndi maulosi ndiponso nkhani zimene “zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.” (1 Akorinto 10:11) Kulabadira mawu a Malaki kungatithandize kukonzekera “tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova,” pamene Iye adzawononga dziko loipali.—Malaki 4:5.
4. Kodi ndi mfundo zisanu ndi imodzi ziti zimene akutisonyeza m’chaputala 1 cha Malaki?
4 Kodi buku la Malaki limene analilemba zaka zoposa 2,400 zapitazo lingatithandize bwanji m’zaka za m’ma 2000 zino kukonzekera tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova? Chaputala choyamba chikutisonyeza mfundo zisanu ndi ziŵiri zofunika kwambiri kuti tilemekeze Yehova ndi kum’yamika kuti atiyanje ndi kupeza moyo wosatha. Mfundozi ndizo: (1) Yehova amakonda anthu ake. (2) Tiziona zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. (3) Yehova amafuna kuti tizim’patsa zinthu zabwino koposa. (4) Chikondi chochokera pansi pa mtima n’chimene chimalimbikitsa kulambira koona osati dyera ayi. (5) Utumiki wovomerezeka kwa Mulungu si mwambo wamba ndiponso siwolemetsa. (6) Tonsefe, aliyense payekha, tidzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu. Tsopano, tiyeni tione mfundo iliyonse mwa mfundo zimenezi pamene tikupenda Malaki chaputala 1 m’nkhani yoyamba ino mwa nkhani zitatu zofotokoza buku la Malaki.
Yehova Amakonda Anthu Ake
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anakonda Yakobo? (b) Kodi tingayembekezere chiyani ngati titsanzira kukhulupirika kwa Yakobo?
5 Chikondi cha Yehova achifotokoza momveka bwino m’mavesi oyamba a Malaki. Bukuli likuyamba ndi mawu akuti: “Katundu wa mawu a Yehova wa kwa Israyeli.” Ndiyeno Mulungu anapitiriza kuti: “Ndakukondani.” Yehova popereka chitsanzo m’vesi lomweli, akuti: “Ndinakonda Yakobo.” Yakobo ankakhulupirira Yehova. Patapita nthaŵi, Yehova anasintha dzina la Yakobo n’kukhala Israyeli, ndipo anakhala kholo la mtundu wa Israyeli. Yehova anakonda Yakobo chifukwa cha kukhulupirira kwake. Yehova anakondanso anthu ena a mtundu wa Israyeli amene anali kumukhulupirira monga Yakobo.—Malaki 1:1, 2.
6 Ngati tikonda Yehova ndi kugwirizanabe ndi anthu ake, mawu a pa 1 Samueli 12:22 angatilimbikitse. Mawuwo amati: “Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu.” Yehova amakonda anthu ake ndipo adzawapatsa mphoto yaikulu ya moyo wosatha. N’chifukwa chake tikuŵerenga kuti: “Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata choonadi. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.” (Salmo 37:3, 4) Kukonda kwathu Yehova kukuphatikizapo mfundo yachiŵiri imene aifotokoza pa Malaki chaputala 1.
Onani Zinthu Zopatulika Kukhala Zofunika Kwambiri
7. N’chifuwa chiyani Yehova anada Esau?
7 Pamene tiŵerenga pa Malaki 1:2, 3, Yehova atanena kuti “ndinakonda Yakobo,” ndiyeno anati “Esau ndinamuda.” N’chifukwa chiyani anakonda Yakobo n’kuda Esau? Yakobo analemekeza Yehova, koma Esau, mchimwene wake amene anabadwa naye mapasa, sanatero. Esau anali kutchedwanso Edomu. Pa Malaki 1:4, dziko la Edomu alitcha dziko la choipa, ndipo Yehova wawakwiyira anthu a mmenemo. Dzina lakuti Edomu (limene limatanthauza “Zofiira”) anam’patsa Esau chifukwa chakuti anagulitsa ukulu wake kwa Yakobo pousinthanitsa ndi mphodza zofiira. Lemba la Genesis 25:34 limati: “Esau ananyoza ukulu wake.” Mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kusamala kuti “pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nawo mtanda umodzi wa chakudya.”—Ahebri 12:14-16.
8. Kodi n’chiyani chinam’chititsa Paulo kugwirizanitsa Esau ndi wachigololo?
8 N’chifukwa chiyani Paulo anagwirizanitsa zimene Esau anachita ndi chigololo? Chifukwa chakuti kukhala ndi mtima wa Esau kungapangitse munthu kusaona zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. Kenako, zimenezi zingathe kum’loŵetsa munthu m’machimo aakulu, monga chigololo. Motero, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nthaŵi zina ndimafuna kusinthanitsa choloŵa changa chachikristu chomwe ndi moyo wosatha ndi chinthu chosakhalitsa chomwe chingafanane ndi mbale ya mphodza? Kapena kodi mosadziŵa ndimanyozera zinthu zopatulika?’ Esau ankangofuna atakhutiritsa chilakolako chake chakuthupi, ndipo sanaleze mtima. Polankhulana ndi Yakobo iye anati: “[Fulumira, NW], undipatse ndidye chofiiracho.” (Genesis 25:30) N’zomvetsa chisoni kuti ena mwa atumiki a Mulungu anenadi kuti: “Ndikufuna zofulumira! N’kudikiriranji ukwati wolemekezeka?” Chilakolako chawo cha kugonana mosaganizira kuti pakhala zotsatira zotani chakhala mbale yawo ya mphodza.
9. Kodi tingatani kuti tipitirize kuopa Yehova kom’patsa ulemu?
9 Tiyenitu tisanyozere zinthu zopatulika mwa kunyalanyaza chiyero, kukhulupirika, ndi choloŵa chathu chauzimu. M’malo mokhala ngati Esau, tiyeni tikhale ngati Yakobo wokhulupirika ndi kupitirizabe kuopa Mulungu kom’patsa ulemu mwa kuona zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero mwa kuchita mosamala zimene Yehova amafuna. Zimenezi zikutifikitsa pa mfundo yachitatu yomwe chaputala choyamba cha Malaki chikutisonyeza. Kodi ndi mfundo yotani?
Kum’patsa Yehova Zinthu Zabwino Koposa
10. Kodi ansembewo ananyoza bwanji gome la Yehova?
10 Ansembe a Yuda amene anali kutumikira pa kachisi mu Yerusalemu m’nthaŵi ya Malaki sanali kum’patsa Yehova nsembe zabwino koposa. Malaki 1:6-8 amati: “Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa.” “Tapeputsa dzina lanu motani?” anafunsa motero ansembewo. Yehova anayankha kuti: “Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe.” Ansembewo anafunsa kuti: “Takudetsani motani?” Motero Yehova anawauza kuti: “Mwakuti munena, Gome la Yehova n’lonyozeka.” Ansembewo ankanyoza gome la Yehova nthaŵi zonse popereka nsembe yolakwika, amvekere: “Palibe choipa!”
11. (a) Kodi Yehova anati chiyani za nsembe zosavomerezeka? (b) N’chifukwa chiyani anthu ena omwe sanali ansembe analinso ndi mlandu?
11 Kenako Yehova anawauza za nsembe yosavomerezekayo kuti: “Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzam’komera kodi? kapena adzakuvomerezani kodi?” Zosatheka! Kazembe wawo sangalole mphatso ngati imeneyo. Kodi Wolamulira Wamkulu wa Chilengedwe Chonse ndiye angalole nsembe zolakwikazo? Komatu si ansembe okha amene anali ndi mlandu. Zoonadi, anali kunyoza Yehova mwa kupereka nsembe yeniyeniyo. Kodi anthu ena amene sanali ansembe analibe mlandu? Anali nawo! Ndi anthuwo amene ankasankha nyama zakhungu, zotsimphina, ndi zodwala ndipo ndi amene anali kuzibweretsa kwa ansembe kuti azipereke nsembe. Uchimo wakewo inu!
12. Kodi gulu la Yehova likutithandiza bwanji kupatsa iye zabwino koposa?
12 Kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa ndi njira imodzi yosonyezera kuti timam’konda kwambiri. (Mateyu 22:37, 38) Mosiyana ndi ansembe osamvera a m’nthaŵi ya Malaki, gulu la Yehova lerolino limapereka malangizo abwino a m’Malemba amene amatithandiza kulemekeza Yehova ndi kum’yamika mwa kuchita zimene iye amafuna. Mfundo yofunika kwambiri yachinayi imene tikuipeza m’Malaki chaputala 1 n’njokhudzana ndi zimenezi.
Chikondi N’chimene Chimalimbikitsa Kulambira Koona Osati Dyera
13 Kodi ansembe ankachita chiyani chimene chinasonyeza kuti ankatumikira pa kachisi n’zolinga zadyera?
13 Ansembe a m’nthaŵi ya Malaki anali adyera, opanda chikondi, ndiponso ongofuna ndalama basi. Tikudziŵa bwanji zimenezi? Malaki 1:10 amati: “Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe pa guwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu.” Inde, ansembe adyera amenewo ankafuna malipiro ngakhale pa ntchito yaing’ono yomwe agwira pakachisi! Tangoganizani! Ankafuna kuwalipira ngakhale chifukwa chotseka zitseko ndi kuyatsa moto wa paguwa lansembe! Ndiye chifukwa chake Yehova sanalandire chopereka m’dzanja lawo.
14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mboni za Yehova zimatumikira chifukwa cha chikondi?
14 Dyera ndi kudzikonda kwa ansembe ochimwawo m’Yerusalemu wakale zikutikumbutsa kuti adyera sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu malinga ndi mmene Mawu a Mulungu amanenera. (1 Akorinto 6:9, 10) Kusinkhasinkha zoti ansembe aja anali kungofuna kupezerapo phindu pautumiki wawo kukutipangitsa kuyamikira kwambiri ntchito yolalikira yomwe ife Mboni za Yehova tikuchita. Timaichita mofuna tokha, ndipo sitilipiritsa utumiki wathu. Eetu, ‘sitichita nawo malonda mawu a Mulungu.’ (2 Akorinto 2:17) Mofanana ndi Paulo, aliyense wa ife anganene ndi mtima wonse kuti: “Ndinalalikira kwa inu mosangalala Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaulere.” (2 Akorinto 11:7, NW) Onani kuti Paulo ‘analalikira mosangalala uthenga wabwino.” Zimenezi zikutifikitsa pa mfundo yachisanu yopezeka mu Malaki chaputala 1.
Kutumikira Mulungu Sindiko Mwambo Wamba Ndiponso Sikolemetsa
15, 16. (a) Kodi ansembe ankaona motani kupereka nsembe? (b) Kodi Mboni za Yehova zimapereka motani nsembe zawo?
15 Ansembe osakhulupirira mu Yerusalemu wakale ankaona kupereka nsembe ngati mwambo wamba komanso wotopetsa. Ankaona ngati ndi chimtolo cholemetsa. Monga momwe Malaki 1:13 amanenera, Mulungu anawauza kuti: “Mukutinso, Taonani, n’cholemetsa ichi! ndipo mwachipeputsa.” Ansembe amenewo anapeputsa, kapena kuti kunyozera, zinthu zopatulika za Mulungu. Tiyeni tizipemphera kuti aliyense wa ife asafanane nawo. M’malo mwake, tiyeni nthaŵi zonse tisonyeze mzimu umene uli pa 1 Yohane 5:3 pomwe pamati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”
16 Tiyeni tisangalale popereka nsembe zauzimu kwa Mulungu, osaona ngati chimtolo cholemetsa. Tiyeni timvere mawu aulosi aŵa akuti: “Nenani kwa [Yehova], chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mawu milomo yathu ngati ng’ombe.” (Hoseya 14:2) Mawu akuti “milomo yathu ngati ng’ombe” akutanthauza nsembe zauzimu, mawu amene timalankhula potamanda Yehova ndiponso kufotokoza zolinga zake. Ahebri 13:15 amati: “Potero mwa [Yesu Kristu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” Ndife osangalalatu kwabasi kuti nsembe zathu zauzimu sizili mwambo wamba, koma ndi chizindikiro chakuti timakonda Mulungu ndi mtima wonse. Mfundo imeneyi ikutifikitsa pa mfundo yachisanu ndi chimodzi yomwe tingaiphunzire m’Malaki chaputala 1.
Aliyense Adzadziŵerengera Mlandu
17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anatemberera “wonyengayo”? (b) Kodi amene anachita monyenga sanaganizire mfundo iti?
17 Anthu omwe analipo m’nthaŵi ya Malaki anadziŵerengera mlandu pa zochita zawo aliyense payekha, ndipo n’chimodzimodzinso ndi ifeyo lerolino. (Aroma 14:12; Agalatiya 6:5) Ndiye chifukwa chake Malaki 1:14 amati: “Wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna [yabwino] m’gulu lake, naŵinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema.” Munthu amene anali ndi gulu la nyama anali nazo zambiri. Sikuti anali ndi imodzi yokha moti sakanachitira mwina koma kungopereka yomweyo. Posankha nyama yoti akapereke, akanatha kusankha yomwe sinali yakhungu, yotsimphina, kapena yodwala. Ngati akanasankha nyama yachilema ngati imeneyo, zikanasonyeza kuti amanyozera makonzedwe a Yehova a nsembe, chifukwa munthu amene anali ndi gulu la nyama mosakayika akanatha kupeza ina yopanda chilema.
18 Ndiye n’chifukwa chaketu Yehova anatemberera wonyenga amene anali ndi nyama yabwino koma anabweretsa, mwinanso kuchita kududuluzira nyama yakhungu, yotsimphina, kapena yodwala kwa wansembe kuti aipereke. Komabe, palibe ngakhale kachizindikiro kakang’ono kosonyeza kuti wansembe wina aliyense anagwirapo mawu Chilamulo kuti Mulungu savomereza nyama yachilema ngati imeneyo. (Levitiko 22:17-20) Munthu aliyense woganiza bwino ankadziŵa kuti sizikanamuyendera bwino ngati akanayerekeza kupereka mphatso ngati imeneyo kwa kazembe wawo. Komano pano anali kupereka mphatso kwa Wolamulira wa Chilengedwe chonse, Yehova, yemwe ndi wokwezeka kwambiri kuposa kazembeyo. Malaki 1:14 akuti: “Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.”
19. Kodi tikulakalaka chiyani, ndipo tiyenera kumachita chiyani?
19 Monga atumiki okhulupirika a Mulungu, tikulakalaka nthaŵi imene Mfumu Yaikuluyo, Yehova, adzalemekezedwa ndi anthu onse. Panthaŵi imeneyo, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Pakali pano, tiyeni tiyesetse kuchita zimene Yehova amafuna mwa kutsanzira wamasalmo amene anati: “Ndidzam’bukitsa [“Ndidzam’lemekeza,” NW] ndi kum’yamika.” (Salmo 69:30) Kuti tichite zimenezo, buku la Malaki lili ndi malangizo ena amene angatithandize kwambiri. Ndiyetu tiyeni tipende mosamalitsa mbali zina za buku la Malaki m’nkhani ziŵiri zotsatirazi.
Kodi Mukukumbukira?
• N’chifukwa chiyani tifunika kulemekeza Yehova?
• N’chifukwa chiyani Yehova sanavomereze nsembe zimene ansembe ankapereka m’nthaŵi ya Malaki?
• Kodi timapereka motani nsembe zotamanda kwa Yehova?
• Kodi n’chiyani chiyenera kulimbikitsa kulambira koona?
[Chithunzi patsamba 9]
Ulosi wa Malaki unafotokoza zokhudza nthaŵi yathu ino
[Chithunzi patsamba 10]
Esau sanaone zinthu zopatulika kukhala zofunika kwambiri
[Chithunzi patsamba 11]
Ansembe ndi anthu ena omwe sanali ansembe anapereka nsembe zosavomerezeka
[Chithunzi patsamba 12]
Mboni za Yehova padziko lonse zimapereka nsembe zotamanda popanda kulipiritsa